Mawu Anu “Asakhale Inde Kenako Ayi”
Taganizirani chitsanzo ichi: Mkulu wina amene ali mu Komiti Yolankhulana ndi Achipatala anapangana ndi m’bale wina wachinyamata kuti adzayende limodzi mu utumiki Lamlungu m’mawa. Tsikuli litafika, mkuluyu akulandira foni kuchokera kwa m’bale wina yomudziwitsa kuti mkazi wake wachita ngozi ndipo ali kuchipatala. M’baleyu akupempha mkuluyo kuti amuthandize kupeza dokotala amene sangavute pa nkhani ya magazi. Choncho mkuluyu akuuza m’bale wachinyamata uja kuti sizitheka kuti ayendere limodzi mu utumiki chifukwa akufuna kukathandiza amene ali kuchipatalawo.
Ganiziraninso chitsanzo china ichi: Mayi amene akulera yekha ana awiri anaitanidwa ndi banja lina la mumpingo wawo kuti tsiku lina madzulo akacheze kwawo. Anawo atamva zimenezi akusangalala kwambiri ndipo akungoona kuchedwa kuti tsikuli lifike. Koma kutangotsala tsiku limodzi, banjali likuuza mayiyu kuti zimene anapanganazo sizitheka chifukwa pali vuto lina. Patapita nthawi, mayiyu akumva kuti banjali linaitanidwanso ndi anzawo ena pa tsiku lomwelo ndipo iwo anasintha pulogalamu kuti apite kumeneko.
Popeza ndife Akhristu, tiyenera kusunga pangano. Mawu athu “asakhale Inde kenako Ayi.” (2 Akor. 1:18) Komabe, zitsanzo ziwirizi zikusonyeza kuti nthawi zina zingaoneke kuti sitingathe kuchita zimene tapangana pa zifukwa zomveka. Izi zinachitikirapo mtumwi Paulo.
PAULO ANKAMUNENA KUTI ANALI WOSAPANGANIKA
Mu 55 C.E., Paulo ali ku Efeso pa ulendo wake wachitatu waumishonale, anakonza pulogalamu yoti awoloke nyanja ya Ejani n’kupita ku Korinto kenako n’kukafika ku Makedoniya. Pobwerera ku Yerusalemu, anakonza zokafikanso ku Korinto kuti akatenge mphatso za abalewo zopita ku Yerusalemuko. (1 Akor. 16:3) Tikudziwa zimenezi tikawerenga 2 Akorinto 1:15, 16 chifukwa Paulo analemba kuti: “Popeza ndine wotsimikiza za zimenezi, ndinali ndi cholinga chofika kwa inu poyamba, kuti mudzakhale ndi mwayi wachiwiri wosangalala. Kuti ndikadzacheza nanu pang’ono ndidzapite ku Makedoniya, ndipo ndikadzachoka ku Makedoniya ndidzabwerenso kwa inu kuti mudzandiperekeze popita ku Yudeya.”
Zikuoneka kuti m’kalata ina, Paulo anauza abale a ku Korinto za pulogalamu yakeyi. (1 Akor. 5:9) Koma atangolemba kalatayi, Paulo anauzidwa ndi anthu a m’banja la Kuloe kuti mu mpingo wa Korinto muli magawano. (1 Akor. 1:10, 11) Choncho Paulo anaganiza zosintha pulogalamu yake n’kungolemba kalata imene timaitchula kuti 1 Akorinto. M’kalatayi iye anawalangiza komanso kuwadzudzula mwachikondi. Anawauzanso kuti wasintha pulogalamu yake ndipo apita kaye ku Makedoniya kenako n’kufika ku Korintoko.—1 Akor. 16:5, 6.a
Zikuoneka kuti abale a ku Korinto atalandira kalata ya Paulo, ena mwa “atumwi apamwamba” a mumpingowo ankanena kuti Paulo ndi wosapanganika. Poyankha zimene iwo ankanenazi, Paulo anawafunsa kuti: “Kodi ndinali kulingalira mwachibwana? Kapena kodi zimene ndimaganiza kuti ndichite, ndimaziganiza ndi zolinga zadyera, kuti ndikati ‘Inde, inde’ nthawi yomweyo ndisinthe ndinene kuti ‘Ayi, ayi’?”—2 Akor. 1:17; 11:5.
Kodi pamenepa tingati Paulo ankachitadi zinthu “mwachibwana”? Ayi. Palembali, mawu amene anawamasulira kuti “mwachibwana” amatanthauza kusapanganika kapena kusadalirika. Ndiyeno Paulo anawafunsa kuti: “Kodi zimene ndimaganiza kuti ndichite, ndimaziganiza ndi zolinga zadyera?” Funso limeneli liyenera kuti linathandiza Akhristu a ku Korinto kudziwa kuti Paulo sanali munthu wosapanganika.
Ndiyeno potsutsa zimene ankamunenezazo, Paulo analemba kuti: “Koma Mulungu ndi wodalirika kuti mawu athu kwa inu asakhale Inde kenako Ayi.” (2 Akor. 1:18) Paulo anali ndi zolinga zabwino pamene ankasintha pulogalamu yake yokachezera abale ndi alongo a ku Korinto. Pa 2 Akorinto 1:23, Paulo ananena kuti sanapite ku Korinto pa nthawiyo chifukwa chakuti ‘sanafune kuwonjezera chisoni chawo.’ Anafuna kuwapatsa mpata wokonza zinthu iye asanafike. Ali ku Makedoniya, Paulo anauzidwa ndi Tito kuti Akhristu a ku Korinto anamva chisoni ndi kalata yake yoyamba ija ndipo analapa. Apatu zimene ankafuna zinatheka ndipo anasangalala kwambiri.—2 Akor. 6:11; 7:5-7.
“AME” AMANENEDWA KWA MULUNGU
Ponena kuti Paulo anali wosapanganika anthuwo ankatanthauza kuti sanali wodalirika pa ntchito yake yolalikira. Koma Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Korinto kuti iye analalikira Yesu Khristu kwa iwo. Iye anati: “Mwana wa Mulungu, Khristu Yesu, amene analalikidwa pakati panu kudzera mwa ineyo, Silivano, ndi Timoteyo, sanakhale Inde kenako Ayi, koma mwa iye, Inde wakhalabe Inde.” (2 Akor. 1:19) Kodi Yesu Khristu, amene Paulo ankamutsanzira, anali wosadalirika? Ayi. Nthawi zonse Yesu ankanena zoona pa moyo wake wonse. (Yoh. 14:6; 18:37) Ngati zimene Yesu ankalalikira zinali zoona komanso zodalirika, ndipo Paulo ankalalikira zomwezo, ndiye kuti uthenga wake unalinso wodalirika.
Tikudziwa kuti Yehova ndi “Mulungu wachoonadi.” (Sal. 31:5) Zimene Paulo analemba zikutsimikizira zimenezi. Iye anati: “Malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani, akhala Inde kudzera mwa [Khristu].” Yesu ali padziko lapansi anatumikira Mulungu mokhulupirika ndipo izi zinapereka umboni wakuti malonjezo onse a Yehova amakwaniritsidwa. Paulo anapitiriza kuti: “Choteronso kudzera mwa iye, ‘Ame’ amanenedwa kwa Mulungu kuti Mulungu alandire ulemerero kudzera mwa ife.” (2 Akor. 1:20) Yesu ndi “Ame” kapena kuti umboni wosonyeza kuti malonjezo onse a Yehova Mulungu adzakwaniritsidwa.
Mofanana ndi Yehova komanso Yesu amene nthawi zonse amanena zoona, Paulo nayenso ankalankhula zoona nthawi zonse. (2 Akor. 1:19) Iye sanali wosapanganika kapena kuti sankalonjeza zinthu “ndi zolinga zadyera.” (2 Akor. 1:17) Koma ‘ankayenda mwa mzimu.’ (Agal. 5:16) Nthawi zonse ankakhala ndi zolinga zabwino akafuna kuchita zinthu ndi anthu. Akati Inde ankakhaladi Inde.
KODI MUKATI INDE AMAKHALADI INDE?
Masiku ano anthu ambiri amene satsatira mfundo za m’Baibulo akalonjeza zinthu amasintha pakangochitika kavuto kakang’ono kapena akaona kuti mwayi wina wawatsegukira. Nthawi zina “inde” wawo sakhala “inde” ngakhale pa zinthu zimene anasainirana. Ambiri saona kuti ukwati ndi mgwirizano wa moyo wawo wonse. Iwo amaona kuti ukhoza kutha nthawi ina iliyonse ndipo mabanja ambirimbiri akungotha mwachisawawa.—2 Tim. 3:1, 2.
Kodi inuyo mukati Inde amakhaladi Inde? Monga taonera mu chitsanzo choyamba chija, nthawi zina tikhoza kusintha pulogalamu pa zifukwa zomveka. Koma Akhristufe tikalonjeza zinazake, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tikwaniritse lonjezolo. (Sal. 15:4; Mat. 5:37) Mukamatero anthu azikudalirani podziwa kuti mumanena zoona ndipo mukati Inde amakhaladi Inde. (Aef. 4:15, 25; Yak. 5:12) Anthu akadziwa kuti ndinu wodalirika pochita zinthu akhoza kumvetsera mukamawauza uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu. Choncho tiyeni tiziyesetsa kuti tikati Inde azikhaladi Inde.
a Atangolemba kalata ya 1 Akorinto, Paulo anauyamba ulendo wopita ku Makedoniya kudzera ku Torowa. Ali ku Makedoniyako analemba kalata ya 2 Akorinto. (2 Akor. 2:12; 7:5) Ndiyeno atachoka kumeneko anafika ku Korinto.