Mutu 41
Tsiku Lopereka Chiweruzo la Mulungu Lidzabweretsa Madalitso Osangalatsa Kwambiri
Masomphenya 15—Chivumbulutso 20:11–21:8
Nkhani yake: Kuuka kwa akufa, Tsiku la Chiweruzo, ndi madalitso obwera chifukwa cha kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000
1. (a) Kodi anthu anataya chiyani Adamu ndi Hava atachimwa? (b) Kodi ndi cholinga chiti cha Mulungu chimene sichinasinthe, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?
ANTHUFE tinalengedwa kuti tikhale ndi moyo kwamuyaya. Adamu ndi Hava sakanafa akanamvera malamulo a Mulungu. (Genesis 1:28; 2:8, 16, 17; Mlaliki 3:10, 11) Koma iwo atachimwa, anataya mwayi wokhala ndi moyo komanso wokhala anthu angwiro. Zimenezi zinakhudzanso mbadwa zawo, ndipo imfa inayamba kulamulira anthu monga mdani wosowetsa mtendere kwambiri. (Aroma 5:12, 14; 1 Akorinto 15:26) Koma cholinga cha Mulungu choti anthu angwiro akhale ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi sichinasinthe. Chifukwa chakuti Mulungu amakonda kwambiri anthu, anatumiza Yesu, Mwana wake wobadwa yekha, kudziko lapansi kudzapereka moyo wake monga munthu wangwiro kuti ukhale dipo lowombola ana “ambiri” a Adamu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Tsopano Yesu adzagwiritsira ntchito nsembe yake yangwiroyi kuti athandize anthu okhulupirira Mulungu kukhalanso ndi moyo wangwiro m’paradaiso padziko lapansi. (1 Petulo 3:18; 1 Yohane 2:2) Chimenechi ndi chifukwadi chabwino kwambiri choti anthufe “tisangalale ndi kukondwera.”—Yesaya 25:8, 9.
2. Kodi Yohane ananena chiyani pa Chivumbulutso 20:11, ndipo “mpando wachifumu waukulu woyera” n’chiyani?
2 Satana akadzatsekeredwa kuphompho, ulamuliro wosangalatsa wa Yesu wa zaka 1,000 udzayamba. Limeneli lidzakhala “tsiku” limene Mulungu ‘akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika.’ (Machitidwe 17:31; 2 Petulo 3:8) Yohane anati: “Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso.” (Chivumbulutso 20:11) Kodi “mpando wachifumu waukulu woyera” umenewu n’chiyani? Uyenera kuti si winanso ayi, koma ndi mpando woweruzira milandu wa “Mulungu, Woweruza wa onse.” (Aheberi 12:23) Tsopano iye adzaweruza anthu kuti aone amene akuyenera kulandira madalitso chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu.—Maliko 10:45.
3. (a) Kodi mfundo yakuti mpando wachifumu wa Mulungu ndi “waukulu” komanso “woyera” ikutanthauza chiyani? (b) Kodi ndani adzagwire ntchito yoweruza pa Tsiku la Chiweruzo, ndipo adzagwiritsira ntchito mfundo za ndani?
3 Lembali lafotokoza kuti mpando wachifumu wa Mulungu ndi “waukulu.” Zimenezi zikutsindika mfundo yakuti Yehova ndi wamkulu, popeza iye ndi Ambuye Wamkulu Koposa. Komanso mpando wachifumuwu ndi “woyera,” posonyeza kuti Mulungu amachita chilungamo nthawi zonse. Iye ndiye Woweruza wamkulu wa anthu onse. (Salimo 19:7-11; Yesaya 33:22; 51:5, 8) Komabe, iye wapereka udindo woweruza kwa Yesu Khristu. Baibulo limati: “Atate saweruza munthu aliyense, koma wapereka udindo wonse woweruza kwa Mwana.” (Yohane 5:22) Yesu adzagwira ntchito imeneyi limodzi ndi oweruza anzake okwana 144,000, amene “anapatsidwa mphamvu yoweruza . . . [kwa] zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:4) Ngakhale zili choncho, poweruzapo adzagwiritsira ntchito mfundo za Yehova kuti adziwe mmene akuyenera kuweruzira munthu aliyense pa Tsiku la Chiweruzo limeneli.
4. Kodi mawu akuti “dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake” akutanthauza chiyani?
4 Kodi “dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake,” m’njira yotani? Kumwamba kumeneku n’komwe kuja kumene kunakanganuka ngati mpukutu pamene chidindo cha 6 chinamatulidwa. Kukuimira anthu olamulira amene ‘awasungira moto m’tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.’ (Chivumbulutso 6:14; 2 Petulo 3:7) Dziko lapansi likuimira dongosolo lochitira zinthu limene lilipo pa nthawi ya olamulira amenewa. (Chivumbulutso 8:7) Kumwamba ndi dziko lapansi kudzathawa pamaso pa Mulungu iye akadzawononga chilombo, mafumu a dziko lapansi ndi magulu awo a nkhondo, anthu amene analandira chizindikiro cha chilombo, komanso amene analambira chifaniziro chake. (Chivumbulutso 19:19-21) Chiweruzo chimenechi chikadzaperekedwa pa “dziko lapansi” ndi “kumwamba” zolamulidwa ndi Satana, tsopano Woweruza Wamkulu adzalamula kuti tsiku lina lopereka chiweruzo liyambe.
Tsiku la Chiweruzo la Zaka 1,000
5. Dziko lapansi lakale ndiponso kumwamba kwakale zikadzathawa pamaso pa Mulungu, kodi ndani amene adzatsale kuti aweruzidwe?
5 Dziko lapansi lakale ndiponso kumwamba kwakale zikadzathawa pamaso pa Mulungu, kodi ndani amene adzatsale kuti aweruzidwe? Sadzakhala anthu ena a 144,000 omwe adzakhale adakali padziko lapansi, chifukwa amenewa adzakhala ataweruzidwa ndi kuikidwa kale chidindo. Ngati anthu ena a 144,000 adzakhale adakali ndi moyo padziko lapansi Aramagedo itatha, iwo adzafunika kufa pasanapite nthawi yaitali n’kuukitsidwa kuti akalandire mphoto yawo kumwamba. (1 Petulo 4:17; Chivumbulutso 7:2-4) Koma anthu mamiliyoni ambiri a khamu lalikulu amene adzatuluke m’chisautso chachikulu adzaimirira moonekera “pamaso pa mpando wachifumu.” Iwo adzakhala oti Mulungu akuwaona kale kuti ndi olungama chifukwa chokhulupirira magazi amene Yesu anakhetsa. N’chifukwa chake adzawapulumutse pa Aramagedo. Komabe, iwo adzayenera kupitiriza kuweruzidwa pa zaka 1,000 pamene Yesu azidzawatsogolera “ku akasupe a madzi a moyo.” Iwo akadzathandizidwa kusintha n’kukhalanso angwiro, kenako n’kuyesedwa, Mulungu adzawaona kuti tsopano ndi olungamadi. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14, 17) Ana amene adzapulumuke pa chisautso chachikulu, komanso ana alionse amene adzabadwe kwa anthu a khamu lalikulu pa Zaka 1,000, nawonso adzafunika kuweruzidwa pa zaka zimenezo.—Yerekezerani ndi Genesis 1:28; 9:7; 1 Akorinto 7:14.
6. (a) Kodi anthu ochuluka amene Yohane anaona ndi ndani, ndipo mawu akuti “olemekezeka ndi onyozeka” akutanthauza chiyani? (b) Kodi zikuoneka kuti anthu mamiliyoni ochuluka amene Mulungu akuwakumbukira adzaukitsidwa motani?
6 Koma Yohane anaona anthu ochuluka zedi kuposa khamu lalikulu limene lidzapulumuke pa chisautso chachikulu. Anthuwa adzakhalapo okwana mamiliyoni ambiri zedi. Yohane anati: “Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa.” (Chivumbulutso 20:12a) “Olemekezeka ndi onyozeka” amenewa ndi anthu omwe anali ndi maudindo apamwamba komanso anthu wamba amene anakhala ndi moyo n’kufa padziko lapansi pa zaka 6,000 zapitazi. Mu Uthenga Wabwino umene mtumwi Yohane analemba atangomaliza kumene kulemba buku la Chivumbulutso, Yesu ponena za Atate ake anati: “Amupatsanso [Yesu] mphamvu zoweruza, chifukwa iye ndi Mwana wa munthu. Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:27-29) Imeneyi idzakhala ntchito yosangalatsa kwambiri, yobwezeretsanso moyo kwa anthu ambirimbiri amene akhala akufa n’kumaikidwa m’manda m’mbiri yonse ya anthu. Zikuoneka kuti anthu mamiliyoni ochuluka amene Mulungu akuwakumbukira adzaukitsidwa pang’onopang’ono. Izi zidzachitika kuti anthu a khamu lalikulu, omwe adzakhale ochepa powayerekezera ndi anthu omwe adzaukitsidwe, adzakwanitse kuthana ndi mavuto alionse amene angadzakhalepo pa nthawiyo. Mwina anthu oukitsidwawo poyamba angamadzakhalebe moyo wofanana ndi moyo wawo wakale, n’kumatsatira zilakolako zoipa za thupi komanso kumachita makhalidwe ena oipa.
Kodi Ndani Amene Adzaukitsidwe ndi Kuweruzidwa?
7, 8. (a) Kodi panatsegulidwa mpukutu uti ndipo kenako chinachitika n’chiyani? (b) Kodi ndani amene sadzaukitsidwa?
7 Yohane akupitiriza kuti: “Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo. Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.” (Chivumbulutso 20:12b, 13) Zimenezi zidzakhala zochititsa chidwi kwambiri. ‘Nyanja, imfa ndi Manda’ zonse zikukhudzidwa, komabe sizikutanthauza kuti munthu amene wafera m’nyanja ndiye kuti sali m’Manda.a Mwachitsanzo, pamene Yona anali m’mimba mwa chinsomba m’nyanja, ananena kuti anali m’Manda. (Yona 2:2) Choncho ngati munthu wamwalira chifukwa cha uchimo wochokera kwa Adamu, ndiye kuti mwina ali m’manda a anthu onse, ndipo Mulungu akumukumbukirabe. Mawu aulosi amene ali pa Chivumbulutso 20:12, 13, akutipatsa umboni wamphamvu wotsimikizira kuti onse amene Mulungu akuwakumbukira adzaukitsidwa.
8 Komabe, pali anthu ena amene sadzaukitsidwa ndipo chiwerengero chawo sichikudziwika. Ena mwa anthu amenewa ndi alembi ndi Afarisi osalapa amene anakana Yesu ndi atumwi ake, komanso “munthu wosamvera malamulo” yemwe akuimira atsogoleri a zipembedzo, ndiponso Akhristu odzozedwa omwe “anagwa.” (2 Atesalonika 2:3; Aheberi 6:4-6; Mateyu 23:29-33) Yesu ananenanso za anthu angati mbuzi amene pamapeto a dzikoli adzapita “kumoto wosatha wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake.” Motowu ukutanthauza “chiwonongeko chotheratu.” (Mateyu 25:41, 46) Ndithudi, anthu onsewa sadzaukitsidwa.
9. Kodi mtumwi Paulo ananena chiyani za anthu amene adzaukitsidwe, ndipo ena mwa anthu amenewa ndani?
9 Koma ponena za kuuka kwa akufa, mtumwi Paulo anati: “Ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Ena mwa anthu “olungama” amene adzaukitsidwe n’kukhala ndi moyo padziko lapansi ndi amuna ndi akazi akale, omwe anali okhulupirika monga Abulahamu, Rahabi, ndi ena ambiri. Mulungu ankaona anthu amenewa kuti anali olungama ndipo anali mabwenzi ake. (Yakobo 2:21, 23, 25) Komanso m’gulu la anthu olungamawa muli anthu a nkhosa zina amene anafa ali okhulupirika kwa Yehova m’nthawi yathu ino. Ndipo zikuoneka kuti anthu onsewa, amene anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, adzaukitsidwa cha kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yesu wa zaka 1,000. (Yobu 14:13-15; 27:5; Danieli 12:13; Aheberi 11:35, 39, 40) N’kutheka kuti ambiri mwa anthu olungama omwe adzaukitsidwewa adzapatsidwa mwayi wapadera woyang’anira ntchito yaikulu kwambiri yobwezeretsa Paradaiso padzikoli.—Salimo 45:16; yerekezerani ndi Yesaya 32:1, 16-18; 61:5; 65:21-23.
10. Pa anthu amene adzaukitsidwe, kodi “osalungama” ndani?
10 Nanga kodi “osalungama” amene atchulidwa pa Machitidwe 24:15, ndani? M’gulu limeneli muli anthu ambirimbiri amene akhala akumwalira m’mbiri yonse ya anthu, makamaka amene anakhala ndi moyo ‘m’nthawi ya kusadziwa.’ (Machitidwe 17:30) Anthu amenewa analibe mwayi wophunzira za Yehova kuti azitha kuchita chifuniro chake, mwina chifukwa cha kumene anabadwira kapena nyengo imene anabadwa. Komanso n’kutheka kuti pali anthu ena amene anamva uthenga wa chipulumutso, koma pa nthawiyo sanasinthe moyo wawo mokwanira kapena anamwalira asanafike podzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa. Anthu amenewa akadzapatsidwa mwayi woukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo, adzafunika kupitiriza kusintha maganizo awo komanso moyo wawo kuti adzalandire moyo wosatha.
Mpukutu wa Moyo
11. (a) Kodi “mpukutu wa moyo” n’chiyani ndipo muli mayina a ndani? (b) N’chifukwa chiyani mpukutu wa moyo udzatsegulidwe mu Ulamuliro wa Zaka 1,000?
11 Yohane ananenanso za “mpukutu wa moyo.” Mumpukutu umenewu muli mayina a anthu amene Yehova adzawapatse moyo wosatha. Ena mwa mayina amene alembedwa mumpukutuwu ndi a abale a Yesu odzozedwa, a anthu a khamu lalikulu, ndiponso a anthu akale okhulupirika, monga Mose. (Ekisodo 32:32, 33; Danieli 12:1; Chivumbulutso 3:5) Pa nthawiyo, mayina a anthu “osalungama” adzakhala asanalembedwe mumpukutu wa moyowu. Choncho mpukutu wa moyo udzatsegulidwa mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 n’cholinga choti mulembedwe mayina a anthu ena amene adzayesetse kuchita zinthu zowayenereza kulembedwa mumpukutuwu. Ndipo anthu amene mayina awo sadzalembedwa mumpukutu wa moyo, kapena kuti m’buku la moyo, ‘adzaponyedwa m’nyanja yamoto.’—Chivumbulutso 20:15; yerekezerani ndi Aheberi 3:19.
12. Kodi n’chiyani chimene chidzachititse kuti dzina la munthu lilembedwe mumpukutu wa moyo womwe udzakhale wotsegula, nanga Woweruza amene Yehova anamusankha anatipatsa chitsanzo chotani?
12 Nanga n’chiyani chimene chidzachititse kuti dzina la munthu lilembedwe mumpukutu wa moyo womwe udzakhale wotsegula pa nthawiyo? Mfundo yaikulu idzakhala kumvera Yehova, ngati mmene zinalili m’masiku a Adamu ndi Hava. Mtumwi Yohane analembera Akhristu anzake okondedwa kuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yohane 2:4-7, 17) Pa nkhani ya kumvera, Woweruza amene Yehova anamusankha anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. Baibulo limati: “Ngakhale kuti [Yesu] anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo. Ndipo atakhala wangwiro, anakhala ndi udindo wopereka chipulumutso chamuyaya kwa onse omumvera.”—Aheberi 5:8, 9.
Mipukutu Inanso Idzatsegulidwa
13. Kodi anthu oukitsidwa adzayenera kuchita chiyani posonyeza kuti ndi omvera, ndipo adzayenera kutsatira mfundo zotani?
13 Kodi anthu oukitsidwawo adzayenera kuchita chiyani posonyeza kuti ndi omvera? Yesu anatchula malamulo awiri aakulu kwambiri pamene anati: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi. Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’ Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” (Maliko 12:29-31) Palinso mfundo za Yehova zodziwika bwino zimene iwo adzayenera kutsatira, monga kusiya kuba, kunama, kupha anthu, ndi chiwerewere.—1 Timoteyo 1:8-11; Chivumbulutso 21:8.
14. Kodi padzatsegulidwanso mipukutu ina iti, ndipo m’mipukutu imeneyi mudzakhala chiyani?
14 Koma Yohane wangotchula kumene mipukutu ina imene idzatsegulidwe pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000. (Chivumbulutso 20:12) Kodi m’mipukutu imeneyi mudzakhala zotani? Nthawi zina, Yehova waperekapo malangizo apadera oti anthu atsatire pa nthawinso zapadera. Mwachitsanzo m’nthawi ya Mose, iye anapereka malamulo atsatanetsatane ndipo ngati Aisiraeli akanamvera malamulo amenewa, akanakhalabe ndi moyo. (Deuteronomo 4:40; 32:45-47) Mu nthawi ya atumwi, Mulungu anapereka malangizo atsopano kuti athandize anthu okhulupirika kutsatira mfundo za Yehova mumpingo wachikhristu. (Mateyu 28:19, 20; Yohane 13:34; 15:9, 10) Tsopano Yohane akutiuza kuti akufa ‘adzaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.’ Choncho zikuoneka kuti mipukutu imeneyi ikadzatsegulidwa, anthu adzapatsidwa malangizo atsatanetsatane a Yehova ofotokoza zimene anthuwo adzafunike kuchita pa zaka 1,000. Anthu omvera amene adzatsatire malangizo ndi malamulo a m’mipukutu imeneyo adzakhala ndi moyo wautali, ndipo pamapeto pake adzakhala ndi moyo wosatha.
15. Kodi pa nthawi ya kuuka kwa akufa, anthu adzafunika kugwira ntchito yotani yophunzitsa ena, ndipo zikuoneka kuti akufa adzaukitsidwa potsatira ndondomeko yotani?
15 Zoonadi, padzakhala ntchito yaikulu kwambiri yophunzitsa anthu za chifuniro cha Mulungu. Mu 2010 pa avereji, Mboni za Yehova zinkaphunzira Baibulo ndi anthu okwana 8,058,359 m’malo osiyanasiyana. Koma anthu akadzaukitsidwa, mosakayikira padzakhala anthu mamiliyoni osawerengeka amene azidzaphunzitsidwa pogwiritsira ntchito Baibulo ndi mipukutu yatsopanoyo. Anthu onse a Mulungu adzafunika kukhala aphunzitsi ndiponso adzafunika kugwira ntchito imeneyi mwakhama. Mosakayikira anthu oukitsidwa akamaphunzitsidwa, nawonso adzayamba kugwira nawo ntchito yaikulu yophunzitsa anthu ena. Zikuoneka kuti anthu akamadzaukitsidwa, ndondomeko yake idzakhala yakuti amene ali ndi moyo adzakhale ndi mwayi wolandira ndi kuphunzitsa achibale awo ndi anzawo amene anamwalira. Ndipo kenako amenewanso adzatha kulandira ndi kuphunzitsa achibale awo ndi anzawo ena. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 15:19-28, 58.) Anthu a Mboni za Yehova oposa 7 miliyoni amene akugwira ntchito yolengeza choonadi masiku ano, akuyala maziko abwino a ntchito yapadera imene akuyembekezera kudzagwira pa nthawi ya kuuka kwa akufa.—Yesaya 50:4; 54:13.
16. (a) Kodi mumpukutu wa moyo, kapena kuti m’buku la moyo, simudzalembedwa mayina a ndani? (b) Kodi ndi anthu ati amene kuuka kwawo kudzakhaladi koti “alandire moyo”?
16 Ponena za anthu amene adzaukitsidwe padziko lapansi, Yesu anati “amene anali kuchita zabwino adzauka kuti alandire moyo. Amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.” Palembali akusiyanitsa “moyo” ndi ‘kuweruzidwa,’ kutanthauza kuti anthu oukitsidwa amene ‘adzachite zoipa’ pambuyo pophunzitsidwa mfundo za m’Malemba ouziridwa ndiponso za m’mipukutu, adzaweruzidwa kuti ndi osayenera kukhala ndi moyo. Mayina awo sadzalembedwa mumpukutu wa moyo, kapena kuti m’buku la moyo. (Yohane 5:29) Zidzakhalanso chimodzimodzi ndi munthu aliyense amene m’mbuyomu anali wokhulupirika koma pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000, n’kukhala wosamvera pa zifukwa zina, chifukwa mayina akhoza kufufutidwa m’bukuli. (Ekisodo 32:32, 33) Koma mayina a anthu amene adzatsatire malangizo olembedwa m’mipukutu adzakhalabe mumpukutu wa moyo, ndipo iwo adzapitirizabe kukhala ndi moyo. Kwa anthu amenewa, kuuka kwawo kudzakhaladi koti “alandire moyo.”
Mapeto a Imfa ndi Manda
17. (a) Kodi Yohane anafotokoza zinthu zotani zosangalatsa kwambiri? (b) Kodi ndi liti pamene m’manda a anthu onse simudzakhalanso anthu? (c) Kodi imfa yochokera kwa Adamu idzaponyedwa liti “m’nyanja yamoto”?
17 Kenako Yohane anafotokoza zinthu zosangalatsa kwambiri. Iye anati: “Ndipo imfa ndi Manda zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri. Komanso, aliyense amene sanapezeke atalembedwa m’buku la moyo anaponyedwa m’nyanja yamoto.” (Chivumbulutso 20:14, 15) Pofika kumapeto kwa Tsiku la Chiweruzo la zaka 1,000, “imfa ndi Manda” zidzachotsedwa, ndipo sizidzakhalaponso. Koma kodi n’chifukwa chiyani zidzatenge zaka 1,000 kuti zimenezi zitheke? M’manda a anthu onse simudzakhalanso munthu aliyense pambuyo poti anthu onse akufa amene Mulungu anali kuwakumbukira aukitsidwa. Koma kwa nthawi yonse imene anthu adzakhale ndi uchimo umene anatengera kwa makolo awo, imfa yochokera kwa Adamu idzakhala idakali nawobe. Anthu onse amene adzaukitsidwe padziko lapansi, komanso a khamu lalikulu amene adzapulumuke pa Aramagedo, adzafunika kumvera zinthu zimene zidzalembedwe m’mipukutu kufikira pamene dipo la Yesu lidzachotseretu matenda, ukalamba, ndi zofooka zina zimene anatengera kwa makolo awo. Kenako imfa yochokera kwa Adamu, limodzi ndi Manda, ‘zidzaponyedwa m’nyanja yamoto,’ ndipo sizidzakhalaponso mpaka kalekale.
18. (a) Kodi mtumwi Paulo ananena chiyani posonyeza kuti ulamuliro wa Yesu monga Mfumu udzakwaniritsa cholinga chake? (b) Kodi Yesu adzachita chiyani ndi mtundu wa anthu amene adzakhale atasintha n’kukhalanso angwiro? (c) Kodi pamapeto pa zaka 1,000 padzachitikanso zinthu zina zotani?
18 Choncho ndondomeko imene mtumwi Paulo anafotokoza m’kalata yake yopita kwa Akorinto idzafika pamapeto pake. Iye anati: “Pakuti [Yesu] ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Imfa [yochokera kwa Adamu] nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.” Kodi kenako n’chiyani chidzachitike? “Zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake.” Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu “adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.” (1 Akorinto 15:24-28) Inde, Yesu akadzagonjetsa imfa yochokera kwa Adamu pogwiritsa ntchito nsembe yake ya dipo, adzapereka kwa Atate ake, Yehova, mtundu wa anthu amene adzakhale atasintha n’kukhalanso angwiro. Zikuoneka kuti pa nthawi imeneyi, pamapeto pa zaka 1,000, Satana adzamasulidwa ndipo anthu adzayesedwa komaliza kuti amene mayina awo akuyenera kukhala mpaka kalekale mumpukutu wa moyo, adziwike. Choncho “yesetsani mwamphamvu” kuti dzina lanu lidzakhale limodzi mwa mayina amenewa.—Luka 13:24; Chivumbulutso 20:5.
[Mawu a M’munsi]
a Anthu oipa omwe anafa pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa sali m’gulu la anthu amene adzaukitsidwe kuchokera m’nyanja. Chilango chimene anthu amenewo anapatsidwa n’chomaliza, mofanana ndi chilango chimene Yehova adzapereke poweruza anthu pa chisautso chachikulu.—Mateyu 25:41, 46; 2 Petulo 3:5-7.
[Chithunzi patsamba 298]
“Osalungama” amene adzaukitsidwe, omwe adzamvere malangizo a m’mipukutu imene idzatsegulidwe pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000, mayina awo akhozanso kudzalembedwa mumpukutu wa moyo