Musalole Aliyense Kukuipsirani Makhalidwe Anu Okoma
“Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” —1 AKORINTO 15:33.
1, 2. (a) Kodi mtumwi Paulo anamva motani kulinga kwa Akristu a ku Korinto, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ndiuphungu wachindunji uti umene tidzakambitsirana?
CHIKONDI cha makolo nchamphamvu motani nanga! Chimasonkhezera makolo kudzimana kaamba ka ana awo, kuwaphunzitsa ndi kuwalangiza. Mwinamwake mtumwi Paulo sanali atate weniweni, koma analembera Akristu a ku Korinto kuti: “Pakuti mungakhale muli nawo aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala inu mwa uthenga wabwino.”—1 Akorinto 4:15.
2 Poyambirira, Paulo adapita ku Korinto, kumene analalikira kwa Ayuda ndi Agiriki. Iye anathandiza kupanga mpingo m’Korinto. M’kalata ina Paulo anayerekezera chisamaliro chake ndi chija cha mlezi, koma anali ngati atate kwa Akorintowo. (1 Atesalonika 2:7) Monga momwe amachitira atate weniweni wachikondi, Paulo anachenjeza ana ake auzimu. Mungapindule ndi uphungu wake wonga wa atate umene anapereka kwa Akristu a ku Korinto wakuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Kodi nchifukwa ninji Paulo analemba zimenezo kwa Akorinto? Kodi tingagwiritsire ntchito motani uphunguwo?
Uphungu wa Iwo ndi Ife
3, 4. Kodi timadziŵa chiyani ponena za mzinda wa Korinto wa m’zaka za zana loyamba ndi anthu ake?
3 M’zaka za zana loyamba, katswiri wodziŵa malo Wachigiriki, Strabo analemba kuti: “Mzinda wa Korinto umatchedwa ‘wolemera’ chifukwa cha malonda ake, popeza kuti uli pamalo otchedwa Isthmus ndipo uli pakati pamadoko aŵiri, amene limodzi limamka ku Asia, ndipo linalo ku Italy; ndipo umachititsa kusinthana malonda kukhala kosavuta m’maiko onse aŵiri.” Zaka ziŵiri zilizonse maseŵera otchuka a ku Isthmus anakopa makamu ambiri kubwera ku Korinto.
4 Kodi anthu a mumzinda umenewo womwe unali ponse paŵiri phata la ulamuliro wa boma ndi kulambira kopambanitsa kwa Aphrodite anali otani? Profesa T. S. Evans analongosola kuti: “Mwinamwake [kunali] anthu pafupifupi 400,000. Chitaganya chinali cha anthu apamwamba, koma chokhala ndi makhalidwe olekerera, ngakhale oipa. . . . Nzika Zachigiriki za ku Achaïa zinali zodziŵika chifukwa cha kulankhula ndi kufuna kumva zatsopano. . . . Kudzikonda kwawo kunali chinthu chosonkhezera timagulu totsutsa.”
5. Kodi abale a ku Korinto anayang’anizana ndi upandu wotani?
5 M’kupita kwa nthaŵi ngakhale mpingo unagaŵidwa ndi ena amene anali okhotererabe pamalingaliro odzikweza. (1 Akorinto 1:10-31; 3:2-9) Vuto lalikulu linali lakuti ena anali kunena kuti: “Kulibe kuuka kwa akufa.” (1 Akorinto 15:12; 2 Timoteo 2:16-18) Mosasamala kanthu za zimene anakhulupirira (kapena kusakhulupirira), Paulo anayenera kuwawongolera ndi umboni woonekera bwino wakuti Kristu ‘anaukitsidwa kwa akufa.’ Motero, Akristu akanakhulupirira kuti Mulungu akawapatsa “chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Akorinto 15:20, 51-57) Mukanakhala kuti munali kumeneko, kodi mwina mukanayambukiridwa ndi mzimu umenewo?
6. Kodi uphungu wa Paulo wa pa 1 Akorinto 15:33 unagwira ntchito makamaka kwa yani?
6 Popereka umboni wamphamvu wakuti akufa adzaukitsidwa, Paulo anawauza kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Mfundo yaikulu ya uphunguwu inakhudza awo amene anayanjana ndi mpingo amene sanavomereze chiphunzitso cha chiukiriro. Kodi iwo anali kungokayikira mfundo imene sanamvetsetse? (Yerekezerani ndi Luka 24:38.) Ayi. Paulo analemba kuti “ena mwa inu anena . . . kuti kulibe kuuka kwa akufa,” chotero awo oloŵetsedwamo anali kusonyeza kusagwirizana, akumakhoterera kumpatuko. Paulo anadziŵa bwino lomwe kuti iwo akakhoza kuipsa makhalidwe okoma ndi kulingalira kwa ena.—Machitidwe 20:30; 2 Petro 2:1.
7. Kodi ndimumkhalidwe umodzi uti umene tingagwiritsire ntchito uphungu wa pa 1 Akorinto 15:33?
7 Kodi tingagwiritsire ntchito motani chenjezo la Paulo lonena za mayanjano? Iye sanatanthauze kuti tiyenera kukana kuthandiza munthu wina mumpingo amene avutika kumvetsetsa vesi la m’Baibulo kapena chiphunzitso. Ndithudi, lemba la Yuda 22, 23 limatifulumiza kupereka chithandizo mwachifundo kwa owona mtima amene ali ndi zikayikiro zotero. (Yakobo 5:19, 20) Komabe, uphungu wonga wa atate wa Paulo uyeneradi kugwira ntchito ngati munthu wina apitiriza kutsutsa zimene timadziŵa kukhala chowonadi cha m’Baibulo kapena apitiriza kupereka ndemanga zokayikira kapena zoipa. Tiyenera kuchenjera ndi kuyanjana ndi munthu wamtundu umenewo. Ndithudi, ngati wina akhaladi wampatuko, abusa auzimu ayenera kuchitapo kanthu kutetezera gulu la nkhosa.—2 Timoteo 2:16-18; Tito 3:10, 11.
8. Kodi tingachite motani mwanzeru pamene wina savomereza chiphunzitso cha Baibulo?
8 Tingagwiritsirenso ntchito mawu onga a atate a Paulo a pa 1 Akorinto 15:33 pamene tikuchita ndi anthu akunja kwa mpingo amene amachilikiza ziphunzitso zonama. Kodi tingayambe bwanji kuyanjana nawo? Zingachitike ngati tilephera kusiyanitsa pakati pa awo amene angathandizidwe kuphunzira chowonadi ndi awo amene akungodzutsa mkangano kotero kuti achilikize chiphunzitso chonama. Mwachitsanzo, m’ntchito yathu yaumboni, tingakumane ndi munthu amene savomereza mfundo ina koma amene ali wofunitsitsa kupitiriza kukambitsirana. (Machitidwe 17:32-34) Zimenezo siziyenera kupereka vuto, popeza kuti timakhala achimwemwe kufotokoza chowonadi cha Baibulo kwa aliyense amene akufunitsitsadi kudziŵa zimenezo, ngakhale kubwererako kukapereka umboni wokhutiritsa. (1 Petro 3:15) Komabe, ena sangakhale akufunadi kudziŵa chowonadi cha Baibulo.
9. Kodi tiyenera kuchita motani ngati wina atokosa zikhulupiriro zathu?
9 Anthu ambiri angafunse mafunso kwa maola ambiri, mlungu ndi mlungu, koma osati chifukwa chakuti akufuna kudziŵa chowonadi. Iwo amangofuna kunyozetsa chikhulupiriro cha munthu pamene akuwonetsera zimene amalingalira kukhala kudziŵa kwawo Chihebri, Chigiriki, kapena sayansi ya chisinthiko. Pamene zikumana ndi anthu oterowo, Mboni zina zimaona ngati kuti zingagonjetsedwe ndipo chotero zimapitiriza kuyanjana nawo mwakukhala ndi makambitsirano aatali ozikidwa paziphunzitso zonama za chipembedzo, nthanthi, kapena chinyengo cha sayansi. Nkowonekeratu kuti Yesu sanalole zimenezo kumchitikira, ngakhale kuti akanapambana m’kutsutsanako ndi atsogoleri achipembedzo amene anali akatswiri a Chihebri kapena Chigiriki. Pamene anatokosedwa, Yesu anayankha mwachidule ndiyeno anatembenukira kwa odzichepetsa, nkhosa zenizeni.—Mateyu 22:41-46; 1 Akorinto 1:23–2:2.
10. Kodi nchifukwa ninji Akristu amene ali ndi makompyuta ndi njira yogwiritsira ntchito ma electronic bulletin board ayenera kuchenjera?
10 Makompyuta amakono atsegulanso njira zina zokhalira ndi mayanjano oipa. Makampani ena amalonda amakhozetsa wolembetsa aliyense amene amagwiritsira ntchito kompyuta ndi telefoni kutumiza uthenga ku amene amatchedwa kuti ma electronic bulletin board (ziwiya zimene zimatheketsa anthu olembetsa kutumiza mauthenga kwa olembetsa ena kudzera pakompyuta ndi telefoni); motero munthu akhoza kutumiza uthenga pa bulletin board umene olembetsa onse angathe kuuwona. Zimenezi zachititsa mikangano yotchedwa electronic debates ya nkhani zachipembedzo. Mkristu angakopeke kuloŵa m’mikangano imeneyi ndipo angathere maola ambiri ndi wokhala ndi malingaliro ampatuko amene angakhale atachotsedwa mumpingo. Uphungu wa pa 2 Yohane 9-11 umamveketsa bwino uphungu wonga wa atate wa Paulo wonena za kupeŵa mayanjano oipa.a
Peŵani Kunyengedwa
11. Kodi mkhalidwe wamalonda mu Korinto unapereka mwaŵi wotani?
11 Monga momwe tawonera, mzinda wa Korinto unali phata la malonda, wokhala ndi masitolo ndi mabizinesi ambiri. (1 Akorinto 10:25) Anthu ambiri amene anabwera kumaseŵera a ku Isthmus anakhala m’mahema, ndipo mkati mwa chochitikacho amalonda ankagulitsa zinthu ali m’timisasa kapena m’khonde. (Yerekezerani ndi Machitidwe 18:1-3.) Zimenezi zinatheketsa Paulo kupeza ntchito yopanga mahema kumeneko. Ndipo anatha kugwiritsira ntchito malo antchitowo kupititsa patsogolo mbiri yabwino. Profesa J. Murphy-O’Connor analemba kuti: “Ataima m’sitolo pamsika wa anthu ali piringupiringu . . . akuyang’ana khwalala lokhala ndi khamu la anthu, Paulo anali ndi mwaŵi wa kulankhula, osati ndi ogwira nawo ntchito okha ndi odzagula malonda, komanso khamu lomwe linali kunjalo. Panthaŵi imene analibe zochita zambiri iye anakhoza kuima pakhomo ndi kuimitsa amene anawalingalira kuti akhoza kumvetsera . . . Nkovuta kuyerekezera kuti changu chake ndi chikhulupiriro cholimba sizinampange kukhala ‘munthu wotchuka’ m’malowo, ndipo zimenezi ziyenera zinakopa ambiri, osati anthu opanda chochita okha komanso awo amene anafunitsitsadi kumva mawu. . . . Akazi okwatiwa limodzi ndi adzakazi awo, amene anamva za iye, anafika kwa iye akumanamizira kudzagula zinthu. M’nthaŵi zamavuto, pamene kubuka kwa chizunzo kapena nsautso kunali kothekera, okhulupirira anafika kwa iye monga odzagula malonda. Malo antchitowo anamtheketsanso kukumana ndi oyang’anira mzinda.”
12, 13. Kodi ndimotani mmene lemba la 1 Akorinto 15:33 lingagwirire ntchito moyenerera pamalo antchito?
12 Komabe, Paulo anazindikira kuthekera kwa kukhala ndi “mayanjano oipa” m’malo antchito. Nafenso tiyenera kutero. Mokondweretsa, Paulo anagwira mawu mkhalidwe wamaganizo umene unali wofala pakati pa ena wakuti: “Tidye timwe pakuti maŵa timwalira.” (1 Akorinto 15:32) Mwamsanga anatsatira mawu amenewo ndi uphungu wake wonga wa atate wakuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Kodi malo antchito ndi kufunafuna zosangulutsa kungagwirizane bwanji ndi kudziika paupandu wothekera?
13 Akristu amafuna kukhala paubwenzi ndi ogwira nawo ntchito, ndipo zokumana nazo zambiri zimasonyeza mmene zimenezi zingakhalire zokhutiritsa m’kutsegula njira yochitira umboni. Komabe, wogwira naye ntchito angaone molakwa ubwenziwo kukhala mayanjano abwino kuti mudzisangalalira pamodzi. Iye angakuitaneni kukadya chakudya chamasana pamodzi, kupita kukamwa moŵa pamodzi pambuyo poŵeruka kuntchito, kapena kupita kukasanguluka pakutha pa mlungu. Munthuyu angawoneke kukhala wachifundo ndi wamakhalidwe abwino, ndipo chiitanocho chingawoneke kukhala chopanda chivulazo. Komabe, Paulo akutichenjeza kuti: “Musanyengedwe.”
14. Kodi Akristu ena anyengedwa motani ndi mayanjano?
14 Akristu ena anyengedwa. Mwapang’onopang’ono anakulitsa mkhalidwe wolekerera ndi ogwira nawo ntchito. Mwinamwake ubwenziwo unayamba chifukwa chokonda maseŵera kapena kukhala ndi chizoloŵezi chofanana. Kapena munthu wogwira naye ntchito yemwe sali Mkristu angakhale wachifundo kwambiri ndi wolingalira za ena, zimene zingakuchititseni kuthera nthaŵi yochuluka ndi munthuyo, mukumakondadi kucheza ndi iyeyo kuposa ena a mumpingo. Ndiyeno mayanjanowo angakuchititseni kuphonya msonkhano umodzi. Mwinamwake angakuchititseni kupita kocheza mpaka usiku kwambiri ndi kutaya chizoloŵezi cha kukhala ndi phande muutumiki wakumunda m’maŵa. Angakuchititseni kupenyerera kanema kapena vidiyo imene mwachizoloŵezi Mkristu angaikane. ‘Ha, zimenezo sizingachitike kwa ine,’ tingalingalire motero. Komatu ambiri a awo amene ananyengedwa poyamba angakhale anayankha mofananamo. Tifunikira kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wotsimikiza mtima motani kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo?’
15. Kodi tiyenera kukhala ndi kawonedwe kachikatikati kotani kulinga kwa anansi?
15 Zimene tangokambitsirana kumenezi ponena za kumalo antchito zingagwirenso ntchito m’mayanjano athu ndi anansi athu. Ndithudi, Akristu mu Korinto wakale anali ndi anansi. M’midzi ina muli chizoloŵezi cha kukhala aubwenzi ndi ochilikiza kwa anansi. M’madera akumidzi anansi amadalirana chifukwa cha kukhala kumalo akutali. Chibale nchamphamvu kwambiri m’mafuko ena, chikumachititsa kuitanirana nthaŵi zambiri kuchakudya. Mwachiwonekere, lingaliro lachikatikati nlofunika, monga momwe Yesu anasonyezera. (Luka 8:20, 21; Yohane 2:12) M’zochita zathu ndi anansi achibale, kodi tili ndi chikhoterero cha kupitirizabe kuchita monga momwe tinkachitira tisanakhale Akristu? M’malomwake, kodi sitiyenera kupendanso zochita zimenezo ndi kuika malire oyenerera?
16. Kodi tiyenera kumva motani mawu a Yesu a pa Mateyu 13:3, 4?
16 Panthaŵi ina Yesu anayerekezera uthenga wa Ufumu ndi mbewu zimene “zinagwa m’mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira izo.” (Mateyu 13:3, 4, 19) Panthaŵiyo, nthaka ya m’mbali mwa njira inali kulimba chifukwa cha mapazi a anthu oyenda. Ndimo mmene ziliri kwa anthu ambiri. Miyoyo yawo njodzazidwa ndi anansi, achibale, ndi ena amene amabwera ndi kupita, akumawatangwanitsa nthaŵi zonse. Zimenezi, kunena kwake titero, zimapondereza nthaka ya mitima yawo kukuchititsa kukhala kovuta kwa mbewu za chowonadi kuzika mizu. Kusamva kofananako kungachitike kwa munthu yemwe ali kale Mkristu.
17. Kodi kuyanjana kwathu ndi anansi ndi ena kungatiyambukire motani?
17 Anansi ndi achibale ena akudziko angakhale aubwenzi ndi othandiza, ngakhale kuti samasonyeza chikondwerero m’zinthu zauzimu kapena kukonda chilungamo. (Marko 10:21, 22; 2 Akorinto 6:14) Kukhala kwathu Akristu sikuyenera kutanthauza kuti tikhale opanda ubwenzi, kapena osasamala anansi athu. Yesu anatilangiza kuti tiyenera kusonyeza chikondwerero chenicheni mwa ena. (Luka 10:29-37) Komabe uphungu wa Paulo wakuti tiyenera kusamala mayanjano athu nawonso ngwouziridwa ndi wofunika. Pamene tikugwiritsira ntchito uphungu wa Yesu, sitiyenera kuiŵala uphungu wa Paulo. Ngati sitikumbukira malamulo onse aŵiriwo, makhalidwe athu angayambukiridwe. Kodi makhalidwe anu ngotani powayerekezera ndi a anansi kapena achibale anu pankhani ya kuwona mtima kapena kulabadira malamulo a Kaisara? Mwachitsanzo, akhoza kuganiza kuti polipira msonkho, kusonyeza malipiro ochepa kapena mapindu a bizinesi nkwabwino, ngakhale kofunika kuti akhalebe ndi moyo. Akhoza kulankhula moumirira ponena za malingaliro awo panthaŵi yopuma kapena paulendo wocheza waufupi. Kodi zimenezo zingayambukire motani kalingaliridwe kanu ndi makhalidwe owona mtima? (Marko 12:17; Aroma 12:2) “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”
Makhalidwe a Achicheperenso
18. Kodi nchifukwa ninji uphungu wa pa 1 Akorinto 15:33 umagwiranso ntchito kwa achichepere?
18 Achichepere amayambukiridwa kwambiri ndi zimene amawona ndi kumva. Kodi simunaone ana amene majesichala awo kapena zizoloŵezi zili zofanana kwambiri ndi za makolo awo kapena abale awo? Pamenepo, sitiyenera kudabwa kuti ana angayambukiridwe kwambiri ndi anzawo oseŵera nawo kapena ophunzira nawo. (Yerekezerani ndi Mateyu 11:16, 17.) Ngati mwana wanu amakhala ndi achichepere amene amalankhula mwamwano ponena za makolo awo, kodi mungayerekezere motani kuti zimenezi sizingayambukire ana anu? Bwanji ngati kaŵirikaŵiri amva achichepere ena akutukwana? Bwanji ngati anzawo akusukulu kapena a m’mudzimo amatengeka ndi nsapato kapena zovala zamakono? Kodi tiyenera kulingalira kuti Akristu achichepere sadzakopeka ndi chisonkhezero chimenecho? Kodi Paulo ananena kuti uphungu wa pa 1 Akorinto 15:33 umangoyambukira amene afika pamsinkhu wakutiwakuti?
19. Kodi makolo ayenera kuyesayesa kukhomereza lingaliro lotani mwa ana awo?
19 Ngati ndinu kholo, kodi mumakumbukira uphungu umenewo pamene mukukambitsirana ndi kupanga zosankha zokhudza ana anu? Mwinamwake zingakuthandizeni ngati mutavomereza kuti zimenezi sizikutanthauza kuti achichepere ena onse amene amakhala ndi ana anu m’mudzimo kapena kusukulu siabwino. Ena angakhale abwino ndi odekha, monga momwe aliri ena a anansi anu, achibale, ndi ogwira nawo ntchito. Yesani kuthandiza ana anu kuwona zimenezi ndi kumvetsetsa kuti ndinu wachikatikati m’kugwiritsira ntchito kwanu uphungu wanzeru, wonga wa atate wa Paulo kwa Akorinto. Pamene awona njira imene mumalinganizira zinthu, zimenezo zingawathandize kukutsanzirani.—Luka 6:40; 2 Timoteo 2:22.
20. Achichepere, kodi mukuyang’anizana ndi vuto lotani?
20 Inu amene mudakali achichepere, yesani kuzindikira mmene mungagwiritsirire ntchito uphungu wa Paulo, mukumadziŵa kuti ngwofunika kwa Mkristu aliyense, wachichepere kapena wachikulire. Zimenezi zidzakhala zovuta, koma bwanji osakhala ofunitsitsa kuthetsa vutolo? Dziŵani kuti kungodziŵana ndi ena a achicheperewo kuchokera paubwana sikumatanthauza kuti sangayambukire makhalidwe anu, kapena kuipsa makhalidwe amene mukuumba monga Mkristu wachichepere.—Miyambo 2:1, 10-15.
Njira Zotsimikizirika Zotetezera Makhalidwe Athu
21. (a) Kodi timafunikira chiyani ponena za mayanjano? (b) Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti mayanjano ena angakhale aupandu?
21 Tonsefe timafunikira oyanjana nawo. Komabe, tiyenera kuzindikira kuti mayanjano athu akhoza kutiyambukira, kutichititsa kukhala abwino kapena oipa. Zinali choncho kwa Adamu ndi ena onse m’zaka mazana ambiri zotsatirapo. Mwachitsanzo, Yehosafati, mfumu yabwino ya Yuda, anasangalala ndi chiyanjo ndi madalitso a Yehova. Koma pamene analola mwana wake kukwatira mwana wamkazi wa Mfumu Ahabu wa Israyeli, Yehosafati anayamba kuyanjana ndi Ahabu. Mayanjano oipa amenewo anatsala nenene kutayitsa Yehosafati moyo wake. (2 Mafumu 8:16-18; 2 Mbiri 18:1-3, 29-31) Ngati tipanga zosankha zopanda nzeru pamayanjano athu, zikhoza kukhala zaupandu mofananamo.
22. Kodi nchiyani chimene tiyenera kukumbukira, ndipo chifukwa ninji?
22 Pamenepo, tiyeni tilabadiretu uphungu wachikondi umene Paulo akutipatsa pa 1 Akorinto 15:33. Amenewo sali kokha mawu amene tawamva nthaŵi zambiri amene tingakhoze kuwabwereza pamtima. Amasonyeza chikondi chautate chimene Paulo anali nacho kwa abale ndi alongo ake a ku Korinto, ndiponso, chimafutukulidwa kwa ife. Ndipo mosakayikira ali ndi uphungu umene Atate wathu wakumwamba amapereka chifukwa amafuna kuti zoyesayesa zathu zikhale zachipambano.—1 Akorinto 15:58.
[Mawu a M’munsi]
a Upandu wina umene ma bulletin board amenewo ali nawo ndiwo chiyeso cha kuika m’kompyuta yanu maprogramu ndi mabuku amene eni ake kapena owalemba samawalola kulembedwanso, kumene kungakhale kusemphana ndi malamulo a padziko lonse oletsa kulembanso zimene ena analemba.—Aroma 13:1.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Paulo analemba lemba la 1 Akorinto 15:33 ndi chifukwa chotani?
◻ Kodi tingagwiritsire ntchito motani uphungu wa Paulo m’malo antchito?
◻ Kodi nkawonedwe kachikatikati kotani kamene tiyenera kukhala nako kwa anansi?
◻ Kodi nchifukwa ninji lemba la 1 Akorinto 15:33 lili ndi uphungu wofunika koposa kwa achichepere?
[Chithunzi patsamba 17]
Paulo anagwiritsira ntchito malo antchito kupititsa patsogolo mbiri yabwino
[Chithunzi patsamba 18]
Achichepere ena angaipse makhalidwe anu Achikristu