Mutu 21
Cholinga cha Yehova Chikwaniritsidwa ndi Ulemerero
ZOLENGEDWA zonse zanzeru zikulambira Mulungu woona yekha mogwirizana ndipo zonse zili ndi ufulu wa ulemerero monga ana a Mulungu. Chimenechitu ndicho cholinga cha Yehova chimene chimasonyeza chikondi chake. N’zimenenso onse okonda chilungamo amafunitsitsa zitachitika.
2 Yehova anayamba kukwaniritsa cholinga chake chachikulu chimenechi pamene anayamba ntchito yake yolenga. Anayamba ndi kulenga Mwana amene kuchokera pa kuuka kwake wakhala “chinyezimiro cha ulemerero [wa Mulungu], ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.” (Ahebri 1:1-3) Mwana ameneyu anali wapadera, chifukwa analengedwa ndi Mulungu yekhayo basi. Kenako, kunali kudzera mwa Mwana ameneyu kuti ena onse anadzakhalako: choyamba angelo kumwamba, ndiyeno anthu padziko lapansi. (Yobu 38:7; Luka 3:38) Onseŵa anapanga banja limodzi la m’chilengedwe chonse. Iwo onse, anaona Yehova kukhala Mulungu wawo, kukhala Wolamulira Chilengedwe Chonse, ndiponso Atate wawo wachikondi.
3 Makolo athu aumunthu oyambirira ataweruzidwa kuti afe chifukwa chochimwa mwadala, Mulungu anawakana ndipo anawathamangitsa m’Edene. Zitatero, iwo anasiya kukhala m’banja lake la m’chilengedwe chonse. (Genesis 3:22-24; Deuteronomo 32:4, 5) Ife tonse ndife ana awo, choncho tinabadwa ndi uchimo. Koma Yehova anadziŵa kuti ena mwa ana a Adamu ndi Hava adzakonda chilungamo. Ndiye, posonyeza chikondi Chake, anakonza zoti ameneŵa akapeze “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:20, 21.
Israyeli Sakukhalanso Woyanjidwa
4 Patapita zaka pafupifupi 2,500 kuchokera pamene Adamu analengedwa, Yehova anapereka kwa anthu ena mwayi wokhala naye pa ubale wapadera. Anasankha Israyeli wakale kukhala anthu ake ndipo anawapatsa Chilamulo chake. (Genesis 12:1, 2) Anawasandutsa mtundu ndipo anawagwiritsa ntchito kukwaniritsa cholinga chake. (Deuteronomo 14:1, 2; Yesaya 43:1) Ngakhale zinali choncho, iwo anali adakali akapolo a uchimo ndi imfa, ndipo sanapeze ufulu wa ulemerero umene Adamu ndi Hava anali nawo pachiyambi.
5 Komano, Aisrayeliwo anali oyanjidwa ndi Mulungu. Analinso ndi udindo wolemekeza Yehova amene anali Atate wawo ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake. Yesu anagogomeza kuti iwo anafunika kukwaniritsa udindo wawowo. (Mateyu 5:43-48) Koma mtundu wa Israyeli unalephera kuchita zimenezo. Pamene Ayudawo anati “tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu,” Yesu anati zochita zawo ndi mzimu umene iwo anali kusonyeza zinasemphana ndi zimene iwo anali kunenazo. (Yohane 8:41, 44, 47) Mu 33 C.E., Mulungu anathetsa Chilamulo, ndipo ubale wapadera umene Israyeli anali nawo ndi iye unathera pomwepo. Kodi zimenezi zinatanthauza kuti anthu sakanakhala pa ubale ndi Mulungu?
Kusonkhanitsa “za Kumwamba”
6 Mtumwi Paulo anasonyeza kuti ena mwa anthu atha kukhala pa ubale wapadera ndi Mulungu. Mwachitsanzo, iye analemba za makonzedwe a Yehova akuti aja amene ali ndi chikhulupiriro angakhale m’banja Lake. Anati: “[Mulungu] anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunam’komera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye, kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.” (Aefeso 1:9, 10) “Makonzedwe” ameneŵa agona pa Yesu Kristu. Kudzera mwa iyeyo, anthu akuyanjidwa ndi Mulungu. Ena oŵerengeka mwa anthuŵa akuyembekeza kukakhala kumwamba. Koma ochuluka adzakhala pa dziko lapansi kosatha.
7 Choyamba, kuchokera pa Pentekoste mu 33 C.E., amayang’ana makamaka “za kumwamba,” kutanthauza, aja amene akakhala oloŵa nyumba anzake a Kristu mu Ufumu wakumwamba. Chifukwa chakuti iwo anakhulupirira kuti nsembe ya Yesu ndi yofunika kwambiri, Mulungu anawayesa olungama. (Aroma 5:1, 2) M’kupita kwa nthaŵi, ameneŵa anaphatikizapo Ayuda ndi Akunja, ndipo chiŵerengero cha “za kumwamba” chikakwana 144,000. (Agalatiya 3:26-29; Chivumbulutso 14:1) Amene adakali pa dziko lapansi ndi ochepa chabe.
Kusonkhanitsa “za Padziko”
8 Ndi makonzedwe omwewo, akusonkhanitsanso “za padziko.” Anthu mamiliyoni ambiri akusonkhanitsidwa panopa amene akuyembekeza kudzakhala pa dziko lapansi kosatha. Iwo amalemekeza dzina la Yehova ndi kukweza kulambira kwake mogwirizana ndi otsalira a oloŵa Ufumu. (Yesaya 2:2, 3; Zefaniya 3:9) Iwonso amati Yehova ndi “Atate” wawo chifukwa amazindikira kuti iyeyo ndiye gwero la moyo. Ndipo iye amawayanja chifukwa chakuti amakhulupirira mwazi umene Yesu anakhetsa. (Chivumbulutso 7:9, 14) Koma popeza adakali opanda ungwiro, m’tsogolo m’pamene Mulungu adzawavomereza kukhaliratu ana ake.
9 Anthu ameneŵa odzakhala pa dziko lapansi akuyembekeza ndi chidwi nthaŵi imene anthu onse ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi.’ (Aroma 8:21) Kumasuka kumeneku kudzayamba pamene Kristu ndi magulu ake a nkhondo akumwamba adzathetsa chisautso chachikulu mwa kuchifikitsa pachimake pa Armagedo. Pamenepo adzawononga dziko lonse loipa la Satanali, ndipo padzatsatira madalitso a Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000 mu Ufumuwo.—Chivumbulutso 19:17-21; 20:6.
10 Komatu ndiye zidzasangalatsa pamene atumiki a Yehova padziko lapansi nawonso mogwirizana adzanena mawu amene atumiki ake akumwamba amanena mosangalala kuti: “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu n’zolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.” (Chivumbulutso 15:3, 4) Inde, atumiki onse a Yehova adzagwirizana kulambira Mulungu woona yekha. Ngakhale akufa adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mpata wogwirizana ndi enawo potamanda Yehova mofuula.—Machitidwe 24:15.
Kutsogoloku Kuli Ufulu Wodabwitsa
11 Chisautso chachikulu, limodzi ndi Armagedo imene ndi pachimake pa chisautso chachikulucho, zidzayeretsa dzikoli kuchotsapo kuipa. Satana Mdyerekezi sadzakhalanso “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.” Olambira Yehova sadzafunikanso kulimbana ndi mphamvu yoipa ya Satana. (2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 20:1, 2) Chipembedzo chonyenga sichidzaipitsanso dzina la Yehova ndi kugaŵanitsa anthu. Atumiki a Mulungu woona sadzachitidwanso mopanda chilungamo kapena kulimidwa pa msana ndi maboma a anthu. Umenewotu udzakhala ufulu wodabwitsa kwambiri!
12 Pokhala “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi,” Yesu adzagwiritsa ntchito mtengo wa nsembe yake kufafaniza machimo a anthu. (Yohane 1:29) Pamene Yesu anali padziko lapansi anakhululukira anthu machimo awo, ndipo atawakhululukira anawachiritsa kutsimikiza kuti wawakhululukira. (Mateyu 9:1-7; 15:30, 31) Momwemonso, Kristu Yesu, monga Mfumu yakumwamba ya Ufumu wa Mulungu, adzachita zozizwitsa mwa kuchiritsa olemala, ovutika maganizo, ndi ena onse amene ali ndi matenda amtundu uliwonse. (Chivumbulutso 21:3, 4) “Lamulo” la uchimo adzalithetsa mwa anthu onse omvera kuti maganizo awo ndi zochita zawo ziziwasangalatsa iwowo ndiponso zizisangalatsa Mulungu. (Aroma 7:21-23) Mmene zaka 1,000 zizidzatha, anthu adzakhala atafika pa ungwiro, kukhala ‘m’chifanizo ndi chikhalidwe’ cha Mulungu woona yekha.—Genesis 1:26.
13 Kristu atafikitsa anthu pa ungwiro, adzabwezera kwa Atate ulamuliro umene anapatsidwa woti agwirire ntchitoyi. “Adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe. Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira [Mulungu] ataika adani onse pansi pa mapazi ake.” (1 Akorinto 15:24, 25) Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Ufumuwo udzakhala utamaliza ntchito yake yonse; choncho sipadzafunikanso boma lina laling’ono limeneli loti likhale pakati pa Yehova ndi anthu. Ndipo popeza uchimo ndi imfa zidzakhala zitathetsedweratu komanso anthu adzakhala atawomboledwa, Yesu sadzafunikanso kukhala Momboli. Baibulo limati: “Pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anam’gonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.”—1 Akorinto 15:28.
14 Zitatha izi, anthu angwiro adzapatsidwa mwayi woonetsa ngati anasankhadi kuti adzatumikira Mulungu woona yekha kosatha. Choncho, asanawalandire kuti akhaliretu ana ake, Yehova adzalola anthu onsewo angwiro kuyesedwa komaliza. Satana ndi ziwanda zake adzamasulidwa ku phompho. Aja amene amakondadi Yehova zimenezi sizidzawapweteka mpaka kalekale. Koma aliyense amene sadzakhulupirika n’kulola kunyengedwa ndi kupandukira Yehova adzawonongedwa kotheratu, limodzi ndi wambanda woyambirira uja ndi ziwanda zake.—Chivumbulutso 20:7-10.
15 Kenako Yehova adzawalandira kukhala ana ake anthu onse angwiro amene pa chiyeso chomaliza anakweza ulamuliro wake. Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya, adzakhala ndi ufulu wonse wa ulemerero wa ana a Mulungu m’banja lake la m’chilengedwe chonse. Zolengedwa zonse zanzeru kumwamba ndi padziko lapansi pano zidzagwirizana kachiŵirinso kum’lambira iyeyo monga Mulungu woona yekha. Cholinga cha Yehova chidzakhala chitakwaniritsidwa ndi ulemerero! Kodi mukufuna kukhala m’banja la m’chilengedwe chonse losangalala limene lidzakhala mpaka kalekale limenelo? Ngati mukuti mukufuna, ndiye tikukulimbikitsani kulabadira zimene Baibulo limanena pa 1 Yohane 2:17. Limati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Chipanduko chisanayambe m’Edene, kodi onse olambira Yehova anali naye pa ubale wotani?
• Kodi atumiki a Mulungu ali ndi udindo wotani?
• Kodi ndani amene adzakhale ana a Mulungu m’tsogolo muno, nanga zimenezi zikukhudza bwanji cholinga cha Yehova chakuti pakhale kugwirizana pa kulambira?
[Mafunso]
1, 2. (a) Kodi cholinga cha Yehova pa zolengedwa zake zanzeru n’chiyani? (b) Kodi amene anaphatikizidwa m’banja la Mulungu la olambira ake ogwirizana ndani?
3. (a) Kodi ife tonse tinalandira chiyani kwa makolo athu oyambirira? (b) Kodi Yehova anawakonzera zotani ana a Adamu posonyeza chikondi chake?
4. Kodi Yehova anapatsa Israyeli wakale mwayi wotani?
5. Kodi Aisrayeli anataya bwanji chiyanjo chapadera chimene anali nacho ndi Mulungu?
6. Kodi cholinga cha “makonzedwe” amene Paulo anatchula pa Aefeso 1:9, 10 n’chiyani?
7. Kodi “za kumwamba” ndani?
8. Kodi “za padziko” ndani, nanga ubale wawo ndi Yehova n’ngotani?
9. Kodi Aroma 8:21 akuwalonjeza chiyani anthu?
10. Kodi atumiki a Yehova adzaimba nyimbo yotani yom’tamanda?
11. Kodi opulumuka chisautso chachikulu adzakhala ndi ufulu wotani wodabwitsa kwambiri?
12. Kodi onse adzamasuka bwanji ku uchimo ndi mavuto akewo?
13. Pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, kodi Kristu adzachitanji, nanga zotsatira zake zidzakhala zotani?
14. Kodi n’chiyani chimene chidzachitikira anthu onse angwiro, nanga chifukwa chake n’chiyani?
15. Kodi zinthu zidzakhala bwanji kachiŵirinso pakati pa zolengedwa zonse zanzeru za Yehova?
[Chithunzi patsamba 190]
Anthu omvera adzakhala ndi moyo wosangalatsa m’paradaiso padziko lonse