-
Kodi Yesu Anaukitsidwadi?Nsanja ya Olonda—2013 | March 1
-
-
Akhristu ena a ku Korinto ankakayikira ngati Yesu anaukitsidwadi ndipo ena sankakhulupirira n’komwe zoti munthu wakufa angaukitsidwe. M’kalata yoyamba imene analembera Akhristuwo, mtumwi Paulo ananena zimene zikanachitika zikanakhala kuti akufa sangaukitsidwe. Iye analemba kuti: “Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanauke. Koma ngati Khristu sanauke, kulalikira kwathu n’kopanda pake, ndipo chikhulupiriro chathu n’chopanda pake. Ndiponso, ndiye kuti ifenso takhala mboni zonama za Mulungu, . . . chikhulupiriro chanu chilibe ntchito ndipo mukadali m’machimo anu. Ndiye kutinso anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu, kutha kwawo kunali komweko.”—1 Akorinto 15:13-18.
“Anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi . . . Kenako anaonekera kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse. Koma pomalizira pake anaonekera kwa ine.”—1 Akorinto 15:6-8.
-
-
Kodi Yesu Anaukitsidwadi?Nsanja ya Olonda—2013 | March 1
-
-
Komanso zikanakhala kuti Khristu sanaukitsidwe, bwenzi chikhulupiriro cha Akhristu chili chopanda ntchito komanso chabodza. Ndiponso Paulo ndi Akhristu ena akanakhala akunena zabodza, osati zokhudza Yesu yekha, koma zokhudzanso Yehova Mulungu amene ankati anaukitsa Yesuyo. Kuwonjezera pamenepa, mfundo yoti Khristu “anafera machimo athu,” ikanakhala yabodza chifukwa ngati munthu sanapulumutsidwe ku imfa angakhale bwanji Mpulumutsi wa anthu ena? (1 Akorinto 15:3) Zimenezi zikanatanthauzanso kuti Akhristu amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, anafa ndi chikhulupiriro chabodza choti adzaukitsidwa.
-