Mgwirizano wa Akhristu Umalemekeza Mulungu
“Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimu.”—AEF. 4:3.
1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti m’nthawi ya atumwi, Akhristu a ku Efeso anachititsa kuti Mulungu alemekezedwe?
MGWIRIZANO umene unali mu mpingo wachikhristu ku Efeso unachititsa kuti Mulungu woona, Yehova, alemekezedwe. Mumzinda umenewu, momwe munkachitika malonda osiyanasiyana, Akhristu ena ayenera kuti anali olemera ndipo anali ndi akapolo pamene Akhristu ena anali akapolo ndipo ayenera kuti anali osauka. (Aef. 6:5, 9) Ena anali Ayuda amene anaphunzira choonadi miyezi itatu m’mbuyomo, pamene mtumwi Paulo analalikira m’sunagoge. Ena poyamba ankalambira Atemi ndipo ankachita zamatsenga. (Mac. 19:8, 19, 26) Apa n’zoonekeratu kuti Chikhristu chinagwirizanitsa anthu osiyanasiyana. Paulo ankadziwa kuti mgwirizano wa anthu mu mpingo unachititsa kuti Yehova alemekezedwe. Mtumwiyu analemba kuti: “Kwa iye kukhale ulemerero kudzera mwa mpingo.”—Aef. 3:21.
2. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanasokoneza mgwirizano wa Akhristu a ku Efeso?
2 Komabe panali zinthu zina zimene zikanasokoneza mgwirizano wa mu mpingo wa ku Efeso. Paulo anachenjeza akulu a mu mpingowu kuti: “Pakati pa inu nomwe padzauka anthu amene adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti akanganule ophunzira aziwatsatira.” (Mac. 20:30) Panalinso abale ena amene sanasiyiretu mzimu wogawanitsa anthu umene Paulo anachenjeza kuti “ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.”—Aef. 2:2; 4:22.
Kalata Imene Imatsindika Kufunika kwa Mgwirizano
3, 4. Kodi kalata ya Paulo yopita kwa Akhristu a ku Efeso ikutsindika bwanji nkhani ya mgwirizano?
3 Paulo ankadziwa kuti ngati Akhristu akufuna kupitirizabe kukhala ogwirizana, aliyense anayenera kuchita khama kwambiri kulimbikitsa mgwirizanowo. Mulungu anauzira Paulo kulembera kalata Akhristu a ku Efeso ndipo nkhani yaikulu m’kalata yakeyi inali yonena za mgwirizano. Mwachitsanzo, Paulo analemba za cholinga cha Mulungu ‘chosonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu.’ (Aef. 1:10) Iye anayerekezera Akhristu ndi miyala yosiyanasiyana yomangira nyumba. Anati: “Nyumba yonse, pokhala yolumikizana bwino, ikukula kukhala kachisi woyera wa Yehova.” (Aef. 2:20, 21) Paulo anatsindikanso za mgwirizano wa pakati pa Ayuda ndi Akhristu amitundu ina ndipo anawakumbutsanso kuti onse analengedwa ndi Mulungu mmodzi. Iye ananena kuti Yehova ndi “Atate, amene apangitsa banja lililonse, kumwamba ndi padziko lapansi, kukhala ndi dzina.”—Aef. 3:5, 6, 14, 15.
4 Pamene tikukambirana chaputala chachinayi cha buku la Aefeso, tiona chifukwa chake khama lili lofunika kuti tikhale ogwirizana, mmene Yehova amatithandizira kuti tikhale ogwirizana ndiponso makhalidwe amene angatithandize kukhalabe ogwirizana. Mungachita bwino kuwerenga chaputala chonsechi kuti mupindule kwambiri ndi phunziroli.
Pamafunika Kuchita Khama Kuti Tikhale Ogwirizana
5. N’chiyani chimachititsa kuti angelo a Mulungu azitumikira mogwirizana, nanga n’chifukwa chiyani nthawi zina zimenezi zimakhala zovuta kwa anthufe?
5 Paulo anapempha abale a ku Efeso kuti ‘aziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wawo mwa mzimu.’ (Aef. 4:3) Kuti timvetse kufunika kwa zimenezi, tiyeni tione chitsanzo cha angelo a Mulungu. Palibe zamoyo ziwiri padziko lapansi zimene ndi zofanana ndendende. Choncho tikhoza kunena kuti pa angelo mamiliyoni amene Yehova analenga, aliyense ndi wosiyana ndi mnzake. (Dan. 7:10) Ngakhale zili choncho, onse amatumikira Yehova mogwirizana chifukwa amamumvera ndiponso amachita chifuniro chake. (Werengani Salmo 103:20, 21.) Mofanana ndi angelo okhulupirika, Akhristu ali ndi makhalidwe osiyanasiyana koma kuwonjezera pamenepo, Akhristu ali ndi zofooka zosiyanasiyana. Izi nthawi zina zingachititse kuti kugwirizana kukhale kovuta.
6. Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kukhala ogwirizana ndi abale amene ali ndi zofooka zosiyana ndi zathu?
6 Nthawi zina zimakhala zovuta kuti anthu opanda ungwiro akhale ogwirizana. Mwachitsanzo, kodi chingachitike n’chiyani ngati m’bale wofatsa koma wokonda kuchedwa, akutumikira Yehova limodzi ndi m’bale wina amene amasunga nthawi koma sachedwa kupsa mtima? Aliyense akhoza kumaona kuti mnzakeyo ali ndi vuto koma n’kumaiwala kuti nayenso ali ndi vuto. Kodi zingatheke bwanji kuti abale awiriwa azitumikira mogwirizana? Tiyeni tione mmene makhalidwe amene Paulo ananena angawathandizire. Ndiyeno tionanso mmene kusonyeza makhalidwe amenewa kungatithandizire kukhala ogwirizana. Paulo analemba kuti: “Ndikukuchondererani kuti muziyenda moyenera . . . modzichepetsa kotheratu ndi mofatsa, moleza mtima, mololerana wina ndi mnzake m’chikondi. Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwa mtendere monga chomangira chotigwirizanitsa.”—Aef. 4:1-3.
7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizigwirizana ndi Akhristu anzathu omwenso ndi opanda ungwiro ngati ifeyo?
7 Kuphunzira kutumikira Mulungu mogwirizana ndi anzathu omwe ndi opanda ungwiro n’kofunika chifukwa pali gulu limodzi lokha la olambira oona. “Pali thupi limodzi ndi mzimu umodzi, mogwirizana ndi chiyembekezo chimodzi chimene munaitanidwira. Palinso Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi; Mulungu mmodzi amenenso ndi Atate wa anthu onse.” (Aef. 4:4-6) Yehova amapereka mzimu wake ndiponso kudalitsa gulu la abale amene iye akuwagwiritsa ntchito. Ngakhale winawake atatikhumudwitsa mu mpingo, kodi tingapitenso kuti? Palibe malo ena alionse kumene tingakamve mawu a moyo wosatha.—Yoh. 6:68.
“Mphatso za Amuna” Zimalimbikitsa Mgwirizano
8. Kuti tikhale olimba ndiponso osagawanika, kodi Khristu amagwiritsa ntchito ndani?
8 Paulo anagwiritsa ntchito zimene zinkachitika pakati pa asilikali nthawi zakale pofotokoza mmene Yesu anaperekera “mphatso za amuna” kuti mpingo ukhale wogwirizana. Msilikali amene wapambana ku nkhondo ankabweretsa munthu, amene wamugwira ku nkhondoko, kuti akhale kapolo wothandiza mkazi wake ntchito zapakhomo. (Sal. 68:1, 12, 18) Mofanana ndi zimenezi, Yesu atagonjetsa dziko anatenga anthu amene akufuna kukhala akapolo ake. (Werengani Aefeso 4:7, 8.) Kodi iye anagwiritsa ntchito bwanji anthu amene tingati ndi akapolo? Iye “anapereka ena monga atumwi, ena monga aneneri, ena monga alaliki, ena monga abusa ndi aphunzitsi, kuti awongolere oyerawo, achite ntchito yotumikira, amange thupi la Khristu, kufikira tonse tidzafike pa umodzi m’chikhulupiriro.”—Aef. 4:11-13.
9. (a) Kodi “mphatso za amuna” zimathandiza bwanji kuti mgwirizano ukhalepobe? (b) N’chifukwa chiyani aliyense mu mpingo ayenera kuyesetsa kulimbikitsa mgwirizano?
9 Abusa achikondi amenewa omwe ndi “mphatso za amuna” amathandiza kuti tikhalebe ogwirizana. Mwachitsanzo, mkulu akaona abale awiri ‘akuyambitsa mpikisano pakati pathu’ angathandize kwambiri kuti mu mpingo mukhale mgwirizano mwa ‘kuwawongolera ndi mzimu wachifatso.’ (Agal. 5:26–6:1) “Mphatso za amuna” zimenezi zimatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa kutiphunzitsa mfundo za m’Baibulo. Mwa kuchita zimenezi amalimbikitsa mgwirizano ndipo amatithandiza kuti tikhale Akhristu okhwima mwauzimu. Paulo analemba kuti: “Tisakhalenso tiana, otengekatengeka ngati kuti tikukankhidwa ndi mafunde, ndiponso otengeka uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso chonyenga cha anthu, mwa kuchenjera kwa anthu popeka mabodza.” (Aef. 4:13, 14) Mkhristu aliyense ayenera kuyesetsa kulimbitsa mgwirizano wa abale onse ngati mmene chiwalo chilichonse chimathandizira kuti thupi lonse likule bwino ndi kupeza zinthu zonse zofunikira.—Werengani Aefeso 4:15, 16.
Yambani Kuona Zinthu Moyenera
10. Kodi khalidwe la chiwerewere lingasokoneze bwanji mgwirizano wathu?
10 Kodi mwaona kuti chaputala chachinayi cha kalata ya Paulo yopita kwa Aefeso chimasonyeza kuti chikondi n’chofunika kwambiri kuti Akhristu okhwima mwauzimu akhale ogwirizana? Kalatayi ikusonyezanso zimene munthu wachikondi amachita. Munthu wachikondi sachita chiwerewere kapena khalidwe lotayirira. Paulo analimbikitsa abale ake kuti: “Musamayendenso monga amitundu amayendera.” Amitunduwo ‘sankathanso kuzindikira makhalidwe abwino’ ndipo “anadzipereka okha ku khalidwe lotayirira.” (Aef. 4:17-19) Khalidwe la chiwerewere limene lafala m’dzikoli likhoza kusokoneza mgwirizano wathu. Anthu amakamba nthabwala, kuimba ndiponso kuonerera zinthu zachiwerewere. Iwo amachitanso chiwerewere mobisa kapena moonetsera. Komanso kukopa munthu wina tilibe maganizo okwatirana naye kungasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova komanso ndi mpingo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti khalidwe limeneli lingachititse munthu kuchita chiwerewere mosavuta. Kukopana kungachititse munthu wapabanja kuchita chigololo ndipo zotsatira zake zimakhala zoipa chifukwa zingachititse kuti asiyanitse ana ndi makolo komanso kuti munthuyo asiyane ndi mnzake wa mu ukwati. Izitu ndi zosokoneza kwambiri. Mpake kuti Paulo ananena kuti: “Simunaphunzire Khristu kukhala wotero.”—Aef. 4:20, 21.
11. Kodi Baibulo limalimbikitsa Akhristu kusintha zinthu ziti?
11 Paulo ananena kuti tiyenera kusintha maganizo athu oipa n’kuyamba kuona zinthu moyenerera n’cholinga choti tizikhala mogwirizana ndi ena. Iye anati: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale, umenenso ukuipitsidwa malinga ndi zilakolako zonyenga za umunthuwo. . . . Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo choona ndi kukhulupirika.” (Aef. 4:22-24) Kodi tingatani kuti ‘tikhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo athu’? Tikamasinkhasinkha moyamikira zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu ndiponso chitsanzo chabwino cha Akhristu okhwima mwauzimu komanso kuchita khama, tikhoza kuvala umunthu watsopano “umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.”
Pezani Njira Zatsopano Zolankhulira Bwino
12. Kodi kulankhula zoona kumalimbikitsa bwanji mgwirizano, ndipo n’chifukwa chiyani n’zovuta kwa ena kulankhula zoona?
12 Kulankhula zoona n’kofunika kwambiri kwa anthu amene ali m’banja kapena mu mpingo. Kulankhulana moona mtima, momasuka ndiponso mokoma mtima kumathandiza kuti anthu azigwirizana. (Yoh. 15:15) Koma kodi chimachitika n’chiyani munthu akanamiza m’bale wake? M’bale wakeyo akazindikira samukhulupiriranso. Tsopano mukhoza kumvetsa chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnansi wake, chifukwa ndife ziwalo kwa wina ndi mnzake.” (Aef. 4:25) Munthu amene ali ndi chizolowezi chonama kuyambira ali mwana angavutike kuyamba kulankhula zoona. Koma Yehova angayamikire kwambiri khama lake ndipo angamuthandize.
13. Kodi munthu angatani kuti asiye kulankhula mawu oipa?
13 Yehova amatiphunzitsa kuti tizilimbikitsa ulemu ndi mgwirizano mu mpingo ndiponso m’banja mwa kutiuza zimene sitiyenera kulankhula. Iye amati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu. . . . Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” (Aef. 4:29, 31) Njira imodzi imene ingatithandize kupewa kulankhula mawu oipa ndi kukhala ndi mtima wolemekeza ena. Mwachitsanzo, mwamuna amene amanyoza mkazi wake, ayenera kusintha mmene amaonera mkazi wakeyo n’kuyamba kumuona mmene Yehova amaonera akazi. Mulungu amadzoza akazi ndi mzimu woyera n’kuwapatsa chiyembekezo chokalamulira ngati mafumu limodzi ndi Khristu. (Agal. 3:28; 1 Pet. 3:7) Mofananamo, mkazi amene amakonda kulalatira mwamuna wake ayenera kusintha n’kumatsatira zimene Yesu ankachita akaputidwa.—1 Pet. 2:21-23.
14. N’chifukwa chiyani kulephera kulamulira mkwiyo n’koopsa?
14 Khalidwe lina logwirizana ndi kulankhula mawu oipa ndi kulephera kulamulira mkwiyo. Khalidwe limeneli limadanitsanso anthu amene amagwirizana. Mkwiyo uli ngati moto. Ukhoza kufika posalamulirika n’kuwononga zinthu. (Miy. 29:22) Munthu akakwiya pa zifukwa zomveka ayenera kulamulira mkwiyo wakewo kuti apewe kusokoneza mgwirizano wake ndi anthu ena. Akhristu ayenera kuyesetsa kukhululukira ena, osasunga chidani ndiponso sayenera kuyambitsanso nkhaniyo. (Sal. 37:8; 103:8, 9; Miy. 17:9) Paulo analangiza Aefeso kuti: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndipo musam’patse malo Mdyerekezi.” (Aef. 4:26, 27) Munthu akalephera kulamulira mkwiyo amapereka mpata woti Mdyerekezi ayambitse chidani kapena mikangano mu mpingo.
15. Kodi kuba kumakhala ndi zotsatirapo zotani?
15 Kupewa kuba kungathandizenso kuti mu mpingo mukhale mgwirizano. Baibulo limati: “Wakubayo asabenso.” (Aef. 4:28) Anthu a Yehova amakhulupirirana kwambiri. Ngati Mkhristu angamapezerepo mwayi n’kumaba zinthu za ena, akhoza kusokoneza mgwirizano.
Kukonda Mulungu Kumatigwirizanitsa
16. Kodi kulankhulana bwino kungalimbikitse bwanji mgwirizano?
16 Kukonda Mulungu kumalimbikitsa kukonda anthu ena ndipo zimenezi zimabweretsa mgwirizano mu mpingo wachikhristu. Kuyamikira kukoma mtima kwa Yehova kumatilimbikitsa kuchita khama kuti titsatire malangizo akuti: “[Lankhulani mawu] alionse omanga monga kungafunikire, kuti asangalatse owamva. . . . Koma khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.” (Aef. 4:29, 32) Yehova amakhululukira anthu opanda ungwirofe. Kodi ifenso sitiyenera kukhululukira ena akatilakwira?
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita khama kuti tilimbikitse mgwirizano?
17 Mgwirizano wa anthu a Mulungu umalemekezetsa Yehova. Mzimu wake umatitsogolera m’njira zosiyanasiyana kuti tilimbikitse mgwirizano. Choncho sitiyenera kukana mzimu ukamatitsogolera. Paulo analemba kuti: “Musamamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu.” (Aef. 4:30) Mgwirizano ndi chinthu cha mtengo wapatali ndipo tiyenera kuuteteza. Umachititsa anthu kukhala osangalala ndiponso umalemekezetsa Yehova. “Chifukwa chake, khalani otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi.”—Aef. 5:1, 2.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ndi makhalidwe ati amene amalimbikitsa mgwirizano pakati pa Akhristu?
• Kodi khalidwe lathu lingalimbikitse bwanji mgwirizano mu mpingo?
• Kodi zolankhula zathu zingatithandize bwanji kuti tikhale ogwirizana ndi ena?
[Chithunzi patsamba 17]
Anthu azikhalidwe zosiyanasiyana ndi ogwirizana
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi mukudziwa kuopsa kwa kukopana?