MUTU 14
“Madalitso Oti Mudzasowa Powalandirira”
1, 2. (a) Kodi aliyense wa ife angasankhe kuchita chiyani kuti zinthu zimuyendere bwino? (b) Kodi tingapeze madalitso chifukwa cha kukwaniritsidwa kwa ulosi uti?
TIKUKHALA ndi moyo pa nthawi imene anthu akuweruzidwa komanso kudalitsidwa. Masiku ano zipembedzo zikuchita zinthu zoipa zambiri, komabe atumiki enieni a Mulungu akumulambira m’njira yovomerezeka. N’zachidziwikire kuti inuyo mungakonde kukhala m’gulu la anthu amene akulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Anthu amenewa akulandira madalitso panopa komanso akuyembekezera madalitso ena m’tsogolo. Koma kodi mungatani kuti mupeze madalitso amenewa? Yankho la funso limeneli likupezeka mu ulosi umene unakwaniritsidwa kwambiri “masiku otsiriza” atangoyamba kumene mu 1914. (2 Timoteyo 3:1) Malaki analosera kuti: “‘Ambuye woona [Yehova], amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi Wake. Adzabwera ndi mthenga wa pangano amene mukumuyembekezera mosangalala. Iye adzabwera ndithu,’ watero Yehova wa makamu.”—Malaki 3:1.
2 Ulosi umenewu, womwe ndi wofunika kwambiri pa moyo wanu, ukupezeka m’buku lomalizira pa mabuku amene aneneri 12 analemba. Buku limeneli analemba ndi Malaki ndipo zomwe analembazo n’zofunika kuziganizira pamene tikukambirana mutu womaliza uno. Buku la Malaki lili ndi malangizo ofunika amene angakuthandizeni inuyo komanso atumiki ena a Yehova kuti mudzapeze “madalitso oti mudzasowa powalandirira.” (Malaki 3:10) Tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane chaputala 3 cha buku la Malaki.
NTHAWI YOYERETSEDWA MWAUZIMU
3. Kodi anthu a Mulungu anachita chiyani chomwe chinachititsa kuti “Isiraeli wa Mulungu” asankhidwe?
3 Patapita zaka pafupifupi 500 kuchokera nthawi ya Malaki, Yehova, kudzera mwa Khristu (yemwe ndi “mthenga [wa Mulungu] wa pangano” la Abulahamu) anabwera kukachisi wa ku Yerusalemu kudzaweruza anthu ake amene anali naye m’pangano. Zinthu zimene mtundu umenewu unkachita zinachititsa kuti Yehova asapitirize kuukonda, moti anaukana. (Mateyu 23:37, 38) Umboni wa zimenezi ndi zomwe zinachitika mu 70 C.E. Kenako Mulungu anasankha “Isiraeli wa Mulungu,” womwe ndi mtundu wa Akhristu odzozedwa okwana 144,000 ochokera m’mitundu yonse. (Agalatiya 6:16; Aroma 3:25, 26) Koma zimenezi sizikusonyeza kuti kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Malaki kunathera pompa. Mbali ina ya ulosiwu ikukwaniritsidwanso masiku ano komanso ikukhudza madalitso amene inuyo mungayembekezere kudzapeza “oti mudzasowa powalandirira.”
4. Kodi ndi funso liti limene linafunika kuyankhidwa Yesu atakhala mfumu m’chaka cha 1914?
4 Kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kumatsimikizira kuti Yesu Khristu anakhazikitsidwa monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Yehova mu 1914. Kenako inakwana nthawi yoti Yesu asankhe gulu la Akhristu omwe Mulungu ankakondwera nawo. Koma kodi ndani amene akanapezeka kuti akuyesetsa pa nkhani yokhala oyera mwauzimu? Tingapeze yankho la funso limeneli m’mawu amene Malaki ananena. Iye anati: “Ndani adzapirire pa tsiku limene adzabwere? Ndipo ndani adzaime chilili iye akadzaonekera? Iye adzakhala ngati moto wa woyenga zitsulo komanso ngati sopo wa ochapa zovala.” (Malaki 3:2) Kodi Yehova anabwera liti “kukachisi” wake kudzaweruza anthu, nanga anabwera motani?
5, 6. (a) Pamene Yehova anabwera kudzayendera kachisi wake, kodi anapeza chiyani pakati pa anthu amene ankati ndi olambira ake? (b) Kodi atumiki a Mulungu odzozedwa ndi mzimu woyera ankafunikira chiyani?
5 Kachisi womaliza wolambiriramo Mulungu woona anawonongedwa mu 70 C.E. Choncho n’zodziwikiratu kuti Mulungu sanabwere kukachisi weniweni womangidwa ndi miyala ndi matope. M’malomwake, Yehova anabwera kukachisi wauzimu, yemwe ndi njira imene imathandiza kuti anthu azilankhula ndi Mulungu komanso kumulambira. Zimenezi zimatheka chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Aheberi 9:2-10, 23-28) Kachisi wauzimu ameneyu sakuimira matchalitchi amene amati ndi achikhristu chifukwa matchalitchiwa ali m’gulu la zipembedzo zomwe zili ndi mlandu wokhetsa magazi komanso wolowerera ndale. Zipembedzozi zimaphunzitsa anthu zinthu zabodza m’malo mowalimbikitsa kulambira Mulungu woona. Ichi n’chifukwa chake Yehova ‘sanazengereze kupereka umboni wotsutsa’ zipembedzo zimenezi ndipo n’zachidziwikire kuti chiweruzo chake chinali cholungama. (Malaki 3:5) Komabe Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa, panali gulu la Akhristu oona amene ankatumikira m’bwalo la kachisi wauzimu wa Mulungu. Ndipo pa nthawi ya mayesero aakulu, Akhristu amenewa anasonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Mulungu. Komabe Akhristu odzozedwawa, nawonso ankafunikira kuyeretsedwa. Ndipo zimene aneneri 12 aja analemba zimasonyeza kuti zimenezi zinachitikadi. M’mabuku awo muli malonjezo osangalatsa osonyeza kuti zinthu zidzayambiranso kuyenda bwino mwauzimu komanso mwakuthupi pakati pa atumiki a Mulungu. Malaki analosera kuti padzakhala anthu amene Yehova “adzawayeretsa ngati golide ndi siliva.” Anthu amenewa “azidzapereka nsembe zawo ngati mphatso [ndipo] Yehova adzaona kuti nsembe zawozo akuzipereka molungama.”—Malaki 3:3.
6 Umboni wodalirika umene ulipo ukusonyeza kuti kungoyambira mu 1918, Yehova anagwira ntchito yoyeretsa Akhristu odzozedwa. Iye anayenga kulambira kwawo, zochita zawo komanso ziphunzitso zawo.a Odzozedwawa pamodzi ndi “khamu lalikulu” limene linagwirizana nawo pambuyo pake, apindula kwambiri ndi kuyengaku. (Chivumbulutso 7:9) Iwo apanga gulu limodzi logwirizana ndipo akupitiriza ‘kupereka nsembe zawo ngati mphatso ndipo akuzipereka molungama.’ Apa n’zoonekeratu kuti nsembe zimenezi ‘zikusangalatsa Yehova.’—Malaki 3:3, 4.
7. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati amene angatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu?
7 Izi n’zimene zinachitikira gulu lonse la anthu a Mulungu. Koma kodi zingachitikenso kwa ifeyo aliyense payekhapayekha? Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndi zinthu ziti zokhudza makhalidwe anga komanso zochita zanga zimene ndikufunika kusintha? Kodi makhalidwe anga akufunika kuyengedwa ngati mmene Yehova anayengera Akhristu odzozedwa?’ Taona kale kuti aneneri 12 aja anafotokoza maganizo ndiponso makhalidwe olakwika amene anthu anali nawo, komanso anatchula zinthu zabwino zimene anthu ena ankachita. Zomwe anafotokozazi zingakuthandizeni kudziwa zimene ‘Yehova akufuna kwa inu.’ (Mika 6:8) Lembali likusonyeza kuti aliyense payekha ayenera kudzifufuza kuti adziwe ngati akufunikirabe kuyengedwa kapena kuti kuyeretsedwa.
“NDIYESENI CHONDE”
8. Kodi Yehova akupempha anthu ake kuti achite chiyani?
8 Ganizirani mawu enanso amene Yehova ananena kudzera mwa Malaki. Pa Malaki 3:10 Yehova akutipempha mokoma mtima kuti: “‘Bweretsani gawo limodzi mwa magawo 10 alionse a zinthu zanu n’kuziika mosungiramo zinthu zanga, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya. Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira,’ watero Yehova wa makamu.” Apa Yehova akupempha anthu ake onse monga gulu. Koma kodi inuyo panokha mukuonanso kuti mukufunika kuchita zimene Yehova akupempha palembali?
9. Kodi mungapereke nsembe komanso chakhumi chotani kwa Yehova?
9 Kodi mungapereke bwanji kwa Yehova “gawo limodzi mwa magawo 10”? Tikudziwa kuti sitikuyenera kupereka nsembe za nyama ndi mbewu komanso chakhumi zotchulidwa m’Chilamulo. Nsembe zomwe Yehova akufuna masiku ano ndi zosiyana ndi nsembe zimenezi. Malinga ndi zimene tinakambirana m’Mutu 13, Paulo ananena kuti tikamagwira ntchito yolalikira ndiye kuti tikupereka nsembe. (Hoseya 14:2) Kenako mtumwiyu anatchulanso nsembe yamtundu wina pamene anati: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheberi 13:15, 16) Izi zikusonyeza kuti mawu akuti “gawo limodzi mwa magawo 10” otchulidwa pa Malaki 3:10 akutanthauza ntchito zauzimu zimene timagwira komanso mphatso zosiyanasiyana zimene timapereka kwa ena. Ngati ndinu Mkhristu wobatizidwa, ndiye kuti munadzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova. Koma chakhumi chimene mumapereka chikuimira gawo la zinthu zanu zomwe mungathe kupereka kwa Yehova kapena kuzigwiritsa ntchito pomutumikira. Zinthu zimenezi ndi monga nthawi yanu, mphamvu zanu, chuma chanu komanso zinthu zina zomwe mungapereke kuti zigwiritsidwe ntchito potumikira Yehova.
10. Kodi ‘mungamuyese’ bwanji Yehova moyenerera?
10 Tikuyeneradi kupereka chakhumi chophiphiritsa chimenechi kwa Yehova chifukwa chakuti tinadzipereka kwa iye ndipo timamukonda. Tikuyenera kuchita zimenezi mwamsanga chifukwa tikudziwa kuti tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi kwambiri komanso kuti ndi “lochititsa mantha.” (Yoweli 2:1, 2, 11) Moyo wa anthu uli pa ngozi, choncho inuyo panokha mungachite zimene Yehova Mulungu akukupemphani. Iye akukupemphani kuti ‘mumuyese.’ N’zoona kuti anthu sayenera kuyesa Yehova ngati mmene amayesera munthu wosadalirika. (Aheberi 3:8-10) Koma modzichepetsa mungamuyese m’njira yoyenera. Kodi mungamuyese motani? Pamene akutipempha kuti timuyese iye akutilonjeza madalitso, choncho mukamamumvera mumakhala mukumuyesa. Zimakhala ngati mukufunsa kuti, ‘Kodi andidalitsadi?’ Mukachita zimenezi, iye amaonetsetsa kuti wakudalitsani mogwirizana ndi lonjezo lake. Choncho, mwayi umene Mulungu wakupatsani woti ‘mumuyese’ umakuthandizani kuti mukhale wotsimikiza ndi mtima wonse kuti adzakupatsani madalitso ochuluka.
11, 12. Kodi inuyo panokha mwaona umboni wotani wosonyeza kuti Yehova akudalitsa anthu ake?
11 Inu mukudziwa kuti anthu a Yehova apereka nsembe zosiyanasiyana mowolowa manja. Ndipo Yehova wawapatsa ‘madalitso oti akusowa powalandirira.’ Mwina mwaona madalitso amene Mulungu wapereka kwa anthu ake, monga kuwonjezeka kwa Mboni za Yehova kungoyambira kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Komanso mwaona kuti panopa tikudziwa “zinthu zozama za Mulungu” zochuluka kwambiri kuposa kale. (1 Akorinto 2:10; Miyambo 4:18) Koma tsopano ganizirani madalitso amene inuyo panokha mwapeza.
12 Pa nthawi ina mwina munali m’chipembedzo china kapena munali mutangoyamba kumene kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Kodi pa nthawi imeneyo munkadziwa mfundo za choonadi cha m’Baibulo zochuluka bwanji? Tsopano yerekezerani ndi zimene mukudziwa panopa zomwe mukhoza kufotokoza umboni wake kuchokera m’Baibulo. Kapena ganizirani zinthu zozama zimene mwaphunzira, kuphatikizapo maulosi amene akukwaniritsidwa masiku ano. Ganiziraninso mmene mukugwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wanu. N’zodziwikiratu kuti panopa mukudziwa zinthu zambiri komanso mukutsatira mfundo za m’Malemba kuposa kale. Choncho inunso munganene zimene mtumwi Petulo ananena kuti: “Mawu aulosiwa ndi odalirika kwambiri.” (2 Petulo 1:19) Mfundo yaikulu ndi yakuti: Inuyo panokha ‘mwaphunzitsidwa ndi Yehova’ ndipo muli m’gulu la Akhristu enieni amene akufuna kutumikira Yehova kwamuyaya. (Yesaya 54:13) Choncho munganene mosapita m’mbali kuti Yehova wakudalitsani kwambiri.
DZINA LANU LINGALEMBEDWE M’BUKU LA MOYO
13. Kodi zingatheke bwanji kuti dzina la munthu lilembedwe m’buku lachikumbutso la Mulungu?
13 Madalitso ena amene Yehova amapereka akutchulidwa pa Malaki 3:16, kuti: “Pa nthawi imeneyo anthu oopa Yehova analankhulana, aliyense ndi mnzake, ndipo Yehova anatchera khutu ndi kumvetsera. Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizira za dzina lake.” Akhristu odzozedwa komanso a khamu lalikulu amasonyeza kuti ‘amaopa Yehova.’ N’zachidziwikire kuti mumaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala m’gulu la Mboni za Yehova. Gulu limeneli lili ndi anthu osangalala amene amaganizira za dzina la Yehova ndipo akulilengeza padziko lonse lapansi. Muyenera kukhala osangalala kwambiri chifukwa Yehova akukutsimikizirani kuti sangaiwale kukhulupirika kwanu.—Aheberi 6:10.
14. Kodi mabuku a aneneri 12 akuthandizani bwanji kudziwa makhalidwe amene Yehova amadana nawo?
14 Koma kodi inuyo panokha mungatani kuti dzina lanu lilembedwe ‘m’buku la chikumbutso,’ lomwe panopa linayamba kale kulembedwa pamaso pa Yehova? Kumbukirani ena mwa malangizo anzeru amene akupezeka m’mabuku amene aneneri 12 aja analemba. M’mitu ya m’mbuyomu taphunzira za makhalidwe ndiponso maganizo amene Yehova amadana nawo. Mwachitsanzo, aneneriwa anatichenjeza za makhalidwe omwe Mulungu amanena kuti amatsutsana ndi mfundo zake zolungama ndiponso amene angawononge moyo wathu, monga “khalidwe lotayirira” komanso “mtima wadama.” (Hoseya 4:12; 6:9) Mulungu sasangalala anthu akamachita zachinyengo kwa amuna awo, akazi awo kapena anthu ena a m’banja lawo. (Malaki 2:15, 16) Yehova anauzira aneneriwa kuti alembe zoti iye sasangalala ndi zinthu zilizonse zachiwawa. (Amosi 3:10) Iye anawauziranso kuti alembe zoti anthu ayenera kupewa kuchita zinthu mopanda chilungamo komanso mwachinyengo pa nkhani zamalonda komanso zandalama. (Amosi 5:24; Malaki 3:5) Mabuku amene aneneri 12 amenewa analemba amatsindikanso kufunika koti amuna audindo asamaweruze mokondera.—Mika 7:3, 4.
15. Kodi mungapeze madalitso otani mukamatsatira malangizo opezeka m’mabuku a aneneri 12?
15 Komatu aneneriwa sanangotiuza zinthu zimene tiyenera kupewa. Iwo anatiuzanso madalitso amene tingapeze tikamatsatira mfundo za Mulungu. Mwachitsanzo, iwo anasonyeza kuti Yehova adzakhala bwenzi lathu lapamtima. (Mika 4:5) Tikamachita zinthu mwachilungamo, mpingo wathu udzakhala wolimba komanso wakhama pa ntchito yolalikira. Banja lathu lidzakhala lolimba, logwirizana komanso lokonda zinthu zauzimu. (Hoseya 2:19; 11:4) Tikamachita zinthu mwachilungamo komanso moona mtima, anthu ena adzatilemekeza. Potengera chitsanzo cha Yehova, tidzakhala achifundo ndi okoma mtima ndipo zimenezi zidzachititsanso kuti abale ndi alongo athu azitisonyeza chifundo ndi kutikomera mtima. (Mika 7:18, 19) Makhalidwe amenewa adzachititsa kuti tizikondedwa ndi abale ndi alongo athu omwe amakonda zinthu zauzimu, choonadi ndi mtendere. Ndipo koposa zonsezi, tidzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Zekariya 8:16, 19) Mosakayikira amenewa ndi ena mwa madalitso amene mwapeza kale m’gulu la Yehova.
16. Kodi masiku ano atumiki a Mulungu akusiyana bwanji ndi anthu ena, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti chidzachitike n’chiyani pa tsiku limene Yehova adzapereke chiweruzo?
16 Zimene takambiranazi zikuchititsa kuti “kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa,” kapena kuti pakati pa Akhristu oona ndi Akhristu onyenga, kuonekere kwambiri. (Malaki 3:18) Pamene ifeyo tikuyesetsa kutsatira mfundo za Yehova, anthu ena onse m’dzikoli akulowerera kwambiri m’makhalidwe amene Mulungu amadana nawo. Ndipotu kusiyana kumeneku kudzakhala ndi zotsatira zoopsa kwambiri “tsiku lalikulu la Yehova” likadzafika.—Zefaniya 1:14; Mateyu 25:46.
17. Kodi m’tsogolo mungadzagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene zili m’buku lino?
17 Choncho, n’zodziwikiratu kuti malangizo amene aneneri 12 amenewa alemba ndi ofunikabe mpaka pano. Mukakumana ndi mavuto osiyanasiyana kapena mukamafuna kusankha zochita pa nkhani inayake, ndi bwino kuwerenganso malangizo othandiza amene ali m’bukuli. Mukamachita zimenezi mudzasonyeza kuti mukufunitsitsa kuphunzitsidwa njira za Yehova ndiponso ‘kuyenda m’njira zakezo.’ (Mika 4:2) Komatu cholinga chathu poyenda m’njira zimenezi si kungopeza madalitso a pano pokha. Cholinga chathu chachikulu n’choti dzina lathu lilembedwe kwamuyaya m’buku la chikumbutso la Yehova. Choncho mabuku amene aneneri 12 analemba angakuthandizeni kuti zimenezi zitheke.
CHIKHULUPIRIRO N’CHOFUNIKA KUTI TIDZAPULUMUKE
18. Kodi lemba la Yoweli 2:32 limasonyeza kuti tikufunika kuchita chiyani kuti tidzapulumuke, nanga mtumwi Paulo anatchula chinthu chinanso chiti chofunikira?
18 Potsindika mfundo yaikulu imene ingathandize kuti Mulungu azitikonda mpaka kalekale, Yoweli anati: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32) Mfundo yofunika kwambiri imeneyi inabwerezedwanso ndi mtumwi Petulo komanso mtumwi Paulo. (Machitidwe 2:21; Aroma 10:13) Paulo anatchula chinthu chinanso chofunika kwambiri pa nkhaniyi pamene anafunsa kuti: “Kodi angaitane bwanji munthu amene samukhulupirira?” (Aroma 10:14) Sitikukayikira kuti inuyo mukufuna kuitana pa dzina la Yehova ndiponso kumukhulupirira mpaka kalekale.
19. Kodi munthu angaitane bwanji pa dzina la Yehova?
19 Kuitana pa dzina la Yehova kumafuna zambiri, osati kungodziwa ndiponso kugwiritsira ntchito dzina lenileni la Mulungu. (Yesaya 1:15) Yoweli asananene mawu opezeka pa Yoweli 2:32, anali atafotokoza kufunika kolapa mochokera pansi pa mtima ndi kukhulupirira kuti Yehova angatikhululukire. (Yoweli 2:12, 13) Kuitana pa dzina la Mulungu kumaphatikizapo kumudziwa bwino, kumukhulupirira, kumumvera ndiponso kumuona kuti ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu. Choncho, kutumikira Yehova kuyenera kukhala chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu. Zimenezi zidzatithandiza kuti tidzapeze moyo wosangalatsa komanso wosatha, amene ndi madalitso ochokera kwa Mulungu.—Mateyu 6:33.
20. Kodi mukamasonyeza chikhulupiriro mudzapeza madalitso otani?
20 Kudzera mwa Habakuku, Yehova anati: “Wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Habakuku 2:4) Muzikumbukira mfundo imeneyi nthawi zonse chifukwa ndi imodzi mwa mfundo za choonadi zofunika kwambiri. Paulo anatchula mfundo imeneyi katatu m’mabuku ake.b (Aroma 1:16, 17; Agalatiya 3:11, 14; Aheberi 10:38) Mfundoyi ikusonyeza kuti inuyo mukuyenera kukhulupirira nsembe imene Yesu Khristu anapereka chifukwa cha machimo athu. Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye . . . akhale ndi moyo wosatha.” Kenako Yesu anawonjezera kuti: “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16, 36) Nsembe imeneyi inachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu achiritsidwe mwauzimu. Choncho Yesu yekha, yemwe ndi Wotiwombola, ndi amene akanatha kuchiritsa anthu mwauzimu. Malaki atalemba zimene Yehova ananena zokhudza zimene adzachitire dziko la Satanali pa tsiku lake lalikulu, anapitiriza ndi mawu akuti: “Inu amene mukuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani ndipo m’mapiko mwake mudzakhala mphamvu yochiritsa.” Zoonadi, Yesu adzawala ndi mphamvu zochiritsa. Zimenezi zikuphatikizapo kuchiritsa mwauzimu kumene kukuchitika panopa. Komatu n’zosangalatsa kwambiri kuti m’dziko latsopano anthu adzachiritsidwanso mwakuthupi.—Malaki 4:2.
21. N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa cholinga chake?
21 M’pofunikanso kuti tizikhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake. Nthawi ya Mika, zinali zovuta kuti munthu akhulupirire munthu mnzake. Mneneriyu anati: “Musamakhulupirire anzanu. Musamadalire mnzanu wapamtima.” Ngakhale zinali choncho, Mika sizinkamuvuta kukhulupirira Yehova ndipo nanunso muyenera kumukhulupirira. Iye anati: “Koma ine ndidzadikirira Yehova.” (Mika 7:5, 7) Mosiyana ndi anthu omwe ndi osadalirika, Yehova akufunitsitsa kukwaniritsa cholinga chake komanso ali ndi mphamvu zochitira zimenezi. Iye adzakwaniritsadi cholingachi pofuna kutsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse komanso kuti anthu okhulupirika adzapeze moyo wosatha.
22. Kodi amene akuitana pa dzina la Yehova angapeze madalitso otani?
22 Molimba mtima nanunso munganene mawu amene Habakuku ananena, akuti: “Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.” (Habakuku 3:18) Mneneri Yoweli anafotokoza momveka bwino chimene chimachititsa kuti anthu omwe amaitana pa dzina la Yehova akhale osangalala. Iye ananena kuti anthu amenewa “adzapulumuka,” ndipo nayenso mtumwi Paulo anatchula mfundo imeneyi. (Yoweli 2:32; Aroma 10:13) Kodi mawu akuti “adzapulumuka” akutanthauza chiyani? Chikhulupiriro chanu chinakupulumutsani kale ku misampha ya Satana ndiponso ku zinthu zambiri zopweteka zimene anthu oipa amakumana nazo. (1 Petulo 1:18) Kuwonjezera pa zimenezi, muli ndi chikhulupiriro chonse kuti mudzapulumuka dziko loipali likamadzawonongedwa. Zimenezi zidzakupatsani mwayi wosangalala ndi madalitso ochuluka amene aneneri 12 aja analosera.
MMENE ZINTHU ZIDZAKHALIRE M’PARADAISO
23, 24. (a) Kodi aneneri 12 anafotokoza motani mmene zinthu zidzakhalire m’Paradaiso? (b) Kodi zimene aneneri 12 amenewa analemba zalimbitsa bwanji chikhulupiriro chanu?
23 “Anthu oopa Yehova” akuyembekezera madalitso osatha. (Malaki 3:16) Ena mwa aneneri 12 aja anafotokoza mmene zinthu zidzakhalire m’Paradaiso ndipo zomwe anafotokozazo zingakupatseni chimwemwe komanso chiyembekezo. Mwachitsanzo, Mika analemba kuti: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.” (Mika 4:4) Izi zikutitsimikizira kuti mu Ufumu wa Mulungu tidzakhala otetezeka ndiponso tidzasangalala ndi ntchito imene tagwira.
24 Pa nthawi imeneyo, mavuto monga matenda, chisoni komanso imfa, adzatha. Ndipotu sikuti tikungowerengera madzi amphutsi tikamayembekezera zimenezi. Taganizirani mmene adzasangalalire anthu amene adzaukitsidwe n’kumayembekezera kukhala angwiro. Iwo adzasangalala ndi kukwaniritsidwa kwakukulu kwa zimene lemba la Hoseya 13:14 limanena. Lembali limati: “Ine ndidzawawombola ku Manda ndiponso ku imfa. Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti? Iwe Manda amene umawononga, kodi uli kuti?” Paulo anagwiritsa ntchito lembali ponena za kuuka kwa anthu amene adzapite kumwamba.—1 Akorinto 15:55-57.
25. Kodi mudzamva bwanji m’dziko latsopano?
25 Tisakayikire zoti anthu ena adzaukitsidwa kuti adzakhale ndi moyo padziko lapansi. (Zekariya 8:6) Pamene Amosi ndi Mika ankalosera zoti anthu a Mulungu adzabwerera kudziko lawo kuchoka ku ukapolo, mwina anthu ankaona ngati n’zosatheka. Komatu zimene aneneriwa analosera zinachitikadi. (Amosi 9:14, 15; Mika 2:12; 4:1-7) Anthu amene anabwererawo ananena kuti: “Tinakhala ngati tikulota. Pa nthawiyo tinaseka kwambiri, ndipo lilime lathu linatulutsa mawu okondwa. . . . Yehova watichitira zazikulu. Tasangalala.” (Salimo 126:1-3) Umu ndi momwe nanunso mudzamvere m’dziko latsopano Yehova atakupatsani “madalitso oti mudzasowa powalandirira.”
Atumiki a Yehova ndi anthu okonda choonadi komanso chilungamo
26. Kodi amene amakumbukira tsiku la Yehova nthawi zonse akuyembekezera chiyani?
26 Anthu onse oipa adzachotsedwa padziko lapansi pa “tsiku la Yehova,” kenako “ufumu udzakhala wa Yehova.” (Obadiya 15, 21) Amenewatu adzakhala madalitso aakulu kwa anthu ake onse okhala padziko lapansi. Inunso mungakhale m’gulu la anthu amene akutchulidwa m’chaputala 3 cha buku la Malaki. Mneneri Malaki ananena kuti: “‘Iwo adzakhala anthu anga,’ . . . watero Yehova wa makamu. ‘Ndidzawachitira chifundo monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.’” (Malaki 3:17) Izi zikusonyeza kuti pa nthawi imeneyo, chikhulupiriro chimene muli nacho chidzakuthandizani kupeza “madalitso oti mudzasowa powalandirira.” Chikhulupiriro chimenechi n’chomwenso panopa chikukuthandizani kukhala ndi chiyembekezo choti mudzapulumuka. Ndithudi tikuyembekezera madalitso amtengo wapatali zedi.
a Kuti mumve zambiri onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya June 15, 1987, tsamba 14 mpaka 20.
b Polemba zimenezi, Paulo anatsatira mawu a m’Baibulo lachigiriki la Septuagint, omwe ndi osiyana pang’ono ndi mawu a m’mipukutu yachiheberi.