‘Chachikulu cha Izi Ndicho Chikondi’
‘Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.’—1 AKORINTO 13:13.
1. Kodi katswiri wa miyambo ndi zikhulupiriro za anthu ananenanji ponena za chikondi?
MMODZI wa akatswiri otchuka kwenikweni a miyambo ndi zikhulupiriro za anthu m’dziko ananenapo kuti: “Tamvetsetsa kwanthaŵi yoyamba m’mbiri yamafuko athu kuti chinthu chofunikira koposa m’maganizo mwa munthu ndicho chikondi. Icho chiri pakati pa zosoŵa zonse za munthu monga mmene dzuŵa lathu liriri pakati pa thambo lathu nilimazungululidwa ndi maplaneti. . . . Mwana wosakondedwa amakhala wosiyana kwambiri mkapangidwe ka zam’minyewa yake, kagwiridwe ka thupi lake, ndi maganizo ake ndi amene amakondedwa. Woyambayo amakula mosiyana ndi wapambuyoyo. Chomwe tsopano tikudziŵa nchakuti munthu amabadwira kuti akhale ndi moyo monga ngati kukhala ndi moyoko ndikukonda nchinthu chimodzi chogwirizana. Ndithudi, ichi sichatsopano. Uwu ndi umboni weniweni wa Ulaliki wa Paphiri.”
2. (a) Kodi mtumwi Paulo anakusonyeza motani kufunika kwa chikondi? (b) Kodi ndimafunso otani amene tsopano afunikira kulingaliridwa?
2 Inde, monga mmene munthu wamaphunziro a kudzikoyu anafotokozera, mawu owonawa ponena za kufunika kwa chikondi kaamba ka moyo wabwino wa anthu sichinthu chatsopano. Icho changozindikiridwa tsopano ndi anthu ophunzira a kudziko, koma chinawonekera m’Mawu a Mulungu zaka zoposa mazana 19 zapitazo. Ndicho chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.’ (1 Akorinto 13:13) Kodi mukudziŵa chifukwa chimene chikondi chikukhalira chachikulu kuposa chikhulupiriro ndi chiyembekezo? Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chikondi ndicho chachikulu pa mikhalidwe ya Mulungu ndi zipatso za mzimu?
Mitundu Inayi ya Chikondi
3. Kodi ndizitsanzo zotani za m’Malemba zomwe ziripo za chikondi chosonyezedwa kwa mwamuna ndi mkazi?
3 Kuthekera kwa munthu kusonyeza chikondi ndiko chisonyezero cha nzeru ya Mulungu ndi nkhaŵa yachikondi kaamba ka anthu. Mosangalatsa, Agiriki akale anali ndi mawu anayi a “chikondi.” Limodzi linali eʹros, kutanthauza chikondi chokhala pakati pa mwamuna ndi mkazi chogwirizanitsidwa ndi chikhumbo cha kugonana. Alembi a Malemba Achikristu Achigiriki analibe nthaŵi yogwiritsira ntchito eʹros, chinkana kuti Septuagint imagwiritsira ntchito mawu ofanana nayo pa Miyambo 7:18 ndi 30:16, ndipo muli zilozero zina zokhudza chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazichi m’Malemba Achihebri. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti Isake “anamkonda” Rebeka. (Genesis 24:67) Chitsanzo chodziŵikadi cha chikondi cha mtundu uwu chikupezedwa mnkhani ya Yakobo, amene mwachiwonekere anamkonda Rakele wokongolayo kungomuwona nthaŵi yoyamba. Kwenikweni, ‘Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.’ (Genesis 29:9-11, 17, 20) Nyimbo ya Solomo imafotokozanso chikondi chapakati pa mwamuna ndi mkazichi chokhala kwa mbusa ndi namwali. Koma sikungagogomezeredwe kwambiri kuti mtundu umenewu wa chikondi, chimene chingakhale magwero a kukhala wokhutiritsidwa kwambiri ndi chisangalalo, chiyenera kusonyezedwa mogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino achilungamo a Mulungu okha. Baibulo likutifotokozera kuti chikondi cha ‘kukondwa ndi chikondi chake osaleka’ chiyenera kusonyezedwa kwa mkazi wokwatiwa yekha ndi mwamuna.—Miyambo 5:15-20.
4. Kodi chikondi chapabanja chasonyezedwa motani mwafanizo m’Malemba?
4 Ndiyeno pali chikondi champhamvu cha pabanja, kapena chikondi chachibadwidwe, chozikidwa paunansi wam’banja, umene Agiriki anali nacho ndi liwu lakuti stor·geʹ. Ndicho chinabweretsa mwambi wakuti, “Wako Ndiwako.” Tiri nacho chitsanzo chabwino cha ichi m’chikondi chimene alongo otchedwa Mariya ndi Marita anali nacho pa mbale wawo Lazaro. Kuti iye anali wapamtima kwa iwo kungazindikiridwe ndi mmene analirira kwambiri pamene anafa mwadzidzidzi. Ndipo iwo anasangalala chotani nanga pamene Yesu anaukitsa wokondedwa wawo Lazaro kumoyo! (Yohane 11:1-44) Chikondi chimene mayi amakhala nacho kwa mwana wake nchitsanzo china cha chikondi cha mtundu uwu. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:7.) Chotero, kuti asonyeze mmene chikondi chake kaamba ka Ziyoni chinaliri chachikulu, Yehova anati chinalidi chachikulu kuposa chosonyezedwa ndi mayi kwa mwana wake.—Yesaya 49:15.
5. Kodi kusoŵeka kwa chikondi chachibadwidwe kukuwonekera motani lerolino?
5 Chisonyezero chimodzi chakuti tikukhala “m’masiku otsiriza” okhala ndi “nthaŵi [zake] zovuta kuchita nazo” ndicho kupanda “chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1, 3, NW) Chifukwa chakuti chikondi chapabanja chikusoŵeka, achichepere ena amathawa panyumba, ndipo ana achikulire ena amanyalanyaza makolo awo okalamba. (Yerekezerani ndi Miyambo 23:22.) Kusoŵeka kwa chikondi chachibadwidwe kumawonekeranso m’kuchuluka kwa kuchitira ana nkhanza—makolo ena amamenya ana awo moipa kwabasi kwakuti amafunikira kuperekedwa kuchipatala. Kusoŵeka kwa chikondi chaukholochi kumawonekeranso, m’kulephera kwa makolo ambiri kulanga ana awo. Kuwalola ana kuchita zinthu zomwe amakonda sindiko umboni wa chikondi koma kumatanthauza kutsatira njira za kukhala wolekerera. Bambo amene amakondadi ana ake adzawalanga kutakhala koyenera.—Miyambo 13:24; Ahebri 12:5-11.
6. Perekani zitsanzo za m’Malemba za chikondi chapakati pa mabwenzi.
6 Ndiyeno palinso liwu Lachigiriki lakuti phi·liʹa, kutanthauza chikondi (chosakhala ndi chikhumbo cha kugonana) chapakati pamabwenzi, monga ngati pakati pa amuna kapena akazi achikulire aŵiri. Tiri ndi chitsanzo chabwino chosonyezera ichi m’chikondi chimene Davide ndi Jonatani anali nacho. Pamene Jonatani anaphedwa kunkhondo, Davide anamulira nati: ‘Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Jonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu akazi.’ (2 Samueli 1:26) Timaphunziranso kuti Kristu anamkonda mwapadera mtumwi Yohane, amene anadziŵika kukhala wophunzira ‘amene Yesu anamkonda.’—Yohane 20:2.
7. Kodi a·gaʹpe njamtundu wanji, ndipo kodi chikondichi chasonyezedwa motani?
7 Kodi ndiliwu Lachigiriki liti limene Paulo anagwiritsira ntchito pa 1 Akorinto 13:13, pamene anatchula chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chikondi nati ‘chachikulu cha izi ndicho chikondi’? Panopa liwulo nlakuti a·gaʹpe, nlimodzimodzilo lomwe mtumwi Yohane anagwiritsira ntchito pamene anati: ‘Mulungu ndiye chikondi.’ (1 Yohane 4:8, 16) Ichi ndicho chikondi chotsogozedwa kapena kulamulidwa ndi lamulo lamakhalidwe abwino. Icho chingathe kapena sichingathe kuphatikizapo kukondana kwachibadwa kapena kozoloŵerana, koma icho ndicho maganizo kapena kulingalira kopanda dyera kodera nkhaŵa kuchitira ena zabwino mosasamala kanthu za maubwino a wochitiridwayo kapena mapindu aliwonse olandiridwa ndi wochisonyezayo. Chikondi cha mtundu uwu nchomwe chinachititsa Mulungu kupereka Mwana wake wobadwa yekha, wapamtima pake, Yesu Kristu, “kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Paulo akutikumbutsanso bwino motere: ‘Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino. Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera.’ (Aroma 5:7, 8) Inde, a·gaʹpe imachitira ena zabwino mosasamala kanthu za kaimidwe kawo m’moyo kapena zotaika zomwe zidzagwera wosonyeza chikondiyo.
Kodi Nchachikulu Bwanji Kuposa Chikhulupiriro ndi Chiyembekezo?
8. Kodi nchifukwa ninji a·gaʹpe ili yaikulu kuposa chikhulupiriro?
8 Koma kodi nchifukwa ninji Paulo anati chikondi cha mtundu uwu (a·gaʹpe) chinali chachikulu kuposa chikhulupiriro? Iye analemba motere pa 1 Akorinto 13:2: ‘Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziŵe zinsinsi zonse, ndinzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe chikondi, ndiri chabe.’ (Yerekezerani ndi Mateyu 17:20.) Inde, ngati kuyesayesa kwathu kwa kukundika chidziŵitso ndikukula m’chikhulupiriro kudati kuchitidwe ndi chifuno chadyera, kuteroku sikukatibweretsera phindu lochokera kwa Mulungu. Mofananamo, Yesu anasonyeza kuti ena ‘akanenera m’dzina lake, kutulutsa ziwanda m’dzina lake, ndikuchita ntchito zazikulu m’dzina lake’ koma sakawavomereza.—Mateyu 7:22, 23.
9. Kodi nchifukwa ninji chikondi chiri chachikulu kuposa chiyembekezo?
9 Kodi nchifukwa ninji chikondi cha mtundu wa a·gaʹpe chirinso chachikulu kuposa chiyembekezo? Chifukwa chakuti chiyembekezo chingathe kuzikidwa pawekha, munthu wodera nkhaŵa kwakukulukulu madalitso ogwera mwini yekhayo, pamene kuli kwakuti chikondi ‘sichitsata za mwini yekha.’ (1 Akorinto 13:4, 5) Kuwonjezera apa, chiyemebekezo—chonga chija chokhalapo ndi moyo kupyola ‘chisautso chachikulu’ ndikukalowa m’dziko latsopano—chimatha pamene choyembekezeredwacho chapezedwa. (Mateyu 24:21) Monga momwe Paulo akunenera motere: ‘Tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka sichiri chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya? Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.’ (Aroma 8:24, 25) Chikondi chokhacho chimapilira zinthu zonse, ndipo sichilephera. (1 Akorinto 13:7, 8) Chotero, chikondi chopanda dyera (a·gaʹpe) nchachikulu kuposa kaya chikhulupiriro kapena chiyembekezo.
Kodi Nchachikulu Kuposa Nzeru, Chiweruzo Chachilungamo, ndi Mphamvu?
10. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chikondi ndicho chachikulu pamikhalidwe inayi ya Mulungu?
10 Tsopano tiyeni tilingalire mikhalidwe inayi yaikulu iyi ya Yehova Mulungu: nzeru, chiweruzo chachilungamo, mphamvu, ndi chikondi. Kodi kunganenedwenso kuti chikondi nchachikulu kuiposa? Chingakhaledi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chikondi ndicho mphamvu yosonkhezera chimene Mulungu amachita. Ndicho chifukwa chake mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Mulungu ndiye chikondi.’ Inde, Yehova mwiniyo ndichikondi. (1 Yohane 4:8, 16) Palibe kulikonse m’Malemba kumene timaŵerenga kuti Mulungu ndiye nzeru, chiweruzo chachilungamo, kapena mphamvu. Mmalo mwake, tikuuzidwa kuti Yehova ali nayo mikhalidwe imeneyi. (Yobu 12:13; Salmo 147:5; Danieli 4:37) Mwa iye mikhalidwe inayiyi njolinganizika bwino. Posonkhezeredwa ndi chikondi, Yehova amakwaniritsa zifuno zake mwakugwiritsira ntchito mikhalidwe ina itatuyo kapena kuilingalira.
11. Kodi nchiyani chinasonkhezera Yehova kulenga thambo ndi zolengedwa zauzimu ndi zaumunthu?
11 Chotero, pamenepa, kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yehova kulenga thambo ndi zolengedwa zauzimu ndi zaumunthu zaluntha? Kodi inali nzeru kapena mphamvu? Ayi, popeza kuti Mulungu anangogwiritsira ntchito nzeru ndi mphamvu zake polenga. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti: “Yehova anakhazika dziko ndi nzeru.” (Miyambo 3:19) Kuwonjezera apa, mkhalidwe wake wa chiweruzo chachilungamo sindiwo unafunikiritsa kuti alenge zamoyo zodzisankhira zochita. Chikondi cha Mulungu ndicho chinamsonkhezera kuti agawane ndi ena chisangalalalo cha kukhala nalo kwake luntha. Chinali chikondi chimene chinapeza njira yochotsera kukanidwa kumene chiweruzo chachilungamo chinaika pa anthu chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu. (Yohane 3:16) Inde, ndipo nchikondi chimene chinasonkhezera Yehova kufuna kuti anthu omvera akakhale ndi moyo m’Paradaiso wapadziko lapansi akudzayo.—Luka 23:43.
12. Kodi tiyenera kuchita motani kulinga ku mphamvu, chiweruzo chachilungamo, ndi chikondi cha Mulungu?
12 Chifukwa cha mphamvuyonse ya Mulungu, sitifunikira kumchititsa nsanje. Paulo anafunsa kuti: ‘Kodi tichititsa nsanje Yehova? Kodi mphamvu zathu ziposa iye?’ (1 Akorinto 10:22) Ndithudi, Yehova ndi “Mulungu wansanje,” osati mlingaliro loipa, koma “m’kufuna kudzipereka kotheratu.” (Eksodo 20:5; King James Version) Monga Akristu, timazizwa ndi kusonyezedwa kwa nzeru zakuya za Mulungu. (Aroma 11:33-35) Ulemu wathu waukulu kaamba ka chiweruzo chachilungamo chake uyenera kutipangitsa kusachita tchimo lodzifunira. (Ahebri 10:26-31) Koma mosakaikira chikondi ndicho chachikulu pamikhalidwe inayi yaikulu ya Mulungu. Ndipo nchikondi chopanda dyera cha Yehova chimene chimatiyandikitsa kwa iye ndikutipangitsa kufuna kumkondweretsa, kumlambira, ndikukhalamo ndi phande m’kuyeretsedwa kwa dzina lake loyera.—Miyambo 27:11.
Chachikulu pa Zipatso za Mzimu
13. Kodi chikondi chiri pamalo ati pakati pa zipatso za mzimu wa Mulungu?
13 Kodi chikondi chiri pamalo ati pakati pa zipatso za mzimu wa Mulungu, zotchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23? Izi ndizo ‘chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.’ Pokhala ndi chifukwa chabwino, Paulo anandandalitsa chikondi kukhala choyamba. Kodi chikondi chiposa chimwemwe, mkhalidwe wachiŵiri umene anautchula? Inde, chimaterodi, pakuti sipangakhale chimwemwe chosatha popanda chikondi. Kwenikweni, dziko nlopanda chimwemwe kwambiri chifukwa cha dyera, lomwe liri kusoŵeka kwa chikondi. Koma Mboni za Yehova ziri nacho chikondi pakati pawo, ndipo ziri nacho chikondi kaamba ka Atate wawo wakumwamba. Chotero, tiyenera kuwayembekezera kukhala achimwemwe, ndipo kunanenedweratu kuti iwo “adzayimba ndi mtima wosangalala.”—Yesaya 65:14.
14. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chikondi nchachikulu kuposa chipatso cha mzimu cha mtendere?
14 Chikondi nchachikulunso kuposa chipatso cha mzimu cha mtendere. Chifukwa cha kusoŵeka kwa chikondi, dziko nlodzala ndi kukangana ndi ndewu. Koma anthu a Yehova ali pamtendere kwa wina ndi mnzake padziko lonse lapansi. Owona kwa iwo ndimawu a wamasalmo awa: ‘Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.’ (Salmo 29:11) Iwo ali nawo mtendere umenewu chifukwa chakuti ali nacho chozindikiritsa Akristu owona, kuchitchula, ndicho chikondi. (Yohane 13:35) Chikondi chokha chingalake anakatande onse achinyengo, kaya akhale aufuko, a mtundu, kapena mwambo. Ndicho ‘chomangira chamtima wamphumphu.’—Akolose 3:14.
15. Kodi malo apamwamba a chikondi akuwonekera motani poyerekezera ndi chipatso cha mzimu cha kuleza mtima?
15 Malo aakulu a chikondi amawonedwanso chitayerekezedwa ndi kuleza mtima, kupirira moleza mtima cholakwika chakutichakuti kapena kuputidwa. Kukhala woleza mtima kumatanthauza kuyembekezera modekha limodzinso ndikusakwiya msanga. Kodi nchiyani chimene chimapangitsa anthu kukhala osaleza mtima ndi kukwiya mofulumira? Kodi sikusoŵeka kwa chikondi? Komabe, Atate wathu wakumwamba ngwoleza mtima ndi “wosakwiya msanga.” (Eksodo 34:6, NW; Luka 18:7) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amatikonda ndipo ‘safuna kuti ena awonongeke.’—2 Petro 3:9.
16. Kodi chikondi chimayerekezedwa motani ndi chifundo, kukoma mtima, chifatso, ndi chiletso?
16 Tawona poyambapo chifukwa chimene chikondi chiriri chachikulu kuposa chikhulupiriro, ndipo zifukwa zoperekedwazo zimagwira ntchito ku zipatso za mzimu, ndiko kuti, chifundo, kukoma mtima, chifatso, ndi chiletso. Mikhalidwe yonseyi njofunikira, koma sidzatipindulitsa popanda chikondi, mongadi mmene Paulo anadziŵitsira pa 1 Akorinto 13:3, pomwe analemba motere: ‘Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndiribe chikondi, sindipindula kanthu ai.’ Kumbali ina, chikondi ndicho chimene chimabweretsa mikhalidwe yonga chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi kuleza mtima. Chotero, Paulo anapitirizabe kunena kuti chikondi nchachifundo ndikuti ‘chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.’ Inde, ndipo ‘chikondi sichilephera.’ (1 Akorinto 13:4, 7, 8) Tawona bwino lomwe kuti zipatso zina za mzimu ndizo zisonyezero, kapena mbali zosiyanasiyana za chikondi, chomwe chatchulidwa poyambacho. Zowonadi, nkwanzeru kunena kuti pazipatso zonse zisanu ndi zinayi za mzimu, chikondi nchachikuludi.
17. Kodi ndi ndemanga za m’Malemba ziti zimene zimachilikiza mawu akuti chikondi nchipatso chachikulu cha mzimu?
17 Ochilikiza mawu akuti chikondi nchachikulu pa zipatso za mzimu wa Mulungu ndi mawu awa a Paulo: ‘Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo. Pakuti . . . lamulo lina lirilonse, limangika pamodzi m’mawu amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha. Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chiri chokwanitsa lamulo.’ (Aroma 13:8-10) Molunjika kwenikweni, wophunzira Yakobo akusonya ku lamulo limeneli la kukonda mnzako monga udzikonda wekha kukhala ‘lamulo lachifumu.’—Yakobo 2:8.
18. Kodi pali umboni wowonjezereka wotani womwe ulipo wakuti chikondi ndicho mkhalidwe waukulu?
18 Kodi udakalipobe umboni wowonjezereka kuti chikondi ndicho mkhalidwe waukulu? Indedi. Lingalirani chimene chinachitika pamene mlembi anafunsa Yesu kuti: “Lamulo la m’tsogolo la onse ndi liti?” Iye ayenera kukhala anayembekezera bwino lomwe kuti Yesu akagwira mawu a Malamulo Khumi. Koma Yesu anagwira mawu a Deuteronomo 6:4, 5 naati: ‘Mvera, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi; ndipo uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.’ Kenaka Yesu anawonjezera kuti: ‘Lachiŵiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.’—Marko 12:28-31.
19. Kodi ndizipatso zina zapadera ziti za a·gaʹpe?
19 Zowonadi, Paulo sanakuze mawu ndi mkamwa pamene anatchula chikhulupiriro, chiyembekezo, ndi chikondi naati: ‘Chachikulu cha izi ndicho chikondi.’ Kusonyezedwa kwachikondi kumatulukapo unansi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba ndi ena, kuphatikizapo okhala mumpingo ndi ziŵalo za mabanja athu. Chikondi chiri ndi chiyambukiro chomangirira pa ife. Ndipo nkhani yotsatira idzasonyeza mmenedi chikondi chenicheni chimafupira.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi chikondi nchachikulu motani kuposa chikhulupiriro ndi chiyembekezo?
◻ Kodi a·gaʹpe nchiyani, ndipo kodi chikondichi chimasonyezedwa motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji chikondi chiri chachikulu pa mikhalidwe inayi ya Mulungu?
◻ Kodi ndim’njira zotani mmene chikondi chiri chachikulu kuposa zipatso zina za mzimu?
[Chithunzi patsamba 13]
Chikondi chinasonkhezera Mulungu kulenga anthu kaamba ka moyo m’paradaiso wa padziko lapansi. Kodi mumayembekezera kukhalamo?