-
Kodi Yesu Anaukitsidwadi?Nsanja ya Olonda—2013 | March 1
-
-
Paulo sankakhulupirira kuti zimene Akhristu amakhulupirira ndi zabodza ndipo ankadziwa kuti Yesu anaukitsidwadi. Iye analembera Akhristu a ku Korinto umboni wa zimenezi kuti: “Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba. Ndiponso kuti anaikidwa m’manda, kenako anaukitsidwa tsiku lachitatu, mogwirizana ndi Malemba. Panalinso zoti anaonekera kwa Kefa, kenako kwa atumwi 12 aja.”b Paulo anawonjezeranso kuti: “Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero, koma ena anagona mu imfa. Kenako anaonekera kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse. Koma pomalizira pake anaonekera kwa ine.”—1 Akorinto 15:3-8.
-
-
Kodi Yesu Anaukitsidwadi?Nsanja ya Olonda—2013 | March 1
-
-
b Mawu akuti “atumwi 12 aja” akunena za “atumwi okhulupirika” ngakhale kuti pa nthawi ina Yudasi Isikariyoti atafa, atumwi analipo 11 okha. Pa nthawi inanso pamene Yesu ankaonekera kwa atumwi, panali atumwi 10 okha chifukwa Tomasi panalibe. Komabe atumwi 10 amenewa anaimira atumwi 12.—Yohane 20:24.
-