Timasangalala Kwambiri Kugwira Ntchito Limodzi ndi Mulungu
“Pamene tikugwira naye ntchito limodzi, tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.”—2 AKOR. 6:1.
1. Ngakhale kuti Yehova ndi wamkulu m’chilengedwe chonse, kodi amapereka mwayi wotani kwa ena?
YEHOVA ndi wamkulu m’chilengedwe chonse, ndi Mlengi wa zinthu zonse komanso ali ndi nzeru ndiponso mphamvu zopanda malire. Yobu anazindikira zimenezi moti Yehova atamufunsa zokhudza zimene analenga, anayankha kuti: “Ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse, ndipo palibe zimene simungakwanitse.” (Yobu 42:2) Yehova angathe kuchita chilichonse chimene akufuna popanda wina kumuthandiza. Komabe kuyambira kale, amapereka mwayi kwa ena kuti agwire naye ntchito limodzi pokwaniritsa cholinga chake.
2. Kodi Yehova anauza Yesu kuti agwire naye ntchito yotani?
2 Yehova analenga Mwana wake, Yesu, asanalenge china chilichonse. Kenako analola kuti Mwana wakeyo agwire naye ntchito yolenga zinthu zina zonse. (Yoh. 1:1-3, 18) Ponena za Yesu, mtumwi Paulo anati: “Kudzera mwa iye zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka, kaya ndi mipando yachifumu, kapena ambuye, kapena maboma, kapena maulamuliro. Zinthu zina zonse zinalengedwa kudzera mwa iye, ndiponso chifukwa cha iye.” (Akol. 1:15-17) Choncho Yehova anapatsa Yesu ntchito yoti agwire komanso anauza ena zimene Yesuyo anachita. Izi zikusonyeza kuti amaona kuti Mwana wakeyu ndi wofunika kwambiri.
3. Kodi Yehova anapatsa Adamu ntchito yotani, ndipo n’chifukwa chiyani?
3 Yehova anaperekanso mwayi kwa anthu kuti agwire naye ntchito. Mwachitsanzo, anauza Adamu kuti atchule mayina nyama zonse. (Gen. 2:19, 20) Adamu ayenera kuti anasangalala kwambiri kudziwa bwino nyamazo, kuona mmene zimachitira zinthu kenako n’kupeza dzina loyenera nyama iliyonse. Popeza Yehova ndi amene analenga nyamazo, akanatha kuzitchula yekha mayina. Koma anapatsa Adamu mwayi umenewu chifukwa chomukonda. Anamupatsanso ntchito yoti akonze dziko lonse kuti likhale Paradaiso. (Gen. 1:27, 28) Koma n’zomvetsa chisoni kuti Adamu sanafune kugwirabe ntchito ndi Mulungu. Zimene anachita zinabweretsa mavuto aakulu padziko lonse.—Gen. 3:17-19, 23.
4. Kodi anthu ena anagwira ntchito zotani pothandiza kukwaniritsa cholinga cha Mulungu?
4 Kenako Mulungu anaperekanso mwayi kwa anthu ena kuti agwire naye ntchito. Mwachitsanzo, Nowa anakhoma chingalawa ndipo chinathandiza kuti iye ndi banja lake apulumuke Chigumula. Mose anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo. Yoswa anatsogolera Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Solomo anamanga kachisi wa ku Yerusalemu. Komanso Mariya anabereka Yesu. Anthu onsewa ndiponso ena ambiri anagwira ntchito limodzi ndi Yehova pokwaniritsa cholinga chake.
5. (a) Kodi Yehova watipatsa mwayi wogwira ntchito iti? (b) Kodi Yehova sangathe kugwira ntchitoyi popanda ife? (Onani chithunzi patsamba 28.)
5 Masiku anonso Yehova watipatsa mwayi woti tigwire ntchito zosiyanasiyana zokhudza Ufumu wa Mesiya ndipo amafuna kuti tizichita zimenezi mwakhama. N’zoona kuti pali ntchito zina zimene Akhristu ena sangakwanitse kugwira. Koma tonse tikhoza kugwira nawo ntchito yolalikira. Yehova akanatha kugwira yekha ntchitoyi. Mwachitsanzo, akanatha kumalankhula ndi anthu yekha kuchokera kumwamba. Yesu ananenanso kuti Yehova akanatha kugwiritsa ntchito miyala kuti izifuula pouza anthu za Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Luka 19:37-40) Komabe Yehova watipatsa ifeyo mwayi woti tikhale “antchito anzake.” (1 Akor. 3:9) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene tikugwira naye ntchito limodzi, tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.” (2 Akor. 6:1) Timasangalala kwambiri kugwira ntchito ndi Mulungu ndipo timaona kuti ndi mwayi waukulu. Tiyeni tione chifukwa chake tikunena zimenezi.
TIKAMAGWIRA NTCHITO NDI MULUNGU TIMASANGALALA
6. Kodi Yesu ananena mawu ati osonyeza kuti ankasangalala kugwira ntchito ndi Atate wake?
6 Kuyambira kale, atumiki a Yehova akhala akusangalala kwambiri kugwira ntchito ndi Mulungu. Ponena za moyo wake asanabwere padzikoli, Yesu anati: “Yehova anandipanga monga chiyambi cha njira yake. . . . Ndinali pambali pake monga mmisiri waluso. Tsiku ndi tsiku, iye anali kusangalala kwambiri ndi ine. Ineyo ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (Miy. 8:22, 30) Yesu akamagwira ntchito ndi Atate wake ankasangalala chifukwa cha ntchito imene ankagwirayo komanso chifukwa chodziwa kuti Atatewo amamukonda. Ifenso tikamagwira ntchito ndi Mulungu timasangalala.
7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yolalikira imatithandiza kukhala osangalala?
7 Yesu ananena kuti munthu amasangalala akapatsidwa zinthu komanso akapatsa ena zinthu. (Mac. 20:35) Choncho pamene munthu wina anatiphunzitsa mfundo za m’Baibulo tinasangalala kwambiri. Timasangalalanso tikamauza ena zimene tinaphunzirazo. Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, ena amasangalala kwambiri chifukwa amayamba kudziwa Mulungu ndiponso kumvetsa mfundo za m’Mawu ake. Ifenso timasangalala kuona kuti anthuwo akusintha mmene amaganizira komanso zochita zawo. Izi zimatithandiza kuzindikira kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Ntchitoyi imathandiza anthu kuti agwirizanenso ndi Mulungu ndiponso kuti adzapeze moyo wosatha. (2 Akor. 5:20) Choncho palibe ntchito yosangalatsa kwambiri kuposa yolalikira chifukwa imathandiza kuti anthu adzakhale ndi moyo wosatha.
8. Kodi anthu ena ananena zotani zokhudza kugwira ntchito ndi Mulungu?
8 Timasangalala tikathandiza munthu kuti adziwe Mulungu. Timasangalalanso podziwa kuti Yehova akusangalala kuti tikugwira mwakhama ntchito yolalikira. (Werengani 1 Akorinto 15:58.) M’bale wina wa ku Italy dzina lake Marco anati: “Ndimasangalala kwambiri kutumikira Yehova ndi mtima wanga wonse, ndipo ndikudziwa kuti sangaiwale zimene ndimachita.” M’bale Franco, amene amakhalanso ku Italy, anati: “Yehova amagwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso zinthu zina potikumbutsa tsiku lililonse kuti amatikonda komanso kuyamikira zimene timachita pomutumikira. Mwina tingaone kuti zimene timachita n’zochepa koma Yehova amaona kuti n’zofunika kwambiri. N’chifukwa chake ndimasangalala kwambiri ndikamagwira ntchito limodzi ndi Mulungu.”
UBWENZI WATHU NDI MULUNGU UMALIMBA KOMANSO TIMAGWIRIZANA NDI AKHRISTU ANZATHU
9. Kodi panali ubwenzi wotani pakati pa Yehova ndi Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani?
9 Tikamagwira ntchito ndi anthu amene timawakonda, timayamba kuwadziwa bwino ndiponso kugwirizana nawo kwambiri. Timadziwanso zolinga zawo pa moyo komanso zimene akufuna kuchita kuti akwaniritse zolingazo. Yesu anagwira ntchito ndi Yehova kwa zaka mabiliyoni ambiri ndipo anayamba kukondana naye kwambiri. Yesu anati: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” (Yoh. 10:30) Izi zikusonyeza kuti iye ndi Atate wake ankagwirizana kwambiri ndipo ankasangalala kugwira ntchito limodzi.
10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yolalikira imatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu komanso kugwirizana ndi Akhristu anzathu?
10 Yesu anapempha Yehova kuti aziyang’anira ophunzira ake. Pofotokoza chifukwa chake, anati: “Kuti akhale amodzi mmene ife tilili.” (Yoh. 17:11) Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo komanso kugwira ntchito yolalikira, timayamba kuzindikira makhalidwe abwino a Mulungu. Timaonanso kuti zinthu zimatiyendera bwino tikamamukhulupirira komanso kutsatira malangizo ake. Tikamayesetsa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, nayenso amatiyandikira. (Werengani Yakobo 4:8.) Timayambanso kukondana kwambiri ndi abale ndi alongo athu. Zili choncho chifukwa timakhala ndi zolinga zofanana, timalalikira nawo limodzi, kusangalala nawo limodzi komanso timalimbikitsana tikakumana ndi mavuto. Mlongo wina dzina lake Octavia, yemwe amakhala ku Britain, anati: “Ndikamagwira ntchito ndi Yehova ndimayambanso kugwirizana kwambiri ndi Akhristu anzanga chifukwa tonse tikugwira ntchito yofanana ndiponso tili ndi cholinga chimodzi.” Kodi inunso mumakondana kwambiri ndi abale ndi alongo chifukwa choona kuti akuyesetsa kutumikira Yehova?
11. N’chiyani chidzatithandize kukonda kwambiri Yehova komanso Akhristu anzathu m’dziko latsopano?
11 M’dziko latsopano tidzakhala pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Mulungu komanso tizidzagwirizana kwambiri ndi Akhristu anzathu kuposa panopa. Tikutero chifukwa padzakhala ntchito yambiri komanso yosangalatsa imene tizidzagwira limodzi. Padzakhala ntchito yolandira komanso kuphunzitsa anthu amene adzaukitsidwe. Tidzafunikanso kukonza dzikoli kuti likhale paradaiso. Imeneyi idzakhala ntchito yaikulu, komabe tidzasangalala kwambiri kugwira ntchitoyi mogwirizana mpaka pamene tonse tidzakhale angwiro. Anthu onse azidzakondana kwambiri komanso kukonda Mulungu amene ‘adzakhutiritse zokhumba za chamoyo chilichonse.’—Sal. 145:16.
NTCHITO YOLALIKIRA IMATITETEZA
12. Kodi ntchito yolalikira imatiteteza bwanji?
12 Tonsefe tiyenera kuteteza ubwenzi wathu ndi Yehova. Popeza ndife ochimwa komanso tikukhala m’dziko la Satana, n’zosavuta kutengera maganizo ndiponso makhalidwe oipa a m’dzikoli. Tingayerekezere zinthu za m’dzikoli ndi mtsinje umene madzi ake akuyenda mwamphamvu. Kuti munthu awoloke, ayenera kusambira mwamphamvu mpaka kukafika kumtunda. Ifenso timafunika kuyesetsa kuti tisatengeke ndi zinthu za m’dzikoli. Ntchito yolalikira imatithandiza kuti tiziganizira zinthu zolimbikitsa osati zinthu zoipa zomwe zingatifooketse. (Afil. 4:8) Tikamalalikira timaganiziranso mfundo za Mulungu komanso zimene analonjeza ndipo izi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu. Ntchito yolalikira imatithandizanso kukhala ndi makhalidwe abwino omwe angatiteteze m’dziko loipali.—Werengani Aefeso 6:14-17.
13. Kodi m’bale wina ananena zotani zokhudza ntchito yolalikira?
13 Tikamatanganidwa ndi kulalikira ndiponso kuchita zinthu zina zokhudza kulambira, sitikhala ndi nthawi yoganizira kwambiri mavuto athu. M’bale wina wa ku Australia dzina lake Joel anafotokoza mmene kulalikira kumamuthandizira. Anati: “Ntchito yolalikira imandithandiza kudziwa zimene zikuchitika m’dzikoli. Ndikamalalikira ndimaona mavuto amene anthu akukumana nawo ndipo ndimazindikira kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kwandithandiza kwambiri pa moyo wanga. Ntchitoyi imandithandizanso kukhala wodzichepetsa komanso kuti ndizidalira Yehova ndi Akhristu anzanga.”
14. Kodi zimene timachita pa ntchito yolalikira zimasonyeza bwanji kuti mzimu wa Mulungu umatithandiza?
14 Ntchito yolalikira imatithandizanso kukhulupirira kwambiri kuti Mulungu amatipatsa mzimu wake. Tiyerekeze kuti mwapatsidwa ntchito yoti muzipita kunyumba za anthu am’dera lanu n’kumakagawa chakudya. Koma mukugwiritsa ntchito ndalama zanu pogwira ntchitoyi ndipo simukulandira malipiro. Ndiyeno pasanapite nthawi mukuona kuti anthu sakufuna kulandira chakudyacho ndipo ena akudana nanu chifukwa chowapititsira chakudya. Kodi mungapitirize kugwira ntchitoyi? Mwina mukhoza kukhumudwa n’kusiya. Komabe ambirife takhala tikulalikira kwa nthawi yaitali ngakhale kuti anthu ambiri amatitsutsa komanso kutinyoza. Ndipotu timachita zimenezi popanda kulandira ndalama iliyonse. Izi zikusonyezeratu kuti mzimu wa Mulungu umatithandiza.
TIMASONYEZA KUTI TIMAKONDA MULUNGU KOMANSO ANTHU ENA
15. Kodi ntchito yolalikira imathandiza bwanji kuti cholinga cha Mulungu chokhudza anthu chidzakwaniritsidwe?
15 Ntchito yolalikira imathandiza kuti cholinga cha Mulungu chokhudza anthu chidzakwaniritsidwe. Mulungu amafuna kuti anthu akhale ndi moyo wosatha padzikoli. Ngakhale kuti Adamu anachimwa, Yehova sanasinthe cholinga chakechi. (Yes. 55:11) Koma anakonza zoti anthu amasulidwe ku uchimo ndi imfa. Yesu anabwera padzikoli kudzapereka moyo wake kuti awombole anthu omvera. Komabe kuti munthu azimvera Mulungu, ayenera kudziwa zimene Mulunguyo amafuna. Choncho Yesu anaphunzitsa anthu zimene Mulungu amafuna ndipo anauza ophunzira ake kuti azichitanso zimenezi. Tikamalalikira, timakhala tikugwira ntchito ndi Mulungu pothandiza kuti anthu amasulidwe ku uchimo ndi imfa.
16. Kodi tikamalalikira timasonyeza kuti tikumvera malamulo awiri ati?
16 Tikamathandiza anthu kuti ayambe kuyenda pamsewu wopita ku moyo, timasonyeza kuti timawakonda komanso timakonda Yehova amene “chifuniro chake n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Munthu wina atafunsa Yesu lamulo lalikulu pa malamulo amene Aisiraeli anapatsidwa, Yesu anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” (Mat. 22:37-39) Choncho tikamalalikira timasonyeza kuti tikumvera malamulo awiri amenewa.—Werengani Machitidwe 10:42.
17. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira mwayi wathu wolalikira?
17 Ndi mwayi waukulu kwambiri kugwira ntchito ndi Mulungu. Yehova watipatsa ntchito imene imatithandiza kuti tizisangalala, tikhale naye pa ubwenzi wolimba, tizigwirizana ndi ena komanso imene imatiteteza. Ntchito yolalikira imatipatsanso mwayi wosonyeza kuti timakonda Mulungu komanso anthu. Atumiki a Mulungu ndi osiyanasiyana. Pali achinyamata, achikulire, olemera, osauka, amphamvu ndipo ena ndi ofooka. Koma onsewa amayesetsa kulalikira mwakhama. Mwina mungagwirizane ndi zimene mlongo wina wa ku France, dzina lake Chantel, ananena. Mlongoyu anati: “Ndimangomva ngati Yehova yemwe ndi wamkulu m’chilengedwe chonse, Mlengi wa zonse komanso Mulungu wachimwemwe akundiuza kuti: ‘Pita, kauze anthu za ine kuchokera pansi pa mtima. Ndakupatsa mphamvu, Mawu anga, angelo, abale ndi alongo ako komanso ndimakuphunzitsa mmene ungagwirire ntchitoyi.’ Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kuchita zimene Yehova amafuna komanso kugwira naye ntchito limodzi.”