‘Kusamalira Nyumba ya Munthuwe’—Kuyang’anizana ndi Chitokosocho m’Maiko Omatukuka
“NDITHUDI ngati munthu aliyense sasamalira awo amene ali ake, ndipo makamaka awo amene ali a m’nyumba mwake, wataya chikhulupiriro ndipo ali woipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro.” Ndimo mmene mtumwi Paulo ananenera. (1 Timoteo 5:8, NW) Pamene kuli kwakuti kusamalira banja kwakhala kovuta mowonjezereka m’maiko achuma, kuchita zimenezo m’maiko omatukuka kaŵirikaŵiri kumabweretsadi chitokoso chachikulu.
Mwachitsanzo, mu Afirika, vuto la zachuma kaŵirikaŵiri ndilo mkhalidwe osati chinthu chachilendo. Ntchito nzosoŵa, ndipo pamene zipezeka, mwamuna ndi mkazi yemwe mwina adzafunikira kugwira ntchitozo kotero kuti angopeza zodzichirikizira. Mitu ya mabanja imafunikira kuyenda mitunda yaitali kukafunafuna ntchito, ikumasiya akazi awo ndi ana ali okha kwa miyezi yambiri—kapena kwa zaka. Malo okhala abwino angakhalenso ovuta kuwapeza. Mabanja ambiri a mu Afirika ngaakulu; motero malo okhala amakhala aang’ono kwambiri, opanda ziŵiya zofunika. Kaŵirikaŵiri pamakhala mikhalidwe yoipa.
Kuwonjezera pa zimenezi, miyambo yakumaloko, miyambo yachikale, ndi malingaliro a anthu onse kumaloko angawombane ndi mzimu wa Mawu a Mulungu, Baibulo. Lingalirani za maganizo ena opezeka ponena za ukwati ndi ana. Mitu ina ya mabanja imakhulupirira kuti ili ndi thayo la kungolipirira lendi ndi ndalama zofunika kusukulu. Akazi awo—ndipo nthaŵi zina ngakhale ana okulirapo—amawasiyira ntchito ya kupeza zinthu zofunika zonga chakudya ndi zovala.
Ndiponso, amuna ena ali ndi lingaliro lakuti “ndalama zanga ndi zanga, koma ndalama zako ndi zanganso.” Kaŵirikaŵiri zimenezi zimasonkhezera mkwiyo pakati pa akazi olandira ndalama. Mkazi wina wa ku Tanzania anadandaula kuti: “Amathera ndalamazo ku moŵa, osati pa ife ndi ana. Timathandizana ntchito, kapenanso kuchita yochuluka, koma amuna amatenga ndalama zonse akumatiuza kuti ndi zawo—kuti amazipeza okha.”
Komabe, Akristu amaika Mawu a Mulungu pamalo oyamba m’malo mwa mwambo wakumaloko kapena lingaliro lofala. Baibulo limapereka chitsogozo chothandiza pankhani ya kusamalira banja la munthuwe. Mwachitsanzo, ilo limati “ana sayenera kuunjikira atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuunjikira ana.” (2 Akorinto 12:14) Chotero, amuna owopa Mulungu amene ali okhoza kugwira ntchito samasiyira akazi awo kapena ana awo okulirapo kupezera chakudya ndi zovala banjalo chifukwa cha ulesi; thayo limenelo limaikidwa mwachindunji pamapeŵa pa mutu wa banja.—1 Akorinto 11:3.
Zoonadi, ndalama za mwamuna zingakhale zosakwanira kusamalira zofunikira zonse za banja lake. Koma ngati mkazi wake amalandira ndalama kuntchito yolembedwa, mwamuna wachikristu sadzakhala wansanje. M’malo mwake iye adzamchitira monga ‘mnzake’ wolemekezeka. (Malaki 2:14) Motero, sadzamlanda ndalama zimenezo zopezedwa movutikira mokakala mtima ndi kuziwawanya mosalingalira konse za iye. M’malo mwake, iye ndi mkazi wakeyo ‘adzakambitsirana’ ndi kusankha mmene angagwiritsirire ntchito bwino koposa ndalama zawo kuti banja lawo lipindule. (Miyambo 13:10) Pamene kuli kotheka, mwamuna angapatsedi mkazi wake mlingo wina wa ufulu wa kuyang’anira kayendetsedwe ka ndalama, wonga womwe “mkazi wangwiro” anali nawo m’nthaŵi za Baibulo. (Miyambo 31:10, 11, 16) Kutsatira uphungu wa Baibulo m’nkhani zimenezo kumachirikiza chimwemwe ndi chikhutiro cha banja.
Kuyang’anizana ndi Vuto la Ulova
Komabe, lingalirani za vuto la ulova. Pamene ntchito zili zochepa ndipo malipiro ake ali otsika, mitu yambiri ya mabanja a mu Afirika imakafunafuna ntchito kutali—kumigodi, kumafakitale, kumafamu, ndi kuminda yaikulu. Ngati mwamuna wachikristu ali mu mkhalidwe umenewu, angapezeke kuti ali kutali ndi olambira anzake ndi kukhala mu mkhalidwe wa mayanjano oipa kwambiri. (Miyambo 18:1; 1 Akorinto 15:33) Pamene kuli kwakuti banja lake lingakhale likuyesayesa kulimbana ndi zinthu zambiri pa mkhalidwewo, mwachionekere ilo lingavutike chifukwa cha kusakhala ndi atate panyumba kuti atsogolere mwauzimu kapena kuti apereke chichirikizo cha mtima. Chomvetsa chisoni nchakuti, kusakhalapo kwanthaŵi yaitaliko kungabweretsedi chinthu chenichenicho chimene chinafunikira kutsekerezedwa—mavuto a ndalama.
Nakubala wina akuti: “Mwamuna wanga anapita kukakumba golidi. Anafuna kuti adzabwereko patatha mwezi kapena mwina patatha miyezi iŵiri. Komano anathako chaka chimodzi! Anandisiyira ana asanu ndi mmodzi ofuna kusamalira. Ndiyeno ndinafunikira kulipira lendi. Popeza kuti ndinali wodwaladwala, ndinafunikira kulipira ndalama kuchipatala. Tinafunikira zovala, ndipo tinafunikira kudya tsiku lililonse. Sindinali pantchito. Zinali zovuta. Mbali yovuta kwambiri inali ya kusamalira ana mwauzimu—phunziro la banja, misonkhano, ndi ntchito yolalikira. Komabe mwa thandizo la Yehova tinakwanitsa.”
Ngakhale anakubala ena aumirizika kusiya mabanja awo kwa miyezi yambiri kuti akagwire ntchito. Ena amapeza ndalama monga amalonda oyendayenda ndipo kaŵirikaŵiri samapezeka panyumba. Motero ana okulirapo amaumirizika kuchita ntchito yaukholo ndi kukonza chakudya, kuchita ntchito zapanyumba, ndipo ngakhale kulanga abale awo ang’ono. Kukhala kwawo ndi phande m’ntchito zauzimu kumasokonezeka. Inde, chipsinjo pa banjapo chingakhaledi chachikulu!
Zoonadi, pamene mikhalidwe yachuma ili yoipa, kholo silingachitire mwina kuti lisamalire banja lake kusiyapo kukafunafuna ntchito kutali. M’nthaŵi za Baibulo ana aamuna a Yakobo mwachionekere anafunikira kusiya mabanja awo kuti akapeze chakudya ku Igupto. (Genesis 42:1-5) Chotero pamene mkhalidwe wofananawo ubuka lerolino, mitu ya mabanja iyenera kupenda mapindu alionse akuthupi amene ntchito yakutaliyo ingawabweretse mowononga mkhalidwe wauzimu ndi wamalingaliro chifukwa cha kusiyana ndi banja kwanthaŵi yaitali. Mabanja ambiri amasankha kupirira vuto la ndalama m’malo mwa kusiyana kwa nyengo zazitali. Amakumbukira mawu a Paulo opezeka pa 1 Timoteo 6:8 akuti: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”—Yerekezerani ndi Miyambo 15:17.
Kaŵirikaŵiri pamakhala zinthu zina zochita m’malo mwa kuyendayenda. Mwa kuyamba kusonyeza luntha ndi luso, ena atha kudzipangira ntchito mwa kupereka mautumiki othandiza.a (Yerekezerani ndi Miyambo 31:24.) Kapena ingakhale nkhani ya kuchita ntchito zotsika zimene ena amaziona kukhala zawamba. (Aefeso 4:28) Mtumwi Paulo mwiniyo ‘anagwira ntchito usiku ndi usana’ kuti apeŵe kulemetsa ena pa zandalama. (2 Atesalonika 3:8) Amuna achikristu lerolino angathe kutsatira chitsanzo chimenecho.
Vuto la Sukulu
Vuto lina limaphatikizapo sukulu. M’madera ena a kutali, kuli kofala kwa makolo kutumiza ana awo kutali kukakhala ndi achibale kwa nyengo zazitali kuti anawo akaphunzire mokwanira. Pokhala osiyana ndi makolo awo, kaŵirikaŵiri ana amenewo amakhala ndi vuto la kufika pa misonkhano kapena kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda. Pokhala osapatsidwa chilango chofunikira, amagwera m’mayanjano oipa mosavuta. Monga chotulukapo chake, ambiri asiya moyo wachikristu.
Palibe chikayikiro chakuti maphunziro a kusukulu ali ndi mapindu ake. Koma Baibulo limaŵerengera kwambiri maphunziro auzimu, ndipo Mulungu wapatsa makolo thayo la kupereka malangizo amenewo. (Deuteronomo 11:18, 19; Miyambo 3:13, 14) Motero, kutumiza mwana kutali kwanyengo zazitali kudzafooketsa zoyesayesa za kholo za kumlera “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.b
Pamene mipata ya maphunziro kumaloko ionekera kukhala yosakwanira, makolo sangachitire mwina kusiyapo kuchita zimene iwo eniwo angathe kuti aphunzitse ana awo maluso ofunika. Thandizo limaperekedwanso ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ Yehova. (Yesaya 30:20, NW) Mipingo yakumaloko ya Mboni za Yehova ili ndi makonzedwe angapo a maphunziro. Mipingo yambiri imachititsa makalasi a kuphunzira kulemba ndi kuŵerenga. Sukulu Yautumiki Wateokratiki nayonso ili makonzedwe othandiza amene anganole luso la mwana la kuŵerenga ndi kulankhula momveka.
Lingaliro Loyenera la Kubala Ana
Kusamalira ana kungakhale kovuta kwambiri makamaka pamene ali ambiri. Makolo a mu Afirika kaŵirikaŵiri amanena kuti amakonda ana; nchifukwa chake amabala ambiri monga momwe angathere! Pamene kuli kwakuti ana angaonedwe monga obweretsa chuma, makolo ambiri samatha kusamalira mokwanira ana ambiri.
Zoonadi, Baibulo limanena kuti “ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.” (Salmo 127:3) Komabe, onani kuti mawu amenewo analembedwa m’nyengo ya mikhalidwe yabwino ku Israyeli. Pambuyo pake, njala yaikulu ndi nkhondo zinachititsa kubala ana kukhala chiyeso. (Maliro 2:11, 20; 4:10) Polingalira za mkhalidwe wovuta umene ulipo m’maiko omatukuka kumene, Akristu athayo ayenera kulingalira mwamphamvu kuti ndi ana angati amene angathedi kuwadyetsa, kuwaveka, kuwapatsa malo okhala, ndi kuwaphunzitsa. Ataŵerengera mtengo wake, okwatirana ambiri amasankha kuti ndi bwino kwambiri kusatsatira mwambo ndi kukhala ndi ana ochepa.c—Yerekezerani ndi Luka 14:28.
Mwachionekere, zino ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Pamene dongosololi likupitiriza kugwera kumapeto ake otsimikizirika, mosakayikira zitsenderezo zidzawonjezereka pa mabanja a m’maiko omatukuka kumene. Komabe, mwa kumamatira kwambiri ku mapulinsipulo a Mawu a Mulungu, mitu ya mabanja ingathe kusamalira mwachipambano zosoŵa zakuthupi ndi zauzimu zomwe za mabanja awo, pakuti Yehova akunena lonjezo ili kwa aja amene amamtumikira mokhulupirika kuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Inde, ngakhale m’maiko osauka, Akristu angayang’anizane mwachipambano ndi chitokoso cha kusamalira nyumba zawo!
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Kudzipangira Ntchito m’Maiko Osatukuka” mu kope la November 8, 1994, anzake a magazini athu ano, Galamukani!
b Kaamba ka tsatanetsatane wowonjezereka, onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1983.
c Chidziŵitso chothandiza chinaperekedwa mu mpambo wa nkhani zakuti “Family Planning—A Global Issue,” umene unatuluka mu Galamukani! [wachingelezi] wa February 22, 1993.