Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi munthu angachotsedwe mumpingo wachikristu chifukwa chochita chidetso monga momwe zingakhalire atachita dama kapena khalidwe lotayirira?
Inde, munthu angathe kuchotsedwa mumpingo ngati ali wadama, kapena ngati amachita zodetsa ku mlingo winawake, kapenanso ngati ndi wakhalidwe lotayirira, ndipo sakulapa. Mtumwi Paulo anatchula machimo onse atatuwa limodzi ndi machimo ena amene munthu angachotsedwere mumpingo, pamene analemba kuti: “Ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa [kapena kuti khalidwe lotayirira] . . . ndikuchenjezani nazo . . . kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”—Agalatiya 5:19-21.
Dama (m’Chigiriki, por·neiʹa) ndilo makhalidwe oipa achiwerewere ochitika kunja kwaukwati wovomerezeka m’Malemba. Limaphatikizapo chigololo, uhule, ndi kugonana pakati pa anthu osakwatirana ndiponso kugonana m’kamwa ndi kumatako komanso kuseweretsa mpheto za munthu wina yemwe si mwamuna kapena mkazi wako. Munthu amene amachita za dama popanda kulapa sakhala mumpingo wachikristu.
Khalidwe lotayirira (m’Chigiriki, a·selʹgei·a) limatanthauza “kutayirira; kufuna chisangalalo chogonana nthawi zonse; khalidwe lopanda manyazi; khalidwe lonyansa.” Buku la The New Thayer’s Greek-English Lexicon limati mawu a Chigirikiwa amatanthauza “chilakolako chosaletseka, . . . khalidwe lolakwika kwambiri, kupanda manyazi, mwano.” Malinga ndi zomwe linanena buku linanso lotanthauzira mawu, khalidwe lotayirira ndi khalidwe “losalemekeza chikhalidwe cha anthu m’pang’ono pomwe.”
Monga momwe taonera m’matanthauzowa, “khalidwe lotayirira” limaphatikizapo mbali ziwiri: (1) Khalidweli limaphwanya kwambiri malamulo a Mulungu; ndipo (2) munthu wolakwayo n’ngopanda ulemu, wamwano.
Motero, “khalidwe lotayirira” si kungoipa makhalidwe pang’ono ayi. Koma ndi zochita za munthu zosweratu malamulo a Mulungu, zimene zimasonyeza kuti munthuyo n’ngopanda manyazi, kapena zosonyeza kusalemekeza ngakhalenso kunyoza ulamuliro ndiponso malamulo. Paulo anaika chonyansa, kapena kuti khalidwe lotayirira, m’gulu limodzi ndi chigololo chonyansa. (Aroma 13:13, 14) Popeza kuti lemba la Agalatiya 5:19-21 limatchula khalidwe lotayirira limodzi ndi machimo ena omwe angalepheretse munthu kulowa Ufumu wa Mulungu, munthu angathe kudzudzulidwa ndipo mwinanso kuchotsedwa kumene mumpingo wachikristu chifukwa cha khalidweli.
Chidetso (m’Chigiriki, a·ka·thar·siʹa) chimasiyana ndi “dama,” ndiponso “khalidwe lotayirira,” chifukwa chakuti chimaphatikizapo zambiri. Chimaphatikizapo kudetsedwa mwamtundu uliwonse, monga pankhani za kugonana, pa kalankhulidwe, m’zochita, ndiponso pa zinthu zauzimu. Mawu akuti ‘chidetso’ amakhudza machimo akuluakulu osiyanasiyana.
Malinga ndi mawu a pa 2 Akorinto 12:21, Paulo ananena za anthu omwe “adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo [dama], ndi kukhumba zonyansa [khalidwe lotayirira] zimene anachita.” Popeza kuti ‘chidetso’ chikutchulidwa pamodzi ndi “dama ndi khalidwe lotayirira,” mitundu ina ya chidetso ingachititse kuti papangidwe komiti ya chiweruzo. Koma mawu akuti chidetso amatanthauza zambiri kuphatikizapo zina zimene sizingafunike komiti ya chiweruzo. Monga momwe nyumba ingakhalire yakuda kapena yauve kwambiri, khalidwe la chidetso limachitika ku mlingo wosiyanasiyana.
Mogwirizana ndi lemba la Aefeso 4:19, Paulo ananena kuti anthu ena ‘sanazindikirenso kanthu’ kapena kuti anali opandiratu khalidwe ndipo “anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa [akhale akhalidwe lotayirira], kuti achite chidetso chonse mu umbombo.” Motero, Paulo anaika kuchita “chidetso . . . mu umbombo” m’gulu limodzi ndi khalidwe lotayirira. Ngati munthu wobatizidwa amachita za “chidetso . . . mu umbombo” popanda kulapa, angachotsedwe mumpingo chifukwa cha chidetso choipitsitsa.
Tiyerekeze kuti anthu awiri otomerana anali kugwiranagwirana kwambiri nthawi zambiri. Akulu angaone kuti ngakhale kuti anthuwo sanasonyeze mzimu wopanda manyazi, n’kuchita zinthu motayirira, anthuwo anasonyeza khalidwe la umbombo. Motero iwo angasankhe komiti ya chiweruzo chifukwa chakuti anthuwo achita chidetso choipitsitsa. Chidetso choipitsitsa chingakhalenso maziko oyenera osamalirira mlandu wa wofalitsa yemwe amakambirana nthawi zambiri ndi munthu wina pafoni, nkhani zolaula zokhudza kugonana makamaka ngati munthuyo anapatsidwapo uphungu pankhaniyo.
Akulu amafunika kukhala ozindikira posamalira nkhani zotere. Kuti adziwe ngati m’pofunika komiti ya chiweruzo, iwo afunika kupenda mosamala zinthu zimene zinachitika ndiponso kuti zinachitika mpaka pati. Sikuti aliyense amene sakulabadira uphungu wa m’Malemba ndiye kuti ndi wakhalidwe lotayirira ayi; ndiponso si nkhani yofuna kungowerengetsera kuti munthu wachita zimenezi kangati ndiyeno n’kupanga komiti ya chiweruzo. Akulu ayenera kupenda mosamala chochitika chilichonse, n’kupempherera nkhaniyo ndi kufufuza chimene chinachitika, kuwirikiza kwake, kukula ndiponso mtundu wa khalidwe loipalo, komanso cholinga cha munthu wolakwayo.
Sikuti chidetso choipitsitsa chimangokhala pa machimo okhudza kugonana okha. Mwachitsanzo, mnyamata wobatizidwa wa pasukulu angasute ndudu zingapo panthawi yochepa n’kukaulula zimenezi kwa makolo ake. Mnyamatayo watsimikiza kuti sadzasutanso. Khalidweli ndi chidetso, koma silinafike pokhala chidetso choipitsitsa kapena kuti “chidetso . . . mu umbombo.” Uphungu wa m’Malemba woperekedwa ndi mkulu mmodzi kapena akulu awiri, limodzi ndi thandizo la makolo a mwanayo zingakhale zokwanira. Koma ngati mwanayo amasuta fodya mowirikiza, kuchita zimenezi kungakhale kudetsa thupi mwadala, ndipo payenera kupangidwa komiti ya chiweruzo kuti isamalire nkhani ya chidetso choipitsitsayi. (2 Akorinto 7:1) Ngati mnyamatayo sanalape, angachotsedwe mumpingo.
Akristu ena akhala akuonerera zinthu zolaula. Mulungu amaona kuti izi ndi zoipa, ndipo akulu angadabwe kumva kuti wokhulupirira mnzawo wachita zimenezi. Koma sikuti kuonerera zolaula konse kungakhale maziko opangira komiti ya chiweruzo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mbale waonererapo maulendo angapo zinthu zolaula, zimene amati sizoipa kwenikweni. Chifukwa chodzimvera chisoni, waulula kwa mkulu, ndipo watsimikiza kuti sadzabwerezanso tchimo limeneli. Mkuluyo angaone kuti khalidwe la mbaleyo silinafike poti wachita “chidetso . . . mu umbombo”; ndiponso sanasonyeze mzimu wopanda manyazi, n’kusonyeza kuti ndi wakhalidwe lotayirira ayi. Ngakhale kuti sipangafunikire kupanga komiti ya chiweruzo, chidetso chamtunduwu chingafunike uphungu wamphamvu wa m’Malemba ndipo mwinanso akulu angafunike kupitiriza kum’thandiza.
Koma tiyerekeze kuti Mkristu wina wakhala akuonerera mwamseri kwa zaka zambiri zinthu zolaula zoipa kwambiri komanso zosalemekeza kugonana ndipo wakhala akuyesetsa kubisa tchimo limeneli. Mwa zinthu zolaulazo, mwina pamakhala anthu angapo akugwirira munthu mmodzi, anthu atamangirira anzawo, anthu akuzunza anzawo ndiponso kuchitira nkhanza amayi, mwinanso zithunzi zolaula zosonyeza munthu akugona ana aang’ono. Anthu ena atazindikira khalidwe lakeli, Mkristuyo akumva chisoni kwambiri. Iye sanasonyeze mzimu wopanda manyazi, koma akulu angaone kuti ‘wadzipereka yekha,’ kuchita khalidwe lauveli, ndipo wakhala akuchita ‘chidetso mu umbombo,’ chimene ndi chidetso choipitsitsa. Komiti ya chiweruzo iyenera kupangidwa pa mlandu wa chidetso choipitsitsa. Ngati wolakwayo sasonyeza kulapa komwe Mulungu amafuna, ndipo sakuonetsa mtima wofuna kusiya chizolowezi choonerera zithunzi zolaula, ayenera kuchotsedwa mumpingo. Ngati anali kuitanira ena kunyumba kwake kuti akaonerere zithunzi zolaula, komwe kunali kulimbikitsa khalidwe limeneli, iye angakhale akusonyeza umboni wakuti ali ndi mzimu wopanda manyazi umene munthu wakhalidwe lotayirira amakhala nawo.
M’Malemba, mawu akuti “khalidwe lotayirira” nthawi zonse amakhala akunena za tchimo lalikulu, ndipo nthawi zambiri tchimo lokhudza kugonana. Pofuna kuzindikira khalidwe lotayirira, akulu afunika kuona ngati munthuyo ali ndi mzimu wopanda manyazi, khalidwe lofuna chisangalalo cha kugonana nthawi zonse, lauve, lochititsa manyazi ndiponso lodabwitsa anthu kwambiri. Koma kuswa kwambiri malamulo a Yehova kwa munthu amene sasonyeza mzimu wopanda manyazi kungakhudzane ndi “umbombo.” Popeza nkhani zotere zimaphatikizapo chidetso choipitsitsa, ziyenera kusamaliridwa pa maziko a chidetso choipitsitsa.
Kuona ngati munthu wachita mlandu wa chidetso choipitsitsa kapena khalidwe lotayirira ndi udindo waukulu kwambiri, chifukwa chakuti zimakhudza moyo wa anthu. Amene akuweruza milandu yotero afunika kupemphera kwa Mulungu, kum’pempha nzeru yowathandiza kuzindikira, kumvetsa, ndiponso kumupempha mzimu wake woyera. Akulu afunika kusungitsa chiyero mumpingo ndi kuweruza mogwirizana ndi Mawu a Mulungu komanso malangizo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 18:18; 24:45) Ndipo m’masiku oipa ano, kusiyana ndi kale lonseli, akulu akufunika kukumbukira mawu akuti: “Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova.”—2 Mbiri 19:6.