Chuma Chathu, Uminisitala Wamakono Waulemerero
“Tiri nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.”—2 AKORINTO 4:7.
1. (a) Kodi ndichuma chaulemerero chotani chimene tingakhale nacho, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi Baibulo limafotokoza motani kuperekedwa kwa Chilamulo cha Mose?
UMINISITALA wa kulalikidwa kwa “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” mkati mwa chimaliziro cha dongosolo la zinthu ulidi chuma, katundu wamtengo wapatali koposa. Chifukwa chakuti Yehova ali Mulungu waulemerero, utumiki kwa Mulungu uli uminisitala waulemerero, motero uli chuma. (Mateyu 24:14; 2 Akorinto 3:18–4:1) Ponena za kaperekedwe kaulemerero ka Chilamulo cha Mose, kwalembedwa pa Eksodo 34:29, 30 kuti: “Ndipo kunali pakutsika Mose pa Phiri la Sinai, ndi magome aŵiri a mboni m’dzanja lake la Mose, pakutsika iye m’phirimo, Mose sanadziŵa kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza iye adalankhula naye [Yehova]. Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israyeli anawona Mose, tawonani, khungu la nkhope yake linanyezimira; ndipo anawopa kumyandikiza.”
2. Kodi utumiki wa Chilamulo cha Mose unachitira chithunzi chiyani, ndipo nchifukwa ninji uminisitala wapambuyo pake uli waulemerero koposa?
2 Mavesi 32 mpaka 34 amawonjezera kuti: “Ndipo atatero, ana onse a Israyeli anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m’Phiri la Sinai. Ndipo Mose atatha kulankhula nawo, anaika chophimba pankhope pake. Koma pakuloŵa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka.” Utumiki wa Chilamulo cha Mose umenewo unachitira chithunzi uminisitala wa pangano latsopano la Nkhosweyo, Yesu Kristu. Motero, ngati uminisitala wakale unali waulemerero, uyenera kukhala woposa chotani nanga wapambuyo pake, “utumiki wa mzimu,” ndi kupambana muulemerero! (2 Akorinto 3:7-11) Uli waulemerero koposa chifukwa chakuti ulemerero wake ukhalabe, ndipo atsatiri a Yesu Kristu amakhalamo ndi phande.—Aroma 12:11.
3. (a) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chowona ponena za uminisitala wa Mboni za Yehova, komabe nchifukwa ninji ichi sichikuwonedwa motero ndi anthu ambiri? (b) Kodi nchiyani chinatsimikizira kuti Mose adaali pamaso pa ulemerero wa Yehova?
3 Motero, mofananamo uminisitala wa Mboni za Yehova ngwaulemerero. Komabe, ichi sichikuwonedwa ndi anthu ambiri ochititsidwa khungu ndi chipembedzo chonyenga. Ngakhale kuti ambiri ali ndi Baibulo ndipo angaliŵerenge, iwo alibe ‘maso owona.’ (2 Petro 1:5-9) Kuti achotse chophimba kumaso awo, ayenera kutembenukira kwa Yehova Mulungu mwa chikhulupiriro, popeza kuti pamene Mose anapita pamaso pa Yehova, anachotsa chophimba chimene chinabisa nkhope yake kwa Ayudawo. (2 Akorinto 3:16) Aisrayeli anawopa kuwona ulemerero wa Mulungu pankhope ya nkhoswe yawo ndipo anapempha kuti uphimbidwe pamaso pawo. Monga mmene nsanganizo yonyezimira younikiridwa ndi kuŵala imatulutsanso kuŵala mumdima, motero Mose, nkhonswe yawo, anaunikira ulemerero wa Yehova, kutsimikizira kuti iye adaali pamaso pa Yehova.
4. Kodi ndimotani mmene anthu osakhulupirira lerolino amatsanzirira Ayuda akale, komabe kodi nchiyani chimene atsatiri a Mose Wamkulu sakuwopa?
4 Mose anachitira chithunzi Mneneri wamkulu wa Mulungu, Yesu Kristu. Mofanana ndi amene anaphiphiritsiridwa naye, Mose Wamkulu ameneyu sakuwopa kuyang’ana ulemerero wa Yehova mwachindunji. Komabe, kufikira lerolino, anthu osakhulupirira ochititsidwa khungu ndi Mdyerekezi ndi chipembedzo chake Chachibabulo akutsanzira Ayuda akale amenewo ndipo amakana kuwona, kapena kuzindikira, ulemerero wa Mose Wamkulu kwambiri, Yesu Kristu. (2 Akorinto 3:12-15) Komabe, atsatiri ake owona samawopa kuyang’ana kunyezimira kwa ulemerero wa Yehova pamene ukutulutsidwa kuchokera ku nkhope ya Yesu Kristu. Pokhala omasulidwa kuchisonkhezero cha Babulo, iwo ali odzala kusonyeza ulemerero wa Mulungu. “Pokhala nacho,” akulemba motero Paulo, “chiyembekezo chotero, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu.”—2 Akorinto 3:12.
Osonyeza Ulemerero wa Mulungu
5. Kodi tingasonyeze motani ulemerero wa Mulungu ndi kukhala ngati Mose ali pamwamba paphiri pamaso pa Yehova?
5 Yesu Kristu wachotsa chophimba mwakuvumbula ndi kulengeza Yehova Mulungu kwa ife. (Yohane 1:14, 17, 18) Chotero tiyenera kuŵala, ndipo mwakutero ulemerero wa Mulungu umaŵalitsa “chiŵalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu,” umene tiyenera kulengeza. Kunyezimira kwake ndiko “chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.” Tiyenera kusonyeza ulemerero umenewu mwa kulankhula za ulemerero wa Yehova ndi ulemerero wa Ufumu wake wokhala m’manja mwa Mwana wake. (2 Akorinto 4:4-6) Mofanana ndi Mose ali pamwamba paphiripo pamaso pa Yehova, Mboni Zake padziko lapansi sizimaphimba mitima yawo pamaso pa ulemerero wa Yehova. Izo zimakhumbira ulemerero wosonyezedwa pankhope pa Mwana wa Yehova ndi Mfumu, Yesu Kristu. Motero, iwo ayenera kuunikira kwa ena kuŵala kwa ulemerero wa Mulungu.
6. Kodi Paulo akulongosola motani uminisitala wathu waulemerero pa 2 Akorinto 3:18, ndipo kodi ‘timasandulika’ m’njira zotani?
6 Kwa Mboni zinzake zonse za ulemerero wa Yehova, mtumwi Paulo akulongosola m’mawu aŵa: “Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalilore ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kumka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.” (2 Akorinto 3:18) Pamene tilandira ulemerero woonjezereka wa kuunika kumeneku, ndipamenenso tidzasonyeza woonjezereka, ndipamenenso timasandulika moonjezereka. Malingaliro amakhalitsidwa atsopano ndi kukonzedwanso, ngakhale kuti palibe masinthidwe alionse athupi ndi nkhope amene angawoneke. Kuli kuunika kwa uthenga waulemerero kumene timaŵalitsira kumene kumatisiyanitsa. Miyoyo yathu imasandulizidwa kukhala ngati Kristu, pamene tikudzikonzekeretsa kuchita utumiki wapadera wa kufalitsa kwa ena kuunika kwaulemerero kumeneko.—Ahebri 13:15.
7. Kodi ulemerero weniweni umachokera kumagwero otani, ndipo tingasonyeze motani ulemerero woterowo?
7 Kusandulika konseko kukuchititsidwa ndi mzimu, kapena mphamvu yogwira ntchito, ya Mulungu. Atsogoleri a Chikristu Chadziko samasonyeza ulemerero wa Yehova Mulungu koma amangodziwonetsera kotero kuti awonekere kwa onse. Ulemererowo suuli ulemerero wathu, ndipo sitifunikira kudziveka zovala zamtengo wapatali za atsogoleri achipembedzo za silika, za golidi, ndi majuwelo onyezimira. Ulemerero weniweni umachokera kumzimu wa Mulungu ndipo umasonyezedwa mwa kupereka umboni wa ulemerero wa Yehova, Mzimuyo.
Onyamula kuunika Onse Odalitsidwa
8, 9. Kodi Paulo akutipatsa chirimbikitso chotani pa 2 Akorinto 4:1, 2, ndipo timafunikira chitsimikizo chotani?
8 Pa 2 Akorinto 4:1, 2, timaŵerenga kuti: “Chifukwa chake popeza tiri nawo utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka; koma takaniza zobisika zamanyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga; koma ndi mawonekedwe a chowonadi tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.” Mulungu watichitira chifundo potigaŵira uminisitala umenewu. Ichi nchisonkhezero chotirimbikitsa kupitirizabe molimba mtima, ndipo tidzaterodi! Popeza kuti talandira kuunika kwa Mawu a Mulungu, tiri ndi thayo la kukuŵalitsira kwa ena.—Yerekezerani ndi Mateyu 5:14-16.
9 Zinthu zimene anthu akuchita nazo manyazi, zonga ngati chinyengo, amazibisa mwakunama ndi uphyuta. Koma ife tiribe chochitira manyazi chifukwa chakuti uthenga wathu ndi ntchito siziri zachinyengo koma zolungama ndi zowona. Motero, tiyenera kuŵalitsira ulemerero wokwanira wa kuunikako. Sitikuchita nawo mwachinyengo Mawu a Mulungu. Kutero kukatanthauza kuchita nawo mwadyera kaamba ka geni lathu, ulemerero, kupindula, ndi mphamvu ya dziko ndi kufuna kuzemba chitsutso ndi chizunzo zochokera kudziko. Awo amene samawopa kufikira Yehova ndi nkhope zosaphimbidwa ndikuyang’ana kuŵala kwaulemerero kwa chowonadi mofananamo sadzawopa kusenza thayo lawo. Iwo adzalola kuunika kuŵala kuchokera kwa iwo.
10. Kodi nchifukwa ninji suuli mlandu wa Mboni za Yehova ngati uthenga wabwino wa Ufumu uphimbidwa kwa anthu ena?
10 Ngati alionse aphimbidwa kusawona uthenga wabwino wa Ufumu, suuli mlandu wa Mboni za Yehova koma uli mlandu wawo. Mbiri yabwino ya Ufumu siikubisidwa. Ntchito ya Mboni za Yehova yolalikira ya padziko lonse njodziŵika bwino lomwe. Motero, izo zinganene monga momwe anachitira mtumwi Paulo kuti: “Ichi sichinachitika m’tseri.” Ndithudi, monga mmene iye analembera, mbiri yabwino yalalikidwa mu “chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”—Machitidwe 26:26; Akolose 1:23.
11. Kodi nchifukwa ninji mbiri yabwino yaulemerero iri yophimbidwa kwa anthu ambiri?
11 Amene uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu wabisidwa kwa iwo ali otsutsa, ochititsidwa khungu ndi Mdyerekezi. (Yerekezerani ndi Mateyu 12:30.) Iwo ayenera kuonjoka kuchipembedzo chonyenga ndi misampha ya Mdyerekezi, apo phuluzi, ali panjira ya kuchiwonongeko. Pansi pa chisonkhezero chauchiwanda, anthu oterowo amaika chophimba pamaso pawo penipeni, popeza kuti mtumwi Paulo amati pa 2 Akorinto 4:3-5: “Koma ngatinso uthenga wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutaika; mwa amene mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisaŵaŵalire. Pakuti tilalikira sizaife tokha, koma Kristu Yesu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Kristu.”
12. Mosiyana ndi ochititsidwa khungu mwamaganizo, kodi anthu a Yehova amalabadira motani mawu a pa 2 Akorinto 4:6?
12 Ochititsidwa khungu m’maganizo safuna kukhulupirira. Kusakhulupirira kwawo kumatsegulira maganizo awo kuukiridwa ndi ziŵanda. (1 Timoteo 4:1) Iwo sangawone ulemerero wa Yehova kapena kuŵala kwake kwa kunyezimira kwa Yesu, Mose Wamkulu. Anthu a Yehova amapeza kuunika kwaulemerero kuchokera m’Baibulo ndikukuŵalitsa kwa ena. Motero atumiki a Mulungu onse ali zounika, ndipo Mulungu amalamulira kuunikako kuti kuŵale. Kuunikako kuyenera kuŵala kuchokera kwa anthu a Mulungu ndi kukuunikira pa ena okhala mumdima ndi ngozi ya chiwonongeko. Izi ziridi monga momwe 2 Akorinto 4:6 akunene kuti: “Pakuti Mulungu amene anati, kuunika kudzaŵala kutuluka mumdima, ndiye amene anaŵala m’mitima yathu kutipatsa chiŵalitsiro cha chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.” Chifukwa cha zimenezi, Mboni za Yehova zimamvera lamulo laumulungu ndi kulola kuunika kwawo kuŵalira pa ena, kuulemerero wa Mulungu.
Chuma Chaulemerero m’Zotengera Zofooka
13. Kodi nzotulukapo zotani za utumiki wodalitsika wa kukhala ndi mwaŵi wonyamula kuunika pa zolengedwa zaumunthu?
13 Posenza mwaŵi wautumiki waukulu wosaneneka umenewu, nkofunika koposa kuti onyamula kuunika atsimikizire kukhala oyenerera kunyamula kuunikako mwakusunga umphumphu wawo kwa Mulungu. Kusamalira mwaŵi wapadera wa utumiki umenewu, Mulungu sanagwiritsire ntchito angelo oyera, omwe amakhumbira kusuzumira m’zinthu zimenezi, koma iye wapereka utumiki wodalitsidwa umenewu kwa zolengedwa zanyama. (1 Petro 1:12) Iye wachita chimenechi kaamba ka kulemekezedwa kwa mphamvu yake mwa anthu ofooka. Monga mmene 2 Akorinto 4:7 akunenera kuti: “Koma tiri nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.”
14. (a) Kodi “chuma ichi m’zotengera zadothi” nchiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji Mose ndi Yesu Kristu ali zitsanzo zanzeru kwa ife ponena za chumacho?
14 M’nthaŵi zakale zotengera zinagwiritsiridwa ntchito monga nsupa zosungiramo chuma. Kodi nchiyani chimene chiri chuma chaulemerero chomwe Mboni za Yehova ziri nacho m’zotengera zofooka, zadothi—iwo eni, monga zolengedwa zosalimba za fumbi lanthaka? Chuma chimenechi sichiri kokha kuunika kumene kwaŵalitsidwa m’mitima yawo. Icho ndicho uminisitala wa kuunika kumeneko, uminisitala, kapena utumiki, umene uyenera kusonyezedwa m’matupi awo anthaka. Uminisitalawo ndiwo kutumizidwa kwa kuunika kumene Mulungu waŵalitsa pamitima yawo. Uminisitala umenewu uli chuma chabwino kwakuti wakhala mwaŵi wamtengo wapatali wa utumiki umene okhalamo ndi phande samakhala otsalira odzozedwa okha a “kagulu ka nkhosa” komanso ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. (Luka 12:32; Yohane 10:14-16; Chivumbulutso 7:9) Mose ndi amene anaphiphiritsira, Yesu Kristu, ali zitsanzo zathu zanzeru, kuti tisumike mitima yathu pa chuma chimenechi chautumiki waumulungu, “pakuti kumene kuli chuma chako, komweko udzakhala mtima wakonso.”—Mateyu 6:19-21; Ahebri 11:26.
15, 16. (a) Kodi ndimotani mmene mphamvu yoposa yachibadwa ikusonyezedwera kukhala yochokera kwa Mulungu ndipo osati yochokera kwa ife? (b) Kodi nchifukwa ninji chitsutso chonse cha dziko chidzalephera kuswa zotengera za Mulungu zadothi?
15 Pamenepa, kodi ndimotani mmene mphamvu yoposa yachibadwa ikusonyezedwera kukhala yochokera kwa Mulungu osati mwa ife eni? Mwanjira iyi: Zotengera zofooka zadothi, monga ife amene tiri ndi utumiki ndi ntchito yapadera imeneyi ndife osayenerera ndipo sitikadakhala konse ndi ulemu woterowo mwa ife tokha. Ndiponso, ife Mboni za Yehova ndife mikhole yachipsinjo cha mitundu yonse cha adani oyesa kutiswa kuti tisayenerere kusenza ntchito imeneyo yochokera kwa Mulungu. Motero, iyenera kukhala mphamvu ya Wopereka Ntchito Wamkuluyo imene imatithandiza kulaka kuchitiridwa moipa ndi dziko lino ndi kugwiritsitsa mwamphamvu ntchitoyo ndi kutsimikizira kukhala oyenerera kukhalabe muutumiki wake. Motero, chitsutso chonse cha dziko chidzalephera kuswa zotengera zadothi za Mulungu ndi kuzilanda chuma chawo chamtengo wapatali, pakuti kwalembedwa pa 2 Akorinto 4:8-12 kuti:
16 “Ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osawonongeka; nthaŵi zonse tiri kusenzasenza m’thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi mwathu. Pakuti ife amene tiri ndi moyo tiperekeka ku imfa nthaŵi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi lathu lakufa. Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo [kupyolera mwa kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu] mwa inu.”
Khamu Lalikulu Limaŵerengera “Chuma Ichi” Kukhala Chamtengo Wapatali
17. Kodi ndimotani mmene khamu lalikulu limachiŵerengerera “chuma ichi” cha uminisitala waulemerero?
17 “Imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu.” Mawu amenewa amagwira ntchito kwa Akristu odzozedwa ndi mzimu. Chikhalirechobe, angatichititsedi kulingalira za unansi wa otsalira odzozedwa a Mulungu ndi khamu lalikulu la nkhosa zina. Odzozedwawo amadziŵa kuti pomalizira pake ayenera kumaliza njira yawo ya moyo wa padziko lapansi monga momwe Yesu anachitira, koma ali ndi atsamwali ogaŵana nawo chuma chaulemerero cha utumikicho, kuwathandiza mwakuchita mbali yaikulu ya kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu. Mofanana ndi otsalira odzozedwawo, khamu lalikulu la nkhosa zina lerolino limadziŵa kuti chuma chokha chimene chidzapulumuka nkhondo yoyaka moto ya Armagedo ndi kuloŵa m’dziko latsopano popanda kutenthedwa kapena kuŵaulidwa ndicho chuma chimenechi cha uminisitala wodalitsidwa, utumiki kwa Yehova Mulungu ndi Mfumu yake yaulemerero, Yesu Kristu. Khamu lalikulu siridzaleka konse kutumikira, “[Mulungu] usana ndi usiku m’kachisi mwake.”—Chivumbulutso 7:15.
18. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitika posachedwapa kuulemerero wonama wa dziko lino? (b) Kodi ‘ndiulemerero’ wotani umene Yesu anakana, ndipo iye anapeza ulemerero wopambana mwakuchitanji?
18 Mwamsanga, Mulungu adzathetsa ulemerero wonama wa dongosolo la zinthu loipa liripoli—“ulemerero” umene wapitirizabe chiyambire pamene Satana Mdyerekezi anatengera Yesu paphiri lalitali ndi kumsonyeza maulamuliro onse a dziko ndi “ulemerero wawo.” (Luka 4:5, 6) Yesu anakana chopereka chaulemerero chochokera kumagwero oterowo ndipo anatsatirabe njira ya kachitidwe yovomerezedwa ndi Mulungu padziko lapansi. Kaamba kochita motero, iye akalemekezedwa ndi ulemerero wokwezeka woposa ngakhale ulemerero umene iye, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, anali nawo kumwamba asanasenze gawo lake la padziko lapansi lolinganizidwa ndi Yehova.—Yohane 5:36; 17:5; Afilipi 2:9-11.
19. Kodi ndimwaŵi wautumiki wolemekezeka wotani umene ukuyandikira kukwaniritsidwa kwake kotheratu, ndipo chitsimikizo chathu nchotani ponena za nkhaniyi?
19 Chimaliziro chonenedweratu cha dongosolo lazinthu lauchiŵanda liripoli sichidza umboni wa Ufumu usanaperekedwe padziko lonse lapansi monga chimake chotheratu cha ntchito ya atsatiri a Yesu Kristu, Mboni za Yehova. (Mateyu 24:14) Umboni wa Ufumu tsopano wakhala ukuperekedwa kwa mbali zitatu mwa zinayi za zaka zana limodzi, ndipo monga kwasonyezedwa ndi zochitika za dziko za m’nthaŵi zathu, chimaliziro chonenedweratucho chiyenera kukhala pafupi. Motero, mwaŵi wolemekezeka wa kukhala ndi phande muuminisitala wa boma lachifumu loyera, uyenera kukhala ukuyandikira kukwaniritsidwa kwake kotheratu. (Mateyu, machaputala 24, 25; Marko, chaputala 13; Luka, chaputala 21) Mwaŵi wathu wa kutengamo mbali m’kupereka umboni wa padziko lonse wonena za Ufumu wokhazikitsidwa ulidi chuma chaulemerero chimene Mboni za Yehova, monga atsatiri a Mwana wake wopatsidwa ufumu, Yesu Kristu, amachiwona kukhala chamtengo wapatali. Iwo alidi ndi chikhumbo chowona mtima chakufuna kumamatira ku uwo kufikira umboni wa Ufumu utamalizidwa ndipo Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, afupa mkhalidwe wa chilengedwe chonse ndi umboni wake waumwini ku Ufumu wake wachilengedwe chonse.—Zefaniya 3:8.
Kodi Ndiati Ali Mayankho Anu?
◻ Kodi nchifukwa ninji uminisitala wa Mboni za Yehova uli waulemerero?
◻ Kodi nchifukwa ninji mbiri yabwino iri yophimbidwa kwa ambiri lerolino?
◻ Kodi “chuma ichi m’zotengera zadothi” nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu wagwiritsira ntchito zotengera zofooka ndizadothi, kaamba ka utumiki wake wamtengo wapatali?
◻ Kodi anthu a Yehova amachiŵerengera motani “chuma ichi,” ndipo chifukwa ninji?
[Chithunzi patsamba 17]
Ulemerero wa Mulungu umasonyezedwa ndi kunyezimira kwa Yesu Kristu, Mose Wamkuluyo. Mboni za Yehova ziri ndi mwaŵi wakutenga kuunika kwa ulemerero wa Mulungu kuchokera m’Baibulo ndi kumakuŵalitsira kwa ena