Kukulitsa Umunthu Watsopano mu Ukwati
“Muyenera kupangidwa kukhala atsopano mwamphamvu yosonkhezera maganizo anu, ndipo muyenera kuvala umunthu watsopano.”—AEFESO 4:23, 24, NW.
1. Kodi nchifukwa ninji ukwati suyenera kuwonedwa mopepuka?
UKWATI ndi chimodzi cha zinthu zazikulu koposa zimene munthu amachita m’moyo, chotero suyenera kutengedwa mopepuka konse. Nchifukwa ninji ziri choncho? Chifukwa chakuti umafunikiritsa pangano la moyo wonse kwa munthu winayo. Umatanthauza kugawana moyo wathunthu ndi munthu ameneyo. Chosankha chauchikulire nchofunika ngati panganolo liti likhale lokhalitsa. Kumafunikiritsanso chisonkhezero chotsimikizirika ‘chosonkhezera maganizo ndipo chotero kuumba umunthu watsopano.’—Aefeso 4:23, 24; yerekezerani ndi Genesis 24:10-58; Mateyu 19:5, 6.
2, 3. (a) Kodi chofunika nchiyani kusankha mnzanu wamuukwati mwanzeru? (b) Kodi chophatikizidwa mu ukwati nchiyani?
2 Pali chifukwa chabwino chakusafulumirira kuloŵa mu ukwati, kugonjetsedwa msanga ndi chikhumbo champhamvu chakuthupi. Pamafunikira nthaŵi kufikira umunthu wachikulire ndi makhalidwe. Chidziŵitso ndi nzeru zimene zingatumikire monga maziko akulingalira kolama zimafunikiranso nthaŵi. Pamenepo, kusankha mnzanu wamuukwati woyenerana naye wamoyo wonse kungakhale ndi chipambano chokulirapo. Mwambi Wachispanya umanena momvekera bwino kuti: “Nkwabwinopo kuyenda uli mbeta koposa kukwatira moipa.”—Miyambo 21:9; Mlaliki 5:2.
3 Kusankha mnzanu woyenerera mwachiwonekere kuli chofunika chachikulu ku ukwati wachipambano. Kuti zitero Mkristuyo ayenera kugwiritsira ntchito ndi kutsatira malangizo a Baibulo, mosatsogozedwa ndi kukongola kokha kwakuthupi ndi kutengeka maganizo kosayenerera ndi zitsenderezo za chikondi cha mwamuna ndi mkazi. Ukwati umatanthauza zambiri kuposa kugwirizanitsa matupi aŵiri. Ndiwo kugwirizanitsa pamodzi maumunthu aŵiri, mikhalidwe iŵiri ya mabanja ndi yamaphunziro, mwinamwake miyambo iŵiri ndi zinenero ziŵiri. Kugwirizanitsidwa kwa anthu aŵiri mu ukwati ndithudi kumatanthauza kugwiritsira ntchito bwino lilime; ndi mphamvu yakulankhula, timapasula kapena kumanga. Mwazonsezi, timawonanso nzeru ya uphungu wa Paulo ya ‘kukwatira kokha mwa ambuye,’ ndiko kuti, wokhulupirira mnzathu.—1 Akorinto 7:39; Genesis 24:1-4; Miyambo 12:18; 16:24.
Kuyang’anizana ndi Zipsinjo Zaukwati
4. Kodi nchifukwa ninji nthaŵi zina kusagwirizana ndi chipsinjo zimabuka mu ukwati?
4 Ngakhale patakhala maziko abwino, padzakhalabe nthaŵi zakusemphana, zachitsenderezo, ndi zakupsinjika. Zimenezi nzachibadwa kwa munthu aliyense, kaya ngwokwatira kapena wosakwatira. Mavuto achuma ndi athanzi angachititse chipsinjo mu unansi uliwonse. Kusintha kwa makhalidwe kungachititse kuwombana kwa maumunthu m’maukwati abwino koposa. Mfundo ina njakuti palibe ngakhale mmodzi amene amalamulira kotheratu lirime, monga momwe Yakobo anafotokozera kuti: ‘Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse. . . . Lilimenso liri chiŵalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Tawonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!’—Yakobo 3:2, 5.
5, 6. (a) Kodi chofunika nchiyani pamene kusamvetsetsana kubuka? (b) Kodi nchiyani chingafunikire kuchitidwa kuthetsa vuto?
5 Pamene zitsenderezo zibuka muukwati, kodi tingalamulire motani mkhalidwewo? Kodi tingatetezere motani kuti zophophonya zisakule kukhala kulongolola kumenenso kungatsogolere m’kusweka kwaukwatiwo? Apa ndipo pamene mphamvu yosonkhezera maganizo imagwira ntchito. Mzimu wosonkhezera umenewu ungakhale kaya wothandiza kapena wotsutsa, wolimbikitsa ndi wachisonkhezero chauzimu kapena woluluza, wolamulidwa ndi zikhoterero zathupi. Ngati uli wolimbikitsa, munthuyo adzachitapo kanthu kuchiritsa m’ng’aluwo kuti asunge ukwati wake ukuyenda bwino. Mikangano ndi kusavomerezana siziyenera kuthetsa ukwati. Kusamvana kungathetsedwe ndipo kulemekezana ndi kugwirizana kungabwezeretsedwe mwakugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo.—Aroma 14:19; Aefeso 4:23, 26, 27.
6 M’mikhalidwe imeneyi mawu a Paulo ngoyenerera kwambiri akutiwo: “Chifukwa cha chimenecho, monga osankhidwa a Mulungu, oyera ndi okondedwa, dzivekeni mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa maganizo, kudekha, kuleza mtima. Pitirizanibe kupirirana ndi kukhululukirana mwaufulu ngati aliyense ali ndi chifukwa chodandaulira ndi wina. Monga momwenso Yehova mwaufulu anakukhululukirani, teroni inunso. Koma, kuphatikiza pa zinthu zonsezi, dzivekeni chikondi, pakuti icho ndicho chomangira changwiro chachigwirizano.”—Akolose 3:12-14, NW.
7. Kodi ndivuto lotani limene ena angakhale nalo mu ukwati wawo?
7 Lembalo nlosavuta kuŵerenga, koma chifukwa cha zopsinja za moyo wamakono, siliri nthaŵi zonse losavuta kuligwiritsira ntchito. Kodi nchiyani chingakhale vuto lalikulu? Nthaŵi zina, mosakuzindikira, Mkristu angakhale ndi moyo wa miyezo iŵiri. Pa Nyumba Yaufumu, amakhala pakati pa abale, ndipo amachita mokoma mtima ndi mwachifundo. Ndiyeno, atabwerera kunyumba, m’zochitika za pabanja, angakhale wokhoterera kukuiŵala unansi wake wauzimu. Kumeneko amangokhala chabe mwamuna ndi mkazi, “mwamunayo” ndi “mkaziyo.” Ndipo atapanikizika mwamunayo (kapena mkazi) angafikire pakulankhula mawu ankhalwe amene sakananenedwa konse pa Nyumba Yaufumu. Kodi chachitika nchiyani? Kwakanthaŵi, umunthu wake Wachikristu wazimiririka. Mtumiki wa Mulungu waiŵala kuti iye adakali mbale kapena mlongo Wachikristu pa nyumba. Mphamvu yosonkhezera maganizo yakhala yotsutsa mmalo mwa kusonkhezera.—Yakobo 1:22-25.
8. Kodi chingatulukepo nchiyani pamene mphamvu yosonkhezera maganizo iri yotsutsa?
8 Kodi chotulukapo nchiyani? Mwamunayo angasiye ‘kukhala ndi mkazi wake mogwirizana ndi chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.’ Mkaziyo angakhale asakuperekanso ulemu kwa mwamuna wake; “mzimu wofatsa ndi wachete” wakewo wataika. Mphamvu yosonkhezera maganizo yakhala yakuthupi mmalo mwakukhala yauzimu. “Kaimidwe ka maganizo kakuthupi” katenga malo. Chotero, kodi chingachitidwe nchiyani kupangitsa mphamvu yosonkhezera kukhala yauzimu ndi yabwino? Tiyenera kulimbitsa mkhalidwe wathu wauzimu.—1 Petro 3:1-4, 7; Akolose 2:18.
Limbitsani Mphamvuyo
9. Kodi ndizosankha zotani zimene tiyenera kupanga m’moyo wa tsiku ndi tsiku?
9 Mphamvu yosonkhezera ndiyo chikhoterero cha maganizo chimene chimagwira ntchito pamene tifunikira kugamula ndi kupanga zosankha. Moyo umapereka mpambo wosalekeza wa zosankha—zabwino kapena zoipa, zadyera kapena zopanda dyera, zamakhalidwe abwino kapena oipa. Kodi chidzatithandiza kupanga zosankha zolungama nchiyani? Mphamvu yosonkhezera maganizo ngati iri yosumikidwa pa kuchita chifuniro cha Yehova. Wamasalmo anapemphera kuti: ‘Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; ndidzaisunga kufikira kutha kwake.’—Salmo 119:33; Ezekieli 18:31; Aroma 12:2.
10. Kodi tingalimbitse motani mwanjira yabwino mphamvu yosonkhezera maganizo?
10 Unansi wamphamvu ndi Yehova udzatithandiza kumkondweretsa ndi kupatuka pa choipa, kuphatikizapo kusakhulupirika mu ukwati. Israyeli analimbikitsidwa ‘kuchita zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wawo.’ Koma Mulungu anaperekanso uphungu wakuti: ‘Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.’ Mogwirizana ndi lamulo lachisanu ndi chiŵiri la Malamulo Khumi lakuti: ‘Usachite chigololo,’ Aisrayeli anafunikira kuda chigololo. Lamulo limenelo linasonyeza lingaliro lamphamvu la Mulungu la kukhulupirika mu ukwati.—Deuteronomo 12:28; Salmo 97:10; Eksodo 20:14; Levitiko 20:10.
11. Kodi tingalimbikitse mowonjezera chotani mphamvu yosonkhezera maganizo athu?
11 Kodi ndimotani mmene tingalimbitsire mowonjezereka mphamvu imene imasonkhezera maganizo? Mwakuyamikira ntchito zauzimu ndi makhalidwe abwino. Zimenezo zitanthauza kuti tiyenera kukwaniritsa chofunika cha kuphunzira Mawu a Mulungu mokhazikika ndipo tiyenera kuphunzira kusangalala ndi kukambitsirana pamodzi ziganizo za Yehova ndi uphungu wake. Maganizo athu ochokera pansi pa mtima ayenera kukhala ofanana ndi a wamasalmo: ‘Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nawo malamulo anu. Ndinawabisa mawu anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire inu. Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; ndidzaisunga kufikira kutha kwake. Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.’—Salmo 119:10, 11, 33, 34.
12. Kodi ndizinthu ziti zimene zingagwirizanitse m’kusonyeza maganizo onga a Kristu?
12 Mtundu wachiyamikiro cha makhalidwe abwino olungama a Yehova umenewu umasungidwa osati kokha mwakuphunzira Baibulo komanso mwakukhala ndi phande nthaŵi zonse m’misonkhano Yachikristu ndi kukhala ndi phande mu uminisitala Wachikristu pamodzi. Zisonkhezero zamphamvu ziŵiri zimenezi zingalimbitse mosalekeza mphamvu yosonkhezera maganizo athu kotero kuti nthaŵi zonse njira yathu ya moyo yopanda dyera isonyeze maganizo onga a Kristu.—Aroma 15:5; 1 Akorinto 2:16.
13. (a) Kodi nchifukwa ninji pemphero liri chinthu chofunika m’kulimbitsa mphamvu yosonkhezera maganizo? (b) Kodi nchitsanzo chotani chimene Yesu anapereka pa mfundoyi?
13 Mfundo ina ndiyo imene Paulo akugogomezera m’kalata yake kwa Aefeso: ‘Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthaŵi yonse mwa mzimu.’ (Aefeso 6:18) Amuna ndi akazi awo afunikira kupempherera pamodzi. Kaŵirikaŵiri mapemphero otero amatsegula mtima ndipo amatsogolera kukukambitsirana zakukhosi kumene kumakonza ming’alu iriyonse. M’nthaŵi za mayesero ndi chiyeso, tifunikira kutembenukira kwa Mulungu m’pemphero, tikumapempha chithandizo, cha nyonga yauzimu kuti tichite mogwirizana ndi maganizo a Kristu. Ngakhale Yesu wangwiroyo anatembenukira kwa Atate wake m’pemphero pa nthaŵi zambiri, akumapempha nyonga. Mapemphero ake anali ochokera pansi pa mtima ndi amphamvu. Mofananamo lerolino, m’nthaŵi za chiyeso, tingapeze nyonga yakupanga chosankha cholungama mwakuitanira pa Yehova kutithandiza kukaniza chilakolako chakugonjera thupi ndi kusakhulupirika ku choŵinda chaukwati.—Salmo 119:101, 102.
Zitsanzo Zosiyana Zakudzisungira
14, 15. (a) Kodi Yosefe anachita motani poyesedwa? (b) Kodi chinathandiza Yosefe nchiyani kukaniza chiyesocho?
14 Kodi tingalimbane motani ndi chiyeso? Pamfundo ino tiri ndi kusiyana kwakukulu pakati pa njira yotengedwa ndi Yosefe ndi Davide. Pamene mkazi wa Potifara mwaliuma anayesa kunyenga Yosefe wokongolayo, amene mwachiwonekere anali wosakwatira panthaŵiyo, potsirizira pake anamuyankha mwakumati: ‘Mulibe wina m’nyumba wamkulu ndine; ndipo [mwamuna wanu] sanandikaniza ine kanthu, koma inu, chifukwa kuti muli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?’—Genesis 39:6-9.
15 Kodi chinathandiza Yosefe kutenga njira yolungama pamene kukanakhala kosavuta kugonjera nchiyani? Iye anali ndi mphamvu yosonkhezera maganizo ake. Anali kuzindikira kwambiri unansi wake ndi Yehova. Anadziŵa kuti kuchita dama ndi mkazi wa chiwerewere ameneyu kukanakhaladi tchimo osati kokha kuchimwira mwamuna wa mkaziyo, koma kwakukulukulu kuchimwira Mulungu.—Genesis 39:12.
16. Kodi Davide anachita motani poyesedwa?
16 Mosiyana, kodi chinachitika kwa Davide nchiyani? Iye anali mwamuna wokwatira, wokhala ndi akazi angapo monga analoledwera ndi Chilamulo. Madzulo ena anali kuyang’ana ali panyumba yake yachifumu mkazi wina akusamba. Anali Bateseba wokongolayo, mkazi wa Uriya. Mwachiwonekere Davide anali ndi chosankha—kupitirizabe kuyang’anitsitsa pamene chilakolako choipa chinali kukula mumtima mwake kapena kutembenuka ndi kukaniza chiyesocho. Kodi anasankha kuchita chiyani? Iye anamuitanitsa kudza kunyumba yake yachifumu, ndipo anachita naye chigololo. Zoipirapodi, iye anachititsa imfa ya mwamuna wake.—2 Samueli 11:2-4, 12-27.
17. Kodi tingazindikirenji ponena za mkhalidwe wauzimu wa Davide?
17 Kodi vuto la Davide linali chiyani? Kuchokera m’kulapa kwake komva chisoni kwa pambuyo pake kwa mu Salmo 51, tingathe kuzindikira maumboni ena. Iye anati: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika mkati mwanga.” Kuli kwachiwonekere kuti panthaŵi ya chiyeso chake, analibe mzimu wangwiro ndi wokhazikika. Mwinamwake anali atanyalanyaza kuŵerenga kwake Chilamulo cha Yehova, ndipo monga chotulukapo, mkhalidwe wake wauzimu unafooka. Kapena angakhale atalola malo ake antchito ndi ulamuliro monga mfumu kuipitsa maganizo ake kotero kuti anakhala mkhole wachilakolako choluluza. Ndithudi, mphamvu yosonkhezera maganizo ake panthaŵiyo inali yadyera ndi yauchimo. Chotero, iye anazindikira kufunikira kwake kwa ‘mzimu watsopano, wokhazikika.’—Salmo 51:10; Deuteronomo 17:18-20.
18. Kodi ndiuphungu wotani umene Yesu anapereka wonena za kuchita chigololo?
18 Maukwati ena Achikristu asweka chifukwa chakuti mmodzi kapena onse aŵiri okwatiranawo alola kugwera mumkhalidwe wakufooka mwauzimu wofanana ndi wa Mfumu Davide. Chitsanzo chake chiyenera kutichenjeza kusapitirizabe kuyang’anitsitsa mkazi, kapena mwamuna, mwachilakolako, pakuti potsirizira pake chigololo chingatulukepo. Yesu anasonyeza kuti anazindikira maganizo a munthu pa mfundoyi, pakuti anati: ‘Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.’ M’chochitika chotere, mphamvu yosonkhezera maganizo iri yadyera ndi yathupi, siyauzimu ayi. Pamenepa, kodi Akristu akachitanji kupeŵa kuchita chigololo ndi kusunga maukwati awo ali achimwemwe ndi okhutiritsa?—Mateyu 5:27, 28.
Limbitsani Zomangira Zaukwati
19. Kodi ukwati ungalimbitsidwe motani?
19 Mfumu Solomo analemba kuti: ‘Ndipo wina akalaka mmodziyo, aŵiri adzachirimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.’ Ndithudi, aŵiri muukwati wogwirizana angaimirire pamodzi mu nsautso koposa mmodzi. Koma ngati chomangira chawo chiri chofanana ndi chingwe cha nkhosi zitatu kukhala ndi Mulungu mkati mwake, ukwatiwo udzakhala wolimba. Ndipo kodi Mulungu angakhale motani mu ukwati? Mwakugwiritsira ntchito kwa aŵiri okwatiranawo malamulo ake amakhalidwe abwino ndi uphungu wake waukwati.—Mlaliki 4:12.
20. Kodi ndiuphungu wa Baibulo wotani umene ungathandize mwamuna?
20 Ndithudi, ngati mwamuna agwiritsira ntchito uphungu wa malemba otsatira, ukwati wake udzakhala ndi maziko abwinopo achipambano:
‘Amuna inu, khalani nawo monga mwachidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.’—1 Petro 3:7.
‘Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha mmalo mwake; koteronso amuna adzikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha.’—Aefeso 5:25, 28.
‘Mwamuna wake namtama, nati, ana aakazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo.’—Miyambo 31:28, 29.
‘Kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake? Chomwecho woloŵa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango. Wochita chigololo . . . akuwononga moyo wake.’—Miyambo 6:28, 29, 32.
21. Kodi ndiuphungu wa Baibulo wotani umene ungathandize mkazi?
21 Ngati mkazi asamala ziphunzitso za Baibulo zotsatirazi, zidzathandiza ukwati wake kukhalitsa:
“Akazi inu, khalani ogonjera kwa amuna a inu eni, mmalo mwakuti, ngati ena ali osamvera mawu, iwo akapindulidwe popanda liwu kupyolera mwa khalidwe la akazi awo, chifukwa chakukhala atakhala mboni zowona ndi maso za khalidwe lanu loyera limodzi ndi ulemu waukulu [ndi la] mzimu wanu wachete ndi wodekha.”—1 Petro 3:1-4, NW.
“Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake [akugonana]; koma chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna . . . Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwanthaŵi.”—1 Akorinto 7:3-5.
22. (a) Kodi ndimikhalidwe ina iti imene ingayambukire ukwati mopindulitsa? (b) Kodi Yehova amawona bwanji chisudzulo?
22 Baibulo limasonyezanso kuti chikondi, kukoma mtima, chifundo, kuleza mtima, kuzindikira, chilimbikitso, ndi kutamanda ndizo mbali zina zofunika za ngaleyo ukwati. Ukwati wopanda mbalizi ngwofanana ndi chomera chosalandira kuŵala kwa dzuŵa ndi madzi—sichimakula. Chotero mphamvu yosonkhezera maganizo athu itisonkhezeretu kuti tilimbikitsane ndi kutsitsimulana mu ukwati wathu. Kumbukirani kuti Yehova ‘amada chisudzulo.’ Ngati chikondi cha Mkristu chikusonyezedwa, sipayenera kukhala kuthekera kwa kuchita chigololo ndi kusweka kwaukwati. Chifukwa ninji? ‘Chifukwa chakuti chikondi sichimalephera konse.’—Malaki 2:16; 1 Akorinto 13:4-8; Aefeso 5:3-5.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi chofunika chachikulu nchiyani chopezera ukwati wachimwemwe?
◻ Kodi mphamvu yosonkhezera maganizo ingayambukire motani ukwati?
◻ Kodi tingachitenji kulimbitsa mphamvu yosonkhezera maganizo athu?
◻ Kodi Yosefe ndi Davide anasiyana motani poyang’anizana ndi chiyeso?
◻ Kodi ndiuphungu wa Baibulo uti umene udzathandiza amuna ndi akazi kulimbikitsa chomangira cha ukwati?
[Zithunzi patsamba 18]
Kodi ife timakhala ndi moyo wa miyezo iŵiri—wokoma mtima mumpingo ndi wankhalwe panyumba?