MUTU 9
Zotsatira za Ntchito Yolalikira—“M’mindamo Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu anadabwa kwambiri ndi zimene ananena? (b) Kodi Yesu ankanena kukolola kotani?
OPHUNZIRA a Yesu anadabwa kwambiri atawauza kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” Atayang’ana minda imene Yesu ankaloza anaona kuti minda yonse inali ndi mbewu za barele zobiriwira bwino zomwe zinali zitangomera kumene, osati ngati mmene Yesu ankanenera. Mosakayikira ophunzirawa ankadzifunsa kuti, ‘Kodi akunena mbewu ziti?’ chifukwa pa nthawiyi kunali ‘kutatsala miyezi inayi kuti ayambe kukolola.’—Yoh. 4:35.
2 Ponena mawu amenewa, Yesu sankatanthauza kukolola mbewu zenizeni. Iye ankafuna kuthandiza ophunzira ake kuti adziwe mfundo ziwiri zofunika kwambiri pa ntchito yokolola mwauzimu, yomwe ndi yokolola anthu. Kodi mfundo ziwiri zimenezi ndi ziti? Kuti tizidziwe, tiyeni tikambirane zimene zinachitika Yesu asananene mawu amenewa.
Anawalimbikitsa Kugwira Ntchito Kuti Akhale Osangalala
3. (a) N’chiyani chinachititsa Yesu kunena kuti: “M’mindamo mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola”? (Onani mawu a m’munsi.) (b) Kodi Yesu anatani pofuna kuthandiza ophunzira ake kumvetsa mfundo imeneyi?
3 Zimene tafotokoza m’ndime yoyambirira zija zinachitika chakumapeto kwa chaka cha 30 C.E., ndipo Yesu ndi ophunzira ake anali pafupi ndi tawuni ya Sukari ku Samariya. Pa nthawiyi ophunzira akewo analowa mumzinda ndipo Yesu anakhala pachitsime. Ali pachitsimepo analalikira mzimayi wina yemwe sanachedwe kuzindikira kufunika kwa zimene Yesu ankalalikirazo. Ophunzira aja atafika, mzimayi uja anathamanga n’kulowa mumzinda wa Sukari kukauza anthu ena zinthu zodabwitsa zimene anaphunzira kuchokera kwa Yesu. Anthu anachita chidwi ndi zimene anamva kwa mzimayiyu moti ambiri ananyamuka kuti akakumane ndi Yesu. Pa nthawi imeneyi Yesu anaona anthu akubwera chapatali ndithu, akudutsa m’minda, ndipo mwina m’pamene ananena mawu akuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.”a Ndiyeno pofuna kuthandiza ophunzira akewo kudziwa kuti sankanena za mbewu zenizeni koma mbewu zauzimu, Yesu ananena kuti: “Wokolola . . . akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha.”—Yoh. 4:5-30, 36.
4. (a) Kodi ndi mfundo ziwiri ziti zimene Yesu ananena zokhudza ntchito yokolola? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
4 Kodi Yesu anaphunzitsa mfundo ziwiri ziti zokhudza ntchito yokolola mwauzimu? Mfundo yoyamba ndi yakuti, ntchitoyi ikufunika kugwiridwa mwamsanga. Pamene ananena kuti “m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola” kwenikweni ankalimbikitsa ophunzira ake kuti agwire ntchito yolalikira. Pofuna kuthandiza ophunzira akewo kuona kufunika koti agwire ntchitoyo mwamsanga, Yesu ananenanso kuti: “Wokolola akulandira kale malipiro.” Zimenezi zikusonyeza kuti ntchito yokolola inayamba kale kuchitika ndipo anafunika kuchita changu pogwira ntchitoyi. Mfundo yachiwiri ndi yakuti, anthu amene akugwira ntchitoyi amakhala osangalala. Yesu ananena kuti ofesa mbewu ndi okolola ‘adzasangalalira pamodzi.’ (Yoh. 4:35b, 36) Mmene Yesu anasangalalira ataona kuti ‘Asamariya ambiri . . . akhulupirira mwa iye,’ ndi mmenenso ophunzira ake adzasangalalire chifukwa chogwira ntchito yokolola ndi mtima wonse. (Yoh. 4:39-42) Zimene zinachitika nthawi imeneyi zili ndi tanthauzo lapadera kwa ife chifukwa zinkaimira ntchito yokolola mwauzimu imene ikuchitika masiku ano. Koma kodi ntchito yokolola mwauzimu imene ikuchitika masiku ano inayamba liti? Kodi ndani akugwira nawo ntchitoyi? Nanga pali zotsatira zotani?
Mfumu Yathu Ikutsogolera Ntchito Yaikulu Yokolola
5. (a) Kodi ndani akutsogolera ntchito yokolola yomwe ikuchitika padziko lonse? (b) Kodi masomphenya amene Yohane anaona akusonyeza bwanji kuti ntchitoyi iyenera kugwiridwa mwamsanga?
5 M’masomphenya amene mtumwi Yohane anaona, Yehova anasonyeza kuti anasankha Yesu kuti atsogolere pa ntchito yokolola anthu padziko lonse. (Werengani Chivumbulutso 14:14-16.) M’masomphenyawa, Yesu akuoneka atavala chisoti chachifumu komanso atanyamula chikwakwa. “Chisoti chachifumu chagolide” chomwe chili “kumutu kwa [Yesu]” chikusonyeza kuti akulamulira monga Mfumu. “Chikwakwa chakuthwa” chimene “chili m’dzanja lake,” chikusonyeza ntchito yomwe ali nayo monga Wokolola. Pofuna kusonyeza kuti ntchitoyi ndi yofunika kugwiridwa mwamsanga, Yehova analankhula kudzera mwa mngelo wake kuti: “Zokolola za padziko lapansi zapsa bwino.” Zimenezi zikusonyeza kuti ‘ola lomweta lafika’ ndipo ntchitoyi iyenera kugwiridwa mwamsanga. Pomvera zimene Mulungu akumuuza kuti, “tsitsa chikwakwa chako,” Yesu akutsitsira chikwakwa chake kudziko lapansi n’kumweta anthu. Masomphenyawa akutikumbutsanso kuti ‘m’minda mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.’ Akutithandizanso kudziwa nthawi imene ntchito yokolola yomwe ikuchitika padziko lonse inayamba.
6. (a) Kodi “nyengo yokolola” inayamba liti? (b) Kodi ntchito ‘yokolola za padziko lapansi’ inayamba liti? Fotokozani.
6 Masomphenya amene Yohane anaona, amene analembedwa mu Chivumbulutso chaputala 14, amasonyeza Yesu yemwe ndi Wokolola atavala chisoti chachifumu (vesi 14). Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu akugwira ntchitoyi ataikidwa kale kukhala Mfumu mu 1914. (Dan. 7:13, 14) Kenako patangopita nthawi yochepa, Yesu anauzidwa kuti ayambe kugwira ntchito yokolola (vesi 15). Mmene zinthu zikuchitikira m’masomphenyawa ndi mmenenso zikuchitikira m’fanizo la Yesu lofotokoza za ntchito yokolola tirigu. M’fanizoli Yesu ananena kuti: “Nthawi yokolola ikuimira mapeto a nthawi ino.” Zimenezi zikutanthauza kuti nyengo yokolola ndiponso mapeto a nthawi ino zinayambira limodzi mu 1914. Koma kukolola kwenikweni kunayamba “m’nyengo yokolola.” (Mat. 13:30, 39) Panopo tikutha kuona kuti ntchito yokolola inayamba patangopita zaka zochepa Yesu atayamba kulamulira monga Mfumu. Poyamba, kuchokera m’chaka cha 1914 mpaka kumayambiriro kwa chaka cha 1919, Yesu anagwira ntchito yoyeretsa otsatira ake odzozedwa. (Mal. 3:1-3; 1 Pet. 4:17) Ndiyeno mu 1919, ntchito ‘yokolola za padziko lapansi’ inayambika. Yesu anagwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika, amene anali atangomusankha kumene, kuti athandize abale kudziwa kuti ntchitoyi ikufunika kugwiridwa mofulumira kwambiri. Tiyeni tione zimene zinachitika.
7. (a) Kodi abale anamvetsa bwino mfundo iti yomwe inawathandiza kuona kuti ntchito yolalikira ikufunika kugwiridwa mwamsanga? (b) Kodi abale athu analimbikitsidwa kuchita chiyani?
7 M’mwezi wa July 1920, Nsanja ya Olonda inanena kuti: “Chifukwa chomvetsa bwino zimene Malemba akunena, mpingo wapatsidwa mwayi waukulu kwambiri wolengeza uthenga wonena za Ufumu.” Mwachitsanzo, ulosi wa Yesaya unathandiza abale amene ankatsogolera ntchitoyi kuona kuti uthenga wa Ufumu uyenera kulengezedwa padziko lonse. (Yes. 49:6; 52:7; 61:1-3) Abalewa sanadziwe kuti ntchito imeneyi idzachitika bwanji koma ankakhulupirira kuti Yehova adzawathandiza. (Werengani Yesaya 59:1.) Chifukwa chomvetsa kuti ntchito yolalikirayi iyenera kuchitika mwamsanga, abale onse analimbikitsidwa kuchita khama kwambiri pogwira ntchitoyi. Koma kodi iwo anachitadi khama?
8. Kodi abale anamvetsa bwino mfundo ziwiri ziti zokhudza ntchito yolalikira mu 1921?
8 M’mwezi wa December 1921, Nsanja ya Olonda inanena kuti: “Chaka chino chaposa zaka zina zonse. Anthu ambiri amva uthenga wa choonadi m’chaka chino cha 1921 kuposa zaka zina zonse m’mbuyomu.” Nsanja ya Olonda yomweyi inanenanso kuti: “Koma padakali ntchito yambiri yoti tigwire. . . . Tiyeni tigwire ntchitoyi ndi mtima wosangalala.” Pamenepatu abale athu anamvetsa mfundo ziwiri zofunika kwambiri zokhudza ntchito yolalikira zimene Yesu anauza ophunzira ake. Mfundo zake ndi zakuti: Ntchitoyi ikufunika kugwiridwa mwamsanga ndiponso yakuti, anthu amene akugwira ntchitoyi amakhala osangalala.
9. (a) Kodi Nsanja ya Olonda ina imene inatuluka m’chaka cha 1954 inanena chiyani zokhudza ntchito yokolola? (b) Kodi chiwerengero cha ofalitsa padziko lonse lapansi chakhala chikuwonjezeka bwanji m’zaka 50 zapitazi? (Onani tchati chakuti, “Kuwonjezeka kwa Ofalitsa Padziko Lonse.”)
9 M’zaka za m’ma 1930, abale atamvetsa kuti khamu lalikulu lidzagwira ntchito yolalikira za Ufumu, anachita khama kwambiri pogwira ntchitoyi. (Yes. 55:5; Yoh. 10:16; Chiv. 7:9) Kodi zotsatira zake zinali zotani? M’chaka cha 1934, anthu omwe ankalalikira uthenga wa Ufumu analipo 41,000 koma pofika m’chaka cha 1953 analipo 500,000. Nsanja ya Olonda ya December 1, 1954, inanena kuti: “Ntchito yokolola imene ikuchitika padziko lonse ikutheka chifukwa cha mzimu wa Yehova komanso mphamvu ya Mawu ake.”b—Zek. 4:6.
Dziko |
1962 |
1987 |
2013 |
---|---|---|---|
Australia |
15,927 |
46,170 |
66,023 |
Brazil |
26,390 |
216,216 |
756,455 |
France |
18,452 |
96,954 |
124,029 |
Italy |
6,929 |
149,870 |
247,251 |
Japan |
2,491 |
120,722 |
217,154 |
Mexico |
27,054 |
222,168 |
772,628 |
Nigeria |
33,956 |
133,899 |
344,342 |
Philippines |
36,829 |
101,735 |
181,236 |
U.S. of America |
289,135 |
780,676 |
1,203,642 |
Zambia |
30,129 |
67,144 |
162,370 |
1950 |
234,952 |
1960 |
646,108 |
1970 |
1,146,378 |
1980 |
1,371,584 |
1990 |
3,624,091 |
2000 |
4,766,631 |
2010 |
8,058,359 |
Mafanizo Amene Analosera Zotsatira za Ntchito Yokolola
10, 11. Kodi fanizo la kanjere ka mpiru limafotokoza mfundo ziti zokhudza kakulidwe ka kanjereka?
10 M’mafanizo ake onena za Ufumu, Yesu ananeneratu momveka bwino zotsatira za ntchito yokolola. Tiyeni tikambirane fanizo la kanjere ka mpiru ndi la zofufumitsa. Tikambirana kwambiri za mmene mafanizo amenewa akwaniritsidwira m’nthawi ya mapeto ino.
11 Fanizo la kanjere ka mpiru. Munthu anabzala kanjere ka mpiru ndipo kanakula n’kukhala mtengo waukulu moti mbalame zinkakhala pamthunzi wake. (Werengani Mateyu 13:31, 32.) Kodi fanizoli linafotokoza mfundo ziti zokhudza kakulidwe ka kanjere ka mpiru? (1) Kanjereka kamakula kwambiri. Kanjere ka mpiru ndi “kakang’ono kwambiri mwa njere zonse za padziko lapansi” koma kamakula n’kukhala mtengo wa “nthambi zikuluzikulu.” (Maliko 4:31, 32) (2) Palibe chimene chingalepheretse kanjereka kumera ndi kukula. “[Kanjere ka mpiru] akakafesa, kamamera.” Yesu sananene kuti: “Kakhoza kumera,” koma ananena kuti: “Kamamera.” Zimenezi zikusonyeza kuti palibe chimene chingakalepheretse kumera ndi kukula. (3) Mtengowu ukakula umakhala ndi mthunzi woti n’kukhalapo. “Mbalame zam’mlengalenga zimabwera” ndipo “zimatha kupeza malo okhala mumthunzi wake.” Kodi mfundo zitatu zimenezi zikugwirizana bwanji ndi ntchito yokolola mwauzimu imene ikuchitika masiku ano?
12. Kodi fanizo la kanjere ka mpiru likugwirizana bwanji ndi ntchito yokolola yomwe ikuchitika masiku ano? (Onani bokosi lakuti, “Chiwerengero cha Ophunzira Baibulo Chikukula.”)
12 (1) Kukula kwake: Fanizoli limasonyeza mmene uthenga wa Ufumu komanso mpingo wachikhristu udzakulire. Kuyambira m’chaka cha 1919, anthu amene akugwira mwakhama ntchito yokololayi akhala akusonkhanitsidwa mu mpingo wachikhristu umene unayambiranso kugwira ntchito. Pa nthawi imeneyo chiwerengero cha anthuwa chinali chochepa kwambiri koma chinakula mofulumira. Kukula kumene kwachitika kuchokera m’zaka za m’ma 1900 kufika pano n’kochititsa chidwi kwambiri. (Yes. 60:22) (2) Palibe chimene chingalepheretse kukula: Palibe chimene chalepheretsa mpingo wachikhristu kukula. Ngakhale kuti mpingo wachikhristu wakhala ukutsutsidwa kwambiri, wapitirizabe kukula. (Yes. 54:17) (3) Mthunzi woti n’kukhalapo. “Mbalame zam’mlengalenga” zimene zimapeza malo okhala mumtengowu zikuimira anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mayiko pafupifupi 240 omwe atamva uthenga wa Ufumu analowa mu mpingo wachikhristu. (Ezek. 17:23) Mu mpingowu amalandira chakudya chauzimu, amalimbikitsidwa komanso amatetezedwa.—Yes. 32:1, 2; 54:13.
13. Kodi fanizo la zofufumitsa limafotokoza mfundo ziti?
13 Fanizo la zofufumitsa. Mkazi wina anatenga zofufumitsa n’kuzisakaniza ndi ufa ndipo mtanda wonse unafufuma. (Werengani Mateyu 13:33.) Kodi fanizoli linafotokoza mfundo ziti? Tiyeni tione mfundo ziwiri. (1) Kukula kumachititsa zinthu kusintha. Zofufumitsazo zinalowerera moti “mtanda wonsewo unafufuma.” (2) Kukula kumafalikira. Zofufumitsazo zimafufumitsa “ufa [wonse] wokwana mbale zitatu zazikulu zoyezera.” Kodi mfundo ziwiri zimenezi zikugwirizana bwanji ndi ntchito yokolola mwauzimu imene ikuchitika masiku ano?
14. Kodi fanizo la zofufumitsa likugwirizana bwanji ndi ntchito yokolola yomwe ikuchitika masiku ano?
14 (1) Kusintha: Zofufumitsazo zikuimira uthenga wa Ufumu ndipo ufa ukuimira anthu. Zofufumitsa zikasakanizidwa ndi ufa zimachititsa kuti ufawo usinthe. Uthenga wa Ufumu umachititsanso kuti mtima wa munthu amene wamvetsera uthengawo usinthe. (Aroma 12:2) (2) Kufalikira: Kulowerera kwa zofufumitsa kukuimira kufalikira kwa uthenga wa Ufumu. Zofufumitsazo zimalowerera mu ufa wonsewo ndipo zimachititsa kuti mtanda wonsewo ufufume. Mofanana ndi zimenezi, uthenga wa Ufumu wafalikira “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Mfundo imeneyi ikusonyezanso kuti uthenga wa Ufumu udzafalikira m’madera onse, kuphatikizapo m’madera amene ntchito yathu ndi yoletsedwa, ngakhale kuti ntchito yolalikira m’madera amenewa siingakhale yoonekera kwenikweni.
15. Kodi mawu a pa Yesaya 60:5, 22 akwaniritsidwa bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “Yehova Ndi Amene Anachititsa Kuti Zitheke,” patsamba 93, ndi lakuti “Zimene Zachitika Kuti ‘Wamng’ono Asanduke Mtundu Wamphamvu,’” patsamba 96-97.)
15 Kudakali zaka pafupifupi 800 Yesu asanafotokoze mafanizo amenewa, Yehova ananeneratu momveka bwino kudzera mwa Yesaya kuti ntchito yokolola mwauzimu imene ikuchitika masiku ano idzafalikira kwambiri komanso kuti anthu adzasangalala chifukwa cha ntchitoyi.c Yehova anafotokoza kuti anthu ambiri ‘ochokera kutali’ adzalowa m’gulu lake. Kenako analankhula kwa “mkazi,” yemwe masiku ano akuimira otsalira odzozedwa, kuti: “Pa nthawi imeneyo, nkhope yako idzasangalala ukadzaona zimenezi. Mtima wako udzanthunthumira ndi kufutukuka, chifukwa chuma cha m’nyanja chidzabwera kwa iwe. Katundu wa mitundu ya anthu adzabwera kwa iwe.” (Yes. 60:1, 4, 5, 9) Zimenezi zikuchitikadi masiku ano. Anthu amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali akusangalala kwambiri chifukwa choona mmene chiwerengero cha anthu olalikira Ufumu chakulira m’madera awo kuchokera pa anthu ochepa kufika pa anthu masauzande ambiri.
Zimene Zimachititsa Kuti Atumiki Onse a Yehova Azisangalala
16, 17. Tchulani chifukwa chimodzi chimene chachititsa kuti ‘ofesa mbewu ndi okolola asangalalire pamodzi.’ (Onaninso bokosi lakuti, “Mmene Timapepala Tiwiri Tinathandizira Anthu Awiri M’dera la Amazon.”)
16 Paja Yesu anauza atumwi ake kuti: “Wokolola . . . akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha, kuti wofesa mbewu ndi wokolola asangalalire pamodzi.” (Yoh. 4:36) Kodi ntchito yokolola yomwe ikuchitika padziko lonse imatichititsa bwanji kuti ‘tizisangalala pamodzi’? Pali njira zambiri koma tiyeni tikambirane njira zitatu zokha.
17 Yoyamba, timasangalala kudziwa zimene Yehova akuchita pa ntchitoyi. Tikamalalikira uthenga wa Ufumu timakhala tikufesa mbewu. (Mat. 13:18, 19) Tikathandiza munthu kukhala wotsatira wa Khristu timakhala tikukolola. Ndipo tonsefe timasangalala tikamaona mmene Yehova amachititsira mbewu za Ufumu ‘kumera ndi kukula.’ (Maliko 4:27, 28) Mbewu zina zimene timafesa zimamera pakapita nthawi ndipo amadzakolola ndi anthu ena. Mwina munakumanapo ndi zimene mlongo wina wa ku Britain, dzina lake Joan, amene anabatizidwa zaka 60 zapitazo, anakumana nazo. Iye ananena kuti: “Ndakumanapo ndi anthu amene anandiuza kuti ndinabzala mbewu ya choonadi mumtima mwawo pamene ndinawalalikira zaka zambiri zapitazo. Patapita nthawi, abale ndi alongo ena anaphunzira nawo Baibulo n’kuwathandiza kukhala atumiki a Yehova koma sindinkadziwa kuti anapitiriza kuphunzira Baibulo. Ndimasangalala kuti mbewu zimene ndinabzala zinamera ndipo ena anakolola.”—Werengani 1 Akorinto 3:6, 7.
18. Kodi lemba la 1 Akorinto 3:8 limatchula chifukwa chiti chosangalalira?
18 Yachiwiri, timasangalala tikamaganizira zimene Paulo ananena kuti: “Aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake.” (1 Akor. 3:8) Aliyense adzalandira mphoto chifukwa chogwira nawo ntchito yolalikira, osati chifukwa cha zimene wakolola pogwira ntchitoyi. Mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri kwa amene akugwira ntchito yolalikira m’madera amene anthu sachita chidwi ndi uthenga wathu. Mulungu amaona kuti mtumiki aliyense amene akugwira nawo ntchito yofesa mbewu ndi mtima wake wonse ‘akubala zipatso zambiri.’ Zimenezi n’zimene zimachititsa mtumikiyo kukhala wosangalala.—Yoh. 15:8; Mat. 13:23.
19. (a) Kodi ulosi wa Yesu wopezeka pa Mateyu 24:14 umagwirizana bwanji ndi kukhala wosangalala? (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati anthu sakutimvetsera pamene tikugwira ntchito yopanga ophunzira?
19 Yachitatu, timasangalala chifukwa timadziwa kuti ntchito yathu ikukwaniritsa ulosi. Taganizirani zimene Yesu anayankha atumwi ake atamufunsa kuti: “[Kodi] chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” Iye anawauza kuti ntchito yolalikira ndi mbali imodzi ya chizindikiro cha kukhalapo kwake. Kodi pamenepa Yesu ankanena za kupanga ophunzira? Ayi, chifukwa ananenanso kuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni.” (Mat. 24:3, 14) Choncho, kulalikira za Ufumu, komwe ndi kufesa mbewu, ndi mbali ya chizindikiro. Ndiyetu tikamalalikira uthenga wabwino wa Ufumu tisamaganize kuti ntchito yathu siikuyenda bwino chifukwa chakuti sitikupanga ophunzira, koma tizikumbukira kuti ngati tikuchitira “umboni” ndiye kuti ntchito yathu ikuyenda bwino.d Kaya anthu akumvetsera uthenga wathu kapena ayi, ifeyo timakhala tikukwaniritsa ulosi wa Yesu komanso tili ndi mwayi wokhala “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Zimenezitu ndi zifukwa zabwino zotichititsa kukhala osangalala.
“Kuchokera Kotulukira Dzuwa Kukafika Kumene Limalowera”
20, 21. (a) Kodi mawu opezeka pa Malaki 1:11 akukwaniritsidwa bwanji? (b) Pa ntchito yokololayi, kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani, ndipo chifukwa chiyani?
20 M’nthawi ya atumwi, Yesu anathandiza atumwi ake kuona kuti ntchito yokolola inkafunika kuchitika mwamsanga. Kuyambira m’chaka cha 1919, Yesu wakhalanso akuthandiza atumiki ake a masiku ano kuti aziona ntchitoyi chimodzimodzi. Chifukwa chomvera mawu amenewa, atumiki a Mulungu akhala akugwira ntchito yokolola mwakhama ndipo palibe chimene chalepheretsa ntchitoyi. Malinga ndi zimene mneneri Malaki analosera, masiku ano ntchito yolalikira ikuchitika “kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera.” (Mal. 1:11) Kulikonse komwe ali, ofesa mbewu komanso okolola akugwira ntchito ndipo akusangalalira pamodzi. Tsiku lililonse kuyamba m’mawa mpaka madzulo, timagwira ntchitoyi mwakhama chifukwa chodziwa kuti ikufunika kugwiridwa mwamsanga.
21 Pa zaka 100 zapitazi taona mmene kagulu kakang’ono ka atumiki a Mulungu kakulira n’kukhala “mtundu wamphamvu.” Zimenezi zimachititsa mitima yathu ‘kunthunthumira ndiponso kufutukuka’ ndi chisangalalo. (Yes. 60:5, 22) Chifukwa chosangalala ndi ntchitoyi komanso chifukwa chokonda Yehova, yemwe ndi “Mwini zokolola,” tiyeni tipitirize kugwira nawo ntchito yofunika kwambiri yokololayi mpaka mapeto.—Luka 10:2.
a N’kutheka kuti Yesu ananena mawu akuti “m’mindamo mwayera” ataona khamu la Asamariya amene anali atavala mikanjo yoyera akubwera kudzakumana naye.
b Kuti mudziwe zambiri zimene zinachitika pa zaka zimenezi komanso m’zaka zotsatira, werengani buku la Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, masamba 425 mpaka 520, amene akufotokoza zimene zakhala zikuchitika pa ntchito yokololayi kuyambira m’chaka cha 1919 mpaka chaka cha 1992.
c Kuti mudziwe zambiri za ulosi umenewu, onani buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 2, masamba 303 mpaka 320.
d Ophunzira Baibulo oyambirira ankamvetsa mfundo ya choonadi imeneyi. Magazini ya Zion’s Watch Tower ya November 15, 1895, inanena kuti: “Ngati takwanitsa kusonkhanitsa tirigu wochepa, ndiye kuti n’zotheka kuchitira umboni choonadi kwa anthu ambiri. . . . Aliyense akhoza kugwira nawo ntchito yolalikira.”