-
“Kodi Akufa Adzaukitsidwa Motani?”Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2020 | December
-
-
3. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 15:30-32, kodi zimene Paulo ankakhulupirira zoti akufa adzaukitsidwa zinamuthandiza bwanji?
3 Paulo anakwanitsa kupirira mavuto osiyanasiyana chifukwa choti ankakhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa. (Werengani 1 Akorinto 15:30-32.) Iye anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Tsiku ndi tsiku ndimakhala pa ngozi yoti ndikhoza kufa.” Paulo analembanso kuti: “Ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso.” N’kutheka kuti iye ankanena zomenyana ndi zilombo zenizeni m’bwalo la masewera ku Efeso. (2 Akor. 1:8; 4:10; 11:23) Kapenanso ankanena za Ayuda ndi anthu ena ankhanza amene anali ngati “zilombo zakutchire.” (Mac. 19:26-34; 1 Akor. 16:9) Kaya ankanena za chiyani, Paulo anakumana ndi mavuto aakulu komabe ankakhulupirira kuti m’tsogolo adzakhala ndi moyo wosangalala.—2 Akor. 4:16-18.
-
-
“Kodi Akufa Adzaukitsidwa Motani?”Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2020 | December
-
-
5. Kodi ndi maganizo oopsa ati amene angatipangitse kuti tisiye kukhulupirira kuti akufa adzauka?
5 Paulo anachenjeza abale ake kuti apewe maganizo oopsa omwe anthu ena anali nawo, akuti: “Ngati akufa sadzauka, ‘tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.’” Ndipotu anthu ena anali ndi maganizo amenewa ngakhale nthawi ya Paulo isanafike. N’kutheka kuti iye ananena mawu opezeka pa Yesaya 22:13, amene akufotokoza maganizo omwe Aisiraeli anali nawo. M’malo molimbitsa ubwenzi wawo ndi Mulungu, iwo ankakonda zinthu zosangalatsa. Tinganene kuti Aisiraeliwo anali ndi maganizo akuti, ‘Tisangalaliretu ndi moyo panopa chifukwa tikhoza kufa nthawi iliyonse.’ Maganizo amenewa ndi ofalanso masiku ano. Koma Baibulo limafotokoza zinthu zoipa zimene zinachitikira mtundu wa Isiraeli chifukwa cha maganizo olakwika omwe anali nawowa.—2 Mbiri 36:15-20.
6. Kodi kukhulupirira kuti akufa adzauka kumatithandiza bwanji kusankha bwino ocheza nawo?
6 Tikudziwa kuti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalira ndipo zimenezi ziyenera kutithandiza kusankha bwino anthu ocheza nawo. Abale a ku Korinto ankafunika kupewa kucheza ndi anthu amene ankatsutsa zoti akufa adzauka. Pamenepa phunziro kwa ife ndi lakuti: Tikamacheza kwambiri ndi anthu amene saganizira zam’tsogolo koma amangoganizira zinthu zosangalatsa, angatisokoneze. Ngati Mkhristu weniweni atamacheza ndi anthu amenewa, angayambe kutengera maganizo ndi makhalidwe oipa. Ndipotu anthu amenewa angamuchititse kuti ayambe kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. N’chifukwa chake Paulo akutilimbikitsa kuti: “Dzukani ku tulo tanu kuti mukhale olungama ndipo musamachite tchimo.”—1 Akor. 15:33, 34.
-