Kodi Mulungu Analiuzira Motani Baibulo?
KULANKHULANA makono nkochititsa chidwi kwambiri kuposa panthaŵi ina iliyonse kumbuyoku. Zaka zapitazo, ndani akanaganiza kuti nthaŵi idzafika pamene adzatumiza mauthenga kamodzinkamodzi kulikonse padziko mwa kugwiritsira ntchito mafoni, makina a fax, ndi makompyuta?
Koma kulankhulana kochititsa chidwi koposa ndi kuja komwe munthu sangakutsanzire—kuuzira kwa Mulungu. Yehova anauzira alembi aumunthu okwanira ngati 40 kulemba Mawu ake, Baibulo Lopatulika. Monga momwe anthu alili ndi njira zambiri zolankhulirana, Yehova anagwiritsiranso ntchito njira zambiri zolankhulirana kuti auzire Malemba.
Kulankhula. Mulungu anapereka mauthenga ena amene pambuyo pake analembedwa m’Baibulo.a Mwachitsanzo, talingalirani za malamulo opanga pangano la Chilamulo. “Ulembere mawu awa,” Yehova anauza Mose, “pakuti monga mwa mawu awa ndapangana ndi iwe ndi Israyeli.” (Eksodo 34:27) “Mawu” amenewo, amene ‘adaikidwa ndi angelo,’ Mose anawakopa ndipo tsopano ali m’mabuku a Babulo a Eksodo, Levitiko, Numeri, ndi Deuteronomo.—Machitidwe 7:53.
Aneneri ena ambiri, kuphatikizapo Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, Amosi, Nahumu, ndi Mika, analandira mauthengawo kwa Mulungu kupyolera mwa angelo. Nthaŵi zina amuna ameneŵa anayamba mauthenga awo ndi mawu akuti: “Atero Yehova.” (Yesaya 37:6; Yeremiya 2:2; Ezekieli 11:5; Amosi 1:3; Mika 2:3; Nahumu 1:12) Ndiyeno analemba zimene Mulungu ananena.
Masomphenya, Maloto, ndi Kutengeka Maganizo. Masomphenya ndiwo chithunzithunzi, chochitika, kapena uthenga woikidwa m’maganizo a munthu mwanjira yachilendo pamene ali maso. Mwachitsanzo, Petro, Yakobo, ndi Yohane, “mmene anayera m’maso ndithu,” anaona masomphenya a Yesu atasandulika. (Luka 9:28-36; 2 Petro 1:16-21) Nthaŵi zina, uthenga unali kuperekedwa m’maloto, kapena masomphenya ausiku, kuikidwa m’maganizo a woulandirayo pamene iye ali m’tulo. Chotero, Danieli analemba za “masomphenya a m’mtima mwanga pakama panga”—kapena, malinga ndi kumasulira kwa Ronald A. Knox, “pamene ndinali kuyang’ana m’maloto anga.”—Danieli 4:10.
Munthu amene Yehova anamtengetsa maganizo mwachionekere maganizo akewo anamwerekera kwambiri ndi kuganiza, ngakhale kuti anali maso pang’ono. (Yerekezerani ndi Machitidwe 10:9-16.) M’Baibulo liwu lachigiriki lomasulidwa “kutengeka maganizo” (ekʹsta·sis) limatanthauza ‘kuchotsa kapena kusuntha.’ Limapereka lingaliro la kusuntha maganizo kuwachotsa m’malo mwake. Choncho, munthu amene watengeka maganizo sazindikira zimene zamzinga pamene wamwerekera ndi kuona masomphenyawo. Mtumwi Paulo angakhale atatengeka maganizo pamene “anakwatulidwa kumka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.”—2 Akorinto 12:2-4.
Kusiyana ndi aja amene analemba mauthenga ochita kuwatchulira Mulungu, nthaŵi zambiri olemba Baibulo omwe anaona masomphenya kapena maloto kapena kutengeka maganizo anali nawo ufulu pang’ono wofotokoza m’mawu awoawo zimene anaona. Habakuku anauzidwa kuti: “Lembera masomphenyawo, nuwachenutse pamagome, kuti awaŵerenge mofulumira.”—Habakuku 2:2.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti mbali za Baibulo zimenezi zili zosauziridwa kwenikweni kuposa zija zimene mawu ake anachita kuwatchulira kuti awalembe? Ayi. Mwa mzimu wake, Yehova anaika zolimba uthenga wake m’maganizo a mlembi aliyense, kotero kuti malingaliro a Mulungu ndiwo analembedwa, osati a munthu ayi. Pamene Yehova analola mlembi kusankha mawu oyenera, analamulira maganizo a mlembiyo ndi mtima wake ncholinga choti asasiye chidziŵitso chilichonse chofunika ndipo pomaliza pake mawuwo moyenera anaonedwa ngati a Mulungu.—1 Atesalonika 2:13.
Vumbulutso la Mulungu. Baibulo lili ndi ulosi—mbiri yovumbulidwa ndiponso yolembedwa pasadakhale—zimene munthu wamba sangachite. Chitsanzo chake ndi chija cha kuuka ndi kugwa kwa “mfumu ya Helene [“Girisi,” NW],” Alexander Wamkulu, koloseredwa zaka ngati 200 pasadakhale! (Danieli 8:1-8, 20-22) Baibulo limavumbulanso zochitika zomwe anthu sanazionepo ndi maso awo. Chitsanzo chake ndicho kulengedwa kwa miyamba ndi dziko lapansi. (Genesis 1:1-27; 2:7, 8) Kenaka pali makambitsirano omwe anachitikira kumwamba, onga aja omwe limasimba buku la Yobu.—Yobu 1:6-12; 2:1-6.
Ngati Mulungu mwini sanamvumbulire mlembi zochitika, iye Mulungu anali kudziŵitsa wina kotero kuti zimenezo zikhale mbiri yapakamwa kapena yolembedwa, yomwe mbadwo wina unapatsira wotsatira mpaka italembedwa m’Baibulo. (Onani bokosi patsamba 7.) Mulimonse momwe zinalili, tikhulupirira kuti Yehova ndiye anapereka chidziŵitso chonse chimenecho, ndipo anatsogoza alembi ake ncholinga choti zolemba zawo zisakhale ndi zolakwa, kusinjirira, kapena nthano. Za ulosi, Petro analemba kuti: “Anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.”b—2 Petro 1:21.
Anafunika Khama Ndithu
Ngakhale kuti olemba Baibulo ‘anagwidwa ndi mzimu woyera,’ anafunikabe kusamala kwambiri. Mwachitsanzo, Solomo “anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri. [Iye] anasanthula akapeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mawu oona.”—Mlaliki 12:9, 10.
Ena olemba Baibulo anafufuza kwambiri kuti apeze maumboni a zolemba zawo. Mwachitsanzo, Luka analemba za Uthenga wake Wabwino kuti: ‘Ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulemba tsatanetsatane.’ Inde, mzimu wa Mulungu unamdalitsa Luka pakhama lake, ndipo mosakayika unamthandiza kupeza maumboni odalirika a zakumbuyo ndi kufunsa mboni zoona ndi maso zodalirika, monga ophunzira omwe anali ndi moyo ndipo mwina ndi mayi wa Yesu, Mariya. Ndiye mzimu wa Mulungu unamtsogolera Luka kulemba mawuwo molongosoka bwino.—Luka 1:1-4.
Kusiyana ndi Uthenga Wabwino wa Luka, wa Yohane unali woonako ndi maso, ndipo unalembedwa zaka ngati 65 pambuyo pa imfa ya Yesu. Mosakayika mzimu wa Yehova unachirikiza chikumbuko cha Yohane kuti chisafooke ndi kupita kwa nthaŵi. Zimenezo zinagwirizana ndi zimene Yesu anawalonjeza otsatira ake: “Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.”—Yohane 14:26.
Nthaŵi zina olemba Baibulo anaphatikizapo zimene anasonkhanitsa kuchokera m’zimene olemba mbiri akale analemba omwe ena sanali ouziridwa, koma anali mboni zoona ndi maso. Kwenikweni, Yeremiya analemba 1 Mafumu ndi 2 Mafumu mwanjira imeneyi. (2 Mafumu 1:18) Ezara anafufuza zolemba zina zosachepera 14 zosauziridwa posonkhanitsa zimene analemba mu 1 Mbiri ndi 2 Mbiri, kuphatikizapo “bukhu la mbiri ya mfumu Davide” ndi “buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.” (1 Mbiri 27:24; 2 Mbiri 16:11) Mose anagwira mawu ngakhale “buku la Nkhondo za Yehova”—mwachionekere buku lodalirika la mbiri ya nkhondo za anthu a Mulungu.—Numeri 21:14, 15.
Pochita zimenezo mzimu woyera unalipo, kuwasonkhezera olemba Baibulo kungosankha zinthu zodalirika basi, zimene zinadzakhala mbiri youziridwa ya Baibulo.
Uphungu Wake Wothandiza—Kodi Unachokera kwa Yani?
Baibulo lili ndi uphungu wothandiza wochuluka kwambiri woperekedwa ndi anthu anzeru kwambiri. Mwachitsanzo, Solomo analemba kuti: “Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera ku dzanja la Mulungu.” (Mlaliki 2:24) Paulo ananena kuti uphungu wake pa ukwati unali “monga mwa kuyesa [kwake],” ngakhale anawonjeza kuti: “Ndiganiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.” (1 Akorinto 7:25, 39, 40) Inde, Paulo anali nawo mzimu wa Mulungu, pakuti malinga ndi zimene mtumwi Petro ananena, zimene Paulo analemba zinali ‘monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye.’ (2 Petro 3:15, 16) Chotero, motsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, iye anali kulankhula maganizo ake.
Pamene olemba Baibulo anali kulankhula zinthu ngati zimenezo zomwe iwo anakhulupirira, anatero ataŵerenga ndi kutsatira malemba omwe anali nawo. Tikhulupirira kuti zolemba zawo zinagwirizana ndi kuganiza kwa Mulungu. Zimene analemba zinakhala m’Mawu a Mulungu.
Zoona, Baibulo lili ndi mawu a anthu ena omwe kuganiza kwawo kunali kolakwa. (Yerekezerani Yobu 15:15 ndi 42:7.) Lilinso ndi mawu angapo osonyeza nsautso ya mtima ya atumiki a Mulungu, ngakhale kuti mawuwo sanapereke chithunzi chonse cha nkhaniyo.c Polemba mawu ngati amenewo aumwini, mlembiyo anatsogozedwabe ndi mzimu wa Mulungu kuti alembe zolongosoka, zimene zinasonyeza ndi kuvumbula kalingaliridwe kolakwa. Ndiponso, panthaŵi iliyonse, nkhani yake imamsonyeza bwino woŵerenga aliyense wolingalira bwino ngati kuganiza kwa mlembiyo kuli kwabwino.
Mwachidule, tikhulupirira kuti Baibulo lonse ndi uthenga wa Mulungu. Indedi, Yehova anatsimikiza kuti zonse zomwe zilimo zayenerana ndi chifuno chake ndipo zili ndi malangizo ofunika kwambiri kwa aja ofuna kumtumikira.—Aroma 15:4.
Anagwiritsiranji Ntchito Anthu Kulilemba?
Kugwiritsira ntchito kwake anthu kulemba Baibulo kumasonyeza nzeru yaikulu ya Yehova. Taganizani zotsatirazi: Ngati Mulungu akanapatsa angelo ntchitoyo, kodi Baibulo likanakopa chidwi momwe limachitiramu? Zoona, tikanachitabe chidwi kuŵerenga za mikhalidwe ya Mulungu ndi zochita zake malinga ndi kufotokoza kwa angelo. Koma ngati uthenga wa Baibulo ukanapandiratu umunthu, tikanavutika kuumvetsa.
Tinene chitsanzo: Baibulo likanangotchula kuti Mfumu Davide anachita chigololo ndi mbanda ndi kuti pambuyo pake analapa. Komatu zimamveka bwino bwanji kumva mawu ake Davide, pamene akufotokoza kuzunzika kwake mtima chifukwa cha zochita zake ndi kupempha Yehova kumkhululukira! “Choipa changa chili pamaso panga chikhalire,” analemba tero. “Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:3, 17) Ndiye chifukwa chake Baibulo limamveka bwino, lili ndi mafotokozedwe amitundumitundu, ndipo limakopa chifukwa linalembedwa ndi anthu.
Inde, Yehova anasankha njira yabwino koposa kuti atipatse Mawu ake. Ngakhale kuti anagwiritsira ntchito anthu okhala ndi zofooka, iwo anagwidwa ndi mzimu woyera kuti m’zolemba zawo musakhale zolakwa. Choncho, phindu lake la Baibulo nlopambana. Uphungu wake ngwabwino, ndipo maulosi ake a Paradaiso wa mtsogolo padziko lapansi ngodalirika.—Salmo 119:105; 2 Petro 3:13.
Bwanji osakhala ndi chizoloŵezi choŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku? Petro analemba kuti: “Kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu, kuti kupyolera mwa iwo mukafikire chipulumutso.” (1 Petro 2:2, NW) Popeza Mulungu analiuzira, mudzaona kuti Lemba lililonse “lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
[Mawu a M’munsi]
a Kamodzi kokha, popereka Malamulo Khumi, mawuwo analembedwa ndi “chala cha Mulungu” mwini. Ndiyeno Mose anangokopa mawuwo pamipukutu ndi zolembapo zina.—Eksodo 31:18; Deuteronomo 10:1-5.
b Mtundu wina wa liwu lachigiriki lotembenuzidwa panopa kuti “ogwidwa,” pheʹro, wagwiritsidwa ntchito pa Machitidwe 27:15, 17 kufotokoza chombo chotengeka ndi mphepo. Choncho mzimu woyera ‘unawongola njira’ ya olemba Baibulo. Unawasonkhezera kusiya chidziŵitso chonyenga ndi kuikamo kokha choona.
c Mwachitsanzo, yerekezerani 1 Mafumu 19:4 ndi mavesi 14 ndi 18; Yobu 10:1-3; Salmo 73:12, 13, 21; Yona 4:1-3, 9; Habakuku 1:1-4, 13.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]
Kodi Mose Anazichotsa Kuti Zomwe Analemba?
MOSE ndiye analemba buku la Baibulo la Genesis, koma zonse zomwe analemba zinachitika kalekale iye asanabadwe. Nanga iye anazichotsa kuti zinthu ngati zimenezo? Mwina Mulungu mwini anazivumbula kwa iye, kapena anthu a mbadwo wina anapatsira chidziŵitsocho a mbadwo wotsatira mwa kuwasimbira zochitikazo. Popeza moyo wa anthu kalelo unali wautali kwambiri, zochuluka zomwe Mose analemba m’Genesis zingakhale zitachoka kwa Adamu kufika kwa Mose mwa anthu asanu okha—Metusela, Semu, Isake, Levi, ndi Amramu.
Ndiponso, Mose angakhale atafufuza mipukutu ya mbiri yakale. Pano, ndi bwino kutchula kuti Mose nthaŵi zambiri amagwiritsira ntchito mawu akuti “Mibadwo ya . . . ndi iyi [“Iye ndi mbiri ya,” NW],” asanatchule munthu amene akufuna kumfotokoza. (Genesis 6:9; 10:1; 11:10, 27; 25:12, 19; 36:1, 9; 37:2) Akatswiri ena a maphunziro amati liwu lachihebri lotembenuzidwa panopa kuti “mbiri,” toh·le·dhohthʹ, limanena za mpukutu womwe ulipo kale wa mbiri yakale umene Mose anatengamo zimene analemba. Komabe, sitinganene zimenezi motsimikiza.
Mwina zimene analemba m’buku la Genesis anazipeza mwa njira zonse zitatu zimene tatchulazo—zina mwa kuvumbulidwa kwa iye, zina mwa mawu a pakamwa, ndipo zina anazichotsa m’mipukutu ya mbiri yakale. Chachikulu nchakuti mzimu wa Yehova unauzira Mose. Chifukwa chake, zomwe analemba zimaonedwa moyenera monga mawu a Mulungu.
[Chithunzi patsamba 4]
Mwanjira zosiyanasiyana, Mulungu anauzira anthu kulemba Baibulo