Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga
‘Tulukani pakati pawo, . . . ati [Yehova, “NW”], Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; Ndipo ine ndidzalandira inu.’—2 AKORINTO 6:17.
1. Kodi ndikugulitsana kotani kumene Satana anafuna kuchita ndi Yesu, ndipo kodi ndizinthu ziŵiri ziti zimene chopereka chakechi chimatiphunzitsa?
‘ZONSE ndikupatsani inu, ngati mudzagwa pansi ndi [kuchita kachitidwe kakundilambira, NW].’ Ngakhale kuti choperekachi chinapangidwa zaka zikwi zambiri pambuyo pakuyambika kwa chipembedzo chonyenga, icho chimapereka mfungulo yodziŵira amene ali kumbuyo kwa kulambira konyenga ndi chimene chiri chifuno chake. Kumapeto kwa chaka cha 29 C.E., Mdyerekezi anapatsa Yesu maufumu onse apadziko mosinthana ndi kachitidwe kakulambira. Chochitikachi chimatiuza zinthu ziŵiri: kuti maufumu a dziko lino anali a Satana ndipo kunali kwa iye kuwapereka ndikuti cholinga chachikulu cha chipembedzo chonyenga ndicho kulambira Mdyerekezi.—Mateyu 4:8, 9.
2. Kodi timaphunziranji m’mawu a Yesu pa Mateyu 4:10?
2 Mwa yankho lake, Yesu sanangokana chipembedzo chonyenga komanso anasonyeza chimene chipembedzo chowona chimaloŵetsamo. Iye analengeza kuti: “Choka, Satana! Pakuti kwalembedwa, ‘Ndiye Yehova Mulungu wako amene uyenera kumlambira, ndipo ndi kwa iye yekha kumene uyenera kuperekako utumiki wopatulika.” (Mateyu 4:10, NW) Chotero, cholinga chachikulu cha chipembedzo chowona ndicho kulambiridwa kwa Mulungu yekha wowona, Yehova. Chimaphatikizapo chikhulupiriro ndi chimvero, kuchitidwa kwa chifuniro cha Yehova.
Chiyambi cha Chipembedzo Chonyenga
3. (a) Kodi nliti ndipo ndimotani mmene chipembedzo chonyenga chinayambira padziko lapansi? (b) Kodi ndikachitidwe kati koyamba kulembedwa ka nkhanza yachipembedzo, ndipo kodi ndimotani mmene kuzunza kwachipembedzo kwapitirizirabe chiyambire pamenepo?
3 Chipembedzo chonyenga chinayamba padziko lapansi pamene anthu oyamba sanamvere Mulungu nalandira lingaliro la Njoka lakudzisankhira “zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:5) Mwakutero iwo anakana ulamuliro wolungama wa Yehova ndikutaya kulambira koyenera, chipembedzo chowona. Iwo anali anthu oyamba omwe ‘anasandutsa chowonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo.’ (Aroma 1:25) Cholengedwa chomwe iwo mosafuna anasankha kuchilambira sichinali wina koma Satana Mdyerekezi, “njoka yokalambayo.” (Chibvumbulutso 12:9) Mwana wawo wamkulu, Kaini, anakana kutsatira uphungu wokoma mtima wa Yehova choncho anapandukira ulamuliro Wake. Modziŵa kapena ayi, Kaini anakhala “mwana wa woipayo,” Satana, ndi wolambira Mdyerekezi. Iye anapha mphwake Abele, yemwe analondola kulambira kowona, chipembedzo chowona. (1 Yohane 3:12, Revised English Bible; Genesis 4:3-8; Ahebri 11:4) Mwazi wa Abele unali mwazi woyamba kukhetsedwa chifukwa cha nkhanza yachipembedzo. Nzachisoni kuti, chipembedzo chonyenga chapitirizabe kukhetsa mwazi wopanda liŵongo kufikira m’tsiku lathu.—Onani Mateyu 23:29-35; 24:3, 9.
4. M’chochitika cha Nowa, kodi ndimalemba ati amene amafotokoza mwafanizo mkhalidwe wa chipembedzo chowona?
4 Chigumula chisanadze, Satana anapambana kupatutsa anthu ambiri pachipembedzo chowona. Komabe, Nowa, “anapeza ufulu pamaso pa Yehova.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “anayendabe ndi Mulungu.” M’mawu ena, iye analondola kulambira kowona. Chipembedzo chowona sichiri mwambo kapena dzoma koma njira ya moyo. Chimaloŵetsamo kukhulupirira Yehova ndi kumtumikira momvera, ‘kuyenda naye.’ Nowa anachita zimenezi.—Genesis 6:8, 9, 22; 7:1; Ahebri 11:6, 7.
5. (a) Kodi nchiyani chimene Mdyerekezi anayesa kukhazikitsa pambuyo pa Chigumula, ndipo motani? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova analepheretsera chiwembu cha Mdyerekezi, ndipo kodi chotulukapo chinali chiyani?
5 Pasanapite nthaŵi yaitali kwambiri pambuyo pa Chigumula, mwachiwonekere Mdyerekezi anagwiritsira ntchito Nimrode, mwamuna woipitsitsa “m’kutsutsana ndi Yehova,” poyesayesa kugwirizanitsa anthu onse mumpangidwe wa kulambira kumene kukakhalanso kotsutsana ndi Yehova. (Genesis 10:8, 9, NW; 11:2-4) Iko kukadakhala chipembedzo chonyenga chimodzi chogwirizana, kulambira Mdyerekezi kogwirizana, kozikidwa pamzinda ndi nsanja imene olambira ake anamanga. Yehova analepheretsa chiwembu chimenechi mwakusokoneza ‘chinenedwe chimodzi’ cholankhulidwa panthaŵiyo ndi anthu onse. (Genesis 11:5-9) Chifukwa chake, mzindawo unadzatchedwa Babele, pambuyo pake Babulo, maina onse aŵiriŵa otanthauza “Chisokonezo.” Chisokonezo chachinenero chimenechi chinapangitsa kumwazikana kwa anthu padziko lonse lapansi.
6. (a) Kodi ndimalingaliro achipembedzo otani amene anaikidwa m’maganizo mwa olambira Satana m’Babulo asanamwazikane? (b) Kodi nchifukwa ninji zipembedzo padziko lonse ziri ndi zikhulupiriro zofanana? (c) Kodi nchifuno chausatana chotani chimene Babulo anatumikira, ndipo kodi mzinda wamakedzana umenewo unadzaphiphiritsira chiyani?
6 Komabe, malinga ndi mbiri yakale ya nthanthi ndi chipembedzo, kukuwonekera kuti Yehova asanachititse kumwazikana kwa anthu kumeneku, Satana adaloŵetsa kale m’malingaliro a olambira ake mfundo zina zazikulu za chipembedzo chonyenga. Izi zinaphatikizapo malingaliro achipembedzo a kukhalapobe kwa moyo pambuyo pa imfa, kuwopa akufa, ndi kukhalapo kwa dziko lokhalako akufa, pamodzi ndi kulambira milungu ndi milungu yachikazi yambirimbiri, ina yomwe inaikidwa m’mautatu. Zikhulupiriro zoterozo zinafalitsidwa padziko lonse ndi magulu a zinenero zosiyanasiyana. M’kupita kwa nthaŵi, malingaliro aakulu ameneŵa anasinthasintha. Koma kwakukulukulu, iwo akupanga lukanelukane wa chipembedzo chonyenga m’mbali zonse za dziko. Ngakhale kuti zoyesayesa zake zakupanga chipembedzo chonyenga chimodzi chogwirizana chokhala ndi likulu lake m’Babulo zinalephera, Satana anayamba mitundu yosinayasiyana ya kulambira konyenga, imene inali ndi chisonkhezero Chachibabulo ndipo yokhala ndi cholinga chakupatutsa kulambira kukuchotsa kwa Yehova kumka kwa iyemwini. Babulo anapitiriza kwa zaka mazana ambiri kukhala chimake cha kulambira mafano, matsenga, kubwebweta, ndi kupenda nyenyezi—zonsezi zokhala mbali zazikulu zopanga chipembedzo chonyenga. Mosadabwitsa, bukhu la Chibvumbulutso limaphiphiritsa ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga kukhala mkazi wachigololo wonyansa wotchedwa Babulo Wamkulu.—Chibvumbulutso 17:1-5.
Chipembedzo Chowona
7. (a) Kodi nchifukwa ninji chipembedzo chowona sichinayambukiridwe ndi chisokonezo cha chinenero? (b) Kodi ndani amene anadzatchedwa “kholo la onse akukhulupira,” ndipo chifukwa ninji?
7 Mowonekeratu, chipembedzo chowona sichinakhudzidwe ndi kusokonezedwa kwa njira yolankhulira ya anthu pa Babele kumene Yehova anakuchita. Kulambira kowona kunalondoledwa Chigumula chisanadze ndi amuna ndi akazi okhulupirika onga, Abele, Enoke, Nowa, mkazi wa Nowa, ndi ana aamuna a Nowa ndi azipongozi ake. Pambuyo pa Chigumula kulambira kowona kunasungidwa mumzera wobadwira wa Semu, mwana wamwamuna wa Nowa. Abrahamu, mbadwa ya Semu, analondola chipembedzo chowona ndipo anadziŵika monga “kholo la onse akukhulupira.” (Aroma 4:11) Chikhulupiriro chake chinachirikizidwa ndi ntchito. (Yakobo 2:21-23) Chipembedzo chake chinali njira ya moyo.
8. (a) Kodi ndimotani mmene chipembedzo chowona chinayang’anizirana ndi chipembedzo chonyenga m’zaka za zana la 16 B.C.E., ndipo kodi panali chotulukapo chotani? (b) Kodi ndimakonzedwe atsopano otani amene Yehova anayambitsa ponena za kulambiridwa kwake koyera?
8 Kulambira kowona kunapitirizabe kulondoledwa mumzera wa mbadwa za Abrahamu—Isake, Yakobo (kapena, Israyeli), ndi ana aamuna 12 a Yakobo, kwa amene kunachokera mafuko 12 a Israyeli. Pofika kumapeto kwa zaka za zana la 16 B.C.E., mbadwa za Abrahamu kupyolera mwa Isake zinali kuchita mwamphamvu kusunga chipembedzo choyera m’malo achikunja ankhalwe—Igupto—kumene anatsitsidwa kukhala akapolo. Yehova anagwiritsira ntchito Mose, mtumiki wake wokhulupirika wa fuko la Levi, kumasula olambira Ake m’goli la Igupto, dziko lozama m’chipembedzo chonyenga. Kupyolera mwa Mose, Yehova anapanga pangano ndi Israyeli, akuwatenga kukhala anthu Ake osankhidwa. Panthaŵiyo, Yehova anakonza mpambo wa malamulo omlambirira, mwakanthaŵi akuuika kokha mkati mwa dongosolo la kupereka nsembe kochitidwa ndi ansembe m’malo opatulika akuthupi, poyamba chihema chokomanako chonyamulika ndiyeno pambuyo pake kachisi ku Yerusalemu.
9. (a) Kodi ndimotani mmene kulambira kowona kunachitidwira chipangano Chalamulo chisanakhale? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti zinthu zakuthupi za Chilamulo sizinali zokhaliratu?
9 Komabe, tiyenera kudziŵa kuti cholinga cha zinthu zakuthupi zimenezi sichinali chakuti zikhale mbali zokhaliratu za chipembedzo chowona. Chilamulo chinali “mthunzi wa zirinkudzazo.” (Akolose 2:17; Ahebri 9:8-10; 10:1) M’nthaŵi zamakolo akale, Chilamulo cha Mose chisanakhale, mwachiwonekere mitu ya banja inaimira mabanja awo popereka nsembe pamaguwa omwe anawamanga. (Genesis 12:8; 26:25; 35:2, 3; Yobu 1:5) Koma panalibe unsembe wolinganizidwa kapena dongosolo la kupereka nsembe, lokhala ndi miyambo ndi madzoma. Ndiponso, Yesu iyemwini anasonyeza kusakhaliratu kwa kulambira koima pa mpambo wa malamulo kozikidwa m’Yerusalemu pamene anauza mkazi Wachisamariya kuti: ‘Ikudza nthaŵi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri iri [Gerizimu, malo akale a kachisi Wachisamariya] kapena m’Yerusalemu. . . . Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano iripo, imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:21-23) Yesu anasonyeza kuti chipembedzo chowona chiyenera kulondoledwa, osati ndi zinthu zakuthupi, koma ndi mzimu ndi chowonadi.
Ukapolo wa ku Babulo
10. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova analola anthu ake kutengedwa muukapolo ku Babulo? (b) Kodi ndi m’njira ziŵiri ziti zimene Yehova anamasulira otsalira okhulupirika mu 537 B.C.E., ndipo kodi nchiyani chimene chinali chifuno chawo chachikulu chobwererera ku Yuda?
10 Chiyambire chipanduko cha m’Edene, pakhala chidani chosalekeza pakati pa chipembedzo chowona ndi chipembedzo chonyenga. Nthaŵi zina olambira owona, kunena m’mawu ophiphiritsira, atengedwa muukapolo ndi chipembedzo chonyenga, chofaniziridwa ndi Babulo chiyambire m’nthaŵi ya Nimrode. Yehova asanalole anthu ake kutengedwa muukapolo ku Babulo mu 617 B.C.E. ndi 607 B.C.E., iwo adagwera kale m’chipembedzo chonyenga Chachibabulo. (Yeremiya 2:13-23; 15:2; 20:6; Ezekieli 12:10, 11) Mu 537 B.C.E., otsalira okhulupirika anabwerera ku Yuda. (Yesaya 10:21) Iwo analabadira chiitano chaulosi chakuti: ‘Tulukani inu m’Babulo.’ (Yesaya 48:20) Ichi sichinayenera kukhala chipulumutso wamba chakuthupi. Chinalinso chipulumutso chauzimu kuchoka m’malo odetsedwa, achipembedzo chonyenga chakulambira mafano. Chotero otsalira okhulupirika ameneŵa analamulidwa kuti: ‘Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.’ (Yesaya 52:11) Chifuno chachikulu chobwererera ku Yuda chinali kukakhazikitsanso kulambira koyera, chipembedzo chowona.
11. Pambali pa kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera m’Yuda, kodi nzochitika zachipembedzo zatsopano zotani zimene zinakhalapo m’zaka za zana la chisanu ndi chimodzi B.C.E.?
11 Mosangalatsa, m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E. mmenemo, panakhala mphukira zatsopano za chipembedzo chonyenga mkati mwa Babulo Wamkulu. Panaphukira Chibuda, Chikomfyushasi, Chizowasitiriya, ndi Chijaini, kuwonjezera pa nthanthi Yachigiriki ya kulingalira imene pambuyo pake inasonkhezera kwambiri matchalitchi a Chikristu Chadziko. Chotero pamene kuli kwakuti kulambira koyera kunkabwezeretsedwa m’Yuda, mdani wamkulu wa Mulungu anali kupereka mpambo wa zosankhapo zochuluka za chipembedzo chonyenga.
12. Kodi nkumasulidwa kotani ku ukapolo Wachibabulo kumene kunachitika m’zaka za zana loyamba C.E., ndipo kodi ndichenjezo lotani limene Paulo anapereka?
12 Podzafika panthaŵi imene Yesu anawonekera m’Israyeli, Ayuda ambiri ankalondola mitundu yosiyanasiyana ya kulambira Kwachiyuda, mtundu wa chipembedzo chimene chinatengera malingaliro achipembedzo ambiri Achibabulo. Icho chinadziphatika ku Babulo Wamkulu. Kristu anachitsutsa ndipo anamasula ophunzira ake ku ukapolo Wachibabulo. (Mateyu, mutu 23; Luka 4:18) Popeza kuti chipembedzo chonyenga ndi nthanthi Zachigiriki zinali zofalikira m’malo amene mtumwi Paulo analalikiramo, iye anagwira mawu ulosi wa Yesaya ndi kuugwiritsira ntchito pa Akristu, omwe anafunikira kudzipatula ku chisonkhezero chodetsa cha Babulo Wamkulu. Iye analemba kuti: ‘Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano [Achibabulo]? Pakuti ife ndife kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga. Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati [Yehova, NW], Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; Ndipo ine ndidzalandira inu.’—2 Akorinto 6:16, 17.
Kumasuka ku Chipembedzo Chonyenga m’Nthaŵi ya Mapeto
13. Kodi nchiyani chimene chikusonyezedwa m’mauthenga amene Kristu anatumiza ku mipingo isanu ndi iŵiri m’Asiya Minor, ndipo kodi nchiyani chimene chinakhala chotulukapo?
13 Mauthenga amene Kristu anatumiza ku mipingo isanu ndi iŵiri mu Asiya Minor kupyolera m’Chibvumbulutso chopatsidwa kwa mtumwi Yohane amasonyeza bwino lomwe kuti pofika kumapeto kwa zaka za zana loyamba C.E., machitachita ndi maganizo achipembedzo Achibabulo ankaloŵerera mumpingo Wachikristu. (Chibvumbulutso, mitu 2 ndi 3) Mpatuko unaphukira makamaka kuchokera m’zaka za zana lachiŵiri kufika m’zaka za zana lachisanu C.E., ukubala chifaniziro chachinyengo cha chipembedzo choyera Chachikristu. Ziphunzitso Zachibabulo zonga kusakhoza kufa kwa moyo, helo woyaka moto, ndi Utatu zinaphatikizidwa m’ziphunzitso za Chikristu champatuko. Matchalitchi Achikatolika, Chiorthodox, ndipo pambuyo pake Chiprotestanti onse anatengera ziphunzitso zonyenga zimenezi, ndipo motero, zinakhala mbali ya Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga wa Mdyerekezi.
14, 15. (a) Kodi fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole linasonyeza chiyani? (b) Kodi nchiyani chimene chinachitika chakumapeto kwa zaka za zana la 19, ndipo pofika 1914, kodi nkupita patsogolo kotani kumene Akristu owona anakupanga ponena za chiphunzitso?
14 Chipembedzo chowona sichinafafanizidwepo kotheratu. M’zaka za mazana onse pakhalapo okonda chowonadi, ena amene anataya miyoyo yawo kaamba ka kukhulupirika kwawo kwa Yehova ndi Mawu ake, Baibulo. Koma monga momwe fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole limasonyezera, tirigu wophiphiritsirayo, kapena ana odzozedwa a Ufumu, akalekanitsidwa ndi namsongole, kapena ana a woipayo, pa “chimaliziro cha [dongosolo la zinthu, NW].” (Mateyu 13:24-30, 36-43) Pamene nthaŵi yamapeto—nthaŵi yakuti kulekanitsa kumeneku kuchitike—inayandikira, ophunzira Baibulo okhulupirika anayamba kumasuka ku ukapolo wa chipembedzo chonyenga chakumapeto kwa zaka za zana la 19.
15 Pofika mu 1914 Akristu ameneŵa, lero otchedwa Mboni za Yehova, anakulitsa chikhulupiriro cholimba m’dipo. Iwo anadziŵa kuti kukhalapo kwa Kristu kuyenera kukhala kosawoneka. Anamvetsetsa kuti 1914 inazindikiritsa mapeto a “nthawi za Akunja.” (Luka 21:24, King James Version) Ndipo anamvetsetsa bwino lomwe tanthauzo la moyo ndi chiukiriro. Iwo anaunikiridwanso pazolakwa zazikulu za ziphunzitso za matchalitchi za moto wa helo ndi Utatu. Iwo anaphunzira ndi kuyamba kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu ndi kuzindikira kulakwika kwa nthanthi ya chisinthiko ndi kukhulupirira mizimu.
16. Kodi nchiitano chotani chimene Akristu odzozedwa anayankha mu 1919?
16 Chiyambi chabwino chinapangidwa chakutaya matangadza a chipembedzo chonyenga. Ndipo mu 1919, Babulo Wamkulu analephereratu kuchita ulamuliro pa anthu a Mulungu. Monga momwe otsalira a Ayuda anamasulidwira ku Babulo mu 537 B.C.E., choteronso otsalira okhulupirika a Akristu odzozedwa analabadira chiitano cha ‘kutuluka pakati pake [Babulo Wamkulu].’—Yesaya 52:11.
17. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika kuyambira mu 1922 kumka mtsogolo, ndipo kodi nchofunikira chotani chimene chinadziŵika kwa anthu a Mulungu? (b) Kodi ndikaimidwe konkitsa kotani kamene kanatengedwa, ndipo nchifukwa ninji zimenezi zinali zomveka?
17 Kuyambira mu 1922 kumka mtsogolo, zowonadi za Baibulo zokantha mwamphamvu zinafalitsidwa ndi kugaŵiridwa poyera, kuvumbula chipembedzo chonyenga Chachibabulo, makamaka matchalitchi a Chikristu Chadziko. Anthu a Mulungu anakuwona kufunika kwa kulekana kotheratu ndi mitundu yonse ya chipembedzo chonyenga. Chotero, kwazaka zambiri, ngakhale kugwiritsira ntchito liwu lakuti “chipembedzo” kunapeŵedwa polankhula za kulambira koyera. Mfuu, zonga ngati “Chipembedzo Chiri Msampha ndi Malonda,” zinasonyezedwa pazikwangwani m’makwalala a mizinda yaikulu. Mabuku onga Boma (1928) ndi “The Truth Shall Make You Free” (1943) analongosola bwino lomwe kusiyana kwa “Chikristu” ndi “chipembedzo.” Kaimidwe konkitsa kameneka kali komveka, popeza kuti kulekana kowonekera bwino ndi madongosolo oluluzika onse achipembedzo a Babulo Wamkulu kunayenera kupangidwa.
Chipembedzo Chowona ndi Chonyenga
18. Kodi ndikamvedwe katsopano kotani ka liwu lakuti “chipembedzo” kamene kanaperekedwa mu 1951, ndipo kodi zimenezi zikufotokozedwa motani mu 1975 Yearbook?
18 Ndiyeno, mu 1951, nthaŵi inafika yakuti Yehova amveketse bwino kwambiri kwa anthu ake kusiyana kokhala pakati pa chipembedzo chowona ndi chonyenga. Lipoti la 1975 Yearbook of Jehovah’s Witnesses limati: “Mu 1951, ochirikiza kulambira kowona anaphunzira chinachake chofunika kwambiri ponena za liwu lakuti ‘chipembedzo.’ Ena a iwo angakumbukirebe 1938 pamene, panthaŵi zina, ananyamula chikwangwani chodzutsa maganizo chakuti ‘Chipembedzo Chiri Msampha ndi Malonda.’ Malinga ndi lingaliro lawo panthaŵiyo, ‘chipembedzo’ chirichonse sichinali Chikristu, chinali cha Mdyerekezi. Koma The Watchtower ya March 15, 1951, inavomereza kuikako mawu ofotokoza chinthu akuti ‘chowona’ ndi ‘chonyenga’ ku liwu lakuti chipembedzo. Ndiponso, bukhu lokopa lakuti What Has Religion Done for Mankind? (lofalitsidwa mu 1951 ndi kutulutsidwa pa Msonkhano wa ‘Kulambira Koyera’ ku Bwalo la Wembley, London, Mangalande) linanena izi: ‘Malinga ndi mmene limagwiritsiridwira ntchito, liwu lakuti “chipembedzo” m’kamasuliridwe kake kosavuta limatanthauza dongosolo la kulambira, mtundu wa kulambira, mosasamala kanthu kaya kuli kulambira kowona kapena konyenga. Ichi chimagwirizana ndi tanthauzo la liwu lake Lachihebri, ‘a·boh·dáh, limene m’lingaliro lenileni limatanthauza “utumiki”, mosasamala kanthu za amene ukuperekedwako.’ Pambuyo pake, mawu akuti ‘chipembedzo chonyenga’ ndi ‘chipembedzo chowona’ anadzakhala ofala pakati pa Mboni za Yehova.”—Tsamba 225.
19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji olambira owona sanafunikire kudzimva olakwa kugwiritsira ntchito liwu lakuti “chipembedzo” kutanthauza kulambira koyera? (b) Kodi kamvedwe katsopano kameneka kanakhozetsa anthu a Yehova kuchita chiyani?
19 Poyankha funso la woŵerenga, kope la The Watchtower la August 15, 1951, linati: “Palibe amene ayenera kudzimva wolakwa kugwiritsira ntchito liwu lakuti ‘chipembedzo’. Pamene tikuligwiritsira ntchito sizitanthauza kuti tikudziika tokha m’gulu la zipembedzo zonyenga zomangika m’miyambo, monga momwe kudzitcha tokha Akristu sikumatiphatikiza pamodzi ndi Akristu onyenga a Chikristu Chadziko.”
20 Posakhala kulolera molakwa mpang’ono ponse, kamvedwe katsopano kameneka ka liwu la “chipembedzo” kanakhozetsa anthu a Yehova kukulitsa mpata pakati pa kulambira kowona ndi konyenga, monga momwe nkhani yotsatira idzasonyezera.
Kuyesa Kamvedwe Kathu
◻ Kodi nliti ndipo ndimotani mmene chipembedzo chonyenga chinayambira padziko lapansi?
◻ Kodi Satana anayesa kukhazikitsanji pambuyo pa Chigumula, ndipo kodi chiwembu chakecho chinalepheretsedwa motani?
◻ Kodi Babulo anadzaphiphiritsira chiyani?
◻ Kodi ndikumasulidwa kotani kumene kunachitika mu 537 B.C.E., m’zaka za zana loyamba C.E., ndi mu 1919?
◻ Kodi ndikamvedwe katsopano kotani ka liwu lakuti “chipembedzo” kamene kanaperekedwa mu 1951, ndipo nchifukwa ninji kunadzaperekedwa panthaŵiyo?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]
Ziphunzitso zonyenga zokhulupiriridwa padziko lonse zinayambira m’Babulo:
◻ Milungu ya utatu, kapena yokhala m’magulu atatu atatu
◻ Moyo wa munthu umapulumuka pa imfa
◻ Kukhulupirira mizimu—kulankhula ndi “akufa”
◻ Kugwiritsira ntchito mafano polambira
◻ Kugwiritsira ntchito matsenga kutonthoza ziŵanda
◻ Ulamuliro wa mtsogoleri wachipembedzo wamphamvu