Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingalake Motani Kupunduka Kwanga?
“AKHOZA kuyenda,” akutero nakubala wa mtsikana wina wachichepere amene tikumpatsa dzina lakuti Maggie. “Koma kutakasuka kwake sikokwanira, ndipo kunena kwake nkosamveka bwino.” Maggie ali ndi nthenda yotchedwa multiple sclerosis ndipo ali mmodzi wa mamiliyoni ambiri a achichepere kuzungulira dziko lonse amene ali opunduka mwakuthupi.
Mwinamwake ndinu mmodzi wa iwo. Ndipo kaya munabadwa muli wopunduka kapena kupundukako kunachitika chifukwa cha kudwala kapena ngozi,a palibe chifukwa chonenera kuti kwanu kwatha. Mwakuchitapo kanthu modekha, mungatenge njira zabwino zolakira mkhalidwe wanu mogwira mtima.
Msampha wa Kulakalaka
Ndithudi, kuli kwachibadwa kusafuna kuvomereza mkhalidwe weniweni woipa umene ulipo koma mosinkhasinkha kuyembekezera kuti kupundukako kudzangotha. Mtumwi Paulo mwachionekere anali kudwala mtundu winawake wa matenda umene unayambukira maso ake. (Yerekezerani ndi Agalatiya 6:11.) Ponena za ulendo wake woyamba kwa Akristu a ku Galatiya, Paulo anati: “M’kufooka kwa thupi ndinakulalikirani uthenga wabwino poyamba: ndipo chija cha m’thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputsa, kapena sichinakunyansirani.” (Agalatiya 4:13, 14) Akatswiri ena amaganiza kuti nthenda ya Paulo inachititsa maso ake kutulutsa manthongo kapena kuti mwanjira ina inapangitsa kawonekedwe ka kumaso kwake kukhala konyansa. Pamenepo, mposadabwitsa kuti Paulo ‘anapempha Ambuye katatu’ kuti nthendayo ichoke. Komatu sinachoke. (2 Akorinto 12:8, 9) Komabe, mosasamala kanthu za nthenda yake, anasangalala ndi ntchito yapadera monga mmishonale, katswiri wodziŵa malamulo, ndi mlembi.
Nanunso mungavomereze uchikhalire wa kupunduka kwanu. M’buku lake lakuti Living With the Disabled, wolemba buku Jan Coombs analemba kuti: “Kuti wodwalayo asinthire kumkhalidwe wake wopunduka choyamba ayenera kuvomereza kuti iye ngwopunduka. Ayenera kudziŵa kuti kusakhoza kwake kungamletse ndi kusamuyeneretsa kuchita zinthu zina koma sikukumpanga kukhala munthu wosanunkha kanthu.” Ngati palibe chiyembekezo chenicheni cha kuchira, kukana zenizeni za mkhalidwe wanu kudzangokuloŵetsani mumkhalidwe wovuta kwambiri wodziimba mlandu, kuvutika maganizo, ndi kugwiritsidwa mwala. Kumbali ina, “nzeru ili ndi odzichepetsa,” Baibulo limatero pa Miyambo 11:2, ndipo munthu wodzichepetsa amadziŵa ndi kuvomereza zopereŵera zake. Zimenezi sizitanthauza kukhala wodzipatula kapena kukhutiritsidwa ndi mkhalidwe wosakondweretsa, kukhalapo kopanda chisangalalo. Mmalomwake, kudzichepetsa kumafuna kupenda mowona mtima mkhalidwe wanu ndi kudziikira zonulirapo zotsimikizirika.
Chitaponi Kanthu Mwanzeru
Mufunikiranso chidziŵitso cholongosoka ponena za mtundu wa kupunduka kwanu. “Yense wochenjera amachita mwanzeru,” pamatero pa Miyambo 13:16. (Yerekezerani ndi Miyambo 10:14.) Zimenezi zingatanthauze kuti muŵerenge mabuku ena onena za matenda ndi mankhwala kapena kufunsa mafunso olunjika kwa dokotala wanu ndi akatswiri ena a zathanzi amene amakupatsani mankhwala. Kudziphunzitsa pankhani imeneyi kungakuchotsereni malingaliro olakwa amene angakuletseni kuchita zimene mungathe.
Kuyendera limodzi ndi zochitika za mankhwala ndi kuchiritsa matenda zimene zingawongolere mkhalidwe wanu kudzathandizanso. Mwachitsanzo, ziŵalo zoikirira (prostheses) zopangidwa ndi zinthu zopepuka zimene zimatheketsa kupeza bwino kwakukulu ndi kutakasuka kwa kayendedwe ka thupi zatulukiridwa. Kunena zowona, magazini a Time akusimba za “kuwonjezereka kwadzidzidzi” kwa zipangizo zothandiza anthu opunduka. Mwinamwake zipangizo zimenezo ziliko kwanuko ndipo banja lanu lingathe kuzigula.
Zipangizo zozoloŵereka, monga ngati ziwiya zothandiza munthu kumva, ndodo yopapasira njira, ndodo zamkhwapa zoyendera, ndi makhoza ochilikizira mfundo, zingakhalenso zothandiza kwambiri. Tsopano, achichepere ena angakhale amanyazi kwambiri ndi osapeza bwino kugwiritsira ntchito zothandizira zimenezo. Koma Mfumu Solomo mwanzeru ananena kuti: “Ngati nkhwangwa yako ili yobuntha ndipo suinola, uyenera kuchita mwamphamvu kuti igwire ntchito.” (Mlaliki 10:10; Today’s English Version) Mofananamo mungangodzilanga—kapena kudziletsa kuloŵa nawo m’machitachita osangalatsa—ngati mulephera kugwiritsira ntchito bwino zipangizo zimene zingakuthandizeni. Kodi nchifukwa ninji mungalole kunyada kupangitsa moyo wanu kukhala wovuta kuposa mmene uyenera kukhalira? Solomo anamaliza mwakunena kuti: “Kugwiritsira ntchito nzeru m’njira yopambana kumatanthauza phindu.”—NW.
Inde, kugwiritsira ntchito kanthu kena kamene kadzakuthandizani kuyenda, kuwona, kapena kumva bwinopo kudzakupindulitsani. Zowona, kungafunikire kuyeseza kwakutikwakuti ndi kuleza mtima kuti muzoloŵere kugwiritsira ntchito ndodo yamkhwapa yoyendera, chiŵalo choikirira, kapena chiwiya chokuthandizani kumva. Ndipo ziwiya zimenezi sizingakongoletse kawonekedwe kanu. Komatu taganizani za ufulu umene zinthu zimenezi zingakupatseni ndi mipata imene zingakutsegulireni! Msungwana wina wopunduka wa mu Africa wotchedwa Jay anali ndi moyo wodzipatula, akumatuluka koyamba m’kompaundi yaing’ono imene anali kukhala m’zaka zake 18. Ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anayamba kuloŵa misonkhano Yachikristu. Zimenezi zinafuna kuti “ayende” ulendo wopyola midadada ya nyumba zingapo, akumakwaŵa. Pamene Mboni ina ku Ulaya inamva za vuto la Jay, inamtumizira mpando wa magudumu atatu. Unali ndi chopalasira chimene Jay akanatha kuchigwiritsa ntchito ndi manja ake. Zambambande eti? Kutalitali. Koma choyendera chosawoneka bwino chimenechi chinamkhozetsa kumka kumisonkhano ndi kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba.
Dzisonkhezereni!
Komabe, chenjerani ndi kukulitsa mkhalidwe wa maganizo amphwayi. Mfumu Solomo anati: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.” (Mlaliki 11:4) Kodi mumalola mantha kapena kusatsimikizirika kukuletsani kuchita zinthu zimene mumafuna kuchita? Lingalirani za Mose. Pamene Mulungu anamsankha kukalanditsa Aisrayeli muukapolo wa ku Igupto, Mose anayesa kukana pachifukwa cha kusakhoza kulankhula bwino. “Ndine wa milomo yosadula,” Mose anatero, mwinamwake sankatha kutulutsa bwino mawu m’kamwa. (Eksodo 6:12) Koma Mose anali kungodzinyozetsa. Mkupita kwa nthaŵi, anatsimikizira kuti anali wokhoza kulankhula mosadodoma—akumanena ndi mtundu wonse wa Israyeli.—Deuteronomo 1:1.
Musapange cholakwa chofananacho cha kudzinyozetsa. Yesetsani ndipo dzisonkhezereni! Mwachitsanzo, Becky wachichepere ali ndi vuto polankhula chifukwa cha kuvulala kumene anali nako kumene kunachitika pausinkhu wa zaka zisanu. Koma makolo ake sanamlole kuleka kuyesayesa. Mosiyana, anamlembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki ku Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova. Pamene anafika zaka zisanu ndi ziŵiri, Becky anali kukambira nkhani zazifupi omvetsera. Becky akukumbukira kuti: “Kukamba nkhani kunandithandiza. Kunandisonkhezera kuwongolera kwambiri kalankhulidwe kanga.” Becky analimbikitsidwanso kukhala ndi phande lokwanira m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. “Nthaŵi zina ndimaganiza kuti anthu amanyansidwa ndi kulankhula kwanga; ndimavutika maganizo ndi zimene amaganiza. Komano ndimanena ndekha kuti, ‘Ndikuchitira zimenezi Yehova,’ ndipo ndimampempha kuti andithandize kuzilaka.” Lerolino, Becky akutumikira monga mlaliki wanthaŵi yonse.
Craig, yemwe ali wachikulire tsopano, amadwala matenda aubongo otchedwa cerebral palsy. Nayenso wakana kulola kupunduka kwake kumletsa kukhala chiŵalo choŵerengeredwa cha mpingo Wachikristu. Iye akuti: “Ndimadalira Yehova, ndipo iye wandilola kulandira madalitso ambiri. Ndakhala wokhoza kutumikira monga mpainiya wothandiza [mlaliki] kasanu. Ndimakamba nkhani za m’Baibulo pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki, ndipo ndili wokhoza kusamalira maakaunti ampingo.”
Palinso “mphindi ya kuseka,” ndipo mwakuyeseza kwakutikwakuti, inu mwina mungakhale wokhoza kusangalala ndi maseŵera ena amene achichepere ena amasangalala nawo. (Mlaliki 3:4) Becky akuvomereza kuti: “Sindingathe kuseŵera maseŵera onga volleyball chifukwa chakuti thupi langa limatakasuka mochedwa kwambiri. Koma ndikhoza kuthamanga. Ndipo mwamsanga pambuyo pa ngoziyo, amayi anandilimbikitsa kuphunzira kukwera njinga. Nthaŵi zonse anandilimbikitsa kuyesa kuchita kanthu kena katsopano.”
Musalimbane ndi Vutolo Nokha
Kulimbana ndi mkhalidwe wopunduka nkovuta. Mtumwi Paulo anatcha nthenda yake kukhala “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7) Mwamwaŵi, simuyenera kulimbana ndi mavuto anu muli nokha. Msungwana wina wotchedwa Sarne wotsimphina mwendo, akuti: “Ndapeza kuti kuyanjana Kwachikristu koyenerera ndi chichilikizo chachikondi chochokera m’banja ndi mabwenzi a mumpingo zakhala zamtengo wapatali kwambiri kwa ine.” Inde, musadzipatule. (Miyambo 18:1) Kufikira kumlingo wothekera, khalani ndi “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.” (1 Akorinto 15:58, NW) Sarne akufotokoza mapindu ake: “Kukhala wokangalika m’zinthu za Ufumu kumandithandiza kuwona moyenera mavuto anga.” Becky akuti: “Umalankhula ndi anthu amene ali mumkhalidwe woipa kwambiri kuposa wako chifukwa chakuti alibe chiyembekezo chamtsogolo. Zimenezo zimandithandiza kuiŵala mavuto anga.”
Koposa zonse, yang’anani kwa Yehova Mulungu kuti muchilikizidwe. Amadziŵa zosoŵa zanu ndi mmene mumamvera ndipo angathedi kukupatsani “mphamvu zoposa zachibadwa” kukuthandizani kulimbana ndi vutolo. (2 Akorinto 4:7, NW) Mwinamwake mkupita kwa nthaŵi mungakhale ndi lingaliro lotsimikiza la wachichepere wina Wachikristu wotchedwa Terrence. Pausinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi, Terrence anakhala wosawona koma sanalole kugonjetsedwa nako, iye akuti: “Kusawona kwanga sikupunduka; kwangokhala chinthu chododometsa.”
[Mawu a M’munsi]
a Ngati kupunduka kwanu kwangochitika kumene, momvekera bwino inu mungakhale mukulimbana ndi malingaliro opweteka, mkwiyo, ndi chisoni. Kwenikweni, zimenezi nzachibadwa kwambiri—ndiponso nzabwino—kuvutika pamene mwakanthidwa ndi vuto lalikulu. (Yerekezerani ndi Oweruza 11:37; Mlaliki 7:1-3.) Tsimikizirani kuti mkupita kwa nthaŵi ndi chichilikizo chachikondi cha banja ndi mabwenzi, malingaliro opweteka kwambiri potsirizira pake adzachepa.
[Chithunzi patsamba 18]
Dziŵani zonse zomwe mungathe ponena za kupunduka kwanu