Mutu 14
Kulemekeza Mphatso ya Moyo
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza kulemekeza kwambiri mphatso ya moyo?
KULEMEKEZA kwambiri mphatso ya moyo ndiko maziko a mtendere ndi chisungiko. Koma ulemu woterowo kaamba ka moyo ukusoweka momvetsa chisoni lerolino. Anthu akhala akatswiri akupha moyo, koma palibe aliyense wa iwo angabwezeretse moyo pamene wachoka.
2 Kulemekeza moyo ndiko thayo lopatulika kwa Wopereka moyo, Yehova Mulungu. Ponena za iye, Wamasalmo anati: “Pakuti chitsime cha moyo chiri ndi inu.” (Salmo 36:9) Miyoyo yathu timailandira kwa Mulungu, osati kokha chifukwa chakuti iye analenga munthu komanso chifukwa chakuti iye walola anthu kupitirizabe kufikira tsopano ndipo wawagawira njira zochirikizira moyo. (Machitidwe 14:16, 17) Koposa zimenezo, iye anachita makonzedwe akuti Mwana wake akhale Muomboli, kapena womasula, wabanja la anthu, akumaligula ndi mwazi wake wamoyo. (Aroma 5:6-8; Aefeso 1:7) Monga chotulukapo, iye tsopano akupereka kwa onse amene adzavomereza mwaŵi wakukhala ndi moyo kosatha m’Dongosolo lake Latsopano. Chifukwa cha zonsezi, kodi tingasonyeze motani ulemu wathu wakuya ndi chiyamikiro kaamba ka mphatso ya Mulungu ya moyo?
3. Kodi ndimotani mmene kuwonerera chiwawa kaamba kachisangalalo kumayambukilira lingaliro la munthu kulinga ku moyo?
3 Choyamba, ngati tiri otsimikizira ponena za kulemekeza moyo, sitidzagwirizana ndi awo amene, kaamba ka chisangalalo chokha, amadyetsa maganizo awo chosangalatsa chimene chimasonyeza chiwawa. Kulandira chiwawa kukhala “chosangalatsa” kwachititsa ambiri kukhala ouma mtima ndi osamvera chisoni kuvutika kwa anthu ndi kutaika kwa moyo. Koma ngati ife tiri oyamikira ubwino wa Mulungu ndi chiyembekezo chimene amapereka, tidzakaniza mzimu wotero. Tidzakulitsa chiyamikiro cha moyo monga mphatso yochokera kwa Mulungu. Kumeneku kudzayambukira mmene timagwiritsirira ntchito miyoyo ya ife eni, ngakhalenso mmene timalingalirira awo amene sanabadwebe.
Kulemekeza Moyo wa Amene Asanabadwe
4. (a) Kodi ndiliti pamene moyo umaperekedwa kwa mwana? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kaya Mulungu amakondwera ndi moyo wa munthu asanabadwe?
4 Mphamvu yakupereka moyo iri mwaŵi waukulu, woperekedwa ndi Mulungu. Moyo umenewo umaperekedwa, osati pakubadwa, koma panthawi yakukhala ndi pakati. Monga momwe Encyclopædia Britannica imalongosolera, ndipanthawi imeneyo pamene “moyo wa munthu, monga chokhalako chapadera ndi chamoyo, umayamba.” Iyo imatinso: “Munthu watsopano amalengedwa pamene nsanganizo za ubwamuna wamphamvu zigwirizana ndi dzira lokhala ndi mphamvu ya kubala.”60 Momwemonso kukondwerera kwa Mulungu moyo wa munthu kumayamba asanabadwe. Wamasalmo Davide analemba, akumanena kwa Mulungu kuti: “Munanditsekera m’mimba mwa amayi wanga. . . . Maso anu anawona ngakhale m’luza wanga, ndipo m’bukhu lanu ziŵalo zake zonse zinalembedwa.”—Salmo 139:13-16, NW; Mlaliki 11:5.
5. Kodi nchifukwa ninji zigomeko zoperekedwa m’kuyesayesa kulungamitsa kutaya mimba ziri zosamveka?
5 Miyoyo ya ana osabadwa mamiliyoni ambiri imaphedwa mwadala mwakutaya mimba chaka chirichonse. Kodi kumeneku nkoyenera mwamakhalidwe abwino? Ena amapereka chigomeko chakuti khanda losabadwa liribe kuzindikira chimene chiri moyo ndipo liri losakhoza kukhala palokha litaturuka m’mimba. Koma zimenezo zirinso chimodzimodzi kwambiri ndi khanda lobadwa chatsopano. Pakubadwa sirimadziŵa tanthauzo lirilonse la moyo, ndiponso silingathe kupitirizabe kukhalapo popanda chisamaliro chosalekeza. Selo lamoyo lopangidwa m’mimba panthawi yakutenga mimba limafikira kukhala khandalo ngati silinadodometsedwe. Chotero ngati kupha khanda lobadwa chatsopano kumawonedwa kukhala upandu pafupifupi kulikonse, ndipo zoyesayesa zamphamvu zimapangidwa kupulumutsa ngakhale makanda obadwa masiku asanafike, pamenepa, chifukwa ninji sulinso upandu kupha mwana wosabadwa? Kodi nchifukwa ninji moyo ungawonedwe kukhala wopatulika pambuyo pokha pakuchoka m’mimba ndipo osatinso pamene ukali m’mimba?
6. Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera lingaliro la Mulungu kukupha dala moyo wamwana wosabadwa?
6 Chinthu chofunika sindicho chabe mmene anthu angawonere zinthu koma chimene Mulungu, Wopereka moyo, amanena. Kwa Yehova moyo wa mwana wosabadwa ngwamtengo wapatali, wosati nkuseŵera nawo. Iye anapereka lamulo kwa Israyeli wakale lotetezera kotheratu moyo umenewo. Ngati, m’kulimbana, pakati pa amuna aŵiri, mkazi wapakati anavulazidwa kapena ngati kupita padera kunachitika, lamulo limenelo linapereka zilango zamphamvu. (Eksodo 21:22, 23) Kupha moyo wamwana wosabadwa mwadala kukakhaladi kowopsa kopambana. Malinga ndi kunena kwa lamulo la Mulungu, aliyense wakupha moyo wa munthu mwadala anayenera kuweruziridwa ku imfa monga wambanda. (Numeri 35:30, 31) Mulungu ali ndi kulemekeza moyo kwambiri kofananako tsopano.
7. Kodi timatetezeredwa kuchiyani pamene tilemekeza chifuniro cha Mulungu chonena za moyo wamwana wosabadwa?
7 Kulemekeza kwambiri chifuniro cha Mulungu chonena za moyo wa mwana wosabadwa kumachititsa phindu lenileni. Mwakupangitsa kwake makolo kukhala ndi thayo lokwanira kaamba ka moyo umenewo, Yehova amapereka choletsa kukugonana kosasankha limodzi ndi ziyambukiro zake zonse zoipa. Zimenezi zimaphatikizapo nthenda zopatsana mwakugonana, mimba zosafunika, ana apathengo, mabanja osweka, ndi chipsinjo chamaganizo cha chikumbumtima chodetsedwa. Motero, kulemekeza moyo kungathandizire mtendere wabanja tsopano ndipo ndiko chochititsa chofunika m’kupeza kwathu madalitso amtsogolo.
Kulemekeza Moyo wa Inumwini
8. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza kulemekeza chifuniro cha Mulungu mwanjira ya mmene timachitira ndi thupi lathu?
8 Bwanji ponena za mmene timachitira ndi thupi lathu la ife eni? Anthu ambiri amanena kuti: ‘Sindinasankhe kubadwa. Motero chimene ndikuchita ndi moyo wanga ziri kwa ine. Ndidzachita chirichonse chimene ndifuna.’ Koma kodi mphatso iyenera kupemphedwa kuti woilandirayo ayiyamikire? Moyo weniweniwo mosakaikira ngwabwino. Ndiko chabe kupanda ungwiro kwa anthu ndi kusakhulupirika zimene zimachotsera moyo chochuluka cha chisangalalo chake. Yehova Mulungu sindiye ali ndi liwongo la zimenezo. Ndipo iye akulonjeza kuziwongola mwaboma lake Laufumu. Chotero, tiyenera kukhala ndi moyo m’njira imene imasonyeza kulemekeza chifuniro ndi chifuno chake.—Aroma 12:1.
9. Kodi Baibulo limanenanji ponena za kudya mopambanitsa ndi kuledzera?
9 Njira imodzi imene tingasonyezere chiyamikiro chotero ndiyo mwakukhala achikatikati m’zakudya ndi zakumwa. Kususuka ndi kuledzera zikutsutsidwa ndi Mulungu. (Miyambo 23:20, 21) Ndiponso, monga momwedi kudya mwachikatikati kuli koyenera chimodzimodzinso kumwa zakumwa zoledzeretsa mwachikatikati. Chimenechi chikusonyezedwa ndi malemba ambiri.—Deuteronomo 14:26; Yesaya 25:6; Luka 7:33, 34; 1 Timoteo 5:23.
10. (a) Kodi ndimotani mmene woledzera amasonyezera kusalemekeza moyo? (b) Monga momwe kwasonyezedwera pa 1 Akorinto 6:9, 10, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kupewa kuledzera?
10 Chotero sindiko kumwa kumene kuli kotsutsidwa m’Baibulo. Ndiko kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa. Ndipo ndichifukwa chabwino, chifukwa chakuti izo zimavulaza thupi, kupangitsa akumwawo kuchita mopusa, ndipo kungawapangitse kukhaladi apandu kwa ena. (Miyambo 23:29-35; Aefeso 5:18) Mu United States mokha anthu okwanira mamiliyoni 10 amakanthidwa ndi uchidakwa, choturukapo chimodzi ndicho anthu akufa oposa 30 000 ndi nthenda yakutupa chiwindi chaka chirichonse. Bungwe Lamtunduwo lowona za Uchidakwa limati: “Kutaika konse kumtunduwo kuli pafupifupi madolala mabiliyoni 43 pachaka chifukwa cha kulova kuntchito, kudwala ndi mautumiki a welofeyala, kuwonongedwa kwakatundu ndi ndalama zowonongedwera chisamaliro chachipatala. . . . Pangozi zonse zakupha zochitika pamsewu lerolino, 50 peresenti zimalowetsamo zakumwa zoledzeretsa. Yoposa 80 peresenti ya imfa zochititsidwa ndi moto, 65 peresenti ya omizidwa ndi madzi, 22 peresenti yangozi m’banja, 77 peresenti yakugwa, 36 peresenti yangozi za oyenda ndi miyendo pamsewu ndi 55 peresenti za omangidwa zagwirizanitsidwa ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa zakumwa zoledzeretsa. Kufikira 44 peresenti ya oyendetsa ndege olowetsedwa m’ngozi anali kumwa. Kudzisungira kwachiwawa konenedwa kukhala kochititsidwa ndi zakumwa zoledzeretsa kwachititsa pafupifupi 65 peresenti zambanda, 40 peresenti za ziukiro, 35 peresenti zakugwirira chigololo, 30 peresenti za maupandu ena akugonana, 30 peresenti kudzipha, 55 peresenti ya ndewu kapena ziukiro m’banja ndipo 60 peresenti za kuchitira ana nkhanza.”61 Mtengo wake wa mabanja osweka, miyoyo yoipitsidwa, ndi kuvutika kwa anthu nzosaŵerengeka. Motero sikuli kodabwitsa kuti Mawu a Mulungu amati: “Musasocheretsedwe; adama . . . kapena oledzera kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.
11. Kodi nkwanzeru kuyesa kupewa mavuto anu mwakumwa kopambanitsa?
11 Nzowona, ena amamva kwambiri chiyambukiro chotsendereza chamkhalidwe wadziko. Nkhondo zake, upandu, kukwera kwamitengo, umphaŵi, ndiponso kuchita tondovi ndi zipsinjo zake zimachititsa mavuto athu. Koma palibe chirichonse chikupindulidwa mwakuyesa kupewa zimenezi kupyolera mwa zakumwa zochulukitsitsa zovulaza. Zimenezi zimangopanga mavuto owonjezereka kwa munthuwe ndi kwa ena ndipo, m’kupita kwanthawi, kuwononga ulemu wa munthuwe, chifuno ndi kaimidwe ndi Mulungu.
Kugwiritsiridwa Ntchito Kwa Mankhwala Oledzeretsa
12. Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri amatembenukira ku mankhwala oledzeretsa?
12 M’kuyesa kupewa mavuto a moyo, anthu ochuluka atembenukira ku mankhwala oledzeretsa. Ogwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa otere amasinthanitsa zenizeni ndi lingaliro la kulota kapena mkhalidwe wachizwezwe. Ochuluka amagwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa monga chamba ndi kokaini. Ena amamwa mankhwala osiyanasiyana ochuluka mu mpangidwe wa mibulu. Kodi miyoyo yawo imayambukiridwa motani?
13. Kodi ena amankhwala amenewa amakhala ndi ziyambukiro zotani pa ogwiritsira ntchito, ndipo kodi Baibulo limachenjeza motani za zimenezi?
13 Kugwiritsira ntchito kwawo mankhwala amenewa kumatsogolera mosavuta kukutaikiridwa ndi kudziletsa, kukumatulutsa ziyambukiro ndi zowonedwa mwa munthu woledzera. (Miyambo 23:29-34) Ndipo kaŵirikaŵiri kukuvomerezedwa kuti mankhwala amenewa angathe kukhala aupandu. Mwachitsanzo, mu Mzinda wa New York, kumwerekera ndi chamba ndiko chochititsa imfa choyambilira pakati pa anthu amausinkhu azaka 18 ndi 35. Ha ndikusalemekeza moyo kwakukulu chotani nanga!
14, 15. Kodi nchifukwa ninji awo osuta chamba sakusonyeza kulemekeza mphatso ya moyo?
14 Koma bwanji ponena za mankhwala osamwerekeretsa kwambiri chamba (marijuana)? Nawonso angakhale aupandu m’njira zambiri. Kaŵirikaŵiri ogwiritsira ntchito chamba amachititsidwanso kugwiritsira ntchito mankhwala omwerekeretsa kupyolera mwakukumana ndi ogulitsa mankhwala oledzeretsa ndi ogwiritsira ntchito ena. Ndiponso, ambiri amene afikira pakudalira pa mankhwalawo, amakhulupilira kuti adzachepetsa nkhawa ndi kuchita tondovi, mwachiwonekere adzapitirizabe kumka kumankhwala amphamvu kwambiri.
15 Koma ngakhale ngati zimenezi sizichitika, kusuta chamba kwenikweniko nkwaupandu. Chiri ndi nsanganizo zochititsa kensa zochuluka kwambiri koposa ndudu, ndipo chimavulaza kwambiri mapapu. Kupitirizabe kuchigwiritsira ntchito kungachititse kuwonongeka kwachiwindi, zirema zachibadwa, ndi kuwonongeka kwaubongo. Bungwe la Addiction Research Foundation la Canada likunena kuti chamba “ndicho mankhwala oledzeretsa amphamvu kwambiri okhala ndi mipangidwe yochuluka yamaupandu kuthanzi.”62 Katswiri wina wamankhwala oledzeretsa anati: “Chamba ndicho mankhwala oledzeretsa aupandu kwambiri. M’kati mwazaka 10 zapita kanthu kena kofanana ndi mapepala 10 000 kafalitsidwa ndi akatswiri asayansi kusonyeza upandu wathanzi.” Iye anatchula za “upandu waukulu umene uli wowopsa kwambiri mwa achichepere oyesa kuloŵeza mawu pamtima,” m’chakuti chimafowoketsa malo osungira chikumbukiro ndi luso lakusumika maganizo. Ponena za wosuta chamba, mwamunayu anati: “Iye sangathe kuyendetsa bwino galimoto kapena kulemba ndi tayipi. Kugwiritsiridwa ntchito kwanthawi yaitali kumachititsa chivulazo chowonjezereka chachikulu kudongosolo lathupi lotetezera nthenda.”63 Akazi amene amasuta chamba panthawi yakukhala kwawo ndi pakati ali ndi kuthekera kokulira kwambiri kwa kubala ana ovulazika ubongo. Polingalira zonsezi, kodi kunganenedwe kuti kusuta chamba kumasonyeza kulemekeza mphatso ya moyo?
16. Kodi kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa kungapereke munthu kuupandu wowopsa wotani, ndipo kodi ndimotani mmene chimenechi chiyenera kuyambukilira lingaliro lathu pankhaniyi?
16 Pali chifukwa china chaphamvu chopewera kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala oledzeretsa. Iwo angatsegulire munthu njira ya kuloŵa mu ulamuliro wa ziwanda. Kugwirizanitsidwa kwamankhwala oledzeretsa ndi kulankhula ndi mizimu kumeneku sikwatsopano konse. Openduza m’nthawi zakale anagwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa. Expository Dictionary of New Testament Words la Vine limalongosola kuti: “M’kupenduza, kugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala oledzeretsa, kaya opanda kapena amphamvu, kaŵirikaŵiri kunatsagana ndi kunenerera ndi kuitana mphamvu za mizimu.” Mawu amenewa akunenedwa mogwirizana ndi liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kukhala “kachitidwe ka kulankhula ndi mizimu” (phar·ma·kiʹa, kwenikweni “nyanga”) pa Agalatiya 5:20. (Wonaninso Chivumbulutso 9:21; 18:23.) Chotero mankhwala oledzeretsa angachititse munthu kuyambukiridwa ndi ziwanda. Kodi ndimotani mmene munthu amene amalemekeza mpatsi Wamoyo wake angadziloŵetsere paupandu wotero kokha kaamba ka chisangalalo chakanthawi?
17, 18. (a) Kodi ndizipatso zina zoipa zotani zimene zagwirizanitsidwa ndi kugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala oledzeretsa? (b) Chotero, kodi ndimotani mmene Mboni Zachikristu za Yehova zimawonera kugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala oledzeretsa?
17 Kuli kodziŵika bwino lomwe kuti kugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala oledzeretsa kukugwirizanitsidwa kwambiri ndi upandu ndi kusweka kwamakhalidwe abwino m’chitaganya. Kugulitsa mankhwala oledzeretsa kosavomerezedwa ndiko magwero aakulu opezera ndalama kaamba ka upandu wolinganizidwa. Unyinji wa omwerekera ndi mankhwala oledzeretsa umaba kuti uchilikize chizoloŵezi chawo. Ena amatembenukira ku uhule. Mabanja ambiri amasweka pamene chiŵalo china chikhala chomwerekera ndi mankhwla oledzeretsa. Akazi apakati amapatsira makanda awo kumwerekera ndi mankhwala oledzeretsa, amene nthawi zina amafa chifukwa chakuvutika ndi ululu wakusowa mankhwalawo. Ndipo m’maiko ambiri kukhala ndi kugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala aupandu oterowo kaamba ka zifukwa zosakhala zakuchiritsira matenda kuli kosavomerezedwa ndi lamulo.—Mateyu 22:17-21.
18 Kodi inu mukufuna kukhala ndi mbali iriyonse ndi chizoloŵezi chimene chagwirizanitsidwa ndi zipatso zonse zoipa zotero? Mboni za Yehova sizikufuna! Izo sizimafuna kukhala ndi mbali iriyonse yakugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala oledzeretsa kaamba ka zikondwerero kapena kupewa zenizeni. Izo ziri ndi ulemu waukulu kaamba ka moyo ndipo zimafuna kugwiritsira ntchito miyoyo yawo m’njira imene iri yogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.
Kugwiritsiridwa Ntchito kwa Fodya ndi Zinthu Zofananazo
19. Kodi nchifukwa ninji kulemekeza mphatso ya moyo kumaloŵa m’lingaliro la munthu kulinga kukugwiritsiridwa ntchito kwa fodya, mtedza wabetelo, ndi masamba amtengo wa coca?
19 Chofala kwambiri lerolino ndicho kugwiritsiridwa ntchito kwa fodya ndipo, maiko ena, mtedza wabetelo ndi masamba amtengo wa coca. Chirichonse chimawononga thupi ndipo, m’zochitika zina, maganizo. Maboma achenjeza za kugwirizanitsidwa kwa fodya ndi nthenda zonga kensa yamapapu, nthenda yamtima, chifuwa chosatha, ndi kutupa mapapu. Kodi kumeneku kumasonyeza kulemekeza mphatso yamoyo kugwiritsira ntchito zinthu zomwerekeretsa ndi zovulaza zoterozo?
20, 21. (a) Kodi chenicheni chakuti Baibulo silimatsutsa zizoloŵezi zoterozo mwakuzitchula dzina chimatanthauza kuti izo zonse ziri bwino? (b) Kodi ndimalamulo amakhalidwe abwino otani amene amasonyeza kuti zizoloŵezi zoterozo ziribe malo m’moyo wamtumiki wa Mulungu?
20 Munthu wina anganene kuti zinthu zonse zimenezi zinalengedwa ndi Mulungu. Nzowona, koma zirinso chimodzimodzi ndi bowa. Chikhalirechobe mitundu yosiyanasiyana imatsimikizira kukhala yakupha ngati itadyedwa. Munthu wina anganene kuti Baibulo silimatsutsa mwachindunji zizoloŵezi zotero. Ayi, koma monga momwe tawonera, pali zinthu zambiri zosatsutsidwa mwachindunji ndi Baibulo zimene mwachiwonekere ziri zolakwa. Palibe paliponse pamene Baibulo limaletsa mwachindunji kugwiritsira ntchito bwalo la munthu woyandikana naye kukhala malo otayako zinyalala. Komabe lamulo lake la ‘kukonda mnansi wanu monga inumwini’ liyenera kukhala lokwanira kwa aliyense wa ife kuzindikira mmene kumeneku kukakhalira kulakwa. Mofananamo, kusuta ndudu kumasonyeza kupanda chikondi, popeza kuti utsi ungavutitse ena ndipo ungakhaledi wovulaza thanzi lawo.—Mateyu 22:39.
21 Pa 2 Akorinto 7:1 Mawu a Mulungu amatiuza ‘kuleka chodetsa chathupi ndi chamzimu, ndi kutsiriza chiyero kuwopa Mulungu.’ Kuti kanthu kakhale ‘koyera’ kumatanthauza kuti kayenera kukhala ‘konyezimira, kaudongo, ndi kosadetsedwa.’ Yehova amadzisunga kukhala woyera kuchinyengo, samadzitsutsira konse kukuchita mwanjira yopanda chiyero. Moyenelera amatiyembekezera kupitirizabe “kutsiriza chiyero” kumlingo wothekera wa anthufe. (Aroma 12:1) Ndiponso, iye amatiyembekezera ‘kumkonda ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo ndi nyonga.’ Koma kodi ndimotani mmene munthu aliyense angachitire zimenezi ngati alowa m’machitachita amene amadetsa thupi lake, kuwononga thanzi lake, ndi kufupikitsa moyo wake?—Marko 12:29, 30.
22. Kodi nchiyani chimene chingatheketse munthu kuonjoka pa kugwira kumene chizoloŵezi choipa choterocho kungakhale nako pa iye?
22 Ngakhale kuli kwakuti chimodzi kapena china cha zizoloŵezi zoterozo chingawonekere kukhala chitagwira zolimba pamunthu, iye angachilake ndi kumasuka. Kudziŵa Mulungu ndi zifuno zake zabwino kwambiri kumapereka chisonkhezero chochitira motero. Munthu angathe kupangidwa ‘kukhala watsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo ake.’ (Aefeso 4:23) Kumeneku kudzatsegula njira yatsopano njira yamoyo, imene imachititsa chikhutiro chanu ndi kulemekeza Mulungu.
Kulemekeza Moyo monga Momwe Waimiridwira ndi Mwazi
23. (a) Kodi ndikugwiritsiridwa ntchito kokha kwa mwazi kuti kumene Mulungu anavomereza m’chilamulo chake kwa Aisrayeli? (b) Kodi nchifukwa ninji tanthauzo lansembe zimenezo liyenera kutichititsa kulingalira mosamalitsa chifuniro cha Mulungu pankhani imeneyi?
23 Mwazi wathunso, umafunikira kulingaliridwa, pamene tikunena za moyo. Mulungu wasankha mwazi waponse pawiri wa anthu ndi wa nyama kukhala chizindikiro cha moyo. Chimenechi chikusonyezedwa m’lamulo limene anapereka kwa Nowa ndipo pambuyo pake kumtundu wa Israyeli. Kugwiritsidwa ntchito kokha kwa mwazi kovomerezedwa kunali nsembe. (Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:10-14) Nsembe zonsezo zinaphiphiritsira nsembe imodzi ya Yesu, mwa imene anakhetsa mwazi wake wamoyo mmalo mwa anthu. (Ahebri 9:11-14) Kumeneku mwa iko kokha kuyenera kutichititsa kulingalira mosamalitsa chifuniro cha Mulungu m’nkhani imeneyi.
24. Kodi Machitidwe 15:28, 29 amanenanji ponena za lingaliro limene Akristu ayenera kukhala nalo kulinga ku kugwiritsiridwa ntchito kwamwazi?
24 Kodi chiletso cha Mulungu chonena zakugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi chikugwirabe ntchito kwa Akristu owona? Inde, monga momwe kwasonyezedwera ndi mawu aukumu onenedwa ndi atumwi ndi akulu ena ampingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba. Motsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, iwo analemba kuti: “Chinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe zamafano, ndi mwazi, ndi zopotola [ndiko kuti, zosakhetsedwa mwazi], ndi dama; ngati mudzisungitsa pazimenezi, kudzakhala bwino kwa inu.”—Machitidwe 15:28, 29.
25. Kodi dziko limasonyeza kusalemekeza chifuniro cha Mulungu chonena za mwazi mwamachitidwe otani?
25 Anthu ambiri amanyalanyaza chifuniro cha Mulungu chonena za mwazi. Iwo amaugwiritsira ntchito monga chakudya, kaamba ka zifuno za kuchiritsa matenda, ngakhale m’zinthu zamalonda. Koma izi siziyenera kutidabwitsa, chifukwa chakuti dziko limasonyeza nkhawa yochepa kwambiri kaamba ka mphatso yeniyeniyo ya moyo. Komabe, ngati ife timayamikira moyo ndi kukhala kwathu ofunikira kudziyankhira kwa Mulungu, sitidzanyalanyaza chifuniro chake kapena kumchitira chipongwe mwakuswa malamulo ake.
26, 27. Kodi nchifukwa ninji zoyesayesa za kupulumutsa moyo wa munthuwe watsopano lino mwakusamvera Mulungu ziliri kusasonyeza kumlemekeza?
26 Motero, ngakhale kuli kwakuti tiyenera kukhala odera nkhawa ndi thanzi lathu ndi kufunafuna kutetezera miyoyo yathu, pali malire ena oti asungidwe. Yesu anasonyeza amenewa pamene anati: “Iye wokonda moyo [kapena umoyo] wake auwononga, koma wodana ndi moyo wake m’dziko lino adzausungira ku moyo wosatha.”—Yohane 12:25, NW.
27 Ngati iri nkhani yakuyang’anizana ndi imfa chifukwa chakumvera Mulungu kapena kusam’mvera kuti apewe imfa, mtumiki wa Mulungu adzasankha imfa koposa kusam’mvera. Mwakusamvera Mulungu, Yesu akanatha kupewa imfa. Koma iye sanatero. Ndipo amuna ena iye asanabwere anali atasonyeza kudzipereka kosasweka kumodzimodziko kwa Mulungu. (Mateyu 26:38, 39, 51-54; Ahebri 11:32-38) Iwo sanalole moyo wawo watsopano lino kupinga kuyenelera kwawo moyo wosatha.
28. Mwakukulitsa chiyamikiro kaamba ka lingaliro la Baibulo kulinga ku moyo, kodi ife tikukonzekera chiyani?
28 Kodi mmenemo ndimo mmene inunso mumawonera moyo? Kodi mumazindikira kuti, kuti moyo ukhale ndi tanthauzo lenileni, muyenera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu? Kukulitsa lingaliro limenelo tsopano ndiko mbali yakukonzekera moyo m’Dongosolo Latsopano la Mulungu. Ha tidzakhala tiri otetezereka ndi osungika chotani nanga pamenepa, kulikonse ndi panthawi iriyonse, kudziŵa kuti awo onse okhala ndi moyo padziko lapansi amalemekeza mowona mtima mphatso ya Mulungu ya moyo!