Mungathe Kupeza Chitonthozo m’Nthaŵi ya Nsautso
KODI kupsinjika maganizo tiyenera kukuwona motani? Ngati ndife odzipatulira kwa Yehova, kodi tiyenera kukuyesa kwachilendo chifukwa cha chiyembekezo chathu chabwino kwambiri ndi maluso athu auzimu? Kodi malingaliro otero amatanthauza kuti ife mwauzimu tiri osayenerera utumiki wa Mulungu?
“Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife,” analemba motero mtumwi Yakobo. (Yakobo 5:17) Ngakhale kuti Mulungu anagwiritsira ntchito Eliya m’njira yodabwitsa, mneneri wokhulupirika ameneyo anapsinjika maganizo. “Kwafikira,” anadzuma motero Eliya panthaŵi ina. “Chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindiri wokoma woposa makolo anga.” (1 Mafumu 19:4) Yobu mwamuna wosunga umphumphu, mkazi wokhulupirika Hana, ndi atumiki ena okhulupirika a Yehova anapsinjika maganizo. Ngakhale wamasalmo wopembedza Davide anapemphera kuti: “Masautso a mtima wanga akula: munditulutse m’zondipsinja.”—Salmo 25:17.
Pamene Yehova akugwiritsira ntchito anthu muutumiki wake sizimatanthauza kuti iwo adzakhaliratu opanda nkhaŵa. Amakhalabe ndi zofooka zaumunthu ndi malingaliro ndipo angathe kupsinjika maganizo poyesedwa. (Machitidwe 14:15) Koma, atumiki a Yehova ali ndi chithandizo chabwinopo koposa ena chochitira ndi kupsinjika maganizo. Tiyeni tipende zitsanzo zingapo za m’Baibulo kuti tiwone zimene zinathandiza anthu ena kulaka kupsinjika maganizo kwawo ndi kuvutika mtima.
Mtumwi Wopsinjika Maganizo Apeza Chitonthozo
Mtumwi Paulo anadziŵa bwino lomwe zimene kukhala wopsinjika maganizo kunatanthauza. “Pakutinso,” iye anatero, “pakudza ife m’Makedoniya thupi lathu linalibe mpumulo; . . . kunjako zolimbana, mkatimo mantha. Koma iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito.” (2 Akorinto 7:5, 6) Kupsinjika maganizo kwa Paulo kunachititsidwa ndi mikhalidwe ingapo yovutitsa yochitika panthaŵi imodzimodzi. ‘Kunjako kunali zolimbana’—chizunzo chokakala choika moyo weniweniwo paupandu. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 1:8.) Ndiponso, ‘mkati munali mantha’ mumpangidwe wa nkhaŵa kaamba ka mipingo, monga uja wa ku Korinto.
Miyezi ingapo yoyambirira, Paulo anali atalemba kalata yake yoyamba kwa Akristu a ku Korinto. M’kalatayo anatsutsa mikhalidwe yoŵerengeka yoipitsitsa mumpingo ndipo mwachiwonekere anali wodera nkhaŵa za mmene Akorinto akachitira atalandira kalata yake. Komabe, Paulo anatonthozedwa pamene Tito anadza kuchokera ku Korinto ndi mbiri yabwino yosimba za kulabadira kwawo. Mofananamo, Yehova angagwiritsire ntchito mmodzi wa atumiki ake amakono kutibweretsera mbiri yabwino ndi kutonthoza maganizo athu.
Mmene Tiyenera Kuwonera Ntchito Zopatsidwa ndi Mulungu
Akristu ena amapsinjika mtima chifukwa cha utumiki wawo. Ndithudi, atumiki ena a Yehova alingalira kuti ntchito zopatsidwa ndi Mulungu zikafuna zochulukitsitsa kwa iwo kotero kuti sakakhoza kuzikwaniritsa. Mwachitsanzo, Mose anadzilingalira kukhala wosayenerera kukhala woimira wa Mulungu mmalo mwa Aisrayeli m’Igupto. Pakati pa zinthu zina, ananena kuti sanali wolankhula waluso. (Eksodo 3:11; 4:10) Koma podalira mwa Mulungu ndi pokhala ndi Aroni monga womlankhulira, Mose anayamba kusenza thayo lake.
Mkupita kwa nthaŵi Mose sanadalirenso pa Aroni. Mofananamo, ena poyamba amapeza uminisitala Wachikristu kukhala wovuta, koma amaphunzitsidwa nakhala alaliki aluso. Mwachitsanzo, Mboni zambiri zachichepere za Yehova zafikira pakukhala alaliki anthaŵi yonse monga apainiya ndi amishonale. Nkotonthoza kudziŵa kuti Yehova nthaŵi zonse angadaliridwe kuyeneretsa aminisitala Achikristu ndi kuwapatsa mphamvu yokwaniritsira ntchito zawo zopatsidwa ndi Mulungu.—Zekariya 4:6; 2 Akorinto 2:14-17; Afilipi 4:13.
Chitonthozo Popsinjika Maganizo ndi Zisoni
Tingagwetsedwe ulesi chifukwa chochita chisoni kuti sitinachite zochuluka muutumiki wa Mulungu. Mbale wina amene anali wosakangalika kwa zaka zambiri anayambiranso kukhala ndi phande muuminisitala wakumunda. Mwamsanga pambuyo pake, anadwala kwambiri ndipo anabindikiritsidwa pakama kwachikhalire. Mbale wosweka mtimayo anati: “Poyamba, pamene ndikanakhala wokangalika, ndinazemba thayo. Tsopano, pamene ndifuna kukhala wokangalika, ndiri wosakhoza kutero.”
Kodi sikukakhala kwanzeru kuchita zirizonse zotheka tsopano mmalo motaya nthaŵi kusinkhasinkha za zochitika zakale? Abale a Yesu a mimba ina Yaboko ndi Yuda sanakhale okhulupirira kufikira pambuyo pa imfa ndi chiukiriro chake. Ngati anamva chisoni ndi zimenezo, sizinawaletse kukhala atumiki a Mulungu ndipo ngakhale kukhala olemba Baibulo.
Osanyalanyaza Konse Pemphero
Popsinjika maganizo, anthu a Mulungu ayenera kupemphera mwakhama. Kunena zowona, Malemba ali ndi mapemphero ambiri operekedwa m’nthaŵi za nsautso. (1 Samueli 1:4-20; Salmo 42:8) Ena angalingalire kuti: ‘Ndiri wopsinjika maganizo kwambiri kotero kuti sindikhoza kupemphera.’ Pamenepo bwanji osalingalira za Yona? Pamene anali m’mimba mwa nsomba, iye anati: “Pokomoka moyo wanga mkati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira inu m’kachisi wanu wopatulika. . . . Koma ine ndidzakupherani inu nsembe ndi mawu akuyamika, ndidzakwaniritsa choŵinda changa. Chipulumutso ncha Yehova.” (Yona 2:4-9) Inde, Yona anapemphera, ndipo Mulungu anamtonthoza nampulumutsa.
Ngakhale kuti mlongo wina ku Sweden anali mpainiya kwa zaka zambiri, anachita tondovi mwadzidzidzi nataya mtima mosasamala kanthu za uminisitala wofupa. Anatchula kusweka mtima kwake m’pemphero kwa Yehova. Pambuyo pa masiku angapo, analandira foni kwa mbale wina wa panthambi ya Watch Tower Society. Mbaleyo anafunsa ngati mlongoyo akakonda kukathandiza kumeneko kwa tsiku limodzi pamlungu pantchito yofutukula Beteli. Mlongo ameneyu pambuyo pake anati: “Mkhalidwe wa pa Beteli ndi kukhala ndi mpata wakuwona ntchito yofutukulayo ndi kukhalamo ndi phande kunandipatsa nyonga yowonjezereka imene ndinafunikira.”
Ngati tipsinjika maganizo, ndibwino kukumbukira kuti pemphero ndiimodzi ya njira zolimbanira ndi kupsinjika maganizo. (Akolose 4:2) Poyankha mapemphero athu, Yehova angatsegule khomo loloŵera ntchito yokulirapo muutumiki wake, kapena angadalitse uminisitala wathu ndi zipatso zowonjezereka. (1 Akorinto 16:8, 9) Mulimonse mmene zingakhalire, “madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.” (Miyambo 10:22) Ndithudi zimenezi zidzatitsitsimula.
Kodi Mukuchita Tondovi ndi Zikaikiro?
Nthaŵi zina, mmodzi wa atumiki a Yehova angakhale ndi zikaikiro. Ngati zimenezo zingatichitikire, sitiyenera panthaŵi yomweyo kugamula kuti tataya chiyanjo cha Mulungu. Yesu sanakane mtumwi Tomasi chifukwa chokaikira malipoti a mboni zowona ndi maso chiukiriro cha Mbuyake. Mmalomwake, Yesu mwachikondi anathandiza Tomasi kuchotsa zikaikiro zake. Ndipo Tomasi anachita chidwi chotani nanga pamene anazindikira kuti Yesu anali wamoyo!—Yohane 20:24-29.
Mwa ziphunzitso zawo zonama, kung’ung’udza, ndi zina zotero, “anthu osapembedza” amene anakwaŵira mumpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba anali kuchititsa ena kukhala ndi zikaikiro zovutitsa maganizo. Chifukwa chake, wophunzira Yuda analemba kuti: “Ena osinkhasinkha muwachitire chifundo. Koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto.” (Yuda 3, 4, 16, 22, 23) Kuti apitirize kulandira chifundo cha Mulungu, olambira anzake a Yuda—makamaka akulu mumpingo—anafunikira kuchitira okaikakaika chifundo chowayenerera. (Yakobo 2:13) Moyo wawo wosatha unali pachiswe, pakuti anali paupandu wa “moto” wa chiwonongeko chamuyaya. (Yerekezerani ndi Mateyu 18:8, 9; 25:31-33, 41-46.) Ndipo nchimwemwe chotani nanga chimene chimakhalapo pamene chithandizo chiperekedwa mokoma mtima kwa okhulupirira anzathu okaikakaika nakhalanso olimba mwauzimu!
Ngati ziyeso zosautsa zingatipangitse kukaikira kuti Mulungu ali nafe, tifunikira kukhala achindunji m’mapemphero athu. M’mikhalidwe yotero, tiyeni tilimbike kupempha nzeru kwa Yehova. Amapatsa mowoloŵa manja popanda kutitonza chifukwa chakusoŵa nzeru ndi kuipempherera. Tiyenera ‘kupemphabe ndi chikhulupiriro, osakaika konse,’ pakuti wokaikayo “afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuŵinduka nayo” kupita kulikonse. Anthu otero samapeza kalikonse kwa Mulungu chifukwa ngamitima iŵiri, “osinkhasinkha” m’mapemphero ndi m’njira zawo zonse. (Yakobo 1:5-8) Chotero tiyeni tikhale ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatithandiza kuwona ziyeso zathu moyenera ndi kuzipirira. Tingakumbutsidwe Malemba ndi okhulupirira anzathu kapena paphunziro Labaibulo. Zochitika zoyendetsedwa ndi kakonzedwe ka Mulungu zikhoza kutithandiza kuwona zimene tiyenera kuchita. Angelo angakhale ndi phande m’kutitsogoza, kapena tingalandire chitsogozo cha mzimu woyera. (Ahebri 1:14) Chinthu chachikulu ndicho kupempherera nzeru modalira kotheratu pa Mulungu wathu wachikondi.—Miyambo 3:5, 6.
Kumbukirani Kuti Yehova Amapereka Chitonthozo
Paulo mwapemphero anadalira pa Yehova ndipo anamdziŵa kukhala Magwero a chitonthozo. Mtumwiyo analemba kuti: “Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m’nsautso iriyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.”—2 Akorinto 1:3, 4.
Mulungu wa chitonthozo chonse amadziŵa mavuto onse ogwera atumiki ake ndipo amafuna kuwapatsa mpumulo. Ponena za nkhaŵa ya Paulo kaamba ka Akorinto, mpumulo unadza kupyolera mwa Mkristu mnzake Tito. Imeneyi ndiimodzi ya njira zimene tingatonthozedwe nazo lerolino. Chifukwa chake, pamene tiri m’nsautso, tiyenera kupeŵa kudzilekanitsa ndi ena. (Miyambo 18:1) Kuyanjana ndi Akristu anzathu ndiimodzi ya njira zimene Mulungu amatitonthozera. Mwina tingalingalire kuti: ‘Ndiri wosweka mtima kwambiri kotero kuti ndiribe nyonga zokwanira zokhalira pamodzi ndi mabwenzi Achikristu.’ Chikhalirechobe, tiyenera kulimbana ndi malingaliro otero kuti tisadzimane chitonthozo chimene okhulupirira anzathu angapereke.
Musasiye!
Mwina ena a ife sitinakumanepo ndi chiyeso champhamvu motero chotichititsa kupsinjika maganizo kwambiri. Koma nthenda zofooketsa, imfa ya mnzathu wamuukwati, kapena mkhalidwe wina wopereka chiyeso kwambiri zingachititse kupsinjika maganizo. Ngati zimenezo zingachitike, tisalingalire konse kuti kwenikweni tiri odwala mwauzimu. Munthu wopsinjika maganizo angakhalenso woyeneretsedwa kaamba ka utumiki wa Mulungu, ngakhale kutha kuthandiza ena mwauzimu. Paulo anafulumiza abale “kulankhula motonthoza kwa miyoyo yopsinjika,” osati monyumwa kulingalira kuti anachita kanthu kolakwa ndipo ngodwala mwauzimu. (1 Atesalonika 5:14, NW) Ngakhale kuti nthaŵi zina kupsinjika maganizo kumachititsidwa ndi kuchimwa ndi liwongo, sindimo mmene ziliri ndi amene akutumikira Mulungu ndi mtima woyera. Kulambira kwawo, mwinamwake koperekedwa movutikira kwambiri, nkolandirika kwa Yehova. Amaŵakonda ndipo amaŵapatsa chithandizo chofunikira ndi chitonthozo.—Salmo 121:1-3.
Ziŵalo za otsalira a Israyeli wauzimu zinavutika maganizo kwadzawoneni ndi ziyeso m’chaka cha 1918. (Yerekezerani ndi Agalatiya 6:16.) Ntchito yawo yakulalikira inatsala nenene kuwonongedwa, ena a iwo anaponyedwa m’ndende opanda mlandu, ndipo ambiri mwa amene kale anali oyanjana nawo anakhala osakhulupirika, ampatuko otsutsa. Ndiponso, odzozedwa okhulupirikawo sanamvetsetse chifukwa chimene Mulungu analolera zonsezo kuchitika. Kwa nthaŵi yakutiyakuti ‘anabzala ndi misozi,’ koma sanasiye. Anapitirizabe kutumikira Yehova ndiponso anadzipenda. Kodi chotulukapo chinali chotani? ‘Anabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yawo.’ (Salmo 126:5, 6) Tsopano odzozedwa amazindikira kuti Mulungu analola ziyeso zotero kuti aŵayeretse kaamba ka ntchito yawo yakututa yadziko lonse yomwe inkayandikira.
Ngati tingapsinjike maganizo chifukwa chokumana ndi ziyeso zosiyanasiyana, tingathe kupindula ndi chokumana nacho cha otsalira odzozedwa. Mmalo mosiya, tipitirizetu kuchita chabwino, ngakhale ngati tiyenera kutero tikumalira. Mkupita kwa nthaŵi, njira yochokera m’ziyeso zathu idzapezeka, ndipo ‘tidzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera.’ Inde, chimwemwe—chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu—chidzakhala chathu pokhala titapirira ziyeso zathu. Kwa ife, Yehova adzatsimikiziradi kukhala “Mulungu wa chitonthozo chonse.”