“Iye Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”
Lemba la chaka cha 2018: “Anthu odalira Yehova adzapezanso mphamvu.”—YES. 40:31.
1. Kodi masiku ano timakumana ndi mavuto ati, nanga Yehova amasangalala akaona atumiki ake akutani? (Onani zithunzi zoyambirira.)
TONSEFE timadziwa kuti moyo m’dzikoli ndi wovuta. Ena mwa abale ndi alongo athu akuvutika ndi matenda aakulu. Ena ndi achikulire koma akusamaliranso achibale awo okalamba. Ena amavutika kwambiri kuti apeze zinthu zofunika pa moyo. Ndipo ena ali ndi mavuto ngati amene tatchulawa, osati limodzi koma angapo. Zimenezi zimachititsa kuti azifooka, maganizo azisokonezeka komanso aziwononga ndalama zambiri. Ngakhale zili choncho, tonsefe timakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu ndipo sitikayikira zoti m’tsogolomu adzathetsa mavuto onse. Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona tili ndi chikhulupiriro choterechi.
2. Kodi lemba la Yesaya 40:29 lingatilimbikitse bwanji, koma kodi anthu a Mulungu ena amachita zinthu zolakwika ziti?
2 Koma kodi nthawi zina mumaona kuti mavuto anu akufika poti simungathe kuwapirira? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Baibulo limasonyeza kuti m’mbuyomu anthu ena amene ankatumikira Mulungu mokhulupirika ankamvanso chimodzimodzi. (1 Maf. 19:4; Yobu 7:7) Koma m’malo motaya mtima, iwo ankadalira Yehova kuti awapatse mphamvu. Ndipo sanagwiritsidwe mwala chifukwa Mulungu wathu “amapereka mphamvu kwa munthu wotopa.” (Yes. 40:29) Koma chomvetsa chisoni n’chakuti anthu a Mulungu ena akakumana ndi mavuto amasiya kuchita zinthu zokhudza kulambira. Iwo amaona kuti zinthu zimenezo n’zimene zikuwapanikiza, osati kuwabweretsera madalitso. Amasiya kuwerenga Mawu a Mulungu, kupezeka pamisonkhano ndiponso kulalikira. Koma vuto ndi lakuti zimene akuchitazo n’zimene Satana amafuna.
3. (a) Kodi tingapewe bwanji zimene Satana amafuna? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Mdyerekezi safuna kuti tizichita khama pa zinthu zokhudza kulambira chifukwa amadziwa kuti zinthu zimenezo zingatipatse mphamvu. Choncho mukatopa kwambiri ndi mavuto enaake, musamasiye kuchita zinthu zokhudza kulambira Yehova. M’malomwake muziyesetsa kumuyandikira ndipo iye “adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.” (1 Pet. 5:10; Yak. 4:8) Munkhaniyi tikambirana zinthu ziwiri zimene zingatichititse kuti tisiye kuchita khama potumikira Mulungu. Tionanso mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire kuti tilimbane ndi zinthu zimenezo. Koma choyamba tiyeni tikambirane lemba la Yesaya 40:26-31, lomwe limasonyeza kuti Yehova akhoza kutipatsa mphamvu.
ANTHU ODALIRA YEHOVA ADZAPEZANSO MPHAMVU
4. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa lemba la Yesaya 40:26?
4 Werengani Yesaya 40:26. Palibe munthu amene angakwanitse kuwerenga nyenyezi zonse m’chilengedwechi. Asayansi amaona kuti mumlalang’amba wathu wokha muli nyenyezi pafupifupi 400 biliyoni. Ngakhale zili choncho, Yehova amatha kutchula dzina la nyenyezi iliyonse. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngati Yehova amachita chidwi ndi zinthu zopanda moyo zimene analenga, kuli bwanji inuyo? Mumamutumikira chifukwa choti mumamukonda, osati chifukwa chakuti munalengedwa m’njira yoti muzingochita zimenezo. (Sal. 19:1, 3, 14) Atate wathu wakumwamba amadziwa chilichonse chokhudza ifeyo. Paja Baibulo limanena kuti ngakhale ‘tsitsi lenilenilo la m’mutu mwathu amaliwerenga.’ (Mat. 10:30) Wolemba masalimo amatitsimikiziranso kuti: “Yehova amadziwa za moyo wa anthu osalakwa.” (Sal. 37:18) Iye amaona mavuto amene tikukumana nawo ndipo amatha kutipatsa mphamvu kuti tipirire.
5. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova akhoza kutipatsa mphamvu?
5 Werengani Yesaya 40:28. Yehova ali ndi mphamvu zambiri. Tangoganizirani za mphamvu zimene Mulungu anaika m’dzuwa. Wasayansi wina dzina lake David Bodanis anati: “Pa sekondi iliyonse, dzuwa limatulutsa mphamvu yofanana ndi mphamvu ya mabomba [anyukiliya okwana mabiliyoni ambiri].” Wasayansi winanso ananena kuti ‘mphamvu zimene zimachokera kudzuwa pa sekondi iliyonse, zikhoza kukhala zokwanira kuthandiza anthu kwa zaka 200,000.’ Ndiye ngati Mulungu amapatsa dzuwa mphamvu zochuluka chonchi, kodi angalephere kutipatsanso mphamvu zoti tipirire mavuto athu?
6. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti goli la Yesu ndi lofewa, nanga kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji?
6 Werengani Yesaya 40:29. Kutumikira Yehova n’kosangalatsa kwambiri. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Senzani goli langa.” Koma anawonjezera kuti: “Mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Mfundo imeneyi ndi yoona. Nthawi zina timakhala otopa kwambiri tikamanyamuka kupita kumisonkhano kapena mu utumiki. Koma kodi timamva bwanji tikamabwerera kunyumba? Timamva bwino ndipo zimatithandiza kupirira mavuto athu. Izi zikusonyeza kuti goli la Yesu ndi lofewadi.
7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti lemba la Mateyu 11:28-30 ndi loona.
7 Mlongo wina, yemwe tangomupatsa dzina loti Kayla, amadwala matenda enaake ofooketsa thupi, amavutika maganizo komanso mutu waching’alang’ala umamupweteka pafupipafupi. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zina amavutika kuti apezeke pamisonkhano. Koma atayesetsa tsiku lina kuti akapezeke kumisonkhano, analemba kuti: “Nkhani imene inakambidwa inali yolimbikitsa anthu amene ayamba kutaya mtima. Wokambayo anafotokoza zinthu mosonyeza kuti amamvera chisoni kwambiri anthu oterewa moti ndinayamba kulira. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti kupezeka pamisonkhano ndi kothandiza kwambiri.” Kayla anasangalala kuti anayesetsa kufika kumisonkhanoyo.
8, 9. Kodi mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu”?
8 Werengani Yesaya 40:30. Tonsefe, kaya tili ndi maluso otani, pali zinthu zina zimene sitingakwanitse patokha. Aliyense ayenera kuzindikira mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, Paulo anali waluso kwambiri, koma panali zinthu zina zimene sankakwanitsa kuchita. Iye atauza Mulungu nkhawa zake, Mulunguyo anamuuza kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.” Paulo anamvetsa zimenezi ndipo anati: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.” (2 Akor. 12:7-10) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani?
9 Iye anazindikira kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita popanda kuthandizidwa ndi Mulungu. Choncho mzimu wa Mulungu unkamupatsa mphamvu pamene ankafooka komanso kuti achite zinthu zimene payekha sakanakwanitsa. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Mulungu akhozanso kutipatsa mphamvu zambiri.
10. Kodi Yehova anathandiza bwanji Davide?
10 Nayenso Davide ankathandizidwa ndi mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu. Iye anaimba kuti: “Ndi thandizo lanu, ndingathamangitse gulu la achifwamba. Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.” (Sal. 18:29) Pali mavuto ena okhala ngati khoma lomwe sitingakwere patokha ndipo timafunika kuti Mulungu azitithandiza.
11. Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji tikakumana ndi mavuto?
11 Werengani Yesaya 40:31. Chiwombankhanga sichiuluka mtunda wautali pogwiritsa ntchito mphamvu zake zokha. Mpweya wotentha ndi umene umachithandiza kuti chipite m’mwamba n’kumauluka popanda kugwiritsa ntchito mphamvu zambiri. Choncho mukakumana ndi vuto lalikulu muziganizira za chiwombankhanga. Muzipempha Yehova kuti akhale ngati akukunyamulani pogwiritsa ntchito “mthandizi, amene ndi mzimu woyera.” (Yoh. 14:26) N’zosangalatsa kuti mzimu woyera ukhoza kutithandiza nthawi iliyonse imene tikufunika thandizo. Nthawi ina imene timafunika thandizo kwambiri m’pamene tasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzathu. Koma kodi n’chifukwa chiyani Akhristu amasemphana maganizo nthawi zina?
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu nthawi zina amasemphana maganizo? (b) Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza Yehova pa nkhani ya Yosefe?
12 Timatha kusiyana maganizo chifukwa tonsefe si angwiro. N’chifukwa chake nthawi zina Akhristu anzathu akhoza kutikhumudwitsa kapena ifeyo tikhoza kuwakhumudwitsa. Nkhani ngati zimenezi zikachitika zingakhale zovuta kupirira. Koma mofanana ndi mayesero ena, Yehova amalola kuti zimenezi zichitike. Iye amafuna kuti tisonyeze kuti ndife okhulupirika. Amafunanso kuti tiphunzire kugwira ntchito mogwirizana ndi anthu amene iye amawakonda ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina.
13 Nkhani ya Yosefe imasonyeza kuti Yehova amatha kulola kuti atumiki ake akumane ndi mayesero. Yosefe ali wachinyamata, abale ake ankamuchitira nsanje moti anamugulitsa ndipo anakakhala kapolo ku Iguputo. (Gen. 37:28) Yosefe anali munthu wolungama komanso mnzake wa Mulungu. Choncho Yehova ayenera kuti anadandaula kwambiri kuona zoipa zimene zinkamuchitikira. Komabe, sanaletse kuti zimenezi zichitike. Pa nthawi ina Yosefe anaimbidwa mlandu woti ankafuna kugwiririra mkazi wa Potifara ndipo anamangidwa. Koma Yehova sanaletsenso zimenezi. Kodi izi zikutanthauza kuti Mulungu anamuiwala? Ayi. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene [Yosefe] anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.”—Gen. 39:21-23.
14. Kodi kupewa kukwiya kumatithandiza bwanji?
14 Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Davide. Si anthu ambiri amene akumanapo ndi mavuto aakulu ngati amene Davide anakumana nawo. Koma iye sanalole kuti azingokhala wokwiya. M’malomwake, analemba kuti: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya. Usapse mtima kuti ungachite choipa.” (Sal. 37:8) Chifukwa chachikulu chopewera kukwiya n’chakuti timafuna kutsanzira Yehova yemwe “sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu.” (Sal. 103:10) Kupewa kukwiya kumatithandizanso m’njira zina. Munthu amene amakonda kukwiya akhoza kudwala matenda monga othamanga magazi kapena a m’mapapo. Akhozanso kudwala matenda a chiwindi, a mphafa kapena a m’mimba. Munthu akakwiya saganizanso bwino. Vuto lina ndi lakuti pambuyo pokwiya kwambiri, munthu akhoza kuvutika maganizo kwa nthawi yaitali. Koma Baibulo limanena kuti: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” (Miy. 14:30) Ndiye kodi tingatani kuti tisakwiye ngati m’bale wathu watikhumudwitsa? Nanga tingatani kuti tikhazikitse mtendere ndi m’bale wathuyo? Kutsatira mfundo zanzeru za m’Baibulo n’kumene kungatithandize.
ABALE ATHU AKATIKHUMUDWITSA
15, 16. Kodi tingatani kuti tiyambenso kugwirizana ndi munthu amene watikhumudwitsa?
15 Werengani Aefeso 4:26. Anthu a m’dzikoli akatichitira zoipa sitidabwa kwenikweni. Koma Mkhristu mnzathu kapena wachibale wathu akachita zinthu zotikhumudwitsa, zimatipweteka kwambiri. Ndiye kodi tingatani ngati zikutivuta kuiwala nkhaniyo? Kodi tidzapitiriza kumusungira chakukhosi kwa zaka zambiri? Kapena kodi tidzatsatira malangizo anzeru a m’Baibulo akuti tizithetsa nkhani mwamsanga? Tiyenera kudziwa kuti tikachedwa kwambiri kuthetsa nkhani m’pamene nkhaniyonso imavuta kwambiri kuithetsa.
16 Ndiye tiyerekeze kuti zoterezi zakuchitikirani ndipo mukuvutika kuiwala nkhaniyo. Kodi mungatani kuti muyambenso kugwirizana ndi m’bale wanuyo? Choyamba, muyenera kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima. Muzimupempha kuti akuthandizeni kukambirana bwinobwino ndi m’baleyo. Muzikumbukira kuti nayenso ndi mnzake wa Yehova ndipo Yehovayo amamukonda kwambiri. (Sal. 25:14) Mulungu amakomera mtima anzake ndipo amafuna kuti nafenso tizichita zomwezo. (Miy. 15:23; Mat. 7:12; Akol. 4:6) Kenako muyenera kuganizira mofatsa zimene mungakalankhule kwa m’bale wanuyo. Musamafulumire kuganiza kuti wakukhumudwitsani dala. Muyeneranso kuzindikira kuti mwina inunso munachita zinazake zimene zinachititsa kuti musemphane maganizo ndi m’baleyo. Polankhula naye, mukhoza kuyamba ndi mawu ngati akuti: “Mwina vuto ndi ine, koma pamene munandilankhula dzulo, ndinkamva ngati . . .” Ngati simunamvane pambuyo pokambirana, mungayese kukambirananso nthawi ina. Koma musanalankhule naye mungachite bwino kupempha Yehova kuti adalitse m’bale wanuyo. Mungapemphenso Mulungu kuti akuthandizeni kuganizira zinthu zabwino zimene m’baleyo amachita. Ngakhale zitavuta kukhazikitsa mtendere, dziwani kuti Yehova adzasangalala kwambiri kuti mwachita zimene mungathe pofuna kugwirizananso ndi m’bale wanuyo, yemwe ndi mnzake wa Mulungu.
TIKAMADZIIMBA MLANDU PA ZIMENE TINALAKWITSA M’MBUYOMU
17. Kodi Yehova angatithandize bwanji ngati tachita tchimo lalikulu, ndipo n’chifukwa chiyani sitiyenera kuzengereza kugwiritsa ntchito njira zimene wapereka?
17 Anthu ena amaona kuti si oyenera kutumikira Yehova chifukwa choti anachita tchimo lalikulu m’mbuyomu. Koma munthu akamangodziimba mlandu amakhala wosasangalala. Mwachitsanzo, Mfumu Davide ankadziimba mlandu kwambiri ndipo analemba kuti: “Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga. Pakuti dzanja lanu linali kundilemera usana ndi usiku.” Koma chosangalatsa n’chakuti Davide anali munthu wolimba mwauzimu ndipo anathana ndi vuto lakeli m’njira yabwino. Iye anati: “Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo . . . munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.” (Sal. 32:3-5) Ngati mwachita tchimo lalikulu, Yehova amafunitsitsa kuti akuthandizeni kukhalanso naye pa ubwenzi. Koma muyenera kugwiritsa ntchito njira zimene Yehova wapereka kudzera mumpingo. (Miy. 24:16; Yak. 5:13-15) Musazengereze pochita zimenezi chifukwa mukatero mukhoza kulephera kudzalandira moyo wosatha. Koma kodi mungatani ngati pambuyo pokhululukidwa tchimo linalake, mukudziimbabe mlandu?
18. Kodi chitsanzo cha Paulo chingathandize bwanji anthu amene amadandaula chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyomu?
18 Nayenso Paulo nthawi zina ankadandaula chifukwa cha zinthu zimene analakwitsa m’mbuyomu. Iye ananena kuti: “Ineyo ndine wamng’ono kwambiri mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.” Koma iye ananenanso kuti: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.” (1 Akor. 15:9, 10) Yehova ankakonda Paulo mmene analili ndipo ankafuna kuti nayenso aziona chimodzimodzi. Ngati mwalapa machimo amene munachita m’mbuyomu ndipo mwawaulula kwa anthu oyenerera, musamakayikire kuti Yehova adzakuchitirani chifundo. Choncho muzikhulupirira kuti Yehova wakukhululukirani monga mmene analonjezera.—Yes. 55:6, 7.
19. Kodi lemba la chaka cha 2018 ndi loti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani lili loyenera?
19 Popeza mapeto a dzikoli akuyandikira kwambiri, tingayembekezere kuti mavuto azichulukirachulukira. Koma dziwani kuti Yehova adzakupatsaninso mphamvu zokwanira kuti mupitirize kupirira. Paja iye “amapereka mphamvu kwa munthu wotopa, ndipo wofooka amam’patsa nyonga zochuluka.” (Yes. 40:29; Sal. 55:22; 68:19) Chaka chino cha 2018, tikhala tikukumbukira mfundo yofunikayi nthawi iliyonse imene tapita ku Nyumba ya Ufumu. Zili choncho chifukwa mfundoyi ikupezeka pachikwangwani cha mu Nyumba ya Ufumu chokhala ndi lemba la chaka lakuti: “Anthu odalira Yehova adzapezanso mphamvu.”—Yes. 40:31.