Chilimikani mu Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu!
‘Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.’—AGALATIYA 5:1.
1, 2. Kodi ufulu woperekedwa ndi Mulungu unataika motani?
ANTHU a Yehova ali aufulu. Koma samafuna kuchoka kwa Mulungu, popeza kuti chimenecho chikatanthauza ukapolo kwa Satana. Amasangalala ndi unansi wawo wathithithi ndi Yehova ndipo amakondwera ndi ufulu umene iye akuwapatsa.
2 Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, anataya ufulu woperekedwa ndi Mulungu mwakuchimwa ndi kukhala akapolo a uchimo, imfa, ndi Mdyerekezi. (Genesis 3:1-19; Aroma 5:12) Eya, Satana anaika dziko lonse panjira yochimwa yonka kuchiwonongeko! Koma amene amachilimika mu ufulu woperekedwa ndi Mulungu amayenda pamsewu wopita kumoyo wamuyaya.—Mateyu 7:13, 14; 1 Yohane 5:19.
Kumasuka ku Ukapolo
3. Kodi Mulungu anapereka chiyembekezo chotani mu Edeni?
3 Yehova anafuna kuti anthu olemekeza dzina lake akhale omasuka ku ukapolo wa Satana, uchimo, ndi imfa. Chiyembekezo chimenecho chinaperekedwa pamene Mulungu anauza njoka yogwiritsiridwa ntchito ndi Satana mu Edeni kuti: ‘Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.’ (Genesis 3:14, 15) Yesu Kristu, Mbewu ya gulu lakumwamba la Yehova, analumidwa kuchitende pamene anafa pamtengo, koma mwakutero Mulungu anapereka nsembe yadipo kumasula anthu okhulupirira ku uchimo ndi imfa. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) M’kupita kwanthaŵi, Yesu adzalalira mutu wa Satana, Njoka yokalambayo.—Chivumbulutso 12:9.
4. Kodi Abrahamu anasangalala ndi ufulu wotani, ndipo kodi Yehova anamlonjeza chiyani?
4 Zaka 2,000 pambuyo pa lonjezo loperekedwa mu Edeni, Abrahamu, “bwenzi la [Yehova, NW]” anamvera Mulungu nachoka mumzinda wa Uri kupita kumalo ena. (Yakobo 2:23; Ahebri 11:8) Mwakutero analandira ufulu woperekedwa ndi Mulungu ndipo sanakhalenso monga kapolo m’dziko la Satana la chipembedzo chonyenga, ndale zoipa, ndi malonda aumbombo. Ku ulosi wa mu Edeni, Mulungu anawonjezera malonjezo akuti mabanja onse ndi mitundu akadzidalitsa okha mwa Abrahamu ndi Mbewu yake. (Genesis 12:3; 22:17, 18) Abrahamu anali womasuka ku chiweruzo chifukwa chakuti ‘anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.’ (Genesis 15:6) Lerolino, unansi wathithithi ndi Yehova umabweretsanso ufulu woperekedwa ndi Mulungu ku chiweruzo ndi ukapolo wa dziko lokhala muulamuliro wa Satana.
Chochitika Chogwira Mtima Chophiphiritsira
5. Kodi kubadwa kwa Isake kunagwirizanitsidwa ndi mikhalidwe yotani?
5 Kuti Abrahamu akhale ndi mbewu, Sara, mkazi wake wouma, anampatsa mdzakazi wake, Hagara, kuti ambalire mwana. Mwa iye, Abrahamu anabala Isimayeli, koma Mulungu sanamusankhe iye kukhala Mbewu yolonjezedwa. Mmalomwake, pamene Abrahamu anali ndi zaka 100 zakubadwa ndipo Sara ali ndi 90, Yehova anawatheketsa kukhala ndi mwana wotchedwa Isake. Pamene Isimayeli anaseka Isake, Hagara ndi mwana wake anathamangitsidwa, namsiya mwana wa Abrahamu wobadwa kwa Sara mkazi waufulu monga mbewu yosatsutsika ya Abrahamu. Mofanana ndi Abrahamu, Isake anasonyezanso chikhulupiriro ndipo anasangalala ndi ufulu woperekedwa ndi Mulungu.—Genesis 16:1-16; 21:1-21; 25:5-11.
6, 7. Kodi aphunzitsi onyenga anakhutiritsa Akristu ena aku Galatiya ponena za chiyani, koma kodi Paulo anafotokoza chiyani?
6 Zochitika zimenezi zinaphiphiritsira zinthu zofunika kwambiri kwa okonda ufulu woperekedwa ndi Mulungu. Izi zinasonyezedwa m’kalata imene mtumwi Paulo analembera mipingo ya ku Galatiya pafupifupi 50 mpaka 52 C.E. Panthaŵiyo bungwe lolamulira linagamula kuti mdulidwe sunali wofunika kwa Akristu. Koma aphunzitsi onyenga anakakamiza Agalatiya ena kukhulupirira kuti unali mbali yofunika ya Chikristu.
7 Paulo anauza Agalatiya kuti: Munthu amalengezedwa wolungama mwa chikhulupiriro mwa Kristu, osati ndi ntchito Zachilamulo cha Mose. (1:1–3:14) Chilamulo sichinathetse lonjezo logwirizanitsidwa ndi pangano la Abrahamu koma linawonetsera zolakwa ndipo linatumikira monga namkungwi wakutsogolera kwa Kristu. (3:15-25) Mwa imfa yake, Yesu anamasula okhala pansi pa Chilamulo, kuwatheketsa kukhala ana a Mulungu. Chifukwa chake, kubwerera ku kakonzedwe kakusunga masiku, miyezi, nyengo, ndi zaka kukatanthauza kubwerera muukapolo. (4:1-20) Ndiyeno Paulo analemba kuti:
8, 9. (a) Fotokozani mwachidule m’mawu anu zimene Paulo ananena pa Agalatiya 4:21-26. (b) M’chochitika chophiphiritsira chimenechi, kodi ndani kapena nchiyani chimene chinachitiridwa fanizo ndi Abrahamu ndi Sara, ndipo kodi ndani amene ali Mbewu yolonjezedwa?
8 ‘Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo? Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nawo ana aamuna aŵiri, mmodzi [Isimayeli] wobadwa mwa mdzakazi [Hagara], ndi mmodzi [Isake] wobadwa mwa mfulu [Sara]. Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa; pakuti akaziwa ali mapangano aŵiri, mmodzi [pangano Lachilamulo] wa ku phiri la Sinai [kumene Mulungu anakhazikitsa pangano limenelo ndi Aisrayeli], akubalira ukapolo, ndiye Hagara. [Pangano lina linali limene linapangidwa ndi Abrahamu ponena za Mbewu yake.] Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, m’Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu watsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake [mbadwa za Abrahamu, Isake, ndi Yakobo]. Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amayi wathu.’—Agalatiya 4:21-26.
9 M’chochitika chophiphiritsira chimenechi, Abrahamu anaimira Yehova. “Mfulu,” Sara, anachitira chithunzi “mkazi” wa Mulungu, kapena gulu lopatulika lakumwamba. Ilo linatulutsa Kristu, Mbewu ya mkazi wophiphiritsira ameneyo ndi ya Abrahamu Wamkulu. (Agalatiya 3:16) Kuti awasonyeze anthu njira yomasulidwira ku kulambira kodetsedwa, uchimo, ndi Satana, Yesu anaphunzitsa chowonadi navumbula chipembedzo chonyenga, koma Yerusalemu ndi ana ake anakhalabe muukapolo wachipembedzo chifukwa anamkana. (Mateyu 23:37, 38) Otsatira a Yesu Achiyuda anakhala omasuka ku Lamulo, lomwe linasonyeza ukapolo wawo wa kupanda ungwiro, uchimo, ndi imfa. Anthu onse amene amavomereza Yesu monga Amene anabadwa kwa “mkazi” wa Mulungu kukhala Mfumu Yaumesiya ndi Womasula ‘wolengeza ufulu kwa am’nsinga’ alidi aufulu!—Yesaya 61:1, 2; Luka 4:18, 19.
Peŵani Goli Laukapolo
10, 11. Kodi Kristu anamasula otsatira ake ku goli laukapolo lotani, ndipo kodi pali kufanana kotani komwe tingawone lerolino?
10 Kwa awo amene akupanga mbewu ya Abrahamu limodzi ndi Kristu, Isake Wamkulu, Paulo akuti: ‘Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amayi wathu. . . . Ife, abale, monga Isake, tiri ana a lonjezano. Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi [Isimayeli] anazunza wobadwa monga mwa mzimu [Isake], momwemonso tsopano. . . . Sitiri ana a mdzakazi, komatu a mfulu. Kristu anatisandutsa mfulu [ku Chilamulo], kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.’—Agalatiya 4:26–5:1.
11 Aliyense wa otsatira a Yesu akanabindikiritsidwa m’goli la ukapolo ngati anagonjera ku Chilamulo. Chipembedzo chonyenga ndicho goli laukapolo lamakono, ndipo Chikristu Chadziko chimalingana ndi Yerusalemu wakale ndi ana ake. Koma odzozedwa ali ana a Yerusalemu wakumwamba, gulu lakumwamba laufulu la Mulungu. Iwo ndi okhulupirira anzawo okhala ndi ziyembekezo zapadziko lapansi sali mbali ya dziko lino ndipo sali muukapolo kwa Satana. (Yohane 14:30; 15:19; 17:14, 16) Pokhala tinamasulidwa ndi chowonadi ndi nsembe ya Yesu, tiyeni tichilimike mu ufulu wathu woperekedwa ndi Mulungu.
Kuchilikiza Ufulu Woperekedwa ndi Mulungu
12. Kodi ndinjira yotani yomwe yatengedwa ndi okhulupirira, ndipo kodi tsopano tidzakambitsirana chiyani?
12 Tsopano mamiliyoni ambiri amasangalala ndi ufulu weniweni monga Mboni za Yehova. Maphunziro Abaibulo akuchitidwa ndi mamiliyoni ena, ambiri a iwo ali ‘oikidwiratu ku moyo wosatha.’ Pamene akhala okhulupirira, iwo amachilikiza ufulu woperekedwa ndi Mulungu mwakubatizidwa. (Machitidwe 13:48; 18:8) Koma kodi ndimasitepe otani amene amakhalapo ubatizo Wachikristu usanachitike?
13. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chidziŵitso ndi ubatizo?
13 Munthu asanabatizidwe, ayenera kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Malemba ndi kuchitapo kanthu. (Aefeso 4:13) Chotero, Yesu anauza otsatira ake kuti: ‘Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’—Mateyu 28:19, 20.
14. Kubatizidwa m’dzina la Atate, la Mwana, ndi mzimu woyera kumafunikira chidziŵitso chotani?
14 Kubatizidwa m’dzina la Atate kumatanthauza kuvomereza udindo ndi ulamuliro wa Yehova monga Mulungu, Mlengi, ndi Mfumu Yachilengedwe chonse. (Genesis 17:1; 2 Mafumu 19:15; Chivumbulutso 4:11) Kubatizidwa m’dzina la Mwana kumafunikira kuti tizindikire udindo ndi ulamuliro wa Kristu monga cholengedwa chauzimu chokwezedwa, Mfumu Yaumesiya, ndi amene kupyolera mwa iye Mulungu wapereka “dipo lolinganira.” (1 Timoteo 2:5, 6, NW; Danieli 7:13, 14; Afilipi 2:9-11) Munthu wobatizidwa m’dzina la mzimu woyera amazindikira kuti uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu yomwe Yehova anagwiritsira ntchito m’kulenga ndi kuuzira olemba Baibulo, limodzinso ndi m’njira zina. (Genesis 1:2; 2 Petro 1:21) Ndithudi, pali zina zambiri zimene tingaphunzire ponena za Mulungu, Kristu, ndi mzimu woyera.
15. Kodi nchifukwa ninji munthu afunikira kukhala ndi chikhulupiriro asanabatizidwe?
15 Ubatizo usanachitike, munthu ayenera kusonyeza chikhulupiriro chozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka. ‘Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Yehova].’ (Ahebri 11:6) Munthu wosonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu, Kristu, ndi chifuno cha Mulungu adzafuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, wokhala mogwirizana ndi Mawu a Mulungu ndi kukhala ndi phande lokwanira m’kulalikira mbiri yabwino. Iye adzalankhula za ulemerero wa ufumu wa Yehova.—Salmo 145:10-13; Mateyu 24:14.
16. Kodi kulapa nchiyani, ndipo nkogwirizana motani ndi ubatizo Wachikristu?
16 Kulapa kuli chiyeneretso china cha ubatizo. Kulapa kumatanthauza “kusintha maganizo ponena za kachitidwe kakale (kapena kamene muganiza kukachita), kapena khalidwe, chifukwa cha kuipidwa kapena kusakhutira,” kapena “kuchita chisoni, kukhumudwa, kapena kunyansidwa ndi chimene munachita kapena kulephera kuchita.” Ayuda a m’zaka za zana loyamba anafunikira kulapa machimo awo kwa Yesu Kristu. (Machitidwe 3:11-26) Okhulupirira ena a ku Korinto analapa machimo a dama, kulambira mafano, chigololo, kugonana kwa ofanana ziŵalo, kuba, umbombo, kuledzera, kulalatira, ndi kulanda. Chotulukapo chinali chakuti, ‘anasambitsidwa’ m’mwazi wa Yesu, ‘anayeretsedwa’ monga opatulidwa kaamba ka utumiki wa Yehova, ndipo ‘anayesedwa olungama’ m’dzina la Yesu Kristu ndi mzimu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Chotero kulapa kuli sitepe lofunika kulinga ku chikumbumtima chabwino ndi ufulu woperekedwa ndi Mulungu kuchoka ku liŵongo lovulaza la tchimo.—1 Petro 3:21.
17. Kodi kutembenuka kumatanthauzanji, ndipo kodi kumafunanji kwa munthu amene akukonzekera kubatizidwa?
17 Kutembenuka kuyenera kuchitika munthuyo asanabatizidwe monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Kutembenuka kwa munthu wolapa kumachitika pambuyo pakukana njira yake yolakwa ndi kutsimikiza mtima kuchita cholondola. Aneni Achihebri ndi Chigiriki ofanana ndi kutembenuka amatanthauza “kubwerera m’mbuyo, kupotokola, kapena kubwerera.” Pamene agwiritsiridwa ntchito m’lingaliro labwino lauzimu, amatanthauza kutembenukira kwa Mulungu kuchoka ku njira yolakwa. (1 Mafumu 8:33, 34) Kutembenuka kumafuna ‘ntchito zoyenera kutembenuka mtima,’ kuti tichite zimene Mulungu amalamula, kusiya chipembedzo chonyenga, ndi kulunjikitsa mtima wathu mosagwedera kwa Yehova kotero kuti timtumikire iye yekha. (Machitidwe 26:20; Deuteronomo 30:2, 8, 10; 1 Samueli 7:3) Izi zimafunikira “mtima watsopano, ndi mzimu watsopano,” kulingalira kosinthidwa, kuganiza, ndi cholinga m’moyo. (Ezekieli 18:31) Umunthu watsopano wotulukapo umachotsa mikhalidwe yopanda umulungu ndi kuikamo yaumulungu. (Akolose 3:5-14) Inde, kulapa kowona kumachititsa munthu “kutembenuka.”—Machitidwe 3:19, NW.
18. Kodi nchifukwa ninji tifunikira kudzipatulira kwa Mulungu m’pemphero, ndipo kodi sitepeli nlofunika motani?
18 Munthu ayenera kudzipatulira kwa Mulungu m’pemphero asanabatizidwe. (Yerekezerani ndi Luka 3:21, 22.) Kudzipatulira kumatanthauza kuika pambali kaamba ka chifuno chopatulika. Sitepe limeneli liri lofunika kwambiri kwakuti tiyenera kumfotokozera Mulungu m’pemphero chosankha chathu chakudzipereka kotheratu kwa iye ndi kumtumikira kosatha. (Deuteronomo 5:8, 9; 1 Mbiri 29:10-13) Ndithudi, sitimadzipatulira ku ntchito koma kwa Mulungu iyemwini. Mfundo imeneyo inamveketsedwa pamaliro a prezidenti woyamba wa Watch Tower Society, Charles Taze Russell. Pachochitika chimenecho mu 1916, mlembi wosunga chuma wa Sosaite, W. E. Van Amburgh, anati: “Ntchito yaikulu yapadziko lonse imeneyi siiri ntchito ya munthu mmodzi. Njaikulu kwambiri yoti sangaithe. Iyo ndintchito ya Mulungu ndipo simasintha. Mulungu anagwiritsira ntchito atumiki ambiri m’nthaŵi zakale ndipo Iye mosakaikira adzagwiritsira ambiri mtsogolo. Kudzipatulira [kudzipereka] kwathu sikuli kwa munthu, kapena ku ntchito ya munthu, koma kuchita chifuniro cha Mulungu, monga momwe Iye adzativumbulira kudzera m’Mawu Ake ndi zitsogozo zaumulungu. Mulungu adakali mutu.” Koma kodi nchiyani chinanso chimene chiyenera kuchitidwa ponena za kudzipatulira kwa Mulungu?
19. (a) Kodi ndimotani mmene anthu amaperekera umboni wapoyera wakudzipatulira kwa Yehova? (b) Kodi ubatizo wa m’madzi uli chizindikiro cha chiyani?
19 Umboni wapoyera wa kudzipatulira kwa Yehova umaperekedwa pamene munthu abatizidwa. Ubatizo uli chizindikiro chakuti munthu amene akumizidwa m’madziyo wapanga kudzipatulira kotheratu kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. (Yerekezerani ndi Mateyu 16:24.) Pamene munthu wopita kuubatizo amizidwa m’madzi ndi kutulutsidwa, iye amafa mophiphiritsira ku njira yake yakale ya moyo ndi kuukitsidwa ku njira yatsopano ya moyo, kuti achite chifuniro cha Mulungu mosasiyako. (Yerekezerani ndi Aroma 6:4-6.) Pamene Yesu anabatizidwa, iye anadzipereka mwini kwa Atate wake wakumwamba m’njira yotheratu. (Mateyu 3:13-17) Ndipo Malemba amasonyeza mobwerezabwereza kuti okhulupirira oyeneretsedwa ayenera kubatizidwa. (Machitidwe 8:13; 16:27-34; 18:8) Chotero, kuti munthu akhale mmodzi wa Mboni za Yehova lerolino, ayenera kukhala wokhulupirira amene alidi ndi chikhulupiriro ndi kubatizidwa.—Yerekezerani ndi Machitidwe 8:26-39.
Chilimikani!
20. Kodi nzitsanzo zina ziti Zabaibulo zotsimikizira kuti tidzadalitsidwa chifukwa chakuchilimika mu ufulu woperekedwa ndi Mulungu monga Mboni zobatizidwa za Yehova?
20 Ngati mwachilimika mu ufulu woperekedwa ndi Mulungu mwakukhala Mboni yobatizidwa ya Yehova, iye adzakudalitsani monga momwe anadalitsira atumiki ake kale. Mwachitsanzo, Yehova anadalitsa Abrahamu ndi Sara okalambawo mwakuwapatsa Isake, mwana wowopa Mulungu. Mwachikhulupiriro mneneri Mose anasankha kuchitidwa zoipa ndi anthu a Mulungu ‘kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi; naŵerengera thonzo la [kukhala] Kristu [kapena Wodzozedwa wa Mulungu] chuma choposa zolemera za Aigupto.’ (Ahebri 11:24-26) Mose anali ndi mwaŵi wakugwiritsiridwa ntchito ndi Yehova kutsogolera Aisrayeli kutuluka muukapolo wa Igupto. Ndiponso, chifukwa chakuti anatumikira Mulungu mokhulupirika, iye adzaukitsidwa ndipo adzatumikira monga mmodzi wa “mafumu m’dziko lonse lapansi” pansi pa Mose Wamkulu, Yesu Kristu.—Salmo 45:16; Deuteronomo 18:17-19.
21. Kodi nzitsanzo zolimbikitsa zotani zimene zaperekedwa ponena za akazi opembedza a nthaŵi zakale?
21 Lerolino Akristu odzipatulira akhozanso kulimbikitsidwa mwakulingalira akazi amene anakhala aufuludi ndi achimwemwe. Pakati pawo panali Rute Mmoabu, yemwe anakumana ponse paŵiri ndi kuwawa mtima kwakukhala mkazi wamasiye ndi chimwemwe cha ufulu woperekedwa ndi Mulungu wakumasuka ku chipembedzo chonyenga. Akumasiya anthu ake ndi milungu yake, iye anamamatira kwa apongozi ake amasiye, Naomi. “Kumene mumukako ndimuka inenso,” anatero Rute, “ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Monga mkazi wa Boazi, Rute anakhala amayi wa Obedi, agogo a Davide. (Rute 4:13-17) Eya, Yehova anapatsa mkazi wosakhala Mwiisrayeli wodzichepetsa ameneyu “mphotho yokwanira” mwakumulola kukhala kholo lalikazi la Yesu Mesiyayo! (Rute 2:12) Rute adzasangalala motani nanga pamene adzaukitsidwa ndi kuzindikira kuti anali ndi mwaŵi woterowo! Mosakaikira chisangalalo chofananacho chidzadzaza mitima ya yemwe kale anali mkazi wadama Rahabi, yemwe anamasuka ku chisembwere ndi kulambira konyenga, limodzinso ndi Bateseba wochimwa yemwe analapa, chifukwa nawonso adzazindikira kuti Yehova anawalola kukhala makolo aakazi a Yesu Kristu.—Mateyu 1:1-6, 16.
22. Kodi nchiyani chimene chidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira?
22 Kuŵerengera olandira ufulu woperekedwa ndi Mulungu kungapitirizebe. Mwachitsanzo, chiŵerengero chawo chimaphatikizapo amuna ndi akazi achikhulupiriro otchulidwa mu Ahebri mutu 11. Iwo anazunzidwa ndi kuchitiridwa zoipa, ndipo “dziko lapansi silinayenera iwo.” Wonjezerani ku chiŵerengero chawo otsatira okhulupirika a Kristu a m’zaka za zana loyamba ndi okhulupirika ena kuyambira nthaŵiyo, kuphatikizapo mamiliyoni omwe tsopano akutumikira Yehova monga Mboni zake. Monga momwe tidzawonera, ngati mwachilimika mu ufulu woperekedwa ndi Mulungu, mungakhale ndi zifukwa zambiri zokhalira achimwemwe.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Mulungu anapereka chiyembekezo chotani pamene ufulu woperekedwa ndi Mulungu unataika?
◻ Kodi Kristu anamasula otsatira ake ku ‘goli la ukapolo’ lotani?
◻ Kodi ndimasitepe otani amene amayambirira munthu asanabatizidwe monga mmodzi wa Mboni za Yehova?
◻ Kodi nzitsanzo Zamalemba zotani zimene zimatsimikizira kuti tidzadalitsidwa chifukwa chochilikiza ufulu woperekedwa ndi Mulungu?
[Chithunzi patsamba 16]
Kodi mumawadziŵa masitepe oyambirira munthu asanabatizidwe monga mmodzi wa Mboni za Yehova?