NKHANI YOPHUNZIRA 10
NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu
‘Pitirizani Kutsatira’ Yesu Mukabatizidwa
“Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo nʼkupitiriza kunditsatira tsiku ndi tsiku.”—LUKA 9:23.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza tonsefe kuganizira mmene kudzipereka kumakhudzira mmene timachitira zinthu pa moyo wathu. Ithandizanso makamaka amene angobatizidwa kumene kuti apitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova.
1-2. Kodi munthu amapeza madalitso ati akabatizidwa?
TIMASANGALALA tikabatizidwa n’kukhala m’banja la Yehova. Anthu amene anabatizidwa angagwirizane ndi zimene Davide analemba, pomwe anati: “Wosangalala ndi munthu amene inu Yehova mwamusankha nʼkumubweretsa pafupi ndi inu, kuti akhale mʼmabwalo anu.”—Sal. 65:4.
2 Sikuti Yehova amangolola aliyense kuti alowe m’mabwalo ake. Monga mmene taonera mu nkhani yapita ija, iye amasankha kuyandikira anthu amene asonyeza kuti akufunitsitsa kukhala naye pa ubwenzi. (Yak. 4:8) Ndiye mukadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, mumakhala naye pa ubwenzi wapadera. Zikatero mungakhale otsimikiza kuti mukabatizidwa iye ‘adzakukhuthulirani madalitso mpaka simudzasowa kanthu.’—Mal. 3:10; Yer. 17:7, 8.
3. Kodi Akhristu amene anadzipereka ndiponso kubatizidwa amakhala ndi udindo waukulu uti? (Mlaliki 5:4, 5)
3 N’zoona kuti kubatizidwa chimangokhala chiyambi chabe. Koma mukabatizidwa, mumayenera kuchita zonse zomwe mungathe kuti muzikwaniritsa lonjezo lanu ngakhale pamene mukukumana ndi mayesero. (Werengani Mlaliki 5:4, 5.) Monga wophunzira wa Yesu, mumafunika kutengera chitsanzo chake komanso kumvera malamulo ake mosamala kwambiri. (Mat. 28:19, 20; 1 Pet. 2:21) Nkhaniyi ikuthandizani kuona mmene mungachitire zimenezi.
‘PITIRIZANI KUTSATIRA’ YESU NGAKHALE PAMENE MUKUKUMANA NDI MAYESERO
4. Kodi ophunzira a Yesu amanyamula “mtengo wozunzikirapo” m’njira iti? (Luka 9:23)
4 Musamaganize kuti mukabatizidwa simuzikumana ndi mavuto. Ndipotu Yesu anafotokoza momveka bwino kuti ophunzira ake ayenera kunyamula ‘mtengo wawo wozunzikirapo.’ Komanso iwo ayenera kumachita zimenezi “tsiku ndi tsiku.” (Werengani Luka 9:23.) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza kuti nthawi zonse otsatira ake azivutika? Ayi sichoncho. Iye ankangotanthauza kuti kuwonjezera pa madalitso amene azipeza, azikumananso ndi mavuto. Ena mwa mavutowo angakhale aakulu.—2 Tim. 3:12.
5. Kodi Yesu analonjeza kuti amene amadzimana zinthu zina adzapeza madalitso ati?
5 N’kutheka kuti inuyo mwakumana kale ndi mavuto monga kutsutsidwa ndi achibale, kapenanso mwalolera kuti musakhale ndi zinthu zambiri n’cholinga choti muziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. (Mat. 6:33) Ngati ndi choncho, dziwani kuti Yehova amaona zimene mukuchita pomutumikira mokhulupirika. (Aheb. 6:10) Mwina inunso mwaona kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu akuti: “Palibe amene wasiya nyumba, azichimwene, azichemwali, amayi, abambo, ana kapena minda chifukwa cha ine komanso chifukwa cha uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100 mʼnthawi ino. Iye adzapeza nyumba, azichimwene, azichemwali, amayi, ana ndi minda, komanso adzazunzidwa, ndipo mʼnthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha.” (Maliko 10:29, 30) Madalitso amene mungapeze ndi aakulu kuposa zimene munadzimana.—Sal. 37:4.
6. N’chifukwa chiyani pambuyo pobatizidwa muyenera kupitiriza kulimbana ndi zimene ‘thupi lanu limalakalaka’?
6 Pambuyo pobatizidwa, muyenera kupitirizabe kulimbana ndi zimene ‘thupi limalakalaka.’ (1 Yoh. 2:16) Zimenezi zili choncho chifukwa monga mbadwa ya Adamu, mudakali wochimwa. Nthawi zina mungamamve ngati mmene mtumwi Paulo anamvera. Iye analemba kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi malamulo a Mulungu, koma ndimaona lamulo lina mʼthupi langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga nʼkundichititsa kukhala kapolo wa lamulo la uchimo limene lili mʼthupi langa.” (Aroma 7:22, 23) Mungamafooke chifukwa cha zinthu zoipa zimene mumalakalaka. Komabe, kuganizira zimene munalonjeza kwa Yehova pamene munkadzipereka kungakupatseni mphamvu kuti mupitirize kulimbana ndi mayesero. Zoona n’zakuti lonjezo lanu la kudzipereka ndi limene limakuthandizani mukakumana ndi mayesero. Kodi limakuthandizani bwanji?
7. Kodi kudzipereka kwanu kwa Yehova kumakuthandizani bwanji kuti mupitirize kukhala wokhulupirika?
7 Mukadzipereka kwa Yehova mumadzikana nokha. Zimenezi zikutanthauza kuti mumakana zolakalaka komanso zofuna zanu zomwe mukuona kuti sizingasangalatse Yehova. (Mat. 16:24) Choncho ngati mutakumana ndi mayesero, simudzachedwa ndi kuganizira zomwe mungachite. Mudzakhala mukudziwa kale chochita, chomwe ndi kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Mudzafunitsitsa kupitiriza kusangalatsa Yehova. Pochita zimenezo, mudzafanana ndi Yobu. Ngakhale kuti anakumana ndi mayesero aakulu, iye ananena motsimikiza kuti: “sindidzasiya kukhala wokhulupirika.”—Yobu 27:5.
8. Kodi kuganizira zimene munalonjeza Yehova m’pemphero podzipereka kungakuthandizeni bwanji kukana mayesero?
8 Kuganizira zimene munalonjeza Yehova podzipereka kungakupatseni mphamvu kuti muthe kukana mayesero alionse. Mwachitsanzo, kodi mungayambe kukopana ndi mwamuna kapena mkazi wamwini wake? Ayi simungatero, chifukwa munalonjeza kale Yehova kuti simungachite zinthu ngati zimenezo. Ngati simungalole kuti maganizo oipa akhazikike mumtima mwanu, pambuyo pake simudzavutika ndi kulimbana nawo kuti muwathetse. ‘Mudzapatuka’ kuti ‘musatengere zochita za anthu oipa.’—Miy. 4:14, 15.
9. Kodi kuganizira zimene munalonjeza m’pemphero podzipereka, kungakuthandizeninso bwanji kuti muziika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba?
9 Bwanji ngati mutapatsidwa mwayi wa ntchito imene ingamakulepheretseni kupezeka pamisonkhano nthawi zonse? Apanso mungadziwiretu chochita. Tikutero chifukwa ntchitoyo isanapezeke munali mutasankha kale kuti simudzagwira ntchito ngati imeneyo. Choncho simudzavomera ntchitoyo mukumaganiza kuti mupeza njira yakuti muziikabe zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba. Kuganizira mmene Yesu analili wotsimikiza kuti azisangalatsa Atate wake, kudzakuthandizani kuti mwamsanga komanso molimba mtima mukane zilizonse zomwe mukudziwa kuti sizingasangalatse Mulungu, yemwe munadzipereka kwa iye.—Mat. 4:10; Yoh. 8:29.
10. Pambuyo poti mwabatizidwa, kodi Yehova adzakuthandizani bwanji kuti ‘mupitirize kutsatira’ Yesu?
10 Mayesero amene mumakumana nawo amakupatsani mwayi woti musonyeze kuti ndinu ofunitsitsa ‘kupitiriza kutsatira’ Yesu. Ndipo mungakhale otsimikiza kuti Yehova adzakuthandizani. Baibulo limati: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.”—1 Akor. 10:13.
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUPITIRIZE KUTSATIRA YESU
11. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe ingatithandize kupitiriza kutsatira Yesu? (Onaninso chithunzi.)
11 Yesu ankatumikira Yehova ndi mtima wonse ndipo pemphero linamuthandiza kuti apitirize kukhala naye pa ubwenzi. (Luka 6:12) Ndipotu njira yabwino yopitirizira kutsatira Yesu pambuyo pobatizidwa ndi kukhala ndi chizolowezi chochita zinthu zomwe zingakuthandizeni kuyandikira Yehova. Baibulo limati: “Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.” (Afil. 3:16) Nthawi zambiri muzimva zimene zachitikira abale ndi alongo anu omwe ayesetsa kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Mwina iwo analowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu kapenanso anasamukira kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Inunso mungathe kudziikira zolinga ngati zimenezi. Anthu a Yehova amafunitsitsa kuti azichita zambiri pomutumikira. (Mac. 16:9) Koma bwanji ngati inuyo simungakwanitse kuchita zimenezi panopa? Musamaganize kuti ndinu olephera poyerekezera ndi amene akwanitsa kuchita zimenezo. Chofunika kwambiri n’chakuti mukupitirizabe kutumikira Mulungu. (Mat. 10:22) Musamayiwale kuti Yehova amasangalala ndi zimene mumachita pomutumikira mogwirizana ndi luso lanu komanso mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Imeneyi ndi njira yofunika kwambiri yomwe mungapitirizire kutsatira Yesu pambuyo pobatizidwa.—Sal. 26:1.
12-13. Kodi mungatani ngati simukutumikiranso Yehova mwakhama ngati kale? (1 Akorinto 9:16, 17) (Onaninso bokosi lakuti “Pitirizani Kuthamanga.”)
12 Kodi mungatani ngati mwayamba kuona kuti mapemphero anu si ochokeranso mumtima kapenanso simukusangalala ndi ntchito yolalikira ngati kale? Bwanji ngati simukusangalalanso mukamawerenga Baibulo? Ngati zimenezi zitayamba kukuchitikirani pambuyo pobatizidwa, musamaganize kuti Yehova wasiya kukuthandizani ndi mzimu wake. Monga munthu yemwe si wangwiro, nthawi ndi nthawi mungamasinthe mmene mumamvera. Ngati mwayamba kuona kuti simukuchitanso khama muziganizira chitsanzo cha mtumwi Paulo. Ngakhale kuti ankayesetsa kutsanzira Yesu, ankadziwa kuti si nthawi zonse pomwe angachite zimene akulakalaka. (Werengani 1 Akorinto 9:16, 17.) Iye anati: “Ngakhale nditachita mokakamizika, ndinebe woyangʼanira mogwirizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.” M’mawu ena tingati Paulo anali wotsimikiza kukwaniritsa utumiki wake posatengera mmene akumvera.
13 Mofanana ndi zimenezi, inunso musamalole kuti muzisankha zochita potengera mmene mukumvera. Muzitsimikiza kuchita zoyenera ngakhale kuti si zimene mungakonde kuchita. Mukamachita zoyenera nthawi zonse mungayambe kusintha mmene mumamvera. Mukapitiriza kukhala ndi chizolowezi chochita zinthu zokhudza kulambira zidzakuthandizani kupitiriza kutsatira Yesu pambuyo pobatizidwa. Khama lanu potumikira Yehova lingalimbikitsenso abale ndi alongo anu.—1 Ates. 5:11.
“PITIRIZANI KUDZIYESA”
14. Kodi nthawi zonse muyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (2 Akorinto 13:5)
14 Zingakhalenso zothandiza ngati pambuyo pobatizidwa mungapitirize kumadzifufuza. (Werengani 2 Akorinto 13:5.) Nthawi ndi nthawi, muziona zimene mukuchita pa moyo wanu kuti muone ngati mumapemphera tsiku lililonse, kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. Muziganizira zimene mungachite kuti muzisangalala ndi zinthu zokhudza kulambirazi. Mwachitsanzo, muzidzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi ndingathe kufotokozera ena mfundo zoyambirira za m’Baibulo? Kodi pali zimene ndingachite kuti ndizisangalala ndi ntchito yolalikira? Kodi mapemphero anga amakhala ochokera mumtima komanso amasonyeza kuti ndimadalira kwambiri Yehova? Kodi nthawi zonse ndimapezeka pamisonkhano? Kodi ndingasinthe zinthu ziti kuti ndizimvetsera mwatcheru komanso kuyankha pamisonkhano?’
15-16. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene m’bale wina anachita pokana mayesero?
15 Mungachite bwinonso kudzifufuza moona mtima kuti mudziwe zofooka zanu. Mungamvetse zimenezi poona zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Robert. Iye anafotokoza kuti: “Ndili ndi zaka za m’ma 20, ndinapeza ntchito yomwe ndinkagwira kwa masiku ochepa. Tsiku lina nditaweruka, mtsikana yemwe ndinkagwira naye ntchito anandiitanira kunyumba kwake. Iye anandiuza kuti tikakhala tokhatokha ndipo tikasangalala kwambiri. Poyamba ndinapereka zifukwa zosamveka, koma kenako ndinakana n’kufotokoza chifukwa chake.” Robert anakana mayeserowo ndipo anachita bwino kwambiri. Komabe pambuyo pake anaona kuti akanatha kuchita bwino kwambiri pa zimene zinamuchitikirazo. Iye anavomereza kuti: “Sindinakane mwamphamvu komanso mwamsanga ngati mmene Yosefe anachitira pokana zimene mkazi wa Potifara ankafuna. (Gen. 39:7-9) Ndipotu ndimadabwa kuti zinanditengera nthawi kuti ndikane. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti ndinkafunika kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova.”
16 Inunso mungachite bwino kumadzifufuza ngati mmene Robert anachitira. Ngakhale mutapambana mayesero enaake, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi panatenga nthawi yaitali bwanji kuti ndikane mayeserowa?’ Ngati mukuona kuti pali pena pomwe mukufunika kusintha, musafooke. Muzisangalala kuti mwazindikira vuto limenelo. Muziipempherera nkhaniyo ndipo muzichita zimene zingakuthandizeni kuti muzitsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino.—Sal. 139:23, 24.
17. Kodi zimene zinachitikira Robert zinakhudza bwanji dzina la Yehova?
17 Pali chinanso chomwe tingaphunzire kuchokera pa zimene zinachitikira Robert. Iye anapitiriza kunena kuti: “Nditakana kupita kunyumba kwa mtsikanayo, iye anandiuza kuti, ‘Wakhoza mayeso.’ Nditamufunsa zimene ankatanthauza anandiuza kuti mnzake wina yemwe poyamba anali wa Mboni anamuuza kuti achinyamata onse a Mboni amakhala moyo wachiphamaso, ndipo angachite zoipa ngati mpata utapezeka. Ndiye iye anamuuza mnzakeyo kuti ayeserera zimenezi pa ine. Ndinasangalala kwambiri nditaona kuti ndachititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe.”
18. Kodi mukufunitsitsa kupitiriza kuchita chiyani pambuyo pobatizidwa? (Onaninso bokosi lakuti “Nkhani Zomwe Zingakuthandizeni.”)
18 Pamene munadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, munasonyeza kuti mumafuna kuyeretsa dzina lake zivute zitani. Ndipotu Yehova amadziwa mavuto amene mukukumana nawo ndiponso mayesero amene mukulimbana nawo. Iye adzakudalitsani chifukwa choyesetsa kukhalabe okhulupirika. Musamakayikire kuti pogwiritsa ntchito mzimu wake, iye adzakupatsani mphamvu yochitira zimenezo. (Luka 11:11-13) Choncho mothandizidwa ndi Yehova, mudzakwanitsa kupitiriza kutsatira Yesu pambuyo pobatizidwa.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi Akhristu amanyamula bwanji ‘mtengo wozunzikirapo tsiku ndi tsiku’?
Kodi mungatani kuti ‘mupitirize kutsatira’ Yesu pambuyo pobatizidwa?
Kodi kuganizira zimene munalonjeza m’pemphero podzipereka, kungakuthandizeni bwanji kukhalabe okhulupirika?
NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso