Akazi
Tanthauzo: Anthu achikulire achikazi. M’Chihebri, liwu lakuti mkazi ndiro ’ish·shahʹ, limene kwenikweni limatanthauza “mwamuna wachikazi.”
Kodi Baibulo limaluluza akazi kapena kuwachitira ngati kuti anali anthu apansi?
Gen. 2:18, NW: “Yehova Mulungu anapitirizabe kunena kuti: ‘Sikuli bwino kuti mwamuna apitirizebe kukhala yekha. Ndidzampangira womthangata, monga womkwaniritsa.’” (Panopa mwamuna sakulongosoledwa ndi Mulungu kukhala munthu wabwino kwambiri kuposa mkazi. Mmalo mwake, Mulungu anasonyeza kuti mkazi akakhala ndi mikhalidwe imene ikwaniritsa ya mwamuna mkati mwa kakonzedwa ka Mulungu. Chokwaniritsa ndicho chimodzi cha zinthu ziŵiri zimene zimapanga chinthu chimodzi. Motero akazi monga kagulu ali apadera m’mikhalidwe ina ndi maluso; amuna, mu ina. Yerekezerani ndi 1 Akorinto 11:11, 12.)
Gen. 3:16: “Kwa mkaziyo ndipo [Mulungu] anati . . . udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” (Chilengezo chimenechi chapambuyo pa kuchimwa kwa Adamu ndi Hava sichinali mawu amene amuna ayenera kuchita koma chimene Yehova anadziŵiratu kuti iwo akachita chifukwa chakuti tsopano dyera linali mbali ya moyo waumunthu. Pambuyo pa zimenezo zolembedwa zingapo Zabaibulo zimasimba za mikhalidwe yomvetsa chisoni kwambiri imene inabuka chifukwa cha ulamuliro wadyera wotero wochitidwa ndi amuna. Koma Baibulo silimanena kuti Mulungu anavomereza mkhalidwe wotero kapena kuti ndiwo chitsanzo chooti ena atsatire.)
Kodi kupatsidwa umutu kwa amuna kumachepetsa akazi?
Kukhala pansi pa umutu mwa iko kokha sikumatanthauza kuchepetsedwa. Umutu umathandizira kusamalira zinthu mwa kakonzedwe ka dongosolo, ndipo Yehova ali ‘Mulungu osati wachisokonezo, koma wamtendere.’ (1 Akor. 14:33) Yesu Kristu ali pansi pa umutu wa Yehova Mulungu, ndipo amapeza chikhutiro chachikulu muunansi umenewo.—Yoh. 5:19, 20; 8:29; 1 Akor. 15:27, 28.
Umutu wocheperapo waperekedwanso kwa mwamuna, makamaka m’banja ndi mu mpingo Wachikristu. Mulungu sanapatse mwamuna ulamuliro wotheratu pamkazi; mwamuna ayenera kuyankha ku mutu wake, Yesu Kristu, ndi kwa Mulungu kaamba ka mmene akugwiritsira ntchito umutu wotero. (1 Akor. 11:3) Ndiponso, amuna akulamulidwa kuti “azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha” ndi ‘kuchitira ulemu’ akazi awo. (Aef. 5:28; 1 Pet. 3:7) Zofunika zamangaŵa aukwati za mwamuna siziyenera kukhala pamwamba pa za mkazi wake m’kakonzedwe ka Mulungu kwa okwatirana. (1 Akor. 7:3, 4) Ntchito ya mkazi waluso, monga momwe yalongosoledwera m’Baibulo, imagogomezera kufunika kwake kubanja ndi ku chitaganya. Imampatsa mpata waukulu umene angagwiritsiremo ntchito luso lake pamene akusonyeza ulemu wake kaamba ka umutu wa mwamuna wake. (Miy. 31:10-31) Baibulo limalamulira ana kulemekeza osati kokha atate wawo komanso amawo. (Aef. 6:1-3) Limaperekanso chisamaliro chapadera ku kusamalira zosoŵa za akazi amasiye. (Yak. 1:27) Motero pakati pa Akristu owona, akazi angadzipezere chitetezo chachikulu, ulemu wowona kaamba ka iwo eni monga anthu, ndi chikhutiro chawo muutumiki wawo.
Kulemekezeka kwa malo antchito a mkazi m’kakonzedwe ka Mulungu kwasonyezedwanso ndi chenicheni chakuti Yehova amatchula gulu lake la zolengedwa zauzimu zokhulupirika monga mzimayi, mkazi wake, mayi wa ana ake. (Chiv. 12:1; Agal. 4:26) Ndiponso, mpingo wa odzozedwa ndi mzimu wa Yesu Kristu umalankhulidwa monga mkwatibwi wake. (Chiv. 19:7; 21:2, 9) Ndipo m’lingaliro lauzimu palibe kusiyana pakati pa mwamuna ndi mkazi pakati pa oitanidwira kukhala ndi phande mu Ufumu wakumwamba limodzi ndi Kristu.—Agal. 3:26-28.
Kodi akazi ayenera kukhala aminisitala?
Awo opatsidwa uyang’aniro wampingo amafotokozedwa m’Baibulo kukhala amuna. Atumwi onse 12 a Yesu Kristu anali amuna, ndipo awo amene pambuyo pake anaikidwa kukhala oyang’anira ndi atumiki otumikira m’mipingo Yachikristu anali amuna. (Mat. 10:1-4; 1 Tim. 3:2, 12) Akazi amalangizidwa ‘kuphunzira ali chete ndi chigonjero chokwanira’ pamisonkhano yampingo, m’chakuti samadzutsa mafunso otsutsana ndi amuna mu mpingo. Akazi ‘sayenera kulankhula’ pamisonkhano yotero ngati zimene anganene zingasonyeze kusagonjera. (1 Tim. 2:11, 12; 1 Akor. 14:33, 34) Motero, ngakhale kuli kwakuti akazi akuthandizira kwambiri ntchito yampingo, palibe kakonzedwe kakuti iwo atsogoze, kapena kutsogolera mwa kulangiza mpingo, pamene amuna oyeneretsedwa alipo.
Koma kodi akazi angakhale alaliki, olengeza, aminisitala a mbiri yabwino, kunja kwa misonkhano yampingo? Pa Pentekoste wa 33 C.E. mzimu woyera unatsanuliridwa pa onse amuna ndi akazi omwe. Polongosola, mtumwi Petro anagwira mawu Yoweli 2:28, 29 kumati: “Kudzali m’masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira chamzimu wanga pathupi lirilonse, ndipo ana anu aamuna ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzawona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m’masiku awa, ndidzathira chamzimu wanga; ndipo adzanenera.” (Mac. 2:17, 18) Mofananamo, akazi lerolino moyenelera amakhala ndi phande muuminisitala Wachikristu, kulalikira kunyumba ndi nyumba ndi kuchititsa maphunziro Abaibulo apanyumba.—Wonaninso Salmo 68:11; Afilipi 4:2, 3.
Kodi nchifukwa ninji Akazi Achikristu amavala chophimba kumutu panyengo zina?
1 Akor. 11:3-10: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wamkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu. . . . Mkazi yense wa kupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake . . . Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wamwamuna. Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi, koma mkazi wa kwa mwamuna; pakutinso mwamuna sanalengedwa chifukwa cha mkazi; koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nawo ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.” (Pamene mkazi Wachikristu avala chophimba mutu panyengo zoyenerera, umenewu uli umboni wa kulemekeza kwake kakonzedwe kaumutu kamene kanayambidwa ndi Mulungu. Kristu amalemekeza umutu wateokratiki; mwamuna ndi mkazi alinso ndi thayo lakutero. Mwamuna woyamba, Adamu, sanakhaleko mwa kubadwa kupyolera mwa mkazi koma analengedwa ndi Mulungu. Polenga Hava, Mulungu anagwiritsira ntchito nthiti yochokera kwa Adamu monga maziko, ndipo Mulungu anafotokoza kuti iye anali wothangata wa Adamu. Chotero kwa mwamuna, amene analengedwa choyamba, kunagaŵiridwa malo antchito a kukhala mutu. Mwamunayo samavala chophimba mutu pamene ‘apemphera kapena kunenera’ chifukwa cha, kuchitira ulemu umutu, mwamuna ali “fanizo la Mulungu,” chifukwa chakuti alibe mutu wa padziko lapansi m’nkhani zokhudza banja lake. Komabe, kwa mkazi ‘kupemphera kapena kunenera’ popanda chophimba mutu kukakhala kunyozera malo antchito a mwamuna operekedwa ndi Mulungu ndipo kukachititsa mwamunayo manyazi. Ngakhale angelo, amene ali ziwalo za gulu lakumwamba longa mkazi la Yehova, amawona “chizindikiro cha ulamuliro” chovalidwa ndi akazi okhulupirika Achikristu ndipo amakumbutsidwa za kugonjera kwawo kwa Yehova.)
Kodi ndiliti pamene kuli kofunika kwa mkazi kuvala chophimba mutu?
‘Popemphera kapena ponenera,’ monga momwe kwafotokozedwera pa 1 Akorinto 11:5. Chimenechi sichitanthauza kuti chophimba mutu chiri chofunikira pamene apemphera yekha kapena pamene akambitsirana ndi ena ulosi Wabaibulo. Komabe, ayenera kuvala chophimba mutu chimenecho monga chizindikiro chakunja kaamba ka kuchitira ulemu kwake umutu wa mwamuna pamene iye asamalira nkhani zoloŵetsamo kulambira zimene kwenikweni zikanasamaliridwa ndi mwamuna wake kapena ndi mwamuna wina. Ngati apemphera mofuula kaamba ka iyemwini ndi ena kapena achititsa phunziro Labaibulo lanthaŵi zonse, mwa kutero kuphunzitsa, pamaso pa mwamuna wake, ayenera kuvala chophimba mutu, ngakhale ngati mwamunayo sakugaŵana naye chikhulupiriro chake. Koma popeza kuti ngovomerezedwa ndi Mulungu kuphunzitsa ana ake, palibe chophimba mutu chimene chiri chofunika popemphera kapena pophunzira ndi ana ake osadzipatulira panthaŵi zina pamene mwamuna wake palibe. Ngati, m’mikhalidwe yakamodzikamodzi, chiŵalo chodzipatulira champingo chiripo kapena pamene akuperekezedwa ndi woyang’anira woyendayenda wochezetsa, pamenepo, pamene achititsa phunziro Labaibulo lolinganizidwa pasadakhale ayenera kuphimba mutu wake, koma mbaleyo ayenera kupereka pemphero.
Kodi kuli koyenera kuti akazi adzole mafuta osalalitsa khungu kapena kuvala majuwelo?
2 Pet. 3:3, 4, NW: “Musalole kudzikometsera kwanu kukhala kuja kwakunja kwa kuluka tsitsi ndi kwa kuvala zokometsera zagolidi kapena kuvala zovala zakunja, koma kuloleni kukhale munthu wobisika wamtima wovala chovala chosavunda chamzimu wachete ndi wodekha, chimene chiri chamtengo waukulu m’maso mwa Mulungu.” (Kodi zimenezi zitanthauza kuti akazi sayenera kuvala zokometsera? Ndithudi ayi; monga momwedi mwachiwonekere kuliri kuti sikumatanthauza kuti iwo sayenera kuvala zovala zakunja. Koma panopa iwo akulimbikitsidwa kukhala odekha mumkhalidwe wawo wonena za kasamaliridwe katsitsi ndi kavalidwe, akumaika chigogomezero chachikulu pakudzikometsera kwauzimu.)
1 Tim. 2:9, 10: “Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya amtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomerezeka kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.” (Kodi nchiyani chimene chiri kanthu kwenikweni kwa Mulungu—mawonekedwe akunja a munthuyo kapena mkhalidwe wake wamtima? Kodi Mulungu akakondwera ngati mkazi sanadzole mafuta osalalitsa kapena kuvala majuwelo koma anakhala moyo wachisembwere? Kapena kodi iye angavomere akazi amene ali odekha ndi olama m’maganizo pogwiritsira ntchito kwawo mafuta osalalitsa ndi kuvala kwawo majuwelo ndi amene kwakukulukulu amadziveka ndi mikhalidwe yaumulungu ndi mkhalidwe Wachikristu? Yehova amati: “Pakuti Yehova sawona monga awona munthu; pakuti munthu ayang’ana chowoneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mu mtima.”—1 Sam. 16:7.)
Miy. 31:30: “Kukongola kungonyenga, mawonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi wowopa Yehova adzatamandidwa.”