-
Mafunso Ochokera kwa OwerengaNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | December
-
-
Kodi mawu oti Paulo “anakwatulidwira kumwamba kwachitatu” komanso ‘kulowa m’paradaiso’ amatanthauza chiyani?—2 Akor. 12:2-4.
Pa 2 Akorinto 12:2, 3, Paulo ananena kuti munthu wina “anakwatulidwira kumwamba kwachitatu.” Kodi ankanena za ndani? M’kalata imene Paulo analembera mpingo wa ku Korinto, iye anasonyeza kuti anali mtumwi wosankhidwa ndi Mulungu. (2 Akor. 11:5, 23) Kenako ananena za “masomphenya ndi mauthenga ochokera kwa Ambuye.” Atanena zimenezi, Paulo sanatchule abale ena. Choncho ayenera kuti ankanenabe za iyeyo kuti ndi amene analandira masomphenya ndi mauthengawo.—2 Akor. 12:1, 5.
Pa chifukwa chimenechi tinganene kuti Pauloyo ndi amene “anakwatulidwira kumwamba kwachitatu” komanso ‘kulowa m’paradaiso.’ (2 Akor. 12:2-4) Iye anagwiritsa ntchito mawu oti “masomphenya” posonyeza kuti zinthuzi ndi zoti zidzachitike m’tsogolo.
Kodi “kumwamba kwachitatu” kumene Paulo anaona n’chiyani?
M’Baibulo, mawu akuti “kumwamba” angatanthauze m’mlengalenga. (Gen. 11:4; 27:28; Mat. 6:26) Koma mawuwa amatanthauzanso zinthu zina. Mwachitsanzo, angatanthauze ulamuliro wa anthu. (Dan. 4:20-22) Angatanthauzenso ulamuliro wa Mulungu kapena Ufumu wake.—Chiv. 21:1.
Koma Paulo anaona “kumwamba kwachitatu.” Kodi ankatanthauza chiyani? Nthawi zina Baibulo limatchula zinthu zina katatu pofuna kutsindika kapena kutsimikizira. (Yes. 6:3; Ezek. 21:27; Chiv. 4:8) Zikuoneka kuti pamene Paulo ananena za “kumwamba kwachitatu,” ankanena za ulamuliro wapamwamba kwambiri. Iye ankanena za Ufumu wa Mesiya umene olamulira ake ndi Yesu Khristu komanso anthu 144,000. (Onani buku lachingelezi la Insight on the Scriptures, Vol. 1, tsamba 1059, 1062.) Mogwirizana ndi zimene mtumwi Petulo analemba, tikuyembekezera “kumwamba kwatsopano” kumene Mulungu analonjeza.—2 Pet. 3:13.
-
-
Mafunso Ochokera kwa OwerengaNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | December
-
-
Mawu akuti “kumwamba kwachitatu” otchulidwa pa 2 Akorinto 12:2 ayenera kuti akutanthauza Ufumu wa Mesiya wolamuliridwa ndi Yesu Khristu komanso anthu 144,000, omwe ndi “kumwamba kwatsopano.”—2 Pet. 3:13.
Ananena kuti “kumwamba kwachitatu” chifukwa chakuti Ufumuwo ndi ulamuliro wapamwamba kwambiri.
-