Kutulutsa “Ubwino Wonse”
‘Chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse.’—AEFESO 5:9.
1, 2. Kodi ndimagulu aŵiri ati amene akhalapo chiyambire nthaŵi zakale, ndipo kodi mikhalidwe yawo iri yosiyana motani lerolino?
PAMBUYO pa kupanduka m’Edene, pafupifupi zaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapitazo, ndiponso pambuyo pa Chigumula cha tsiku la Nowa, anthu anagaŵikana m’magulu aŵiri, lina linapangidwa ndi awo amene anakalamira kutumikira Yehova, linalo la awo amene anatsatira Satana. Kodi magulu ameneŵa adakalipo? Ndithudi alipo! Mneneri Yesaya anatchula magulu aŵiriwa ndipo ananeneratu mkhalidwe wawo m’nthaŵi yathu kuti: ‘Taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.’—Yesaya 60:1, 2.
2 Inde, kusiyana kwapakati pa magulu aŵiriwa kuli kwakukulu mofanana ndi kusiyana kwapakati pa mdima ndi kuunika. Ndipo monga momwedi cheza cha kuunika chidzakopera munthu yemwe wataika mumdima, momwemonso kuunika kochokera kwa Yehova kowalikira padziko lamdimali kwakopera mamiliyoni ambiri owongoka mtima ku gulu la Mulungu. Monga momwe Yesaya anapitirizira kunena kuti: ‘Amitundu [nkhosa zina] adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu [oloŵa Ufumu odzozedwa] kwa kuyera kwa kutuluka kwako.’—Yesaya 60:3.
3. Kodi ndi m’njira zotani zimene Akristu amasonyezera ulemerero wa Yehova?
3 Kodi anthu a Yehova amasonyeza motani ulemerero wa Yehova? Choyamba, iwo amalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wakumwamba wokhazikitsidwa wa Mulungu. (Marko 13:10) Koma kuposa pamenepo, iwo amatsanzira Yehova, chitsanzo chabwino koposa cha ubwino, ndipo chotero mwakhalidwe lawo amakopera ofatsa ku kuunikako. (Aefeso 5:1) Paulo ananena kuti: ‘Pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika.’ Iye anapitiriza kuti: ‘Chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi chowonadi, kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse.’ (Aefeso 5:8-11) Kodi Paulo anatanthauzanji mwakunena kuti “ubwino wonse”?
4. Kodi ubwino nchiyani, ndipo kodi umawonekera motani mwa Mkristu?
4 Monga momwe nkhani yathu yapita inasonyezera, ubwino uli khalidwe kapena mkhalidwe wa khalidwe labwino, ukoma. Yesu ananena kuti Yehova yekha ndiye ali wabwino m’lingaliro lotheratu. (Marko 10:18) Komabe, Mkristu angatsanzire Yehova mwakukulitsa ubwino womwe uli chipatso cha mzimu. (Agalatiya 5:22) Pothirira ndemanga pa liwu lakuti a·ga·thosʹ, liwu Lachigiriki lotanthauza “bwino,” Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words imanena kuti, “[Ilo] limafotokoza chinthu chimene, pokhala chabwino m’kawonekedwe kapena kapangidwe, chimatulutsa zotulukapo zopindulitsa.” Chotero Mkristu wokulitsa ubwino adzakhala ponse paŵiri wabwino ndipo adzachita zabwino. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 12:28.) Adzapeŵanso zinthu zimene ziri zosemphana ndi ubwino, ‘ntchito za mdima zosabala kanthu.’ Njira zosiyanasiyana zimene Mkristu angasonyezere ubwino m’mayendedwe ake ndizo ‘ubwino wonse’ umene Paulo anautchula. Kodi zina za izo nzotani?
‘Chita Chabwino’
5. Kodi nchiyani chimene chiri mbali imodzi ya ubwino wonse, ndipo kodi nchifukwa ninji Mkristu ayenera kuikulitsa?
5 Paulo anasonya ku umodzi wa ubwino umenewu m’kalata yake ya kwa Aroma. Polankhula za kugonjera kwa “maulamuliro a akulu,” iye anati: ‘Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m’menemo.’ ‘Chabwino’ chimene akusonyako ndi kumvera malamulo ndi makonzedwe a olamulira akudziko. Kodi nchifukwa ninji Mkristu ayenera kugonjera kwa iwo? Kotero kuti apeŵe kuwombana kosayenerera ndi olamulira, komwe kungam’bweretsere chilango ndipo—chofunika koposa—kuti akhale ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu. (Aroma 13:1-7) Pamene akusunga chimvero chake choyambirira kwa Yehova, Mkristu ‘amalemekeza mfumu,’ samapandukira maulamuliro amene Yehova Mulungu wawalola kukhalapo. (1 Petro 2:13-17) Mwanjirayi, Akristu ali anansi abwino, nzika zabwino, ndi zitsanzo zabwino.
Kulingalira Ena
6. (a) Kodi ndiiti imene ili mbali ina ya ubwino? (b) Kodi ndani amene amatchulidwa m’Baibulo kukhala oyenerera kulingalira kwathu?
6 Ubwino wa Yehova umasonyezedwa mwakupereka kwa onse okhala padziko lapansi “mvula ndi nyengo za zipatso.” Ichi chimatulukapo ‘kudzaza . . . ndi chakudya ndi chikondwero’ ndipo zimamsonyeza kukhala Mulungu wolingaliradi. (Machitidwe 14:17) Tingamtsanzire m’mbali imeneyi mwakusonyeza kulingalira ena m’zinthu zazing’ono ndi zazikulu. Kodi makamaka kwa yani? Paulo akusonya makamaka kwa akulu, ‘iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu.’ Iye akufulumiza Akristu kuwapatsa ameneŵa ‘ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo.’ (1 Atesalonika 5:12, 13) Kodi tingachite zimenezi motani? Mwakugwirizana nawo kotheratu—mwachitsanzo, mwakukhala ndi phande m’ntchito yofunika pa Nyumba Yaufumu. Pamene kuli kwakuti nthaŵi zonse tiyenera kukhala omasuka kufikira akulu kaamba ka thandizo lofunikira, sitiyenera kukhala okokosa mopambanitsa. M’malomwake, m’njira zonse zimene tingathe, tiyenera kuyesayesa kupeputsa katundu wa abusa ogwira ntchito zolimba ameneŵa, amene unyinji wa iwo ali ndi mathayo abanja kuwonjezera pa ntchito zawo zamumpingo.
7. Kodi ndi m’njira zotani zimene tingasonyezere kulingalira kwa okalamba?
7 Okalamba nawonso afunikira kulingalira kwathu. Lamulo lachindunji la m’Chilamulo cha Mose linati: ‘Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; ine ndine Yehova.’ (Levitiko 19:32) Kodi kulingalira kumeneku kungasonyezedwe motani? Achichepere angadzipereke mwaufulu kuthandiza kukawagulira zinthu kapena kuwagwirira ntchito zina. Akulu angafufuze moyenerera kuwona ngati okalamba alionse akufunikira thandizo kuti afike pamisonkhano. Pamisonkhano yadera, anthu achichepere, anyonga pofuna kudutsa mofulumira, adzapeŵa kukankha okalamba oyenda pang’onopang’ono, ndipo adzakhala oleza mtima ngati wokalamba akuchedwa kupeza mpando kapena chakudya.
8. Kodi tingasonyeze motani kulingalira ku gulu lina lofunikira lotchulidwa m’Baibulo?
8 Wamasalmo akutchula gulu lina limene limafunikira kulingalira: “Wodala iye amene asamalira wosauka.” (Salmo 41:1) Kungakhale kopepuka kusamalira anthu otchuka kapena achuma, koma bwanji ponena za osauka kapena amphaŵi? Wolemba Baibulo Yakobo anasonyeza kuti kusamalira kolingana kwa ameneŵa kuli chiyeso cha chilungamo chathu ndi chikondi Chachikristu. Tiyenitu tichipambane chiyeso chimenechi mwakukhala olingalira kulinga kwa onse mosasamala kanthu za mikhalidwe yawo.—Afilipi 2:3, 4; Yakobo 2:2-4, 8, 9.
‘Khalani Achifundo’
9, 10. Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhala achifundo, ndipo kodi ubwino umenewu ungasonyezedwe motani?
9 Ubwino wina ukuwonekera m’mafanizo ena a Yesu. M’limodzi la ameneŵa, Yesu anasimba za Msamariya yemwe anapeza munthu amene anafwambidwa, kumenyedwa kwabasi, ndikusiidwa mphepete mwa msewu. Mlevi ndi wansembe anamlambalala munthu wovulazidwayo, osamthandiza. Koma Msamariyayo anaima nampatsa chithandizo, akumachita zochuluka kuposa zimene zinafunikira. Kaŵirikaŵiri nkhaniyo m’Chingelezi imatchedwa fanizo la Msamariya Wabwino. Kodi ndi ubwino wotani umene Msamariyayo anasonyeza? Chifundo. Pamene Yesu anafunsa mvetseri wake kutchula amene anatsimikizira kukhala mnansi wa munthu wovulazidwayo, yankho lolondola ili linaperekedwa: ‘Iye wakumchitira chifundo.’—Luka 10:37.
10 Akristu achifundo amatsanzira Yehova, za amene Mose anauza Aisrayeli kuti: ‘Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuwonongani, kapena kuiŵala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.’ (Deuteronomo 4:31) Yesu anasonyeza mmene chifundo cha Mulungu chiyenera kutiyambukirira: ‘Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo.’ (Luka 6:36) Kodi tingasonyeze motani chifundo? Monga momwe fanizo la Yesu linasonyezera, njira imodzi ndiyo kukhala wokonzeka kuthandiza munthu mnzathu, ngakhale ngati kukatanthauza kukhala paupandu kapena kudzivutitsa. Munthu wabwino samanyalanyaza kuvutika kwa mbale wake ngati iye angakhoze kuchitapo kanthu.—Yakobo 2:15, 16.
11, 12. Malinga ndi fanizo la Yesu la akapolo, kodi chifundo chimaphatikizapo chiyani, ndipo kodi ndimotani mmene tingachisonyezere lerolino?
11 Fanizo lina la Yesu linasonyeza kuti ubwino wachifundo umaphatikizapo kukonzeka kukhululukira ena. Iye anasimba za kapolo yemwe anali ndi ngongole ya matalente zikwi khumi kwa mbuye wake. Polephera kubweza, kapoloyo anapempha chifundo, ndipo mbuye wakeyo anamkhululukira mokoma mtima ngongole yaikulu ya marupiya 60,000,000 imeneyo. Koma kapoloyo anachoka napeza kapolo wina yemwe anali naye ngongole ya marupiya zana limodzi lokha. Mopanda chifundo kapolo wokhululukiridwayo anaponya wamangawayo m’ndende kufikira atambwezera. Mowonekera bwino, kapolo wopanda chifundoyo sanali munthu wabwino, ndipo pamene mbuye wake anamva zimene zinachitika, anamlipitsa.—Mateyu 18:23-35.
12 Tiri mumkhalidwe wofanana ndi kapolo wokhululukiridwayo. Pamaziko a nsembe ya Yesu, Yehova wakhululukira ngongole yaikulu ya tchimo pa cholembedwa chathu. Ndithudi, tiyenera kukhala okonzeka kukhululukira ena. Yesu ananena kuti tiyenera kukhala okonzeka kukhululukira ‘kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri,’ ndiko kuti popanda malire. (Mateyu 5:7; 6:12, 14, 15; 18:21, 22) Chifukwa chake, Mkristu wachifundo sadzasunga chidani. Iye sadzasunga zinthu kukhosi kapena kukana kulankhula ndi Mkristu mnzake chifukwa cha malingaliro oipa otsalira chifukwa cha kusamvana. Kupanda chifundo koteroko sindiko chizindikiro cha ubwino Wachikristu.
Kuoloŵa Manja ndi Kuchereza
13. Kodi nchiyaninso chimene ubwino umaphatikizapo?
13 Ubwino umasonyezedwanso mwakuoloŵa manja ndi kuchereza. Panthaŵi ina mwamuna wachichepere anadzafuna uphungu kwa Yesu. Iye anati: ‘Mphunzitsi, chabwino nchiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?’ Yesu anamuuza kuti ayenera kupitiriza kusunga malamulo a Mulungu. Inde, kumvera malamulo a Yehova kuli mbali ya ubwino. Mwamuna wachichepereyo analingalira kuti anali kuchita kale zimenezi monga momwe akanathera. Mowonekeratu, kwa anansi ake anawoneka kale kukhala munthu wabwino, komabe analingalira kuti anasoŵa chinachake. Chotero Yesu anamuuza kuti: ‘Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphaŵi, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.’ (Mateyu 19:16-22) Mwamuna wachichepereyo anapita wachisoni. Iye anali ndi chuma chambiri. Ngati akanatsatira uphungu wa Yesu, iye akanasonyeza kuti sanali wokondetsa zinthu zakuthupi. Ndipo akanachita kachitidwe kabwino ka kuoloŵa manja kopanda dyera kwenikweni.
14. Kodi ndiuphungu wabwino wotani umene Yehova ndi Yesu anapereka ponena za kuoloŵa manja?
14 Yehova anafulumiza Aisrayeli kukhala ooloŵa manja. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti: ‘Mudzimpatsa ndithu [mnansi wanu waumphaŵi], osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m’zonse muikapo dzanja lanu.’ (Deuteronomo 15:10; Miyambo 11:25) Yesu Kristu mwaumwini anafulumiza kukhala wooloŵa manja: ‘Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhuchumuka, wosefukira.’ (Luka 6:38) Ndiponso, Yesu iyemwini anali wooloŵa manja. Panthaŵi ina, anapatula nthaŵi kuti apumule pang’ono. Makamu anadziŵa kumene iye anali ndipo anadza kwa iye. Mooloŵa manja Yesu anaiwala zakupumula ndipo analithandiza khamulo. Pambuyo pake, iye anasonyeza kuchereza kwapadera mwakupatsa khamu lalikululo chakudya.—Marko 6:30-44.
15. Kodi ndimotani mmene ophunzira a Yesu anakhazikitsira chitsanzo chabwino koposa m’kusonyeza kuoloŵa manja?
15 Pokhala okhulupirika ku uphungu wa Yehova ndi Yesu, ophunzira ambiri a Yesu anali ooloŵa manja ndi ochereza. M’masiku oyambirira a mpingo Wachikristu, chiŵerengero chachikulu cha awo amene anapezekapo paphwando la Pentekoste mu 33 C.E. anamva kulalikira kwa atumwi nakhulupirira. Chakudya chawo chinapereŵera pamene anakhala kwa nthaŵi yaitali pambuyo pa phwandolo kuti aphunzire zowonjezereka. Chotero, okhulupirira akumaloko anagulitsa katundu wawo napereka ndalamazo kuti adyetse abale awo atsopano kotero kuti aŵanso akhazikike m’chikhulupiriro. Kunali kuoloŵa manja kotani nanga!—Machitidwe 4:32-35; onaninso Machitidwe 16:15; Aroma 15:26.
16. Tchulani njira zina zimene tingakhalire ochereza ndi ooloŵa manja lerolino.
16 Lerolino, kuoloŵa manja konga kwa Kristu kofananako kumawonedwa pamene Akristu apereka nthaŵi ndi ndalama zawo ku mipingo yakumaloko ndi ku ntchito yolalikira yapadziko lonse. Kumawonetsedwa pamene athandiza abale ovutika ndi tsoka lachilengedwe kapena nkhondo. Kumasonyezedwa pamene woyang’anira dera asamaliridwa mkati mwa kuchezetsa kwake kokhazikika. Kapena pamene “ana amasiye” aitanidwa mooloŵa manja kukakhala ndiphande m’kusanguluka ndi maphunziro Abaibulo abanja ndi mabanja ena Achikristu, uku kulinso kuchereza, kusonyezedwa kwa ubwino Wachikristu.—Salmo 68:5.
Kunena Zowonadi
17. Kodi nchifukwa ninji kunena zowona kuli chitokoso lerolino?
17 Pamene Paulo analongosola zipatso za kuunika, anagwirizanitsa ubwino ndi chilungamo ndi chowonadi, ndipo kukakhala kolondola kunena kuti kunena zowonadi ndi mbali ina ya ubwino. Anthu abwino samanena bodza. Komabe, kunena zowonadi kuli chitokoso chapadera lerolino pamene kunama kuli kofala. Anthu ambiri amanama pamene akudzaza zikalata zamsonkho zosonyeza malipiro awo. Olembedwa ntchito amanama ponena za ntchito imene amachita. Ophunzira amanama m’maphunziro awo ndi mayeso. Anthu abizinesi amanama popanga mapangano abizinesi. Ana amanama kuti apeŵe chilango. Odyera miseche anjiru amawononga mbiri yabwino ya ena mwakunena bodza.
18. Kodi Yehova amawawona motani onama?
18 Kunama kumamnyansa Yehova. Pakati pa zinthu ‘zisanu ndi ziŵiri’ zimene amazida pali “lilime lonama” ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza.” (Miyambo 6:16-19) “Onse a mabodza” andandalitsidwa pakati pa amantha, ambanda, ndi achigololo, amene sadzakhala ndi malo m’dziko latsopano la Mulungu. (Chibvumbulutso 21:8) Ndiponso, mwambi umatiuza kuti: ‘Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; koma wokhota m’njira yake amnyoza.’ (Miyambo 14:2) Wabodza ali wokhota m’njira yake. Chifukwa chake, wabodza amapereka umboni wakunyoza Yehova. Ndilingaliro loipa chotani nanga! Tiyeni nthaŵi zonse tinene chowonadi, ngakhale ngati chingatipangitse kudzudzulidwa kapena kutaikiridwa m’zandalama. (Miyambo 16:6; Aefeso 4:25) Awo amene amanena zowonadi amatsanzira Yehova, ‘Mulungu wa chowonadi.’—Salmo 31:5.
Kulitsani Ubwino
19. Kodi nchiyani chimene nthaŵi zina chimawonedwa m’dziko, chimene chimalemekeza Mlengi?
19 Iyi ndi mitundu yoŵerengeka yokha ya ubwino ‘wonse’ umene Mkristu ayenera kukulitsa. Nzowona kuti anthu m’dziko amasonyeza ubwino kumlingo winawake. Mwachitsanzo, ena ali ochereza ndipo ena ngachifundo. Ndithudi, chimene chinapangitsa fanizo la Msamariya Wabwino kukhala lapadera chinali chakuti Yesu anasimba za munthu wosakhala Myuda amene anasonyeza chifundo pamene akulu a mpingo Wachiyuda sanatero. Kulidi kolemekeza Mlengi wa munthu kuti zikhoterero zoterozo zimawonekerabe mwachibadwa mwa anthu ena ngakhale pambuyo pa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi za kupanda ungwiro.
20, 21. (a) Kodi nchifukwa ninji ubwino Wachikristu uli wosiyana ndi ubwino umene tingawone mwa anthu akudziko? (b) Kodi ndimotani mmene Mkristu angakulitsire ubwino, ndipo nchifukwa ninji tiyenera kukhala akhama pochita zimenezo?
20 Komabe, kwa Akristu ubwino suli kokha mkhalidwe womwe angakhale nawo kapena kusakhala nawo. Uli mkhalidwe umene ayenera kukulitsa m’mbali zake zonse, popeza kuti ayenera kukhala akutsanza a Mulungu. Kodi zimenezi nzotheka motani? Baibulo limatiuza kuti tikhoza kuphunzira ubwino. Wamasalmo anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mundiphunzitse [ubwino, NW].” Motani? Iye anapitiriza kuti: “Pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.” Iye anawonjezera kuti: ‘Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino; mundiphunzitse malemba anu.’—Salmo 119:66, 68.
21 Inde, ngati tiphunzira malamulo a Yehova ndikuwalabadira, tidzakulitsa ubwino. Kumbukirani nthaŵi zonse kuti ubwino uli chipatso cha mzimu. Ngati tifunafuna mzimu wa Yehova kupyolera m’pemphero, mayanjano, ndi phunziro Labaibulo, pamenepo tidzathandizidwadi kukulitsa mkhalidwewu. Ndiponso, ubwino uli wamphamvu. Ukhoza kugonjetsa choipa. (Aroma 12:21) Pamenepo, kuli kofunika chotani nanga kuti tichite zabwino kwa onse, makamaka kwa abale athu Achikristu. (Agalatiya 6:10) Ngati tichita zimenezo, tidzakhala pakati pa awo amene adzasangalala ndi “ulemerero ndi ulemu ndi mtendere” zomwe zalonjezedwa kwa ‘aliyense wakuchita zabwino.’—Aroma 2:6-11.
Kodi Mungayankhe?
◻ Kodi ndimotani mmene tingachitire zabwino kwa maulamuliro aakulu?
◻ Kodi ndani, mwa ena, amene ali oyenerera kulingalira kwathu?
◻ Kodi ndi m’njira zotani zimene chifundo chingadzisonyezere?
◻ Kodi ndimachitidwe otani a kuoloŵa manja ndi kuchereza amene amadziŵikitsa Akristu lerolino?
◻ Kodi ndimotani mmene ubwino ungakulitsidwire?
[Chithunzi patsamba 20]
Kulingalira ena kuli mbali ina ya ubwino
[Chithunzi patsamba 23]
Monga Mphunzitsi Wamkulu, Yesu anadzipereka mooloŵa manja