Kodi Tikhalire Moyo Zalero Kapena Zamtsogolo Mosatha?
“Tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo [ichi, NW].”—AROMA 8:24.
1. Kodi otsatira Epicurus anaphunzitsanji, ndipo kodi filosofi imeneyo inawakhudza motani Akristu ena?
MTUMWI Paulo analembera Akristu a ku Korinto kuti: “Nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa?” (1 Akorinto 15:12) Mwachionekere, filosofi yoipitsitsa ya mwamuna wina wanzeru wachigiriki Epicurus inali italoŵerera Akristu ena a m’zaka za zana loyamba. Choncho Paulo anatchula za chiphunzitso cha Epicurus chakuti: “Tidye timwe pakuti maŵa timwalira.” (1 Akorinto 15:32) Atanyozera chiyembekezo chilichonse cha moyo pambuyo pa imfa, otsatira wafilosofi ameneyu anakhulupirira kuti chisangalalo chakuthupi ndicho chinali chinthu chabwino koposa m’moyo. (Machitidwe 17:18, 32) Filosofi ya Epicurus inali yongoganizira za iwe mwini, yofuna kupeza ena zifukwa, ndipo yoluluza kotheratu.
2. (a) Kodi nchifukwa ninji kunali kwangozi kwambiri kukana za chiukiriro? (b) Kodi Paulo analimbitsa motani chikhulupiriro cha Akristu a ku Korinto?
2 Kukana chiukiriro kumeneku kunatanthauza zazikulu. Paulo anati: “Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa; ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe. . . . Ngati tiyembekezera Kristu m’moyo uno wokha, tili ife aumphaŵi oposa a anthu onse.” (1 Akorinto 15:13-19) Inde, popanda chiyembekezo chamtsogolo mosatha, Chikristu chikanakhala ‘chachabe.’ Chikanakhala chopanda pake. Ndiye chifukwa chake, utasonkhezeredwa ndi malingaliro achikunja ameneŵa, mpingo wa ku Korinto unali utadzala mavuto okhaokha. (1 Akorinto 1:11; 5:1; 6:1; 11:20-22) Chotero, Paulo anali ncholinga cholimbitsa chikhulupiriro chawo pachiukiriro. Mwa kugwiritsira ntchito kulingalira kotsatirika bwino, kugwira mawu Malemba, ndi mafanizo, iye anapereka umboni wosatsutsika wakuti chiyembekezo cha chiukiriro sichinali nthanthi koma chinthu chenicheni chimene chidzakwaniritsidwadi. Pamaziko ameneŵa, analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”—1 Akorinto 15:20-58.
“Dikirani”
3, 4. (a) Malinga ndi Petro, kodi ndi mzimu wangozi wotani umene ambiri adzagwidwa nawo m’masiku otsiriza? (b) Kodi tiyenera kumakumbukira chiyani?
3 Lerolino, ambiri ali ndi mzimu wokayikakayika, wongokhalira zalero. (Aefeso 2:2) Zili monga momwe mtumwi Petro ananeneratu. Iye ananena za “onyoza ndi kuchita zonyoza, . . . kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.” (2 Petro 3:3, 4) Alambiri oona atatengako lingaliro limeneli, akhoza kukhala “aulesi kapena opanda zipatso.” (2 Petro 1:8) Komabe, sizili tero ndi anthu a Mulungu ochuluka lerolino.
4 Sikulakwa kusamala za mapeto akudzawo a dongosolo loipali. Kumbukirani chisamaliro chimene atumwi a Yesuwo anasonyeza: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” Yesu anayankha nati: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa Iye yekha.” (Machitidwe 1:6, 7) Mawuwo ali ndi uthenga waukulu umene anapereka pa Phiri la Azitona wakuti: “Simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. . . . Munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mateyu 24:42, 44) Nthaŵi zonse tiyenera kumakumbukira uphungu umenewu! Ena anganyengedwe ndi maganizo akuti, ‘Mwina ndiyenera kungochepetsako changu ndi kusada nkhaŵa kwambiri ndi zinthu.’ Kungakhaledi kulakwa kotani kumeneko! Talingalirani za Yakobo ndi Yohane, “Ana a bingu.”—Marko 3:17.
5, 6. Kodi tingaphunzirenji pa zitsanzo za Yakobo ndi Yohane?
5 Tikudziŵa kuti Yakobo analidi mtumwi wachangu kwambiri. (Luka 9:51-55) Mpingo wachikristu utakhazikitsidwa, ayenera kuti anachita mbali yaikulu. Koma Herode Agripa I anamupha Yakobo akali wamng’ono ndithu. (Machitidwe 12:1-3) Kodi tingaganize kuti Yakobo, ataona moyo wake ulikutha mosayembekezereka, anamva chisoni kuti anali wachangu kwambiri, kuti analimbikira kuchita utumiki wake? Mpang’ono pomwe! Ndithudi anasangalala kuti moyo wake waufupiwo anauthera mu utumiki wa Yehova. Leroli, palibe aliyense wa ife amene akudziŵa ngati moyo wake udzatha mosayembekezereka. (Mlaliki 9:11; yerekezerani ndi Luka 12:20, 21.) Choncho nkwanzerudi kukhalabe achangu kwambiri ndi ogwiritsa ntchito potumikira Yehova. Tikatero tidzakhalabe ndi dzina labwino kwa iye ndi kupitirizabe kukhala ndi moyo tikumayembekezera mtsogolo mosatha.—Mlaliki 7:1.
6 Pali chochitika china chopereka phunziro chokhudza mtumwi Yohane, amene analipo pamene Yesu analimbikitsa mwamphamvu kuti: “Dikirani.” (Mateyu 25:13; Marko 13:37; Luka 21:34-36) Yohane analabadira zimenezo, natumikira mwachangu zaka makumi ambiri. Ndipotu zikuoneka kuti ndiye anatsala atumwi ena onse atafa. Yohane atakalamba kwambiri, natha kukumbukira zaka makumi ambiri za ntchito yokhulupirika, kodi iye anaona monga analakwitsa, kuti unali moyo umene anawawanya kapena umene unali wosalinganizika? Kutalitali! Anali kuyembekezerabe mwachidwi zamtsogolo. Yesu woukitsidwayo atanena kuti, “Indetu; ndidza msanga,” pomwepo Yohane anayankha kuti, “Amen; idzani Ambuye Yesu.” (Chivumbulutso 22:20) Ndithudi Yohane sanali kukhalira moyo zapanthaŵiyo, namalakalaka moyo wabata ndi ‘wabwino’ wongoti phee. Anatsimikiza mtima kutumikirabe ndi moyo wake wonse ndi mphamvu zake zonse, mpaka nthaŵi iliyonse imene Ambuye akadza. Nanga ifeyo?
Maziko a Chikhulupiriro cha Moyo Wosatha
7. (a) Kodi ndi motani mmene chiyembekezo cha moyo wosatha ‘anachilonjezera zisanayambe nthaŵi zosayamba’? (b) Kodi Yesu anaunikirapo motani pankhani ya chiyembekezo cha moyo wosatha?
7 Musakayikire konse kuti mwina chiyembekezo cha moyo wosatha ndi loto la munthu kapena nchongoyerekezera. Monga momwe Tito 1:2 amanenera, kudzipereka kwathu kwaumulungu kwazikidwa pa “chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthaŵi zosayamba.” Chifuno choyambirira cha Mulungu chinali chakuti anthu onse omvera akhale ndi moyo kosatha. (Genesis 1:28) Palibe chilichonse chimene chingasokoneze chifuno chimenechi, osati ngakhale kupanduka kwa Adamu ndi Hava. Monga momwe zalembedwera pa Genesis 3:15, Mulungu nthaŵi yomweyo analonjeza za “mbewu” imene idzachotsapo zopweteka zonse zodzetsedwa pa anthu. Pamene “mbewu” imeneyo kapena kuti Mesiya, Yesu, anafika, anapanga chiyembekezo cha moyo wosatha kukhala chimodzi cha ziphunzitso zake zazikulu. (Yohane 3:16; 6:47, 51; 10:28; 17:3) Mwa kupereka dipo moyo wake wangwiro, Kristu mwalamulo anakhala ndi kuyenera kopatsa moyo wosatha kwa anthu. (Mateyu 20:28) Ena mwa ophunzira ake, 144,000 onse pamodzi, adzakhala kosatha kumwamba. (Chivumbulutso 14:1-4) Choncho amene nthaŵi ina anali anthu okhoza kufa ‘adzavala chosafa’!—1 Akorinto 15:53.
8. (a) Kodi ‘kusakhoza kufa’ nchiyani, ndipo nchifukwa ninji Yehova akuwapatsa moyo wotero a 144,000? (b) Kodi Yesu anawapatsa chiyembekezo chotani a “nkhosa zina”?
8 ‘Kusakhoza kufa’ sikumangotanthauza kusafa. Kumaphatikizapo “mphamvu ya moyo wosawonongeka.” (Ahebri 7:16; yerekezerani ndi Chivumbulutso 20:6.) Komabe, kodi Mulungu akukwaniritsanji mwa kupereka mphatso yabwino kwambiri imeneyi? Kumbukirani kutsutsa kwa Satana kuti mwa zolengedwa zonse za Mulungu palibe chimodzi chimene chingakhale chokhulupirika. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Mwa kupatsa a 144,000 moyo wosakhoza kufa, Mulungu akusonyeza chidaliro chake chonse mwa gulu limeneli limene layankha chitsutso cha Satana m’njira yabwino koposa. Komano bwanji za anthu otsalawo? Yesu anauza mamembala oyambirira a “kagulu ka nkhosa” kameneka ka oloŵa Ufumu kuti ‘adzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.’ (Luka 12:32; 22:30) Zimenezi zikutanthauza kuti ena adzalandira moyo wosatha padziko lapansi monga nzika za Ufumu wake. Pamene kuli kwakuti “nkhosa zina” zimenezi sazipatsa moyo wosakhoza kufa, izo zikulandira “moyo wa nthaŵi zonse.” (Yohane 10:16; Mateyu 25:46) Choncho chiyembekezo cha Akristu onse ndicho moyo wosatha. Si maloto koma nchinthu chimene “Mulungu, wosanamayo,” analonjeza mwalumbiro ndipo chinalipiridwa ndi mwazi wamtengo wapatali wa Yesu.—Tito 1:2.
Kutsogolo Kwambiri?
9, 10. Kodi pali zizindikiro zotani zosonyeza kuti tili pafupi ndi mapeto?
9 Mtumwi Paulo ananeneratu kuti “nthaŵi zoŵaŵitsa” zidzasonyeza kuti ndithudi tafika mu “masiku otsiriza.” Pamene anthu otizinga awonongeka nakhala opanda chikondi, aumbombo, okonda kudzikhutiritsa iwo eni, ndi osaopa Mulungu, kodi sitikuona kuti tsiku la Yehova lopereka chiweruzo chake pa dongosolo loipa la dzikoli likuyandikira mwamsanga? Pamene chiwawa ndi udani zikuwonjezeka, kodi sitikuona potizinga ponse kukwaniritsidwa kwa mawu enanso a Paulo akuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire”? (2 Timoteo 3:1-5, 13) Ena mwachidaliro angamafuule kuti “Mtendere ndi mosatekeseka,” koma chiyembekezo chonse cha mtendere chidzazimiririka, chifukwa “chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” Sitinasiyidwe mumdima ponena za tanthauzo la nthaŵi zathu. Choncho, “tidikire, ndipo tisaledzere.”—1 Atesalonika 5:1-6.
10 Ndiponso, Baibulo limasonyeza kuti masiku otsiriza ndi “kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12; yerekezerani ndi 17:10.) Mbali yaikulu ya “kanthaŵi” kameneko yathadi kale. Ulosi wa Danieli, mwachitsanzo, umafotokoza molongosoka mkangano wa pakati pa “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera” umene wafika mpaka m’zaka za zana lino. (Danieli 11:5, 6) Chimene changotsala kukwaniritsidwa ndicho kuukira komaliza kwa “mfumu ya kumpoto,” kofotokozedwa pa Danieli 11:44, 45.—Onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1987, ndi November 1, 1993, pankhani yofotokoza ulosiwu.
11. (a) Kodi Mateyu 24:14 wakwaniritsidwa kufikira pati? (b) Kodi mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 10:23 akusonyezanji?
11 Palinso zimene Yesu ananeneratu kuti “uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Lerolino, Mboni za Yehova zikuchita ntchito yawo m’maiko, zisumbu, ndi magawo 233. Nzoona kuti pakali magawo amene sanakhudzidwebe, ndipo mwina panthaŵi yake ya Yehova, khomo lamwaŵi lidzatseguka. (1 Akorinto 16:9) Ngakhale zili choncho, mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 10:23 ngotonthoza: “Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.” Pamene kuli kwakuti uthenga wabwino udzalengezedwa padziko lonse lapansi, sitidzafika mwachindunji kumbali zonse za dziko lapansi ndi uthenga wa Ufumu Yesu ‘asanadze’ monga Wakupha.
12. (a) Kodi ndi ‘kusindikiza’ kotani kumene kukunenedwa pa Chivumbulutso 7:3? (b) Kodi kuchepa kwa chiŵerengero cha odzozedwa padziko lapansi kukutanthauzanji?
12 Talingalirani lemba la Chivumbulutso 7:1, 3, limene limanena kuti “mphepo zinayi” zachiwonongeko zagwidwa “kufikira tidasindikiza chizindikiro akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pawo.” Mawuwa sakunena za kusindikiza koyamba, kumene kumachitika a 144,000 atalandira maitanidwe akumwamba. (Aefeso 1:13) Akunena za kusindikiza komaliza, pamene mosasinthika adzadziŵika monga “akapolo a Mulungu wathu” oyesedwa ndi okhulupirika. Chiŵerengero cha ana a Mulungu odzozedwadi amene akali moyo padziko lapansi nchochepa kwambiri. Ndiponso, Baibulo limanena momveka bwino kuti mbali yoyambirira ya chisautso chachikulu ‘idzafupikitsidwa’ “chifukwa cha osankhidwawo.” (Mateyu 24:21, 22) Ochuluka odzinenera kuti ndi odzozedwa ngokalamba kwambiri. Kachiŵirinso, kodi zimenezi sizingasonyeze kuti mapeto ali pafupi kwenikweni?
Mlonda Wokhulupirika
13, 14. Kodi udindo wa gulu la mlonda nchiyani?
13 Pakali pano, tichita bwino kulabadira chitsogozo choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika.” (Mateyu 24:45) Kwa zaka zoposa zana limodzi, “kapolo” wamakono watumikira mokhulupirika monga “mlonda.” (Ezekieli 3:17-21) Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 1, 1984, inafotokoza kuti: “Mlonda ameneyu akupenyerera mmene zinthu zikuchitikira padziko lapansi mokwaniritsa ulosi wa Baibulo, akupereka chenjezo la ‘masauko aakulu [“chisautso chachikulu,” NW] monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko’ ndipo akubukitsa ‘uthenga wabwino wa zinthu zabwino.’”—Mateyu 24:21; Yesaya 52:7.
14 Kumbukirani: Ntchito ya mlonda ndiyo kufuula “chimene achiona.” (Yesaya 21:6-8) M’nthaŵi za Baibulo mlonda ankapereka chenjezo ngakhale pamene ngozi inali kutali kwambiri moti siikuoneka bwino. (2 Mafumu 9:17, 18) Ee, kalelo kunalinso machenjezo olakwika. Koma mlonda wabwino sanali kungokhala chete kuopa kuchita manyazi. Nyumba yanu itakhala pamoto, kodi mungamve bwanji ngati ozimitsa moto sanabwere chifukwa anaganiza kuti mwina simunawaitanire zenizeni? Ayi, timayembekezera amunawa kuchitapo kanthu mwamsanga ataona chizindikiro chilichonse changozi! Mofananamo, gulu la mlonda lalankhula pamene mikhalidwe yafuna kuti achite motero.
15, 16. (a) Kodi nchifukwa ninji pamakhala kusintha pakamvedwe kathu ka maulosi? (b) Kodi tingaphunzirenji pa atumiki okhulupirika a Mulungu amene anamva molakwa maulosi ena?
15 Komabe, pamene zinthu zikuchitika, tayamba kuwamvetsa maulosi. Mbiri yakale ikusonyeza kuti ndi mwa kamodzikamodzi, ngati zinachitikapo nkomwe, kuti maulosi a Mulungu amamvetsetsedwa bwino asanakwaniritsidwe. Mulungu anauza Abramu utali wake weniweni umene mbewu yake idzakhala “alendo m’dziko la eni,” umene unali zaka 400. (Genesis 15:13) Komabe, Mose anadzipereka monga mlanditsi nthaŵi yake isanakwane.—Machitidwe 7:23-30.
16 Lingaliraninso za maulosi onena za Mesiya. Tikakumbukira zakale tikuona kuti zinali zoonekeratu kuti imfa ndi kuukitsidwa kwa Mesiya zinali zonenedweratu. (Yesaya 53:8-10) Komatu ophunzira enieniwo a Yesu analephera kumvetsa choonadi chimenechi. (Mateyu 16:21-23) Iwo sanaone kuti Danieli 7:13, 14 adzakwaniritsidwa mkati mwa pa·rou·siʹa, kapena kuti “kukhalapo” kwa Kristu kwamtsogolo. (Mateyu 24:3, NW) Choncho kuŵerengera kwawo kunali kolakwika ndi zaka pafupifupi 2,000 pamene anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” (Machitidwe 1:6) Ngakhale mpingo wachikristu utakhazikitsidwa bwino, malingaliro olakwika ndi ziyembekezo zolakwika zinkakhalapobe. (2 Atesalonika 2:1, 2) Ngakhale kuti ena nthaŵi zina anali ndi malingaliro olakwika, mosakayikira Yehova anadalitsa ntchito ya okhulupirira a m’zaka za zana loyamba amenewo!
17. Kodi kusintha kamvedwe kathu ka Malemba ena tiyenera kukuona motani?
17 Gulu la mlonda lamakono nalonso nthaŵi ndi nthaŵi lafotokozanso mwatsopano malingaliro ake. Komabe, kodi aliyense akhoza kukayikira kuti Yehova wadalitsa “kapolo wokhulupirika” ameneyo? Ndiponso, titaiyang’ana yonse nkhani yake, kodi kusintha kochuluka kumene kwakhalapo sikwakung’ono? Kamvedwe kathu ka Baibulo lonse sikanasinthe. Chitsimikizo chathu chakuti tikukhala m’masiku otsiriza ncholimba kuposa ndi kale lomwe!
Kukhalira Moyo Mtsogolo Mosatha
18. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kungokhalira moyo zalero?
18 Dziko linganene kuti “Tidye timwe, pakuti maŵa timwalira,” koma ifeyo sitiyenera kukhala ndi mzimu umenewo. Nkulimbikiriranji kupeza zosangalatsa zimene tingapeze m’moyo tsopano pamene mukhoza kulimbikira kuti mukakhale ndi mtsogolo mosatha? Chiyembekezo chimenecho, kaya chikhale cha moyo wosakhoza kufa kumwamba kapena cha moyo wosatha padziko lapansi, si maloto, sizongoyerekezera ayi. Ndi chinthu chenicheni cholonjezedwa ndi “Mulungu, wosanamayo.” (Tito 1:2) Pali umboni wochuluka wakuti chiyembekezo chathu chili pafupi kwambiri kukwaniritsidwa! “Yafupika nthaŵi.”—1 Akorinto 7:29.
19, 20. (a) Kodi Yehova amakuona motani kudzimana kumene tapanga kaamba ka Ufumu? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala moyo moyembekezera nthaŵi zosatha?
19 Nzoona kuti dongosololi lakhala kale kwautali umene ambiri sanaganizire. Angapo tsopano angamaganize kuti akanadziŵa zimenezi poyamba, sakanadzimana mmene anachitiramu. Koma munthu sayenera kuchita chisoni kuti anachita zimenezo. Ndipotu kudzimana ndiko mbali ina yaikulu ya kukhala Mkristu. Akristu ‘amadzikana okha.’ (Mateyu 16:24) Sitiyenera konse kuona monga kuyesayesa kwathu kutumikira Mulungu kwapita pachabe. Yesu analonjeza kuti: “Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, . . . ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.” (Marko 10:29, 30) Zaka chikwi kuyambira pano, kodi ntchito yanu, nyumba, kapena chuma zidzakhala ndi tanthauzo lotani? Komatu, kudzimana kwanu chifukwa cha Yehova kudzakhala kwa tanthauzo zaka miliyoni imodzi kuyambira tsopano—zaka mamiliyoni chikwi kuyambira tsopano! “Pakuti Mulungu saali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu.”—Ahebri 6:10.
20 Chotero, tiyeni tizikhala tikumalingalira za nthaŵi yosatha, kusumika maso athu ‘osati pa zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthaŵi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.’ (2 Akorinto 4:18) Mneneri Habakuku analemba kuti: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3) Kodi ‘kulindirira’ mapeto kumakhudza motani mmene timasamalirira maudindo athu aumwini ndi a pabanja? Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza zimenezi.
Mfundo Zobwereza
◻ Kodi angapo lerolino akhudzidwa motani ndi kumene kwaoneka ngati kuchedwa kwa mapeto a dongosololi la zinthu?
◻ Kodi maziko a chiyembekezo chathu cha moyo wosatha nchiyani?
◻ Kodi kudzimana kumene tapanga kaamba ka zinthu za Ufumu tiyenera kukuona motani?
[Chithunzi patsamba 15]
Ntchito yolalikira ya padziko lonse iyenera kumalizidwa mapeto asanafike