MUTU 6
Kodi Mungasankhe Bwanji Zosangalatsa Zabwino?
“Chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 AKORINTO 10:31.
1, 2. Kodi tifunika kuchita chiyani pa nkhani ya zosangalatsa?
TAYEREKEZERANI kuti mukufuna kudya chipatso chokoma kwambiri, koma mukuona kuti chipatsocho ndi chowola mbali ina. Kodi mungatani? Mungathe kuchita chimodzi mwa zinthu zitatu izi: Kudya chipatso chonsecho limodzi ndi mbali yowolayo, kutaya chipatso chonsecho, kapena kudula mbali yowolayo ndi kudya yabwinoyo. Kodi inuyo mungasankhe kuchita chiyani?
2 Zinthu zosangalatsa zingafanane ndi chipatso chimenechi. Nthawi zina mungafune kusangalalako, koma zosangalatsa zambiri masiku ano ndi zoipa kwambiri, tingoti ndi zowola. Kodi inuyo mungatani pamenepa? Ena alibe nazo vuto zinthu zoipa ndipo angalole zosangalatsa zilizonse za m’dzikoli. Koma ena amapewa zosangalatsa zonse kuti asakhudzidwe ngakhale pang’ono ndi zoipa. Pomwe ena amayesetsa kupewa zosangalatsa zoipa koma amalola zosangalatsa zimene tingati ndi zabwino. Kodi inuyo muyenera kusankha chiyani kuti Mulungu apitirize kukukondani?
3. Kodi tiyamba kukambirana chiyani?
3 Ambirife, tingasankhe kuchita zimene zafotokozedwa mbali yachitatuyo. Timadziwa kuti zinthu zosangalatsa n’zofunika, koma timafuna kusangalala ndi zinthu zabwino zokha. Choncho, tikufunika kukambirana mmene tingadziwire zosangalatsa zabwino ndi zoipa. Koma tiyeni tikambirane kaye mmene zosangalatsa zingakhudzire kulambira kwathu Yehova.
“CHITANI ZONSE KU ULEMERERO WA MULUNGU”
4. Kodi kukumbukira kuti tinadzipereka kwa Yehova kungatithandize bwanji posankha zosangalatsa?
4 M’bale wina wachikulire yemwe anabatizidwa mu 1946, ananena kuti: “Ndimaonetsetsa kuti ndizipezeka pa nkhani iliyonse ya ubatizo ndi kumvetsera mwatcheru kwambiri, ngati kuti ndi pa ubatizo wanga.” Kodi n’chifukwa chiyani amachita zimenezi? M’baleyo anati: “Kukumbukira nthawi zonse kuti ndinadzipereka kwa Yehova kumandithandiza kwambiri kuti ndikhalebe wokhulupirika.” Sitikukayikira kuti inunso mukuvomereza zimenezi. Kukumbukira kuti munalonjeza Yehova kuti mudzamutumikira kwa moyo wanu wonse, kumakulimbikitsani kupirira. (Werengani Mlaliki 5:4.) Ndipotu, kuganizira mofatsa kuti munadzipereka kwa Mulungu kumakhudza mmene mumaonera utumiki wanu wachikhristu ndiponso zinthu zina zonse zimene mumachita pa moyo wanu, kuphatikizapo kusankha zosangalatsa. Mtumwi Paulo anasonyeza mfundo yoona imeneyi pamene analembera Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.
5. Kodi lemba la Levitiko 22:18-20 limatithandiza bwanji kumvetsa mawu a pa Aroma 12:1 onena za nsembe?
5 Zonse zimene mumachita pa moyo wanu zimakhudza kulambira kwanu Yehova. Pofuna kutsindika mfundo imeneyi kwa okhulupirira anzake, Paulo anagwiritsa ntchito mawu amphamvu m’kalata yake yopita kwa Aroma. Iye anawachonderera kuti: “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Mawu akuti ‘thupi’ m’lembali, akuimira zinthu monga maganizo, mtima komanso mphamvu. Zonsezi ndi zimene mumagwiritsa ntchito potumikira Mulungu. (Maliko 12:30) Kutumikira Mulungu pogwiritsa ntchito zonsezi n’kutumikira Mulungu ndi mtima wonse, kumene Paulo anati kuli ngati nsembe. Mawu akuti “nsembe” amenewa akusonyeza kuti tiyenera kuchita zinthu mosamala potumikira Mulungu. Malinga ndi Chilamulo cha Mose, Mulungu ankakana nsembe yachilema. (Levitiko 22:18-20) Mofanana ndi zimenezi, ngati nsembe yauzimu ya Mkhristu ndi yodetsedwa m’njira inayake, Mulungu amaikana. Koma kodi zimenezi zingachitike bwanji?
6, 7. Kodi Mkhristu angadetse bwanji thupi lake, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?
6 Paulo analangiza Akhristu a ku Roma kuti: “Musapereke ziwalo zanu ku uchimo.” Iye anawauzanso kuti ‘aphe zochita za thupi.’ (Aroma 6:12-14; 8:13) Koyambirira kwa kalata yakeyi, iye anapereka zitsanzo zina za “zochita za thupi.” Ponena za anthu ochimwa Baibulo limati: “M’kamwa mwawo mwadzaza mawu otukwana.” “Mapazi awo amathamangira kukhetsa magazi.” “Maso awo saona chifukwa choopera Mulungu.” (Aroma 3:13-18) Mkhristu angadetse thupi lake ngati amagwiritsa ntchito “ziwalo” za thupi lake pochita machimo ngati amenewa. Mwachitsanzo, ngati Mkhristu wasankha kumaonera zinthu zonyansa, monga zolaula kapenanso mafilimu a zachiwawa, ndiye kuti iye ‘akupereka [maso ake] ku uchimo,’ ndipo akudetsa thupi lake lonse. Nsembe iliyonse imene angapereke polambira Mulungu, siikhalanso yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu. (Deuteronomo 15:21; 1 Petulo 1:14-16; 2 Petulo 3:11) Choncho kusankha zosangalatsa zoipa n’koopsa kwambiri.
7 Apa n’zachionekere kuti zinthu zosangalatsa zimene Mkhristu angasankhe zingathe kumubweretsera mavuto aakulu. Choncho, tiyenera kusankha zosangalatsa zimene zimakometsera nsembe imene timapereka kwa Mulungu, osati zimene zingaidetse. Tsopano tiyeni tikambirane mmene tingadziwire zosangalatsa zabwino komanso zoipa.
“NYANSIDWANI NDI CHOIPA”
8, 9. (a) Kodi zosangalatsa tingazigawe m’magulu awiri ati? (b) Kodi timapeweratu zosangalatsa zotani, nanga n’chifukwa chiyani?
8 Zosangalatsa tingazigawe m’magulu awiri. Gulu loyamba ndi la zosangalatsa zimene Akhristu amapeweratu, ndipo gulu lachiwiri ndi la zosangalatsa zimene Akhristu ena angaone kuti ndi zovomerezeka pomwe ena angaone kuti ndi zosavomerezeka. Choyamba, tiyeni tikambirane zosangalatsa za m’gulu loyambalo zomwe ndi zosangalatsa zimene Akhristu amapeweratu.
9 Monga momwe tinaonera m’Mutu 1, zosangalatsa zina zimakhala ndi zinthu zimene Baibulo limaletseratu. Mwachitsanzo, zinthu zachiwawa, zauchiwanda, zolaula ndiponso zolimbikitsa chiwerewere ndi makhalidwe ena oipa, zimapezeka pa Intaneti, m’mavidiyo, pa TV ndiponso m’nyimbo. Popeza kuti zosangalatsa zonyansa ngati zimenezi zimaonetsa zinthu zosemphana ndi mfundo kapena malamulo a m’Baibulo, Akhristu oona ayenera kupeweratu zosangalatsa zimenezi. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8) Mukamapewa zosangalatsa zoipa zimenezi, mumasonyeza Yehova kuti ‘mumanyansidwadi ndi zoipa’ ndipo nthawi zonse ‘mumapatuka pa zoipa.’ Mukamachita zimenezi, ndiye kuti muli ndi “chikhulupiriro chopanda chinyengo.”—Aroma 12:9; Salimo 34:14; 1 Timoteyo 1:5.
10. Kodi anthu ena ali ndi maganizo otani okhudza zosangalatsa, nanga n’chifukwa chiyani maganizo amenewa ndi oopsa?
10 Komabe, ena amaganiza kuti kuonera zosangalatsa zimene zimasonyeza makhalidwe oipa kulibe vuto lililonse. Iwo angaganize kuti, ‘Nditha kuonera zinthu zoipa m’mavidiyo kapena pa TV, koma sikuti ineyo ndingachite zimene ndimaonerazo.’ Maganizo amenewa ndi opusitsa ndiponso oopsa. (Werengani Yeremiya 17:9.) Ngati timasangalala kuonera zinthu zimene Yehova amadana nazo, kodi tingati ‘timanyansidwadi ndi zinthu zoipa’? Ngati timakonda kuonera zinthu zosonyeza makhalidwe oipa, timapha chikumbumtima chathu. (Salimo 119:70; 1 Timoteyo 4:1, 2) Chizolowezi chimenechi chingakhudze zochita zathu komanso mmene timaonera makhalidwe oipa a anthu ena.
11. Kodi n’chiyani chimene chikutsimikizira kuti lemba la Agalatiya 6:7 ndi loona pa nkhani ya zosangalatsa?
11 Zachitikapo kuti Akhristu ena achita chiwerewere chifukwa cha zimene amakonda kuonera. Iwo aphunzira kuti “chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho,” koma aphunzira zimenezi atakumana kale ndi mavuto. (Agalatiya 6:7) Koma mavuto ngati amenewa tingathe kuwapewa. Ngati nthawi zonse mumaganizira zinthu zabwino, mudzakolola zinthu zabwino pa moyo wanu.—Onani bokosi lakuti, “Kodi Ndiyenera Kusankha Zosangalatsa Zotani?”
ZIMENE MUNTHU AYENERA KUSANKHA YEKHA MOGWIRIZANA NDI MFUNDO ZA M’BAIBULO
12. Kodi lemba la Agalatiya 6:5 tingaligwiritse ntchito bwanji pa nkhani ya zosangalatsa, ndipo kodi n’chiyani chimene chingatithandize pa nkhani zimene tiyenera kusankha tokha zochita?
12 Tsopano tiyeni tikambirane gulu lachiwiri lija, la zosangalatsa zokhala ndi zinthu zomwe siziletsedwa kapena kuvomerezedwa mwachindunji m’Mawu a Mulungu. Pa zosangalatsa ngati zimenezi, Mkhristu aliyense ayenera kusankha zimene akuona kuti ndi zabwino. (Werengani Agalatiya 6:5.) Komabe, pali malangizo amene tiyenera kutsatira tikamasankha zosangalatsa ngati zimenezi. M’Baibulo muli mfundo zimene zimatithandiza kudziwa mmene Yehova amaganizira. Tikamaganizira kwambiri mfundo zimenezi, tidzazindikira “chifuniro cha Yehova” pa chilichonse chimene tingachite, kuphatikizapo pa zosangalatsa zimene timasankha.—Aefeso 5:17.
13. Kodi n’chiyani chingatithandize kupewa zosangalatsa zimene zingakhumudwitse Yehova?
13 Kunena zoona, sikuti Akhristu onse ali ndi luso lofanana lotha kuzindikira chabwino ndi choipa. (Afilipi 1:9) Komanso, Akhristufe timadziwa kuti anthu amakonda zosangalatsa zosiyanasiyana. Choncho, sitiyenera kuyembekeza kuti Akhristu onse angasankhe zosangalatsa zofanana. Ngakhale kuti timakonda zosangalatsa zosiyana, tikamalola kuti maganizo athu ndi mtima wathu uzitsatira kwambiri mfundo za Mulungu, tidzakhala okonzeka kupeweratu zosangalatsa zimene zingakhumudwitse Yehova.—Salimo 119:11, 129; 1 Petulo 2:16.
14. (a) Kodi tiyenera kuganizira chiyani posankha zosangalatsa? (b) Kodi tingatani kuti tiziika patsogolo zinthu za Ufumu pa moyo wathu?
14 Pali chinthu chinanso chofunika kwambiri chimene muyenera kuchiganizira mukamasankha zosangalatsa. Chinthu chimenechi ndi nthawi yanu. Zosangalatsa zimene mumakonda, zimasonyeza zimene inuyo mumaona kuti ndi zoyenera. Koma kuchuluka kwa nthawi imene mumathera pa zosangalatsazo kumasonyeza ngati mumaona zinthuzo kukhala zofunika kapena ayi. Akhristu amaona kuti zinthu zauzimu ndi zomwe zili zofunika kwambiri. (Werengani Mateyu 6:33.) Ndiyeno kodi mungatani kuti mupitirize kuika patsogolo zinthu za Ufumu pa moyo wanu? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.” (Aefeso 5:15, 16) Ndithudi, kuika malire pa nthawi imene mumachita zosangalatsa kungakuthandizeni kuti muzipeza nthawi yochitira “zinthu zofunika kwambiri,” zimene zingakuthandizeni pa moyo wanu wauzimu.—Afilipi 1:10.
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kwambiri posankha zosangalatsa?
15 Ndi bwinonso kuti tizisamala kwambiri posankha zosangalatsa. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Ganiziraninso za chitsanzo cha chipatso chija. Kuti mupewe kudya mbali yowola ya chipatsocho, simungacheke ndendende powola pokhapo basi. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kukhala osamala kwambiri posankha zosangalatsa. Mkhristu wanzeru amapewa zosangalatsa zimene zimatsutsana ndi mfundo za m’Baibulo, zosangalatsa zokayikitsa kapenanso zimene zili ndi mbali zina zomwe zingativulaze mwauzimu. (Miyambo 4:25-27) Kuti tithe kuchita zimenezi, tiyenera kutsatira mosamala zimene Mawu a Mulungu amanena.
“ZILIZONSE ZOYERA”
16. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti maganizo athu ndi ofanana ndi a Yehova pa nkhani ya chabwino ndi choipa? (b) Kodi mungatani kuti muzitsatira mfundo za m’Baibulo nthawi zonse?
16 Posankha zosangalatsa, Akhristu oona amaganizira kaye mmene Yehova amaonera zosangalatsazo. Baibulo limatithandiza kudziwa maganizo a Yehova ndi mfundo zake. Mwachitsanzo, Mfumu Solomo inatchula zinthu zingapo zimene Yehova amadana nazo, monga “lilime lonama, manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, mtima wokonzera ena ziwembu, mapazi othamangira kukachita zoipa.” (Miyambo 6:16-19) Kodi mmene Yehova amaonera nkhani zimenezi, zingakuthandizeni kukhala ndi maganizo otani? Wamasalimo akutilimbikitsa kuti: “Inu okonda Yehova danani nacho choipa.” (Salimo 97:10) Zosangalatsa zimene mumasankha zizisonyeza kuti mumadanadi ndi zimene Yehova amadana nazo. (Agalatiya 5:19-21) Muzikumbukiranso kuti zimene mumachita muli kwanokha, ndi zimene zimasonyeza kwambiri kuti ndinu munthu wotani, osati zimene mumachita pamaso pa anthu. (Salimo 11:4; 16:8) Choncho, ngati mumafuna kuti muzisonyeza kuti muli ndi maganizo a Yehova pa nkhani ya chabwino ndi choipa, nthawi zonse muzisankha zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mukamatero, mudzazolowera moti kutsatira mfundo za m’Baibulo kudzangokhala ngati moyo wanu.—2 Akorinto 3:18.
17. Tisanasankhe zosangalatsa, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
17 Mukamasankha zosangalatsa, kodi mungachitenso chiyani kuti muonetsetse kuti mukuchita zinthu mogwirizana ndi maganizo a Yehova? Muyenera kuganizira za funso ili, ‘Kodi zimenezi zindikhudza bwanji ineyo, nanga zikhudza bwanji ubwenzi wanga ndi Mulungu?’ Mwachitsanzo, musanaonere filimu inayake, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimene zili m’filimuyi zikhudza bwanji chikumbumtima changa?’ Tiyeni tione mfundo zimene zingatithandize pa nkhani imeneyi.
18, 19. (a) Kodi mfundo ya pa lemba la Afilipi 4:8 ingatithandize bwanji kudziwa ngati zosangalatsa zimene timakonda ndi zabwino? (b) Kodi ndi mfundo zina ziti zimene zingakuthandizeni kusankha zosangalatsa zabwino? (Onani mawu a m’munsi.)
18 Mfundo yaikulu ikupezeka pa lemba la Afilipi 4:8, limene limati: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.” N’zoona kuti apa Paulo sankanena za zosangalatsa, koma ankanena za zinthu zimene timaganizira, kuti ziyenera kukhala zokondweretsa Mulungu. (Salimo 19:14) Komabe mfundo ya mawu a Paulowa ingagwirenso ntchito pa nkhani ya zosangalatsa. Kodi ingagwire ntchito bwanji?
19 Dzifunseni kuti, ‘Kodi mafilimu, masewera a pakompyuta, nyimbo kapena zosangalatsa zina zimene ndimakonda, zimandithandiza kuganizira zinthu “zilizonse zoyera”?’ Mwachitsanzo, mukatha kuonera filimu inayake, kodi mumatsala mukuganiza zinthu zotani? Ngati zimakhala zabwino, zoyera, komanso zosangalatsa, ndiye kuti filimuyo inali yabwino. Koma ngati mumangoganiza zoipa mutaonera filimu inayake, ndiye kuti sinali yabwino. (Mateyu 12:33; Maliko 7:20-23) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti kumangoganiza zinthu zoipa kumasowetsa mtendere, kumapha chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo ndiponso kungathe kuwononga ubwenzi wanu ndi Mulungu. (Aefeso 5:5; 1 Timoteyo 1:5, 19) Popeza kuti zosangalatsa zoterezi zingakuvulazeni, muyenera kuzipeweratu.a (Aroma 12:2) Khalani ngati wamasalimo amene anapempha Yehova kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”—Salimo 119:37.
TIZIGANIZIRA ZINTHU ZOPINDULITSA ENA
20, 21. Kodi lemba la 1 Akorinto 10:23, 24 lingagwire ntchito bwanji pa nkhani yosankha zosangalatsa zabwino?
20 Paulo anatchula mfundo ya m’Baibulo yofunika kwambiri imene tiyenera kuiganizira tikamasankha zochita. Iye anati: “Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zolimbikitsa. Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:23, 24) Kodi mfundo imeneyi ingagwire ntchito bwanji pa nkhani yosankha zosangalatsa zabwino? Muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosangalatsa zimene ndingasankhe zingakhudze bwanji anthu ena?’
21 Chikumbumtima chanu chingakuloleni kusankha zosangalatsa zinazake zimene inuyo mumaona kuti ndi “zololeka” kapena kuti zovomerezeka. Komabe, ngati okhulupirira anzanu akuona kuti zosangalatsazo n’zokayikitsa chifukwa cha chikumbumtima chawo, mungasankhe kusachita zosangalatsa zimenezo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, monga mmene Paulo ananenera, inuyo simufuna ‘kuchimwira abale anu’ kapenanso ‘kuchimwira Khristu’ pochita zinthu zimene zingapangitse okhulupirira anzanu kulephera kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Muzitsatira malangizo akuti: “Pewani kukhala okhumudwitsa” ena. (1 Akorinto 8:12; 10:32) Akhristu oona masiku ano, amamvera malangizo abwino ndi anzeru a Paulo amenewa popewa zosangalatsa zimene zingakhale “zololeka” koma ‘zosamangirira.’—Aroma 14:1; 15:1.
22. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kulemekeza maganizo a ena pa nkhani yosankha zosangalatsa?
22 Komabe, pali chinthu chinanso chimene tiyenera kuchiganizira pa nkhani yofuna kuchita zinthu zopindulitsa ena. Mkhristu amene chikumbumtima chake chimamuletsa zinthu zina sayenera kukakamiza Akhristu onse mumpingo kuti aziyendera maganizo ake pa nkhani ya zosangalatsa zabwino. Ngati angachite zimenezi, ndiye kuti angafanane ndi dalaivala amene akuyendetsa galimoto ndipo akufuna kuti madalaivala onse pamsewu umenewo aziyendetsa galimoto zawo pa liwiro limene iyeyo akuona kuti ndi labwino. Kunena zoona, ngati angachite zimenezi, ndiye kuti alibe mtima wololera. Chifukwa chokonda Akhristu anzake, munthu amene chikumbumtima chake chimamuletsa zinthu zina, afunika kulemekeza okhulupirira anzake amene ali ndi maganizo osiyana ndi ake pa nkhani ya zosangalatsa zimene sizitsutsana ndi mfundo zachikhristu. Akamachita zimenezi, amasonyeza kuti akufuna kuti ‘anthu onse adziwe kuti ndi wololera.’—Afilipi 4:5; Mlaliki 7:16.
23. Kodi mungatani kuti muzisankha zosangalatsa zabwino?
23 Pofuna kubwereza zimene takambirana, tingafunse kuti, kodi mungatani kuti muzisankha zosangalatsa zabwino? Muzipewa zosangalatsa zonse zimene zimaonetsa zinthu zoipa zomwe Mawu a Mulungu amaletsa. Muzitsatira mfundo za m’Baibulo zimene mungagwiritse ntchito posankha zosangalatsa zimene Baibulo silinanene ngati zili zabwino kapena zoipa. Muzipewa zosangalatsa zimene zingavulaze chikumbumtima chanu ndiponso zina zilizonse zimene zingakhumudwitse anthu ena, makamaka okhulupirira anzanu. Mukachita zimenezi, mudzabweretsa ulemerero kwa Mulungu ndipo iye adzapitiriza kukukondani limodzi ndi banja lanu.
a Mfundo zina zothandiza pa nkhani ya zosangalatsa mungazipeze pa Miyambo 3:31; 13:20; Aefeso 5:3, 4; ndi Akolose 3:5, 8, 20.