Kodi Mumakumbukira?
Kodi mwasangalala kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Eya, tawonani ngati mungathe kuyankha mafunso otsatirawa:
◻ Popeza kuti angelo osamverawo anabindikiritsidwa ku Dzenje, kodi ichi chatanthauzanji kwa iwo? (2 Petro 2:4)
Iwo alibenso malo m’gulu loyera la Yehova ndipo tsopano alibe kuunika kwaumulungu. Komabe, iwo akugwirabe ntchito pansi pa chitsogozo cha Satana ndi kupitirizabe kugwirizana mwathithithi ndi anthu, kukalamira kulamulira amuna, akazi, ndiponso ana. (Chibvumbulutso 12:12, 17)—4/15, tsamba 14.
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika ‘kuda choipa’ m’maso mwa Yehova? (Salmo 97:10)
Awo amene amadana nacho choipa sadzafuna njira yodziloŵetseramo. Kumbali ina, anthu amene samachida angapeŵe mwakuthupi pamene mwamaganizo akukhumba kuti akanakhalako ndi phande m’zinthu zoipa.—4/15, tsamba 21.
◻ M’fanizo la Yesu la matalente, kodi ndi phunziro lofunika lotani limene lakhazikitsidwa kwa awo amene amati ndi atsatiri a Kristu? (Mateyu 25:14-30)
Iwo ayenera kugwira ntchito kuwonjezera chuma cha Mbuye wawo wakumwamba mwakukhala ndi phande lokwanira m’ntchito yolalikira. Ndipokhapo pamene angatsimikiziridwe za chiyamikiro cha Yesu ndi kufupidwa. Iwo ayenera kupeŵa kuponyedwa ku mdima wakunja ndi chiwonongeko chotheratu.—5/1, tsamba 9.
◻ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anauza ophunzira ake kupemphera motere: “Musatitengere kokatiyesa”? (Mateyu 6:13)
Mawu ameneŵa samatanthauza kuti Yehova amatiyesa kuchita tchimo. M’malomwake, ife, kwenikweni tingampemphe Yehova kusatilola kugonja pamene tayesedwa kapena kutsenderezedwa kusamumvera iye. Tingapembedzere Atate wathu kutsogoza mapazi athu kotero kuti palibe chiyeso chomwe chidzatigwera chimene chidzakhala chonkitsa kwa ife. (1 Akorinto 10:13)—5/15, tsamba 19.
◻ Kodi nkoyenera kwa Mkristu kulandira jekeseni wa mbali ya mwazi, monga ngati immune globulin kapena albumin?
Povomereza ku chilamulo cha Mulungu, Akristu samavomereza kuthiridwa mbali zazikulu za mwazi—plasma, maselo ofiira, maselo oyera, kapena maplatelet. Komabe, Mboni zina za Yehova zalingalira mwachikumbumtima chabwino kukhala zokhoza kulandira jekeseni wa imodzi ya maproteni a plasma. Mosangalatsa, ena a maproteni ameneŵa mwachibadwa amadutsa kuchokera ku mwazi wa mkazi wapakati kupita ku dongosolo lamwazi lapadera la mluza wake.—6/1, masamba 30, 31.
◻ Kodi nchifuno chotani chimene chinatumikiridwa ndi utumiki wa Yesu wosambitsa mapazi a ophunzira ake pa Paskha waphindu womalizira?
Yesu anali kuphunzitsa ophunzira ake phunziro la kudzichepetsa. Aliyense sayenera kufunafuna malo oyamba, akumalingalira kuti ngofunika kwambiri. M’malomwake, onse ayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi kukhala ofunitsitsa kutumikirana popanda tsankho, mosasamala kanthu za kutsika kapena kusasangalatsa kumene ntchitoyo ingakhalire. (Yohane 13:12-17)—6/15, tsamba 9.
◻ Kodi ndi m’lingaliro lotani limene Ayuda m’Bereya ‘anasanthulira [Malemba] mosamalitsa’? (Machitidwe 17:11)
Abereyawo sanamkaikire Paulo ndi uthenga womwe anawabweretsera, koma anafufuza kuti atsimikizire kuti Yesu anali Mesiya. Chenicheni chakuti ambiri a iwo anakhala akukhulupirira chimasonyeza kuti cholinga chawo chinali chowona. (Machitidwe 17:12)—6/15, tsamba 18.
◻ Kodi ndiliti limene linali “buku la Nkhondo za Yehova”? (Numeri 21:14)
Ilo linali mbiri yodalirika ya nkhondo za Mulungu mokomera anthu ake. Mwinamwake inayambira ndi chilakiko cha Abrahamu pa oloŵerera okhala ndi zida a Dziko Lolonjezedwa monga kwalembedwa mu Genesis mutu 14. Mapeto olakika a bukhuli adzakhala ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse’ pa Harmagedo. (Chibvumbulutso 16:14, 16)—7/1, masamba 20, 22.
◻ Kodi ndimotani mmene Mawu a Mulungu, Baibulo, amatithandizira kulaka kupweteka?
Baibulo limatiuza chifukwa chake Yehova walola kupweteka, ndipo limatitsimikizira kuti kupweteka kudzatha posachedwapa. (Aroma 5:12; Chibvumbulutso 21:1-5)—7/15, masamba 4; 5.
◻ Kodi ndimotani mmene anthu a Mulungu lerolino ‘angawunikire monga . . . kalirole ulemerero wa Yehova’? (2 Akorinto 3:18)
Ulemerero wa Mulungu unawala kupyolera mwa ‘Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu.’ Mboni za Yehova zimawunikira ulemerero umenewu mwakulankhula za ulemerero wa Yehova ndi ulemerero wa Ufumu wake mwa Mwana wake. (2 Akorinto 4:4-6)—7/15, masamba 15, 16.
◻ Kodi ndiliti pamene munthu ayenera kubatizidwa?
Ubatizo ndi sitepe limene liyenera kutengedwa pamene munthu wakupanga kudzipereka kotheratu, kodzikana, ndipo kopanda malire kwa Yehova kupyolera mwa Kristu Yesu kuchita chifuniro cha Mulungu.—8/1, tsamba 14.