ZAKUMAPETO
Kodi Mlongo Ayenera Kuvala Chinachake Kumutu pa Zochitika Ziti, Ndipo N’chifukwa Chiyani?
Pa nkhani ya kulambira, kodi mkazi wachikhristu ayenera kuvala chinachake kumutu pa zochitika ziti, ndipo n’chifukwa chiyani? Tiyeni tikambirane zimene mtumwi Paulo analemba pa nkhani imeneyi. Iye anapereka malangizo amene tifunikira kutsatira kuti tichite zinthu zoyenera, zimene zingalemekeze Mulungu. (1 Akorinto 11:3-16) Iye anatchula mfundo zitatu zofunika kuziganizira zomwe ndi: (1) zochita zimene zingapangitse kuti mkazi avale chinachake kumutu, (2) malo amene iye ayenera kuchitira zimenezi, ndipo (3) zifukwa zimene ayenera kumvera lamulo limeneli.
Zochita. Paulo anatchula zinthu ziwiri izi: Pemphero ndi kunenera. (Vesi 4 ndi 5) Pemphero limatanthauza kulankhula mwaulemu ndi Yehova. Masiku ano, kunenera kungatanthauze ntchito ina iliyonse yophunzitsa Baibulo imene mtumiki wachikhristu amachita. Kodi Paulo ankatanthauza kuti mkazi azivala chinachake kumutu nthawi zonse akafuna kupemphera kapena kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo? Ayi, sankatanthauza zimenezi. Nkhani yagona pa malo amene mkaziyo akupempherera kapena kuphunzitsira.
Malo. Mawu a Paulo akusonyeza malo awiri omwe ndi m’banja ndi mumpingo. Iye anati: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna . . . Mkazi aliyense amene akupemphera kapena kunenera osavala kanthu kumutu akuchititsa manyazi mutu wake.” (Vesi 3 ndi 5) M’banja, mwamuna ndi amene Yehova anam’patsa udindo kuti akhale mutu wa mkazi wake. Mkazi angachititse manyazi mwamuna wake ngati angagwire ntchito zimene Yehova anapereka kwa mwamunayo chifukwa zimenezi zingasonyeze kuti sakulemekeza udindo wa mwamuna wake. Mwachitsanzo, ngati m’pofunika kuti iye achititse phunziro la Baibulo pali mwamuna wake, angasonyeze kuti akulemekeza udindo wa mwamuna wake povala chinachake kumutu. Iye ayenera kuchita zimenezi kaya mwamunayo ndi wobatizidwa kapena ayi, chifukwa mwamunayo ndi mutu wa banja.a Ngati mkaziyo akupemphera kapena kuphunzitsa pali mwana wamng’ono wamwamuna koma wobatizidwa, ayenera kuvalabe chinachake kumutu. Ayenera kuchita zimenezi, osati chifukwa chakuti mwanayo ndi mutu wa banja, koma chifukwa cha udindo umene Yehova anapereka kwa amuna obatizidwa mumpingo wachikhristu.
Paulo anasonyezanso kuti mkazi ayenera kuvala chinachake kumutu mumpingo, pamene ananena kuti: “Ngati alipo wina amene akuoneka kuti akutsutsa zimenezi pofuna chikhalidwe china, ifeyo, monganso mipingo ya Mulungu, tilibe chikhalidwe chinanso.” (Vesi 16) Mumpingo wachikhristu, udindo wokhala mutu unaperekedwa kwa amuna obatizidwa. (1 Timoteyo 2:11-14; Aheberi 13:17) Amuna okha ndi amene amasankhidwa kukhala akulu ndi atumiki othandiza ndipo Mulungu amawapatsa udindo wosamalira gulu la nkhosa zake. (Machitidwe 20:28) Komabe, nthawi zina pangafunikire kuti mkazi wachikhristu agwire ntchito yoyenera kuchitidwa ndi m’bale wobatizidwa woyenerera. Mwachitsanzo, mlongo angafunikire kuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki wa kumunda chifukwa choti kumaloko kulibe m’bale wobatizidwa woyenerera, kapena pa nthawiyo m’bale woyenerera sanabwere. Kapenanso, angafunikire kuchititsa phunziro la Baibulo pali m’bale wobatizidwa.b Zimenezi ndi mbali ya ntchito yophunzitsa mumpingo wachikhristu, choncho iye ayenera kuvala chinachake kumutu posonyeza kuti akugwira ntchito imene kwenikweni ndi ya amuna.
Komabe, pali zinthu zina zokhudzana ndi kulambira zimene mlongo akamachita safunika kuvala chinachake kumutu. Mwachitsanzo, iye sangafunike kuvala chinthu kumutu akamayankha pamisonkhano yachikhristu, polalikira kunyumba ndi nyumba ali ndi mwamuna wake kapena m’bale wina wobatizidwa, kapenanso pophunzira ndi kupemphera ndi ana ake osabatizidwa. Komabe, pa nkhaniyi pangakhale mafunso ambiri ndipo ngati mlongo sakudziwa chochita pa nkhani inayake, ayenera kufufuza m’mabuku athu ena.c Ngati sakumvetsabe ndipo ngati chikumbumtima chake chikumuuza kuti avale chinachake kumutu, angachite bwino kutero, ngati mmene chithunzichi chikusonyezera.
Zifukwa. Pali zifukwa zimene mkazi wachikhristu ayenera kumvera lamulo limeneli. Pa vesi 10, pali zifukwa ziwiri. Vesili limati: “Mkazi ayenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro kumutu kwake chifukwa cha angelo.” Choyamba, onani kuti agwiritsa ntchito mawu akuti, “chizindikiro cha ulamuliro.” Kuvala chinachake kumutu ndi njira imene mkazi amasonyezera kuti amadziwa udindo umene Yehova anapereka kwa amuna obatizidwa mumpingo. Choncho, akamavala chinachake kumutu amasonyeza kuti amakonda Yehova Mulungu ndiponso ndi wokhulupirika kwa iye. Chifukwa chachiwiri chikupezeka m’mawu akuti, “chifukwa cha angelo.” Kodi mkazi akamavala chinachake kumutu, zimakhudza bwanji zolengedwa zauzimu zamphamvu zimenezi?
Angelo amasangalala akamaona kuti ulamuliro wa Mulungu ukulemekezedwa m’gulu lonse la Yehova, kumwamba ndi padziko lapansi. Iwonso amapindula ndi zitsanzo za anthu opanda ungwiro pa nkhani imeneyi chifukwa nawonso amafunika kugonjera ulamuliro wa Yehova. Ndipotu angelo ambiri anagonja atayesedwa pa nkhani imeneyi. (Yuda 6) Angelo amaphunzira zambiri akaona mkazi wachikhristu waluso, wodziwa zambiri ndiponso wanzeru kwambiri kuposa mwamuna wobatizidwa wa mumpingo, akugonjera ulamuliro wa mwamunayo. Nthawi zina mkaziyo angakhale Mkhristu wodzozedwa amene m’tsogolomu adzalamulire limodzi ndi Khristu. Mkazi ngati ameneyu adzakhala ndi udindo waukulu kuposa wa angelo chifukwa adzalamulira ndi Khristu kumwamba. Pamenepa angelo amaona chitsanzo chabwino kwambiri. Zoonadi, alongo onse ali ndi mwayi wapadera wosonyeza kumvera modzichepetsa, pokhala okhulupirika ndi ogonjera pamaso pa angelo okhulupirika ambirimbiri.
a Mkazi wachikhristu sayenera kupemphera mokweza mawu pali mwamuna wake wokhulupirira, pokhapokha ngati pali zifukwa zina zapadera. Mwachitsanzo, ngati mwamunayo wadwala moti sakulankhula.
b Mlongo sayenera kuvala chinachake kumutu ngati akuchititsa phunziro la Baibulo ali ndi mwamuna amene ndi wofalitsa wosabatizidwa amenenso si mwamuna wake.
c Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 2015 tsamba 30 ndi ya July 15, 2002 patsamba 26 mpaka 27.