Maukwati Osangalatsa Amene Amalemekeza Yehova
Welsh ndi Elthea anakwatirana ku Soweto, South Africa, mu 1985. Nthaŵi ndi nthaŵi, amayang’ana zithunzi za ukwati wawo limodzi ndi mwana wawo wamkazi, Zinzi, n’kumakumbukiranso zochitika patsiku losangalatsa limenelo. Zinzi amakonda kutchula mayina a anthu amene ali pazithunzizo omwe analipo paukwatiwo ndipo amakonda makamaka kuyang’ana zithunzi za amayi ake atatchena.
UKWATIWO unayamba ndi nkhani yaukwati yomwe inakambidwira m’holo ya boma ku Soweto komweko. Kenako anyamata ndi atsikana achikristu anaimba nyimbo zotamanda Mulungu m’tchuni cha mbali zinayi. Pambuyo pake, oitanidwawo anadya chakudya pamene tepi ya nyimbo za Ufumu inali kuimba chamunsimunsi. Panalibe moŵa, ndipo panalibenso nyimbo zokweza kwambiri kapena kuvina. Koma oitanidwawo anasangalala ndi kucheza ndi kuthokoza banjalo. Zochitika zonse zinatenga maola ngati atatu. “Unali ukwati wosangalatsa kwambiri womwe sindidzauiwala,” anatero Raymond, mkulu wachikristu, pokumbukira.
Nthaŵi imene amachita ukwati wawo, Welsh ndi Elthea anali antchito odzifunira panthambi ya ku South Africa ya Watch Tower Bible and Tract Society. Sakanatha kuchita ukwati wofuna ndalama zambiri. Akristu ena asankha kusiya utumiki wanthaŵi zonse kuti akaloŵe ntchito yolembedwa kuti apeze ndalama zochitira ukwati wadzaoneni. Komabe, Welsh ndi Elthea ndi osangalalabe kuti anasankha kukhala ndi ukwati wosafuna zambiri chifukwa chakuti unawalola kupitirizabe kutumikira Mulungu monga atumiki a nthaŵi zonse mpaka kubadwa kwa Zinzi.
Nangano bwanji ngati okwatiranawo akufuna kukhala ndi nyimbo zakudziko ndi kuvina paukwati wawo? Bwanji ngati asankha kudzakhala ndi vinyo ndi moŵa wina? Bwanji ngati ali nazo ndalama zochitira ukwati waukulu wofuna zinthu zambiri? Kodi angachite motani kuti aonetsetse kuti ukwatiwo udzakhala wosangalatsa woyenereradi olambira Mulungu? Mafunso ameneŵa n’ngofunikira kuwafufuza bwino kwambiri, popeza Baibulo limalamula kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.
Kupeŵa Mapokoso
Sitingayerekeze n’komwe za ukwati wopanda chisangalalo. Komanso kusangalala mopambanitsa kuli ndi ngozi yaikulu yochita phwando losalamulirika. Pamaukwati ambiri a anthu osakhala Mboni, pamachitika zinthu zosalemekeza Mulungu. Mwachitsanzo, pamaukwati ambiri anthu amamwa moŵa mpaka kuledzera. N’zomvetsa chisoni kuti zimenezi zachitikanso ngakhale pamaukwati ena achikristu.
Baibulo limachenjeza kuti “chakumwa chaukali chisokosa.” (Miyambo 20:1) Mawu achihebri otembenuzidwa kuti “kusokosa” amatanthauza “kupanga phokoso lalikulu.” Ngati moŵa ungapangitse munthu mmodzi kusokosera, tangolingalirani zimene ungachite kwa chinamtindi cha anthu amene asonkhana pamodzi n’kumwa mopambanitsa! Mosakayikira, zochitika zimenezo zingafike pokhala “kuledzera, mchezo, ndi zina zotere” mosavuta, zomwe Baibulo limandandalitsa monga “ntchito za thupi.” Zochitika zimenezi ndizo zimapangitsa aliyense wosalapa kukhala wosayenerera kulandira moyo wosatha mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.—Agalatiya 5:19-21.
Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “mchezo” ankatchulidwa ponena za achinyamata oledzera omwe ankaimba, kuvina, ndi kuseŵera ndi ziŵiya zoimbira nyimbo mumsewu. Ngati anthu akumwa moŵa mosadziletsa paukwati, ndiponso ngati pali nyimbo zopokosera ndi kuvina kotayirira, pali ngozi yaikulu yakuti chochitikacho chidzakhala ngati mchezo. Zikatero, ofooka angagwere mwamsanga m’chiyeso ndi kuchita ntchito zina zathupi monga “dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, [kapena kuyamba] ndewu.” Kodi n’chiyani chingachitidwe pofuna kupeŵa ntchito zathupi zimenezi kuti zisawononge chisangalalo cha ukwati wachikristu? Kuti tiyankhe funso limenelo, tiyeni tikambirane zimene Baibulo limasimba ponena za ukwati winawake.
Ukwati Umene Yesu Anapezekapo
Yesu ndi ophunzira ake anaitanidwa ku ukwati wina ku Kana wa ku Galileya. Iwo anavomereza kuitanidzako, ndipo Yesu anachitaponso kanthu kena kuti anthu asangalale paukwatiwo. Vinyo atatha, iye mozizwitsa anapanganso wina wabwino koposa. Pambuyo pa ukwatiwo, m’posakayikitsa kuti wotsala anatsala ndi mkwati woyamikirayo ndi banja lake amene anam’gwiritsa ntchito kwa kanthaŵi ndithu.—Yohane 2:3-11.
Pali maphunziro ambiri amene tingaphunzirepo pa ukwati umene Yesu anapezekapo. Choyamba, Yesu ndi ophunzira ake sanapite kuphwando laukwatilo osaitanidwa. Baibulo limanena molunjika kuti anachita kuitanidwa. (Yohane 2:1, 2) Momwemonso, m’mafanizo ake aŵiri a maphwando aukwati, Yesu mobwerezabwereza ananenapo kuti anthuwo analipo chifukwa anachita kuitanidwa.—Mateyu 22:2-4, 8, 9; Luka 14:8-10.
M’mayiko ena, ndi chizoloŵezi chawo kuti aliyense amadzimva kukhala womasuka kupita kuphwando laukwati kaya wachita kuitanidwa kapena ayi. Komabe, zimenezi zingapangitse mavuto a ndalama. Mkwati ndi mkwatibwi omwe alibe ndalama zambiri angaloŵe m’ngongole pofuna kuonetsetsa kuti padzakhale chakudya ndi zakumwa zokwanira khamu laukulu wosadziŵika bwino. Chotero, ngati mkwati ndi mkwatibwi asankha kukhala ndi phwando laling’ono la anthu oŵerengeka okha, Akristu anzawo omwe sanaitanidwe ayenera kumvetsa ndi kulemekeza zimenezi. Mwamuna wina amene anachitira ukwati wake ku Cape Town, South Africa, akukumbukira kuti anaitana anthu 200 kuukwati wake. Koma panapezeka anthu 600, ndipo zakudya zinangotha mosayembekezereka. Pakati pa osaitanidwawo panabwera basi yodzaza ndi anthu omwe anabwera kudzaona mzinda wa Cape Town kumapeto kwa mlungu waukwatiwo. Wotsogolera alendo apabasi amenewo anali wachibale wapatali wa mkwatibwi ndipo anaganiza kuti ali ndi ufulu wobwera ndi gulu lonselo ngakhale popanda kupempha kaye mkwati kapena mkwatibwi!
Pokhapokha atanena kuti aliyense angabwere kuchakudya chaukwati, wotsatira woona wa Yesu adzapeŵa kupita wosaitanidwa kuphwando laukwati ndi kudya nawo zakudya za anthu oitanidwa. Awo amene mtima wawo ukuwasonkhezera kupita ngakhale kuti sanaitanidwe adzifunse kuti, ‘Kodi kupezeka kwanga paphwando laukwati limeneli sikudzasonyeza kuti eni ukwatiwo sindiwakonda? Kodi sindidzasokoneza makonzedwe awo ndi chisangalalo chaukwati wawo?’ M’malo mokhumudwa kuti sanaitanidwe, Mkristu wachifundo atha kutumizira banjalo uthenga wowathokoza mwachikondi ndi kuwafunira madalitso a Yehova. Angaganizirenso ngakhale zothandiza banjalo mwa kuwatumizira mphatso kuti awonjezere chisangalalo chaukwati wawo.—Mlaliki 7:9; Aefeso 4:28.
Kodi ndi Udindo wa Yani?
M’madera ena a mu Afirika, mwambo wawo ndi wakuti achibale achikulire ndi amene amakonza phwando laukwati. Mkwati ndi mkwatibwi angathokoze kwambiri pazimenezi, chifukwa chakuti amawathandiza pankhani ya ndalama. Angaonenso kuti zimawachotsera udindo pa chilichonse chomwe chingachitike. Komabe, asanalole thandizo lina lililonse la achibale achifundo, okwatiranawo ayenera kuonetsetsa kuti zofuna zawo zidzatsatiridwa.
Ngakhale kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu “wotsika Kumwamba,” palibe chilichonse chosonyeza kuti analanda ulamuliro wonse nayang’anira zochitika zochuluka paukwati wa ku Kana. (Yohane 6:41) M’malo mwake, nkhani ya m’Baibulo imatiuza kuti winawake anaikidwa kuti akhale “mkulu wa phwando.” (Yohane 2:8) Mwamunayu tsopano ndi amene anali ndi udindo woonetsetsa kuti zomwe zikuchitika n’zofuna za mutu wa banja watsopano, amene ali mkwati.—Yohane 2:9, 10.
Achibale achikristu ayenera kulemekeza mutu woikidwa ndi Mulungu wa banja latsopanolo. (Akolose 3:18-20) Ndiye ayenera kukhala ndi udindo pa zimene zikuchitika pa ukwati wake. Mwachibadwa, mkwati ayenera kulingalira bwino ndipo, ngati n’kotheka, kulolera zofunanso za mkwatibwi, makolo ake, ndi apongozi ake. Ngakhale zili motero, ngati achibale alimbikira kukonza zinthu motsutsana ndi zofuna za amene akukwatiranawo, ndiye kuti aŵiriwo angafunikire kukana thandizo lawo mwaulemu ndi kudzilipirira ukwati wawo waung’ono. Zikayenda motere palibe chimene chidzachitika chimene chidzasiyira mkwati ndi mkwatibwi madandaulo akamakumbukira zomwe zinachitika. Mwachitsanzo, paukwati wina wachikristu mu Afirika, wachibale wosakhulupirira amene anali woyendetsa ukwati anachita mwambo wolambira makolo akufa pogwiritsa ntchito zakumwa!
Nthaŵi zina banjalo limanyamuka kupita kutchuthi madyerero a ukwati ali m’kati. Ngati zatere, mkwati ayenera kulinganiza kuti anthu ena osamala aonetsetse kuti miyezo ya Baibulo ikutsatiridwa ndi kuti madyererowo athe panthaŵi yabwino.
Kulinganiza Bwino Ndiponso Kusamala
N’zoonekeratu kuti panali chakudya chokwanira paukwati womwe Yesu anapezekapo, popeza Baibulo limati linali phwando laukwati. Monga taonera kale, panalinso vinyo wochuluka. Mosakayikira, panali nyimbo zabwino ndi kuvina modzilemekeza chifukwa chakuti n’zimene Ayuda ankakonda kuchita pamacheza awo. Ndizo zimene Yesu anasonyeza m’fanizo lake lotchukalo la mwana woloŵerera. Atate olemera a m’fanizo limenelo anasangalala kwambiri kuti mwana wawo walapa ndipo wabwerera moti anati: “[Tiyeni] tidye, tisekere.” Malinga n’kunena kwa Yesu, madyererowo anaphatikizapo “kuimba ndi kuvina.”—Luka 15:23, 25.
Chochititsa chidwi n’chakuti Baibulo silitchula mwachindunji kuti paukwati wa ku Kana panali nyimbo ndi kuvina. Ndiponso, nkhani zonse za m’Baibulo zonena za ukwati sizitchula kuvina. Zikuoneka kuti pakati pa atumiki okhulupirika a Mulungu m’nthaŵi za Baibulo, kuvina kunali kwamwadzidzidzi ndipo osati chochitika chofunika koposa cha maukwati awo. Kodi tingatengepo phunziro lililonse pamenepa?
Pamaukwati ena mu Afirika, amagwiritsa ntchito zoimbira zamagetsi zamphamvu kwambiri. Nthaŵi zina nyimbo zimakhala zaphokoso zedi moti anthu sangayankhulane bwinobwino n’kumvana. Nthaŵi zina sipakhala chakudya chokwanira koma pamakhala chigule chadzaoneni chomwe mwamsanga mavinidwe ake amakhala osadziletsa. M’malo mokhala phwando laukwati, zochitika zimenezi zimasanduka nthaŵi yosonyeza ukatswiri wovina. Kuwonjezera apo, nyimbo zaphokosozo zimaitana anthu oyambitsa chipwirikiti, anthu achilendo amene amangobwera osaitanidwa.
Popeza kuti nkhani za m’Baibulo zokhudza maukwati sizigogomeza nyimbo ndi kuvina, kodi zimenezi siziyenera kutsogolera anthu amene akukonzekera ukwati umene udzalemekeza Yehova? Koma pokonzekera maukwati angapo aposachedwapa kumwera kwa Afirika, anyamata achikristu amene anasankhidwa kuti akhale operekeza mkwati ndi mkwatibwi anathera nthaŵi yaitali kwambiri poyeserera masitepe ovuta ovinira. Kwa miyezi ingapo iwo anawononga nthaŵi yawo yochulukitsitsa m’njira imeneyi. Komatu Akristu ayenera ‘kugula nthaŵi’ kaamba ka “zinthu zofunika kwambiri,” monga ntchito yolalikira, phunziro laumwini, ndi kupezeka pamisonkhano yachikristu.—Aefeso 5:16, NW; Afilipi 1:10, NW.
Kungoonera kuchuluka kwa vinyo amene Yesu anapanga, zikuoneka kuti ukwati wa ku Kana unali waukulu, wokhala ndi zambiri. Komabe, tingatsimikizire kuti panalibe chiphokoso paukwatiwo ndi kutinso oitanidwawo sanamwetse moŵa monga momwe zinkachitikira pamaukwati ena achiyuda. (Yohane 2:10) Kodi tingatsimikizire motani zimenezi? Chifukwa chakuti Ambuye Yesu Kristu anali pomwepo. Mwa anthu onse, Yesu akanakhala wosamala koposa kumvera lamulo la Mulungu lonena za mayanjano oipa lakuti: “Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera.”—Miyambo 23:20, Buku Loyera.
Choncho ngati mkwati ndi mkwatibwi asankha kukhala ndi vinyo kapena moŵa wina paukwati wawo, ayenera kulinganiza kuti zimenezi ziyang’aniridwe ndi anthu osamala kwambiri. Ndipo ngati asankha kuti padzakhale nyimbo, ayenera kusankha nyimbo zoyenerera ndi kukhala ndi munthu wosamala woyang’anira kukwera kapena kutsika kwa voliyumu. Anthu oitanidwawo sayenera kuloledwa kuloŵerera ndi kuikapo nyimbo zokayikitsa kapena kukweza kwambiri voliyumu ya choimbiracho. Ngati padzakhala kuvina, zimenezo zingachitidwe m’njira yaulemu ndi modziletsa. Ngati achibale osakhulupirira kapena Akristu osakhwima m’nzeru avina monyanyula kapena modzutsa chilakolako chonyansa, mkwati angafunikire kusintha nyimbo zoimbidwazo kapena mwanzeru kupempha kuti pasakhalenso kuvina. Apo ayi, phwando laukwati lingasanduke chipwirikiti ndi kukhumudwitsa ena.—Aroma 14:21.
Chifukwa cha kuopsa kwa mavinidwe ena amakono, nyimbo zosokosa, ndi kumwa moŵa mosadziletsa, akwati angapo achikristu asankha kusakhala ndi zochitika zimenezi paukwati wawo. Ena anyozedwa pachifukwa chimenechi, koma m’malo mwake ayenera kuthokozedwa kaamba kofunitsitsa kupeŵa chilichonse chimene chingadzetse chitonzo padzina loyera la Mulungu. Komanso, akwati ena amalinganiza nyimbo zoyenerera, nthaŵi yovina, ndi moŵa pang’ono. M’mikhalidwe yonse iŵiri, mkwati ndiye ali ndi udindo pa zimene walola kuchitika paukwati wake.
Mu Afirika anthu ena osakhwima m’nzeru amanyoza maukwati olemekezeka achikristu namanena kuti amakhala ngati ali pamaliro. Koma amenewo si malingaliro anzeru. Ntchito zauchimo zathupi zingadzetse chisangalalo cha kanthaŵi kochepa, koma zimasiya Akristu ndi chikumbumtima chovutika ndipo zimadzetsa chitonzo pa padzina la Mulungu. (Aroma 2:24) M’malo mwake, mzimu woyera wa Mulungu umapatsa chisangalalo choona. (Agalatiya 5:22) Mabanja ambiri achikristu amakumbukira tsiku lawo laukwati monyadira, podziŵa kuti chinali chochitika chosangalatsa, osati “chokhumudwitsa.”—2 Akorinto 6:3.
Welsh ndi Elthea amakumbukirabe ndemanga zambiri zolimbikitsa za achibale osakhulupirira amene anapezeka paukwati wawo. Winawake anati: “Tatopa nawo maukwati aphokoso amene amachitika masiku ano. Zinali zosangalatsa kwambiri kuonako ukwati wochitika mwachifatse.”
Chofunika koposa n’chakuti maukwati achikristu osangalatsa ndiponso aulemu amalemekeza Woyambitsa ukwati, Yehova Mulungu.
[Bokosi/Chitunzi patsamba 22]
MPAMBO WA ZINTHU ZOFUNIKA KUCHITIDWA POKONZEKERA MADYERERO A UKWATI
• Ngati mwapempha wachibale wosakhulupirira kuti adzayankhulepo, kodi mwatsimikizira kuti sadzaloŵetsapo miyambo ina yosakhala yachikristu?
• Ngati padzakhala nyimbo, kodi mwasankha nyimbo zoyenerera zokhazokha?
• Kodi nyimbo zanu zidzaimbidwa mosapokosera?
• Ngati padzakhala kuvina, kodi kudzachitika mwaulemu?
• Kodi moŵa udzaperekedwa mosapambanitsa?
• Kodi anthu osamala adzayang’anira kuperekedwa kwa moŵawo?
• Kodi mwaika nthaŵi yabwino yodzamalizira madyerero aukwati?
• Kodi padzakhala anthu osamala oyang’anira kuti zinthu zikuyenda mwadongosolo mpaka kumapeto?