Muziyenda mwa Mzimu Kuti Mukwaniritse Kudzipereka Kwanu
“Pitirizani kuyenda mwa mzimu, ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.”—AGAL. 5:16.
1. Kodi pa Pentekosite mu 33 C.E., panachitika mitundu iwiri iti ya ubatizo?
PA Pentekosite mu 33 C.E., otsatira a Yesu anabatizidwa ndi mzimu woyera ndipo zimenezi zinachititsa kuti alankhule malilime osiyanasiyana. Mozizwitsa anayamba kusonyeza mphatso za mzimu. (1 Akor. 12:4-10) Kodi zotsatira za zimenezi ndiponso nkhani imene Petulo anakamba zinali zotani? Anthu ambiri ‘analasidwa mtima.’ Iwo anatsatira malangizo amene Petulo anawapatsa ndipo analapa machimo awo n’kubatizidwa. Nkhaniyi imati: “Amene analandira mawu akewo ndi mtima wonse anabatizidwa, moti tsiku limenelo anthu pafupifupi 3,000 anawonjezedwa.” (Mac. 2:22, 36-41) Mogwirizana ndi malangizo a Yesu, anthu amenewa anabatizidwa m’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la mzimu woyera.—Mat. 28:19.
2, 3. (a) Kodi kubatizidwa ndi mzimu woyera kumasiyana bwanji ndi kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera? (b) Kuti munthu akhale Mkhristu woona, n’chifukwa chiyani ayenera kubatizidwa m’madzi?
2 Koma kodi kubatizidwa ndi mzimu woyera n’kofanana ndi kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera? Ayi. Anthu amene amabatizidwa ndi mzimu woyera amabadwanso ndipo amakhala ana a Mulungu obadwa ndi mzimu. (Yoh. 3:3) Iwo amadzozedwa kuti adzalamulire kumwamba monga mafumu komanso ansembe mu Ufumu wa Mulungu ndipo amakhala mbali ya thupi lauzimu la Khristu. (1 Akor. 12:13; Agal. 3:27; Chiv. 20:6) Choncho ubatizo umenewu, wobatizidwa ndi mzimu woyera, ndi umene Yehova anabatiza nawo anthu pa tsiku la Pentekosite komanso pambuyo pake, posankha anthu oti akhale olowa m’nyumba anzake a Khristu. (Aroma 8:15-17) Nanga bwanji za anthu amene amabatizidwa m’madzi m’dzina la mzimu woyera pamisonkhano ikuluikulu ya anthu a Yehova masiku ano?
3 Akhristu oona onse amabatizidwa m’madzi posonyeza kudzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova Mulungu. Izi zimachitika kwa anthu amene aitanidwa kupita kumwamba koma n’zofunikanso kwambiri kwa anthu ambirimbiri amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Choncho, kaya munthu ali ndi chiyembekezo chotani, kubatizidwa m’madzi m’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, n’kofunika kwambiri kuti munthuyo akhale paubwenzi ndi Mulungu. Motero Akhristu onse amene abatizidwa amafunika kupitiriza “kuyenda mwa mzimu.” (Werengani Agalatiya 5:16.) Kodi inuyo mukuyenda mwa mzimu n’cholinga chakuti mukwaniritse kudzipereka kwanu?
Kodi “Kuyenda mwa Mzimu” Kumatanthauza Chiyani?
4. Kodi “kuyenda mwa mzimu” kumatanthauza chiyani?
4 “Kuyenda mwa mzimu” kumatanthauza kulola kuti mzimu woyera uzigwira ntchito pa moyo wanu kapena kuti uzikutsogolerani tsiku lililonse. Chaputala 5 cha Agalatiya chimasiyanitsa zochita za munthu amene akutsogoleredwa ndi mzimu woyera, ndi yemwe akungotsatira ntchito za thupi.—Werengani Agalatiya 5:17, 18.
5. Kodi mukamatsogoleredwa ndi mzimu woyera mumapewa ntchito ziti?
5 Mukamatsogoleredwa ndi mzimu woyera mumayesetsa kupewa ntchito za thupi. Zina mwa ntchito zimenezi ndi ‘dama, chonyansa, khalidwe lotayirira, kupembedza mafano, kukhulupirira mizimu, maudani, ndewu, nsanje, kumapsa mtima, mikangano, magawano, magulu a mpatuko, kaduka, kumamwa mwauchidakwa ndiponso maphwando aphokoso.’ (Agal. 5:19-21) Choncho, tingati mzimu woyera umakuthandizani kupha ntchito za thupi. (Aroma 8:5, 13) Umakuthandizaninso kuti muziganizira zinthu za mzimu ndi kulola kuti mzimuwo uzikutsogolerani m’malo momangotsatira zilakolako za thupi.
6. Perekani chitsanzo chosonyeza zimene tiyenera kuchita n’cholinga choti tikhale ndi zipatso za mzimu.
6 Mzimu woyera ukamagwira ntchito pa inu, mumasonyeza makhalidwe abwino omwe ndi “zipatso za mzimu.” (Agal. 5:22, 23) Koma mukudziwanso kuti mufunika kuchita khama kuti izi zitheke. Mwachitsanzo, taganizirani za mlimi amene wakonza munda wake. Popanda kuwala kwa dzuwa ndiponso madzi iye sangakolole chilichonse. Tingayerekezere mzimu woyera ndi kuwala kwa dzuwa. Mzimu woyera ndi wofunika kwambiri kuti tikhale ndi zipatso za mzimuwo. Koma kodi mlimi angakolole kanthu popanda kugwira ntchito mwakhama? (Miy. 10:4) Mofananamo, zimene mumachita pokonza nthaka ya mtima wanu n’zimene zimachititsa kuti mzimu woyera uzigwira ntchito kwambiri pa inu kapena ayi. Choncho, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikulola mzimu woyera kubala zipatso zake mwa kuchita zinthu zothandiza kuti zimenezi zitheke?’
7. Kuti tikhale ndi zipatso za mzimu woyera, kodi n’chifukwa chiyani tifunika kuphunzira ndiponso kusinkhasinkha?
7 Mlimi amafunikanso kuthirira mbewu zake kuti akolole zochuluka. Kuti mukhale ndi zipatso za mzimu mufunika madzi a choonadi cha m’Baibulo amene amapezeka pamisonkhano ya mpingo. (Yes. 55:1) N’zachidziwikire kuti inuyo mwauzapo anthu ena kuti Baibulo ndi louziridwa ndi mzimu woyera. (2 Tim. 3:16) Nayenso kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatithandiza kumvetsa choonadi cha m’Baibulo chomwe chili ngati madzi abwino. (Mat. 24:45-47) Apa n’zoonekeratu kuti mzimu woyera ungatitsogolere pokhapokha ngati tiwerenga Mawu a Mulungu ndi kusinkhasinkha. Ngati mumachita zimenezi, ndiye kuti mukutengera chitsanzo cha aneneri amene ‘anafufuza mwakhama ndi mosamala’ mfundo zimene Mulungu anapereka. N’zochititsa chidwi kuti nawonso angelo amachita chidwi ndi mfundo za choonadi zokhudza Mbewu yolonjezedwa ndiponso zokhudza mpingo wa Akhristu odzozedwa.—Werengani 1 Petulo 1:10-12.
Kodi Tingatani Kuti Mzimu Woyera Uzititsogolera?
8. N’chifukwa chiyani mufunika kupempha Yehova kuti akupatseni mzimu wake?
8 Komatu nkhani si kungowerenga Malemba ndi kuwasinkhasinkha basi. Nthawi zonse mufunika kupempha Yehova kuti akuthandizeni ndi kukutsogolerani. Iye “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20; Luka 11:13) Koma kodi inuyo mungayankhe bwanji wina atakufunsani kuti, “n’chifukwa chiyani ndiyenera kumupempha Mulungu, popeza iye amadziwa ‘zimene ndikufuna ndisanamupemphe n’komwe?’” (Mat. 6:8) Chifukwa china n’chakuti tikamapempha mzimu woyera timasonyeza kuti timadalira Yehova. Mwachitsanzo, munthu wina akakupemphani kanthu mumachita zonse zimene mungathe kuti mum’thandize. Mumachita zimenezo podziwa kuti munthuyo wakupemphani zimenezo chifukwa chokudalirani. (Yerekezerani Miyambo 3:27.) N’chimodzimodzi ndi Yehova. Iye amasangalala kwambiri mukamamupempha mzimu woyera, ndipo angakupatseni.—Miy. 15:8.
9. Kodi kupezeka pamisonkhano kungakuthandizeni bwanji kuti muzitsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu?
9 Monga mukudziwira, mzimu wa Mulungu umatitsogoleranso kudzera m’misonkhano yampingo ndiponso misonkhano ikuluikulu. Kuyesetsa kupezeka pamisonkhano imeneyi ndiponso kumvetsera mwatcheru, n’kofunika kwambiri. Kuchita zimenezi kumakuthandizani kumvetsa “zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:10) Chinthu china chimene chingatithandize, ndi kuyesetsa kuyankha pamisonkhano. Taganizirani za misonkhano imene munapezekapo milungu inayi yapitayi. Kodi n’kangati pamene munakweza dzanja lanu kuti muyankhe posonyeza chikhulupiriro chanu? Kodi pali zinthu zina zimene mukuona kuti mufunika kusintha kuti muzichita bwino pambali imeneyi? Ngati zilipo, ganizirani zimene mungachite milungu ikubwerayi. Yehova adzaona khama lanu ndipo adzakupatsani mzimu woyera umene ungakuthandizeni kuti muzipindula kwambiri mukapezeka pamisonkhano.
10. Kodi kuyenda mwa mzimu kumaphatikizapo kuitana anthu kuti adzatani?
10 Kuyenda mwa mzimu kumaphatikizaponso kuvomera zimene zalembedwa pa Chivumbulutso 22:17. Lembali limati: “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva anene kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.” Mzimu woyera umene ukugwira ntchito kudzera mwa Akhristu odzozedwa, kapena kuti mkwatibwi, ukuitana anthu kuti adzamwe madzi amoyo. Ngati mwavomera poitanidwa kuti “bwera,” kodi nanunso mukufunitsitsa kuuza ena kuti “Bwera!”? Ndi mwayi wamtengo wapatali kugwira nawo ntchito imeneyi yopulumutsa miyoyo.
11, 12. Kodi mzimu woyera ukuthandiza bwanji pa ntchito yolalikira?
11 Ntchito yofunika kwambiri imeneyi ikugwiridwa motsogoleredwa ndi mzimu woyera. Timawerenga mmene mzimu woyera unathandizira amishonale kulalikira m’madera atsopano m’nthawi ya atumwi. ‘Mzimu woyera unaletsa Paulo ndi anzake kulankhula mawu opatulika m’chigawo cha Asiya.’ Iwo sanaloledwenso kupita ku Bituniya. Sitikudziwa mmene mzimuwo unawaletsera kupita kumadera amenewa, koma chomwe tikudziwa n’chakuti mzimuwo unatsogolera Paulo kupita kumadera ambiri a ku Ulaya. Iye anaona m’masomphenya munthu wina wa ku Makedoniya akumupempha kuti akawathandize.—Mac. 16:6-10.
12 Masiku ano, mzimu wa Yehova ukutsogoleranso anthu pa ntchito yolalikira ya padziko lonse. Izi sizichitika mwa masomphenya, koma Yehova amatsogolera odzozedwa kudzera mwa mzimu woyera. Ndipo mzimu woyera umalimbikitsa abale ndi alongo kuchita zonse zimene angathe pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. N’zosachita kufunsa kuti inunso mukugwira nawo ntchito imeneyi. Kodi mungatani kuti muzisangalala kwambiri ndi ntchito yosangalatsa imeneyi?
13. Kodi mungatani kuti mzimu woyera uzikutsogolerani? Perekani chitsanzo.
13 Mungatsatire malangizo a mzimu woyera mwa kugwiritsa ntchito zimene anthu a Mulungu amaphunzitsidwa. Taganizirani zimene zinachitikira mtsikana wa ku Japan dzina lake Mihoko. Atangoyamba kumene upainiya, ankaona kuti sangathe kuchita maulendo obwereza. Iye ankaona kuti sangathe kukopa chidwi cha anthu amene akulankhula nawo. Koma panthawi imeneyi, Utumiki Wathu wa Ufumu unapereka malangizo okhudza mmene tingachitire maulendo obwereza achidule. Ndiye panatulukanso kabuku kakuti Mmene Mungapezere Moyo Wokhutiritsa. Kabuku kameneka kanali kothandiza kwambiri makamaka kwa anthu a ku Japan. Mihoko anagwiritsa ntchito malangizo a mmene angagwiritsire ntchito kabukuka makamaka popanga maulendo obwereza achidule. Pasanapite nthawi anayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu amene poyamba, sakanalola kuphunzira. Iye anati: “Ndinali ndi maphunziro okwana 12 moti ena ankafunika kudikira kaye ndisanayambe kuphunzira nawo.” Zoonadi, ngati mukuyenda mwa mzimu ndiponso kugwiritsa ntchito malangizo amene Yehova amapereka kwa atumiki ake, mudzapindula kwambiri.
Muzidalira Mzimu wa Mulungu
14, 15. (a) N’chiyani chingathandize anthu opanda ungwiro kukwaniritsa kudzipereka kwawo? (b) Kodi mungatani kuti mukhale ndi mabwenzi abwino?
14 Popeza ndinu mtumiki woikidwa, muli ndi ntchito yoti mugwire. (Aroma 10:14) Mwina mungamaone kuti si inu oyenerera kugwira ntchito imeneyi. Koma mofanana ndi odzozedwa, Mulungu ndi amene amakuchititsani kukhala oyenerera. (Werengani 2 Akorinto 3:5.) Mukhoza kukwaniritsa kudzipereka kwanu mwa kuchita khama ndiponso kudalira mzimu wa Mulungu.
15 N’zoona kuti n’zovuta kwa anthu opanda ungwirofe kukwaniritsa kudzipereka kwathu kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi wangwiro. Vuto lina ndi lakuti anthu amene tinkacheza nawo poyamba sangasangalale ndi zimene tikuchita panopa ndipo ‘angamatinyoze.’ (1 Pet. 4:4) Koma musaiwale kuti panopa muli ndi mabwenzi ambiri kuphatikizapo Yehova ndi Yesu Khristu omwe ndi mabwenzi amtengo wapatali kwambiri. (Werengani Yakobe 2:21-23.) Ndiponso mufunika kumadziwa abale ndi alongo a mumpingo mwanu. Abale ndi alongo amenewa ali ‘m’gulu lonse la abale’ a padziko lonse. (1 Pet. 2:17; Miy. 17:17) Yehova adzakuthandizani kudzera mwa mzimu wake, kuti mukhale ndi mabwenzi amene nthawi zonse adzakuthandizani kuti muzichita zoyenera.
16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘mungamasangalale ndi kufooka’ ngati mmene Paulo anachitira?
16 Ngakhale mutakhala ndi mabwenzi ambiri mumpingo, zikhoza kukhalabe zovuta kuti mupirire mavuto ena. Nthawi zina chifukwa cha mavuto, mungamve ngati muli m’dzenje lomwe simungathe kutulukamo. Nthawi imeneyi ndi imene muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndili wamphamvu.” (Werengani 2 Akorinto 4:7-10; 12:10.) Paulo ankadziwa kuti mzimu wa Mulungu ungathandize pa vuto lina lililonse limene munthu angakhale nalo. Mzimu woyera wa Mulungu ungakulimbitseni pamene mwafooka ndiponso pamene mukufunikira thandizo. Paulo analemba kuti: “Ndimasangalala ndi kufooka.” Iye ankaona kuti akafooka, mzimu woyera unkamuthandiza. Zimenezi zingachitikenso kwa inu.—Aroma 15:13.
17. Kodi mzimu woyera ungakuthandizeni bwanji kukwaniritsa cholinga chanu?
17 Kuti tikwaniritse kudzipereka kwathu kwa Mulungu, timafunika mzimu wake. Tiyerekeze kuti inuyo muli ndi boti loyendera mphepo. Chofunika ndi kudziwa mphepo imene ingakufikitseni kumene mukupita n’kulola kuti ikutsogolereni. Cholinga chanu ndi kutumikira Yehova kosatha. Mzimu woyera uli ngati mphepo imene ingakakufikitseni bwinobwino kumene mukupita. Simungafune kuti muzingotengekera uku ndi uko ndi mzimu wa dziko la Satanali. (1 Akor. 2:12). Mzimu woyera ungakutsogolereni bwino kudzera m’Mawu a Mulungu ndiponso gulu lake lotsogoleredwa ndi mzimuwo.
18. Kodi muyenera kuyesetsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
18 Ngati mwakhala mukuphunzira ndi Mboni za Yehova ndiponso kusonkhana nazo koma simunadziperekebe n’kubatizidwa, dzifunseni kuti, ‘kodi chikundilepheretsa n’chiyani?’ Ngati mwazindikira ntchito ya mzimu woyera pokwaniritsa cholinga cha Yehova masiku ano, ndiponso mmene umagwirira ntchito, chitani zimene mwaphunzira kuti n’zoyenera kuchita. Yehova adzakudalitsani kwambiri. Iye adzakupatsani mzimu wake woyera mowolowa manja. Ngati munabatizidwa kalekale, muyenera kuti mwaona mzimu woyera ukukuthandizani. Mwaonanso Mulungu akukulimbikitsani pogwiritsa ntchito mzimu wake. Iye angapitirizebe kuchita zimenezi mpaka kalekale. Motero, yesetsani kuyendabe mwa mzimu woyera.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi “kuyenda mwa mzimu” kumatanthauza chiyani?
• N’chiyani chingakuthandizeni kuti mupitirizebe “kuyenda mwa mzimu”?
• Kodi mungatani kuti mukwaniritse kudzipereka kwanu kwa Mulungu?
[Chithunzi patsamba 15]
M’pofunika khama kuti mukonze nthaka ya mtima wanu
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Kodi mzimu wa Mulungu ukukutsogolerani?