Kondwerani ndi Chilungamo cha Yehova
“Wolondola chilungamo ndi chifundo apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.”—MIYAMBO 21:21.
1. Ndi njira za anthu ziti masiku ano zimene zayambitsa mavuto?
“IRIPO njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miyambo 16:25) Mwambi wa m’Baibulo umenewu ukufotokoza molondola njira za anthu ambiri masiku ano. Nthaŵi zambiri, anthu amangochita zimene akuona kuti n’zoyenera kwa iwo basi, osaganizira zimene anzawo akufunikira kwambiri. (Miyambo 21:2) Iwo amati amalemekeza malamulo ndi miyezo ya m’dziko limene akukhala, chikhalirecho amayesetsa kupeza njira zopeŵera lamulo mwaukathyali akangopeza mpata. Chifukwa cha zimenezi, anthu ndi ogaŵanika ndiponso osokonezeka maganizo.—2 Timoteo 3:1-5.
2. Kodi n’chiyani chikufunika kwambiri kuti zinthu ziwayendere bwino anthu?
2 Kuti zinthu zitiyendere bwino, ndiponso kuti anthu onse akhale pamtendere ndi kukhala otetezeka, tikufunikira kwambiri titakhala ndi lamulo kapena muyezo wolungama, womwe anthu onse angauvomereze ndi kuumvera. N’zachidziŵikire kuti palibe lamulo kapena muyezo wopangidwa ndi munthu umene ungakwaniritse zimenezo ngakhale munthuyo atakhala wanzeru kapena woona mtima bwanji. (Yeremiya 10:23; Aroma 3:10, 23) Ngati muyezo woterowo ulipo, kodi tingaupeze kuti ndipo ndi wotani? Mwina funso lofunika kwambiri n’lakuti, Ngati muyezowo ulipo, kodi mungakondwere nawo ndi kuumvera?
Kupeza Muyezo Wolungama
3. Kodi ndani amene ali woyenerera kupereka muyezo umene anthu onse angauvomereze ndi kupindula nawo, ndipo chifukwa chiyani?
3 Kuti tipeze muyezo umene anthu onse angauvomereze ndi kupindula nawo, tifunika kupita kwa munthu amene sakhudzidwa ndi kusiyana kwa mafuko, chikhalidwe, ndiponso zandale, ndipo amatha kudziŵa zam’tsogolo komanso alibe zofooka. N’zosachita kufunsa kuti amene angayenerere zimenezo ndi m’modzi yekha, Mlengi Wamphamvuyonse, Yehova Mulungu, amene ananena kuti: “Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.” (Yesaya 55:9) Ndiponso, Baibulo limanena kuti Yehova ndiye “Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) M’Baibulo lonse timapezamo mawu akuti “Yehova ndiye wolungama.” (Eksodo 9:27; 2 Mbiri 12:6; Salmo 11:7; 129:4; Maliro 1:18; Chivumbulutso 19:2) Inde, muyezo woposa wina uliwonse tingaupeze kwa Yehova chifukwa chakuti iye ndi wokhulupirika ndiponso wolungama.
4. Kodi “chilungamo” chimatanthauza chiyani?
4 Komabe, liwu lakuti “chilungamo” anthu ambiri salikonda masiku ano. Ndipotu, ambiri amaipidwa nalo ngakhalenso kulinyoza liwuli chifukwa amaligwirizanitsa ndi munthu wodzionetsera ngati wabwino kuposa ena kapena wopembedza kwambiri. Komabe, buku lina lotanthauzira mawu limati “chilungamo” chimatanthauza “kulungama, makhalidwe abwino; kupanda mlandu, kupanda tchimo; kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu kapena miyezo yovomerezeka ya makhalidwe abwino; kuchita zinthu mwachilungamo.” Kodi inu simungakonde lamulo kapena muyezo umene uli ndi mbali zabwino ngati zimenezi?
5. Fotokozani khalidwe la chilungamo malinga ndi mmene alisonyezera m’Baibulo.
5 Pofotokoza za chilungamo, buku lakuti Encyclopaedia Judaica, linati: “Chilungamo sindicho maganizo chabe, koma ndicho kuchita zolungama pochita zinthu ndi anthu ena alionse.” Mwachitsanzo, chilungamo cha Mulungu sichili chabe khalidwe la m’kati kapena laumwini limene ali nalo, monga mmene zilili ndi chiyero chake. M’malo mwake, ndicho kusonyeza khalidwe lake m’njira zolungama. Tinganene kuti popeza Yehova ndi woyera, zonse zimene amachita ndiponso zonse zimene zimachokera kwa iye n’zolungama. Monga mmene Baibulo limanenera, “Yehova ali wolungama m’njira zake zonse, ndi wachifundo m’ntchito zake zonse.”—Salmo 145:17.
6. Kodi Paulo ananenanji za Ayuda ena osakhulupirira a m’nthaŵi yake, ndipo chifukwa chiyani?
6 Mtumwi Paulo anatsindika mfundo imeneyi m’kalata yake yolembera Akristu a ku Roma. Analemba za Ayuda ena osakhulupirira kuti: “Pakuti pakusadziŵa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja ku chilungamo cha Mulungu.” (Aroma 10:3) N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti Ayuda amenewo ‘sanadziŵe chilungamo cha Mulungu?’ Kodi sanaphunzire Chilamulo, miyezo yolungama ya Mulungu? Anaphunzira. Komabe, ambiri a iwo m’malo moona chilungamo kukhala muyezo wowatsogolera mmene angachitire zinthu ndi anthu anzawo, iwo anachiona kukhala khalidwe labwino la munthu basi, lomwe angalipeze mwa kutsatira mosamalitsa malamulo a chipembedzo. Iwo sanamvetse tanthauzo lenileni la chilungamo, monganso mmene anachitira atsogoleri a chipembedzo amene analipo m’nthaŵi ya Yesu.—Mateyu 23:23-28.
7. Kodi Yehova amasonyeza bwanji chilungamo chake?
7 Mosiyana kwambiri ndi zimenezi, chilungamo cha Yehova chimasonyezedwa pa zonse zimene iye amachita ndipo chimaonekera bwino. Ngakhale kuti chilungamo chake chimaphatikizapo kusanyalanyaza machimo a munthu wolakwa mwadala, zimenezi sizim’chititsa kukhala Mulungu wosaganizira anthu ndiponso wongolamula, amene anthu angamuope ndi kupeŵa kulankhula naye. M’malo mwake, ntchito zake zachilungamo zapereka maziko oti anthu azilankhula naye ndiponso kupulumutsidwa ku uchimo. Motero, n’zoyenerera kuti Baibulo limafotokoza kuti Yehova ndiye “Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi.”—Yesaya 45:21.
Chilungamo ndi Chipulumutso
8, 9. Kodi Chilamulo chinasonyeza chilungamo cha Mulungu m’njira zotani?
8 Kuti timvetse mmene chilungamo cha Mulungu chimagwirizanira ndi chipulumutso chake chachikondi, tiyeni tione Chilamulo chimene iye anapatsa mtundu wa Israyeli kudzera mwa Mose. Palibe amene angakayike kuti Chilamulocho chinali cholungama. Mose anakumbutsa Aisrayeli m’mawu ake omaliza kuti: “Mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nawo malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lerolino?” (Deuteronomo 4:8) Kenako patapita zaka zambiri, Mfumu Davide ya Israyeli inati: “Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.”—Salmo 19:9.
9 Yehova anaonetsa miyezo yake ya chabwino ndi choipa kudzera m’Chilamulo. Icho chinafotokoza mwatsatanetsatane mmene Aisrayeli anayenera kuchitira pankhani za chipembedzo, za bizinesi, za m’banja, chakudya ndi ukhondo, ndiponso za chiweruzo. Chilamulo chinalinso ndi zilango zamphamvu kwa anthu amene angaswe chilamulocho ndipo nthaŵi zina ngakhale chilango cha imfa.a Koma kodi zofuna za Mulungu zolungama zimene zinali m’Chilamulocho zinali zokhwima ndiponso chimtolo cholemetsa chimene chinachititsa anthu kukhala opanda ufulu ndiponso osasangalala, ngati mmene anthu ambiri lerolino akunenera?
10. Kodi anthu amene anali kukonda Yehova anaona bwanji malamulo ake?
10 Amene anali kukonda Yehova anakondwera kwambiri ndi malamulo ake olungama. Mwachitsanzo, Mfumu Davide inazindikira kuti maweruzo a Yehova anali oona ndiponso olungama, monga taonera, ndiponso inawakonda ndi kuwayamikira kuchokera pansi pa mtima. Mfumuyi inalemba za malamulo ndi maweruzo a Yehova kuti: “Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa: Zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo: m’kuzisunga izo muli mphoto yaikulu.”—Salmo 19:7, 10, 11.
11. Kodi Chilamulo chinali bwanji ‘namkungwi wofikitsa kwa Kristu’?
11 Kenako patapita zaka zambiri, Paulo anafotokoza kufunika kwa Chilamulo koposa pamenepa. M’kalata yomwe analembera Agalatiya, iye anati: “Chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.” (Agalatiya 3:24) M’nthaŵi ya Paulo, namkungwi anali mtumiki kapena kapolo wa m’banja lalikulu. Anali ndi ntchito yoteteza ana ndi kuwaperekeza kusukulu. Mofananamo, Chilamulo chinatetezera Aisrayeli ku makhalidwe oipa ndi zipembedzo zonyenga za mitundu ya anthu imene anali nayo pafupi. (Deuteronomo 18:9-13; Agalatiya 3:23) Ndiponso, Chilamulo chinathandiza Aisrayeli kudziŵa kuti anali anthu ochimwa ndi kuti anafunikira chikhululukiro ndi chipulumutso. (Agalatiya 3:19) Makonzedwe a nsembe anasonyeza kuti panafunika nsembe ya dipo ndiponso zinapereka ulosi wa mmene anthu angadzamudziŵire Mesiya weniweni. (Ahebri 10:1, 11, 12) Motero, ngakhale kuti Yehova anasonyeza chilungamo chake kudzera m’Chilamulo, anachita zimenezo n’cholinga choti zinthu ziwayendere bwino anthuwo ndiponso kuti apeze chipulumutso chosatha.
Anthu Amene Mulungu Anawayesa Olungama
12. Kodi Aisrayeli akanapindula chiyani ngati akanatsatira bwino Chilamulo?
12 Aisrayeli akanakhala olungama pamaso pa Mulungu ngati akanamvera Chilamulo, popeza Chilamulo chimene Yehova anapereka chinali cholungama m’mbali zonse. Aisrayeli atatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawakumbutsa kuti: “Kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo aŵa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife.” (Deuteronomo 6:25) Ndiponso Yehova analonjeza kuti: “Muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nawo ndi moyo; ine ndine Yehova.”—Levitiko 18:5; Aroma 10:5.
13. Kodi Yehova sanachite chilungamo pofuna kuti anthu ake asunge Chilamulo cholungama? Fotokozani.
13 N’zomvetsa chisoni kuti mtundu wa Aisrayeli unalephera “kuchita malamulo aŵa onse pamaso pa Yehova” ndipo motero unalephera kulandira madalitso amene anaulonjeza. Unalephera kusunga malamulo onse a Mulungu chifukwa Chilamulo cha Mulungu chinali changwiro pamene mtunduwo sunali wangwiro. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu alibe chilungamo? Ayi. Paulo analemba kuti: “Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? M’satero ayi.” (Aroma 9:14) Mfundo ndi yakuti anthu ena omwe analipo Mulungu asanapereke Chilamulo komanso atapereka, anawayesa olungama ngakhale kuti anali opanda ungwiro ndiponso ochimwa. Ena mwa anthu oopa Mulungu amenewo anali Nowa, Abrahamu, Yobu, Rahabi, ndi Danieli. (Genesis 7:1; 15:6; Yobu 1:1; Ezekieli 14:14; Yakobo 2:25) Ndiyeno funso n’lakuti: N’chifukwa chiyani Mulungu anawayesa olungama anthu ameneŵa?
14. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati munthu “wolungama”?
14 Baibulo likamanena kuti munthu “wolungama,” silitanthauza kuti munthuyo ndi wosalakwa kapena wangwiro. M’malo mwake, limatanthauza kuti iye akuchita zimene Mulungu amafuna kwa anthu. Mwachitsanzo, Nowa anamutcha “munthu wolungama” ndiponso “wangwiro m’mibadwo yake” chifukwa chakuti “anachita . . . monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:9, 22; Malaki 3:18) Zekariya ndi Elisabeti, makolo a Yohane Mbatizi, ‘anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, [chifukwa, NW] anayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.’ (Luka 1:6) Ndiponso Baibulo limafotokoza kuti munthu wina yemwe sanali Mwisrayeli, mkulu wankhondo wa ku Italiya dzina lake Korneliyo, anali “wolungama ndi wakuwopa Mulungu.”—Machitidwe 10:22.
15. Kodi chilungamo n’chogwirizana ndi chiyani?
15 Ndiponso, chilungamo cha munthu n’chogwirizana kwambiri ndi zimene zili mumtima mwake—chikhulupiriro chake ndiponso kuyamikira ndi kukonda kwake Yehova ndi zimene walonjeza—osati kungochita kokha zimene Mulungu amafuna. Malemba amanena kuti Abrahamu “anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.” (Genesis 15:6) Abrahamu anakhulupirira kuti Mulungu alipo ndiponso anakhulupirira lonjezo Lake la “mbewu.” (Genesis 3:15; 12:2; 15:5; 22:18) Yehova anakhala bwenzi ndiponso anadalitsa Abrahamu ndi anthu ena okhulupirika ngakhale kuti anali opanda ungwiro. Anatero chifukwa chakuti anthuŵa anali ndi chikhulupiriro ndiponso ntchito zosonyeza chikhulupirirocho.—Salmo 36:10; Aroma 4:20-22.
16. Kodi n’chiyani chachitika chifukwa chokhulupirira dipo?
16 Pomaliza, chilungamo cha anthu chimadalira pa kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Paulo analemba za Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino kuti: “Ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo [cha Mulungu], mwa chiwombolo cha mwa Kristu Yesu.” (Aroma 3:24) Apa Paulo anali kunena za anthu amene anasankhidwa kukhala olamulira anzake a Kristu mu Ufumu wa kumwamba. Koma nsembe ya dipo ya Yesu inatseguliranso anthu miyandamiyanda mwayi woti angakhale olungama pamaso pa Mulungu. Mtumwi Yohane anaona m’masomphenya “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, . . . akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera.” Zovala zoyera zikuimira kukhala kwawo oyera ndi olungama pamaso pa Mulungu chifukwa chakuti “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.”—Chivumbulutso 7:9, 14.
Kondwerani ndi Chilungamo cha Yehova
17. Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tikhale olungama?
17 Ngakhale kuti Yehova anapereka mwachikondi Mwana wake, Yesu Kristu, monga njira imene anthu angakhalire olungama pamaso pake, sizingatheke kuti munthu akhale wolungama popanda kuchitapo kanthu. Munthu afunika kukhulupirira dipolo, kuchita chifuniro cha Mulungu, kudzipatulira kwa Yehova, ndi kusonyeza kudzipatulirako mwa kubatizidwa m’madzi. Ndiyeno, munthuyo ayenera kupitiriza kuchita chilungamo ndi kusonyeza makhalidwe ena auzimu. Paulo analangiza Timoteo, Mkristu wobatizidwa amene anali ndi chiyembekezo chopita kumwamba, kuti: ‘Tsata chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.’ (1 Timoteo 6:11; 2 Timoteo 2:22) Yesu anatsindikanso kufunika kochitabe zimenezi pamene anati: ‘Koma [pitirizani, NW] kuthanga mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.’ Mwina tingakhale tikuyesetsa kufuna madalitso a Ufumu wa Mulungu, koma kodi tikuyesetsanso kutsatira njira zolungama za Yehova?—Mateyu 6:33.
18. (a) N’chifukwa chiyani n’kovuta kuchita chilungamo? (b) Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Loti?
18 N’zoona kuti n’zovuta kuchita chilungamo. Zili choncho chifukwa chakuti tonsefe ndife opanda ungwiro ndipo mwachibadwa timakonda kuchita zosalungama. (Yesaya 64:6) Ndiponso, tikukhala ndi anthu amene njira zolungama za Yehova alibe nazo ntchito. Tili ngati mmene analili Loti amene anali kukhala mu mzinda woipa kwambiri wa Sodomu. Mtumwi Petro anafotokoza chifukwa chake Yehova anaona kuti kunali koyenera kupulumutsa Loti ku chiwonongeko chimene chinali chitatsala pang’ono kuchitika. Anati: “Wolungamayo pokhala pakati pawo, ndi kuona ndi kumva zawo, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika.” (2 Petro 2:7, 8) Choncho, tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimagwirizana nawo chamumtima makhalidwe oipa amene tikuonaŵa? Kodi ndimaona maseŵera kapena zosangalatsa zotchuka koma zachiwawa kukhala zoipa chabe? Kapena kodi ndimanyansidwa kwambiri ndi zinthu zosalungama zimenezo monga mmene anachitira Loti?’
19. Kodi tingakhale ndi madalitso otani ngati tikondwera ndi chilungamo cha Mulungu?
19 Kukondwera ndi chilungamo cha Yehova ndiko gwero la chitetezo m’nthaŵi zoopsa ndiponso zosinthasintha zino. Mfumu Davide poyankha mafunso akuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika?” inati: “Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo.” (Salmo 15:1, 2) Tingakhalebe paubwenzi wabwino ndi Mulungu ndipo angapitirizebe kutiyanja ndi kutidalitsa ngati titsatira chilungamo chake ndi kukondwera nacho. Tikatero, tidzakhala ndi moyo wokhutiritsa, tidzakhala odzilemekeza ndiponso tidzakhala pamtendere m’maganizo. Mawu a Mulungu akuti: “Wolondola chilungamo ndi chifundo apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.” (Miyambo 21:21) Ndiponso, kuyesetsa mmene tingathere kuchita chilungamo pa zonse zimene timachita kudzatithandiza kukhala ndi mabwenzi abwino. Ndiponso tidzakhala ndi moyo wabwinopo, mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu. Wamasalmo anati: “Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthaŵi zonse.”—Salmo 106:3.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Some Features of the Law Covenant,” m’buku lakuti Insight on the Scriptures, voluyumu 2, masamba 214-20, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mmenemo muli tsatanetsatane wa mbali zimene Chilamulo cha Mose chinakhudza.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi chilungamo n’chiyani?
• Kodi chipulumutso n’chogwirizana bwanji ndi chilungamo cha Mulungu?
• Kodi anthu amayesedwa olungama ndi Mulungu pazifukwa ziti?
• Kodi tingakondwere bwanji ndi chilungamo cha Yehova?
[Zithunzi patsamba 15]
Mfumu Davide inakonda malamulo a Mulungu kuchokera pansi pa mtima
[Zithunzi patsamba 16]
Mulungu anawayesa anthu awa olungama: Nowa, Abrahamu, Zekariya ndi Elisabeti, ndi Korneliyo. Kodi mukudziŵa chifukwa chake?