Nkuululiranji Choipa?
“YEMWE amaulula nkhani amakhala mdani wa anthu,” ena amanena tero ku West Africa. Ndizo zinamchitikira Olu pamene adadzudzula mkulu wake kuti wagona ndi mlongo wake. “Ndiwe wabodza!” anakalipa wamkuluyo. Kenaka anammenya Olu koopsa, kumpirikitsa panyumbapo, ndi kutentha zovala zonse za Olu. Anthu a pamudzipo anakhalira kumbuyo wamkuluyo. Poti sanali wolandiridwanso m’mudzimo, Olu anachoka. Ndi pambuyo poti mtsikanayo anapezeka ndi mimba pamene anthu anazindikira kuti Olu amanena zoona. Wamkuluyo anapepesa, ndipo Olu anayanjidwanso pamudzipo. Komatu zinthu zikadachitikira mwina. Olu akanaphedwa.
Ndithudi, awo amene sakonda Yehova sasangalala pamene zolakwa zawo zivumbulidwa. Chizoloŵezi cha anthu ochimwa ndicho kukana chidzudzulo ndi kuda aliyense amene awadzudzula. (Yerekezerani ndi Yohane 7:7.) Motero nzosadabwitsa kuti ambiri amakhala chete ngati miyala mmalo moulula zolakwa za ena kwa amene ali ndi udindo woziwongolera.
Kuyamikira Kufunika kwa Chidzudzulo
Komabe, pakati pa anthu a Yehova, chidzudzulo amachionera mwina. Amuna ndi Akazi okonda Mulungu amathokoza kwambiri makonzedwe omwe Yehova wakonza othandiza olakwa mumpingo wachikristu. Amaona chilango chimenechi monga chisonyezero cha chikondi chake.—Ahebri 12:6-11.
Zochitika m’moyo wa Mfumu Davide zikhoza kutipatsa chitsanzo. Ngakhale kuti anali wolungama kuyambira pa ubwana wake, inafika nthaŵi pamene anachita tchimo lalikulu. Choyamba, anachita chigololo. Kenaka, poyesa kubisa tchimo lakelo, anakonza chiwembu chopha mwamuna wa mkaziyo. Koma Yehova anaulula tchimo la Davide kwa mneneri Natani, amene anatsutsa Davide za nkhaniyo molimba mtima. Mwa kugwiritsira ntchito fanizo lamphamvu, Natani anafunsa Davide chimene munthu wolemera ayenera kuchitidwa amene anali ndi nkhosa zambiri koma kutamfikira alendo anatenga ndi kupha kankhosa kapamtima kamodzi kokha ka munthu wosauka. Davide, yemwe kale anali mbusa, ananyansidwa ndipo anakwiya. Iye anati: “Munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha.” Kenaka Natani anatembenuzira fanizolo kwa Davide, akumati: “Munthuyo ndi inu nomwe.”—2 Samueli 12:1-7.
Davide sanamkwiyire Natani; komanso sanayese kudzichinjiriza ngakhale kuyankha mwaukali. M’malo mwake, chidzudzulo cha Natanicho chinamdzutsira chikumbumtima. Atalaswa mtima, Davide anavomera kuti: “Ndinachimwira Yehova.”—2 Samueli 12:13.
Pamene Natani anaulula tchimo la Davide ndi kumpatsa chidzudzulo cha Mulungu, panakhala zotsatira zabwino. Ngakhale kuti Davide sanachinjirizidwe ku zotsatira za kulakwa kwake, analapa ndi kuyanjidwanso ndi Yehova. Kodi Davide anamva bwanji za chidzudzulo chimenechi? Iye analemba kuti: “Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane.”—Salmo 141:5.
Masiku anonso, atumiki a Yehova akhoza kugwera m’machimo aakulu, ngakhale awo amene akhala okhulupirika kwa zaka zambiri. Pozindikira kuti akulu akhoza kuthandiza, ambiri amauona monga mwaŵi kuwafikira kupempha chithandizo. (Yakobo 5:13-16) Koma nthaŵi zina wochimwa angayese kubisa tchimo lake, monga momwe inachitira Mfumu Davide. Kodi tiyenera kuchitanji ngati tadziŵa za tchimo lalikulu mumpingo?
Kodi ndi Udindo wa Yani?
Akulu akazindikira zakuti pali tchimo lalikulu, amamfikira munthuyo kuti amthandize ndi kumuongolera. Ndi udindo wa akulu kuweruza oterowo mumpingo wachikristu. Mwa kuonetsetsa kakhalidwe kake kauzimu, amathandiza ndi kuchenjeza aliyense amene akuchita zosayenera kapena kutsatira njira zoipa.—1 Akorinto 5:12, 13; 2 Timoteo 4:2; 1 Petro 5:1, 2.
Koma bwanji ngati sindinu mkulu ndipo mwaona Mkristu wina akuchita tchimo lalikulu? Njira zoti mutsate zimapezeka mu Chilamulo chimene Yehova anapereka ku mtundu wa Israyeli. Chilamulo chimati ngati munthu wina waona machitidwe akupandukira, kusonkhezera ena kuti apanduke, mbanda, kapena maupandu ena oopsa, unali udindo wake kuulula ndi kupereka umboni pa zimene adziŵa. Levitiko 5:1 amati: “Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mawu akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziŵa, koma osaulula, azisenza mphulupulu yake.”—Yerekezerani ndi Deuteronomo 13:6-8; Estere 6:2; Miyambo 29:24.
Ngakhale kuti sali pansi pa Chilamulo cha Mose, lerolino Akristu akhoza kutsatira mapulinsipulo amenewo. (Salmo 19:7, 8) Choncho ngati mwadziŵa kuti Mkristu mnzanu wachita tchimo lalikulu, kodi muyenera kuchitanji?
Momwe Mungachitire
Choyamba, nkofunika kuonetsetsa kuti pali zifukwa zokwanira zokhulupirira kuti tchimo lalikulu lachitikadi. “Usachitire mnzako umboni womtsutsa opanda chifukwa,” anatero munthu wanzeru. “Kodi udzanyenga ndi milomo yako.”—Miyambo 24:28.
Mungasankhe kupita mwachindunji kwa akulu. Si kulakwa kutero. Komabe, njira yabwino kwambiri yachikondi ndiyo kumfikira munthu wolakwayo. Mwinamwake zinthu siziri monga momwe mukuzionera. Mwinanso nkhaniyo ili kale m’manja mwa akulu. Kambitsiranani nkhaniyo ndi munthuyo modekha. Ngati mukuonabe kuti pali zifukwa zokhulupirira kuti tchimo lalikulu lachitika, mlimbikitseni kufikira akulu kuti apeze chithandizo, ndipo muuzeni ubwino wochita zimenezo. Osauza ena nkhaniyo, popeza kutero kungakhale mjedo.
Ngati munthuyo sakukanena kwa akulu panthaŵi yoyenera, ndiye kuti inu muyenera kutero. Mkulu mmodzi kapena aŵiri adzakambirana naye wolakwayo. Akuluwo ayenera ‘kufunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa’ kuti aone ngati tchimo lachitika. Ngati lachitikadi, iwo adzaiona nkhaniyo mogwirizana ndi Malemba.—Deuteronomo 13:12-14.
Pafunikira mboni ziŵiri kuti mutsimikizire za tchimolo. (Yohane 8:17; Ahebri 10:28) Ngati munthuyo akana mlanduwo ndipo pali umboni umodzi wokha, nkhaniyo idzasiyidwa m’manja mwa Yehova. (1 Timoteo 5:19, 24, 25) Izi zimachitidwa pozindikira kuti “zonse zikhala za pambalambanda” kwa Yehova ndi kuti, ngati munthuyo ali wolakwa machimo ake ‘adzampeza.’—Ahebri 4:13; Numeri 32:23.
Koma tinene kuti munthuyo wakana nkhaniyo, ndipo muli nokha monga mboni. Kodi ndiye kuti tsopano inuyo adzakuimbani mlandu wa mijedo? Ayi, pokhapokha ngati mwauzako ena amene sizikuwakhudza. Sikuneneza kuulula nkhani zomwe zikukhudza mpingo kwa amene ali ndi mphamvu ndi udindo woyang’anira ndi kuwongolera zinthu. Kunena zoona, kuchita zimenezo ndi mbali imodzi yochitira cholinga chathu chochita zabwino ndi kukhala wokhulupirika.—Yerekezerani ndi Luka 1:74, 75.
Kusunga Chiyero Mumpingo
Chifukwa chimodzi choulurira tchimo nchakuti kumathandiza kusunga chiyero cha mpingo. Yehova ndi Mulungu woyera, wopatulika. Amafuna onse omlambira akhale oyera mwauzimu ndi mwamakhalidwe. Mawu ake ouziridwa amati: “Monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziŵa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.” (1 Petro 1:14-16) Awo amene amachita zinthu zonyansa kapena zolakwa angadzetse chidetso ndi kutayitsa chiyanjo cha Yehova pampingo wonse mpaka atawongoleredwa kapena kuchotsedwa.—Yerekezerani ndi Yoswa, chaputala 7.
Makalata a mtumwi Paulo ku mpingo wachikristu ku Korinto amasonyeza mmene kuulula tchimolo kunathandizira kuyeretsa anthu a Mulungu kumeneko. M’kalata yake yoyamba, Paulo analemba kuti: “Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati pa inu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.”—1 Akorinto 5:1.
Baibulo silitiuza kuti nkwandani kumene mtumwiyo anamva nkhaniyo. Mwinamwake Paulo anamva nkhaniyo kwa Stefana, Fortunato, ndi Akayiko, omwe anachokera ku Korinto kupita ku Efeso kumene Paulo amakhala. Paulo analinso atalandira kalata yofunsira uphungu kuchokera ku mpingo wachikristu m’Korinto. Kaya adamva kuti, koma pamene Paulo anamva nkhaniyo kwa mboni zokhulupirika, anapeza mphamvu zopereka malangizo pa nkhaniyo. “Chotsani woipayo pakati pa inu nokha,” analemba tero. Munthuyo adachotsedwa.—1 Akorinto 5:13; 16:17, 18.
Kodi malangizo a Paulo anakhala ndi zotsatira zabwino? Inde anaterodi! Mwachionekere, wochimwayo anazindikira kulakwa kwake. M’kalata yake yachiŵiri kwa Akorinto, Paulo analimbikitsa mpingowo kuti “mumkhululukire ndi kumtonthoza” munthu wolapayo. (2 Akorinto 2:6-8) Motero kuulula kunapangitsa kuti pachitike zomwe zinathandiza kuyeretsa mpingo ndi kuyanjitsa munthu wolapayo kwa Mulungu popeza adawononga ubwenzi wake ndi Mulungu.
Timapezanso chitsanzo china m’kalata yoyamba ya Paulo ku mpingo wachikristu ku Akorinto. Nthaŵi ino mtumwiyu akutchula mboni imene inanena nkhaniyo. Analemba kuti: “Pakuti zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu.” (1 Akorinto 1:11) Paulo anazindikira kuti mikangano imeneyi, ndiponso kupatsa anthu ulemu wosayenera, zinapangitsa mzimu wampatuko umene unali pafupi kuwononga umodzi wampingo. Motero, pokhala wodera nkhaŵa kwambiri za kakhalidwe kauzimu ka okhulupirira anzake kumeneko, Paulo anachitapo kanthu msanga ndi kulemba uphungu wowongolera kumpingowo.
Lero, abale ndi alongo ambiri m’mipingo kuzungulira dziko lonse lapansi ali maso kuchinjiriza chiyero chauzimu cha mpingo mwa kudzisunga oyera pamaso pa Mulungu iwo eni. Ena amavutika kuti achite zimenezo; ena afikira ngakhale kufa kuti akhale okhulupirika. Ndithudi kumangonyalanyaza kapena kubisa zolakwa kukhoza kusonyeza kusayamikira pa kuyesayesa kwa ameneŵa.
Thandizo kwa Olakwa
Nchifukwa ninji ena amene agwera m’tchimo lalikulu amaopa kufikira akulu mumpingo? Nthaŵi zambiri nchifukwa chakuti sazindikira ubwino wa kufikira akulu. Ena amalingalira molakwa kuti atakanena, mpingo wonse udzauzidwa za tchimo lawolo. Ena amadzinyenga okha kuti tchimo lawolo nlalikulu kwambiri. Koma pali ena omwe amalingalira kuti akhoza kusintha okha popanda thandizo la akulu.
Koma olakwa oterewa amafunikira thandizo lachikondi kuchokera kwa akulu mumpingo. Yakobo analemba kuti: “Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.”—Yakobo 5:14, 15.
Ndi makonzedwe abwino chotani nanga othandiza olakwa kubwezeretsa kakhalidwe kawo kauzimu! Mwa kugwiritsira ntchito uphungu wotonthoza wa m’Mawu a Mulungu ndi kuwapempherera, akulu akhoza kuthandiza odwala mwauzimu kuti achire pa njira zawo zolakwa. Motero, m’malo momva kuti ngokanidwa, olapa kaŵirikaŵiri amamva kukhala otsitsimulidwa ndi omasuka atakambirana ndi akulu achikondi. Mnyamata wina wa ku West Africa adachita dama ndipo anabisa tchimo lake kwa miyezi ingapo. Pamene tchimo lake linadziŵika, ananena kwa akulu kuti: “Mmene ndimalakalakira wina atandifunsa za chibwenzi changa ndi mtsikana amene uja! Ndapeza mpumulo pamene ndaulula nkhaniyi poyera.”—Yerekezerani ndi Salmo 32:3-5.
Machitidwe a Chikondi cha Lamulo
Atumiki obatizidwa a Mulungu ‘anatuluka mu imfa kuloŵa m’moyo.’ (1 Yohane 3:14) Koma akachita tchimo lalikulu, ndiye kuti abwereranso kuloŵa m’njira ya imfa. Ngati sathandizidwa, akhoza kupimbidzala pa kuchita zoipa, osafunanso kulapa ndi kubwerera kuyamba kulambira Mulungu woona.—Ahebri 10:26-29.
Kuulula wochita tchimo nkusonyeza chikondi chenicheni kwa wolakwayo. Yakobo analemba kuti: “Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa ku njira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzabvundikira machimo aunyinji.”—Yakobo 5:19, 20.
Motero, kodi nkuululiranji wochita choipa? Chifukwa kuteroko kumabweretsa zabwino. Ndithudi, kuulula tchimo ndiko chikondi cha lamulo chachikristu kwa Mulungu, kumpingo, ndiponso kwa wochimwayo. Pamene aliyense mumpingo asunga malamulo olungama a Mulungu mokhulupirika, Yehova adzadalitsa kwambiri mpingo wonse. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Amenenso [Yehova] adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Kristu.”—1 Akorinto 1:8.
[Chithunzi patsamba 26]
Kulimbikitsa Mboni yolakwa kuti ilankhule ndi akulu kumasonyeza chikondi
[Chithunzi patsamba 28]
Akulu amathandiza wolakwa kuti ayanjidwenso ndi Mulungu