Tukiko—Kapolo Mnzake Wokhulupirika
PA ZOCHITIKA zosiyanasiyana, Tukiko anali kuyenda ndi mtumwi Paulo ndipo anali ngati mthenga wake. Anali nthumwi imene ikanapatsiridwa ndalama ndiponso uyang’aniro. Popeza kuti Malemba amafotokoza kuti iye anali wokhulupirika—khalidwe lofunika kwa Akristu onse—mwina mungakonde kudziŵa zambiri ponena za iye.
Paulo anati Tukiko anali ‘mbale [wake] wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzake mwa Ambuye.’ (Akolose 4:7) Kodi nchifukwa chiyani mtumwiyo ananena tero?
Ntchito Yokapereka Thandizo ku Yerusalemu
Cha m’ma 55 C.E., Akristu a ku Yudeya anali kufunikira thandizo lakuthupi. Mothandizidwa ndi mipingo ya ku Ulaya ndi Asia Minor, Paulo analinganiza zosonkhanitsa thandizolo kuti akawapatse. Tukiko, amene ankachokera ku chigawo cha Asia, anali nawo paulendo wokapereka thandizowo.
Atawapatsa malangizo a mmene anayenera kupangira zoperekazi, Paulo analingalira kuti amuna odalirika atumidwe ku Yerusalemu kapena atsagane naye, kuti akatule zoperekazo. (1 Akorinto 16:1-4) Pamene anali paulendo wautali wochokera ku Greece kupita ku Yerusalemu, anatsagana ndi anthu ambiri, mmodzi wa iwo mwachionekere anali Tukiko. (Machitidwe 20:4) Kunalidi kofunikira kuti akhale ambiri chifukwa ananyamula ndalama zimene mipingo yambiri inawapatsira. Iwo ayenera kuti anayenda motero makamaka ncholinga chotetezera ndalamazo ku anthu olanda omwe ankakonda kukhalizira anthu m’njiramo.—2 Akorinto 11:26.
Popeza kuti Aristarko ndi Trofimo anatsagana ndi Paulo kupita ku Yerusalemu, ena amalingalira kuti mwina Tukiko ndi enanso anali nawo paulendowo. (Machitidwe 21:29; 24:17; 27:1, 2) Chifukwa chakuti Tukiko anali nawo pa programu yokapereka thandizoyi, iye ali mmodzi mwa anthu angapo amene amawaganizira kuti ndi “mbaleyo” amene ankasonkhanitsa zopereka ndi Tito ku Greece ndi amene “anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi [Paulo] m’chisomo ichi.” (2 Akorinto 8:18, 19; 12:18) Ngati ntchito yoyamba imene Tukiko anachita inafuna kudalirika, yachiŵiri inalinso yotero.
Kuchoka ku Roma Kupita ku Kolose
Patapita zaka zisanu kapena zisanu ndi chimodzi (60-61 C.E.), Paulo anali kuyembekezera kuti atulutsidwe m’ndende atamangidwa koyamba ku Roma. Tukiko anali naye limodzi, makilomita mazanamazana kuchokera kwawo. Tsopano Tukiko anali kubwerera ku Asia. Zimenezi zinatheketsa kuti Paulo atumize makalata ku mipingo yachikristu m’deralo ndi kutumizanso Onesimo, wantchito wa Filemoni yemwe anali atathaŵa, kuti abwerere ku Kolose. Tukiko ndi Onesimo ananyamula makalata ngati atatu amene tsopano ali mbali ya mabuku ovomerezedwa a m’Baibulo—imodzi kwa Aefeso, ina kwa Akolose, ndi ina kwa Filemoni. Angakhalenso atakapereka kalata ina ku mpingo wa ku Laodikaya, mzinda womwe unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 18 kuchokera ku Kolose.—Aefeso 6:21; Akolose 4:7-9, 16; Filemoni 10-12.
Tukiko sanali wopereka makalata chabe. Anali mthenga wankhani zaumwini wokhulupirika, pakuti Paulo analemba kuti: “Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye: amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichi chomwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu.”—Akolose 4:7, 8.
Katswiri wamaphunziro E. Randolph Richards anati wokapereka kalata “kaŵirikaŵiri ankagwirizanitsa wolemba ndi olandira, kuwonjezera pa kugwirizanitsidwa ndi kalatayo. . . . [Chifukwa china] chofunira wokapereka wokhulupirika chinali [chakuti] ankanenanso zowonjezereka. Kalata ingalongosole mkhalidwe wina wake mwachidule chabe, ndipo nthaŵi zochuluka zimenezi zinkachitika malinga ndi mmene wolembayo waonera, koma wokaperekayo ankayembekezeredwa kuti akafotokozere olandirawo mwatsatanetsatane.” Ngakhale kuti mwina kalata inali kulongosola ziphunzitso ndi nkhani zamwamsanga, zinthu zina zinali kunenedwa mwa pakamwa ndi mthenga wokhulupirika.
Makalata a kwa Aefeso, Akolose, ndi Filemoni sanena zambiri za mmene Paulo anali kukhalira. Motero Tukiko anafunikira kufotokoza nkhani zaumwini, zimene Paulo anali kukumana nazo ku Roma, ndi kumvetsetsa bwino kwambiri mmene zinthu zinalili m’mipingo kuti athe kupereka chilimbikitso. Mauthenga ndi ntchito yonga imeneyi inali kupatsidwa kokha kwa anthu omwe anali kuwadalira kuti akaimira wotumizayo mokhulupirika. Tukiko anali munthu wotereyo.
Uyang’aniro m’Magawo Akutali
Atamasulidwa ku ukayidi wapanyumba ku Roma, Paulo ankalingalira zotumiza Tukiko kapena Artema kuti akakumane ndi Tito pachisumbu cha Krete. (Tito 1:5; 3:12) Pamene Paulo anaikidwa m’ndende kachiŵiri ku Roma (mwinamwake cha m’ma 65 C.E.), mtumwiyu anatumizanso Tukiko ku Efeso, mwina kuti akaloŵe mmalo mwa Timoteo amene anafunika kuti apite kukakhala ndi Pauloyo.—2 Timoteo 4:9, 12.
Sizikudziŵika ngati Tukiko anapita ku Krete ndi ku Efeso komwe paulendo uwu. Komabe, maumboni ngati ameneŵa amasonyeza kuti iye anakhalabe mmodzi wa mabwenzi apamtima a Paulo mpaka zaka zakumapeto zautumiki wa mtumwiyo. Ngati Paulo ankaganiza zomtumiza ku maulendo ofunika munthu wodalirika, ndipo mwinanso maulendo ovuta, m’malo mwa Timoteo ndi Tito, nzachionekere kuti Tukiko anali atakhala woyang’anira wachikristu wokhwima. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 1:3; Tito 1:10-13.) Kufunitsitsa kwake kuti aziyenda ndi kugwiritsiridwa ntchito m’magawo akutali, kunampangitsa kukhala wofunika kwa Paulo ndi kwa mpingo wonse wachikristu.
Lerolino, Akristu odzipereka mofunitsitsa amatumikira Mulungu m’mipingo ya Mboni za Yehova ya m’madera a kwawo kapena amadzipereka kuti akapititse patsogolo zinthu za Ufumu ku madera ena. Anthu ena zikwizikwi alola kutumikira monga amishonale, oyang’anira oyendayenda, atumiki a padziko lonse m’ntchito zachimango, kulikulu la Watch Tower Society, kapena pa imodzi mwa nthambi zake. Monga Tukiko, iwo si otchuka, koma amagwira ntchito zolimba, ‘atumiki okhulupirika’ amene Mulungu amawakonda ndiponso Akristu ena amawakonda monga ‘akapolo anzawo [okhulupirika] mwa Ambuye.’