Achimwemwe Ali Awo Amene Amagwiritsira Ntchito Mphamvu Moyenera!
“Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wamphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula.”—NAHUMU 1:3.
1. Kodi nchifukwa ninji kukhala ndi mphamvu yakutiyakuti kwa munthu sikuli maziko akudzitamandira?
PALI mitundu yambiri yamphamvu imene zolengedwa zaluntha zingagwiritsire ntchito m’njira yoyenera. Chifukwa cha chibadidwe kapena chifukwa cha mikhalidwe, ife tingakhale ndi mphamvu ya mtundu wakutiwakuti. Koma kodi imeneyi imapereka maziko a kudzitamandira? Kutalitali. Kodi timawerenga chiyani pa Yeremiya 9:23? “Munthu wanzeru asadzitamandire nzeru zake kapena munthu wolimba asadzitamandire nyonga yake kapena munthu wachuma asadzitamandire chuma chake.” (New International Version) Kulekeranji? Mtumwi Paulo akupereka yankho labwino pa 1 Akorinto 4:7 kuti: “Akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?”
2. Kodi nchifukwa ninji tifunikira kukhala osamala pogwiritsira ntchito mphamvu?
2 Kodi nchifukwa ninji timafunikira kupewa kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu iriyonse imene tingakhale nayo? Chifukwa chakuti “ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira paunyamata wake.” (Genesis 8:21) Popeza kuti tonsefe tiri ndi chikhoterero cha chibadwa ichi cha kuchita dyera, tifunikira nthawi zonse kusamala kuti tikugwiritsira ntchito moyenera mphamvu iriyonse imene tingakhale nayo. Nthawi zina wolemba ndakatulo ananena mfundo iyi: “Chuma sichimadza popanda nkhawa. Mphamvu siimakhala yopanda msampha wamachenjera.” Inde, chifukwa cha kupanda ungwiro kwa cholowa nthawi zonse pali chikhoterero cha kugwiritsira ntchito mphamvu mwadyera.
Yehova—Wamphamvu, Komanso Wanzeru ndi Wolungama
3. Kodi ndimphamvu zamtundu wotani zimene ziri mwa Yehova?
3 Siwina kusiyapo Mlengi, Yehova Mulungu, amene amatipatsa chitsanzo, inde, changwiro m’kugwiritsira ntchito mphamvu. Iye samafulumira koma amachedwa kukwiya ngakhale pamene pali pofunikira kusonyeza mphamvu yake motsutsa. (Nahumu 1:3) Palibe munthu amene ali ndi mphamvu yaikulu kwambiri kuposa Mulungu, kaamba ka chifukwa chimenechi timamtchula kukhala Wamphamvuyonse kapena Wanyonga yonse. Moyenerera iye amagwiritsira ntchito dzina laulemu lakuti “Wamphamvuyonse” kwa iyemwini. (Genesis 17:1) Sikokha kuti iye ali ndi mphamvu yokwanira m’lingaliro la kukhala ndi nyonga yopanda polekezera, komanso iye ali wamphamvuyonse m’chakuti ali ndi ulamuliro wonse wogwirizanitsidwa ndi malo ake antchito monga Ambuye Mfumu wachilengedwe chonse, chimene iye analenga. Ndicho chifukwa chake palibe aliyense amene angalingalire za ‘kuletsa dzanja lake, kapena kunena naye kuti, Muchitanji?’—Danieli 4:35.
4. Kodi nchifukwa ninji iri njira yanzeru kuwopa Yehova?
4 Kaamba ka chenicheni chakuti Yehova Mulungu ngwamphamvuyonse, iri njira yanzeru kwa ife kuwopa kusamkondweretsa. Inde, “chiyambi cha nzeru ndicho kuwopa Yehova; kudziwa woyerayo ndiko luntha.” (Miyambo 9: 10) Paulo akutichenjeza kusasonkhezera Yehova kuchita nsanje mwa kuphatikizidwa m’mpangidwe uliwonse wa kulambira mafano chifukwa chakuti “kodi mphamvu zathu ziposa iye?” Kutalitali! (1 Akorinto 10:22) Komabe, onse amene aswa dala malamulo olungama a Mulungu akuchita ngati kuti ngamphamvu kwambiri koposa Yehova! Ndiponso mawu a Paulo akugogomezera mfundo iyi: “Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.”—Ahebri 12:29.
5. Kodi nchifukwa ninji sitifunikira kukhala ndi mantha achinthenthe ndi Yehova chifukwa cha kukhala kwake wamphamvuyonse?
5 Zenizeni zimenezi zingatichititse kudzazidwa ndi chinthenthe kapena kunthunthumira ngati kukanakhala kwakuti Yehova Mulungu sanali kulinganiza mokwanira mphamvu yake yonse limodzi ndi mikhalidwe yake ina yaikulu itatu: nzeru, chiweruzo cholungama, ndi chikondi. Kugwiritsira ntchito kwake mphamvu m’njira yotsutsa nthawi zonse kuli kogwirizana kapena kumayenderana, ndi mikhalidwe imeneyo. Mwachitsanzo, Chigumula cha nthawi ya Nowa chinalidi chisonyezero chachikulu cha mphamvu ya Yehova. Komabe kodi kusonyeza mphamvu kwa Mulungu kunali kopanda chilungamo kapena kopanda chikondi? Kutalitali! Anthu anali ataipitsa kwambiri njira yawo kotero kuti Mulungu anakhumudwa mu mtima ndi zimene adawona. (Genesis 6:5-11) Popeza kuti anthu oipawo a chigumula chisanakhale anali kugwiritsira ntchito molakwa madalitso a Mulungu, iye anachita molondola kuwasesa onse pysiti padziko lapansi, makamaka chifukwa chakuti ananyalanyaza machenjezo a Nowa, “mlaliki wachilungamo.”—2 Petro 2:5.
6. Kodi zochita za Yehova pa Sodomu ndi Gomora zimasonyezanji?
6 Pamene anthu a ku Sodomu ndi Gomora anadzisonyeza kukhala amphulupulu oluluzika kwadzawoneni, mwa kugwiritsira ntchito molakwa madalitso amene iwo, monga anthu, anali nawo kuchokera kwa Yehova, iye analamula kuti anthuwo ayenera kuwonongedwa. Momverera chisoni bwenzi lake Abrahamu, Yehova anauza mwamuna wachikhulupiriro ameneyo za chifuno Chake ponena za Sodomu ndi Gomora. Abrahamu anawonekera kukhala akulingalira kuti kumeneko kukakhala kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa kwambiri. Chotero iye anafunsa Yehova kuti: “Kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?” Komabe, Abrahamu, analakwa. Potsirizira pake iye anafunikira kuvomereza kuti lamulo la Yehova linalidi lolungama, chifukwa chakuti simunapezeke ngakhale anthu khumi olungama m’mizinda iwiriyo. Ndithudi ichi chimasonyeza mmene Yehova Mulungu aliri wosamala kugwiritsira ntchito mphamvu yake mwachilungamo.—Genesis 18:17-33; Yesaya 41:8.
7. Kodi nchifukwa ninji Farao anayenerera kulandira chisonyezero chowononga cha mphamvu ya Yehova?
7 Pambuyo pake, pamene nthawi ya kulanditsa anthu ake ku ukapolo wankhalwe m’Igupto inafika, Yehova anapatsa Farao mwawi wa kugwirizanako. Izi zikapeŵetsa chivulazo pa Farao ndi anthu ake. Koma monyang’wa ndi mouma khosi anakana kulola pempho la Yehova. Chotero Mulungu anapatsa Farao chitsanzo chimodzi motsatizana ndi chinzake cha mphamvu yake m’Miliri Khumi pa Igupto. (Eksodo 9:16) Farao atalola Aisrayeli kumuka, mouma khosi anapitirizabe kutsutsana ndi Yehova mwa kulondola Aisrayeli. Chifukwa chake, Yehova, molungama anagwiritsira ntchito mphamvu yake kusesa Farao ndi gulu lake lankhondo lamphamvu m’Nyanja Yofiira. (Salmo 136:15) Kuyenera kuwonedwa, kuti m’chochitika chirichonse, Yehova anagwiritsiranso ntchito mphamvu yake yaikuluyo kutetezera atumiki ake okhulupirika: Nowa ndi banja lake; Loti ndi ana ake aakazi aŵiri; ndi mtundu wa Israyeli.—Genesis 19:16.
8. Kodi ndi kaamba ka chifukwa chabwino chiti chimene Yehova anachitira ndi Sanakeribu monga momwe anachitira?
8 Zaka mazana angapo pambuyo pake, m’nthawi ya Mfumu Hezekiya, Yehova Mulungu anasonyeza mphamvu yake yaikulu mwanjira yochititsa chidwi koposa ndi yolungama pamene mfumu ya Asuri Sanakeribu anathupsa Yerusalemu. Anthu a Yehova, limodzi ndi Mfumu Hezekiya wowopa Mulunguyo ndi wokhulupirika monga mutu wawo, anampempha Iye chithandizo. Anali kumtumikira mokhulupirika, chotero Mulungu anachitapo kanthu mmalo mwawo. Kumbali ina, nthumwi za Mfumu Sanakeribu, zidadzitamandira kuti: ‘Musamvere Hezekiya, asakunyengeni mwakulonjeza kuti, Yehova adzakupulumutsani. Kodi milungu iriyonse ya amitundu inapulumutsa anthu awo m’dzanja la Sanakeribu? Popeza kuli kwakuti palibe iriyonse ya milungu imeneyi imene inali yokhoza kutero, kodi mulingaliriranji kuti Yehova adzakhoza kukulanditsani?’ (Yesaya 36:13-20) Chifukwa cha kudzitukumula kotero, Mulungu anangofunikira kusonyeza mphamvu yake yaikulu, akumachititsa kugwa kwa asilikali ankhondo 185, 000 mu usiku umodzi, kutsimikizira kuti, ndithudi, panali kusiyana pakati pa milungu ya amitundu ndi Yehova.
9. Kodi nzitsanzo zina zotani zimene tingatchule zosonyeza kuti Yehova ngwosamala ponena za mmene amagwiritsirira ntchito mphamvu?
9 Tangolingalirani zitsanzo zowonjezereka pang’ono za zambiri zimene zingaperekedwe. Pamene Yehova anakantha Miriyamu ndi khate, chimenecho chinali chisonyezero cholungama ndi chanzeru kotheratu cha mphamvu yake. Miriyamu anayenerera chilango chotero kaamba ka kulankhula modzitukumula motsutsana ndi mbale wake Mose, woikidwa wa Mulungu. (Numeri 12:1-15) Kunali kofanana pamene mwachipongwe Mfumu Uziya inadudukira kulowa m’malo opatulika a kachisi ndi kudzigangira kupereka zonunkhira paguwa lansembe lagolide, ikumakana monyang’wa kuletsedwa ndi ansembe Alevi. Yehova anasonyeza mphamvu Yake yoyenererayo mwakungokantha mfumuyo ndi khate. (2 Mbiri 26:16-21) Monga momwedi machimo awo analiri osiyana, ndimo mmene chilango chawo chochokera kwa Yehova chinaliri: khate la Miriyamu linali lakanthawi, koma Uziya anafa ali wakhate. Pamenepa tingathe kuwona kuti nthawi zonse Yehova ngwosamala kugwiritsira ntchito mphamvu yake m’njira yanzeru ndi yolungama, ali wokhoza kutetezera okhulupirika amene amamkonda ndi kuwononga oipa.—Salmo 145:20.
Chitsanzo cha Yesu Kristu
10, 11. Kodi nzochitika zotani zimene zimasonyeza kuti Yesu anali wodera nkhawa ndikugwiritsira ntchito mphamvu moyenera?
10 Mwana wa Mulungu analidi wotsanzira wabwino kwambiri wa Atate wake m’kugwiritsira ntchito mphamvu. Pakati pa zochitika zoyambirira panali nthawi pamene Satana anakangana naye pamtembo wa Mose. Mosavuta Logos akanadzudzula Satanayo mwamphamvu. Mmalo mwake, Logos analepa, kunena kwake titero, kulola chidzudzulocho kuti chichokere kwa Yehova Mulungu mwiniyo.—Yuda 8, 9.
11 Chiyeso choyamba chenicheni chimene Satana anapereka kwa Yesu m’chipululu chinaphatikizapo nkhaniyi ya kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa. Satana anayesa Yesu kugwiritsira ntchito mphamvu zake zoposa zachibadwa kaamba ka chifuno chadyera, kusanduliza miyala kukhala chakudya. Ichi chinali chiyeso chachikulu chifukwa chakuti Yesu sanadye kwa masiku 40, ndipo “anamva njala.” Satana anapereka chiyeso chimenechi mwanjira yakuti akole Yesu kutenga njira yadyera, chifukwa chakuti anayamba mwakuti, “NGATI muli Mwana wa Mulungu, tauzani miyala iyi isanduke mkate.” Mosakaikira iye anayembekezera kuti Yesu akalabadira mwakumati, ‘Eya ndithudi ndine Mwana wa Mulungu, ndipo kukutsimikizira ndidzasanduliza miyala imeneyo kukhala mkate.’ Mmalo mwakuti, Yesu ayesedwe kapena kukodwa m’kuchita mwadyera kapena mopusa, anayankha kuti: “Kwalembedwa, munthu sadzakhala ndi mOyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:1-4) Iye ananyalanyaza lingaliro lokaikira lakuti kaya anali Mwana wa Mulungu kapena ayi, ndipo anakana kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu imene Mulungu adampatsa.
12. Kodi Yesu anasonyezanso motani kuti sanali waumbombo ndi mphamvu?
12 Pambuyo pake, Yesu Kristu atadyetsa amuna 5, 000 osawerengera akazi ambiriwo ndi ana, Ayuda anafuna kumpanga mfumu. Ngati akanavomereza pempho lawo, kumeneko kukanakhala kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu imene anali nayo kusonkhezera anthu kupyolera mwa zozizwitsa zake. Iye anadziwa kuti anafunikira kusunga uchete kundale za dziko zaudziko ndi kuyembekezera Yehova Mulungu kumpatsa ufumu. (Yohane 6:1-15) Komabe pambuyo pake, pamene gulu la achifwamba linamgwira monga mkaidi, iye akanapempha magulu 12 a angelo ndipo mwakutero akanatetezeredwa kusatengedwa monga mkaidi. Komabe, kutero kukanakhala kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa, chifukwa chakuti chinali chifuniro cha Atate wake kuti agonjere.—Mateyu 26:39, 53.
Ena Amene Sanagwiritsire Ntchito Mphamvu Molakwa
13, 14. (a) Kodi nchitsanzo chabwino kwambiri chotani chimene Gideoni anapereka, kusonyeza kuti sanali waumbombo ndi mphamvu? (b) Kodi ndimotani mmene Sauli anaperekera chitsanzo chabwino panthawi yoyamba atakhala mfumu?
13 Pakati pa anthu opanda ungwiro amene analaka chiyeso cha kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa, Woweruza Gideoni ayenera kutchulidwa. Atatha kulanditsa Israyeli padzanja la Midyani, anthu anafuna kumpanga mfumu yawo. Gideoni anakana, akumafotokoza molondola kuti: “Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.” Inde, kudzichepetsa kumene anasonyeza pachiyambi penipeni pa ntchito yake monga woweruza kunalipobe. Ndipo yankho la Gideoni linasonyeza njira mwa imene Yehova Mulungu mwiniyo analingalirira za kukhala kwa Israyeli ndi mfumu yaumunthu. Tingathe kuzindikira zimenezo m’yankho lake ku pempho la kufuna mfumu kwa Israyeli m’nthawi ya mneneri Samueli.—Oweruza 8:23; 6:12-16; 1 Samueli 8:7.
14 Komabe, pamene, mfumu inasankhidwa, poyamba Sauli anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri cha kudziletsa m’kugwiritsira ntchito mphamvu. Amuna ena achabechabe anati: “Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampepuza, . . . koma iye anakhala chete.” Iye akanakhoza kuchita mwathuku, ndi mphamvu yake yaufumu, koma iye sanatero. Mofananamo, Sauli atatha kupeza chipambano pa Aamoni, ena a anthu ake analingalira kuti imeneyi ikakhala nthawi yabwino kwambiri ya kubwezera awo amene adanyozera Sauli. Chotero iwo anati kwa iye: “Ndani iye amene anati, Kodi Sauli adzatiweruza ife? Tengani anthuwo kuti tiwaphe.” Komabe, Sauli, analibe konse malingaliro amenewo. Mmalo mwake iye anati: “Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso m’lsrayeli.” Ndithudi tingathe kuwona kuti Sauli anayamba bwino ndi modzichepetsa. (1 Samueli 9:21; 10:20-23, 27; 11:12, 13) Ha nzomvetsa chisoni chotani nanga kuti iye anayamba kugwiritsira ntchito molakwa ulamuliro wake wachifumu ndipo motero anali ndi mapeto oipa!—1 Samueli 28:6; 31:3-6.
15, 16. (a) Kodi woweruza Samueli anali wokhoza kupereka umboni wotani ponena za kugwiritsira ntchito kwake mphamvu yakuweruza? (b) Kodi nchitsanzo chofanana chotani chimene Mfumu Davide anapereka?
15 Samueli, mneneri amenenso anaweruza Israyeli anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Mulungu anamgwiritsira ntchito mwamphamvu kuyambira paubwana wake weniweni kumkabe mtsogolo. Moyenerera Samueli anaweruza anthu ake ndipo anachititsa chilanditso chawo. Kodi iye anayamba wagwiritsirapo ntchito malo ake antchito kaamba ka phindu ladyera? Kutalitali! M’nkhani yake yotsazikana ndi anthuwo anati: “Wonani ndinamvera mawu anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu . . . Ndikalipo ine, chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng’ombe ya yani? Kapena ndinalanda buru wayani? Ndinanyenga yani? Ndinasautsa yani? Ndinalandira m’manja mwayani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga?” Anthu akewo anafunikira kuvomereza kuti njira ya Samueli inali yopanda liwongo m’nkhani zonsezi. Sanagwiritsirepo ntchito molakwa mphamvu pa malo ake antchito yoweruza.—1 Samueli 12:1-5.
16 Ndiponso sitingathe kunyalanyaza chitsanzo chabwino kwambiri choperekedwa ndi Davide. Kaŵiri Mfumu Sauli anali m’mkhalidwe wakuti akanakhoza ndipo akanatha kuphedwa. Davide akanalingalira kuti: ‘Sauli akufunafuna kundipha, chotero afe ndi iye osati ine.’ Kapena iye akanalingalira mwadyera kuti: ‘Popeza kuli kwakuti Samueli wandidzoza kukhala mfumu yamtsogolo ya Israyeli, iyi ndiyo njira imene potsirizira pake ziyenera kuchitikira. Kulekeranji tsopano?’ Ayi, Davide anayembekezera moleza mtima kufikira nthawi ya Yehova ya kumpatsa ufumu. (1 Sa- mueli 24:1-22; 26:1-25) Komabe, nzomvetsa chisoni kunena kuti, Davide atakhala mfumu, nthawi ziwiri anagwiritsira ntchito molakwa ulamuliro wake: mwakuchititsa imfa ya Uriya ndi kuwerenga gulu lankhondo la Israyeli. -2 Samueli 11:15; 24:2-4, 12-14.
17. Kodi ndimotani mmene Paulo anasonyezera kuti sanali konse waumbombo kapena kugwiritsira ntchito molakwa ulamuliro wake?
17 Pakati pa otsatira a Yesu Kristu, mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pamfundoyi. Iye akanafunsira chichirikizo kuchokera ku mipingo imene anatumikira. Koma iye sanapindule nayo. Anauza akulu a ku Efeso kuti: “Sindinasirira siliva, kapena chovala cha munthu wina aliyense. Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akumakhala ndi ine.” (Machitidwe 20:33, 34) Polembera mpingo ku Korinto, mtumwiyo ananenadi mwamphamvu kwambiri mfundoyi. (1 Akorinto 9: 1-18) Iye anali ndi ufumu wakusagwira ntchito yakuthupi, pakuti msilikali ndani agwira ntchito nadzifunira zake yekha? Kodi Mose sananene kuti usapunamitse ng’ombe pakupuntha iyo tirigu? “Koma,” Paulo analongosola, “ine sindinachita nako kanthu ka izi.” Kodi mphotho yake inali yotani? “Kuti pakulalikira uthenga wabwino ndiyese uthenga wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa muuthenga wabwino.”
18. (a) Kodi tiyenera kulingalira motani ponena za kugwiritsira ntchito bwino kwambiri mphamvu kwa Yehova? (b) Kodi nchifukwa ninji awo amene amam’tsanzira pamfundoyi anganenedwe kukhala achimwemwe?
18 Ndithudi kungathe kunenedwa kuti, ‘achimwemwe ali awo amene samagwiritsira ntchito molakwa mphamvu yawo.’ Ndimbiri yabwino kwambiri chotani nanga imene Yehova Mulungu ali nayo chifukwa cha kukhazikitsa chitsanzo chabwino kwambiri chotero, akumalola mphamvu yake yonse kukhala yoyendera limodzi ndi mikhalidwe yake inayo ya nzeru, chiweruzo cholungama, ndi chikondi! Motero, ife tinganene, limodzi ndi wamasalimo Davide kuti: “Lemekeza Yehova moyo wanga; ndi zonse zam’kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.” (Salmo 103:1) Onse olondola chitsanzo cha Yehova m’kugwiritsira ntchito mphamvu moyenera alidi achimwemwe. Zitsanzo zimene tapenda kuchokera m’Malemba zimatsimikizira kuti ngakhale kuti ndife anthu opanda ungwiro, nafenso, tingathe kugwiritsira ntchito moyenera mphamvu imene tiri nayo. Mwakutero, tingathe kukhala osati kokha ndi chikumbumtima choyera komanso chivomerezo cha Mulungu ndi ulemu wa anthu anzathu.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji uphungu wonena za kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa uli wofunika?
◻ Kodi nzitsanzo zotani zimene zimasonyeza kuti Yehova Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu yake moyenera?
◻ Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Yesu anali wosamala kusagwiritsira ntchito mphamvu molakwa?
◻ Kodi ndianthu ati m’Malemba Achihebri amene anasonyeza kuti sanagwiritsire ntchito mphamvu molakwa?
◻ Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anadzisonyezera kukhala chitsanzo chabwino m’kugwiritsira ntchito ulamuliro?
[Chithunzi patsamba 7]
Mikhalidwe yaikulu ya Yehova yayeneretsedwa ndendende
Chikondi Mphamvu Chiweruzo cholungama Nzeru
[Zithunzi patsamba 8]
Mwachilungamo Yehova anasonyeza Mphamvu yake
Mwa chigumula
Pa Sodomu ndi Gomora
Pa Nyanja Yofiira