Tiziyamikira ‘Mphatso Yaulere’ Imene Mulungu Anatipatsa
“Tikuyamika Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.”—2 AKOR. 9:15.
1, 2. (a) Tchulani ‘mphatso yaulere’ imene Mulungu anatipatsa. (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?
YEHOVA anasonyeza kuti amatikonda kwambiri pamene anatumiza Mwana wake padzikoli. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9, 10) Mtumwi Paulo ananena kuti pochita zimenezi, Mulungu anatipatsa ‘mphatso yaulere imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.’ (2 Akor. 9:15) N’chifukwa chiyani ananena zimenezi?
2 Paulo ankadziwa kuti zonse zimene Mulungu analonjeza zidzakwaniritsidwa chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Werengani 2 Akorinto 1:20.) Ndiye ponena kuti ‘mphatso yaulere,’ ankatanthauza zinthu zonse zabwino zimene Mulungu angatipatse kudzera mwa Yesu. Mphatsoyi ndi yaikulu kwambiri moti anthufe sitingathe kuifotokoza bwinobwino. Ndiye kodi tiyenera kumva bwanji tikaganizira za mphatso yamtengo wapataliyi? Nanga kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatsoyi tikamakonzekera Chikumbutso cha imfa ya Khristu chimene chidzachitike Lachitatu pa 23 March, 2016?
MPHATSO YAPADERA YOCHOKERA KWA MULUNGU
3, 4. (a) Kodi mumamva bwanji munthu wina akakupatsani mphatso? (b) Kodi mungafune kuchita chiyani mutalandira mphatso yaikulu kwambiri?
3 Munthu akapatsidwa mphatso amasangalala ndiponso kuyamikira. Mphatso zina zimakhala zapadera kwambiri moti zingachititse kuti moyo wa munthu usinthe. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwapezeka wolakwa pa mlandu waukulu ndipo mwaweruzidwa kuti muphedwe. Koma kenako munthu wina amene simukumudziwa, akudzipereka kuti aphedwe m’malo mwa inu. Kodi mungamve bwanji?
4 N’zoonekeratu kuti mungayamikire kwambiri munthuyo ndipo zingakuchititseni kuganiza zosintha zimene mumachita. N’kutheka kuti zingakuchititseni kukhala ndi mtima wopatsa, kusonyeza ena chikondi komanso kukhululukira amene akulakwirani. Mosakayikira, simungadzaiwale zimene munthuyo anakuchitirani.
5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti nsembe imene Mulungu anapereka ndi mphatso yaikulu kuposa mphatso ina iliyonse?
5 Zimene Yehova anatichitira ndi zazikulu kwambiri kuposa zimene munthu wa m’chitsanzochi anachita. (1 Pet. 3:18) Tikutero chifukwa chakuti tonse ndife ochimwa ndipo timayembekezera kufa. (Aroma 5:12) Koma chifukwa chotikonda, Yehova anakonza kuti Yesu abwere padzikoli n’cholinga choti “alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.” (Aheb. 2:9) Choncho Yehova anakonza zoti adzathetseretu imfa. (Yes. 25:7, 8; 1 Akor. 15:22, 26) Aliyense amene amakhulupirira Yesu adzalandira moyo wosatha. Anthu ena adzakhala ndi moyo wosangalala komanso wamtendere padziko lapansi pano n’kumalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo odzozedwa adzapita kumwamba kukalamulira limodzi ndi Yesu. (Aroma 6:23; Chiv. 5:9, 10) Koma kodi ndi madalitso ena ati amene ndi mbali inanso ya mphatsoyi?
6. (a) Kodi inuyo mukulakalaka kudzaona zinthu ziti zitakwaniritsidwa? (b) Tchulani zinthu zitatu zimene tingachite posonyeza kuyamikira chikondi cha Mulungu.
6 Mulungu adzaukitsa akufa, adzathetsa matenda onse komanso kukonza dzikoli kuti likhale paradaiso. (Yes. 33:24; 35:5, 6; Yoh. 5:28, 29) Madalitso onsewa ndi mbali ya mphatso yaulere imene Mulungu watipatsa. N’zodziwikiratu kuti tonsefe timakonda Yehova ndiponso Mwana wake chifukwa chotipatsa mphatsoyi. Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira chikondi chimene Mulungu anatisonyezachi? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tingachite posonyeza kuti timayamikira Mulungu. (1) Tiziyesetsa kutsanzira Yesu mosamala kwambiri. (2) Tizisonyeza kuti timakonda abale athu. (3) Tizikhululukira ena ndi mtima wonse.
KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TIMAYAMIKIRA CHIKONDI CHA KHRISTU?
7, 8. Kodi munthu amene amayamikira chikondi cha Yesu amafunitsitsa kuchita chiyani?
7 Choyamba, tiyenera kuchita zinthu zimene mtumwi Paulo ananena. Iye anati “chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza” kuchita zimene Khristuyo angasangalale nazo. (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Paulo ankadziwa kuti munthu akamayamikira chikondi chimene Yesu anasonyeza, amayamba kukonda kwambiri Yesuyo. Tikamaganizira ndi kumvetsa bwino zimene Yehova anatichitira, timayamikira kwambiri chikondi chake. Komanso timafunitsitsa kukhala ndi moyo wogwirizana ndi zimene Yesu amafuna. Koma kodi tingasonyeze bwanji zimenezi?
8 Popeza timakonda Yehova, timayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yesu mosamala kwambiri komanso kuchita zimene Mulungu ndi Khristu amafuna. (1 Pet. 2:21; 1 Yoh. 2:6) Yesu anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.”—Yoh. 14:21; 1 Yoh. 5:3.
9. Kodi tiyenera kusamala ndi chiyani?
9 Nyengo ya Chikumbutso ndi nthawi yabwino kuganizira kwambiri zinthu zimene timachita. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene ndimachita bwino potsanzira Yesu? Nanga ndi zinthu ziti zimene ndiyenera kusintha?’ Tiyenera kudzifunsa mafunso amenewa chifukwa nthawi zonse timakakamizidwa kutsatira zimene anthu a m’dzikoli amachita. (Aroma 12:2) Ngati sitingasamale, tikhoza kuyamba kutsatira anthu am’dzikoli amene amaoneka anzeru, otchuka kapena akatswiri amasewera. (Akol. 2:8; 1 Yoh. 2:15-17) Kodi tingapewe bwanji zimenezi?
10. Kodi ndi mafunso ati amene tingadzifunse pa nyengo ya Chikumbutso ino, ndipo zimenezi zingatithandize bwanji? (Onani chithunzi patsamba 12.)
10 Pa nyengo ya Chikumbutso tingachitenso bwino kuona zinthu zomwe tili nazo. Mwachitsanzo, tingaone bwinobwino zovala zathu ndiponso nyimbo ndi mafilimu amene tili nawo. Ndi bwinonso kuona zinthu zimene timasunga pakompyuta, pafoni kapena patabuleti yathu. Mukamayang’ana zovala zanu muzidzifunsa kuti: ‘Zitakhala kuti Yesu alipo, kodi ndikhoza kucheza naye momasuka nditavala zovala zimenezi?’ (Werengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) ‘Ndikavala zovala zimenezi, kodi anthu amazindikira kuti ndine wotsatira wa Yesu?’ Pa nkhani ya mafilimu, nyimbo komanso zipangizo zamakono, tingadzifunsenso mafunso ngati awa: ‘Kodi Yesu angaonere filimu kapena kumvera nyimbo imeneyi? Kodi ndikhoza kumubwereka foni kapena tabuleti yanga ndi kumulola kuti aone zimene ndinaikamo?’ Ndipo ngati mumakonda masewera apakompyuta, mungadzifunsenso kuti: ‘Kodi ndingavutike kufotokozera Yesu chifukwa chimene ndimakondera masewera amenewa?’ Ngati timakonda kwambiri Yehova, tidzataya chilichonse chimene Khristu sangasangalale nacho, ngakhale zitakhala kuti tinachigula modula. (Mac. 19:19, 20) Pamene tinkadzipereka kwa Yehova tinamulonjeza kuti sitidzachitanso zofuna zathu koma za Mwana wake. Choncho sitiyenera kukakamira chilichonse chimene chingatilepheretse kutsatira mosamala chitsanzo cha Yesu.—Mat. 5:29, 30; Afil. 4:8.
11. (a) Kodi tingachite chiyani pa ntchito yolalikira chifukwa chokonda Yehova ndiponso Yesu? (b) Kodi chikondi chingatichititse kuthandiza bwanji anthu ena mumpingo?
11 Chifukwa chokonda kwambiri Yesu, timagwiranso mwakhama ntchito yolalikira. (Mat. 28:19, 20; Luka 4:43) Pa nthawi ya Chikumbutso timakhala ndi mwayi wochita upainiya wothandiza wamaola 30 kapena 50. Kodi mungayambiretu kukonza zinthu kuti mudzachite nawo utumikiwu? M’bale wina wazaka 84 amene mkazi wake anamwalira, ankaganiza kuti sangathe kuchita upainiya wothandiza chifukwa chakuti ndi wachikulire komanso amadwaladwala. Komabe apainiya ena amumpingo wawo anamuthandiza. Apainiyawa ankamutenga pa galimoto yawo akamapita mu utumiki komanso anasankha gawo loti m’baleyu akhoza kuyenda bwinobwino. Pa mapeto pake, m’baleyo anakwanitsa kuchita nawo upainiya wamaola 30. Kodi inunso mukhoza kuthandiza winawake mumpingo wanu kuti achite nawo upainiya wothandiza pa nyengo ya Chikumbutso? N’zoona kuti si tonse amene tingakwanitse kuchita upainiya. Komabe tikhoza kuchita zonse zimene tingathe pa ntchito yolalikira. Tikadzachita zimenezi tidzasonyeza kuti tikutsanzira mtumwi Paulo amene ankayamikira kwambiri chikondi cha Khristu. Koma kodi chikondi cha Mulungu chingatithandizenso kuchita chiyani?
TIYENERA KUKONDANA
12. Kodi chikondi cha Mulungu chimatithandizanso kuchita chiyani?
12 Chachiwiri, chikondi cha Mulungu chiyenera kutichititsanso kukonda abale athu. Paja mtumwi Yohane analemba kuti: “Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda chonchi, ndiye kuti ifenso tiyenera kukondana.” (1 Yoh. 4:7-11) Ngati timayamikiradi chikondi cha Mulungu, tiyenera kukonda abale athu. (1 Yoh. 3:16) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timawakonda?
13. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yokonda ena?
13 Chitsanzo cha Yesu chingatithandize pa nkhaniyi. Ali padzikoli, ankaganizira kwambiri anthu onyozeka. Ankathandiza anthu olumala, osaona, osamva ndiponso osalankhula. (Mat. 11:4, 5) Yesu ankasangalala kuphunzitsa anthu omwe atsogoleri a chipembedzo chachiyuda ankawaona ngati ‘otembereredwa.’ (Yoh. 7:49) Iye ankakonda kwambiri anthuwo ndipo ankayesetsa kuwathandiza.—Mat. 20:28.
14. Kodi inuyo mungachite chiyani posonyeza kuti mumakonda abale ndi alongo anu?
14 Pa nthawi ya Chikumbutso tingachitenso bwino kuganizira kwambiri abale ndi alongo amumpingo wathu n’kuona ngati pali ena amene tingawathandize. Mwachitsanzo mwina mumpingo wathu muli abale ndi alongo achikulire. Tikhoza kupita kunyumba kwawo kukawachezera, kukawaphikira komanso kuwathandiza ntchito zina zapakhomo. Tikhozanso kuwathandiza kufika kumisonkhano kapena kuyenda nawo mu utumiki. (Werengani Luka 14:12-14.) Tikamaganizira mmene Mulungu amatikondera timafunitsitsa kusonyeza chikondi kwa abale athu.
TIZICHITIRA CHIFUNDO ABALE NDI ALONGO ATHU
15. Kodi tonsefe tiyenera kukumbukira chiyani?
15 Chachitatu, chikondi cha Yehova chiyenera kutichititsa kuti tizikhululukira abale ndi alongo athu. Tonsefe tinatengera uchimo ndiponso imfa kwa Adamu. Choncho palibe amene anganene kuti nsembe ya Yesu ndi yosafunika kwa iye. Ngakhale munthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika kwambiri amafunika nsembe ya Khristu imene Mulungu anatipatsa. Tonsefe tiyenera kukumbukira kuti Mulungu anatikomera mtima kwambiri potikhululukira machimo athu ndipo zili ngati anatikhululukira ngongole yaikulu. Fanizo lina la Yesu lingatithandize kumvetsa kufunika kokumbukira zimenezi.
16, 17. (a) Kodi tingaphunzire chiyani m’fanizo la Yesu lonena za mfumu ndi akapolo? (b) Kodi mukaganizira fanizo la Yesu, mukufunitsitsa kuchita chiyani?
16 Yesu ananena fanizo la mfumu ina imene inakhululukira kapolo wake ngongole ya matalente 10,000 kapena kuti madinari 60 miliyoni. Koma chodabwitsa n’chakuti kapoloyu analephera kukhululukira mnzake ndalama zochepa kwambiri zokwana madinari 100 zokha. Mfumuyo itamva zimenezi, inakwiya kwambiri n’kumuuza kuti: “Kapolo woipa iwe, ine ndakukhululukira ngongole yonse ija utandidandaulira. Kodi nawenso sukanam’chitira chifundo kapolo mnzako, monga momwe ine ndinakuchitira chifundo?” (Mat. 18:23-35; onani Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu, 18-B.) Kapoloyu akanaganizira chifundo chachikulu chimene mfumu ija inamuchitira, akanathanso kukhululukira mnzakeyo. Kodi ifenso tikaganizira chikondi ndiponso chifundo cha Yehova tingafune kuchita chiyani?
17 Pa nthawi ya Chikumbutso tingachite bwino kudzifufuza kuti tione ngati tikusungira zifukwa abale ndi alongo athu ena. Nthawiyi ndi yabwino kwambiri kuti titsanzire Yehova amene amakhala “wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5; Neh. 9:17) Ngati timayamikira kuti Yehova anatikhululukira ngongole yaikulu, timafunanso kukhululukira ena ndi mtima wonse. Yehova sangatikonde komanso kutikhululukira ngati sitikonda ndiponso kukhululukira anzathu. (Mat. 6:14, 15) N’zoona kuti kukhululukira ena sikungasinthe zimene anatilakwirazo, koma kungatithandize kuti tikhale ndi tsogolo labwino.
18. Kodi kuyamikira chikondi cha Mulungu kunathandiza bwanji mlongo wina amene ankasamalira mlongo wamasiye?
18 Nthawi zambiri, ‘kulolera ndi kukhululukira’ abale ndi alongo athu si kophweka. (Werengani Akolose 3:13, 14; Aefeso 4:32.) Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Lily anadzipereka kuti azithandiza mlongo wina wamasiye.[1] Ankamutenga pa galimoto akafuna kupita kwinakwake komanso ankamuchitira zinthu zina zambiri. Ngakhale kuti Lily ankamuthandiza kwambiri, mlongoyu anali wovuta komanso ankaoneka kuti sankayamikira zimene Lily ankamuchitira. Komabe Lily ankayesetsa kuganizira zinthu zabwino zimene mlongo ameneyu ankachita. Anapitirizabe kumuthandiza kwa zaka zambiri mpaka pamene mlongoyo anadwala kwambiri n’kumwalira. Lily ananena kuti: “Ngakhale kuti zinthu zinali choncho, ndikufunitsitsa kuti ndidzamuonenso akadzaukitsidwa. Ndikufuna ndidzaone mmene azidzachitira zinthu akadzakhala wangwiro.” Ngati timayamikira chikondi chimene Mulungu amatisonyeza timatha kukhululukira abale ndi alongo athu n’kumayembekezera nthawi imene tonse tidzakhale angwiro.
19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mphatso yaikulu imene Mulungu anatipatsa?
19 Taona kuti Yehova anatipatsadi mphatso yamtengo wapatali kwambiri ndipo tiyenera kuiyamikira nthawi zonse. Choncho pa nthawi ya Chikumbutso tiyeni tiziganizira ndiponso kuyamikira kwambiri zonse zimene Yehova ndi Yesu anatichitira. Tizisonyezanso kuti timayamikira chikondi chimenechi poyesetsa kukonda abale athu ndiponso kuwakhululukira ndi mtima wonse.
^ [1] (ndime 18) Mayina ena m’nkhaniyi asinthidwa.