‘Imfa Idzathetsedwa’
“Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” —1 AKORINTO 15:26.
1, 2. (a) Kodi mtumwi Paulo anali ndi chiyembekezo chotani cha akufa? (b) Kodi Paulo anali kuyankha funso lotani la chiukiriro?
“NDIMAKHULUPIRIRA kuti . . . thupi lidzaukitsidwa, ndiponso kuti kuli moyo wosatha.” Chimatero chikalata cha zikhulupiriro chotchedwa Apostles’ Creed. Akatolika ndi Aprotestanti omwe mwalamulo amanena pamtima mawuwa, mosadziŵa kuti zikhulupiriro zawo zimafanana kwambiri ndi nzeru zachigiriki osati zimene atumwi anali kukhulupirira. Komabe, mtumwi Paulo anatsutsa nzeru zachigiriki ndipo sanakhulupirire kuti mzimu sumafa. Ngakhale ndi choncho, anali kukhulupirira zolimba kuti moyo udzakhalako mtsogolo ndipo mouziridwa analemba kuti: “Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:26) Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa anthu amene amafa?
2 Tiyeni tibwerere ku nkhani ya Paulo yonena za chiukiriro yomwe ili pa 1 Akorinto chaputala 15 kuti tiyankhe funsoli. Kumbukirani kuti m’mavesi oyambirira Paulo anasonyeza kuti chiukiriro ndi mbali yofunika kwambiri pa chiphunzitso chachikristu. Tsopano mwachindunji akuyankha funso lakuti: “Koma wina adzati, akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?”—1 Akorinto 15:35.
Ndi Thupi Lotani?
3. Kodi nchifukwa chiyani ena anali kutsutsa chiukiriro?
3 Podzutsa funso limeneli, Paulo angakhale kuti anali kufuna kutsutsa chisonkhezero cha malingaliro a Plato. Plato anali kuphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu umene sumafa thupi likafa. Kwa amene anakula ndi malingaliro ameneŵa, chiphunzitso chachikristu mwachionekere chinali chosafunikira. Ngati mzimu sufa, kodi palinso kufunika kwa kuukitsidwa? Ndiponso, chiukiriro chinaoneka ngati nchosamveka. Thupi likangosanduka fumbi, lingaukenso bwanji? Heinrich Meyer, wothirira ndemanga pa Baibulo, anati anthu ena a ku Korinto anali otsutsa mwinamwake chifukwa cha “filosofi yakuti nkosatheka kubwezeretsanso zinthu zimene zimapanga thupi.”
4, 5. (a) Nchifukwa ninji kutsutsa kwa anthu osakhulupirira kunali kosayenera? (b) Fotokozani fanizo la Paulo la “mbewu yokha.” (c) Kodi ndi matupi otani amene Mulungu amapatsa odzozedwa oukitsidwa?
4 Paulo akusonyeza kuti kulingalira kwawo nkopanda pake mwakuti: “Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa; ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbewu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina; koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbewu yonse thupi lake lake.” (1 Akorinto 15:36-38) Mulungu sadzaukitsa matupi amene anthu anali nawo pamene anali padziko lapansi. M’malo mwake, matupi adzasithidwa.
5 Paulo akuyerekezera chiukiriro ndi kumera kwa mbewu. Kambewu ka tirigu sikafanana nkomwe ndi mtengo wake umene umamera kuchokera ku kambewuko. The World Book Encyclopedia inati: “Mbewu ikayamba kumera imamwa madzi ochuluka. Madziwo amapangitsa kuti chakudya chimene chili mkati mwa mbewuyo chisinthidwesinthidwe. Amapangitsanso kuti minyeŵa ya mkati ifufume ndi kutulukira kuja kwa khungu la mbewuyo.” Mbewuyo imafadi osakhalanso mbewu ndi kutulukapo mtengo. ‘Mulungu amaipatsa thupi’ mlingaliro lakuti iye ndiye anayambitsa malamulo akakulidwe amene amalamulira kakulidwe kake, ndipo mbewu iliyonse imalandira thupi mogwirizana ndi mtundu wake. (Genesis 1:11) Mofananamo, Akristu odzozedwa choyamba amafa ngati anthu. Ndiyeno, panthaŵi yoikika ya Mulungu, amawapatsanso moyo m’matupi enaena atsopano. Zili ngati mmene Paulo anauzira Afilipi kuti, “Yesu Kristu; . . . adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero.” (Afilipi 3:20, 21; 2 Akorinto 5:1, 2) Iwo amaukitsidwa ndi matupi auzimu ndi kukakhala kudziko la mizimu.—1 Yohane 3:2.
6. Nchifukwa ninji kuli koyenera kukhulupirira kuti Mulungu angapatse oukitsidwa matupi auzimu oyenerera?
6 Kodi nzovuta kuzikhulupirira? Iyayi. Paulo akuti nyama zimakhala ndi matupi osiyanasiyana. Ndiponso, akusiyanitsa angelo akumwamba ndi anthu athupi ndi mwazi, mwakuti: “Palinso matupi a m’mwamba, ndi matupi apadziko.” Palinso kusiyana kwakukulu pakati pa zinthu zopanda moyo. Kalekale asayansi asanatulukire zinthu zakumwamba zonga ngati nyenyezi zotchedwa blue stars, red giants, ndi white dwarfs, Paulo anati, “nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m’ulemerero.” Polingalira zimenezi, kodi sikomveka kuti Mulungu angapereke matupi auzimu oyenerera kwa odzozedwa oukitsidwawo?—1 Akorinto 15:39-41.
7. Kodi tanthauzo la chosavunda nchiyani? nanga chosafa?
7 Kenako Paulo anati: “Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m’chivundi, liukitsidwa m’chisavundi.” (1 Akorinto 15:42) Thupi lamunthu ngakhale likhale langwiro, nlovunda. Lingathe kuphedwa. Mwachitsanzo, Paulo anati Yesu woukitsidwayo ‘sadzabwereranso kuchivundi.’ (Machitidwe 13:34) Sadzakhalanso ndi moyo m’thupi laumunthu lovunda, ngakhale litakhala langwiro. Matupi amene Mulungu amapereka kwa odzozedwa oukitsidwa ali osavunda—osakhoza kufa kapena kuwola. Paulo anapitiriza kuti: “Lifesedwa m’mnyozo, liukitsidwa m’ulemerero; lifesedwa m’chifoko, liukitsidwa mumphamvu; lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu.” (1 Akorinto 15:43, 44) Paulo akutinso: ‘Chaimfa ichi chiyenera kuvala chosafa.’ Chosafa chimatanthauza moyo wopanda mapeto, wosaonongeka. (1 Akorinto 15:53; Ahebri 7:16) Mwa njirayi, oukitsidwawo ‘amavala fanizo la wakumwambayo,’ Yesu, amene anatheketsa chiukiriro chawo.—1 Akorinto 15:45-49.
8. (a) Kodi tikudziŵa bwanji kuti oukitsidwa ndi anthu omwewo anali ndi moyo padziko lapansi? (b) Kodi ndi maulosi ati amene akukwaniritsidwa pamene anthu akuukitsidwa?
8 Ngakhale kuti ali kusinthika moteremu, oukitsidwawo ndi anthu amodzimodziwo amene anafa. Adzaukitsidwa ndi malingaliro ndi mikhalidwe yachikristu yapamwamba yofanana ndi imene anali nayo. (Malaki 3:3; Chivumbulutso 21:10, 18) Mwa njirayi amafanana ndi Yesu Kristu. Iye anasintha thupi lauzimu ndi kukhala nlaumunthu. Kenako anafa ndi kuukitsidwa ngati mzimu. Komatu, “Yesu Kristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthaŵi zonse.” (Ahebri 13:8) Odzozedwa ali ndi mwayi wolemekezeka chotani nanga! Paulo anati: “Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mawu olembedwa, Imfayo yamezedwa m’chigonjetso. Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?”—1 Akorinto 15:54, 55; Yesaya 25:8; Hoseya 13:14.
Chiukiriro cha Padziko Lapansi?
9, 10. (a) Malinga ndi 1 Akorinto 15:24, kodi “chimaliziro” nchiyani, ndipo nzochitika zotani zimene zikuchitika pamodzi nacho? (b) Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitika kuti imfa ithetsedwe?
9 Kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa mamiliyoni a anthu amene alibe chiyembekezo chokakhala ndi moyo wauzimu wosafa kumwamba? Chilipodi! Atalongosola kuti chiukiriro chakumwamba chikuchitika m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu, Paulo analongosola zochitika zotsatira kuti: “Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.”—1 Akorinto 15:23, 24.
10 “Chimaliziro” ndicho chimaliziro cha Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi, pamene Yesu modzichepetsa ndi mokhulupirika akukapereka Ufumu kwa Mulungu ndi Atate wake. (Chivumbulutso 20:4) Chifuno cha Mulungu cha ‘kusonkhanitsa pamodzi zonse mwa Kristu’ chidzakhala chitakwaniritsidwa. (Aefeso 1:9, 10) Komabe, choyamba Kristu adzaphwanya “chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe” zotsutsana ndi chifuno cha Uchifumu wa Mulungu. Zimenezi zimaposa chiwonongeko cha pa Armagedo. (Chivumbulutso 16:16; 19:11-21) Paulo anati: “[Kristu] ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:25, 26) Inde, zotsalira zonse za uchimo wa Adamu ndi imfa zidzakhala zitachotsedwa. Choncho chimene chidzakhala chofunika nchakuti Mulungu adzasiya “manda” ali opanda kanthu mwa kuukitsamo akufawo.—Yohane 5:28.
11. (a) Kodi timadziŵa motani kuti Mulungu angalengenso anthu amene anafa? (b) Kodi anthu oukitsidwira padziko lapansi adzapatsidwa matupi otani?
11 Zimenezi zikutanthauza kuti anthu adzalengedwanso. Kodi nzosatheka? Iyayi, chifukwa Salmo 104:29, 30 amatitsimikizira kuti Mulungu angathe kutero: “Mukalanda mpweya wawo, zikufa, nizibwerera kufumbi kwawo. Potumizira mzimu wanu, zilengedwa.” Pamene kuli kwakuti anthu oukitsidwa adzakhala anthu omwewo amene anafa, iwo sadzafunikira kukhala ndi matupi amodzimodziwo. Mulungu adzawapatsa thupi monga momwe iye afunira, mofanana ndi aja oukitsidwira kumwamba. Mosakayikira matupi awo adzakhala athanzi ndi ofananako ndi matupi awo oyamba kotero kuti akathe kuzindikiridwa ndi okondedwa awo.
12. Ndi liti pamene chiukiriro cha padziko lapansi chidzachitika?
12 Kodi chiukiriro cha padziko lapansi chidzachitika liti? Ponena za mlongo wake wakufa Lazaro, Marita anati: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:24) Kodi anadziŵa bwanji? Nkhani ya chiukiriro inali kuutsa mkangano m’tsiku lake popeza kuti Afarisi anali kukhulupirira za chiukiriro pamene Asaduki sankakhulupirira. (Machitidwe 23:8) Ndipo Marita ayenera kuti anadziŵapo za mboni zina za nthaŵi yachikristu isanafike zimene zinakhulupirira chiukiriro. (Ahebri 11:35) Mwina anathanso kuzindikira kuchokera pa Danieli 12:13 kuti chiukiriro chidzachitika m’tsiku lomaliza. Mwinanso anali ataphunzitsidwa zimenezi ndi Yesu mwiniyo. (Yohane 6:39) “Tsiku lomaliza” limenelo likufikira pamodzi ndi Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi. (Chivumbulutso 20:6) Talingalirani za chisangalalo ‘m’tsikulo’ pamene chochitika chachikuluchi chikuyamba!—Yerekezerani ndi Luka 24:41.
Ndani Adzaukitsidwa?
13. Ndi masomphenya otani a chiukiriro amene analembedwa pa Chivumbulutso 20:12-14?
13 Masomphenya a Yohane a chiukiriro cha padziko lapansi analembedwa pa Chivumbulutso 20:12-14 kuti: “Ndinaona akufa, aakulu ndi aang’ono alinkuima ku mpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabuku, monga mwa ntchito zawo. Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m’menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiŵiri, ndiyo nyanja yamoto.”
14. Kodi ndani ena amene adzaukitsidwa?
14 Chiukiriro chidzaphatikiza “aakulu ndi aang’ono,” anthu otchuka ndi osatchuka omwe amene analipo ndi moyo ndiyeno nkufa. Inde, ngakhale makanda adzaphatikizidwa! (Yeremiya 31:15, 16) Pa Machitidwe 24:15, mbali inanso yofunika ikuvumbulidwa: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Osaphonyeka pakati pa “olungama” ndi amuna ndi akazi akale okhulupirika monga ngati Abele, Enoke, Nowa, Abrahamu, Sara, ndi Rahabi. (Ahebri 11:1-40) Talingalirani kuti muli kucheza nawo ndipo akukulongosolerani zochitika za m’Baibulo zakalekale zoti iwo adaziona! “Olungama” adzaphatikizaponso anthu oopa Mulungu zikwizikwi amene afa posachedwapa amene analibe chiyembekezo chakumwamba. Kodi pali wina m’banja lanu kapena wokondedwa wanu amene angakhale pakati pa ameneŵa? Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti mungadzawaonenso! Komabe, “osalungama” amene adzaukitsidwanso ndi ndani? Akuphatikizapo anthu mamiliyoni, mwinanso mamiliyoni zikwizikwi, amene anafa alibe mwayi wophunzira ndi kugwiritsira ntchito choonadi cha Baibulo.
15. Kodi zikutanthauzanji kuti oukitsidwawo ‘adzaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabuku’?
15 Kodi ndi motani mmene anthu oukitsidwawo ‘adzaweruzidwira mwa zolembedwa m’mabuku, monga mwa ntchito zawo’? Mabuku ameneŵa si kaundula wa zochita zawo zakale; pamene anafa, iwo anamasulidwa kumachimo amene anachita ali ndi moyo. (Aroma 6:7, 23) Komabe, anthu oukitsidwawo adzakhalabe ndi uchimo wa Adamu. Ndiye kuti mabuku ameneŵa ayenera kuti adzakhala ndi malangizo aumulungu akuti onse azitsatira kuti apindule ndi nsembe ya Yesu Kristu mokwanira. Pamene uchimo wa Adamu wachotsedweratu, ‘imfa idzathetsedweratu.’ Pamene zaka chikwi zidzafika kumapeto, Mulungu adzakhala “zonse mu zonse.” (1 Akorinto 15:28) Munthu sadzafunikiranso chithandizo cha Mkulu wa Ansembe kapena Moombolo. Anthu onse adzakhala atabwezeretsedwa kuungwiro umene Adamu anasangalala nawo poyambirira.
Kuuka Mwadongosolo
16. (a) Nchifukwa ninji kuli koyenerera kukhulupirira kuti anthu adzaukitsidwa mwadongosolo? (b) Ndani amene ayenera kuti adzakhala pakati pa anthu oyambirira kuukitsidwa?
16 Popeza kuti chiukiriro cha kumwamba chikuchitika mwadongosolo, “yense m’dongosolo lake la iye yekha,” nzachionekere kuti chiukiriro cha padziko lapansi sichidzapangitsa anthu kuchuluka mwachisawawa. (1 Akorinto 15:23) Zoonadi, anthu oukitsidwa kumenewo adzafunikira kuyang’aniridwa. (Yerekezerani ndi Luka 8:55.) Adzafunikira chithandizo chakuthupi ndiponso—chofunika kwambiri—kuthandizidwa mwauzimu kuti apeze chidziŵitso chopatsa moyo cha Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. (Yohane 17:3) Kukakhala kosatheka kusamalira onse bwinobwino ngati atati akauke onse panthaŵi imodzi. Nkoyenera kuganiza kuti chiukiriro chidzachitika mwapang’onopang’ono. Mwachionekere Akristu okhulupirika amene adzafa dongosolo la Satana litatsala pang’ono kutha adzakhala pakati pa awo oyambirira kuukitsidwa. Tingayembekezerenso kuti amuna akale okhulupirika amene adzatumikira ngati “akalonga” adzauka moyambirira.—Salmo 45:16, NW.
17. Ndi nkhani zina ziti zokhudza chiukiriro zimene Baibulo silimatchula, ndipo nchifukwa chiyani Akristu safunika kukhudzidwa nazo mopambanitsa?
17 Komabe, sitiyenera kuumirira pankhani zoterezi. Nkhani zambiri Baibulo silimanenapo chilichonse. Silitchula tsatanetsatane wa mmene zidzakhalira, nthaŵi, kapena malo amene anthu adzaukitsidwirako. Silitiuza mmene awo oukitsidwa adzakhalira ndi nyumba, chakudya, ndi zovala. Sitinganenenso motsimikiza mmene Yehova adzasamalirira nkhani zina zonga ngati kaleredwe ndi kusamalira ana oukitsidwa kapena mmene adzachitira ndi mikhalidwe ina imene idzakhudza mabwenzi athu ndi okondedwa athu. Zoona, nkwachibadwa kuganiza nkhani ngati zimenezi; koma nkopanda nzeru kumayesa kuyankha mafunso amene padakali pano alibe mayankho. Tingosumika malingaliro athu pakutumikira Yehova mokhulupirika ndi kupeza moyo wosatha. Akristu odzozedwa ali ndi chiyembekezo cha chiukiriro chaulemerero kumwamba. (2 Petro 1:10, 11) A “nkhosa zina” akuyembekezera kuti mu Ufumu wa Mulungu adzakhala padziko lapansi kosatha. (Yohane 10:16; Mateyu 25:33, 34) Ponena za tsatanetsatane wa chiukiriro amene sakudziŵika, tingodalira pa Yehova. Chimwemwe chathu chamtsogolo nchosungika mwa Iye amene akhoza ‘kukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.’—Salmo 145:16; Yeremiya 17:7.
18. (a) Kodi Paulo akufotokoza chilakiko chotani? (b) Nchifukwa chiyani timakhulupirira nchidaliro chonse mu chiyembekezo cha chiukiriro?
18 Paulo anamaliza nkhani yake mwakuti: “Ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Akorinto 15:57) Inde, imfa ya mwa Adamu ikugonjetsedwa kupyolera mwa nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, ndipo onse, odzozedwa ndi a “nkhosa zina,” amapeza chilakiko. Ndithudi, a “nkhosa zina” amene ali ndi moyo lerolino ali ndi chiyembekezo cha mbadwo uno wokha. Monga mbali ya “khamu lalikulu” lomakulakulalo, akhoza kupulumuka “chisautso chachikulu” osalaŵako nkomwe imfa! (Chivumbulutso 7:9, 14) Komabe, ngakhale amene angafe chifukwa cha ‘zotigwera m’nthaŵi mwake’ kapena chifukwa cha atumiki a Satana, angaike chidaliro chawo pa chiyembekezo cha chiukiriro.—Mlaliki 9:11.
19. Kodi Akristu onse lerolino ayenera kulabadira chilangizo chotani?
19 Choncho, tikuyembekezera mwachidwi tsikulo pamene imfa idzathetsedwa. Chikhulupiriro chathu chosagwedera mu lonjezo la Yehova la chiukiriro chimatipatsa kaonedwe kabwino ka zinthu. Chilichonse chomwe chingatichitikire m’moyo uno—ngakhale titafa—palibe chomwe chingatilande mphotho yomwe Yehova walonjeza. Motero, mawu omalizira a Paulo kwa Akorinto ndi oyenerera lerolino ngati mmene analili zaka zikwi ziŵiri zapitazo: “Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”—1 Akorinto 15:58.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi Paulo anayankha motani funso lonena za matupi amene odzozedwa adzaukitsidwa nawo?
◻ Kodi ndi motani ndipo ndi liti pamene imfa idzathetsedweratu?
◻ Ndani amene adzaphatikizidwa m’chiukiriro cha padziko lapansi?
◻ Kodi tiyenera kukhala ndi malingaliro otani ponena za nkhani zimene Baibulo silimatchula?
[Zithunzi patsamba 20]
Mbewu ‘imafa’ mwa kusinthika kwakukulu
[Zithunzi patsamba 23]
Amuna ndi akazi akale okhulupirika, monga ngati Nowa, Abrahamu, Sara, ndi Rahabi, adzakhala pakati pa oukitsidwawo
[Chithunzi patsamba 24]
Idzakhala nthaŵi ya chisangalalo chachikulu pamene anthu akuukitsidwa!