Tumikirani Yehova Popanda Kunong’oneza Bondo
“Ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.”—AFIL. 3:13.
1-3. (a) Kodi kunong’oneza bondo n’kutani ndipo kungatikhudze bwanji? (b) Kodi chitsanzo cha Paulo chingatithandize bwanji kutumikira Mulungu popanda kunong’oneza bondo?
WANDAKATULO wina analemba kuti: “Mawu omvetsa chisoni kwambiri amene anthu ananenapo kapena kulemba, ndi akuti: ‘Ndikanadziwa, ndikanachita zakutizakuti!’” Wandakatuloyu anali kunena za zinthu zimene anthu amanong’oneza nazo bondo. “Kunong’oneza bondo” kumatanthauza kuti munthu akumva chisoni kapena kupweteka mumtima chifukwa cha zimene wachita kapena walephera kuchita. Tonsefe tachitapo zinthu zimene timalakalaka titazikonza. Kodi pali zinthu zimene mumanong’oneza nazo bondo?
2 Anthu ena alakwitsapo zinthu zikuluzikulu ngakhale kuchita machimo aakulu. Ndipo ena sanachite zinthu zoipa kwambiri komabe amakayikira ngati zinthu zina zimene anasankha pa moyo zilidi zabwino. Anthu ena amatha kuiwala zakale pamene ena amangokhalira kuvutika maganizo ndi zinthu zimene sanasankhe bwino m’mbuyomo. (Sal. 51:3) Nanga inu muli mbali iti? Kodi mumafuna kuti muzitumikira Mulungu popanda kumva chisoni ndi zimene munalakwitsa m’mbuyomo? Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tiyeni tione chitsanzo cha mtumwi Paulo.
3 Pa moyo wake, Paulo anachita zinthu zoipa ndiponso zabwino. Iye ananong’oneza bondo kwambiri ndi zinthu zoipa zimene anachita. Koma m’malo momangoganizira zinthu zakale, iye anaphunzira kuika maganizo ake pa zimene angachite kuti atumikire Mulungu mokhulupirika. Ndiye tiyeni tione mmene chitsanzo chake chingatithandizire kutumikira Mulungu popanda kunong’oneza bondo.
ZIMENE PAULO ANANONG’ONEZA NAZO BONDO
4. Kodi Paulo anachita zinthu ziti zimene anadzanong’oneza nazo bondo?
4 Paulo ali wachinyamata anali Mfarisi ndipo anachita zinthu zimene anadzanong’oneza nazo bondo. Mwachitsanzo, iye anatsogolera pozunza mwankhanza ophunzira a Khristu. Baibulo limanena kuti Sitefano ataphedwa, “Saulo [yemwe anadzakhala Paulo] anayamba kuzunza mpingo mwankhanza. Anali kulowa m’nyumba ndi nyumba, ndi kukokera panja amuna ndi akazi omwe, n’kukawaponya m’ndende.” (Mac. 8:3) Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kuzunza mwankhanza’ ndi “mawu amphamvu kwambiri” amene amasonyeza kuti “Saulo anazunza mpingo molusa koopsa ngati chilombo chakutchire.” Popeza kuti Saulo anali Myuda wodzipereka kwambiri, ankaganiza kuti akugwira ntchito ya Mulungu yothetsa Chikhristu. Choncho ankazunza Akhristu mwankhanza kwambiri, ‘kuwaopseza komanso anali wofunitsitsa kupha amuna ndi akazi’ omwe.—Mac. 9:1, 2; 22:4.a
5. Fotokozani zimene zinachitika kuti Saulo asiye kuzunza Akhristu n’kuyamba kulalikira za Khristu.
5 Saulo ankafunitsitsa kupita ku Damasiko kuti akatulutse ophunzira a Yesu m’nyumba zawo n’kuwanyamula kupita nawo ku Yerusalemu kuti akalangidwe ndi Khoti Lalikulu la Ayuda. Koma analephera kuchita zimenezi chifukwa zolinga zakezi zinali zosemphana ndi za Mutu wa mpingo wachikhristu. (Aef. 5:23) Saulo akupita ku Damasiko, anakumana ndi Yesu ndipo kuunika kochokera kumwamba kunamuchititsa khungu. Kenako Yesu anatumiza Saulo ku Damasiko podikira kuti alandire malangizo ena. Ndipo timadziwa zimene zinachitika pambuyo pake.—Mac. 9:3-22.
6, 7. N’chiyani chikusonyeza kuti Paulo ankadziwa kuti anachita zoipa?
6 Zinthu zimene Paulo anawona kuti n’zofunika zinasintha iye atangokhala Mkhristu. Iye anasiya kukhala mdani woopsa wa Akhristu n’kuyamba kulalikira za Khristu mwakhama. Patapita nthawi, analemba kuti: “Munamva ndithu zimene ndinali kuchita ndili m’Chiyuda, kuti ndinkazunza kwambiri mpingo wa Mulungu ndi kupitirizabe kuuwononga.” (Agal. 1:13) Anadzanenanso za zimene anachita m’mbuyomo polemba makalata opita kwa Akorinto, Afilipi ndiponso kwa Timoteyo. (Werengani 1 Akorinto 15:9; Afil. 3:6; 1 Tim. 1:13) Paulo sankanyadira zimene anachitazo koma sankafuna kuzibisa ngati kuti sizinachitike. Iye ankadziwa bwino kuti zimene anachita zinali zoipa kwambiri.—Mac. 26:9-11.
7 Katswiri wina wa Baibulo analemba za mmene Paulo anazunzira moopsa Akhristu. Iye anati tikaganizira zimenezi, “timatha kuzindikira chisoni chachikulu chimene iye anali nacho ndiponso kuti adani ake ayenera kuti ankamunenera zinthu zoipa kwambiri.” N’kutheka kuti nthawi zina abale m’mipingo imene Paulo ankayendera akakumana naye koyamba ankati, ‘Ndinu Paulo amene ankatizunza uja eti!’—Mac. 9:21.
8. Kodi Paulo anamva bwanji ndi chifundo komanso chikondi chimene Yehova ndi Yesu anamusonyeza? Nanga chitsanzo chake chikutiphunzitsa chiyani?
8 Koma Paulo ankazindikira kuti anatha kukhala mtumwi chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu basi. Iye anatchula za chifundo cha Mulungu kuposa wolemba Baibulo aliyense. Anatchula zimenezi pafupifupi maulendo 90 m’makalata ake okwana 14. (Werengani 1 Akorinto 15:10.) Paulo ankayamikira kwambiri kuti Mulungu anamuchitira chifundo ndipo ankafunitsitsa kusonyeza kuti kukoma mtima kwa Mulungu kumeneko sikunapite pachabe. Choncho anagwira ntchito “molimbika kuposa atumwi ena onse.” Chitsanzo chake chimasonyeza kuti ngati tilapa machimo athu n’kusintha, Yehova ndi wofunitsitsa kutikhululukira machimo athu ngakhale akuluakulu. Amatha kuchita zimenezi chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu. Chitsanzo cha Paulo ndi cholimbikitsa kwambiri kwa anthu amene amavutika kukhulupirira kuti nsembe ya Khristu ingawathandize. (Werengani 1 Timoteyo 1:15, 16.) Ngakhale kuti m’mbuyomo Paulo ankazunza Akhristu mwankhanza, analemba kuti: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agal. 2:20; Mac. 9:5) Paulo anaphunzira kuti anayenera kuchita zonse zimene angathe potumikira Mulungu mosaganizira kwambiri zakumbuyo. Kodi nanunso mwaphunzira kuchita zimenezi?
KODI PALI ZINTHU ZIMENE MUMANONG’ONEZA NAZO BONDO?
9, 10. (a) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene atumiki ena a Yehova amanong’oneza nazo bondo? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kumangodera nkhawa zakumbuyo?
9 Kodi munachitapo zinthu zimene panopa mumanong’oneza nazo bondo? Kodi munawonongapo nthawi kapena mphamvu zanu pochita zinthu zopanda phindu? Kodi munachitapo zinthu zimene zinapweteka anthu ena? Kapena kodi pali zinthu zina zimene mumamva nazo chisoni? Ngati zili choncho, kodi mungachite chiyani?
10 Anthu ena amangokhalira kuda nkhawa. Nthawi zonse amadzivutitsa ndiponso kudzizunza moti amangokhalira kuvutika maganizo. Koma kodi kuda nkhawa koteroko n’kothandiza? Ayi, n’kosathandiza ngakhale pang’ono. Zili ngati munthu amene akugwira ntchito yokatunga madzi n’kumadzathira m’chimgolo chobooka. Iye akhoza kuchita zimenezi kwa nthawi yaitali ndiponso kuwononga mphamvu zake koma osaphula kanthu. M’malo momangoda nkhawa, ndi bwino kuyesetsa kukonza vutolo. Mwachitsanzo, ngati munalakwira munthu wina, ndi bwino kumupepesa n’kuyesetsa kukhalanso naye pa mtendere. Kapena ngati munalakwitsa zinazake, mungayesetse kupewa zinthu zimene zinakuchititsani kulakwitsa kuti musadzazibwerezenso. Koma nthawi zina mungafunike kungopirira zotsatira za zimene munachita. Kudera nkhawa zakumbuyo n’kosathandiza. Kukhoza kungokulepheretsani kutumikira bwino Mulungu.
11. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atichitire chifundo ndiponso kutikomera mtima? (b) Ngati tinalakwitsa zinazake, kodi ndi malangizo a Mulungu ati amene tiyenera kutsatira kuti tikhale ndi mtendere wa mumtima?
11 Anthu ena amaona kuti zimene anachita m’mbuyomo ndi zoipa kwambiri moti Mulungu sangafune n’komwe kuwachitira chifundo. Mwina amaganiza choncho chifukwa chakuti machimo awo anali aakulu kwambiri kapena anawachita mobwerezabwereza. Komabe kaya anachita zotani m’mbuyomo, akhoza kulapa, kusintha ndiponso kupempha kuti akhululukidwe. (Mac. 3:19) Yehova akhoza kuwachitira chifundo ndiponso kuwakomera mtima ngati mmene wachitira ndi anthu ena ambiri. Iye amakhululukira mokoma mtima anthu odzichepetsa, oona mtima ndiponso amene alapa mochokera pansi pa mtima. Mulungu anachita zimenezi kwa Yobu yemwe anamva chisoni n’kunena kuti: “Ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” (Yobu 42:6) Tonsefe tiyenera kutsatira malangizo a Mulungu otithandiza kupeza mtendere wa mumtima akuti: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.” (Miy. 28:13; Yak. 5:14-16) Tiyenera kuulula machimo athu kwa Mulungu, kupempha kuti atikhululukire ndiponso kuchita zonse zimene tingathe posonyeza kuti tikumva nazo chisoni. (2 Akor. 7:10, 11) Ngati tachita zimenezi, ndiye kuti Yehova, yemwe “amakhululuka ndi mtima wonse,” adzatichitira chifundo.—Yes. 55:7.
12. (a) Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha Davide tikamavutika ndi chikumbumtima? (b) Kodi Yehova amamva chisoni ndi zimene wachita m’njira iti? Kodi kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji? (Onani bokosi.)
12 Pemphero ndi lothandiza kwambiri chifukwa Mulungu amamva mapemphero athu. Davide anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova pamene anamufotokozera m’pemphero mmene ankamvera mumtima. Pemphero limeneli linalembedwa m’buku la Masalimo. (Werengani Salimo 32:1-5.) Davide anafotokoza kuti asanaulule tchimo lake, anafooka chifukwa chakuti chikumbumtima chake chinkamuvutitsa. Iye ankavutika maganizo, kudwala ndiponso kukhala wosasangalala. Koma ataulula tchimo lake n’kukhululukidwa, anakhalanso ndi mtendere wa mumtima. Yehova anayankha mapemphero a Davide ndipo anamupatsa mphamvu. Izi zinamuthandiza kuti apitirize kuchita zinthu zabwino pa moyo wake. Nanunso ngati mumavutika maganizo chifukwa cha zimene munalakwitsa m’mbuyomo, pempherani mochokera pansi pa mtima n’kuyesetsa kukonza zinthu mmene mungathere. Mukachita zimenezi, musamakayikire kuti Yehova wamvetsera mapemphero anu ndipo wakukhululukirani.—Sal. 86:5.
MUZIGANIZIRA ZA M’TSOGOLO
13, 14. (a) Kodi panopa tiyenera kuika maganizo athu pa chiyani? (b) Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kuganizira za moyo wathu?
13 N’zoona kuti tikhoza kuphunzira zambiri kuchokera pa zimene zinachitika m’mbuyomo koma si bwino kumangokhalira kudandaula nazo. M’malomwake, tiyenera kuika maganizo pa zimene tikuchita panopa komanso zam’tsogolo. Kodi panopa tikuchita zotani kapena tikulephera kuchita zinthu ziti zimene m’tsogolo tikhoza kudzanong’oneza nazo bondo? Kodi tikuyesetsa kutumikira Yehova mokhulupirika kuti m’tsogolo tisadzanong’oneze bondo ngakhale pang’ono?
14 Chisautso chachikulu chikuyandikira kwambiri. Choncho ndi bwino kudzifunsa mafunso ngati otsatirawa n’cholinga chakuti m’tsogolo tisadzadandaule ndi zimene tinachita pa moyo wathu. ‘Kodi ndingawonjezere zimene ndimachita potumikira Mulungu? Kodi ndikhoza kuchita upainiya? Kodi n’chiyani chikundilepheretsa kukhala mtumiki wothandiza? Kodi ndikuyesetsa kuvala umunthu watsopano? Kodi ndine munthu amene Yehova angamufune m’dziko lake latsopano?’ Koma tisalole mafunsowa kutidetsa nkhawa kwambiri, m’malomwake, atithandize kuona mmene tingachitire zonse zimene tingathe potumikira Yehova. Kupanda kutero, tikhoza kumangokhala moyo umene tidzanong’oneza nawo bondo m’tsogolo.—2 Tim. 2:15.
MUSAONE NGATI MUNALAKWITSA POSANKHA KUTUMIKIRA MULUNGU
15, 16. (a) Kodi Akhristu ambiri anasankha zotani kuti aike kutumikira Mulungu pa malo oyamba? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudandaula ndi zinthu zimene tinasiya kuti titumikire Mulungu modzipereka?
15 Kodi munasiya kuchita zinazake kuti muchite utumiki wa nthawi zonse? Mwina munasiya ntchito yapamwamba kapena bizinezi yabwino kuti muchite zambiri mu utumiki. Kapena munasankha kusakhala pa banja kapena kusakhala ndi ana n’cholinga choti mutumikire pa Beteli, kuthandiza ntchito zomanga kumayiko ena, kukhala woyang’anira dera kapena kukhala mmishonale. Kodi muyenera kudandaula ndi zimene munasankhazo pamene mukukula? Kodi muyenera kuganiza kuti munasankha molakwika kapena munazisankha pa nthawi yolakwika? Ayi musatero.
16 Musaiwale kuti munasankha zimenezi chifukwa chokonda kwambiri Yehova ndiponso chifukwa chofunitsitsa kuthandiza anthu kuti azimutumikira. Musamaganize kuti moyo wanu ukanakhala wabwino kwambiri mukanasankha kuchita zinthu zina. Koma muzisangalala kwambiri ndi zimene munasankhazo. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawiyo, munasankha zomwe munaona kuti zingakuthandizeni kutumikira Yehova modzipereka. Iye sadzaiwala zimene munachita. M’moyo weniweni umene tikuyembekezera, Yehova adzakudalitsani kwambiri kuposa mmene mukuganizira panopa.—Sal. 145:16; 1 Tim. 6:19.
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUSADZANONG’ONEZE BONDO
17, 18. (a) N’chiyani chinathandiza Paulo kuti apewe kudzanong’oneza bondo m’tsogolo? (b) Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani kuti mutsatire chitsanzo cha Paulo?
17 Kodi Paulo anachita chiyani kuti apewe kudzanong’oneza bondo m’tsogolo? Paulo analemba kuti: “Ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.” (Werengani Afilipi 3:13, 14.) Paulo sanaike maganizo ake pa zinthu zoipa zimene anachita ali m’Chiyuda. M’malomwake, anachita zonse zimene akanatha kuti ayenerere kulandira mphoto ya moyo wosatha m’tsogolo.
18 Tonse tikhoza kutsatira mfundo ya m’mawu a Paulowa. Tisamangodandaula ndi zinthu zakumbuyo zomwe sitingathe kuzisintha. Koma tiziyesetsa kuchita zimene tingathe kuti tidzalandire madalitso a m’tsogolo. N’zoona kuti sitingaiwaliretu zimene tinalakwitsa m’mbuyomo koma sitiyenera kumangodziimba mlandu ndi zimenezo. Tiyenera kuyesetsa kuiwala zakumbuyo. M’malomwake, tizichita zonse zimene tingathe potumikira Mulungu panopa ndiponso tiziganizira za madalitso amene tidzalandire m’tsogolo.
a Baibulo limatchula kangapo konse kuti Saulo ankazunzanso akazi. Zimenezi zimasonyeza kuti akazi ankachita zambiri pa ntchito yolalikira monga mmene amachitiranso masiku ano.—Sal. 68:11.