Yehova Ndiye Ambuye Wathu Wamkulu Koposa
“Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.”—SAL. 73:28.
1. Kodi pamene Paulo ankanena mawu a pa 1 Akorinto 7:31 ayenera kuti ankayerekezera dzikoli ndi chiyani?
MTUMWI Paulo ananena kuti: “Zochitika za padzikoli zikusintha.” (1 Akor. 7:31) Pamenepa, zikuoneka kuti Paulo anali kuyerekezera dzikoli ndi bwalo lochitira zisudzo limene ochita sewero akuchita mbali zawo monga anthu abwino kapena anthu oipa mpaka nthawi yosintha zochitikazo itakwana.
2, 3. (a) Kodi nkhani yotsutsa ulamuliro wa Yehova tingaiyerekezere ndi chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
2 Zinthu zimene zikuchitika masiku ano zili ngati sewero limene nkhani yake ndi yofunika kwambiri ndipo ikukukhudzani inuyo. Nkhani yake yaikulu ndi yotsimikizira kuti Yehova Mulungu ndiye woyenera kulamulira. Tingayerekezere nkhani yochitika m’seweroli ndi zinthu zimene zingachitike m’dziko lina. Tinene kuti m’dzikolo muli boma lovomerezeka limene limakhazikitsa bata. Koma mulinso gulu la zigawenga limene likuchita chinyengo, nkhanza ndiponso likupha anthu kuti lilamulire. Gulu la zigawengalo likutsutsa boma lovomerezeka ndipo likuyesetsa kukopa nzika za m’dzikolo kuti zisakhale zokhulupirika ku boma lawo.
3 Izi n’zimene zikuchitikanso m’chilengedwe chonse. Pali boma lovomerezeka lokhazikitsidwa ndi “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.” (Sal. 71:5) Koma anthu ali pa ngozi chifukwa cha gulu la zigawenga lomwe mtsogoleri wake ndi “woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Gululi likutsutsa boma lovomerezeka la Mulungu ndipo likuyesetsa kukopa anthu kuti asakhale okhulupirika ku ulamuliro wa Mulungu. Kodi nkhani imeneyi inayamba bwanji? N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti izi zichitike? Kodi aliyense payekha ayenera kuchita chiyani?
Mbali za Nkhani Imeneyi
4. Kodi nkhani imene ikuchitika m’chilengedwechi ili ndi mbali ziwiri ziti zimene zikuyendera limodzi?
4 Nkhani imene ikuchitikayi ili ndi mbali ziwiri zimene zikuyendera limodzi. Mbali yoyamba ndi yokhudza ulamuliro wa Yehova ndipo mbali yachiwiri ndi yokhudza kukhulupirika kwa anthu. M’Malemba nthawi zambiri Yehova amatchedwa “Ambuye Wamkulu Koposa.” Mwachitsanzo, wamasalimo anaimba nyimbo yosonyeza kuti amakhulupirira Mulungu ndi mtima wonse. Iye anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.” (Sal. 73:28) Yehova Mulungu ndi Ambuye Wamkulu Koposa wina aliyense m’chilengedwechi. Choncho tili ndi zifukwa zabwino zomuonera kuti ndi Mulungu Wamkulukulu.—Dan. 7:22.
5. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti Yehova ndi woyenera kulamulira?
5 Yehova Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. Choncho ndi woyenera kulamulira dzikoli ndiponso chilengedwe chonse. (Werengani Chivumbulutso 4:11.) Yehova ndi Woweruza, Wopereka Malamulo ndiponso Mfumu ya chilengedwe chonse. (Yes. 33:22) Popeza Mulungu ndi amene anatilenga ndipo moyo wathu umadalira iye, tiyenera kumuona kuti ndi Ambuye wathu Wamkulu. Tingasonyeze kuti Yehova ndi woyenera kulamulira ngati nthawi zonse timakumbukira kuti “Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba. Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.”—Sal. 103:19; Mac. 4:24.
6. Kodi munthu wa mtima wosagawanika ndi wotani?
6 Kuti tisonyeze kuti tili kumbali ya Ulamuliro wa Yehova tiyenera kumutumikira ndi mtima wosagawanika. Munthu wa mtima wotere amakhala wopanda cholakwa komanso woongoka mtima. Umu ndi mmene Yobu analili.—Yobu 1:1.
Mmene Nkhaniyi Inayambira
7, 8. Kodi Satana anatsutsa bwanji zoti Yehova ndi woyenera kulamulira?
7 Zaka zoposa 6,000 zapitazo, mngelo wina anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Iye anachita zimenezi chifukwa chofuna kulambiridwa ndiponso kudzikonda. Iye anakopa Adamu ndi Hava kuti asiye kukhala okhulupirika ku ulamuliro wa Mulungu ndipo anaipitsa dzina la Yehova mwa kunena kuti Yehovayo ananena bodza. (Werengani Genesis 3:1-5.) Mngelo wopandukayu anadzakhala Mdani wamkulu wotchedwa Satana (Wotsutsa), Mdyerekezi (Woneneza), njoka (wonyenga) ndi chinjoka (wakupha).—Chiv. 12:9.
8 Apa Satana anayambitsa gulu loukira. Kodi izi zitachitika, Ambuye wathu Wamkulu Yehova anayenera kuchita chiyani? Kodi akanangowononga Satana, Adamu ndi Hava? Iye analidi ndi mphamvu zochitira zimenezi ndipo izi zikanathetsa kukayikira zoti Mulungu ndi wamphamvu kwambiri. Zikanasonyezanso kuti Yehova ananena zoona pamene anauza anthuwo kuti ngati samvera lamulo lake adzafa. Koma n’chifukwa chiyani Mulungu sanachite zimenezi?
9. Kodi Satana anatsutsa zinthu ziti?
9 Pamene ananamiza Adamu ndi Hava kuti achimwire Mulungu, Satana anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira anthu. Mwa kukopa makolo athu oyambirirawa kuti asamvere Mulungu, Satana anatsutsa zoti anthu ndi angelo angakhale okhulupirika kwa Mulungu. Pa nthawi ya Yobu, yemwe anali wokhulupirika ku ulamuliro wa Yehova, Satana ananena kuti akhoza kuchititsa anthu onse kusiya kumvera Mulungu.—Yobu 2:1-5.
10. Polola zochita za Satana, kodi Mulungu wapereka mpata wotani?
10 Yehova walola zochita za Satana pofuna kuti Satanayo akhale ndi nthawi yotsimikizira zimene anatsutsazo. Mulungu wapatsanso anthu mpata woti asonyeze kuti ndi okhulupirika ku ulamuliro wake. Kodi zotsatira zake ndi zotani pa zaka zonsezi? Satana wapanga gulu lamphamvu la zigawenga. Koma Yehova adzawononga Mdyerekezi ndi gulu lakeli ndipo izi zidzasonyezadi kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira. Yehova Mulungu sanakayikire zotsatira za nkhani imeneyi moti anthu atangomupandukira m’munda wa Edene, iye ananeneratu zimene zidzachitike.—Gen. 3:15.
11. Kodi anthu ambiri achita zotani pa nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova?
11 Anthu ambiri akhala akukhulupirira Yehova ndipo amamutumikira ndi mtima wosagawanika. Iwo amasonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova ndiponso amafuna kuti dzina lake liyeretsedwe. Ena mwa anthu amenewa ndi Abele, Inoki, Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Davide, Yesu, Akhristu oyambirira ndiponso anthu mamiliyoni ambiri okhulupirika a masiku ano. Dzina la Yehova laipitsidwa ndi Mdyerekezi amene amanena monyada kuti akhoza kupatutsa anthu onse kuti asamamvere Mulungu. Koma anthu amene ali kumbali ya ulamuliro wa Yehovawa, amasonyeza kuti Satana ndi wabodza ndipo amathandiza kuyeretsa dzina la Yehova.—Miy. 27:11.
Tikudziwa Mmene Nkhaniyi Idzathere
12. Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu sadzalekerera zoipa mpaka kalekale?
12 Sitikukayikira kuti posachedwapa Yehova adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira. Tikutero chifukwa chakuti iye sangalole kuti zinthu zoipa zizingochitikabe ndipo tikudziwa kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Yehova anawononga anthu oipa pa nthawi ya Chigumula. Iye anawononga mizinda ya Sodomu ndi Gomora komanso Farao ndi asilikali ake. Nayenso Sisera ndi asilikali ake komanso Sanakeribu ndi asilikali a Asuri sanathe kulimbana ndi Wam’mwambamwamba. (Gen. 7:1, 23; 19:24, 25; Eks. 14:30, 31; Ower. 4:15, 16; 2 Maf. 19:35, 36) Choncho n’zosakayikitsa kuti Yehova Mulungu sadzalekerera mpaka kalekale anthu amene salemekeza dzina lake ndiponso amene amachitira nkhanza Mboni zake. Ndipotu panopa tikuona chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu komanso cha mapeto a nthawi yoipa ino.—Mat. 24:3.
13. Kodi tingapewe bwanji kuwonongedwa pamodzi ndi adani a Yehova?
13 Kuti tisadzawonongedwe limodzi ndi adani a Mulungu, tiyenera kukhala okhulupirika ku ulamuliro wa Yehova. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero mwa kupewa kukhala kumbali ya ulamuliro woipa wa Satana ndiponso kukana kumvera anthu amene ali kumbali ya Satanayo chifukwa cha mantha. (Yes. 52:11; Yoh. 17:16; Mac. 5:29) Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tili ku mbali ya Atate wathu wakumwamba pa nkhani ya ulamuliro. Timakhalanso ndi chiyembekezo chodzapulumuka pamene Yehova azidzayeretsa dzina lake komanso kusonyeza kuti iye ndi Mfumu ya Chilengedwe chonse.
14. Kodi Baibulo limafotokoza zinthu ziti?
14 Baibulo limafotokoza mbiri ya anthu ndiponso nkhani ya ulamuliro wa Yehova. Machaputala atatu oyambirira a m’buku la Genesis amafotokoza za kulengedwa kwa zinthu ndi anthu ndiponso kuchimwa kwa anthuwo. Ndipo machaputala atatu omalizira a m’buku la Chivumbulutso amasonyeza mmene anthu adzakhalirenso angwiro. Buku la Genesis limafotokoza chiyambi cha zochita za Satana ndiponso mmene uchimo unalowera m’dziko. Ndipo machaputala omalizira a buku la Chivumbulutso amasonyeza mmene Mulungu adzachotsere zinthu zoipa ndiponso kuwononga Mdyerekezi. Amasonyezanso kuti chifuniro cha Mulungu chidzachitika, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. Baibulo limafotokoza chimene chinayambitsa uchimo ndi imfa ndiponso mmene Mulungu adzachotsere zinthu zimenezi padziko, n’kubweretsa chimwemwe chosaneneka ndi moyo wosatha kwa anthu okhulupirika.
15. Kodi tingatani kuti zinthu zidzatiyendere bwino nkhani ya ulamuliro ikamadzathetsedwa?
15 Posachedwapa zochitika za padzikoli zidzasinthiratu. Nkhani yonse yokhudza ulamuliro idzatha. Ulamuliro wa Satana udzathetsedwa ndipo pa mapeto pake iye adzawonongedwa. Pa nthawiyi chifuniro cha Mulungu chidzachitikadi. Koma kuti zinthu zidzatiyendere bwino pa nthawiyi ndiponso kuti tidzasangalale ndi madalitso amene talonjezedwa m’Mawu a Mulungu, tiyenera kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova masiku anowa. N’zosatheka kukhala opanda mbali pa nkhani imeneyi. Kuti tidzathe kunena kuti “Yehova ali kumbali yanga” ifenso tiyenera kukhalabe kumbali yake.—Sal. 118:6, 7.
N’zotheka Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika
16. Tikudziwa bwanji kuti n’zotheka kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika?
16 Anthufe tikhoza kusonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Yehova ndiponso kumutumikira ndi mtima wosagawanika. Tikutero chifukwa chakuti mtumwi Paulo analemba kuti: “Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene amagwera anthu ena. Koma Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” (1 Akor. 10:13) Kodi mayesero amene Paulo ananena amachokera kuti, nanga Mulungu amapereka bwanji njira yopulumukira?
17-19. (a) Kodi Aisiraeli anagonja ndi mayesero ati? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zotheka kutumikirabe Yehova ndi mtima wosagawanika?
17 Zimene zinachitikira Aisiraeli m’chipululu zimasonyeza kuti anthufe ‘timayesedwa’ kuti tisamvere malamulo a Mulungu ndi zinthu zimene timakumana nazo pa moyo wathu. (Werengani 1 Akorinto 10:6-10.) Aisiraeli akanatha kupewa mayesero, koma ankalakalaka “zinthu zoipa” pamene Yehova anawapatsa mozizwitsa zinziri zomwe akanatha kudya mwezi wathunthu. Ngakhale kuti anthuwo anakhala osadya nyama kwa nthawi yaitali, Mulungu anawapatsa mana okwanira. Koma iwo anagonja pa mayeserowo n’kuyamba kusonkhanitsa mwadyera zinzirizo.—Num. 11:19, 20, 31-35.
18 Izi zisanachitike, Mose anapita kuphiri la Sinai kukalandira Chilamulo. Pa nthawiyi, Aisiraeli anayamba kulambira fano la mwana wa ng’ombe limene anapanga ndiponso kusangalala m’njira yosayenera. Iwo sanathe kudziletsa chifukwa chakuti mtsogoleri wawo kunalibe. (Eks. 32:1, 6) Atangotsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Aisiraeli ambiri anakopedwa ndi akazi a ku Mowabu ndipo anachita nawo chiwerewere. Pa nthawi imeneyi, Aisiraeli masauzande ambiri anaphedwa chifukwa cha machimo awo. (Num. 25:1, 9) Nthawi zina Aisiraeli atayesedwanso anayamba kung’ung’udza komanso kukhala ndi mtima wopanduka. Ndipo nthawi ina iwo anayamba kulankhula motsutsana ndi Mose komanso Mulungu. (Num. 21:5) Aisiraeli anang’ung’udzanso pamene Kora, Datani, Abiramu ndi anzawo ena oipa anaphedwa poganiza kuti kupha anthuwo sichinali chilungamo. Izi zinachititsa kuti Aisiraeli 14,700 aphedwe ndi mliri wochokera kwa Mulungu.—Num. 16:41, 49.
19 Mayesero onse amene tatchulawa anali oti Aisiraeli akanatha kuwapewa. Anthuwo anagonja poyesedwa chifukwa chakuti anasiya kukhulupirira Yehova ndipo anamuiwala. Iwo anaiwalanso zoti iye ndi wachikondi ndiponso zochita zake zonse ndi zachilungamo. Mofanana ndi Aisiraeli, mayesero amene timakumana nawo si osiyana ndi amene amagwera anthu ena. Tikamachita khama kuwakana ndiponso kudalira Mulungu kuti atithandize, tikhoza kukhalabe ndi mtima wosagawanika. Sitiyenera kukayikira zimenezi chifukwa chakuti “Mulungu ndi wokhulupirika” ndipo sadzalola kuti ‘tiyesedwe kufika pamene sitingapirire.’ Yehova sangalole kuti tiyesedwe kufika pamene sitingathe kuchita chifuniro chake.—Sal. 94:14.
20, 21. Kodi Mulungu amapereka bwanji “njira yopulumukira” tikamayesedwa?
20 Yehova amapereka “njira yopulumukira” mwa kutipatsa mphamvu yotithandiza kuti tikane mayesero. Mwachitsanzo, anthu angatizunze n’cholinga choti tisiye chikhulupiriro chathu. Izi zikachitika tikhoza kuganiza zoti tingololera zofuna zawo kuti tipewe kumenyedwa, kuzunzidwa kapenanso kuphedwa kumene. Koma malinga ndi mawu olimbikitsa amene Paulo anauziridwa kulemba pa 1 Akorinto 10:13, tikudziwa kuti mayesero athu ndi a kanthawi kochepa. Yehova sadzalola kuti mayeserowo apitirire n’kufika poti sitingathe kukhalabe okhulupirika kwa iye. Mulungu angalimbitse chikhulupiriro chathu ndiponso kutipatsa mphamvu kuti tizimutumikirabe ndi mtima wosagawanika.
21 Yehova amatithandiza ndi mzimu wake woyera. Mzimuwu umatikumbutsanso mfundo za m’Malemba zimene zingatithandize kuti tisagonje poyesedwa. (Yoh. 14:26) Chifukwa cha zimenezi, sitipusitsidwa n’kuyamba kutsatira njira yolakwika. Mwachitsanzo, tikudziwa bwino nkhani ya ulamuliro wa Yehova ndi ya kukhulupirika kwa anthu. Chifukwa chodziwa bwino zimenezi, anthu ambiri athandizidwa ndi Mulungu kukhalabe okhulupirika mpaka imfa. Sikuti imfa yawo inali njira yopulumukira koma Yehova anawapatsa mphamvu kuti apirire mpaka mapeto ndiponso kuti asagonje. Iye akhoza kuchitanso chimodzimodzi ndi ifeyo. Ndipotu amagwiritsanso ntchito angelo ake okhulupirika amene ‘amatumidwa kukatumikira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo.’ (Aheb. 1:14) Nkhani yotsatira isonyeza kuti anthu okhulupirika okha ndi amene adzakhale ndi mwayi wokhala kumbali ya ulamuliro wa Mulungu mpaka muyaya. N’zotheka kukhala m’gulu la anthu amenewa ngati tipitiriza kukhalabe okhulupirika kwa Yehova n’kumamuona kuti ndi Ambuye wathu Wamkulu Koposa.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kuvomereza Yehova kukhala Ambuye wathu Wamkulu Koposa?
• Kodi kukhalabe ndi mtima wosagawanika kumatanthauza chiyani?
• Kodi tikudziwa bwanji kuti posachedwapa Yehova adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira?
• Malinga ndi lemba la 1 Akorinto 10:13, n’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zotheka kutumikirabe Mulungu ndi mtima wosagawanika?
[Chithunzi patsamba 24]
Satana ananyenga Adamu ndi Hava kuti akhale osakhulupirika kwa Yehova
[Chithunzi patsamba 26]
Musasiye kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova