Sonyezani ‘Chifundo Chachikulu’
MASIKU ano pali anthu ambiri amene akufunika kuwachitira chifundo chifukwa cha njala, matenda, umphawi, ziwawa ndi masoka achilengedwe. Munthu wachifundo ndi amene amamvera anzake chisoni ndipo amayesetsa kuwathandiza. Munthu wachifundo amalimbikitsa anthu amene ali m’mavuto mofanana ndi mmene madzi ozizira amatsitsimulira munthu amene watopa ndi dzuwa.
Tingawasonyeze anthu chifundo mwa zochita zathu ndi zolankhula zathu makamaka kuwathandiza panthawi imene ali m’mavuto. Ndi bwino kusonyeza chifundo kwa anthu onse osati anzathu kapena apabanja pathu okha. Tiyenera kusonyeza chifundo ngakhale anthu amene sitikuwadziwa. Paulaliki wake wa paphiri Yesu Khristu, anafunsa kuti: “Mukamakonda okhawo amene amakukondani, mudzalandira mphoto yotani?” Yesu yemwe anali munthu wachifundo ananenanso kuti: “Chotero zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”—Mateyo 5:46, 47; 7:12.
Mungawerenge mawu amenewa m’Malemba Oyera. Anthu ambiri amavomereza kuti Baibulo ndi buku la malangizo abwino kwambiri a mmene tingasonyezere chifundo. Malemba amatiuza mobwerezabwereza udindo umene tili nawo wothandiza anthu ena amene sangathe kudzithandiza okha pazifukwa zosiyanasiyana. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti Mlembi wake, Yehova Mulungu yemwe ndi Mlengi ndiye kuchimake kwa chifundo.
Mwachitsanzo, timawerenga kuti: “[Mulungu] aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kum’patsa chakudya ndi chovala.” (Deuteronomo 10:18) Baibulo limafotokoza kuti Yehova Mulungu ndi ‘wochitira chiweruzo osautsika; ndi wopatsa anjala chakudya.’ (Salmo 146:7) Yehova anapereka malangizo onena za anthu ovutika othawa kwawo kuti: “Mlendo . . . mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; um’konde monga udzikonda wekha.”—Levitiko 19:34.
Komabe, sikuti zimangochitika mwachibadwa kuti munthu asonyeze chifundo. Mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Kolose kuti: “Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo muvale umunthu watsopano, umene kudzera mwa kudziwa zinthu molondola ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha Iye amene anaulenga . . . Monga osankhika a Mulungu, oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu.”—Akolose 3:9, 10, 12.
Choncho, pamafunika khama kuti tisonyeze chifundo. Ndipo khalidwe limeneli ndi mbali ya “umunthu watsopano” umene Akhristu amafunika kuvala. Paulo anakhala mu nthawi imene anthu anali ankhanza ku Roma. Iye analimbitsa okhulupirira anzake kusinthiratu umunthu wawo kuti azitha kumvera chisoni anzawo komanso kuwasonyeza chifundo kwambiri.
Ubwino Wosonyeza Chifundo
Anthu ena amaganiza kuti munthu wachifundo ndi wofooka. Koma kodi maganizo amenewa ndi olondola?
Ayi ndithu si olondola. Chimene chimachititsa munthu kusonyeza chifundo chenicheni ndi chikondi cha pansi pamtima chimene chimachokera kwa Mulungu yemwe khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:16) Moyenerera Yehova amatchedwa “Tate wa chifundo chachikulu ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Mawu akuti “chifundo chachikulu” amatanthauza “kuwamvera chisoni anthu amene akuvutika.” Ndithudi, Yehova ndi “wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa” omwe.—Luka 6:35.
Mlengi wathu amafuna kuti ifenso tizisonyeza makhalidwe abwino, monga chifundo. Lemba la Mika 6:8 limati: “Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Lemba la Miyambo 19:22 limati: “Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake.” Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene anasonyeza ndendende makhalidwe a Atate wake analimbikitsa otsatira ake chimodzimodzi kuti: “Pitirizani kukhala achifundo, monga Atate wanu ali wachifundo.”—Luka 6:36.
Tili ndi chifukwa chomveka chochitira zimenezi, chifukwa timapindula kwambiri tikasonyeza chifundo. Nthawi zambiri timatsimikiza mawu a pa Miyambo 11:17 akuti: “Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.” Tikachitira chifundo munthu amene akuvutika, Mulungu amaona ngati kuti tachitira Iyeyo. Amaona kuti ali ndi udindo wobwezera chifundo kwa wolambira wake aliyense amene anasonyeza chifundo munthu wina. Mfumu Solomo inalemba mouziridwa kuti: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.” (Miyambo 19:17) Naye Paulo analemba kuti: “Mukudziwa kuti chabwino chilichonse chimene wina aliyense angachite, adzachilandiranso kwa Yehova.”—Aefeso 6:8.
Chifundo chimathandiza anthu kukhala ogwirizana, kuthetsa mikangano ndi kusamvana, ngakhalenso kukhululukirana. Pangakhale kusamvana chifukwa chakuti nthawi zambiri timanena molakwitsa pofotokoza maganizo athu ndi mmene tikumvera mumtima, kapena ena angaone molakwika zochita zathu. Apa m’pamene chifundo chimatithandiza kukhalabe ndi mtendere. Sikovuta kukhululukira munthu amene amadziwika kuti ndi wachifundo. Chifundo chimatithandiza kutsatira malangizo a Paulo kwa Akhristu akuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaula za mnzake.”—Akolose 3:13.
Kusonyeza Chifundo Ndiko Kuchita Zinthu Zothandiza Ena
Chifundo chikhoza kuchepetsa mavuto. Monga taonera munthu wachifundo amamvera chisoni anthu amene akuvutika ndipo amawafunira zabwino komanso amayesetsa kuwathandiza.
Akhristu akamasonyeza chifundo amakhala akutsanzira Yesu. Iye sankalephera kuthandiza ena mwakuthupi ndi mwauzimu chifukwa chotanganidwa. Akadziwa kuti ena akufunikira thandizo, anali kuwachitira chifundo ndi kupeza njira yowathandizira.
Taonani zimene Yesu anachita ataona chikhamu cha anthu osauka mwauzimu. Iye “poona chikhamu cha anthu, anawamvera chisoni, chifukwa anali okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mateyo 9:36) Ponena za mawu akuti “anawamvera chisoni” amene ali palembali, katswiri wina wa maphunziro a Baibulo, anati mawuwa amatanthauza “maganizo amene amachititsa munthu kuchita zinthu mochokera pansi pamtima.” Ndipotu amenewa ndi mawu amene m’chigiriki amatsindika kwambiri mfundo yakuti munthu ndi wachifundo.
Mofananamo, Akhristu amene ali achifundo amathandiza mwamsanga anthu amene ali osowa mwakuthupi ndi mwauzimu. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Nonsenu mukhale a maganizo amodzi, omverana chisoni, okonda abale, a chifundo chachikulu.” (1 Petulo 3:8) Mwachitsanzo taganizirani izi: Banja lina lachikhristu limene linali losauka litasamukira ku dera lina chifukwa chodwala, Akhristu anzawo kumeneko anawapatsa nyumba kuti azikhalamo kwaulere kwa miyezi 6. Mwamuna wa m’banjali anati: “Tsiku lililonse abale ankabwera kudzationa kuti adziwe kuti tikupeza bwanji, ndipo ankatilimbikitsa zimene zinatithandiza kuona ngati kuti tinali kunyumba kwathu kwenikweni.”
Akhristu oona amaderanso nkhawa anthu amene sakuwadziwa. Iwo amasangalala kuthera nthawi yawo, mphamvu zawo ndi zinthu zimene ali nazo kuti athandize anthu amene sakuwadziwa n’komwe. Anthu omwe tawatchula m’nkhani yoyamba ija amene anadzipereka kuthandiza anthu amene sankawadziwa n’komwe anali Mboni za Yehova.
Choncho, mpingo wachikhristu uli ndi anthu amene ali achifundo ndi okoma mtima. Ndipotu, Akhristu amayesetsa kuthandiza ena chifukwa chakuti ali ndi chikondi. Timafunika kuchitira chifundo ndi kuthandiza ana amasiye ndi akazi amasiye a mu mpingo chifukwa amakhala ndi mavuto osiyanasiyana. Tiyeni tiziyesetsa kuthandiza anthu amenewa amene akuvutika ndi umphawi, akusowa chithandizo cha mankhwala, malo ogona, kapena mavuto ena ambiri.
Taganizirani za banja lina ku Greece. Mwamuna anadwala sitiroko. Iye ndi mkazi wake anawatengera ku chipatala china cha kutali kwambiri. Komabe, banjali linkadalira ndalama zochepa zimene linkapeza likagulitsa malalanje amene ankalima. Kodi ndani akanawathandiza kuthyola ndi kuwagulitsira malalanjewo panthawi imene anali kuchipatala? Mpingo wawo ndi umene unagwira ntchitoyo ndipo zimenezi zinathandiza banjalo kupeza ndalama ndiponso kukhala ndi mtendere wa m’maganizo.
Tingasonyeze chifundo m’njira zambirimbiri. Mwachitsanzo, Akhristu achifundo amadziwa kuti nthawi zina chimene anthu ena ovutika amafuna kwambiri ndi kuwayendera, kumvetsera mavuto awo komanso kuwalimbikitsa ndi Malemba.—Aroma 12:15.
Sangalalani Kukhala ndi Anthu Achifundo
Mpingo wachikhristu wapadziko lonse ndi malo a mtendere ndi olimbikitsa amene kumapezeka anthu okoma mtima ndi achifundo. Akhristu oona amadziwa kuti anthu amakonda munthu wachifundo osati wankhanza. Choncho, amayesetsa kwambiri kusonyeza ‘chifundo chachikulu’ m’njira zambiri potsanzira Atate wawo wakumwamba.
Mboni za Yehova zikukupemphani kuti mudzaone nokha chifundo, chikondi ndi kuganizirana kumene kuli pakati pawo. Iwo akukutsimikizirani kuti mudzalandiridwa ndipo mudzasangalaladi kukhala nawo.—Aroma 15:7.
[Chithunzi patsamba 5]
Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Kolose kuvala chifundo chachikulu
[Zithunzi patsamba 7]
Yesu akadziwa kuti ena akufunikira thandizo, anali kuwachitira chifundo ndi kupeza njira yowathandizira