Saulo ndi Omwe Kale Anali Anzake Ndiponso Adani Ake
SAULO yemwe anadzatchedwa mtumwi Paulo, ayenera kuti anachita mantha pang’ono kubwerera ku Yerusalemu nthawi yoyamba atakhala Mkhristu.a Zaka zitatu m’mbuyomo anachoka mu mzindawu, ali wolusabe poopseza ndi kufuna kupha ophunzira a Yesu. Iye analamulidwa kuti agwire Mkhristu aliyense yemwe angam’peze ku Damasiko.—Machitidwe 9:1, 2; Agalatiya 1:18.
Atakhala Mkhristu, Saulo analengeza molimba mtima za chikhulupiriro chake mwa Mesiya woukitsidwa. Chifukwa cha zimenezi, Ayuda a ku Damasiko anafuna kumupha. (Machitidwe 9:19-25) Kodi Saulo akanayembekezera Ayuda omwe kale anali anzake kum’landira bwino ku Yerusalemu? Zimene Saulo ankafuna kwambiri n’zoti akapita kumeneku apeze otsatira a Khristu. Koma zimenezi sizinali zophweka.
“Atafika ku Yerusalemu anayesetsa kuti ayanjane ndi ophunzira kumeneko. Koma onse anamuopa, chifukwa sanakhulupirire kuti anali wophunzira.” (Machitidwe 9:26) Zimenezi n’zomveka. Iwowo ankam’dziwa kuti anali wozunza wankhanza kwambiri. Mwina iwo ankaona kuti Saulo anali kunamizira kuti anali Mkhristu n’cholinga choti alowerere mu mpingo. Motero, iwo sanafune kuyandikirana naye kwambiri.
Koma wina mwa anthuwa anathandiza Saulo. Baibulo limanena kuti Baranaba anam’perekeza “kwa atumwi” omwe zikuoneka kuti anali Petulo (Kefa) ndi Yakobe, m’bale wa Ambuye. Baranaba anawadziwitsa za kutembenuka mtima kwa Saulo ndi za mmene analalikira ku Damasiko. (Machitidwe 9:27; Agalatiya 1:18, 19) Baibulo silifotokoza mmene Baranaba anafikira pokhulupirira Saulo. Kodi awiriwa ankadziwana moti Baranaba anafufuza Saulo n’kuona kuti anali kunena zoona? Kapena kodi Baranaba ankadziwa Akhristu ena ku Damasiko amene anamuuza kuti Saulo anasintha? Mulimonse mmene zinalili, Baranaba anathandiza kuti anthu ena asiye kukayikira Saulo. Motero, Saulo anakhala ndi mtumwi Petulo masiku 15.
Anakhala ndi Petulo Masiku 15
Monga mmene anafotokozera kwa Agalatiya, Saulo anapatsidwa ntchito yake mwachindunji ndi Yesu ndipo sanafunikire kuvomerezedwa ndi munthu aliyense. (Agalatiya 1:11, 12) Koma mosakayikira Saulo anazindikira kufunika koti aphunzire zambiri za utumiki wa Yesu. Motero, kukhala ndi Petulo unali mwayi woti aphunzire zimenezi. (Luka 24:12; 1 Akorinto 15:3-8) Saulo ayenera kuti anali ndi zinthu zambiri zoti afunse Petulo ndi Yakobe. Ndipo iwonso ayenera kuti anali ndi mafunso ponena za masomphenya ndi ntchito yake.
Anapulumutsidwa kwa Omwe Kale Anali Anzake
Sitefano amadziwika kuti ndi woyamba kuphedwa chifukwa cha Chikhristu. Anthu omwe Sitefano anatsutsana nawo anali a “gulu lotchedwa Sunagoge wa Omasulidwa, ndi ena a ku Kurene, a ku Alesandiriya, komanso ena ochokera ku Kilikiya ndi ku Asiya.” Tsopano Saulo anali “kutsutsana ndi Ayuda olankhula Chigiriki,” ndi kuwalalikira molimba mtima. Ndipo iwo anafuna kumupha.—Machitidwe 6:9; 9:28, 29.
N’zomveka kuti Saulo anafuna kwambiri kuuza omwe kale anali anzake za kusintha kwakukulu pamoyo wake ndiponso kuyesa kuwaphunzitsa za Mesiya. Koma Ayuda olankhula Chigiriki amenewa anadana naye kwambiri chifukwa ankamuona ngati wopanduka.
Kodi Saulo anazindikira kuti moyo wake unali pa ngozi yaikulu? Timawerenga kuti pamene anali kupemphera m’kachisi, anachita ngati wagona tulo ndipo anaona Yesu, yemwe anamuuza kuti: “Fulumira, tuluka mu Yerusalemu msanga, chifukwa iwo sadzavomereza umboni wako wonena za ine.” Saulo anayankha kuti: “Ambuye, iwowo akudziwa bwino lomwe kuti ndinali kuponya m’ndende, ndi kukwapula m’sunagoge ndi sunagoge aja anali kukhulupirira mwa inu. Komanso pamene magazi a Sitefano mboni yanu anali kukhetsedwa, ine ndinali kuonerera ndi kumavomereza.”—Machitidwe 22:17-20.
Anthu ena amaganiza kuti mmene Saulo anayankhira zinasonyeza kuti ankadziwa zoti moyo wake unali pa ngozi. Enanso amaganiza kuti Saulo ankanena kuti: ‘Iwo akudziwa kuti inenso ndinali wozunza ngati iwowo. Ndithudi, ayenera kukhudzidwa kwambiri kuti ndinatembenuka mtima. Mwina ndingawathandize kudziwa choonadi.’ Ngakhale n’choncho, Yesu anadziwa kuti Ayuda sangamvetsere ulaliki wa munthu amene amamuona ngati wampatuko. Motero, Yesu anauza Saulo kuti: “Nyamuka, chifukwa ndidzakutumiza kutali kwa amitundu.”—Machitidwe 22:21, 22.
Pamene Akhristu anzake anadziwa kuti moyo wa Saulo uli pa ngozi, anapita naye mwamsanga ku doko la Kaisareya ndi kumutumiza kwawo ku Tariso, ulendo wa makilomita 500. (Machitidwe 9:30) Panapita zaka zambiri Saulo asanabwerere ku Yerusalemu.
Kuchoka mwamsanga kumeneku kuyenera kuti kunateteza mpingo wachikhristu. Saulo akanakhalabe ku Yerusalemu kukanabuka mavuto ambiri. Saulo atachoka, “mpingo mu Yudeya yense, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo ya mtendere, ndipo unakhala wolimbikitsidwa. Ndipo chifukwa unali kuyenda moopa Yehova ndi m’chilimbikitso cha mzimu woyera, unali kuwirikizawirikiza.”—Machitidwe 9:31.
Tiphunzire Kukhala Osamala
Mofanana ndi nthawi ya atumwi, masiku anonso tiyenera kukhala osamala nthawi zina. Sitifunikira kungokayikira anthu onse achilendo. Koma nthawi zina, anthu ena achinyengo ayesa kudyera masuku pamutu anthu a Yehova n’cholinga choti iwowo apindule kapena asokoneze mpingo. Choncho, tifunikira kusamala kuti tisanyengedwe ndi anthu amenewa.—Miyambo 3:27; 2 Timoteyo 3:13.
Zimene Saulo anachita atalalikira ku Yerusalemu zikusonyeza njira ina imene Akhristu angakhalire osamala. Kulalikira ku madera ena kapena kwa anthu ena, ngakhale anthu amene kale anali anzathu, kungativulaze, kungaipitse makhalidwe athu, kapena kungawononge moyo wathu wauzimu. Motero, tiyenera kukhala osamala kwambiri posankha bwino zinthu monga nthawi ndi malo olalikirako.—Miyambo 22:3; Mateyo 10:16.
Tili ndi chikhulupiriro choti uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa mapeto a dongosolo loipali asanafike. Ndithudi, Saulo anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pankhani yolalikira. Iye ‘analankhula molimba mtima m’dzina la Ambuye’ ngakhale kwa omwe kale anali anzake ndiponso adani ake.—Machitidwe 9:28.
[Mawu a M’munsi]
a Masiku ano, Saulo amadziwika kuti mtumwi Paulo. Koma m’mavesi ambiri omwe ali m’nkhani ino, iye akutchulidwa ndi dzina lake lachiyuda lakuti Saulo.—Machitidwe 13:9.
[Chithunzi patsamba 16]
Saulo atafika ku Yerusalemu, analalikira molimba mtima kwa Ayuda olankhula Chigiriki