Kodi Nchiyani Chimene Chiri Mfungulo ya Chikristu Chenicheni?
LEROLINO, anthu ambiri amanena kuti ali kumbali ya Chikristu kuposa gulu lina lirilonse lachipembedzo. Koma zikhulupiriro za odzitcha Akristu ameneŵa nzosemphana, alibe umodzi, ndipo nthaŵi zina amafikira pakuphana. Mowonekera bwino, ambiri sali Akristu enieni. Yesu ananena kuti m’tsiku lathu, ambiri akanena kwa iye, “Ambuye, Ambuye,” kunena m’mawu ena, akadzitcha kukhala Akristu, komabe iye akati kwa iwo: ‘Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.’ (Mateyu 7:21, 23) Zowonadi, palibe aliyense wa ife amene angakonde kukhala pakati pa ameneŵa! Chotero kodi tingadziŵe bwanji ngati ndife Akristu enieni?
Chenicheni nchakuti, pamafunikira zinthu zambiri kuti mukhale Mkristu weniweni. Mkristu weniweni ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa chakuti ‘wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Mulungu].’ (Ahebri 11:6) Chikhulupiriro cholimba chimenecho chiyenera kutsagana ndi ntchito zolungama. Wophunzira Yakobo anachenjeza kuti ‘chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.’ (Yakobo 2:26) Ndiponso, Mkristu ayenera kuzindikira ulamuliro wa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Koma mfungulo ya Chikristu chenicheni iri chinachake osati zinthu zimenezi.
Kodi mfunguloyo nchiyani? Mtumwi Paulo anafotokoza motere m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto: ‘Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziŵe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe chikondi, ndiri chabe. Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndiribe chikondi, sindipindula kanthu ayi.’—1 Akorinto 13:1-3.
Chotero chikondi ndicho mfungulo ya Chikristu chenicheni. Chikhulupiriro, ntchito, ndi mayanjano oyenera ziri zofunika, zosapeŵeka. Koma popanda chikondi, zimakhala zopanda phindu. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho?
Kwakukulukulu, chifukwa cha mtundu wa Mulungu amene timalambira. Mtumwi Yohane anamfotokoza Yehova, Mulungu wa Chikristu chowona, m’mawu aŵa: ‘Mulungu ndiye chikondi.’ (1 Yohane 4:8) Yehova Mulungu ali ndi mikhalidwe ina yambiri, monga ngati mphamvu, chiweruzo chachilungamo, ndi nzeru, koma popeza kuti kwakukulukulu ali Mulungu wachikondi, kodi ndi anthu amtundu wanji amene iye angafune kukhala olambira ake? Ndithudi, anthu amene amamtsanzira ndi kukulitsa chikondi.—Mateyu 5:44, 45; 22:37-39.
Cholinga Choyenera
Inde, chikondi chimapangitsa Akristu kukhala ofanana ndi Mulungu amene amamlambira. Chikutanthauza kuti zolinga zawo nzofanana ndi zolinga za Mulungu. Kodi ncholinga chotani pamwamba pa zonse chimene chinasonkhezera Yehova Mulungu kutumiza Yesu padziko lapansi ndikutipatsa mwaŵi wakukhala ndi moyo wamuyaya? Chikondi. ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike koma akhale nawo moyo wosatha.’ (Yohane 3:16) Pamenepo, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala cholinga chathu pochita chifuniro cha Mulungu? Kachiŵirinso, chikondi. ‘Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.’—1 Yohane 5:3.
Kodi nkotheka kutumikira Mulungu ndi cholinga choipa? Inde. Paulo anatchula anthu ena amene m’tsiku lake anali kutumikira chifukwa cha kaduka ndi ndewu. (Afilipi 1:15-17) Zimenezo zingatichitikire. Dzikoli liri la mpikisano wopambanitsa, ndipo mzimu umenewo ungatiyambukire. Tingakhale onyada kuganiza kuti ndife alankhuli abwinopo kapena kuti timagaŵira mabuku ambiri kuposa ena. Tingamayerekezere mwaŵi wathu wa utumiki ndi wa munthu wina ndikukhala wodzikuza—kapena kuchita kaduka. Mkulu angamachitire nsanje udindo wake waulamuliro, ngakhale kufikira pa kutsekereza mwamuna wachichepere wokhala ndi kukhoza kuti asapite patsogolo. Chikhumbo chakukhala ndi phindu laumwini chingatisonkhezere kupanga ubwenzi ndi Akristu achuma ndi kunyalanyaza osauka.
Zinthuzi zingachitike chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro. Komabe, ngati—mofanana ndi Yehova—tichipanga chikondi kukhala chisonkhezero chathu chachikulu, tidzalimbana ndi zikhoterero zoterozo. Dyera, chikhumbo chakudzilemekeza, kapena kunyada kwansontho zingatsekereze chikondi, kotero kuti ‘sitipindula kanthu ayi.’—Miyambo 11:2; 1 Akorinto 13:3.
Chikondi m’Dziko Ladyera
Yesu ananena kuti otsatira ake “sakhala a dziko lapansi.” (Yohane 17:14) Kodi tingapeŵe motani kungonjetsedwa ndi chisonkhezero cha dziko lotizinga? Chikondi chidzathandiza. Mwachitsanzo, lerolino anthu ali “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:4) Yohane anatichenjeza kuti tisakhale otero. Iye anati: ‘Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. Pakuti chirichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.’—1 Yohane 2:15, 16.
Komabe, sikuli kopepuka kukaniratu ‘chilakolako cha thupi’ ndi ‘chilakolako cha maso.’ Zinthu zimenezi zimakondedwa kwakukulukulu chifukwa chakuti zimasangalatsa thupi lathu. Ndiponso, lerolino pali zokondweretsa zambiri zosiyanasiyana kuposa zimene zinalipo m’nthaŵi ya Yohane, chotero ngati chilakolako cha maso chinali vuto panthaŵiyo, chiridi vuto lalikulu tsopano.
Mosangalatsa, zokondweretsa zambiri zamakono zimene dziko limapereka siziri zoipa mwa izo zokha. Palibe cholakwika ndi kukhala ndi nyumba yaikulu, galimoto labwino, wailesi yakanema, kapena stereo. Ndiponso kutenga maulendo aatali osangalatsa ndi matchuthi okondweretsa sikumaswa lamulo Labaibulo lirilonse. Pamenepo, kodi nchiyani chomwe chiri mfundo ya Yohane? Choyamba, ngati zinthu zoterozo zikhala zofunika koposa kwa ife, zimakulitsa mwa ife mzimu wa dyera, kukondetsa zinthu zakuthupi, ndi kunyada. Ndipo kuyesayesa kwakupeza ndalama zopezera zinthuzo kungatilepheretse muutumiki wathu kwa Yehova. Ngakhale kusangalala ndi zinthu zoterozo kumatenganso nthaŵi, ndipo pamene kuli kwakuti mlingo wabwino wakusanguluka umabweretsa mpumulo, nthaŵi yathu njochepa, polingalira za thayo lathu lakuphunzira Baibulo, kusonkhana ndi Akristu anzathu kaamba ka kulambira, ndi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.—Salmo 1:1-3; Mateyu 24:14; 28:19, 20; Ahebri 10:24, 25.
M’nyengo ino yokondetsa zinthu zakuthupi, kumatenga kutsimikiza mtima ‘kuthanga kufuna Ufumu wa Mulungu’ ndi kupeŵa ‘kuchititsa nalo dziko.’ (Mateyu 6:33; 1 Akorinto 7:31) Chikhulupiriro cholimba chidzathandiza. Koma makamaka chikondi chenicheni kaamba ka Yehova ndi anansi athu ndicho chidzatilimbitsa kupeŵa misampha, yomwe mwa iyo yokha singakhale yoipa, koma ingatilepheretse ‘kukwaniritsa utumiki wathu.’ (2 Timoteo 4:5) Popanda chikondi choterocho, uminisitala wathu ungakhale kuyesayesa wamba.
Chikondi Mumpingo
Yesu anagogomezera kufunika kwa chikondi pamene ananena kuti: ‘Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:35) Kodi nchifukwa ninji akulu akathera nthaŵi yaikulu motero kuŵeta ndi kuthandiza Akristu anzawo ngati samawakonda iwo? Kodi nchifukwa ninji mpingo ukapirira zofooka za anzawo—kuphatikizapo za akulu—ngati unalibe chikondi? Chikondi chimasonkhezera Akristu kuthandizana m’njira yakuthupi pamene amva kuti ena akusoŵa zinthu. (Machitidwe 2:44, 45) M’nthaŵi za chizunzo, Akristu amatetezerana ndipo ngakhale kuferana. Chifukwa ninji? Chifukwa cha chikondi.—Yohane 15:13.
Nthaŵi zina umboni waukulu koposa wa chikondi umachokera ku zinthu zazing’ono. Mkulu, yemwe ali kale pansi pa chitsenderezo chifukwa cha kuchuluka kwa ntchito, angafikiridwe ndi Mkristu mnzake amene abweretsanso dandaulo lomwe likuwonekera kukhala losafunika kwa mkuluyo. Kodi mkuluyo ayenera kukwiya? M’malo molola ichi kukhala chochititsa magaŵano, iye amachita moleza mtima ndi mwachifundo ndi mbale wake. Amakambitsirana nkhaniyo pamodzi, ndipo imalimbitsanso ubwenzi wawo. (Mateyu 5:23, 24; 18:15-17) M’malo moti aliyense aumirire pa zomuyenerera zake, onse ayenera kuyesayesa kukulitsa kuleza mtima kumene Yesu anakuyamikira, kukhala okonzekera kukhululukira abale awo kufikira ‘makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.’ (Mateyu 18:21, 22) Chotero, Akristu amayesayesa zolimba kudziveka chikondi pakuti, ‘ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.’—Akolose 3:14.
Kulimbitsa Chikondi Chathu kwa Wina ndi Mnzake
Inde, chikondi ndicho cholinga chabwino chotumikirira Yehova. Chikondi chimatilimbitsa kupitirizabe kusakhala a dziko, ndipo chikondi chidzatitsimikizira kuti mpingo ukhalebe Wachikristu weniweni. Pamene kuli kwakuti sichimacheutsa kukhoza kwathu, chidzatheketsa awo okhala ndi ulamuliro kusakhala okhutira kopambanitsa kwakuti achite kuiwala kusonyeza chifundo ndi kudekha pochita ndi ena. Chikondi chimatithandiza tonsefe ‘kumvera atsogoleri athu . . . ndi kuwagonjera.’—Ahebri 13:17.
Mtumwi Petro anatifulumiza kuti tiyenera kukhala nacho ‘chikondano chenicheni’ kwa wina ndi mnzake chifukwa chakuti ‘chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.’ (1 Petro 4:8) Kodi tingachite motani zimenezi? Munthu analengedwa m’chifanefane cha Mulungu ndipo chotero ali ndi kuthekera kwachibadwa kwa kukonda. Koma chikondi chimene tikulankhulapo pano chimafuna zina zowonjezereka. Kwenikwenidi, ndicho chipatso chachikulu cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Chotero, kuti tikulitse chikondi, tiyenera kudzipereka enife ku mzimu wa Mulungu. Motani? Mwakuphunzira Baibulo, lomwe linauziridwa ndi mzimu wa Yehova. (2 Timoteo 3:16) Mwakupempherera mzimu wa Yehova kuti umangirire chikondi chathu kwa Yehova ndi abale athu. Ndipo mwakuyanjana ndi mpingo Wachikristu, kumene mzimu wake umatsanulidwa popanda choletsa.
Timafunikiranso kudzisanthula enife kuwona machitidwe ndi malingaliro opanda chikondi aliwonse. Kumbukirani kuti, chikondi ndi mkhalidwe wa mtima, ndipo ‘mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.’ (Yeremiya 17:9) Mosasamala kanthu za chithandizo chonse chimene Yehova akupereka, nthaŵi zina tidzachita zinthu m’njira yopanda chikondi. Tingalankhule mwaukali mosayenerera kwa Mkristu mnzathu, kapena tingakwiye ndi kulipsira chinachake chimene chanenedwa. Chifukwa chake, tingachite bwino kubwereza pemphero la Davide lakuti: ‘Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndiri nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.’—Salmo 139:23, 24.
Monga momwe Baibulo limanenera kuti, ‘chikondi sichilephera.’ (1 Akorinto 13:8) Ngati timasonyeza chikondi kwa wina ndi mnzake, sitidzapereŵera pa nthaŵi ya chiyeso. Chikondi chomwe chiri pakati pa anthu a Mulungu chimathandiza kwakukulukulu kukhala ndi paradaiso wauzimu amene alipo lerolino. Kokha awo amene amakonda kwenikweni kuchokera mumtima ndiwo adzapeza chisangalalo kukhala m’dziko latsopano. Chifukwa chake, tsanzirani Yehova m’kusonyeza chikondi choterocho ndipo limbitsani chomangira cha umodzi. Kulitsani chikondi, ndipo khalani ndi mfungulo ya Chikristu chenicheni.