“Mubwere Nalo Limodzi Limodzi Lonse la Khumi ku Nyumba Yosungiramo”
“Mundiyese nako tsono, . . . ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba.”—MALAKI 3:10.
1. (a) M’zaka za zana lachisanu B.C.E., kodi nchiitano chotani chimene Yehova anapereka kwa anthu ake? (b) M’zaka za zana loyamba C.E., kodi nchiyani chinali chotulukapo chakudza kwa Yehova kukachisi kudzapereka chiweruzo?
M’ZAKA za zana lachisanu B.C.E., Aisrayeli anali osakhulupirika kwa Yehova. Anali ataleka kupereka zakhumi ndipo anabweretsa zoŵeta zopuwala pakachisi monga nsembe. Komabe, Yehova analonjeza kuti ngati iwo akabweretsa zakhumi zonse m’nyumba yosungira, iye akatsanulira madalitso kufikira pakasoŵa malo owaikapo. (Malaki 3:8-10) Pafupifupi zaka 500 pambuyo pake, Yehova, moimiridwa ndi Yesu monga mthenga Wake wa chipangano, anadza kukachisi ku Yerusalemu kudzapereka chiweruzo. (Malaki 3:1) Israyeli monga mtundu anapezeka kukhala wopereŵera, koma aliyense wa amene anabwerera kwa Yehova anadalitsidwa molemerera. (Malaki 3:7) Anadzozedwa kukhala ana auzimu a Mulungu, chilengo chatsopano, “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16; Aroma 3:25, 26.
2. Kodi ndiliti pamene Malaki 3:1-10 anali kudzakhala ndi kukwaniritsidwa kwachiŵiri, ndipo kodi tikupemphedwa kuchitanji mogwirizana ndi zimenezi?
2 Pafupifupi zaka 1,900 pambuyo pa zimenezi, mu 1914, Yesu anaikidwa pampando wachifumu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, ndipo mawu ouziridwa mwaumulungu pa Malaki 3:1-10 anali pafupi kukwaniritsidwa kachiŵiri. Mogwirizana ndi chochitika chochititsa nthumanzi chimenechi, Akristu lerolino akupemphedwa kubweretsa chakhumi chonse m’nyumba yosungiramo. Ngati titero, nafenso tidzalandira madalitso kufikira pakasoŵa malo owaikapo.
3. Kodi ndani amene anali mthenga wokonzekera njira pamaso pa Yehova (a) m’zaka za zana loyamba? (b) nkhondo yadziko yoyamba isanaulike?
3 Ponena za kudza kwake kukachisi, Yehova anati: “Tawonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga.” (Malaki 3:1) Monga kukwaniritsidwa kwa m’zaka za zana loyamba kwa zimenezi, Yohane Mbatizi anadza ku Israyeli akumalalikira za kulapa machimo. (Marko 1:2, 3) Kodi panali ntchito yokonzekera kudza kwachiŵiri kwa Yehova kukachisi wake? Inde. M’zaka makumi ambiri nkhondo yadziko yoyamba isanaulike, Ophunzira Baibulo anawonekera pankhope ya dziko lapansi akumaphunzitsa chiphunzitso choyera cha Baibulo ndi kuulula mabodza otonza Mulungu, onga chiphunzitso cha Utatu ndi cha helo wamoto. Anachenjezanso za kufika kwa mapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914. Ambiri analabadira mawu a onyamula kuunika kwa chowonadi amenewa.—Salmo 43:3; Mateyu 5:14, 16.
4. Kodi ndifunso lotani limene linafunikira kuyankhidwa m’tsiku la Ambuye?
4 Chaka cha 1914 chinayambitsa nyengo imene Baibulo limatcha “tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:10) Zochitika zosaiŵalika zinali kudzachitika mkati mwa tsiku limenelo, kuphatikizapo kudziŵika kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi kuikidwa kwa ameneyo kukhala “woyang’anira zinthu [za Ambuye wake] zonse.” (Mateyu 24:45-47) Kalelo mu 1914, matchalitchi zikwi zambiri anadzinenera kukhala Achikristu. Kodi ndigulu liti limene likazindikiridwa ndi Mbuyeyo, Yesu Kristu, monga kapolo wake wokhulupirika ndi wanzeru? Funso limenelo linali kudzayankhidwa pamene Yehova akadza kukachisi.
Kudza Kukachisi Wauzimu
5, 6. (a) Kodi nkukachisi uti kumene Yehova anadza kudzapereka chiweruzo? (b) Kodi ndichiweruzo chotani chimene Chikristu Chadziko chinalandira kwa Yehova?
5 Komabe, kodi ndikukachisi uti, kumene anadza? Mwachiwonekere sanali kachisi wakuthupi m’Yerusalemu. Wotsiriza wa akachisi amenewo anawonongedwa kalelo mu 70 C.E. Komabe, Yehova ali naye, kachisi wokulirapo amene anaphiphiritsidwa ndi wa m’Yerusalemu. Paulo analankhula za kachisi wokulirapo ameneyu nasonyeza mmene aliridi wamkulu, malo ake opatulika akumakhala kumwamba ndipo bwalo lake pano padziko lapansi. (Ahebri 9:11, 12, 24; 10:19, 20) Kuli kukachisi wamkulu wauzimu ameneyu kumene Yehova anadza kudzachita ntchito yachiweruzo.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 11:1; 15:8.
6 Kodi zimenezi zinachitika liti? Malinga ndi umboni wotsimikizirika umene ulipo, munali mu 1918.a Kodi chotulukapo chinali chiyani? Ponena za Chikristu Chadziko, Yehova anawona kuti chinali gulu limene manja ake anakhathamira ndi mwazi, dongosolo lachipembedzo loluluzika limene linadziloŵetsa m’chigololo ndi dziko lino, lodzigwirizanitsa ndi olemera ndi kutsendereza osauka, lophunzitsa ziphunzitso zachikunja mmalo mwakuchita kulambira koyera. (Yakobo 1:27; 4:4) Kupyolera mwa Malaki, Yehova anali atachenjeza kuti: “Ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye.” (Malaki 3:5) Chikristu Chadziko chinali chitachita zonsezi ndi zina zoipirapo. Podzafika 1919 kunali kwachiwonekere kuti Yehova anali atachiweruzira chiwonongeko limodzi ndi mbali yonse yotsala ya Babulo Wamkulu, ulamuliro wa padziko lonse wa chipembedzo chonama. Kuyambira panthaŵiyo kumkabe mtsogolo, mfuu inamka kwa owona mtima yakuti: “Tulukani m’menemo, anthu anga.”—Chivumbulutso 18:1, 4.
7. Kodi ndani amene Yesu anavomereza kukhala kapolo wake wokhulupirika ndi wanzeru?
7 Pamenepa, ndani nanga anali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru? M’zaka za zana loyamba, anayamba ndi kagulu kochepa kamene kanalabadira ntchito yochitira umboni ya Yohane Mbatizi ndi ya Yesu, mthenga wa chipangano. M’zaka za zana lathu, anali zikwi zoŵerengeka amene analabadira ntchito yokonzekerera ya Ophunzira Baibulo m’zaka zofikitsa ku 1914. Iwoŵa anapirira ziyeso zokakala mkati mwa nkhondo yoyamba yadziko, koma anasonyeza kuti mtima wawo unali pa Yehova.
Ntchito Yoyeretsa
8, 9. Kalelo mu 1918, kodi ndim’njira ziti zimene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anafunikira kuyeretsedwa, ndipo kodi ndilonjezo lotani limene Yehova anali atapereka ponena za zimenezi?
8 Komabe, ngakhale kagulu kameneka kanafunikira kuyeretsedwa. Ena amene anagwirizana nawo anasanduka adani a chikhulupiriro ndipo anafunikira kuchotsedwa. (Afilipi 3:18) Ena anali osafunitsitsa kusenza mathayo ophatikizidwa m’kutumikira Yehova ndipo anabwevuka. (Ahebri 2:1) Kuwonjezerapo, panali zizoloŵezi Zachibabulo zotsalabe zimene zinafunikira kuchotsedwa. Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru nayenso anafunikira kuyeretsedwa m’kakonzedwe kagulu. Mkhalidwe woyenera wa uchete kulinga kudziko lino unafunikira kuphunziridwa ndi kugwiritsiridwa ntchito. Ndipo pamene dziko linapitirizabe kululuzika, iwo anafunikira kumenya nkhondo zolimba kutetezera chidetso chamakhalidwe ndi chauzimu kuti chisaloŵe mumpingo.—Yerekezerani ndi Yuda 3, 4.
9 Inde, kuyeretsa kunali kofunika, koma Yehova mwachikondi anali atalonjeza za Yesu woikidwa pampando wachifumuyo kuti: “Ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.” (Malaki 3:3) Kuyambira mu 1918, Yehova, kupyolera mwa mthenga wachipangano ameneyu, wakwaniritsa lonjezo lake ndi kuyeretsa anthu ake.
10. Kodi ndinsembe za mtundu wanji zimene anthu a Mulungu anabweretsa, ndipo kodi ndichiitano chotani chimene Yehova anawapatsa?
10 Abale odzozedwa a Kristu ndi khamu lalikulu limene pambuyo pake linagwirizana nawo muutumiki wa Yehova onsewo anapindula ndi kuyenga kwa Yehova, monga woyenga ndi woyeretsa siliva. (Chivumbulutso 7:9, 14, 15) Monga gulu iwo anadza, ndipo akudzabe, kudzapereka nsembe zopereka m’chilungamo. Ndipo nsembe zawo ‘zimakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija.’ (Malaki 3:4) Anali amenewa amene Yehova molosera anaitana kuti “Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.”—Malaki 3:10.
Nsembe ndi Zakhumi
11. Kodi nchifukwa ninji zopereka zogwirizana ndi makonzedwe a Chilamulo cha Mose sizikufunikiranso?
11 M’tsiku la Malaki anthu a Mulungu anabweretsa nsembe ndi zakhumi zenizeni, monga dzinthu, zipatso, ndi zifuyo. Ngakhale m’tsiku la Yesu, Aisrayeli okhulupirika anapereka nsembe zenizeni pakachisi. Komabe, pambuyo pa imfa ya Yesu, zonsezo zinasintha. Chilamulo chinachotsedwa, kuphatikizapo lamulo la kupereka nsembe za zinthu zakuthupi ndi zakhumi zenizeni. (Aefeso 2:15) Yesu anakwaniritsa nsembe zaulosi zophiphiritsirazo za m’Chilamulo. (Aefeso 5:2; Ahebri 10:1, 2, 10) Pamenepo, kodi ndim’njira yotani, imene Akristu angabweretsere nsembe ndi zakhumi?
12. Kodi ndimtundu wotani wa zopereka zauzimu ndi nsembe zimene Akristu amapereka?
12 Kwa iwo, nsembe ziri makamaka za mtundu wauzimu. (Yerekezerani ndi Afilipi 2:17; 2 Timoteo 4:6.) Mwachitsanzo, Paulo analankhula za ntchito yolalikira kukhala nsembe pamene anati: “Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” Iye anasonya kumtundu wina wa nsembe yauzimu pamene analimbikitsa kuti: “Koma musaiŵale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” (Ahebri 13:15, 16) Pamene makolo alimbikitsa ana awo kuloŵa muutumiki waupainiya, iwo anganenedwe kuti akuwapereka nsembe kwa Yehova, monga momwe Yefita anaperekera nsembe mwana wake wamkazi monga “nsembe yakuyamika” kwa Mulungu, amene anampatsa chilakiko.—Oweruza 11:30, 31, 39.
13. Kodi nchifukwa ninji Akristu safunikira kupereka chakhumi chenicheni cha ndalama zimene amapeza?
13 Komabe, bwanji zakhumi? Kodi Akristu akukakamizidwa kuika pambali chakhumi cha ndalama zimene amapeza ndi kuipereka kugulu la Yehova, mofanana ndi zimene zimachitidwa m’matchalitchi ena a Chikristu Chadziko? Ayi, zimenezo siziri zofunikira. Palibe lemba limene limapereka lamulo lotero kwa Akristu. Pamene Paulo anali kusonkhanitsa zopereka za osoŵa a ku Yudeya, iye sanaike mlingo weniweni umene unayenera kuperekedwa. Mmalo mwake, anati: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, simwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Polankhula za awo amene ali m’magawo auminisitala apadera, Paulo anasonyeza kuti ngakhale kuti ena anachirikizidwa bwino lomwe ndi zopereka zodzifunira, iye anali wokonzekera kugwira ntchito ndi kudzichirikiza. (Machitidwe 18:3, 4; 1 Akorinto 9:13-15) Panalibe zakhumi zimene zinaikidwa padera kaamba ka chifuno chimenechi.
14. (a) Kodi nchifukwa ninji kubweretsa chakhumi sikumaimira kudzipereka ife eni athunthu kwa Yehova? (b) Kodi chakhumi chikuimira chiyani?
14 Mwachiwonekere, kwa Akristu chakhumi chimaphiphiritsira, kapena chimaimira, kanthu kena. Popeza kuti ndicho mbali yachikhumi ndipo kaŵirikaŵiri chiŵerengero cha khumi chimaphiphiritsira uchikwanekwane wapadziko lapansi m’Baibulo, kodi chakhumi chimaphiphiritsira kudzipereka kwathu athunthu kwa Yehova? Ayi. Pamene tidzipatulira kwa Yehova ndi kuchitira chizindikiro zimenezi mwa ubatizo wa m’madzi, imeneyo ndiyo nthaŵi imene timadzipereka athunthu kwa iye. Kuyambira panthaŵi ya kudzipatulira kwathu, sitimakhala ndi kanthu kalikonse kamene sikali kale ka Yehova. Komabe, Yehova amalola anthu kuti agaŵire chuma chawo. Chotero chakhumi chimaimira mbali ya chuma chathu imene timabweretsa kwa Yehova, kapena imene timagwiritsira ntchito muutumiki wa Yehova, monga chizindikiro cha kumkonda kwathu ndi kuzindikira kwathu chenicheni chakuti ndife ake. Chakhumi chamakono sichitofunikira kukhala gawo la khumi lenileni. M’zochitika zina chidzakhala chocheperapo. M’zina chidzakhala chokulirapo. Munthu aliyense amabweretsa zimene mtima wake umsonkhezera kubweretsa ndi zimene mikhalidwe yake ilola.
15, 16. Kodi chakhumi chathu chauzimu chimaphatikizapo chiyani?
15 Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’chakhumi chauzimu chimenechi? Choyamba, timapatsa Yehova nthaŵi yathu ndi nyonga. Nthaŵi imene timathera pamisonkhano, misonkhano yadera ndi misonkhano yaikulu, muutumiki wakumunda, zonsezi ndizinthu zoperekedwa kwa Yehova—mbali ya chakhumi chathu. Nthaŵi ndi nyonga zimene timathera kuchezera odwala ndi kuthandiza ena—nazonso ziri mbali ya chakhumi chathu. Kuthandizira kumanga Nyumba Zaufumu ndi kukhala ndi phande m’ntchito yokonzanso mogumuka ndi kusesa holo zirinso mbali yake.
16 Chakhumi chathu chimaphatikizaponso zopereka zathu zandalama. Pokhala ndi chiwonjezeko chachikulu kwambiri cha gulu la Yehova m’zaka zaposachedwapa, mathayo andalama awonjezereka. Nyumba Zaufumu zatsopano zikufunika, limodzi ndi maofesi anthambi atsopano ndi Nyumba Zamsonkhano, kuphatikizapo kusamalira zomwe ziripo kale. Kupeza ndalama zogwiritsira ntchito kuthandiza anthu amene ali mu utumiki wapadera—amene kaŵirikaŵiri amadzimana mokulira iwo eni kuti atero—nakonso kumapereka chitokoso chachikulu. Mu 1991 ndalama zogwiritsidwa ntchito kusamalira amishonale, oyang’anira oyendayenda, ndi apainiya apadera okha zinaposa pa 40 miliyoni dola (ya United States), zonsezo zinapezeka mwa zopereka zodzifunira.
17. Kodi kwenikweni nchiyani chimene tiyenera kupereka monga chakhumi chathu chauzimu?
17 Kodi kwenikweni tiyenera kuperekanji monga chakhumi chathu chauzimu? Yehova samapereka mlingo. Komabe, lingaliro la kudzipatulira, chikondi chenicheni kwa Yehova ndi abale, limodzi ndi lingaliro kufulumira kwanthaŵi ndi kuzindikira kuti pali miyoyo yofunikira kupulumutsidwa, zimatilimbikitsa kubweretsa chakhumi chathu chonse chauzimu. Timamva tiri osonkhezereka kutumikira Yehova kumlingo waukulu wothekera. Ngati tikhala ouma dzanja mwakudzipereka ife eni kapena chuma chathu modzikakamiza, zimenezi zikatanthauza kulanda Mulungu.—Yerekezerani ndi Luka 21:1-4.
Odalitsidwa Kufikira Palibe Kusoŵa
18, 19. Kodi ndimotani mmene anthu a Yehova adalitsidwira kaamba ka kubweretsa chakhumi chawo chonse?
18 Chiyambire 1919, anthu a Yehova apereka mowolowa manja nthaŵi yawo, nyonga, ndi ndalama kuzofunika za ntchito yolalikira. Iwo abweretsadi chakhumi chonse m’nyumba yosungiramo. Monga chotulukapo, Yehova wakwaniritsa lonjezo lake ndipo watsanulira madalitso ake kufikira palibenso kusoŵa. Zimenezi zawoneka mokulira m’kuwonjezereka kwawo m’ziŵerengero. Kuyambira pa zikwi zoŵerengeka za odzozedwa amene anali kutumikira Yehova pamene anadza kukachisi wake mu 1918, awonjezereka kufikira lerolino, odzozedwawo limodzi ndi atsamwali awo, nkhosa zina, akumaposa pa mamiliyoni anayi m’maiko osiyanasiyana 211. (Yesaya 60:22) Ameneŵa adalitsidwa mwakupatsidwa chidziŵitso chomakulakula cha chowonadi. Mawu aulosiwo atsimikiziridwa kwa iwo kukhala owona mowonjezerekawonjezereka. Chidaliro chawo m’kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova chatsimikiziridwa zolimba. (2 Petro 1:19) Iwo alidi anthu ‘ophunzitsidwa ndi Yehova.’—Yesaya 54:13.
19 Kupyolera mwa Malaki, Yehova adaneneratu madalitso owonjezereka kuti: “Pamenepo iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi bukhu la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” (Malaki 3:16) Pa magulu onse odzinenera kukhala Achikristu, Mboni za Yehova zokha ndizo zimene zimakumbukira dzina lake ndi kulibukitsa mwa amitundu. (Salmo 34:3) Nzachimwemwe chotani nanga kukhala ndi chitsimikizo chakuti Yehova amakumbukira kukhulupirika kwawo!
20, 21. (a) Kodi ndiunansi wodalitsidwa wotani umene Akristu owona ali nawo? (b) Ponena za Chikristu, kodi nkusiyana kuti kumene kukuwonekera bwino mowonjezerekawonjezereka?
20 Otsalira odzozedwa ali anthu a Yehova apadera, ndipo a khamu lalikulu, amene akudza mu unyinji wawo kudzagwirizana nawo, akututa limodzi nawo madalitso a kulambira koyera. (Zekariya 8:23) Kupyolera mwa Malaki, Yehova akulonjeza kuti: ‘Ndipo adzakhala anga anga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawasonyeza chifundo monga munthu asonyeza chifundo mwana wake womtumikira.’ (Malaki 3:17) Ndidalitso lotani nanga kuti Yehova amapereka chisamaliro chachifundo choterocho kwa iwo!
21 Ndithudi, kusiyana kukuwonekera mowonjezerekawonjezereka pakati pa Akristu owona ndi onama. Pamene anthu a Yehova akuyesayesa kusunga miyezo yake, Chikristu Chadziko chikumiriramirira m’chithaphwi cha chidetso cha dziko lino. Ndithudi, mawu a Yehova atsimikizira kukhala owona akuti: “Pamenepo adzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.”—Malaki 3:18.
22. Kodi tingakhale ndi chidaliro chakusangalala ndi madalitso otani ngati tipitirizabe kubweretsa chakhumi chathu chonse?
22 Posachedwapa, tsiku la kuŵerengeredwa mlandu lidzafikira Akristu onama. “Pakuti tawonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu.” (Malaki 4:1) Anthu a Yehova amadziŵa kuti iye adzawatetezera panthaŵi imeneyo, monga momwe anatetezerera mtundu wake wauzimu kalelo mu 70 C.E. (Malaki 4:2) Ngachimwemwe chotani nanga kukhala ndi chitsimikiziro chimenecho! Chotero, kufikira panthaŵiyo, aliyense wa ife asonyezetu chiyamikiro chathu ndi kukonda kwathu Yehova mwa kubweretsa chakhumi chonse m’nyumba yosungiramo. Pamenepo, tingakhale achidaliro kuti iye adzapitirizabe kutidalitsa kufikira sipadzakhalanso kusoŵa.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani chidziŵitso chowonjezereka mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1987, tsamba 14-20.
Kodi Mungafotokoze?
◻ M’nthaŵi zamakono, kodi ndiliti pamene Yehova anadza kukachisi limodzi ndi mthenga wake wapangano?
◻ Kodi ndani amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, ndipo kodi ndikuyeretsedwa kotani kumene anafunikira pambuyo pa 1918?
◻ Kodi nzopereka zauzimu zotani zimene Akristu owona amabwera nazo kwa Yehova?
◻ Kodi nchiyani chimene chiri chakhumi chimene Akristu akuuzidwa kubweretsa kunyumba yosungiramo?
◻ Kodi ndimadalitso otani amene anthu a Mulungu amasangalala nawo mwa kupereka zakhumi zauzimu?
[Chithunzi patsamba 15]
Zakhumi zathu zauzimu zimaphatikizapo kupereka nyonga yathu ndi chuma, zofunika kumangira Nyumba Zaufumu
[Chithunzi patsamba 16]
Chifukwa cha madalitso a Yehova pa anthu ake, pakhala kufunika kwa kumanga kochuluka, kuphatikizapo Nyumba Zaufumu ndi Nyumba Zamsonkhano