Kuŵeta Gulu la Mulungu Mwachikondi
“Ŵetani gulu la Mulungu lili mwa inu.”—1 PETRO 5:2.
1, 2. Kodi mkhalidwe waukulu wa Yehova nchiyani, ndipo kodi umenewu umaonekera motani?
M’MALEMBA Oyera monse, mwasonyezedwa bwino kwambiri kuti chikondi ndicho mkhalidwe waukulu wa Mulungu. “Mulungu ndiye chikondi,” amatero 1 Yohane 4:8. Popeza kuti chikondi chake chimasonyezedwa mu ntchito, 1 Petro 5:7 amanena kuti Mulungu “asamalira inu.” M’Baibulo, njira imene Yehova amasamalilira anthu ake yafanizidwa ndi njira imene mbusa wachikondi amasamalilira mwachikondi nkhosa zake: “Taonani, Ambuye Yehova . . . adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.” (Yesaya 40:10, 11) Davide anatonthozedwa chotani nanga kuti afikire pa kunena kuti: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasoŵa”!—Salmo 23:1.
2 Nkoyenera kuti Baibulo limafanizira anthu amene Mulungu amayanja ndi nkhosa, pakuti nkhosa zili zamtendere, zogonjera, zomvera kwa mbusa wawo wozisamalira. Monga Mbusa wachikondi, Yehova amasamalira kwambiri anthu ake onga nkhosa. Iye amasonyeza zimenezi mwa kuwagaŵira mwakuthupi ndi mwauzimu ndi mwa kuwatsogolera kupyola mu “masiku otsiriza” ovuta a dziko loipali kumka kudziko lake latsopano limene likudzalo.—2 Timoteo 3:1-5, 13; Mateyu 6:31-34; 10:28-31; 2 Petro 3:13.
3. Kodi ndimotani mmene wamasalmo anafotokozera njira imene Yehova amasamalira nkhosa zake?
3 Tamverani chisamaliro chachikondi cha Yehova pa nkhosa zake: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo. . . . Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa ku masautso awo onse. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi. Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.” (Salmo 34:15-19) Ha, nchitonthozo chachikulu chotani nanga chimene Mbusa Wachilengedwe Chonse ameneyu amapereka kwa anthu ake onga nkhosa!
Chitsanzo cha Mbusa Wabwino
4. Kodi ndi iti imene ili mbali ya Yesu m’kusamalira gulu la nkhosa la Mulungu?
4 Mwana wa Mulungu, Yesu, anaphunzira bwino kwambiri kwa Atate wake, pakuti Baibulo limatcha Yesu kukhala “Mbusa Wabwino.” (Yohane 10:11-16) Utumiki wake wofunika ku gulu la nkhosa la Mulungu walembedwa m’Chivumbulutso chaputala 7. Mu vesi 9, atumiki a Mulungu a m’tsiku lathu amatchedwa “khamu lalikulu, . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Ndiyeno vesi 17 limati: “Mwanawankhosa [Yesu] . . . adzawaŵeta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.” Yesu amatsogolera nkhosa za Mulungu kumadzi a choonadi amene amatsogolera ku moyo wosatha. (Yohane 17:3) Onani kuti Yesu akutchedwa “Mwanawankhosa,” kusonyeza mikhalidwe ya iye mwiniyo yonga ya nkhosa, iyeyo pokhala chitsanzo chachikulu cha kugonjera Mulungu.
5. Kodi Yesu anamva bwanji ponena za anthu?
5 Yesu anayendayenda pakati pa anthu pa dziko lapansi naona mkhalidwe wawo wochititsa chisoni. Kodi iye anachita motani pa vuto lawo? “Anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Nkhosa zopanda mbusa zimavutika kwambiri ndi zilombo zolusa, monga momwe zimachitira nkhosa za mbusa wosasamala. Koma Yesu anasamalira kwambiri, pakuti anati: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
6. Kodi ndi kulingalira kotani kumene Yesu anasonyeza kwa anthu osweka mtima?
6 Ulosi wa Baibulo unaneneratu kuti Yesu akachita mwachikondi ndi anthu: “Yehova wandidzoza ine . . . ndikamange osweka mtima, . . . ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.” (Yesaya 61:1, 2; Luka 4:17-21) Yesu sananyoze konse aumphaŵi ndi opanda mwaŵi. Mmalomwake, iye anakwaniritsa Yesaya 42:3: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi laŵi lozirala sadzalizima.” (Yerekezerani ndi Mateyu 12:17-21.) Anthu ovutika anali ngati bango lophwanyika, ngati zingwe za nyale zotsala pang’ono kuzima chifukwa chosoŵa mafuta. Pozindikira mkhalidwe wawo wochititsa chisoniwo, Yesu anawachitira chifundo ndi kuwapatsa nyonga ndi chiyembekezo, akumawachiritsa mwauzimu ndi mwakuthupi.—Mateyu 4:23.
7. Kodi nkuti kumene Yesu anatsogolera anthu amene anamvera iye?
7 Anthu onga nkhosa anatembenukira kwa Yesu mu unyinji waukulu. Kuphunzitsa kwake kunali kochititsa chidwi kwambiri kwakuti anyamata amene anatumizidwa kukamgwira anasimba kuti: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.” (Yohane 7:46) Eetu, atsogoleri achipembedzo achinyengowo anadandaula kuti: “Dziko litsata pambuyo pake pa Iye”! (Yohane 12:19) Koma Yesu sanadzifunire ulemu kapena ulemerero. Iye anatsogolera anthu kwa Atate wake. Anawaphunzitsa kutumikira Yehova chifukwa cha kukonda mikhalidwe Yake yabwinoyo: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse.”—Luka 10:27, 28.
8. Kodi ndimotani mmene kumvera kumene anthu a Mulungu amasonyeza kwa iye kulili kosiyana ndi kumene ena amasonyeza kwa olamulira adziko?
8 Yehova amakondwera chifukwa chakuti uchifumu wake wachilengedwe chonse umachirikizidwa ndi anthu ake onga nkhosa, kaamba ka kumkonda kwawo. Iwo modzifunira amasankha kumtumikira chifukwa cha kudziŵa kwawo mikhalidwe yake yokondeka. Nzosiyana chotani nanga ndi atsogoleri a dzikoli amene anthu awo amawamvera kokha chifukwa cha mantha, kapena monyinyirika, kapena chifukwa chakuti ali ndi cholinga chinachake! Kwa Yehova kapena kwa Yesu sikunganenedwe konse zomwe zinanenedwa ponena za papa wa Tchalitchi cha Roma Katolika kuti: “Iye anasiriridwa ndi ambiri, anawopedwa ndi onse, sanakondedwe ndi aliyense.”—Vicars of Christ—The Dark Side of the Papacy, lolembedwa ndi Peter De Rosa.
Abusa Ankhanza mu Israyeli
9, 10. Fotokozani za atsogoleri a Israyeli wakale ndi a m’zaka za zana loyamba.
9 Mosiyana ndi Yesu, atsogoleri achipembedzo a Israyeli m’tsiku lake analibe chikondi pa nkhosa. Anali ngati olamulira oyambirira amene Yehova ananena za iwo kuti: “Tsoka abusa a Israyeli odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa? . . . Zofooka simunazilimbitsa; yodwala simunaichiritsa, yothyoka simunailukira tchika, yopitikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi mowopsa.”—Ezekieli 34:2-4.
10 Mofanana ndi abusa andale amenewo, atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’zaka za zana loyamba anali ouma mtima. (Luka 11:47-52) Kuti asonyeze zimenezi, Yesu anasimba za Myuda wina amene anafwambidwa, kumenyedwa, nasiyidwa atakomoka m’mphepete mwa msewu. Wansembe Wachiisrayeli anadzera njirayo, koma poona Myudayo, anadzera mbali ina ya msewuwo. Mlevi anachita chimodzimodzi. Ndiyeno munthu wina wosakhala Mwisrayeli, Msamariya wonyozedwa, anadza pa iye nagwidwa chifundo ndi munthuyo. Anamanga mabala ake, namkweza pa nyama kumka naye kunyumba ya alendo, namsamalira. Iye analipira mwininyumba ya alendo nati adzabweranso kudzalipira ndalama zilizonse zowonjezereka.—Luka 10:30-37.
11, 12. (a) Kodi ndimotani mmene kuipa kwa atsogoleri achipembedzo kunakulira m’tsiku la Yesu? (b) Kodi nchiyani chimene Aroma potsirizira pake anachitira atsogoleri achipembedzo?
11 Atsogoleri achipembedzo a m’tsiku la Yesuwo anali oipa kwambiri kwakuti pamene Yesu anaukitsa Lazaro kwa akufa, akulu ansembe ndi Afarisi anasonkhanitsa Sanhedrin nati: “Titani ife? chifukwa munthu uyu [Yesu] achita zizindikiro zambiri. Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.” (Yohane 11:47, 48) Sanasamale za ubwino umene Yesu anali atachitira munthu wakufayo. Anali kudera nkhaŵa malo awo. Chotero “kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe [Yesu].”—Yohane 11:53.
12 Kuwonjezera kuipa kwawoko, akulu ansembe “anapangana kuti akaphe Lazaronso; pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.” (Yohane 12:10, 11) Zoyesayesa zawo zadyera za kutetezera malo awo zinali zosaphula kanthu, pakuti Yesu anali atawauza kuti: “Nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:38) Mogwirizana ndi mawuwo, mu mbadwo umenewo Aroma anadza nalanda ‘malo awo ndi mtundu wawo,’ ndi miyoyo yawonso.
Abusa Achikondi mu Mpingo Wachikristu
13. Kodi Yehova analonjeza kutumiza yani kukaŵeta gulu lake la nkhosa?
13 Mmalo mwa abusa ankhanza ndi adyera, Yehova akaika Mbusa Wabwino, Yesu, kuti akasamalire gulu Lake la nkhosa. Iye analonjezanso kuika abusa aang’ono achikondi kuti akasamalire nkhosa: “Ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzawopanso.” (Yeremiya 23:4) Motero, monga momwe zinalili m’mipingo Yachikristu ya m’zaka za zana loyamba zilinso chimodzimodzi lerolino, ‘kuika akulu m’midzi yonse’ kukuchitidwa. (Tito 1:5) Akulu auzimu ameneŵa amene amakwaniritsa ziyeneretso zolembedwa m’Malemba ayenera ‘kuŵeta gulu la Mulungu.’—1 Petro 5:2; 1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:7-9.
14, 15. (a) Kodi ndi mkhalidwe wamaganizo wotani umene ophunzira anaona kukhala wovuta kukulitsa? (b) Kodi nchiyani chimene Yesu anachita kuti awasonyeze kuti akulu ayenera kukhala atumiki odzichepetsa?
14 Posamalira nkhosa, “koposa zonse” akulu ayenera kukhala ndi “chikondano chenicheni” pa izo. (1 Petro 4:8) Koma ophunzira a Yesu, pokhala ofuna kwambiri kutchuka ndi malo, anafunikira kuphunzira zimenezi. Chotero pamene amayi a ophunzira aŵiri ananena kwa Yesu kuti: “Lamulirani kuti ana anga aŵiri ameneŵa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu,” ophunzira enawo anapsa mtima. Yesu anati kwa iwo: “Mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.”—Mateyu 20:20-28.
15 Panthaŵi ina, ophunzirawo ‘atatsutsana wina ndi mnzake, kuti wamkulu ndani,’ Yesu anati kwa iwo: “Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.” (Marko 9:34, 35) Kudzichepetsa ndi kufunitsitsa kutumikira kunafunikira kukhala mbali ya umunthu wawo. Komabe ophunzirawo anapitirizabe kukhala ndi vuto ndi malingaliro amenewo, pakuti pausiku weniweniwo Yesu ali pafupi kufa, pa chakudya chake chamadzulo chomaliza, “kutsutsana” kunabuka pakati pawo konena za amene anali wamkulu! Zimenezo zinachitika mosasamala kanthu kuti Yesu anali atawasonyeza mmene mkulu ayenera kutumikirira gulu la nkhosa; iye anali atadzichepetsa ndi kusambitsa mapazi awo. Iye anati: “Ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.”—Luka 22:24; Yohane 13:14, 15.
16. Kodi ndi ndemanga zotani zimene Watch Tower inanena mu 1899 ponena za mkhalidwe wofunika koposa wa akulu?
16 Mboni za Yehova nthaŵi zonse zaphunzitsa kuti akulu ayenera kukhala motero. Pafupifupi zaka zana zapitazo, Watch Tower ya April 1, 1899, inasimba za mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 13:1-8 ndi kuti: “Mtumwiyo akusonyeza bwino lomwe kuti chidziŵitso ndi kudziŵa kukamba bwino sizili zisonyezero zofunika koposa, koma chikondi chimene chimafunga mtima ndi kusonyezedwa m’zochita zonse za moyo, ndi kusonkhezera ndiponso kugwiritsira ntchito matupi athu aimfawa, ndicho chisonyezero chenicheni—umboni weniweni wa unansi wathu ndi Mulungu. . . . Mkhalidwe wofunika koposa umene uyenera kupezeka mwa aliyense wovomerezedwa kukhala mtumiki watchalitchi, kuti atumikire m’zinthu zoyera, choyamba uyenera kukhala mkhalidwe wachikondi.” Inanena kuti amuna amene sangatumikire modzichepetsa ndi chikondi “ali aphunzitsi oipa, ndipo mwachionekere angawononge zinthu kwambiri.”—1 Akorinto 8:1.
17. Kodi ndimotani mmene Baibulo limagogomezerera mikhalidwe imene akulu ayenera kukhala nayo?
17 Motero, akulu sayenera ‘kuchita ufumu’ pa nkhosa. (1 Petro 5:3) Mmalomwake, iwo ayenera kutsogolera m’kukhala “okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo.” (Aefeso 4:32) Paulo anagogomezera kuti: “Valani, . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; . . . koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”—Akolose 3:12-14.
18. (a) Kodi ndi chitsanzo chabwino chotani chimene Paulo anaika pochita ndi nkhosa? (b) Kodi nchifukwa ninji akulu sayenera kunyalanyaza zosoŵa za nkhosa?
18 Paulo anaphunzira kuchita zimenezi, akumati: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:7, 8) Mogwirizana ndi zimenezo, iye anati: “Limbikitsani amantha mtima, chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.” (1 Atesalonika 5:14) Mosasamala kanthu za mtundu wa vuto limene nkhosa zingawabweretsere, akulu ayenera kukumbukira Miyambo 21:13: “Wotseka makutu ake polira waumphaŵi, nayenso adzalira koma osamvedwa.”
19. Kodi nchifukwa ninji akulu achikondi ali dalitso, ndipo kodi ndimotani mmene nkhosa zimachitira ndi chikondi chotero?
19 Akulu amene amaŵeta gulu mwachikondi ndiwo dalitso ku nkhosa. Yesaya 32:2 aneneratu kuti: “Munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” Tili achimwemwe kudziŵa kuti ambiri a akulu athu lerolino amayenerera chithunzithunzi chimenechi chabwino kwambiri cha mpumulo. Aphunzira kugwiritsira ntchito lamulo lotsatirali la mkhalidwe: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Pamene akulu asonyeza mtundu umenewu wa chikondi ndi kudzichepetsa, nkhosa zimalabadira mwa kuwapatsa “ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo.”—1 Atesalonika 5:12, 13.
Lemekezani Kugwiritsiridwa Ntchito kwa Ufulu wa Kusankha
20. Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kulemekeza ufulu wa kusankha?
20 Yehova analenga anthu ndi ufulu wa kusankha zimene afuna. Pamene kuli kwakuti akulu ayenera kupereka uphungu ndipo ngakhale kulanga, iwo sayenera kulamulira moyo kapena chikhulupiriro cha wina. Paulo anati: “Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.” (2 Akorinto 1:24) Inde, “yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Yehova watipatsa ufulu wambiri mkati mwa malamulo ndi malamulo ake amkhalidwe. Motero akulu ayenera kupeŵa kuika malamulo pamene malamulo amkhalidwe a Malemba sakuswedwa. Ndipo ayenera kukaniza chikhoterero chilichonse cha kupereka malingaliro a iwo eni monga chiphunzitso kapena kulola kunyada kwawo kulepheretsa zinthu ngati wina sakugwirizana ndi malingaliro amenewo.—2 Akorinto 3:17; 1 Petro 2:16.
21. Kodi nchiyani chimene chingaphunziridwe pamkhalidwe wamaganizo wa Paulo kulinga kwa Filemoni?
21 Onani mmene Paulo, ali m’ndende ku Roma, anachitira ndi Filemoni, mwini kapolo Wachikristu wokhala ku Kolose ku Asia Minor. Kapolo wa Filemoni wotchedwa Onesimo anathaŵira ku Roma, nakhala Mkristu, ndipo anali kuthandiza Paulo. Paulo analembera Filemoni kuti: “Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m’malo mwako akadanditumikira ine m’ndende za Uthenga Wabwino: koma wopanda kudziŵa mtima wako sindinafuna kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.” (Filemoni 13, 14) Paulo anabweza Onesimo, akumapempha Filemoni kumchitira monga mbale Wachikristu. Paulo anadziŵa kuti gulu la nkhosa silinali lake; linali la Mulungu. Iye sanali mbuye wake koma mtumiki wake. Paulo sanalamulire Filemoni; analemekeza ufulu wake wa kusankha.
22. (a) Kodi nchiyani chimene akulu ayenera kumvetsetsa ponena za chimene chili malo awo? (b) Kodi Yehova akukulitsa gulu la mtundu wotani?
22 Pamene gulu la Mulungu likula, akulu owonjezereka amaikidwa. Iwowo, ndiponso ndi akulu okhala ndi chidziŵitso chambiri, ayenera kuzindikira kuti malo awo ali a utumiki wodzichepetsa. Mwanjira imeneyi, pamene Mulungu akupititsa gulu lake ku dziko latsopano, lidzapitirizabe kukula monga momwe iye akufunira—lolinganizidwa bwino koma losaika pachiswe chikondi ndi chifundo kaamba ka kuyendetsa zinthu bwino. Motero, gulu lake lidzakopa mowonjezereka anthu onga nkhosa amene adzaonamo umboni wakuti “amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino.” Zimenezi ziyenera kuyembekezeredwa m’gulu lozikidwa pa chikondi, chifukwa chakuti “chikondi sichitha nthaŵi zonse.”—Aroma 8:28; 1 Akorinto 13:8.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene Baibulo limafotokozera za chisamaliro cha Yehova kwa anthu ake?
◻ Kodi Yesu amachita mbali yotani m’kusamalira gulu la nkhosa la Mulungu?
◻ Kodi ndi mkhalidwe waukulu uti umene akulu ayenera kukhala nawo?
◻ Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kulingalira za ufulu wa kusankha wa nkhoso?
[Chithunzi patsamba 16]
Yesu, “Mbusa Wabwino,” anasonyeza chifundo
[Zithunzi patsamba 17]
Atsogoleri achipembedzo oipa anapanga chiwembu cha kupha Yesu