“Akufa Adzaukitsidwa”
“Pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.”—1 AKORINTO 15:52.
1, 2. (a) Kodi ndi lonjezo lotonthoza lotani limene linaperekedwa kudzera mwa mneneri Hoseya? (b) Kodi tikudziŵa motani kuti Mulungu ngwofunitsitsa kuukitsa akufa?
KODI munafedwapo wokondedwa wanu? Ndiye kuti mukudziŵa mmene imfa ya wina imapwetekera. Ngakhale zili motero, Akristu amapeza chitonthozo palonjezo limene Mulungu anapereka kudzera mwa mneneri Hoseya lakuti: “Ndidzawaombola ku mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Manda, chiwonongeko chako chili kuti?”—Hoseya 13:14.
2 Lingaliro lakuti akufa adzakhalanso ndi moyo limaoneka ngati lopanda nzeru kwa amene amalikayikira. Koma Mulungu Wamphamvuyonse alidi ndi mphamvu yochita chozizwitsa chimenechi! Funso lalikulu nlakuti, kodi Yehova ngwofunitsitsa kuukitsa anthu akufa? Yobu, munthu wolungamayo, anafunsa kuti: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” Kenako anapereka yankho lotonthozali kuti: “Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Mawu akuti ‘kukhumba’ akusonyeza kulakalaka kapena kufunitsitsa. (Yerekezerani ndi Salmo 84:2.) Inde, Yehova akulakalaka chiukiriro—akufunitsitsa kuonanso anthu okhulupirika amene anamwalira, amene ali amoyo m’chikumbukiro chake.—Mateyu 22:31, 32.
Yesu Afotokoza za Chiukiriro
3, 4. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene Yesu anafotokoza ponena za chiukiriro? (b) Kodi nchifukwa chiyani Yesu anaukitsidwa monga mzimu, osati monga munthu wathupi lanyama?
3 Amuna akale okhulupirika monga Yobu sanali kudziŵa zambiri ponena za chiukiriro. Yesu Kristu ndiye amene anafotokoza zonse zokhudzana ndi chiyembekezo chosangalatsa chimenechi. Anasonyeza ntchito yaikulu imene iye ali nayo pamene anati: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:36) Kodi nkuti komwe adzakhala ndi moyo umenewo? Kwa ambiri amene akukhulupirira, padzakhala pano padziko lapansi. (Salmo 37:11) Komabe, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.” (Luka 12:32) Ufumu wa Mulungu ngwakumwamba. Choncho, lonjezo limeneli likutanthauza kuti “kagulu kankhosa” kadzayenera kukhala ndi Yesu kumwamba monga zolengedwa zauzimu. (Yohane 14:2, 3; 1 Petro 1:3, 4) Chimenechotu nchiyembekezo chaulemerero! Yesu anauzanso mtumwi Yohane kuti “kagulu kankhosa” kadzakhala anthu 144,000 okha basi.—Chivumbulutso 14:1.
4 Komano kodi a 144,000 adzaloŵamo bwanji mu ulemerero wakumwamba? Yesu ‘anaonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino.’ Mwa mwazi wake, iye anakonza “njira yatsopano ndi yamoyo” yoloŵera kumwamba. (2 Timoteo 1:10; Ahebri 10:19, 20) Choyamba, anamwalira, monga momwe Baibulo linaneneratu. (Yesaya 53:12) Kenako, monga momwe mtumwi Petro anadzalengezera pambuyo pake, “Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa.” (Machitidwe 2:32) Koma Yesu sanaukitsidwe monga munthu. Iye anati: “Mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.” (Yohane 6:51) Kutenganso thupi lake kukanapangitsa kuti nsembe imeneyo ikhale yopanda ntchito. Choncho Yesu ‘anaphedwatu m’thupi, koma anapatsidwa moyo mumzimu.’ (1 Petro 3:18) Chotero Yesu ‘analandirapo chiombolo chosatha kaamba ka ife,’ kutanthauza a “kagulu kankhosa.” (Ahebri 9:12, NW) Iye anapereka kwa Mulungu mtengo wa moyo wake waumunthu wangwiro monga dipo la mtundu wa anthu auchimo, ndipo a 144,000 anali oyamba kupindula ndi dipo limenelo.
5. Kodi nchiyembekezo chotani chimene chinaperekedwa kwa otsatira a Yesu a m’zaka za zana loyamba?
5 Si Yesu yekha amene anaukitsidwira kumoyo wakumwamba. Paulo anauza Akristu anzake ku Roma kuti anadzozedwa ndi mzimu woyera kuti akhale ana a Mulungu ndiponso oloŵa nyumba anzake a Kristu atasonyeza umboni wa kudzozedwa kwawo mwa kupirira kufikira mapeto. (Aroma 8:16, 17) Paulo anafotokozanso kuti: “Ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi iye m’chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake.”—Aroma 6:5.
Kuchirikiza Chiyembekezo cha Chiukiriro
6. Kodi nchifukwa ninji kukhulupirira chiukiriro kunatsutsidwa ku Korinto, ndipo mtumwi Paulo anatani?
6 Chiukiriro chili mbali ya “chiphunzitso choyambirira” cha Chikristu. (Ahebri 6:1, 2, NW) Komabe, chiphunzitso chimenechi chinatsutsidwa ku Korinto. Ena mumpingowo, mwachionekere atasonkhezeredwa ndi filosofi yachigiriki, anali kunena kuti: “Kulibe kuuka kwa akufa.” (1 Akorinto 15:12) Mtumwi Paulo atamva za zimenezi anachirikiza chiyembekezo cha chiukiriro, makamaka chiyembekezo cha Akristu odzozedwa. Tiyeni tisanthule mawu a Paulo olembedwa pa 1 Akorinto chaputala 15. Zidzakhala zothandiza ngati mwaŵerenga kale chaputala chonsechi, monga tinanenera m’nkhani yapita.
7. (a) Kodi ndi nkhani yaikulu iti imene Paulo anasumikapo maganizo? (b) Kodi ndani amene anaona Yesu ataukitsidwa?
7 M’mavesi aŵiri oyambirira a 1 Akorinto chaputala 15, Paulo akutchula cholinga cha nkhani yake kuti: “Ndikudziŵitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo, umenenso mupulumutsidwa nawo . . . ngati simunakhulupira chabe.” Ngati Akorinto analephera kuchirimika pauthenga wabwino, ndiye kuti kulandira kwawo choonadi kunali kwachabe. Paulo anapitiriza kuti: “Ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo; ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi aŵiriwo; pomwepo anaoneka panthaŵi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona; pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse; ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.”—1 Akorinto 15:3-8.
8, 9. (a) Kodi kukhulupirira za chiukiriro nkofunika motani? (b) Kodi payenera kuti panali pachochitika chotani pamene Yesu anaonekera kwa “abale oposa mazana asanu”?
8 Kwa awo amene analandira uthenga wabwino, kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa sikunali kopanda umboni. Panali mboni zambiri zoona ndi maso zomwe zinagogomezera kuti “Kristu anafera zoipa zathu” ndi kuti anaukitsidwa. Mmodzi wa mbonizo anali Kefa, kapena kuti Petro, monga momwe ambiri amamdziŵira. Pambuyo pokana Yesu usiku umene anaperekedwa ndi kugwidwa, Petro ayenera kuti anatonthozedwa kwambiri pamene Yesu anaonekera kwa iye. Nawonso “khumi ndi aŵiriwo,” gulu la atumwi, anachezeredwa ndi Yesu woukitsidwayo—chochitika chimene chinawathandizadi kuthetsa mantha awo ndi kuchitira umboni molimba mtima za kuukitsidwa kwa Yesu.—Yohane 20:19-23; Machitidwe 2:32.
9 Kristu anaonekeranso kwa gulu lina lalikulu, “abale oposa mazana asanu.” Popeza kuti ndi ku Galileya kokha kumene anali ndi otsatira ambiri motero, mwina pamenepa panali pachochitika chofotokozedwa pa Mateyu 28:16-20, pamene Yesu anapereka lamulo lopanga ophunzira. Ndiyetu anthu ameneŵa anapereka umboni wamphamvu! Ena anali adakali moyo mu 55 C.E. pamene Paulo analemba kalata yake yoyamba imeneyi kwa Akorinto. Komano, taonani kuti amene anali atamwalira anati iwo “agona.” Anali asanaukitsidwebe kuti alandire mphotho yawo yakumwamba.
10. (a) Kodi msonkhano womaliza wa Yesu ndi ophunzira ake unawasonkhezera motani? (b) Kodi Yesu anaonekera motani kwa Paulo “monga mtayo”?
10 Mboni ina yodziŵika kwambiri ya kuukitsidwa kwa Yesu anali Yakobo, mwana wa Yosefe ndi amayi wa Yesu, Mariya. Yesu asanaukitsidwe, Yakobo mwachionekere sanali wokhulupirira. (Yohane 7:5) Koma Yesu ataonekera kwa iye, Yakobo anakhala wokhulupirira ndiponso mwina anathandizira kuti abale ake enawo atembenuke. (Machitidwe 1:13, 14) Pamsonkhano wake womaliza ndi ophunzira ake, nthaŵi imene anakwera kumwamba, Yesu anawalamula ‘kukhala mboni . . . kufikira malekezero ake a dziko.’ (Machitidwe 1:6-11) Pambuyo pake, anaonekera kwa Saulo wa ku Tariso, wozunza Akristu. (Machitidwe 22:6-8) Yesu anaonekera kwa Saulo “monga mtayo.” Zinali monga kuti Saulo waukitsidwira kale kumoyo wauzimu ndipo akuona Ambuye waulemerero zaka mazana ambiri kuukitsidwa kumeneku kusanachitike. Chokumana nacho chimenechi chinachititsa Saulo kupotoloka mwadzidzidzi pacholinga chake cha kutsutsa ndi kupha a mumpingo wachikristu ndipo chinamsinthiratu. (Machitidwe 9:3-9, 17-19) Saulo anakhala mtumwi Paulo, mmodzi mwa ochirikiza chikhulupiriro chachikristu achangu koposa.—1 Akorinto 15:9, 10.
Kukhulupirira Chiukiriro Nkofunika
11. Kodi Paulo anavumbula motani chinyengo cha mawu akuti, “Kulibe kuuka kwa akufa”?
11 Chotero, kuukitsidwa kwa Yesu kunali choonadi chachidziŵikire. “Koma ngati Kristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa,” akutero Paulo, “nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa?” (1 Akorinto 15:12) Anthu amenewa sanali kungokayikira kapena kukhala ndi mafunso onena za chiukiriro paokha komanso anali kulengeza poyera kuti sakuchikhulupirira. Choncho Paulo akuvumbula chinyengo cha maganizo awo. Iye akunena kuti ngati Kristu sanaukitsidwe, uthenga wachikristu unali wabodza, ndipo onena kuti Kristu anaukitsidwa anali “mboni zonama za Mulungu.” Ngati Kristu sanaukitsidwe, dipo silinalipiridwe kwa Mulungu; Akristu anali ‘chikhalire m’machimo awo.’ (1 Akorinto 15:13-19; Aroma 3:23, 24; Ahebri 9:11-14) Ndipo Akristu amene ‘anagona,’ ena monga ofera chikhulupiriro, anafa popanda chiyembekezo chenicheni. Ungakhale mkhalidwe wochititsa chisoni chotani nanga kwa Akristu moyo uno utakhala wokhawo umene adzakhala nawo! Kuvutika kwawo kungakhale kwachabe.
12. (a) Kodi kutcha Kristu kuti “chipatso choundukula cha iwo akugona” kukusonyezanji? (b) Kodi Kristu anachititsa motani kuti chiukiriro chikhale chotheka?
12 Koma si mmene zinalili. Paulo akupitiriza kuti: “Kristu waukitsidwa kwa akufa.” Ndiponso, iye ali “chipatso choundukula cha iwo akugona.” (1 Akorinto 15:20) Pamene Aisrayeli momvera anapatsa Yehova zipatso zoundukula za zolima zawo, Yehova anawadalitsa ndi zotuta zochuluka. (Eksodo 22:29, 30; 23:19; Miyambo 3:9, 10) Mwa kutcha Kristu kuti “chipatso choundukula,” Paulo akusonyeza kuti padzakhalabe kututa kwa anthu ena amene adzaukitsidwira kumoyo wakumwamba. “Monga imfa inadza mwa munthu,” akutero Paulo, “kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu. Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.” (1 Akorinto 15:21, 22) Yesu anachititsa kuti chiukiriro chikhale chotheka mwa kupereka moyo wake wangwiro waumunthu monga dipo, kutsegula mwayi wakuti anthu amasulidwe kuukapolo wa uchimo ndi imfa.—Agalatiya 1:4; 1 Petro 1:18, 19.a
13. (a) Kodi kuukitsidwira kumwamba kumachitika liti? (b) Kodi zili motani kuti odzozedwa ena ‘sagona’?
13 Paulo akupitiriza kuti: “Koma yense m’dongosolo lake la iye yekha, chipatso choundukula Kristu; pomwepo iwo a Kristu, pa kubwera [“kukhalapo,” NW] kwake.” (1 Akorinto 15:23) Yesu anaukitsidwa mu 33 C.E. Komabe, otsatira ake odzozedwa—“iwo a Kristu”—anayenera kuyembekeza kufikira Yesu atangoyamba kukhalapo kwake monga Mfumu, zimene ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti zinachitika mu 1914. (1 Atesalonika 4:14-16; Chivumbulutso 11:18) Nanga za awo amene adzakhala ali moyo pakukhalapo kumeneko? Paulo akuti: “Taonani ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kutwanima kwa diso, palipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.” (1 Akorinto 15:51, 52) Zoonadi, si odzozedwa onse amene agona m’manda kuyembekezera chiukiriro. Awo amene amwalira m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu amasandulika nthaŵi yomweyo.—Chivumbulutso 14:13.
14. Kodi ndi motani mmene ‘odzozedwa abatizidwira kuti akhale akufa’?
14 “Ngati si choncho,” akufunsa motero Paulo, “adzachita chiyani iwo amene abatizidwa kuti akhale akufa? Ngati akufa sadzaukitsidwa konse, nchifukwa ninji iwo akubatizidwa kuti akhale otero? Nanga ifenso tikhaliranji pangozi ola lililonse?” (1 Akorinto 15:29, 30, NW) Paulo sanali kunena kuti anthu amoyo anali kubatizidwa chifukwa cha akufa, monga momwe mabaibulo ena amasonyezera. Wobatizidwa amakhalatu wophunzira wachikristu, koma anthu akufa sangakhale ophunzira. (Yohane 4:1) M’malo mwake, Paulo anali kunena za Akristu amoyo, ambiri amene anali “pangozi ola lililonse,” monga Paulo iye mwini. Akristu odzozedwa ‘anabatizidwa mu imfa ya Kristu.’ (Aroma 6:3) Kuyambira pa kudzozedwa kwawo, iwo anali “kubatizidwa,” titero kunena kwake, m’njira imene inali kudzawatsogolera ku imfa yonga ya Kristu. (Marko 10:35-40) Iwo anali kudzafa ali ndi chiyembekezo cha kuukitsidwira kumwamba muulemerero.—1 Akorinto 6:14; Afilipi 3:10, 11.
15. Kodi Paulo ayenera kuti anakumana ndi ngozi zotani, ndipo kukhulupirira chiukiriro kunamthandiza motani kupirira?
15 Paulo tsopano akufotokoza kuti iye mwini anakumana ndi ngozi zambiri moti anati: “Ndifa tsiku ndi tsiku.” Podziŵa kuti ena anganene kuti akukokomeza, Paulo akuwonjezera kuti: “Ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwa Kristu Yesu, Ambuye wathu.” The Jerusalem Bible limati pavesili: “Ndiyang’anizana ndi imfa tsiku lililonse, abale, ndipo ndilumbira ponena za izi mwa kunyada kumene ndinyadira inu mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Monga chitsanzo cha ngozi zimene anakumana nazo, pa vesi 32, Paulo akunena za ‘kulimbana ndi zilombo ku Efeso.’ Nthaŵi zambiri Aroma anali kupha apandu mwa kuwaponya ku zilombo m’mabwalo amaseŵero. Ngati Paulo anapulumuka pomenyana ndi zilombo, anangopulumuka chifukwa cha thandizo la Yehova. Popanda chiyembekezo cha chiukiriro, kusankha njira ya moyo yomloŵetsa m’ngozi ngati zimenezi kukanakhala kupanda nzeru kwenikweni. Kupirira mavuto ndi kudzimana chifukwa cha kutumikira Mulungu kukanakhala kopanda pake ngati iye analibe chiyembekezo cha moyo wamtsogolo. “Ngati akufa saukitsidwa,” Paulo akutero, “tidye timwe pakuti maŵa timwalira.”—1 Akorinto 15:31, 32; onani 2 Akorinto 1:8, 9; 11:23-27.
16. (a) Kodi mawu akuti “tidye timwe pakuti maŵa timwalira” ayenera kuti anachokera kuti? (b) Kodi ngozi ya kukhulupirira malingalirowa inali yotani?
16 Paulo ayenera kuti anagwira mawu Yesaya 22:13, amene amafotokoza mzimu wa anthu osamva a mu Yerusalemu ongodziŵa za imfa. Kapena mwina anali kuganizira za zikhulupiriro za Aepikureya, amene anali kunyansidwa ndi zonena kuti pali chiyembekezo cha moyo pambuyo pa imfa namakhulupirira kuti kusangalatsa thupi ndiko chinthu chabwino koposa pamoyo. Mulimonse mmene zinalili, malingaliro akuti “tidye timwe” sanali aumulungu. Choncho, Paulo akuchenjeza kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Kuyanjana ndi awo amene anali kukana za chiukiriro kunali kwangozi. Mayanjano oterowo ndiwo anachititsa ena mwa mavuto amene Paulo anayenera kuthetsa mumpingo wa Akorinto, monga chisembwere, magaŵano, kutengerana kumabwalo amilandu, ndi kusalemekeza Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.—1 Akorinto 1:11; 5:1; 6:1; 11:20-22.
17. (a) Kodi nchilimbikitso chotani chimene Paulo anapatsa Akorinto? (b) Kodi pali mafunso otani oyenera kuyankhidwa?
17 Ndiye chifukwa chake Paulo akulimbikitsa Akorinto kuti: “Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziŵitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.” (1 Akorinto 15:34) Kusakhulupirira za chiukiriro kunachititsa ena kuodzera mwauzimu, monga oledzera. Anafunikira kuuka, kusakhala oledzera. Akristu odzozedwa lerolino afunikiranso kukhala ogalamuka mwauzimu, kusakhudzidwa ndi zikayiko za dzikoli. Iwo ayenera kugwiritsitsa chiyembekezo chawo cha kuukitsidwira kumwamba. Koma mafunso ena anatsalabe—kwa Akorinto panthaŵiyo ndi kwa ifeyo lerolino. Mwachitsanzo, kodi a 144,000 adzaukitsidwira kumwamba ndi thupi lotani? Nanga bwanji ponena za enanso mamiliyoni amene adakali m’manda amene alibe chiyembekezo cha kumwamba? Kodi iwo adzaukitsidwa motani? M’nkhani yathu yotsatira, tidzapenda nkhani yonse yotsala ya Paulo yonena za chiukiriro.
[Mawu a M’munsi]
a Onani kope la February 15, 1991 la Nsanja ya Olonda ngati mukufuna nkhani yonena za dipo.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Yesu anafotokozanji ponena za chiukiriro?
◻ Kodi zina mwa mboni zimene zinaona Kristu ataukitsidwa zinali ziti?
◻ Kodi nchifukwa ninji chiphunzitso cha chiukiriro chinatsutsidwa, ndipo Paulo anachitanji?
◻ Kodi nchifukwa ninji kukhulupirira chiukiriro kunali kofunika kwa Akristu odzozedwa?
[Chithunzi patsamba 15]
Mwana wamkazi wa Yairo anakhala umboni wakuti chiukiriro nchotheka
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Popanda chiyembekezo cha chiukiriro, kufera chikhulupiriro kwa Akristu okhulupirika kukanakhala kwachabe