Tsatirani Njira Yopambana ya Chikondi
YEHOVA MULUNGU iyemwiniyo ndiye chikondi. (1 Yohane 4:8) Mwana wake, Yesu Kristu, ananena kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi mnansi wathu. (Mateyu 22:37-40) Eya, Mulungu amayendetsa chilengedwe chonse pamaziko a mkhalidwe umenewu! Chotero kaamba ka moyo wamuyaya kulikonse, tiyenera kutsatira njira ya chikondi.
Mulungu anasonyeza chikondi kumtundu wa Israyeli koma pambuyo pake anakana gulu limenelo chifukwa cha kusakhulupirika. Iye kenako anasonyeza mpingo wa ophunzira a Yesu kukhala gulu Lake latsopano. Motani? Mwa zisonyezero zapadera za mzimu woyera ukumawapatsa mphamvu za kulankhula m’malilime ndi kulosera. Chotero, pa Pentekoste wa 33 C.E., Ayuda ndi otembenuka 3,000 anafikira kukhala okhulupirira ndipo anasiya gulu lakale moyanja la Mulungu latsopanolo. (Machitidwe 2:1-41) Popeza kuti mphatso za mzimu pambuyo pake zinaperekedwa kupyolera mwa atumwi a Yesu, zizindikirozo zinalekeka iwo atafa. (Machitidwe 8:5-18; 19:1-6) Koma podzafika panthaŵiyo mphatsozo zinali zitatsimikizira kuti chiyanjo cha Mulungu chinali pa Israyeli wauzimu.—Agalatiya 6:16.
Zozizwitsa zochititsidwa ndi mphatso za mzimu zinali zopindulitsa. Komabe, kusonyeza chikondi kapena kuderera nkhaŵa ena mopanda dyera nkofunika kwambiri koposa kukhala ndi mphatso za mzimu. Mtumwi Paulo anasonyeza zimenezi m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto (c. 55 C.E.). Mmenemo iye analankhula za chikondi monga “njira yokoma yoposatu.” (1 Akorinto 12:31) Njira imeneyo yakambitsiridwa mu 1 Akorinto chaputala 13.
Popanda Chikondi, Tiri Chabe
Paulo anapereka chigomeko chakuti: “Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa wowomba, kapena nguli yolira.” (1 Akorinto 13:1) Popanda chikondi, sikukanatanthauza kanthu kulankhula m’chinenero chaumunthu choperekedwa ndi mzimu kapena m’lilime la angelo akumwamba. Paulo anasankha kulankhula mawu olimbikitsa asanu mmalo mwa okwanira zikwi khumi m’lilime limene anthu sanazindikire. (1 Akorinto 14:19) Munthu wopanda chikondi angakhale wofanana ndi “mkuwa wowomba”—belu laphokoso, losautsa—kapena “nguli yolira” popanda mang’ombe. Kulankhula m’malilime kopanda chikondi sikunali njira yotonthoza, yolimbikitsa mwauzimu yolemekezera Mulungu ndi kuthandizira anthu ake. Lerolino, timasonyeza chikondi mwa kugwiritsira ntchito mawu ozindikirika muuminisitala Wachikristu.
Mtumwiyo kenako anati: “Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziŵe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe chikondi, ndiri chabe.” (1 Akorinto 13:2) Kunenera kozizwitsa, chidziŵitso chapadera cha zinsinsi zopatulika, ndi nzeru zoperekedwa ndi mzimu zingapindulitse ena koma osati awo amene ali ndi mphatsowo ngati eni mphatsozo analibe chikondi. Paulo anagwiritsira ntchito chidziŵitso chapadera cha zinsinsi zopatulika kuthandiza ena, ndipo mphatso ya nzeruyo inamkhozetsa kuneneratu za kupulumuka kwa mikhole yoswekeredwa ngalawa. (Machitidwe 27:20-44; 1 Akorinto 4:1, 2) Komabe, ngati anali ndi ‘nzeru zonse ndi chikhulupiriro chonse’ koma analibe chikondi, akakhala chabe m’maso mwa Yehova.
Lerolino, mzimu wa Yehova umakhozetsa Mboni zake kuzindikira maulosi Abaibulo ndi zinsinsi zopatulika niuwatsogoza popatsa ena chidziŵitso choterocho. (Yoweli 2:28, 29) Mzimuwo umapatsanso chikhulupiriro chofunikira kugonjetsa zopinga zonga mapiri. (Mateyu 17:20) Popeza kuti mzimu umachita zinthu zimenezi, nkulakwa kupeza ulemerero waumwini mu izo. Ndife chabe kusiyapo ngati timachita zinthu kaamba ka ulemerero wa Mulungu ndi kaamba ka kumkonda kwathu ndi anthu anzathu.—Agalatiya 5:6.
Sitipindula ndi Nsembe Yopanda Chikondi
Paulo anati: “Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndiribe chikondi, sindipindula kanthu ayi.” (1 Akorinto 13:3) Popanda chikondi, Paulo sakanapindula ngati anapereka kanthu kalikonse kamene anali nako kudyetsa ena. Mulungu amatifupa kaamba ka chikondi chochititsa mphatso zathu, osati kaamba ka mtengo wake kapena chifukwa chakuti tikufunafuna ulemelero monga opatsa, monga Hananiya ndi Safira onamawo. (Machitidwe 5:1-11) Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri mwa kudzipereka iyemwini mwachikondi ponena za uminisitala wachithandizo kwa okhulupirira a m’Yudeya.—1 Akorinto 16:1-4; 2 Akorinto 8:1-24; 9:7.
Ngakhale kufera chikhulupiriro kopanda chikondi monga mboni ya chowonadi sikumatanthauza kanthu kwa Mulungu. (Miyambo 25:27) Yesu analankhula za nsembe yake koma sanadzitame nayo. Mmalo mwa kudzitama iye anadzipereka mofunitsitsa chifukwa cha chikondi. (Marko 10:45; Aefeso 5:2; Ahebri 10:5-10) Abale ake auzimu ‘amapereka matupi awo monga nsembe yamoyo’ muutumiki wa Mulungu osati m’kufera chikhulupiriro kodzilemekeza koma m’njira zosadziwonetsera zimene zimalemekeza Yehova ndi kuchitira chitsanzo chikondi chawo pa iye.—Aroma 12:1, 2.
Njira Zina Zimene Chikondi Chidzatipangitsa Kuchitapo Kanthu
Paulo analemba kuti: “Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima.” (1 Akorinto 13:4a) Kwa ambiri, kuleza mtima kwa Mulungu chiyambire kuchimwa kwa Adamu kwatanthauza kulapa kotsogolera kuchipulumutso. (2 Petro 3:9, 15) Ngati tiri ndi chikondi, moleza mtima tidzaphunzitsa ena chowonadi. Tidzapewa kunyanyuka mwaukali ndipo tidzakhala olingalira ndi okhululukira. (Mateyu 18:21, 22) Chikondi chirinso chokoma mtima, ndipo timakopedwera kwa Mulungu chifukwa cha kukoma mtima kwake. Chipatso cha mzimu wake cha kukoma mtima chimatipangitsa kusafunsira zambiri kwa ena koposa zimene iye amachita kwa ife. (Aefeso 4:32) Chikondi chimatipangadi kukhala okoma mtima kwa anthu osayamikira.—Luka 6:35.
Paulo anawonjezera kuti: “Chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.” (1 Akorinto 13:4b) Nsanje ndintchito yathupi imene idzalepheretsa munthu kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (Agalatiya 5:19-21) Chikondi chimatipangitsa kusachitira nsanje chuma cha munthu wina kapena mikhalidwe yomuyanja. Ngati alandira mwaŵi wautumiki umene ife tinafuna, chikondi chidzatipangitsa kukondwera limodzi naye, kumchirikiza, ndi kuthokoza Mulungu kuti iye angagwiritsiridwe ntchito kupindulitsa mpingo.
Popeza kuti chikondi “sichidziŵa kudzitamanda,” sichimatisonkhezera kudzitama ndi zimene Mulungu amatilola kuchita muutumiki wake. Akorinto ena anadzitamanda monga ngati kuti ndiwo anayambitsa mphatso zamzimu, koma zimenezi zinachokera kwa Mulungu, monga momwe mwaŵi m’gulu lake lamakono uliri. Pamenepa, mmalo mwa kudzitamanda kaamba ka malo athu m’gulu la Mulungu, tichenjere kuti sitikugwa. (1 Akorinto 1:31; 4:7; 10:12) Chikondi “sichidzikuza,” koma maganizo a munthu wopanda chikondi angatukumuke ndi kudziwona kukhala wofunika. Anthu achikondi samadzilingalira kukhala apamwamba koposa ena.—1 Akorinto 4:18, 19; Agalatiya 6:3.
Sichichita Zosayenera, Zadyera, Zopsa Mtima
Chikondi “sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima.” (1 Akorinto 13:5a) Chimapititsa patsogolo makhalidwe abwino, kudzisungira kwaumulungu, kulemekeza ulamuliro, ndi mkhalidwe woyenera pamisonkhano Yachikristu. (Aefeso 5:3-5; 1 Akorinto 11:17-34; 14:40; yerekezerani ndi Yuda 4, 8-10.) Popeza kuti chikondi chimapangitsa aliyense kumva kukhala wofunika, mofanana ndi ziwalo zonse za thupi laumunthu, mpingo wachikondi ndimalo amtendere ndi ngaka. (1 Akorinto 12:22-25) Mmalo mwa ‘kungofunafuna mwadyera zochikomera,’ chikondi chimatipangitsa kulepa zimene tiri ndi kuyenera kwake panthaŵi zina ndi kusonyeza chikondwerero mwa ena ndi zowakomera. (Afilipi 2:1-4) Chikondi chimatipangitsa ‘kukhala zinthu zonse kwa anthu a mitundu yonse, kotero kuti mwina tingapulumutse ena’ mwa uminisitala wathu.—1 Akorinto 9:22, 23.
Chikondi “sichipsa mtima.” Zopsa mtima ndizo ntchito za thupi lauchimo, koma chikondi chimatipangitsa kukhala “odekha pakupsa mtima.” (Yakobo 1:19; Agalatiya 5:19, 20) Ngakhale ngati tiri ndi chifukwa chabwino chokwiyira, chikondi sichimatilola kukhalabe okwiya, chotero kumpatsa malo Mdyerekezi. (Aefeso 4:26, 27) Akulu makamaka ayenera kupewa mkwiyo ngati okhulupirira anzawo alephera kugwiritsira ntchito malingaliro akutiakuti.
Paulo anatinso ponena za chikondi: “Sichilingilira zoipa.” (1 Akorinto 13:5b) Chikondi sichimasunga mpambo wa zolakwa, monga zolembedwa m’bukhu la maakaunti. Chimawona zabwino mwa okhulupirira anzathu ndipo sichimalipsira zolakwa zenizeni kapena zoyerekezera. (Miyambo 20:22; 24:29; 25:21, 22) Chikondi chimatithandiza ‘kulondola zinthu za mtendere.’ (Aroma 14:19) Paulo ndi Barnaba anali ndi mkangano ndipo analekana muutumiki wa Mulungu, koma chikondi chinathetsa kusamvanako nichinawapangitsa kusasungirana kanthu kukhosi.—Levitiko 19:17, 18; Machitidwe 15:36-41.
Chimakonda Chilungamo ndi Chowonadi
Ponena za chikondi, Paulo anapitirizabe kunena kuti: “Sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi chowonadi.” (1 Akorinto 13:6) Ena amakondwera kwambiri ndi chisalungamo kotero kuti “akapanda kuchita zoipa samagona.” (Miyambo 4:16) Koma m’gulu la Mulungu sitimavutana kapena kukondwera ngati wina wakodwa muuchimo. (Miyambo 17:5; 24:17, 18) Ngati munali chikondi chokwanira cha pa Mulungu ndi chilungamo mumpingo wa ku Korinto, mwenzi chisembwere sichinaloledwe mmenemo. (1 Akorinto 5:1-13) Pakati pa zinthu zina, kukonda chilungamo kumatipangitsa kusasangalala ndi wailesi yakanema, akanema, kapena zosonyezedwa m’mabwalo amasewera osalungama.
Chikondi “chikondwera ndi chowonadi.” Panopa chowonadi chikusiyanitsidwa ndi chinyengo. Zimenezi mwachiwonekere zimatanthauza kuti chikondi chimatipangitsa kukondwera ndi chisonkhezero chachilungamo chimene chowonadi chiri nacho pa anthu. Timapeza chisangalalo m’zinthu zimene zimalimbikitsa anthu ndi zimene zimapititsa patsogolo chowonadi ndi chilungamo. Chikondi chimatipangitsa kusalankhula bodza, chimatipatsa chisangalalo pamene owongoka atsimikiziridwa kukhala opanda liwongo, ndi kutipangitsa kukondwera m’chilakiko cha chowonadi cha Mulungu.—Salmo 45:4.
Mmene Chikondi Chimachitira ndi Zinthu Zonse
Akumapitiriza kufotokoza kwake chikondi, Paulo analemba kuti: “Chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) ‘Chikumakwirira zinthu zonse,’ chikondi chimapewa mkwiyo monga momwe tsindwi labwino limachitira mvula. Ngati wina aliyense atikhumudwitsa komano apempha chikhululukiro, chikondi chimatipangitsa kupirira zopweteka, tikumakhululukira wotiputayo mmalo mwa kudyera miseche ponena za nkhaniyo. Mwachikondi timayesa ‘kubweza mbale wathu.’—Mateyu 18:15-17; Akolose 3:13.
Chikondi “chikhulupirira zinthu zonse” zimene ziri m’Mawu a Mulungu ndi kutipangitsa kukhala oyamikira kaamba ka chakudya chauzimu choperekedwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Ngakhale kuti sitiri otengeka maganizo, chikondi chimatipangitsa kusakhala ndi mtima wosakhulupirira ndi kutipangitsa kupewa kupereka malingaliro oipa kwa okhulupirira anzathu. (Mlaliki 7:21, 22) Ndiponso chikondi “chikhulupirira zinthu zonse” zolembedwa m’Malemba, zonga chowonadi chonena za Ufumu wa Mulungu. Mosonkhezeredwa ndi chikondi, timayembekezera ndi kupempherera zotulukapo zabwino m’mikhalidwe yopereka chiyeso. Chikondi chimatisonkhezeranso kuuza ena chifukwa cha chiyembekezo chathu. (1 Petro 3:15) Ndiponso, chikondi “chipirira zinthu zonse,” kuphatikizapo kuchimwiridwa kwathu. (Miyambo 10:12) Kukonda Mulungu kumatithandizanso kupirira chizunzo ndi ziyeso zina.
Paulo anawonjezera kuti: “Chikondi sichitha nthaŵi zonse.” (1 Akorinto 13:8a) Sichingathe konse kapena kulephera monga momwe Yehova samalephelera. Popeza kuti Mulungu wathu wamuyaya ndiye chisonyezero chenicheni cha chikondi, mkhalidwe umenewu sudzatha konse. (1 Timoteo 1:17; 1 Yohane 4:16) Chilengedwe nthaŵi zonse chidzalamuliridwa ndi chikondi. Chifukwa chake tiyenitu tipemphere kuti Mulungu atithandize kugonjetsa zikhoterero zadyera ndi kusonyeza chipatso chosalephera cha mzimu wake chimenechi.—Luka 11:13.
Zinthu Zimene Zinali Kudzatha
Akumasonya mtsogolo, Paulo analemba kuti: “Koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.” (1 Akorinto 13:8b) ‘Mphatso zonenera zinakhozetsa okhala nazo kunenera maulosi atsopano. Ngakhale kuti mphatso zoterozo zinatha pambuyo poti mpingo Wachikristu wakhazikitsidwa monga gulu la Mulungu, mphamvu yake yaulosi siimatha konse, ndipo Mawu ake ali ndi ulosi wonse umene tsopano tifunikira. Luso loperekedwa ndi mzimu la kulankhula m’malilime nalonso linatha, ndipo nzeru zapadera “zinakhala chabe,” monga momwe kunanenedweratu. Koma Mawu achikwanekwane a Yehova amapereka zimene tifunikira kudziŵa kaamba ka chipulumutso. (Aroma 10:8-10) Ndiponso, anthu a Mulungu ngodzazidwa ndi mzimu wake ndipo amabala chipatso chake.
Paulo anapitirizabe kuti: “Pakuti ife tidziŵa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.” (1 Akorinto 13:9, 10) Mphatso za nzeru ndi ulosi zinali zosakwanira. Mwachiwonekere, ulosi woterowo sunali wachikwanekwane, ndipo mneneri aliyense anali wosakwanira povumbula za mtsogolo, pokhala wopanda chidziŵitso chokwanira chonena za zimene analosera. Komabe, tsopano, kuzindikiridwa kwa ulosi kukufikira kukhala kokwanira mwapang’onopang’ono. Mwachitsanzo, maumboni okwaniritsa ulosi Wabaibulo amatsimikizira kuti Yesu analandira ulamuliro waufumu pa mtundu wa anthu mu 1914. Chiyambire panthaŵiyo, takhala tiri mu “nthaŵi ya chimariziro” ndipo tikusangalala ndi kukula kosalekeza kwa nzeru ndi chidziŵitso chauzimu cha ulosi Wabaibulo. (Danieli 12:4) Chotero, kufikira chidziŵitso chokwanira ndi “changwiro” kuyenera kukhala pafupi.
Mkhalidwe Waukulu Kopambana Utsala
Akumatchula kupita patsogolo kwa mpingo, Paulo analemba kuti: “Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinaŵerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.” (1 Akorinto 13:11) Popeza kuti khanda limachita pamaziko a chidziŵitso chochepa ndi kukula kwakuthupi, angapeyulidwe chauku ndi chauko, monga ngati kuti akukankhidwira chauko ndi chauko pakama wakhanda. Koma mwamuna ngwokula msinkhu koposerapo, ali ndi chidziŵitso chokulirapo, ndipo kaŵirikaŵiri samapeyulidwa mosavuta. Iye anasiya malingaliro, makhalidwe, ndi njira zachibwana. Mofananamo, gulu lapadziko lapansi la Mulungu litakula ndi kusakhalanso lakhanda, Iye anawona kuti silinafunikire mphatso za mzimu za kunenera, malilime, ndi nzeru. Ngakhale kuti ziŵalo zamakono zampingo, zimene tsopano zakalamba, nazonso sizikuwona kufunikira kwa mphatso zoterozo, nzachimwemwe kutumikira Mulungu motsogozedwa ndi mzimu wake.
Paulo anawonjezera kuti: “Pakuti tsopano tipenya m’kalilole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.” (1 Akorinto 13:12) Muukhanda wampingo, siinali nthaŵi ya Mulungu kuvumbula zinthu zina. Chotero, izo zinawonedwa m’chimbuuzi, monga ngati kuti Akristu anali kuyang’ana pakalilole wamkuwa wopanda mkhalidwe weniweni wagalasi. (Machitidwe 1:6, 7) Koma tapambana mawonekedwe a chimbuuzi. Tsopano kukwaniritsidwa kwa ulosi ndi zizindikiro nkwachiwonekere kwambiri, popeza kuti ino ndinthaŵi ya Mulungu ya chivumbulutso. (Salmo 97:11; Danieli 2:28) Ngakhale kuti Paulo iyemwiniyo anadziŵa Mulungu, kudziŵa Yehova mwachikwanekwane ndi unansi wapafupi ndi Iye zikadza pamene mtumwiyo akaukitsidwira ku moyo wakumwamba, chotero akumalandira mphotho yokwanira ya njira yake Yachikristu.
Akumatsiriza kutanthauzira kwake chisonyezero cha chikondi, Paulo analemba kuti: “Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.” (1 Akorinto 13:13) Mosasamala kanthu za kusakhalapo kwa mphatso zozizwitsa za mzimu, mpingo tsopano uli ndi chidziŵitso chokwanira ndi chifukwa chokhalira ndi chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chikondi zokulirapo. Uli ndi chikhulupiriro chakuti chirichonse chimene Mulungu walonjeza chiri monga ngati kuti chakwaniritsidwa kale. (Ahebri 11:1) Mbali za chikhulupiriro zidzatha pamene zinthu zonenedweratu m’Mawu a Mulungu zikwaniritsidwa. Mbali za chiyembekezo zidzaleka pamene tiwona zinthu zoyembekezeredwa. Koma chikondi chidzakhalabe kosatha. Chotero, Mboni za Yehova zonse zipitirizetu kutsatira njira yopambana ya chikondi.