Yehova Amakonda Opatsa Mokondwerera
‘Yense achite monga anatsimikiza mtima, simwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda [wopatsa, “NW”] mokondwerera.’—2 AKORINTO 9:7.
1. Kodi ndimotani mmene Mulungu ndi Kristu akhalira opatsa mokondwera?
YEHOVA anali wopatsa mokondwera woyamba. Mwachimwemwe anapatsa moyo kwa Mwana wake wobadwa yekha namgwiritsira ntchito kuchititsa angelo ndi anthu kukhalako. (Miyambo 8:30, 31; Akolose 1:13-17) Mulungu anatipatsa moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse, kuphatikizapo mvula yochokera kumwamba ndi nyengo zobala zipatso, kudzaza mitima yathu ndi chikondwerero chachikulu. (Machitidwe 14:17; 17:25) Ndithudi, onse aŵiri Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ali opatsa mokondwera. Amapatsa mosangalala ndi mopanda dyera. Yehova anakonda dziko la anthu kwambiri moti ‘anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.’ Ndipo Yesu mosaŵiringula ‘anapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’—Yohane 3:16; Mateyu 20:28.
2. Malinga ndi kunena kwa Paulo, kodi Mulungu amakonda wopatsa wamtundu wanji?
2 Chifukwa chake, atumiki a Mulungu ndi Kristu ayenera kukhala opatsa mokondwera. Kupatsa koteroko kunalimbikitsidwa m’kalata yachiŵiri ya mtumwi Paulo kwa Akristu a ku Korinto, yolembedwa pafupifupi 55 C.E. Mwachiwonekere akumaloza ku zopereka zandalama zodzifunira zaumwini zopangidwa kuthandiza makamaka Akristu osoŵa mu Yerusalemu ndi Yudeya, Paulo anati: ‘Yense achite monga anatsimikiza mtima, simwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda [wopatsa] mokondwera.’ (2 Akorinto 9:7; Aroma 15:26; 1 Akorinto 16:1, 2; Agalatiya 2:10) Kodi anthu a Mulungu aulabadira motani mwaŵi wakupatsa? Ndipo kodi uphungu wa Paulo wonena za kupatsa umatiphunzitsanji?
Kusonkhezeredwa ndi Mitima Yofunitsitsa
3. Kodi ndikuukulu wotani umene Aisrayeli anachirikizira kumangidwa kwa chihema cholambirira Yehova?
3 Mitima yofunitsitsa imasonkhezera anthu a Mulungu kudzipereka iwo eni ndi chuma chawo kuchirikiza chifuno cha Mulungu. Mwachitsanzo, Aisrayeli a m’nthaŵi ya Mose anachirikiza mwachimwemwe kumangidwa kwa chihema cholambirira Yehova. Mitima ya akazi ena inawasonkhezera kupota ubweya wa mbuzi, pamene amuna ena anatumikira monga amisiri. Anthu anapereka mokondwera golidi, siliva, matabwa, bafuta, ndi zinthu zina monga ‘chopereka cha Yehova’ chodzifunira. (Eksodo 35:4-35) Anali owoloŵa manja kwambiri moti zinthu zoperekedwa ‘zinakwanira ntchito yonse [yoti] ichitike, zinatsalakonso.’—Eksodo 36:4-7.
4. Kodi Davide ndi anthu ena anali ndi mkhalidwe wamaganizo wotani popanga zopereka ku kachisi?
4 Zaka mazana ambiri pambuyo pake, Mfumu Davide anapereka zochuluka ku kachisi wa Yehova yemwe akamangidwa ndi Solomo mwana wake. Popeza kuti Davide ‘anakondwera nayo nyumba ya Mulungu,’ anapereka ‘chuma chakechake’ cha golidi ndi siliva. Akalonga, mafumu, ndi ena “anadzipatulira [ndi mphatso, NW] kwa Yehova.” Ndi chotulukapo chotani? Eya, ‘anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu, pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova’! (1 Mbiri 29:3-9) Iwo anali opatsa mokondwera.
5. Kodi Aisrayeli anachirikiza motani kulambira kowona kwa zaka mazana ambiri?
5 Kwa zaka mazana ambiri, Aisrayeli anali ndi mwaŵi wakuchirikiza chihema, akachisi apambuyo pake, ndi mautumiki aunsembe ndi a Alevi kumeneko. Mwachitsanzo, Ayuda m’nthaŵi ya Nehemiya anatsimikiza mtima kupanga zopereka kusunga kulambira koyera, pozindikira kuti sanafunikire kunyalanyaza nyumba ya Mulungu. (Nehemiya 10:32-39) Mofananamo lerolino, Mboni za Yehova mokondwera zimapanga zopereka zodzifunira kumanga ndi kusamalira malo osonkhanira ndi kuchirikiza kulambira kowona.
6. Perekani zitsanzo za kupatsa mokondwera kwa Akristu.
6 Akristu oyambirira anali opatsa mokondwera. Mwachitsanzo, Gayo anali kuchita “ntchito yokhulupirika” mwakukhala wochereza kwa oyendayenda opititsa patsogolo zabwino za Ufumu, monga momwedi Mboni za Yehova zimasonyezera kuchereza kwa oyang’anira oyendayenda otumizidwa tsopano ndi Watch Tower Bible and Tract Society. (3 Yohane 5-8, NW) Pamakhala zowonongedwa kutheketsa abale ameneŵa kuyendera mipingo ndi kusonyeza kuchereza kwa iwo, koma kuteroko kumakhala kopindulitsa mwauzimu motani nanga!—Aroma 1:11, 12.
7. Kodi Afilipi anagwiritsira ntchito motani chuma chawo chakuthupi?
7 Mipingo yonse yagwiritsira ntchito chuma chawo chakuthupi kupititsa patsogolo zabwino za Ufumu. Mwachitsanzo, Paulo anauza okhulupirira ku Filipi kuti: ‘Pakuti m’Tesalonikanso munanditumizira pa chosoŵa changa kamodzi kapena kaŵiri. Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiŵerengero chanu.’ (Afilipi 4:15-17) Afilipi anapatsa mokondwera, koma kodi ndizinthu ziti zimene zimasonkhezera kupatsa mokondwera chotero?
Kodi Nchiyani Chimene Chimasonkhezera Kupatsa Mokondwera?
8. Kodi mungatsimikizire motani kuti mzimu wa Mulungu umasonkhezera anthu ake kukhala opatsa mokondwera?
8 Mzimu Woyera wa Yehova, kapena mphamvu yogwira ntchito, umasonkhezera anthu ake kukhala opatsa mokondwera. Pamene Akristu a ku Yudeya anali osoŵa, mzimu wa Mulungu unasonkhezera okhulupirira ena kuwathandiza mwakuthupi. Kuti alimbikitse Akristu ku Korinto kuchita changu popanga zopereka zoterozo, Paulo anatchula chitsanzo cha mipingo ya ku Makedoniya. Ngakhale kuti okhulupirira a ku Makedoniya anali kuvutika ndi chizunzo ndi usiwa, anasonyeza chikondi chaubale mwakupatsa koposa pakukhoza kwawo kwenikweniko. Iwo anapemphadi mwaŵi wa kupatsa! (2 Akorinto 8:1-5) Chifuniro cha Mulungu sichimadalira kotheratu pazopereka za olemera. (Yakobo 2:5) Atumiki ake odzipatulira osauka mwakuthupi akhala magwero aakulu a ndalama zochirikizira ntchito yakulalikira Ufumu. (Mateyu 24:14) Komabe, samavutika chifukwa cha kuoloŵa manja kwawo, pakuti Mulungu mosalephera amapereka zosoŵa za anthu ake m’ntchitoyi, ndipo mphamvu yochirikiza kupitiriza kwake ndi chiwonjezeko ndiyo mzimu wake.
9. Kodi chikhulupiriro, chidziŵitso, ndi chikondi ziri zogwirizana motani ndi kupatsa mokondwera?
9 Kupatsa mokondwera kumasonkhezeredwa ndi chikhulupiriro, chidziŵitso, ndi chikondi. Paulo anati: ‘Koma monga muchulukira [Akorinto] m’zonse, m’chikhulupiriro, ndi m’mawu, ndi m’chidziŵitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m’chisomo ichi. Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena chowonadi cha chikondi chanunso.’ (2 Akorinto 8:7, 8) Kupanga zopereka zochirikiza chifuniro cha Yehova, makamaka pamene wopatsayo ali wosoŵa, kumafunikiritsa chikhulupiriro m’makonzedwe amtsogolo a Mulungu. Akristu omachuluka m’chidziŵitso amafuna kutumikira chifuno cha Yehova, ndipo omachuluka m’chikondi pa iye ndi anthu ake amagwiritsira ntchito mokondwera chuma chawo kupititsa patsogolo chifuniro chake.
10. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti chitsanzo cha Yesu chimasonkhezera Akristu kupatsa mokondwera?
10 Chitsanzo cha Yesu chimasonkhezera Akristu kupatsa mokondwera. Atafulumiza Akorinto kupatsa mosonkhezeredwa ndi chikondi, Paulo anati: ‘Pakuti mudziŵa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.’ (2 Akorinto 8:9) Ngakhale kuti anali wolemera koposa mwana aliyense wa Mulungu kumwamba, Yesu anadzikhuthula kusiya ulemererowo natenga moyo waumunthu. (Afilipi 2:5-8) Komabe, mwakukhala wosauka mwanjira yopanda dyerayi, Yesu anathandiza m’kuyeretsa dzina la Yehova napereka moyo wake monga nsembe yadipo kuti anthu amene akailandira akapindule. Momvana ndi chitsanzo cha Yesu, kodi nafenso sitiyenera kuthandiza ena mokondwera ndi kukhala ndi phande m’kuyeretsa dzina la Yehova?
11, 12. Kodi kulinganiza kwabwino kungatipangitse motani kukhala opatsa mokondwera?
11 Kulinganiza kwabwino kumatheketsa kupatsa mokondwera. Paulo anauza Akorinto kuti: ‘Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.’ (1 Akorinto 16:1, 2) Mwanjira yofananayo yaumwini ndi yodzifunira, amene afuna kupanga zopereka kuchirikiza ntchito ya Ufumu lerolino adzachita bwino kuika padera zina za ndalama zawo kaamba ka chifuno chimenecho. Monga chotulukapo cha kulinganiza kwabwino kotero, Mboni iriyonse, mabanja, ndi mipingo angapange zopereka kupititsa patsogolo kulambira kowona.
12 Kugwiritsira ntchito makonzedwe akupanga zopereka kumatikondweretsa. Monga momwedi Yesu ananenera, “muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa ndi chimene chiri m’kulandira.” (Machitidwe 20:35, NW) Choncho Akorinto akawonjezera chimwemwe chawo mwakutsatira uphungu wa Paulo wakuchita makonzedwe awo achaka chonse akutumiza ndalama ku Yerusalemu. ‘Munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, simonga chimsoŵa,’ iye anatero. Pamene munthu apanga zopereka monga momwe ali nazo, ziyenera kuwonedwa kukhala zamtengo wapatali. Ngati timdalira Mulungu, angalinganize zinthu kotero kuti amene ali ndi zochuluka akhale ooloŵa manja, osati owawanya, ndikuti amene ali ndi zochepa asakhale ndi kusoŵa kumene kungachepetse nyonga yawo ndi maluso akumtumikira.—2 Akorinto 8:10-15.
Kusamalira Bwino Zopereka
13. Kodi nchifukwa ninji Akorinto anali ndi chidaliro m’kuyang’aniridwa kwa zopereka kochitidwa ndi Paulo?
13 Ngakhale kuti Paulo anayang’anira kakonzedwe ka zopereka kotero kuti okhulupirira osoŵa akakhoze kulandira chithandizo chakuthupi ndi kukangalika koposa m’ntchito yolalikira, iye ngakhale enawo sanatenge iriyonse ya ndalamazo monga malipiro a utumiki wawo. (2 Akorinto 8:16-24; 12:17, 18) Paulo anagwira ntchito kuti apeze zosoŵa zake zakuthupi mmalo moika vuto landalama pampingo uliwonse. (1 Akorinto 4:12; 2 Atesalonika 3:8) Chifukwa chake, pompatsa zopereka Akorinto anali kuziikizira kwa mtumiki wa Mulungu wokhulupirika, wogwira ntchito zolimba.
14. Ponena za kagwiritsiridwe ka zopereka, kodi Watch Tower Society iri ndi mbiri yotani?
14 Chiyambire pamene Watch Tower Bible and Tract Society inaloledwa mwalamulo mu 1884, opanga zopereka akhala ndi umboni wakuti ndilo bungwe lokhulupirika loyang’anira zopereka zonse zoikiziridwa pa ilo kaamba ka ntchito ya Ufumu wa Yehova. Malinga ndi kunena kwa tchata chake, Sosaite imakalimira kukwaniritsa chosoŵa chachikulu cha anthu onse, chosoŵa chauzimu. Kumeneku kumachitidwa mumpangidwe wa mabuku ofotokoza Baibulo ndi malangizo a mmene angapezere chipulumutso. Lerolino, Yehova akufulumiza kusonkhanitsidwa kwa anthu onga nkhosa m’gulu lake lomakulakulabe, ndipo dalitso lake pakagwiritsiridwe kanzeru ka zopereka m’ntchito yolalikira Ufumu ndilo umboni wowonekera bwino wa chivomerezo chake. (Yesaya 60:8, 22) Tiri ndi chidaliro chakuti adzapitirizabe kusonkhezera mitima ya opatsa mokondwera.
15. Kodi nchifukwa ninji magazini ano nthaŵi zina amatchula zopereka?
15 Nthaŵi zina Sosaite imalemba m’magazini ano kukumbutsa oŵerenga za mwaŵi wawo wa kupanga zopereka zodzifunira ku ntchito ya padziko lonse yolalikira Ufumu. Kumeneku sindiko kupempha ndalama, koma kuli kukumbutsa onse okhumba kuchirikiza “ntchito yopatulika ya uthenga wabwino” pakuti Mulungu amawadalitsa. (Aroma 15:16, NW; 3 Yohane 2) Sosaite imagwiritsira ntchito ndalama zonse zoperekedwazo mwanjira yosamalitsa kotero kuti idziŵikitse dzina la Yehova ndi Ufumu wake. Zopereka zonse zimalandiridwa moyamikirika, kulengezedwa, ndi kugwiritsiridwa ntchito m’kubukitsa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Mwachitsanzo, kupyolera mwa zimenezi ntchito yaumishonale imachirikizidwa m’maiko ambiri, ndipo malo osindikizira ofunika kaamba ka kuwanditsa chidziŵitso cha Baibulo amasamaliridwa ndi kufutukulidwa. Ndiponso, zopereka ku ntchito ya padziko lonse zimagwiritsiridwa ntchito kulipirira mitengo yomakwera yosindikizira Mabaibulo ndi zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo pamodzi ndi makaseti a tepu ndi a video. Mwanjira zotero zabwino za Ufumu zimapititsidwa patsogolo ndi opatsa mokondwera.
Osati Mokakamiza
16. Ngakhale kuti Mboni za Yehova zambiri sizolemera mwakuthupi, kodi nchifukwa ninji zopereka zawo zimayamikiridwa?
16 Mboni za Yehova zambiri sizolemera mwakuthupi. Ngakhale kuti zingapereke ndalama zochepa kupititsa patsogolo zabwino za Ufumu, zopereka zawo nzazikulube. Pamene Yesu anawona mkazi wamasiye wosauka akuponya timakobiri tiŵiri tamtengo wochepa m’bokosi losungira ndalama la m’kachisi, anati: ‘Wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse; pakuti onse ameneŵa [opereka ena] anaika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma iye mwa kusoŵa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.’ (Luka 21:1-4) Ngakhale kuti mphatso yake inali yaing’ono, mkaziyo anali wopatsa mokondwera—ndipo chopereka chake chinayamikiridwa.
17, 18. Kodi mfundo yeniyeni ya mawu a Paulo pa 2 Akorinto 9:7 njotani, ndipo kodi nchiyani chikusonyezedwa ndi liwu Lachigiriki lomasuliridwa “mokondwera”?
17 Ponena za chithandizo choyenera kuperekedwa kwa Akristu a ku Yudeya, Paulo anati: ‘Yense achite monga anatsimikiza mtima, simwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda [wopatsa] mokondwera.’ (2 Akorinto 9:7) Mtumwiyo angakhale analoza kuchigawo cha Miyambo 22:8 m’matembenuzidwe a Septuagint, chimene chimati: “Mulungu amadalitsa wopatsa mokondwera; ndipo adzapereka zosoŵa za ntchito yake.” (The Septuagint Bible, lotembenuzidwa ndi Charles Thomson) Paulo anagwiritsira ntchito “amakonda” mmalo mwa “amadalitsa,” koma pali kugwirizana, pakuti kupezeka kwa madalitso kumachititsidwa ndi chikondi cha Mulungu.
18 Wopatsa mokondwera amasangalaladi ndi kupatsa. Eya, liwu lakuti “wosangalala” latengedwa ku liwu Lachigiriki lomasuliridwa “mokondwera” pa 2 Akorinto 9:7! Atatchula zimenezi, katswiri R. C. H. Lenski anati: “Mulungu amakonda wopatsa mosangalala, mwachimwemwe, mokondwa . . . [amene] chikhulupiriro chake chimadzala ndi chikondwerero pamene mwaŵi wina wa kupatsa umfikira.” Munthu amene ali ndi mkhalidwe wachimwemwe wotero samapatsa moŵiringula kapena mokakamiza koma amapatsa ndi mtima wake wonse. Kodi inu muli wokondwera motero ponena za kupatsa kuchirikiza zabwino za Ufumu?
19. Kodi Akristu oyambirira anapanga motani zopereka?
19 Akristu oyambirira sanayendetse mbale zosonkhanitsira zopereka kapena kugwiritsira ntchito chachikhumi mwakupereka chigawo chimodzi mwa zigawo khumi za ndalama zawo kuchirikiza zifuno za chipembedzo. Mmalomwake, zopereka zawo zinali zodzifunira kotheratu. Tertullian, amene anatembenuzidwira ku Chikristu pafupifupi 190 C.E., analemba kuti: “Ngakhale kuti tiri ndi mabokosi athu a ndalama, ndalamazo sizogulira chipulumutso, ngati kuti chipembedzo chiri ndi mtengo wochigulira. Patsiku la mwezi [mwachiwonekere kamodzi pamwezi], aliyense ngati afuna, amaponyamo chopereka chochepa; koma kokha pamene chiri chikhumbo chake, ndipo kokha ngati ngwokhoza; pakuti palibe kukakamiza; zonse nzodzifunira.”—Apology, Mutu XXXIX.
20, 21. (a) Kodi nchiyani chimene kope lakumbuyoku la magazini ano linanena ponena za mwaŵi wa kuchirikiza chifuniro cha Mulungu ndi ndalama, ndipo zimenezi zimagwira ntchito motani ngakhale lerolino? (b) Kodi chimachitika nchiyani pamene tilemekeza Yehova ndi chuma chathu?
20 Nthaŵi zonse kupatsa modzifunira kwakhala chizoloŵezi cha atumiki a Yehova amakono. Komabe, nthaŵi zina ena sanaugwiritsire ntchito mokwanira mwaŵi wawo wa kuchirikiza chifuniro cha Mulungu mwakupanga zopereka. Mwachitsanzo, mu February 1883 magazini ano anati: “Ena akusenzera anzawo mavuto azandalama ochuluka kwambiri, moti mphamvu yawo ya kupereka chithandizo cha zandalama ikuzimiririka chifukwa chogwira ntchito mopambanitsa ndi kutopa, ndipo motero phindu lawo limawonongeka; ndipo sizokhazo, komanso amene . . . sanamvetsetse mkhalidwewo, ataya mwaŵi wa kulandira madalitso chifukwa cha liuma lawo popanga zopereka zandalama.”
21 Pamene khamu lalikulu likuloŵa m’gulu la Yehova lerolino, ndipo ntchito ya Mulungu ikufutukuka Kum’maŵa kwa Yuropu ndi madera ena kumene inali yoletsedwa kalelo, pali kufunika kowonjezereka kwa kufutukulidwa kwa zosindikizira ndi malo ena. Mabaibulo owonjezereka ndi zofalitsidwa zina ziyenera kusindikizidwa. Zimango zateokratiki zochuluka zikuchitika; komabe, zina zingamalizidwe mofulumira koposa ngati panali ndalama zokwanira. Ndithudi, tiri ndi chikhulupiriro kuti Mulungu adzapereka zofunikira, ndipo tidziŵa kuti amene ‘alemekeza Yehova ndi chuma chawo chonse’ adzadalitsidwa. (Miyambo 3:9, 10) Indetu, ‘iye wakufesa mooloŵa manja, mooloŵa manjanso adzatuta.’ Yehova ‘adzatilemeretsa m’zonse ku kuoloŵa manja konse,’ ndipo kupatsa kwathu mokondwera kudzachititsa ambiri kumyamikira ndi kumtamanda.—2 Akorinto 9:6-14.
Sonyezani Chiyamikiro Chanu pa Mphatso za Mulungu
22, 23. (a) Kodi mphatso yaulere ya Mulungu yosaneneka njotani? (b) Popeza kuti timayamikira mphatso za Yehova, kodi tiyenera kuchitanji?
22 Mosonkhezeredwa ndi chiyamikiro chakuya, Paulo mwiniyo anati: ‘Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.’ (2 Akorinto 9:15) Monga “nsembe yolipa” machimo a Akristu odzozedwa ndi a dziko, Yesu ndiye maziko ndi njira yodzeramo mphatso yaulere ya Yehova yosaneneka. (1 Yohane 2:1, 2, NW) Mphatso imeneyo ndiyo ‘chisomo choposa cha Mulungu’ chimene wasonyeza kwa anthu ake padziko lapansi kupyolera mwa Yesu Kristu, ndipo chichuluka kuchipulumutso chawo ndi kuulemerero ndi kulemekezedwa kwa Yehova.—2 Akorinto 9:14.
23 Chiyamikiro chathu chakuya chipitetu kwa Yehova kaamba ka mphatso yaulere yosaneneka ndi mphatso zina zambiri zauzimu ndi zakuthupi zimene wapatsa anthu ake. Eya, ubwino wa Atate wathu wakumwamba pa ife ngwodabwitsa kwambiri moti uposa mphamvu zaumunthu za kuyamikira! Ndipo uyeneradi kutifulumiza kukhala opatsa mokondwera. Pamenepo, ndi chiyamikiro chochokera mumtima, tiyeni tichitetu zonse zimene tingathe kupititsa patsogolo chifuniro cha Mulungu wathu wooloŵa manja, Yehova, Wopatsa woyamba ndi wamkulu koposa!
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi mitima yofunitsitsa yasonkhezera anthu a Yehova kuchitanji?
◻ Kodi chimene chimasonkhezera kupatsa mokondwera nchiyani?
◻ Kodi ndimotani mmene Watch Tower Society imagwiritsirira ntchito zopereka zonse zimene imalandira?
◻ Kodi Mulungu amakonda wopatsa motani, ndipo kodi tiyenera kusonyeza motani chiyamikiro chathu kaamba ka mphatso Zake zochuluka?
[Chithunzi patsamba 15]
Pamene chihema chinali kumangidwa, Aisrayeli anagwira ntchito mwaufulu napanga zopereka kwa Yehova mooloŵa manja
[Chithunzi patsamba 18]
Zopereka zonga za mkazi wamasiye waumphaŵi zimayamikiridwa ndipo nzazikulu