Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
“Ngati . . . alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, . . . zobisika za mtima wake ziwonetsedwa, ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi nadzagwadira Mulungu.”—1 AKORINTO 14:24, 25.
1-3. Ndimotani mmene ambiri mu Korinto anathandizidwira kupeza chivomerezo cha Mulungu?
PA ULENDO wake wachiŵiri wa umishonale, mtumwi Paulo anakhala mu mzinda wa Korinto kwa chaka chimodzi ndi theka. Kumeneko iye anali “[wotanganitsidwa kotheratu ndi mawu, kuchitira umboni, NW].” Ndi chotulukapo chotani? “Akorinto ambiri anamva nakhulupirira nabatizidwa.” (Machitidwe 18:5-11) Iwo anakhala “oyeretsedwa . . . , oitanidwa akhale oyera mtima.”—1 Akorinto 1:2.
2 Apolo pambuyo pake anachezera Korinto. Kumayambiriro, Priskila ndi Akula anamthandiza iye kumvetsetsa “njira ya Mulungu mosamalitsa,” kuphatikizapo nkhani ya ubatizo. Iye chotero anakhala Mkristu wokhala ndi kukondwera kwa Mulungu kapena chivomerezo. (Machitidwe 18:24–19:7) Apolo, pambuyo pake, anathandiza Akorinto omwe poyambapo ‘anatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula.’ (1 Akorinto 12:2) Anthu amenewa mwachidziŵikire anapatsidwa chilangizo cha m’Baibulo m’nyumba zawo; iwo akaphunziranso mwa kupezeka pa misonkhano Yachikristu.—Machitidwe 20:20; 1 Akorinto 14:22-24.
3 Chotulukapo cha kuphunzitsa koteroko chinali chakuti omwe kalelo anali ‘osakhulupirira ndi anthu osaphunzira’ anakokeredwa ku kulambira kowona. Chingakhale chinali chokhutiritsa chotani nanga kuwona amuna ndi akazi akukpita patsogolo kulinga ku ubatizo ndi chivomerezo cha Mulungu! Ichi chidakali chokhutiritsa.
Kuthandiza ‘Osakhulupirira ndi Anthu Osaphunzira’
4. Ndi mwanjira zotani mmene ambiri lerolino akuthandizidwira monga mmene analiri awo a mu Korinto?
4 Mboni za Yehova lerolino zikumveranso lamulo la Yesu la “kupanga ophunzira a mitundu yonse, kuwabatiza iwo.” (Mateyu 28:19, 20) Pambuyo pa kudzala mbewu za chowonadi m’mitima yovomereza, iwo amabwerera ndi kuthirira izo. (1 Akorinto 3:5-9; Mateyu 13:19, 23) Mbonizo zimagawira maphunziro a Baibulo a panyumba aulere a mlungu ndi mlungu kotero kuti anthuwo angakhale ndi mafunso awo atayankhidwa ndipo angaphunzire zowonadi za Baibulo. Anthu oterowo amaitanidwanso kukapezeka pa misonkhano ya kumaloko ya Mboni za Yehova, mongadi mmene “osakhulupirira” a m’zana loyamba anapezekera mu Korinto. Koma kodi ndimotani mmene Mboni za yehova zimawonera anthu omwe akuphunzira Baibulo ndi kubwera ku misonkhano?
5. Ndi maziko a m’Malemba otani amene alipo kaamba ka kuchenjera m’kuchita ndi anthu ena?
5 Tiri osangalatsidwa kuwona iwo akufikira Mulungu. Komabe, timasunga m’maganizo kuti iwo adakali akhulupiriri osabatizidwa. Sunganinso m’maganizo maphunziro aŵiri ozikidwa pa nkhani yapitayo. (1) Aisrayeli anasonyeza kuchenjera kulinga ku nzika zachilendo zomwe, ngakhale kuti zinali zozunguliridwa ndi anthu a Mulungu ndipo zinali kumvera ku malamulo ena, anali atembenuki osadulidwa, abale m’kulambira. (2) Akristu a ku Korinto ochita ndi ‘osakhulupirira ndi anthu osaphunzira’ anali ogalamuka chifukwa cha mawu a Paulo: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana. Pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama?”—2 Akorinto 6:14.
6. Ndimotani mmene “osakhulupirira” angakhalire “odzudzulidwa” ndi misonkhano, ndipo nchiyani chomwe chiri mtundu wa chidzudzulo choterocho?
6 Chotero pamene timalandira ‘osakhulupirira ndi anthu osaphunzira,’ timazindikira kuti iwo samakwaniritsabe miyezo ya Mulungu. Monga mmene Baibulo limasonyezera pa 1 Akorinto 14:24, 25, oterowo amafunikira “[kusanthulidwa mosamalitsa, NW],” ngakhale “[kudzudzulidwa, NW],” ndi zimene akuphunzira. Chidzudzulo choterocho sichiri cha mtundu wa chiweruzo; iwo samaitanidwa pamaso pa komiti ya chiweruzo ya mpingo mongadi mmene iwo sali ziwalo zobatizidwa za iwo. M’malomwake, monga chotulukapo cha chimene iwo akuphunzira, achatsopano amenewa amakhala okhutiritsidwa kuti Mulungu amatsutsa njira zadyera zonse ndi za makhalidwe oipa.
7. Ndi kupita patsogolo kowonjezereka kotani kumene ophunzira ambiri afunikira kupanga ndipo nchifukwa ninji?
7 Osabatizidwa ambiri m’kupita kwa nthaŵi angafune kupita kupyola pa kupezeka kokha pa misonkhano monga ophunzira okondweretsedwa. Mawu a Yesu awa amasonyeza chifukwa chake: “Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma yense mmene atakonzedwa mtima adzafanana ndi mphunzitsi wake.” (Luka 6:40) Wophunzira Baibulo angawone kuti mphunzitsi wake amawona utumiki wa m’munda monga wofunika koposa ndipo amapeza chimwemwe kuchokera ku iwo. (Mateyu 24:14) Chotero, ndi chikhulupiriro chomakulakula, mmodzi amene wakhala akuphunzira zowonadi za Baibulo ndi kupezeka pa misonkhano angatenge ku mtima mawu awa: “Ha, akongolatu pa mapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso.” (Yesaya 52:7; Aroma 10:13-15) Ngakhale kuti sanabatizidwe, iye angafune kukhala wofalitsa wa Ufumu kudzimamatiritsa iyemwini ku mpingo wa Mboni za Yehova.
8, 9. (a) Nchiyani chomwe chiyenera kuchitidwa pamene wophunzira Baibulo afuna kugawana mu utumiki wapoyera? (b) Pamene akulu aŵiri akumana ndi woyembekezera kukhala wofalitsa ndi m’phunzitsi wake, nchiyani chomwe iwo adzachita? (c) Ndi thayo lotani limene wofalitsa wachatsopanoyo akutenga?
8 Pamene Mboni yotsogoza phunziro la Baibulo ipeza kuti wophunzirayo akukhumba kugawana mu utumiki wa m’munda, iye angakambitsirane nkhaniyo ndi woyang’anira wotsogoza, yemwe adzakonza kaamba ka akulu aŵiri kukumana ndi wophunzira Baibuloyo ndi mphunzitsi wake. Akuluwo ali osangalatsidwa pamene wachatsopano afuna kutumikira Mulungu. Iwo sadzayembekezera iye kukhala ndi ukulu wa chidziŵitso chokhala ndi awo omwe ali obatizidwa ndi opita patsogolo kwenikweni m’chowonadi, kwa amene zowonjezereka zimafunikira. Komabe, akuluwo adzafunikira kuwona kuti wachatsopanoyo asangawane mu utumiki wa m’munda ndi mpingo, iye ali ndi chidziŵitso chinachake cha ziphunzitso za Baibulo ndipo wasinthira moyo wake ku maprinsipulo a Mulungu. Chotero chiri kaamba ka zifukwa zabwino kuti akulu aŵiri akumane ndi woyembekezera kukhala wofalitsayo ndi Mboni yotsogoza phunziroyo.a
9 Akulu aŵiriwo adzadziŵitsa wophunzirayo kuti pamene iye ayeneretsedwa kaamba ka kugawana mu utumiki wa m’munda, iye angapereke ripoti la utumiki wam’munda ndipo kardi la Cholembera cha Wofalitsa wa Mpingo lidzapangidwa m’dzina lake. Ichi chidzachitira chitsanzo kugwirizana kwake ndi gulu la teokratiki la Mboni za Yehova ndi kugonjera kwake ku ilo. (Ichi chikakhalanso chowona ponena za ena onse opereka maripoti a utumiki wa m’munda.) Kukambitsiranako kuyeneranso kukwaniritsa uphungu wa Baibulo, wonga ngati uja wondandalitsidwa pa masamba 98 ndi 99 a Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu.b Chotero, iyi ikakhala nthaŵi yoyenera kwa wophunzirayo kupeza kope laumwini la bukhu limenelo.
10. (a) Ndimotani mmene wofalitsa wosabatizidwa angapitirizire kupita patsogolo, ndipo ndi chonulirapo chotani? (b) Nchifukwa ninji kuwongolera kukupangidwa ponena za liwu lakuti “tsamwali wovomerezedwa”? (Onani mawu a m’munsi.)
10 Munthu yemwe wayeneretsedwa monga wofalitsa wosabatizidwa wa mbiri yabwino wasinthira ku chitsogozo cha kukhala ‘munthu wokondwera.’c (Luka 2:14) Ngakhale kuti iye sanadzipereke ndi kubatizidwa, tsopano iye angachitire ripoti ntchito yake yochitira umboni limodzi ndi mamiliyoni ena okangalika pa dziko lonse omwe “akubukitsa mawu a Mulungu.” (Machitidwe 13:5; 17:3; 26:22, 23) Chilengezo chakuti iye ali wofalitsa watsopano wosabatizidwa chingapangidwe ku mpingo. Iye ayenera kupitirizabe kuphunzira Baibulo, kutengamo mbali mu misonkhano, kugwiritsira ntchito chimene akuphunzira, ndi kugawana icho ndi ena. Pasanapite nthaŵi yaitali, iye akafuna kutenga sitepi la ubatizo Wachikristu, mwakutero kukhala wovomerezedwa ndi Mulungu ndi ‘kuikidwa chizindikiro’ kaamba ka chipulumutso.—Ezekieli 9:4-6.
Thandizo kaamba ka Yemwe Amachimwa
11. Ndimotani mmene mpingo umachitira ndi ochita cholakwa obatizidwa?
11 M’nkhani yapitayo, tinakambitsirana za makonzedwe a mpingo a kuthandiza Mkristu aliyense wosabatizidwa yemwe amachita chimo lalikulu. (Ahebri 12:9-13) Ndipo tinawona kuchokera m’Baibulo kuti ngati wochita cholakwa wobatizidwa ali wosalapa, mpingo ungafunikire kumuchotsa iye ndipo pambuyo pake kupewa mayanjano alionse ndi iye. (1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11; 2 Atesalonika 2:11, 12) Ndi masitepi otani, ngakhale ndi tero, amene angatengedwe ngati wofalitsa wosabatizidwa achita cholakwa chokulira kapena kuchimwa?
12. (a) Nchifukwa ninji thandizo lachifundo liriponso kaamba ka ofalitsa osabatizidwa ochimwa? (b) Ndimotani mmene prinsipulo la pa Luka 12:48 limagwirira ntchito ku kuwerengera kaamba ka kuchita cholakwa?
12 Yuda anasonkhezera kuti chifundo chisonyezedwe kwa Akristu odzozedwa omwe ayambitsa zikaikiro kapena agwera m’chimo la kuthupi, kokha ngati anali olapa. (Yuda 22, 23; onaninso 2 Akorinto 7:10.) Kodi icho, chotero, sichikakhala choyenera koposa kuti chifundo chisonyezedwe kwa munthu wosabatizidwa wolakwa yemwe akusonyeza kulapa? (Machitidwe 3:19) Inde, popeza kuti maziko ake auzimu sali olimba, ndipo kuzolowera kwake mu umoyo Wachikristu kuli kokhala ndi polekezera koposa. Iye angakhale asanaphunzire kulingalira kwa Mulungu pa nkhani zina. Iye sanapyole mipambo ya kukambitsirana kochitidwa ndi akulu kwa Baibulo ubatizo usanakhale, ndipo iye sanadzigonjetsere ku sitepi lofunika koposa la kumizidwa m’madzi. M’kuwonjezerapo, Yesu ananena kuti “aliyense adamupatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri.” (Luka 12:48) Chotero, zambiri zimayembekezeredwa kuchokera kwa obatizidwa omwe, limodzi ndi kuwonjezereka kwa chidziwitso ndi madalitso, ali ndi kuŵerengera kwapadera.—Yakobo 4:17; Luka 15:1-7; 1 Akorinto 13:11.
13. Ngati wofalitsa wosabatizidwa alakwa, nchiyani chimene akulu adzachita kumuthandiza?
13 Mogwirizana ndi uphungu wa Paulo, abale oyeneretsedwa mwauzimu amafuna kuthandiza wofalitsa aliyense wosabatizidwa yemwe amatenga sitepi la chinyengo asanazindikire ilo. (Yerekezani ndi Agalatiya 6:1.) Akulu angafunse aŵiri a unyinji wawo (mwinamwake awo amene anakumana naye pamayambiriro) kuyesa kumuwongolera iye ngati afuna kuthandizidwa. Iwo angachite tero, osati ndi chikhumbo cha kudzudzula mwaukali, koma m’njira ya chifundo ndi mzimu wofatsa. (Salmo 130:3) M’nkhani zambiri, kuchenjeza kwa m’Malemba ndi malingaliro ogwira ntchito akathandiza kutulutsa kulapa ndi kumuika iye pa njira yolondola.
14, 15. (a) Nchiyani chomwe chikachitidwa ngati wochita cholakwa alapa mowona mtima? (b) Ndi ndemanga yomveketsa yokhala ndi polekezera yotani imene ingapangidwe m’nkhani zina?
14 Akulu aŵiriwo akapereka zitsogozo zoyenerera ku mkhalidwe wa wosabatizidwa wochita cholakwayo. M’nkhani zina, iwo angakonze kuti kwakanthaŵi wochita cholakwayo asakhale mu Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki kapena kuloledwa kuchitira ndemanga pa misonkhano. Kapena iwo angamulangize iye kusagawana mu utumiki wapoyera ndi mpingo kufikira wapanga kupita patsogolo kwina kwauzimu. Kenaka iwo angamuuze iye kuti angayambenso kutengamo mbali mu utumiki wa m’munda. Ngati kuchita cholakwako sikunabweretse kuwuma khosi ndipo sikunaike m’ngozi chiyero cha gulu, sichiri choyenerera kudziŵitsa mpingo ndi chilengezo chirichonse.
15 Bwanji, ngakhale ndi tero, ngati akulu aŵiriwo apeza kuti munthuyo ali mowona mtima wolapa, koma cholakwacho chadziŵika mofala? Kapena bwanji ngati kuchita cholakwako kwakhala kodziŵika mofala pambuyo pake? M’nkhani iriyonse, iwo angadziŵitse Komiti ya Ntchito ya Mpingo, yomwe idzakonza kaamba ka chilengezo chopepuka, monga chotsatirachi: “Nkhani yokhudza . . . yasamaliridwa, ndipo wamwamunayo [wamkaziyo] adzapitiriza kutumikira monga wofalitsa wasabatizidwa ndi mpingo.” Monga m’nkhani zonse zoterozo, bungwe la akulu lingagamulepo kaya ngati chikakhala choyenra pa nthaŵi ina yamtsogolo kupereka nkhani ya m’Malemba ndi uphungu ponena za mtundu wa cholakwa chokhudzidwacho.
16, 17. (a) Ndi mikhalidwe iŵiri yotani imene ingakhale maziko kaamba ka chilengezo chosiyanako? (b) Nchiyani chomwe chiri mtundu wa chilengezo chimenechi?
16 Mwa kamodzikamodzi, wofalitsa wosabatizidwayo yemwe ali wochita cholakwa sadzavomereza ku thandizo lachikondi. Kapena wofalitsa wosabatizidwa angagamulepo kuti iye sakufuna kupitiriza kupita patsogolo kulinga ku ubatizo, ndipo iye wadziŵitsa akulu kuti iye sakufuna kuzindikiritsidwa monga wofalitsa. Nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa? Kachitidwe ka kuchotsa sikatengedwa ponena za oterowo omwe m’chenicheni sanakhale ovomerezedwa ndi Mulungu. Makonzedwe a kuchotsa wochita cholakwa wosalapa amagwira ntchito kwa awo ‘otchedwa abale,’ kwa obatizidwa. (1 Akorinto 5:11) Kodi ichi chimatanthauza, ngakhale ndi tero, kuti cholakwacho chanyalanyazidwa? Ayi.
17 Akuluwo ali ndi thayo la ‘kuweta nkhosa za Mulungu m’chisamaliro chawo.’ (1 Petro 5:2) Ngati akulu aŵiri opereka thandizowo agamulapo kuti wosabatizidwa wochita cholakwayo ali wosalapa ndipo sayeneretsedwa kukhala wofalitsa, iwo adzamudziŵitsa munthuyo.d Kapena ngati wosabatizidwa wina awuza akulu kuti iye sakukhumbanso kuzindikiridwa monga wofalitsa, iwo adzalandira chosankha chake. M’nkhani iriyonse, chiri choyenerera kwa Komiti ya Utumiki ya Mpingo kukhala ndi chilengezo chachifupi chitapangidwa pa nthaŵi yoyenera, chikumanena kuti “. . . salinso wofalitsa wa mbiri yabwino.”
18. (a) Pambuyo pa chilengezo choterocho, nchiyani chimene Akristu adzasunga m’maganizo mwaumwini m’kugamulapo za mmene angachitire? (b) Kodi chiri choyenera kupewa kotheratu osabatizidwa a liwongo la kuchita cholakwa kumbuyoko?
18 Ndimotani mmene Mboni pambuyo pake zidzawonera munthuyo? Chabwino, pa nthaŵi yoyambirira iye anali ‘wosakhulupirira’ wopezeka pa misonkhano. Kenaka ponse paŵiri anafuna kukhala ndipo anayeneretsedwa kukhala wofalitsa wa mbiri yabwino. Umu si mmene ziririnso, chotero iye kachiŵirinso ali munthu wa kudziko. Baibulo silimafuna kuti Mboni zipewe kulankhula naye, popeza kuti iye sali wochotsedwa.e Komabe, Akristu akasonyeza kuchenjera m’chigwirizano ndi munthu wa kudziko woteroyo yemwe sakulambira Yehova, monga mmene Aisrayeli anachitira m’chigwirizano ndi alendo okhalamo osadulidwa. Kuchenjera kumeneku kumathandiza kuchinjiriza mpingo kuchokera ku “chotupitsa chochepa,” chirichonse kapena chinthu choipitsa. (1 Akorinto 5:6) Ngati pa nthaŵi ina kutsogolo iye asonyeza chikhumbo chowona mtima kaamba ka phunziro la Baibulo kuchitidwa kwa iye, ndipo ichi chikuwoneka kukhala choyenera kwa akulu, mwinamwake chingamuthandize iye kuyamikiranso kuti ndi mwaŵi wotani mmene uliri kulambira Yehova ndi anthu ake.—Salmo 100.
19. Ndimotani mmene akulu mwamseri angaperekere thandizo lowonjezereka m’nkhani zina?
19 Ngati akulu awona kuti munthu wina wake wa mtundu umenewu ali chiwopsyezo chachilendo ku gulu, iwo mwamseri angachenjeze awo amene ali m’ngozi. Mwachitsanzo, yemwe anali wofalitsayo angakhale wachichepere yemwe wagonjera ku kuledzera ndi mkhalidwe wachisembwere. Mosasamala kanthu za chilengezo chakuti iye salinso wofalitsa wosabatizidwa, iye angayesere kuyanjana ndi achichepere mu mpingo. Mu mkhalidwe woterowo, akulu angalankhule mwamseri kwa makolo a omwe ali m’ngoziwo, ndipo mwinamwake kwa achichepere amenewonso. (Ahebri 12:15, 16; Machitidwe 20:28-30) M’nkhani yosawonekawoneka ya munthu yemwe ali wosokoneza kapena wachiwawa mowopsya, iye angawuzidwe kuti sali wolandirika pa misonkhano ndi kuti kuyesera kulikonse kulowamo kungadzalingaliridwe kukhala kupyola kosakhala kwa lamulo pa malo oletsedwa.
Kuthandiza Ang’ono Kulambira Mulungu
20. Makolo Achikristu amapereka thandizo lotani kaamba ka ana awo, ndipo ndi chotulukapo chotani?
20 Baibulo limapatsa makolo thayo la kulangiza ana awo m’njira ya chowonadi chaumulungu. (Deuteronomo 6:4-9; 31:12, 13) Chotero, Mboni za Yehova kwa nthaŵi yaitali zalimbikitsa makolo Achikristu kukhala ndi phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu. Makolo Achikristu ayenera kulimbikitsa achichepere awo kupita patsogolo kulinga ku kudzipereka ndi ubatizo ndipo chotero kupeza chivomerezo cha Mulungu. (Miyambo 4:1-7) Timawona m’mipingo chotulukapo chosangalatsa—mazana a zikwi za achichepere a chitsanzo chabwino omwe amakonda Yehova ndi kufuna kumulambira iye kosatha.
21-23. (a) Poyambirira, ndimotani mmene kuchita cholakwa kwa wamng’ono kungasamalidwire? (b) Ndi mbali yotani imene akulu a mu mpingo amachita m’mikhalidwe yoteroyo?
21 Makolo Achikristu alinso ndi thayo loyambirira la kulanga ndi kudzudzula ana awo, kupereka ziletso zirizonse kapena zilango zachikondi zomwe angaziwone kukhala zoyenerera. (Aefeso 6:4; Ahebri 12:8, 9; Miyambo 3:11, 12; 22:15) Ngati, ngakhale ndi tero, mwana wamng’ono yemwe wakhala akuyanjana monga wofalitsa wosabatizidwa akhala wolowetsedwa m’chimo lalikulu, chiri chodetsa nkhaŵa kwa akulu omwe ‘akuyang’anira miyoyo’ ya nkhosa.—Ahebri 13:17.
22 Kwakukulukulu, kuchita cholakwa koteroko kuyenera kusamaliridwa monga mmene zandandalitsidwa kumayambiriroko m’nkhaniyi. Akulu aŵiri angagawiridwe kuyang’ana m’nkhaniyi. Iwo angakhoze, mwachitsanzo, choyamba kukambitsirana ndi makolo (kapena kholo) za chomwe chachitika, umene uli mkhalidwe wa mwanayo, ndi masitepi owongolera omwe atengedwa. (Yerekezani ndi Deuteronomo 21:18-21.) Ngati makolo Achikristu angasamalire mkhalidwewo, akulu angangofufuza ndi iwo kwa nthaŵi ndi nthaŵi kupereka uphungu wothandiza, malingaliro, ndi chilimbikitso chachikondi.
23 Nthaŵi zina, ngakhale ndi tero, kukambitsirana ndi makolo kumasonyeza kuti chikakhala chabwino koposa kwa akulu kukumana ndi wamng’ono wosokerayo ndi makolowo. Akumasunga m’maganizo polekezera ndi zikhoterero za achichepere, oyang’anirawo akakalamira kulangiza wofalitsa wosabatizidwa, wachichepereyo ndi chifatso. (2 Timoteo 2:22-26) M’nkhani zina, chingakhale chowonekera kuti iye sakuyeneretsedwanso kukhala wofalitsa ndi kuti chilengezo choyenerera chiyenera kupangidwa.
24. (a) Ngakhale ngati wamng’ono wagawanako m’kuchita cholakwa chokulira, nchiyani chimene chiri choyenerera kwa makolo kuchita, ndipo ndimotani mmene iwo angakwaniritsire ichi? (b) Ndimotani mmene ichi chikagwirira ntchito kwa wamng’ono yemwe wachotsedwa?
24 Pambuyo pa chimenecho, nchiyani chimene makolo akachita m’malo mwa mwana wawo wamng’ono wolakwayo? Iwo adakali ndi thayo kaamba ka mwana wawo, ngakhale kuti iye sakuyeneretsedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa kapena ngakhale ngati iye wachotsedwa chifukwa cha kuchita cholakwa pambuyo pa kubatizidwa. Mongadi mmene iwo akapitirizira kumpatsa iye chakudya, zovala, ndi malo, iwo akafunikira kumulangiza ndi kumulanga m’chigwirizano ndi Mawu a Mulungu. (Miyambo 6:20-22; 29:17) Makolo achikondi mwakutero angakonze kukhala ndi phunziro la Baibulo la panyumba ndi iye, ngakhale ngati iye ali wochotsedwa.f Mwinamwake iye angakoke phindu lowongolera koposa kuchokera m’kuphunzira kwawo ndi iye yekha. Kapena iwo angagamule kuti iye angapitirizebe kugawana mu makonzedwe a phunziro la banja. Ngakhale kuti iye wasokera, iwo akufuna kumuwona iye akubwerera kwa Yehova, monga mmene anachitira mwana wolowerera mu fanizo la Yesu.—Luka 15:11-24.
25. Nchifukwa ninji chikondwerero chachikondi ndi chithandizo chalunjikitsidwa kulinga kwa “osakhulupirira” lerolino?
25 Chonulirapo cha kulalikira kwathu ndi kuphunzitsa chiri kuthandiza ena kukhala olambira achimwemwe a Mulungu wowona. ‘Osakhulupirira ndi anthu osaphunzira’ mu Korinto anafulumizidwa ‘kugwa nkhope zawo pansi ndi kugwadira Mulungu, akumalengeza kuti: “Mulungu ali ndithu mwa inu.”’ (1 Akorinto 14:25) Ndi chimwemwe chotani nanga mmene chiriri lerolino kuwona anthu owonjezerekawonjezereka akubwera kudzalambira Mulungu! Uku ndi kukwaniritsidwa kwa ulemerero kwa chilengezo cha angelo chakuti: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo [kapena, anthu okhala ndi chivomerezo cha Mulungu].”—Luka 2:14.
[Mawu a M’munsi]
a Mmodzi wa akuluwa ayenera kukhala chiwalo cha Komiti ya Utumiki ya mpingo. Winayo angakhale mkulu wozolowerana kwambiri ndi wophunzirayo kapena mphunzitsi wake, monga ngati Wotsogoza Phunziro la Bukhu.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., 1985.
c Kalelo, munthu wosabatizidwa yemwe anayeneretsedwa kugawana mu utumiki wa m’munda anali kutchedwa “tsamwali wovomerezedwa.” Ngakhale kuli tero, “wofalitsa wosabatizidwa” kali katchulidwe kolongosoka koposa, makamaka m’chiyang’aniro cha chisonyezero cha Baibulo chakuti chivomerezo cha Mulungu chimatulukapo kuchokera ku kudzipereka kotsimikizirika ndi ubatizo Wachikristu.
d Ngati munthuyo ali wosakhutiritsidwa ndi mapeto amenewa, iye angafunse (mkati mwa masiku asanu ndi aŵiri) kukhala ndi nkhaniyo itabwereredwamonso.
e Kalelo, osabatizidwa omwe anachita chimo mosalapa anali kupewedwa kotheratu. Pamene kuli kwakuti, monga mmene kwasinthidwira pamwambapo, ichi sichikufunikira, uphungu wa pa 1 Akorinto 15:33 uyenerabe kusungidwa.
f Achibale ochotsedwa okhala kunja kwa nyumba ayenera kusamaliridwa mogwirizana ndi uphungu wa m’Malemba wokambitsiridwa mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1988, masamba 26-31; March 15, 1982, masamba 26-31.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Nchiyani chomwe chiri kawonedwe ka Akristu kulinga ku “osakhulupirira” omwe amapezeka pa misonkhano?
◻ Pamene wophunzira Baibulo akufuna kugawana mu utumiki wa m’munda, ndi masitepi otani amene akulu amatsatira, ndipo ndi thayo lotani limene wophunzirayo amalandira?
◻ Nchiyani chimene chimachitidwa ngati wofalitsa wosabatizidwa achita chimo lalikulu?
◻ Ndimotani mmene makolo ndi akulu angathandizire ana ang’ono okhala pa nyumba, ngakhale ngati achichepere oterowo alakwa mokulira?
[Chithunzi patsamba 16]
Kukhala wofalitsa, ngakhale kuti sanabatizidwe, iri sitepi yofunika kwambiri ndipo ya thayo kulinga ku kupeza chivomerezo cha Mulungu